Facebook
From TBS, 2 Weeks ago, written in Plain Text.
This paste is a reply to KJV from TBS - view diff
Embed
Download Paste or View Raw
Hits: 115
  1. Chichewa
  2. Mat 1:1 Buku la mbadwo wa Yesu Khristu, mwana wamwamuna wa Davide, mwana wamwamuna wa Abrahamu.
  3. Mat 1:2 Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;
  4. Mat 1:3 Ndipo Yuda anabala Faresi ndi Zara mwa Tamara; ndi Faresi anabala Esiromu; ndi Esiromu anabala Aramu;
  5. Mat 1:4 Ndi Aramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala Salimoni;
  6. Mat 1:5 Ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabu; ndi Boazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jesse;
  7. Mat 1:6 Ndi Jesse anabala Davide mfumuyo; ndipo Davide mfumuyo anabala Solomoni mwa iye [amene adali mkazi] wa Uriyasi;
  8. Mat 1:7 Ndi Solomoni anabala Reboyamu; ndi Reboyamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;
  9. Mat 1:8 Ndi Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Oziyasi;
  10. Mat 1:9 Ndi Oziyasi anabala Yoatamu; ndi Yoatamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Ezekiyasi;
  11. Mat 1:10 Ndi Ezekiyasi anabala Manases; ndi Manases anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiyasi;
  12. Mat 1:11 Ndi Yosiyasi anabala Yekoniyasi ndi abale ake, pa nthawi imene iwo anatengedwa kumka ku Babuloni:
  13. Mat 1:12 Ndipo pambuyo pa kutengedwa iwo ku Babuloni, Yekoniyasi anabala Salatiyeli; ndi Salatiyeli anabala Zorobabele;
  14. Mat 1:13 Ndi Zorobabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;
  15. Mat 1:14 Ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;
  16. Mat 1:15 Ndi Eliyudi anabala Eliezara; ndi Eliezara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;
  17. Mat 1:16 Ndi Yakobo anabala Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene mwa iye anabadwa Yesu, wotchedwa Khristu.
  18. Mat 1:17 Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide [ndiyo] mibadwo khumi ndi inayi; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kumka ku Babuloni mibadwo khumi ndi inayi; ndi kuyambira pa kutengedwa kumka ku Babuloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inayi.
  19. Mat 1:18 ¶Tsopano kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kudali kotere: Pamene amayi wake Mariya adapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, iwowo asadakhale pamodzi, iye adapezedwa ali ndi pakati pa kwa Mzimu Woyera.
  20. Mat 1:19 Kenaka Yosefe mwamuna wake, pokhala [munthu] wolungama, ndiponso posafuna kumpangitsa iye kukhala chitsanzo cha anthu, analingalira kumleka iye mwachinsinsi.
  21. Mat 1:20 Koma pamene iye anali kusinkhasinkha pa zinthu izi, tawonani mngelo wa Ambuye adawoneka kwa iye m’kulota, kunena kuti, Yosefe, mwana wamwamuna wa Davide, usawope kudzitengera kwa iwe Mariya mkazi wako: pakuti chimene chalandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.
  22. Mat 1:21 Ndipo iye adzabala mwana wamwamuna, ndipo iwe udzamutcha dzina lake YESU: pakuti iye adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.
  23. Mat 1:22 Tsopano zonsezi zidachitika, kuti chikakhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa cha Ambuye mwa mneneri, kunena kuti,
  24. Mat 1:23 Tawonani, namwali adzayima, ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo iwo adzamutcha dzina lake Emmanuel, limene potanthawuzidwa ndilo, Mulungu ali nafe.
  25. Mat 1:24 Kenaka Yosefe powukitsidwa kutulo take adachita monga mngelo wa Ambuye adamulamulira iye, ndipo anadzitengera kwa iye yekha mkazi wake:
  26. Mat 1:25 Ndipo sadamdziwa iye kufikira adabala mwana wake wamwamuna woyamba: ndipo iye anamutcha dzina lake YESU.
  27. Mat 2:1 Tsopano pamene Yesu anabadwa mu Betelehemu wa Yudeya m’masiku a Herode mfumu, tawonani, panadza anzeru kuchokera kum’mawa kufika ku Yerusalemu.
  28. Mat 2:2 Kunena kuti, Ali kuti iye amene wabadwa Mfumu ya Ayuda? Pakuti ife tawona nyenyezi yake kum’mawa, ndipo tadzera kudzalambira iye.
  29. Mat 2:3 Ndipo pamene Herode mfumuyo adamva [zinthu izi], iye adavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi ndi iye.
  30. Mat 2:4 Ndipo pamene adasonkhanitsa pamodzi ansembe akulu onse ndi alembi a anthu, iye adafunsira kwa iwo kumene Khristuyo adzabadwira.
  31. Mat 2:5 Ndipo iwo adanena kwa iye, M’Betelehemu wa Yudeya: pakuti kudalembedwa kotero ndi mneneri,
  32. Mat 2:6 Ndipo iwe Betelehemu, [mu] dziko la Yuda, suli wamng’onong’ono pakati pa akulu a Yuda; pakuti kuchokera mwa iwe mudzatuluka Mtsogoleri, amene adzalamulira anthu anga Aisrayeli.
  33. Mat 2:7 Kenaka Herode, pamene iye adayitana anzeruwo mwachinsinsi, anawafunsa iwo mwakhama nthawi imene nyenyeziyo idawoneka.
  34. Mat 2:8 Ndipo iye anawatumiza iwo ku Betelehemu, ndipo anati, Pitani ndipo mufufuzitse kamwanako: ndipo pamene inu mwampeza [iye], mundibwezerenso ine mawu, kuti ine ndidzadze kumlambiranso iye.
  35. Mat 2:9 Pamene iwo adamva mfumu, iwo adanyamuka; ndipo, tawonani, nyenyeziyo, imene iwo adayiwona kum’mawa, idapita patsogolo pa iwo, kufikira idadza niyima pamwamba pomwe padali kamwanako.
  36. Mat 2:10 Pamene adayiwona nyenyeziyo, iwo adakondwera ndi chimwemwe chachikulu choposa.
  37. Mat 2:11 ¶Ndipo pamene adafika m’nyumba, iwo adawona kamwanako kali ndi Mariya amayi wake, ndipo adagwa pansi, anamlambira iye: ndipo pamene anamasula chuma chawo, iwo anapereka kwa iye mphatso; golide, ndi lebano, ndi mure.
  38. Mat 2:12 Ndipo pochenjezedwa ndi Mulungu m’kulota kuti asabwerere kwa Herode, iwo adachoka kupita ku dziko lawo panjira ina.
  39. Mat 2:13 Ndipo pamene iwo ananyamuka, tawonani, mngelo wa Ambuye awonekera kwa Yosefe m’kulota, kunena kuti, Tawuka, ndipo utenge kamwanako ndi amayi ake, ndipo uthawire kulowa mu Igupto, ndipo iwe ukakhale kumeneko kufikira ine ndidzakuwuza iwe mawu: pakuti Herode adzafuna mwanayo kumuwononga iye.
  40. Mat 2:14 Ndipo iye atawuka, iye adatenga kamwana ndi amayi ake usiku, ndipo ananyamuka kulowa mu Igupto:
  41. Mat 2:15 Ndipo anakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode: kuti chikakwaniritsidwe chimene chinanenedwa cha Ambuye mwa mneneri, kunena kuti, Kutuluka ku Igupto ine ndayitana mwana wanga wamwamuna.
  42. Mat 2:16 ¶Kenaka Herode, pamene anawona kuti adapusitsidwa ndi anzeruwo, adapsa mtima kwambiri, ndipo anatumiza [ena], ndi kupha ana onse amene adali m’Betelehemu, ndi malire ake onse, kuyambira okwana zaka ziwiri ndi ochepera, monga mwa nthawi imene iye adafunsa mwakhama kwa anzeruwo.
  43. Mat 2:17 Pamenepo chidakwaniritsidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kunena kuti,
  44. Mat 2:18 Mu Rama mawu adamveka, a maliro, ndi kulira, ndi kubuma kwambiri, Rakele kulirira ana ake, ndipo wosafuna kuti atonthozedwe, chifukwa palibe iwo.
  45. Mat 2:19 ¶Koma Herode atamwalira, tawonani, mngelo wa Ambuye adawonekera m’kulota kwa Yosefe mu Igupto,
  46. Mat 2:20 Kunena kuti, Tawuka, ndipo utenge kamwana ndi amayi wake, ndipo upite ku dziko la Israyeli: pakuti adafa iwo amene amafuna moyo wake wa kamwanako.
  47. Mat 2:21 Ndipo iye adawuka, ndipo anatenga kamwana ndi amayi wake, ndipo anadza m’dziko la Israyeli.
  48. Mat 2:22 Koma pamene iye adamva kuti Arkalawosi adali kulamulira m’Yudeya m’malo mwa atate wake Herode, iye adachita mantha kupita kumeneko: osasamalira, pokhala wochenjezedwa ndi Mulungu m’kulota, iye adatembenukira mbali ina kulowa ku madera a Galileya:
  49. Mat 2:23 Ndipo iye adadza ndipo anakhazikika mu mzinda wotchedwa Nazarete: kuti chikakhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi aneneri, Iye adzatchedwa Mnazareni.
  50. Mat 3:1 M’masiku amenewo adadza Yohane M’batizi, analalikira m’chipululu cha Yudeya,
  51. Mat 3:2 Ndipo ananena, Tembenukani inu: pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.
  52. Mat 3:3 Pakuti uyu ndiye amene adanenedwayo ndi Yesaya mneneri, kunena kuti, Mawu a wofuwula m’chipululu, Konzani inu njira ya Ambuye, wongolani makwalala ake.
  53. Mat 3:4 Ndipo Yohane yemweyo adali nacho chovala chake cha ubweya wa ngamira, ndi lamba wa chikopa m’chiwuno mwake; ndipo chakudya chake chidali dzombe ndi uchi wa kuthengo.
  54. Mat 3:5 Pamenepo adatulukira kwa iye a ku Yerusalemu, ndi Yudeya yense, ndi dera lonse lozungulira Yordano,
  55. Mat 3:6 Ndipo adabatizidwa ndi iye mu Yordano, alikuvomereza machimo awo.
  56. Mat 3:7 ¶Koma pamene iye adawona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki alinkudza ku ubatizo wake, adati kwa iwo, Mbadwo wa njoka, ndani adakuchenjezani inu kuti muthawe ku mkwiyo umene udze?
  57. Mat 3:8 Choncho balani zipatso zakuyenera kulapa:
  58. Mat 3:9 Ndipo musamaganiza mwa inu nokha kunena, Ife tiri naye Abrahamu Atate [wathu]: pakuti ine ndinena kwa inu, kuti Mulungu ali nako kuthekera kwakuti mwa miyala iyi kuwukitsira ana kwa Abrahamu.
  59. Mat 3:10 Ndipo tsopano lino nkhwangwanso yayikidwa ku muzu wa mitengo: choncho mtengo uli wonse umene subala chipatso chabwino udulidwa, ndipo uponyedwa m’moto.
  60. Mat 3:11 Ine ndithu ndibatiza inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima: koma iye wakudza pambuyo panga, ali wamphamvu kuposa ine, amene nsapato zake ine sindiri woyenera kunyamula: iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera, ndi moto.
  61. Mat 3:12 Chokupizira chake [chili] m’dzanja lake, ndipo adzayeretsa bwino lomwe padwale pake, ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m’nkhokwe; koma adzatentha mankhusu ndi moto wosazimitsika.
  62. Mat 3:13 ¶Kenaka adza Yesu kuchokera ku Galileya kufika ku Yordano kwa Yohane, kuti adzabatizidwe ndi iye.
  63. Mat 3:14 Koma Yohane adamkaniza iye, kunena kuti, Ine ndiyenera kubatizidwa ndi inu, ndipo inu mudza kwa ine?
  64. Mat 3:15 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Talola [kuti zikhale motero] tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse. Pamenepo adamlola iye.
  65. Mat 3:16 Ndipo Yesu, pamene adabatizidwa, adakwera nthawi yomweyo kutuluka m’madzi: ndipo, onani, miyamba inatseguka kwa iye, ndipo adapenya Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda, ndikutera pa iye:
  66. Mat 3:17 Ndipo onani mawu akuchokera kumwamba, kunena kuti, Uyu ndi Mwana wanga wamwamuna wokondedwa, amene mwa iyeyu ine ndikondwera bwino.
  67. Mat 4:1 Kenaka Yesu adatsogozedwa ndi Mzimu kupita kulowa m’chipululu kuti akayesedwe ndi mdiyerekezi.
  68. Mat 4:2 Ndipo pemene iye adali atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, pambuyo pake iye adamva njala.
  69. Mat 4:3 Ndipo pamene woyesayo adafika kwa iye, iye anati, Ngati inu muli mwana wa wamwamuna wa Mulungu, lamulirani kuti miyala iyi isanduke mkate.
  70. Mat 4:4 Koma iye adayankha ndipo anati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma mwa mawu onse wotuluka m’kamwa mwa Mulungu.
  71. Mat 4:5 Kenaka mdiyerekezi amtengera iye kukwera ku mzinda woyerawo; ndipo anamuyika iye pamwamba pa nsonga ya denga la kachisi,
  72. Mat 4:6 Ndipo anati kwa iye, Ngati muli Mwana wamwamuna wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu: ndipo m’manja [mwawo] iwo adzakunyamulani inu, kuti mwina pa nthawi ina iliyonse inu mungagunde phazi lanu ku mwala.
  73. Mat 4:7 Yesu adanena kwa iye, Ndipo kwalembedwanso, Iwe sudzayesa Ambuye Mulungu wako.
  74. Mat 4:8 Kenanso, mdiyerekezi anamtengera iye ku phiri lalitali koposa, ndipo anamuwonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wa iwo;
  75. Mat 4:9 Ndipo anena kwa iye, Zinthu zonse izi ine ndidzakupatsani inu, ngati inu mudzagwa pansi ndikundilambira ine.
  76. Mat 4:10 Kenaka Yesu anena kwa iye, Choka iwe pano, Satana: pakuti kwalembedwa, Iwe udzalambira Ambuye Mulungu wako, ndipo iye yekha iwe udzamtumikira.
  77. Mat 4:11 Kenaka m’diyerekezi amsiya iye, ndipo, tawonani, angelo adadza ndi kutumikira kwa iye.
  78. Mat 4:12 ¶Tsopano pamene Yesu adamva kuti Yohane adaponyedwa m’ndende, iye adanyamuka napita kulowa m’Galileya;
  79. Mat 4:13 Ndi kuchoka ku Nazarete, iye anadza ndi kukhalitsa m’Kaperenamu, amene ali wa dera la m’mbali mwa nyanja, m’malire a Zebuloni ndi Nafutalim,
  80. Mat 4:14 Kuti chikakhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi Yesaya mneneri, kunena kuti,
  81. Mat 4:15 Dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutalim, [m’mbali mwa] njira ya kunyanja, kupitirira Yordano, Galileya wa Amitundu;
  82. Mat 4:16 Anthu amene adakhala pansi mu mdima adawona kuwala kwakukulu; ndi kwa iwo amene adakhala m’malo a mthunzi wa imfa kuwala kwawatumphukira.
  83. Mat 4:17 ¶Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kulalikira, ndi kunena kuti, Tembenukani: pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.
  84. Mat 4:18 ¶Ndipo Yesu, akuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, adawona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andereya mbale wake, alikuponya khoka m’nyanja: pakuti adali asodzi.
  85. Mat 4:19 Ndipo iye anena kwa iwo, Nditsateni ine, ndipo ine ndidzakupangani inu [kukhala] asodzi a anthu.
  86. Mat 4:20 Ndipo iwo pomwepo adasiya makhoka [awo], namtsata iye.
  87. Mat 4:21 Ndipo ponyamuka kuchoka pamenepo, iye adawona abale ena awiri, Yakobo [mwana wamwamuna] wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wake, mu ngalawa pamodzi ndi Zebedayo atate wawo, alikukonza [mowonongeka mwa] makhoka awo; ndipo iye adawayitana iwo.
  88. Mat 4:22 Ndipo posakhalitsa adasiya ngalawayo ndi atate wawo; ndipo anamtsata iye.
  89. Mat 4:23 ¶Ndipo Yesu adayendayenda mu Galileya monse, kuphunzitsa mu masunagoge mwawo, ndi kulalikira uthenga wabwino wa ufumu, ndi kuchiritsa kudwala kwa mitundu yonse ndi matenda a mitundu yonse pakati pa anthu.
  90. Mat 4:24 Ndipo kutchuka kwake kunabuka ku Siriya konse: ndipo iwo adabweretsa kwa iye anthu onse wodwala amene adali wogwidwa ndi matenda a mitundumitundu ndi mazunzo, ndi iwo amene adali wogwidwa ndi mizimu yoyipa, ndi iwo amene anali akhunyu, ndi iwo amene anali akufa ziwalo; ndipo iye adawachiritsa iwo.
  91. Mat 4:25 Ndipo lidamtsata khamu lalikulu la anthu wochokera ku Galileya, ndi [wochokera] ku Dekapolisi, ndi [wochokera] ku Yerusalemu, ndi [wochokera] ku Yudeya, ndi [wochokera] kupitirira Yordano.
  92. Mat 5:1 Ndipo pakuwona makamu, iye adapita kukwera m’phiri: ndipo m’mene iye adakhala pansi, wophunzira ake adadza kwa iye.
  93. Mat 5:2 Ndipo iye adatsegula pakamwa pake, ndipo anawaphunzitsa iwo; kunena kuti;
  94. Mat 5:3 Odala [ali] wosawuka mu mzimu: pakuti uli wawo ufumu wa kumwamba.
  95. Mat 5:4 Odala [ali] iwo amene alira: pakuti iwo adzatonthozedwa.
  96. Mat 5:5 Odala [ali] wofatsa: pakuti adzalandira dziko lapansi.
  97. Mat 5:6 Odala [ali] iwo amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo: pakuti adzakhutitsidwa.
  98. Mat 5:7 Odala [ali] achifundo: pakuti adzalandira chifundo.
  99. Mat 5:8 Odala [ali] woyera mtima: pakuti adzawona Mulungu.
  100. Mat 5:9 Odala [ali] akuchita mtendere: pakuti adzatchedwa ana a Mulungu.
  101. Mat 5:10 Odala [ali] iwo akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: pakuti wawo uli ufumu wa kumwamba.
  102. Mat 5:11 Odala muli inu, m’mene [anthu] adzanyazitsa inu, ndi kuzunza [inu], ndipo adzanena zoyipa monama za mitundu yonse kwa inu, chifukwa cha ine.
  103. Mat 5:12 Kondwerani, ndipo sangalalani kopambana: pakuti mphotho yanu [ndi] yayikulu kumwamba: pakuti motero iwo adazunza aneneri amene adakhalawo musadabadwe inu.
  104. Mat 5:13 ¶Inu muli mchere wa dziko lapansi: koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukoleretsa ndi chiyani? Kuyambira pamenepo ukhala wopanda kanthu ka ubwino kalikonse, koma kuti ukaponyedwe kunja, ndi kuti upondedwe pansi pa mapazi a anthu.
  105. Mat 5:14 Inu muli kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda umene uli wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.
  106. Mat 5:15 Kapena anthu sayatsa nyali nayiyika pansi pa mbiya, koma amayiyika iyo pa choyikapo chake; ndipo imawunikira kwa onse amene ali m’nyumbamo.
  107. Mat 5:16 Chomwecho kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu, kuti iwo akhoze kuwona ntchito zanu zabwino, ndi kulemekeza Atate wanu amene ali kumwamba.
  108. Mat 5:17 ¶Musaganize kuti ndidadza ine kudzapasula chilamulo, kapena aneneri: ine sindinadza kudzapasula, koma kukwaniritsa.
  109. Mat 5:18 Pakuti ndithudi ine ndinena kwa inu, Kufikira kumwamba ndi dziko zitapita, kalemba kakang’ono kamodzi kapena kansonga kamodzi sikadzachoka mwa njira iliyonse kuchilamulo, kufikira zonse zitakwaniritsidwa.
  110. Mat 5:19 Choncho wina aliyense adzaphwanya limodzi la malamulo ang’onong’ono amenewa, ndipo adzaphunzitsa anthu chomwecho, iye adzatchulidwa wamng’onong’ono mu ufumu wa kumwamba: koma wina aliyense wochita ndi kuphunzitsa [iwo], yemweyu adzatchulidwa wamkulu mu ufumu wa kumwamba.
  111. Mat 5:20 Pakuti ine ndinena kwa inu, Kuti pokhapokha chilungamo chanu chidzachuluka kuposa [chilungamo] cha alembi ndi Afarisi, inu simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.
  112. Mat 5:21 ¶Inu mwamva kuti kudanenedwa ndi iwo a nthawi yakale, Iwe usaphe; ndipo wina aliyense akadzapha adzakhala wopalamula mlandu wakuweruzidwa:
  113. Mat 5:22 Koma ine ndinena kwa inu; Kuti aliyense amene wakwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu woweruzidwa: ndipo aliyense amene adzanena kwa mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma aliyense amene adzati, Chitsiru iwe; adzakhala wopalamula nyanja ya moto.
  114. Mat 5:23 Choncho ngati iwe ubweretsa mphatso yako pa guwa, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi chifukwa ndi iwe;
  115. Mat 5:24 Usiye pomwepo mphatso yako patsogolo pa guwa, ndipo upite pa njira yako; poyamba uyanjanitsidwe kwa mbale wako, ndipo kenaka idza ndipo upereke mphatso yako.
  116. Mat 5:25 Uyanjane ndi wozengana naye mlandu mofulumira, pamene uli panjira pamodzi ndi iye; kuti mwina pa nthawi ina iliyonse wozengana naye mlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msirikari, ndipo iwe uponyedwe m’ndende.
  117. Mat 5:26 Ndithudi ndithudi ndinena kwa iwe, Iwe sudzatulukamo konse m’menemo, kufikira utalipira kandalama kalikonse komalizira.
  118. Mat 5:27 ¶Inu mwamva kuti kudanenedwa ndi iwo a nthawi yakale, Iwe usachite chigololo:
  119. Mat 5:28 Koma ine ndinena kwa inu, Kuti aliyense woyang’ana pa mkazi momkhumba iye wachita naye kale chigololo mumtima mwake.
  120. Mat 5:29 Ndipo ngati diso lako lamanja likuchimwitsa iwe, ulikolowole, ndipo ulitaye [ilo] kulichotsa kwa iwe: pakuti kuli kopindulitsa kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chiwonongeke, ndipo osati [kuti] thupi lako lonse liponyedwe mu nyanja ya moto.
  121. Mat 5:30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa iwe, ulidule, ndipo ulitaye [ilo] kulichotsa kwa iwe: pakuti kuli kopindulitsa kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chiwonongeke, ndi [kuti] thupi lako lonse lisaponyedwe mu nyanja ya moto.
  122. Mat 5:31 Kwanenedwa, Aliyense amene adzachotsa mkazi wake, ampatse iye kalata ya chilekaniro:
  123. Mat 5:32 Koma ine ndinena kwa inu, Kuti aliyense amene adzachotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chiwerewere, ampangitsa iye kuti achite chigololo: ndipo aliyense amene adzakwatira iye amene wachotsedwayo achita chigololo.
  124. Mat 5:33 ¶Kenanso, inu mwamva kuti kwanenedwa ndi iwo a nthawi yakale, Iwe usadzilumbire wekha, koma udzachita kwa Ambuye malumbiro ako:
  125. Mat 5:34 Koma ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse; kapena mwa [kutchula] kumwamba; chifukwa uli mpando wachifumu wa Mulungu:
  126. Mat 5:35 Kapena mwa [kutchula] dziko lapansi; pakuti liri lopondapo mapazi ake: kapena mwa [kutchula] Yerusalemu, pakuti ndi mzinda wa Mfumu yayikulu.
  127. Mat 5:36 Kapena usalumbire pa mutu wako, chifukwa iwe sungathe kuliyeretsa mbuu tsitsi limodzi kapena kulidetsa bii.
  128. Mat 5:37 Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi: pakuti chilichonse choposera izi chichokera kwa woyipayo.
  129. Mat 5:38 ¶Inu mwamva kuti kwanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:
  130. Mat 5:39 Koma ine ndinena kwa inu, Kuti inu musakaniza choyipa: koma aliyense amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire iye linalonso.
  131. Mat 5:40 Ndipo ngati munthu adzafuna kupita nawe kumlandu, ndi kutenga malaya ako, umlolezenso atengenso chovala pamwamba [chako].
  132. Mat 5:41 Ndipo aliyense amene adzakukakamiza kumperekeza ulendo wamtunda umodzi, upite ndi iye mitunda iwiri.
  133. Mat 5:42 Umpatse iye amene akupempha iwe, ndipo kwa iye amene afuna kukongola kwa iwe usambweze.
  134. Mat 5:43 ¶Inu mwamva kuti kwanenedwa, Iwe uzikondana ndi woyandikana naye, ndi kumuda mdani wako.
  135. Mat 5:44 Koma ine ndinena kwa inu, Muwakonde adani anu, dalitsani iwo akutemberera inu, chitirani zabwino kwa iwo akuda inu, ndi kupempherera iwo amene akukugwiritsani inu ntchito monyazitsa, ndi kukuzunzani inu;
  136. Mat 5:45 Kuti inu mukakhale ana a Atate wanu amene ali kumwamba: pakuti iye amatulutsira dzuwa lake pa woyipa ndi abwino, ndipo avumbitsira mvula pa wolungama ndi pa wosalungama.
  137. Mat 5:46 Pakuti ngati inu mukonda iwo amene akonda inu, ndi mphotho yanji muli nayo inu? Kodi angakhale anthu okhometsa misonkho sachita chomwecho?
  138. Mat 5:47 Ndipo ngati muchitira ulemu abale anu wokha, muchita chiyani inu [choposa ena]? Kodi angakhale anthu okhometsa misonkho sachita chomwecho?
  139. Mat 5:48 Choncho mukhale inu angwiro, monga Atate wanu amene ali kumwamba ali wangwiro.
  140. Mat 6:1 Yang’anirani kuti musachite za chifundo zanu pamaso pa anthu, kuti muwonekere kwa iwo: apo ayi inu mulibe mphotho ndi Atate wanu wa kumwamba.
  141. Mat 6:2 Choncho pamene upatsa mphatso za chifundo [zako], usamawomba lipenga pamaso pako, monga amachita onyenga m’masunagoge ndi m’makwalala, kotero kuti alandire ulemerero wa anthu, Ndithudi ndinena kwa inu, Iwo ali nazo mphotho zawo.
  142. Mat 6:3 Koma pamene iwe upatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene dzanja lako lamanja lichita:
  143. Mat 6:4 Kuti mphatso zako zachifundo zikhale za mseri: ndipo Atate wako amene awona mwa mseri iye mwini adzakupatsa mphotho mowonekera.
  144. Mat 6:5 ¶Ndipo pamene iwe upemphera, iwe usakhale monga momwe wonyengawo [ali]: pakuti iwo akonda kupemphera choyimirira m’masunagoge ndi pa mphambano za makwalala, kuti akhoze kuwonedwa ndi anthu. Ndithudi ndinena kwa inu, Iwo ali nazo mphotho zawo.
  145. Mat 6:6 Koma iwe, pomwe upemphera, lowa m’kachipinda kako, ndipo pamene iwe watseka chitseko chako, upemphere kwa Atate wako amene ali mseri; ndipo Atate wako amene awona mseri adzakupatsa mphotho mowonekera.
  146. Mat 6:7 Koma pamene iwe upemphera, usabwerezebwereze mwachabe iyayi, monga [amachita] achikunja: pakuti aganiza kuti iwo adzamvedwa ndi kuyankhula kwawo kwambiri.
  147. Mat 6:8 Choncho inu musafanane ndi iwo ayi: pakuti Atate wanu adziwa zinthu zomwe muzisowa, musadayambe inu kupempha iye.
  148. Mat 6:9 Choncho pempherani inu mu njira iyi: Atate wathu amene muli kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
  149. Mat 6:10 Ufumu wanu udze. Chifuniro chanu chichitidwe pansi pano, monga [chili] kumwamba.
  150. Mat 6:11 Mutipatse ife lero mkate wathu wa tsiku ndi tsiku.
  151. Mat 6:12 Ndipo mutikhululukire ife mangawa athu, monga ifenso tiwakhululukira amangawa athu.
  152. Mat 6:13 Ndipo musatitengere ife mu mayesero, koma mutipulumutse ife kwa woyipayo: Pakuti wanu uli ufumu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ku nthawi zonse. Amen.
  153. Mat 6:14 Pakuti ngati mukhululukira anthu zochimwa zawo, Atate wanu wa kumwamba adzakhululukiranso inu:
  154. Mat 6:15 Koma ngati simukhululukira anthu zochimwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.
  155. Mat 6:16 ¶Kuwonjezera apo pamene inu musala kudya, musakhale, ngati wonyengawo, ndi nkhope ya chisoni: pakuti ayipitsa nkhope zawo, kuti awonekere kwa anthu kuti alikusala kudya. Ndithudi ndinena kwa inu, Iwo ali nazo mphotho zawo.
  156. Mat 6:17 Koma iwe, pamene usala kudya, dzoza mafuta mutu wako; ndi kusamba nkhope yako;
  157. Mat 6:18 Kuti iwe usawonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma Atate wako amene ali mseri: ndipo Atate wako, amene awona mseri, adzakubwezera mphotho iwe mowonekera.
  158. Mat 6:19 ¶Musadzikundikira nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zichiwononga, ndi pamene mbala zibowola ndi kuba:
  159. Mat 6:20 Koma mudzikundikire nokha chuma kumwamba, kumene kadziwotche kapena dzimbiri siziwononga, ndi kumene mbala sizibowola ndi kuba:
  160. Mat 6:21 Pakuti kumene kuli chuma chako, komweko mtima wako udzakhalanso.
  161. Mat 6:22 Nyali ya thupi ndi diso: choncho ngati diso lako liri langwiro, thupi lako lonse lidzakhala lodzala ndi kuwunika.
  162. Mat 6:23 Koma ngati diso lako liri loyipa, thupi lako lonse lidzakhala lodzala ndi mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo [uli] waukulu motani!
  163. Mat 6:24 ¶Palibe munthu angathe kutumikira ambuye awiri: pakuti kapena adzamuda m’modziyo, ndi kukonda winayo; kapena adzakangamira kwa m’modziyo, ndi kunyoza winayo. Inu simungatumikire Mulungu ndi [kutumikiranso] chuma.
  164. Mat 6:25 Choncho ine ndinena kwa inu, Musadere nkhawa za moyo wanu, chimene inu mudzadya, kapena chimene mudzamwa; kapena tsono za thupi lanu; chimene inu mudzavala. Kodi moyowo si uli woposa chakudya, ndi thupi [liposa] chovala?
  165. Mat 6:26 Tawonani mbalame za mlengalenga: pakuti izo sizimafesa ayi, kapena sizimakolola ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; koma Atate wanu wa kumwamba azidyetsa izo. Si muli inu woposa izo kodi?
  166. Mat 6:27 Ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuwonjezera phazi ndi theka ku msinkhu wake?
  167. Mat 6:28 Ndipo inu muderanji nkhawa ndi chovala? Talingalirani za maluwa a kuthengo, momwe akulira; iwo sagwira ntchito, kapena iwo sapota:
  168. Mat 6:29 Ndipo tsono ine ndinena kwa inu, Kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sadavala monga limodzi la awa.
  169. Mat 6:30 Mwa ichi ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, umene ukhala lero, ndi mawa uponyendwa pamoto, [nanga iye] mopambana koposa ndithu [sadzakuvekani] inu, Inu a chikhulupiriro chaching’ono?
  170. Mat 6:31 Choncho musaganizire, kunena kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Kodi ife tidzakhala wovekedwa ndi chiyani?
  171. Mat 6:32 (Pakuti zinthu izi zonse Amitundu azifunafuna:) pakuti Atate wanu wa kumwamba adziwa kuti inu musowa zinthu izi zonse.
  172. Mat 6:33 Koma mufunefune inu poyamba ufumu wa Mulungu, ndi chilungamo chake; ndipo zinthu izi zonse zidzawonjezedwa kwa inu.
  173. Mat 6:34 Choncho musadere nkhawa za mawa: pakuti mawa lidzadera nkhawa pa zinthu za ilo lokha. Zokwanira ku tsiku [ndi] zoyipa za tsikulo.
  174. Mat 7:1 Musaweruze, kuti inu musaweruzidwe.
  175. Mat 7:2 Pakuti ndi kuweruza kumene inu muweruza nako, inu mudzaweruzidwa: ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, udzayesedwa kwa inunso.
  176. Mat 7:3 Ndipo chifukwa chiyani iwe upenya kafumbi kamene kali m’diso la mbale wako, koma siulingalira chipika chimene chili m’diso la iwe mwini?
  177. Mat 7:4 Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ine ndichotse kafumbi m’diso lako; ndipo, tawona, chipika chili m’diso la iwe mwini.
  178. Mat 7:5 Wonyenga iwe, tayamba kuchotsa chipika m’diso la iwe mwini; ndipo kenaka udzapenya bwino lomwe kutaya kunja kafumbi [kali] m’diso la mbale wako.
  179. Mat 7:6 ¶Musamapatsa chimene chili chopatulika kwa agalu, kapena kuponya inu ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti mwina zingapondereze pansi pa mapazi awo, ndi kutembenukanso ndi kung’amba inu.
  180. Mat 7:7 ¶Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu:
  181. Mat 7:8 Pakuti aliyense amene apempha alandira; ndi iye amene afunafuna apeza; ndi kwa iye amene agogoda chidzatsegulidwa.
  182. Mat 7:9 Kapena bambo ndani alipo mwa inu, amene mwana wake wamwamuna apempha mkate, kodi adzampatsa iye mwala?
  183. Mat 7:10 Kapena ngati iye apempha nsomba, kodi adzampatsa iye njoka?
  184. Mat 7:11 Ngati inu tsono, wokhala woyipa, mudziwa kupatsa mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani nanga Atate wanu amene ali kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo amene amupempha iye?
  185. Mat 7:12 Choncho zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achite kwa inu, muchite inunso motero kwa iwo: pakuti ichi ndicho chilamulo ndi aneneri.
  186. Mat 7:13 ¶Lowani inu pa chipata chopapatiza: chifukwa chipata [chili] chachikulu, ndi njira [ili] yotakata, imene ipita ku chiwonongeko; ndipo alipo ambiri amene alowa pa iyo:
  187. Mat 7:14 Chifukwa chipata [chili] chopapatiza, ndipo [ili] yochepa njirayo, imene ipita ku moyo, ndipo wochepa alipo amene ayipeza iyo.
  188. Mat 7:15 ¶Chenjerani ndi aneneri wonyenga, amene adza kwa inu mu zovala za nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yakung’amba.
  189. Mat 7:16 Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu atchera mphesa pa minga, kapena nkhuyu pa mtula?
  190. Mat 7:17 Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa chipatso chabwino; koma mtengo wovunda upatsa chipatso choyipa.
  191. Mat 7:18 Mtengo wabwino sungathe kupatsa chipatso choyipa, kapena [siungathe] mtengo wovunda kupatsa chipatso chabwino.
  192. Mat 7:19 Mtengo uliwonse umene supatsa chipatso chabwino udulidwa, ndipo utayidwa m’moto.
  193. Mat 7:20 Mwa ichi ndi zipatso zawo inu mudzawazindikira iwo.
  194. Mat 7:21 ¶Si aliyense amene anena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu ufumu wa kumwamba; koma iye amene achita chifuniro cha Atate wanga amene ali kumwamba.
  195. Mat 7:22 Ambiri adzati kwa ine tsiku limenero, Ambuye, Ambuye, kodi ife sitidanenera m’dzina lanu? Ndipo m’dzina lanu kutulutsa mizimu yoyipa? Ndipo m’dzina lanu kuchita zodabwitsa zamphamvu zambiri?
  196. Mat 7:23 Ndipo kenaka ine ndidzanena kwa iwo, Ine sindinakudziwani inu: chokani kwa ine, inu wochita kusaweruzika.
  197. Mat 7:24 ¶Choncho aliyense amene amva zonena izi za ine, ndi kuzichita izo, ine ndidzamfananiza iye kwa munthu wochenjera, amene adamanga nyumba yake pa thanthwe:
  198. Mat 7:25 Ndipo mvula idagwa, ndipo madzi anasefukira, ndipo mphepo zidawomba, ndipo zinagunda pa nyumbayo; ndipo siyidagwa ayi; pakuti idakhazikika pa maziko a pa thanthwe.
  199. Mat 7:26 Ndipo aliyense amene amva zonena izi za ine, ndi kusazichita izo, adzafananizidwa kwa munthu wopusa, amene adamanga nyumba yake pa mchenga:
  200. Mat 7:27 Ndipo mvula idagwa, ndipo madzi anasefukira, ndipo mphepo zidawomba, ndipo zinagunda pa nyumbayo; ndipo idagwa: ndipo kugwa kwa iyo kudali kwakukulu.
  201. Mat 7:28 Ndipo kudachitika, pamene Yesu adamaliza zonena izi, anthuwo adazizwa pa chiphunzitso chake:
  202. Mat 7:29 Pakuti iye adawaphunzitsa iwo monga [iye] wokhala nawo ulamuliro, wosati monga alembiwo.
  203. Mat 8:1 Pamene iye adatsika kuchoka pa phiripo, makamu akulu adamtsata iye.
  204. Mat 8:2 Ndipo, tawonani, panadza wakhate ndipo anamlambira iye, nanena kuti, Ambuye, ngati inu mufuna, inu mungathe kundiyeretsa ine.
  205. Mat 8:3 Ndipo Yesu adatambasula dzanja [lake], ndipo anamkhudza iye, nanena kuti, Ine ndifuna; iwe yeretsedwa. Ndipo posakhalitsa khate lake lidayeretsedwa.
  206. Mat 8:4 Ndipo Yesu adanena kwa iye, Iwe uwone kuti usawuze munthu; koma pita pa njira yako, udziwonetsere wekha kwa wansembe, ndipo upereke mphatso imene Mose adayilamulira, chifukwa cha umboni kwa iwo.
  207. Mat 8:5 ¶Ndipo m’mene Yesu adalowa mu Kaperenamu, panadza kwa iye kenturiyoni, kumpempha iye,
  208. Mat 8:6 Ndipo adati, Ambuye, wantchito wanga ali gone m’nyumba kudwala matenda akufa ziwalo, wozunzidwa kwambiri.
  209. Mat 8:7 Ndipo Yesu adanena kwa iye, Ine ndidzafika ndikumchiritsa iye.
  210. Mat 8:8 Kenturiyoni adayankha ndipo anati, Ambuye, ine sindiri woyenera kuti mudze kulowa pansi pa denga langa: koma nenani mawu wokha, ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa.
  211. Mat 8:9 Pakuti ine ndine munthu wapansi pa ulamuliro, wokhala nawo asilikari a pansi pa ine: ndipo ine ndimanena kwa [munthu] uyu, Pita, ndipo iye apita; ndi kwa wina, Idza, ndipo iye adza; ndi kwa wantchito wanga, Chita ichi, ndipo iye achita [icho].
  212. Mat 8:10 Pamene Yesu adamva [ichi], iye adazizwa, ndipo anati kwa iwo amene amatsatira, Ndithudi ndinena kwa inu, Ine sindidapeza chikhulupiriro chachikulu chotere, ayi, ngakhale mu Israyeli.
  213. Mat 8:11 Ndipo ine ndinena kwa inu, Kuti ambiri adzafika kuchokera kum’mawa ndi kumadzulo, ndipo adzakhala pansi pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu ufumu wa kumwamba.
  214. Mat 8:12 Koma anawo a ufumu adzatayidwa ku mdima wakunja: kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
  215. Mat 8:13 Ndipo Yesu adati kwa kenturiyoniyo, Pita pa njira yako; ndipo monga iwe wakhulupirira, [kotero] kuchitike kwa iwe. Ndipo wantchito wakeyo adachiritsidwa ora lomwero.
  216. Mat 8:14 ¶Ndipo pamene Yesu adafika m’nyumba ya Petro, iye adawona amayi a mkazi wake wa Petro ali gone, akudwala kutentha kwa thupi.
  217. Mat 8:15 Ndipo iye adakhudza dzanja lake, ndipo kutentha kwa thupi kudam’leka iye: ndipo iye adawuka, ndipo anatumikira kwa iwo.
  218. Mat 8:16 ¶Ndipo pamene anadza madzulo, iwo anabwera nawo kwa iye ambiri amene anali wogwidwa ndi mizimu yoyipa: ndipo iye adatulutsa mizimiyo ndi mawu [ake], ndipo anachiritsa onse amene anali wodwala:
  219. Mat 8:17 Kuti chikhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi Yesaya mneneri, kunena kuti, Iye yekha adatenga zofowoka zathu, ndipo ananyamula nthenda [zathu].
  220. Mat 8:18 ¶Tsopano pamene Yesu anawona makamu akulu a anthu womuzungulira iye, iye adapereka lamulo kuti anyamuke kupita ku tsidya lina.
  221. Mat 8:19 Ndipo mlembi wina adadza, ndipo anati kwa iye, Ambuye, ine ndidzakutsatani inu kulikonse inu mupita.
  222. Mat 8:20 Ndipo Yesu anena kwa iye, Nkhandwe ziri ndi mayenje, ndi mbalame za mlengalenga [ziri ndi] zisa; koma Mwana wamwamuna wa munthu alibe pomwe angagoneke mutu [wake].
  223. Mat 8:21 Ndipo wina wa wophunzira ake adati kwa iye, Ambuye, mundilole ine ndiyambe ndapita ndi kuyika maliro a atate wanga.
  224. Mat 8:22 Koma Yesu adanena kwa iye, Tsata ine; ndipo uleke akufa ayike [m’manda] akufa awo.
  225. Mat 8:23 ¶Ndipo pamene iye adalowa m’chombo, wophunzira ake adamtsata iye.
  226. Mat 8:24 Ndipo, tawonani, padawuka namondwe wamkulu panyanja, motero mwakuti chombo chidaphimbidwa ndi mafunde: koma iye adali m’tulo.
  227. Mat 8:25 Ndipo wophunzira ake adadza kwa [iye], ndipo anamudzutsa iye, nanena kuti, Ambuye, tipulumutseni ife: tikuwonongeka ife.
  228. Mat 8:26 Ndipo iye anena kwa iwo, Kodi inu muli ndi mantha bwanji, Inu a chikhulupiriro chaching’ono? Kenaka iye adadzuka, ndipo anadzudzula mphepo ndi nyanja; ndipo padali bata lalikulu.
  229. Mat 8:27 Koma anthuwo adazizwa, nanena kuti, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera iye!
  230. Mat 8:28 ¶Ndipo pamene adafika iye kutsidya lina m’dziko la Ageregesene, padakomana naye awiri wogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, awukali kopambana, kotero kuti munthu aliyense sankatha kupitapo panjira imeneyo.
  231. Mat 8:29 Ndipo, tawonani, iwo adafuwula, nanena kuti, Kodi ife tiri ndi chochita chotani ndi inu, Yesu, inu Mwana wamwamuna wa Mulungu? Kodi mwadza kuno kutizunza ife nthawi yake isadafike?
  232. Mat 8:30 Ndipo padali patali kuchokera kwa iwo gulu la nkhumba zambiri zirinkudya.
  233. Mat 8:31 Ndipo mizimu yoyipayo idampempha iye, ninena kuti, Ngati inu mutitulutsa ife, mutilole ife kuti tilowe m’gulu la nkhumbazo.
  234. Mat 8:32 Ndipo iye adati kwa iyo, Pitani. Ndipo pamene idatuluka, inapita kukalowa mu nkhumbazo: ndipo, tawonani, gulu lonse la nkhumba lidathamangira mwachiwawa kunsi kotsetsereka kozama kulowa m’nyanjamo, ndipo zidafa m’madzimo.
  235. Mat 8:33 Ndipo iwo amene amaziweta izo adathawa, ndipo anapita pa njira zawo kulowa mu mzinda, ndipo ananena chilichonse, ndi zomwe zidachitikira kwa ogwidwa ndi ziwanda aja.
  236. Mat 8:34 Ndipo, tawonani, mzinda wonse udatuluka kukakumana naye Yesu: ndipo m’mene iwo adamuwona iye, iwo adampempha [iye] kuti anyamuke kutuluka m’malire awo.
  237. Mat 9:1 Ndipo iye adalowa m’chombo, ndipo anawoloka, ndipo anafika ku mzinda wa kwawo.
  238. Mat 9:2 Ndipo, tawonani, adabwera naye kwa iye munthu wamwamuna wodwala matenda akufa ziwalo, wogona pa kama: ndipo Yesu pakuwona chikhulupiriro chawo adati kwa wodwala matenda akufa ziwaloyo; Mwana wamwamuna, khala wokondwera; machimo ako akhululukidwira iwe.
  239. Mat 9:3 Ndipo, tawonani, ena mwa alembi adanena mwa iwo wokha, [Munthu] uyu anena zonyoza [Mulungu].
  240. Mat 9:4 Ndipo Yesu podziwa maganizo awo adati, Mwa ichi muli kuganizira inu zoyipa m’mitima yanu?
  241. Mat 9:5 Pakuti chapafupi n’chiti, kunena kuti, Machimo [ako] akhululukidwira iwe; kapena kunena kuti, Tanyamuka, ndipo uyende?
  242. Mat 9:6 Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wamwamuna wa munthu ali nazo mphamvu pansi pano za kukhululukira machimo, (kenaka adanena kwa wodwala matenda akufa ziwaloyo,) Tadzuka, tenga kama wako, ndipo upite ku nyumba kwako.
  243. Mat 9:7 Ndipo iye adadzuka, ndipo ananyamuka kupita kunyumba kwake.
  244. Mat 9:8 Koma pamene makamu adawona [ichi], iwo adazizwa, ndipo analemekeza Mulungu, yemwe adapereka mphamvu yotere kwa anthu.
  245. Mat 9:9 ¶Ndipo Yesu pamene amadutsa kuchokera kumeneko, iye adawona munthu, wotchedwa Mateyu, atakhala pamalo polandirira msonkho: ndipo iye anena kwa iye, Nditsate ine. Ndipo iye adanyamuka, ndipo anatsatira.
  246. Mat 9:10 ¶Ndipo kudachitika, pamene Yesu adakhala pa chakudya m’nyumbayo, tawonani amisonkho ndi wochimwa ambiri adadza nakhala pansi pamodzi ndi iye ndi wophunzira ake,
  247. Mat 9:11 Ndipo pamene Afarisi adawona [ichi], adanena kwa wophunzira ake, Chifukwa chiyani Ambuye wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi wochimwa?
  248. Mat 9:12 Ndipo m’mene Yesu adamva [izi], adati kwa iwo, Iwo amene ali wolimba safuna dotolo ayi, koma iwo amene ali wodwala.
  249. Mat 9:13 Koma pitani ndipo muphunzire chimene [ichi] chitanthawuza, Ine ndifuna chifundo, osati nsembe ayi: pakuti ine sindinadza kudzayitana wolungama, koma wochimwa kukulapa.
  250. Mat 9:14 ¶Kenaka adadza kwa iye wophunzira ake a Yohane, nanena kuti, Chifukwa chiyani ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma wophunzira anu sasala?
  251. Mat 9:15 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Angathe ana a nyumba ya ukwati kulira, pa nthawi yonse imene mkwati ali ndi iwo? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo nthawi imeneyo iwo adzasala kudya.
  252. Mat 9:16 Palibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yatsopano ku chovala chakale, pakuti chimene chayikidwamo kuti chitsekepo chizomola kuchotsa ku chovalacho, ndipo pozomokapo padzakhala papakulu.
  253. Mat 9:17 Kapena anthu sathira vinyo watsopano m’mabotolo aziikopa akale: kapena atatero mabotolo azikopawo asweka, ndipo vinyoyo atayika, ndipo mabotolo azikopawo awonongeka: koma amathira vinyo watsopano m’mabotolo azikopa atsopano, ndipo zonse ziwiri zisungika.
  254. Mat 9:18 ¶M’mene iye adali kuyankhula zinthu zimenezo kwa iwo, tawonani, adadza wolamulira wina, ndipo anamlambira iye, nanena kuti, Mwana wanga wamkazi tsopano wamwalira: komatu mubwere ndi kuyika dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.
  255. Mat 9:19 Ndipo Yesu adanyamuka, ndipo anamtsata iye, ndipo [anateronso] wophunzira ake.
  256. Mat 9:20 ¶Ndipo, tawonani, mkazi, amene adadwala nthenda yokha mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo [pake], ndipo anakhudza mopindira mwa chovala chake:
  257. Mat 9:21 Pakuti iye adanena mwa iye yekha, Koma ngati ine ndikhoza kukhudza chovala chake, ine ndidzachira.
  258. Mat 9:22 Koma Yesu adatembenuka, ndipo pamene anamuwona iye, iye adati, Mwana wamkaziwe khala wokondwera; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe. Ndipo mkaziyo adachira kuyambira ora lomwero.
  259. Mat 9:23 Ndipo pamene Yesu analowa m’nyumba yake ya wolamulirayo, ndi kuwona woyimba zitoliro ndi anthu akupanga phokoso.
  260. Mat 9:24 Iye adanena kwa iwo, Tulukani: pakuti kabuthuko sikanafe, koma kali m’tulo. Ndipo iwo adamseka iye monyoza.
  261. Mat 9:25 Koma pamene anthuwo adatulutsidwa, iye adalowamo, ndipo anamtenga iye pomugwira pa dzanja, ndipo kabuthuko kadawuka.
  262. Mat 9:26 Ndipo mbiri yake ya pamenepa idabuka kutali m’dziko lonse limenero.
  263. Mat 9:27 ¶Ndipo pamene Yesu adanyamuka kumeneko, anthu awiri akhungu adamtsata iye, akufuwula, ndi kunena kuti, [Inu] mwana wamwamuna wa Davide, mutichitire chifundo ife.
  264. Mat 9:28 Ndipo m’mene iye adalowa m’nyumbamo, anthu akhunguwo adadza kwa iye: ndipo Yesu adati kwa iwo, Mukhulupirira inu kodi kuti ine ndingathe kuchita ichi? Iwo adanena kwa iye, Inde, Ambuye.
  265. Mat 9:29 Kenaka iye adakhudza maso awo, kunena kuti, Monga mwa chikhulupiriro chanu zikhale kwa inu.
  266. Mat 9:30 Ndipo maso awo adatseguka; ndipo Yesu adawawuzitsa iwo, nanena kuti, Muwonetsetse [kuti] asadziwe munthu aliyense [ichi].
  267. Mat 9:31 Koma iwo, pamene iwo adanyamuka, anabukitsa kutali kutchuka kwake m’dziko lonselo.
  268. Mat 9:32 ¶Pamene iwo adalikutuluka, tawonani, adabwera naye kwa iye munthu wosayankhula wogwidwa ndi chiwanda.
  269. Mat 9:33 Ndipo m’mene chidatulutsidwa chiwandacho, wosayankhulayo adayankhula: ndipo makamu adazizwa, nanena kuti, Sichidawoneke kale lonse chomwecho mu Israyeli.
  270. Mat 9:34 Koma Afarisi adati, Iye atulutsa ziwanda kudzera mwa mfumu ya ziwanda.
  271. Mat 9:35 Ndipo Yesu adayendayenda m’mizinda yonse ndi midzi, kuphunzitsa m’masunagoge mwawo, ndi kulalikira uthenga wabwino wa ufumuwo, ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi kudwala kulikonse pakati pa anthu.
  272. Mat 9:36 ¶Koma pamene iye anawona makamuwo, iye adagwidwa ndi chisoni pa iwo, chifukwa iwo adalefuka, ndipo anamwazikana kutali, monga nkhosa zopanda mbusa.
  273. Mat 9:37 Kenaka iye anena kwa wophunzira ake, Zokolola zowona ziri zochulukadi, koma antchito [ali] wochepa;
  274. Mat 9:38 Choncho pempherani inu Mbuye wa kholola, kuti iye atumize antchito ku kholola lake.
  275. Mat 10:1 Ndipo pamene iye adadziyitanira kwa [iye] wophunzira ake khumi ndi awiri, iye adapatsa iwo mphamvu [yolimbana] ndi mizimu yoyipa, ya kuyitulutsa iyo, ndi kuchiza nthenda za mitundu iliyonse ndi kudwala kwa mitundu yonse.
  276. Mat 10:2 Tsopano mayina a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa; Woyamba, Simoni, amene atchedwa Petro, ndi Anduru mbale wake; Yakobo [mwana wamwamuna] wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wake;
  277. Mat 10:3 Filipi, ndi Bartimeyasi; Tomasi, ndi Mateyu wokhometsa msonkhoyo; Yakobo [mwana wamwamuna] wa Alifeyasi, ndi Labayusi, amene dzina la atate wake linali Tadeyasi;
  278. Mat 10:4 Simoni Mkanani, ndi Yudasi Isikariyoti, amene adamperekanso iye.
  279. Mat 10:5 Awa khumi ndi awiriwa Yesu adawatumiza, ndipo adawalamulira iwo, kunena kuti, Musapite ku njira ya kwa Amitundu, ndi ku mzinda [wina] uliwonse wa Asamariya musamalowamo inu ayi:
  280. Mat 10:6 Koma makamaka pitani ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli.
  281. Mat 10:7 Ndipo pamene inu mupita, lalikirani, kunena kuti; ufumu wa kumwamba wayandikira.
  282. Mat 10:8 Chiritsani wodwala, yeretsani akhate, ukitsani akufa, tulutsani ziwanda: inu mudalandira kwaulere, patsani kwaulere.
  283. Mat 10:9 Musadzitengere golide, kapena siliva, kapena mkuwa m’zikwama zanu.
  284. Mat 10:10 Kapena thumba la paulendo [wanu], kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo: pakuti wantchito ayenera zakudya zake.
  285. Mat 10:11 Ndipo mu mzinda uliwonse kapena mudzi womwe mudzalowamo, mumfunsitse amene ali woyenera; ndipo khalani komweko kufikira mutulukamo.
  286. Mat 10:12 Ndipo pamene mufika polowa m’nyumba, muwalonjere.
  287. Mat 10:13 Ndipo ngati nyumba ili yoyenera, lolani mtendere wanu udze pa iyo: koma ngati si ili yoyenera, lolani mtendere wanu ubwerere kwa inu.
  288. Mat 10:14 Ndipo aliyense amene sadzakulandirani inu, kapena kusamvera mawu anu, pamene inu mutuluka m’nyumba imeneyo kapena mu mzindamo, sasani fumbi ku mapazi anu.
  289. Mat 10:15 Ndithudi ndinena kwa inu, Udzakhala wochepa mlandu wa Sodomu ndi Gomora pa tsiku la chiweruzo koposa wa mzinda umenewo.
  290. Mat 10:16 ¶Tawonani, ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu: choncho khalani inu wochenjera monga njoka, ndi wodekha monga nkhunda.
  291. Mat 10:17 Koma chenjerani ndi anthu: pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, ndipo adzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo;
  292. Mat 10:18 Ndipo inu mudzatengeredwa pamaso pa a kazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, chifukwa cha umboni wa kwa iwo ndi kwa Amitundu.
  293. Mat 10:19 Koma pamene iwo angakuperekeni inu, musamadera nkhawa momwe mudzayankhulira kapena chimene inu mudzanena: pakuti chidzapatsidwa kwa inu ora lomwero chimene mudzayankhula.
  294. Mat 10:20 Pakuti sindinu amene muyankhula, koma Mzimu wa Atate wanu amene ayankhula mwa inu.
  295. Mat 10:21 Ndipo mbale adzapereka mbale wake ku imfa, ndi atate mwana: ndipo ana adzawukira makolo [awo], ndi kuwapangitsa iwo kuti aphedwe.
  296. Mat 10:22 Ndipo inu mudzadedwa ndi [anthu] onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wopirira kufikira chimaliziro adzapulumutsidwa.
  297. Mat 10:23 Koma pamene iwo akuzunzani inu mumzinda uwu, thawirani inu wina: pakuti Ndithudi ndinena ndi inu, Simudzakhala mutapitirira mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wamwamuna wa munthu atadza.
  298. Mat 10:24 Wophunzira sali pamwamba pa mphunzitsi [wake], kapena wantchito pamwamba pa mbuye wake.
  299. Mat 10:25 Kuli kokwanira kwa wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi wantchito monga mbuye wake. Ngati adamutchula mkulu wa nyumba Belezebule, moposera motani [adzawatchula iwo] apabanja ake?
  300. Mat 10:26 Choncho musawawope iwo: pakuti palibe kanthu kanavundikiridwa, kamene sikadzavumbulutsidwa; ndi kobisika, kamene sikadzadziwika.
  301. Mat 10:27 Chimene ine ndikuwuzani inu mumdima, [chimenecho] tachinenani inu mkuwunika: ndipo chimene muchimva mkhutu, [chimenecho] muchilalikire inu pa madenga a nyumba.
  302. Mat 10:28 Ndipo musawopa iwo amene akupha thupi, koma sangathe kupha moyo: koma makamaka muwope iye amene akhoza kuwononga zonse ziwiri moyo ndi thupi lomwe mu nyanja ya moto.
  303. Mat 10:29 Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa ndi ndalama imodzi? Ndipo imodzi ya izo siyidzagwa pansi popanda Atate wanu.
  304. Mat 10:30 Koma tsitsi lonse la m’mutu mwanu liri lowerengedwa.
  305. Mat 10:31 Choncho inu musamawopa; inu muli a mtengo wopambana mpheta zambiri.
  306. Mat 10:32 Choncho aliyense amene adzavomereza ine pamaso pa anthu, iyeyu ine ndidzam’vomerezanso pamaso pa Atate wanga amene ali kumwamba.
  307. Mat 10:33 Koma aliyense amene adzandikana ine pamaso pa anthu, iyeyu ine ndidzamkananso pamaso pa Atate wanga amene ali kumwamba.
  308. Mat 10:34 Musaganizire kuti ine ndadza kutumiza mtendere pa dziko lapansi: ine sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.
  309. Mat 10:35 Pakuti ine ndadza kuyika munthu pa kumusiyanitsa ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake wamkazi.
  310. Mat 10:36 Ndipo adani ake a munthu [adzakhala] iwo a pabanja ake.
  311. Mat 10:37 Iye wokonda atate kapena amayi ake koposa ine si ali woyenera ine: ndipo iye wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa ine, si ali woyenera ine.
  312. Mat 10:38 Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, si ali woyenera ine.
  313. Mat 10:39 Iye amene apeza moyo wake adzawutaya: ndi iye amene ataya moyo wake chifukwa cha ine adzawupeza.
  314. Mat 10:40 ¶Iye amene alandira inu alandira ine, ndipo iye amene alandira ine alandira iye amene adanditumiza ine.
  315. Mat 10:41 Iye amene alandira mneneri pa dzina la mneneri adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo iye amene alandira munthu wolungama m’dzina la munthu wolungama adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
  316. Mat 10:42 Ndipo aliyense adzapereka kuti amwe kwa m’modzi wa ang’ono awa chikho cha [madzi] wozizira wokha m’dzina la wophunzira, Ndithudi ine ndinena kwa inu, iye sadzataya muli monse mphotho yake.
  317. Mat 11:1 Ndipo kudachitika, pamene Yesu adatha kuwalamulira wophunzira ake khumi ndi awiri, iye adanyamuka kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m’mizinda yawo.
  318. Mat 11:2 Tsopano pamene Yohane adamva ali m’nyumba yandende ntchito za Khristu, iye adatuma wophunzira ake awiri,
  319. Mat 11:3 Ndipo anati kwa iye, Inu ndinu iye wakudzayo kodi, kapena tiyang’anire wina?
  320. Mat 11:4 Ndipo Yesu adayankha ndipo nanena kwa iwo, Pitani ndipo musonyezenso kwa Yohane zinthu zimene inu mulikumva ndi kuziwona:
  321. Mat 11:5 Akhungu akulandira kuwona kwawo, ndi wolumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa, ndipo ogontha akumva, akufa ali kuwukitsidwa, ndi aumphawi uthenga wabwino ulalikidwa kwa iwo.
  322. Mat 11:6 Ndipo wodala ali [iye, amene] aliyense sadzakhumudwa mwa ine.
  323. Mat 11:7 ¶Ndipo m’mene iwo adanyamuka, Yesu adayamba kunena kwa makamuwo zokhudzana ndi Yohane, Mudatuluka inu kumka kuchipululu kukawona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?
  324. Mat 11:8 Koma mudatuluka inu kukawona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, wovala [zovala] zofewa ali m’nyumba za mafumu.
  325. Mat 11:9 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Mneneri kodi? Eya, ine ndinena kwa inu, ndipo woposa mneneri.
  326. Mat 11:10 Pakuti uyu ndi [iye], amene kudalembedwa za iye, Tawonani, ine nditumiza mthenga wanga patsogolo panu, amene adzakonza njira yanu mtsogolo mwanu.
  327. Mat 11:11 Ndithudi ndinena kwa inu, Pakati pa iwo amene ali wobadwa mwa mkazi sadawuke wamkulu woposa Yohane Mbatizi: mosawopa iye amene ali wochepa mu ufumu wa kumwamba ali wamkulu kuposa iye.
  328. Mat 11:12 Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi kufikira tsopano lino ufumu wa kumwamba ulola kukangamizidwa, ndipo okangamirawo awukwatula ndi mphamvu.
  329. Mat 11:13 Pakuti aneneri onse ndi chilamulo zidanenera kufikira pa Yohane.
  330. Mat 11:14 Ndipo ngati mudzachilandira [ichi], uyu ndiye Eliya, amene anali wakuti adze.
  331. Mat 11:15 Iye amene ali ndi makutu akumva, amve.
  332. Mat 11:16 ¶Koma ndidzafanizira mbadwo uwu ku chiyani? Uli wofanana ndi ana wokhala m’misika, ndi kuyitana anzawo,
  333. Mat 11:17 Ndi kunena kuti, Ife tidaliza zitoliro kwa inu, ndipo inu simudavine; ife tidabuma maliro kwa inu, ndipo inu simudalire;
  334. Mat 11:18 Pakuti Yohane adadza wosadya kapena kumwa, ndipo iwo ati, Ali ndi chiwanda.
  335. Mat 11:19 Mwana wamwamuna wa munthu adadza wakudya ndi kumwa, ndipo iwo ati, Tawonani munthu wakudyayidya, ndi wakumwayimwa vinyo, bwenzi la wokhometsa misonkho ndi wochimwa. Koma nzeru ilungamitsidwa kwa ana ake.
  336. Mat 11:20 ¶Kenaka iye adayamba kudzudzula mizindayo m’mene zidachitidwa zambiri za ntchito za mphamvu zake, chifukwa iwo sadalape ayi:
  337. Mat 11:21 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsayida! Pakuti ngati ntchito za mphamvu, zimene zidachitidwa mwa inu, zikadachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akadakhala atalapa kalekale m’ziguduli ndi m’phulusa.
  338. Mat 11:22 Koma ndinena kwa inu, Udzakhala wochepa mlandu kwa Turo ndi Sidoni pa tsiku la chiweruzo koposa wa inu.
  339. Mat 11:23 Ndipo iwe, Kaperenamu, amene wakwezedwa kufikira kumwamba, udzatsitsidwa kufikira ku nyanja ya moto: pakuti ngati ntchito za mphamvu, zimene zachitidwa mwa iwe, zikadachitidwa mu Sodomu, zikadakhalabe kufikira tsiku la lero.
  340. Mat 11:24 Koma ine ndinena kwa inu, Udzakhala wochepa mlandu wake wa dziko la Sodomu pa tsiku la chiweruzo, koposa wako.
  341. Mat 11:25 ¶Pa nthawi imeneyo Yesu adayankha ndipo anati, Ine ndikuyamikani inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa inu mwabisira zinthu izi kwa anzeru ndi kwa wochita mosamalitsa, ndipo mudazivumbulutsira izi kwa makanda.
  342. Mat 11:26 Ngakhale motero, Atate: pakuti motero chidakhala chabwino pamaso panu.
  343. Mat 11:27 Zinthu zonse zaperekedwa kwa ine ndi Atate wanga: ndipo palibe munthu adziwa Mwana wamwamuna, koma Atate; kapena palibe wina adziwa Atate, kupatula Mwana wamwamuna, ndi [iye] kwa aliyense amene Mwana wamwamuna afuna kumuvumbulutsira [iye].
  344. Mat 11:28 ¶Idzani kwa ine, nonse [inu] amene muli wotopetsedwa ndi wosenzetsedwa zolemera; ndipo ine ndidzakupatsani inu mpumulo.
  345. Mat 11:29 Senzani goli langa pa inu, ndipo phunzirani kwa ine; pakuti ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mu mtima: ndipo mudzapeza mpumulo ku miyoyo yanu.
  346. Mat 11:30 Pakuti goli langa [liri] lophweka, ndi katundu wanga ali wopepuka.
  347. Mat 12:1 Pa Nthawi imeneyo Yesu adapita tsiku la sabata pakati pa tirigu; ndipo wophunzira ake adamva njala, ndipo anayamba kubudula ngala za tirigu, ndi kuti adye.
  348. Mat 12:2 Koma pamene Afarisi anawona [ichi], iwo adati kwa iye, Tawonani, wophunzira anu achita chosaloleka mwa lamulo pa tsiku la sabata.
  349. Mat 12:3 Koma iye adati kwa iwo, Kodi inu simudawerenga chimene adachita Davide, pamene iye adamva njala, ndi iwo amene adali ndi iye;
  350. Mat 12:4 Momwe iye adalowa m’nyumba ya Mulungu, ndipo anadya mikate yowonetsa, imene idali yosaloleka kwa iye kuti adye, kapena iwo amene adali ndi iye, koma ansembe okha?
  351. Mat 12:5 Kapena inu simudawerenga kodi m’chilamulo, m’mene pa masiku a sabata ansembe m’kachisi ayipitsa sabata, ndipo akhala osalakwa?
  352. Mat 12:6 Koma ndinena kwa inu, Kuti m’malo ano alipo [m’modzi] wamkulu woposa kachisiyo.
  353. Mat 12:7 Koma inu mukadadziwa chimene [ichi] chitanthawuza, Ine ndifuna chifundo, ndipo osati nsembe ayi, inu simukadatsutsa wopanda mlandu.
  354. Mat 12:8 Pakuti Mwana wamwamuna wa munthu ali Mbuye ngakhale wa tsiku la sabata.
  355. Mat 12:9 Ndipo pamene iye adanyamuka pamenepo, iye analowa m’sunagoge wawo:
  356. Mat 12:10 ¶Ndipo, tawonani, mudali munthu amene dzanja [lake] linali lopuwala. Ndipo iwo adamfunsa iye, kunena kuti, Kodi nkuloleka kuchiritsa pa masiku a sabata? Kuti iwo amuyimbe mlandu iye.
  357. Mat 12:11 Ndipo iye adati kwa iwo. Munthu ndani mwa inu, amene adzakhala nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m’dzenje tsiku la sabata, kodi iye sadzayigwira iyo, ndi kuyitulutsa iyo?
  358. Mat 12:12 Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa n’kotani? Mwa ichi n’kololeka kuchita zabwino pa masiku a sabata.
  359. Mat 12:13 Kenaka anena iye kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo iye adalitambasula [ilo]; ndipo lidabwezeretsedwa lamphumphu, monga linzake.
  360. Mat 12:14 ¶Kenaka Afarisi adatuluka, ndipo anakhala upo womchitira iye, momwe angamuwonongere iye.
  361. Mat 12:15 Koma pamene Yesu adadziwa [ichi], iye adawachokera yekha kumeneko: ndipo makamu akulu adamtsata iye, ndipo iye adawachiritsa iwo onse;
  362. Mat 12:16 Ndipo adawalamulira iwo kuti iwo asapangitse kuti iye adziwike:
  363. Mat 12:17 Kuti chikhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi Yesaya mneneri, kunena kuti,
  364. Mat 12:18 Tawona mtumiki wanga, amene ine ndamsankha; wokondedwa wanga, amene mwa iye moyo wanga ukondwera bwino: ine ndidzayika Mzimu wanga pa iye, ndipo iye adzalalikira chiweruzo kwa Amitundu.
  365. Mat 12:19 Iye sadzalimbana, kapena kufuwula; kapena munthu aliyense sadzamva mawu ake m’makwalala.
  366. Mat 12:20 Bango lokandika iye sadzalithyola, ndi nyali yofuka iye sadzayizima, kufikira iye adzatumiza chiweruzo ku chigonjetso.
  367. Mat 12:21 Ndipo m’dzina lake Amitundu adzakhulupirira.
  368. Mat 12:22 ¶Kenaka adabwera naye kwa iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu, ndiponso wosayankhula: ndipo iye adamchiritsa iye, motero mwakuti wosawona ndi kusayankhulayo adayankhula ndipo anapenya.
  369. Mat 12:23 Ndipo anthu onse adazizwa, ndipo ananena, Uyu si mwana wamwamuna wa Davide kodi?
  370. Mat 12:24 Koma pamene Afarisi adamva [ichi], iwo adati; [Munthu] uyu samatulutsa ziwanda, koma ndi mphamvu yake ya Belezebule mkulu waziwanda.
  371. Mat 12:25 Ndipo Yesu adadziwa maganizo awo, ndipo anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanikana pa iwo wokha umafika ku chiwonongeko; ndi mzinda uliwonse kapena nyumba yogawanika pa yokha siyidzakhalitsa:
  372. Mat 12:26 Ndipo ngati Satana atulutsa Satana, iye ali wogawanika pa yekha; ndipo tsono udzakhala bwanji ufumu wake?
  373. Mat 12:27 Ndipo ngati ine ndi mphamvu yake ya Belezebule ndimatulutsa ziwanda, ndi mwa yani ana anu amazitulutsa [izo]? Choncho iwo adzakhala woweruza anu.
  374. Mat 12:28 Koma ngati ine nditulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pomwepo ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika kwa inu.
  375. Mat 12:29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m’nyumba ya munthu wolimba, ndi kuwononga akatundu ake pokhapokha iye ayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzawononga nyumba yake.
  376. Mat 12:30 Iye amene sali ndi ine atsutsana ndi ine; ndi iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi ine amwazamwaza.
  377. Mat 12:31 ¶Mwa ichi ine ndinena kwa inu. Tchimo la mtundu uliwonse ndi zonyoza [Mulungu] zidzakhululukidwa kwa anthu: koma chonyoza [chonenera Mzimu] Woyera sichidzakhululukidwa kwa anthu.
  378. Mat 12:32 Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wamwamuna wa munthu zoyipa, kudzakhululukidwira iye: koma aliyense amene anganenere motsutsa Mzimu Woyera, sikudzakhululukidwira iye, kapena m’dziko lino, kapena [m’dziko] liri nkudzalo.
  379. Mat 12:33 Kapena mukometse mtengo, ndipo chipatso chake chomwe chikoma; kapena muyipitse mtengo, ndipo chipatso chake chomwe chiyipa: pakuti mtengo udziwika ndi chipatso [chake].
  380. Mat 12:34 Mbadwo wa njoka, mungathe inu bwanji, wokhala woyipa kulankhula zinthu zabwino? Pakuti mwa kusefukira kwake kwa mtima pakamwa payankhula.
  381. Mat 12:35 Munthu wabwino m’chuma cha mtima wake wabwino atulutsa zinthu zabwino: ndipo munthu woyipa kuchokera m’chuma chake choyipa atulutsa zoyipa.
  382. Mat 12:36 Koma ine ndinena kwa inu, Kuti liwu lirilonse lopanda pake limene anthu adzalankhula, iwo adzayenera kufotokoza za mawuwo pa tsiku la kuweruza.
  383. Mat 12:37 Pakuti ndi mawu ako iwe udzalungamitsidwa, ndipo ndi mawu ako iwe udzatsutsidwa.
  384. Mat 12:38 ¶Kenaka ena a alembi ndi Afarisi ena adayankha, nanena kuti, Mphunzitsi, ife tifuna kuwona chizindikiro chochokera kwa inu.
  385. Mat 12:39 Koma iye adayankha nati kwa iwo, Mbadwo woyipa ndi wachigololo ufunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa chizindikiro kwa iwo, koma chizindikiro cha mneneri Yona:
  386. Mat 12:40 Pakuti monga Yona adali masiku atatu ndi usiku utatu m’mimba mwa chinsomba; chomwecho Mwana wamwamuna wa munthu adzakhala masiku atatu ndi usiku utatu mumtima wa dziko.
  387. Mat 12:41 Anthu a ku Nineve adzawuka pa chiweruzo ndi mbadwo uwu, ndipo adzawutsutsa iwo: chifukwa iwo adatembenuka mtima pa kulalikira kwa Yona; ndipo, tawonani, wamkulu woposa Yona [ali] pano.
  388. Mat 12:42 Mfumukazi ya ku m’mwera idzawuka pa chiweruzo ndi mbadwo uwu, ndipo adzawutsutsa: chifukwa iye adachokera ku madera akumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo, tawonani, wamkulu woposa Solomoni [ali] pano.
  389. Mat 12:43 Pamene mzimu wonyansa utuluka mwa munthu, umayenda kudutsa malo wopanda madzi, kufunafuna mpumulo, ndipo osawupeza.
  390. Mat 12:44 Kenaka iwo unena, ine ndidzabwerera kumuka kunyumba kwanga kumene ndidatulukako; ndipo pamene ufikako, uyipeza [iyo] mopanda kalikonse, yosesedwa, ndi yokongoletsedwa.
  391. Mat 12:45 Kenaka iwo upita, ndipo utenga pamodzi ndi iwo mwini mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa yoposa mwini yekhayo, ndipo iyo ilowa nikhalamo: ndipo [makhalidwe] wotsiriza a munthu ameneyo ali oyipa koposa woyambawo. Motero momwemo udzakhalanso kwa mbadwo woyipa uwu.
  392. Mat 12:46 ¶Pamene iye adali chiyankhulire kwa anthu, tawonani amayi [ake] ndi abale ake adayima panja, kufuna kuyankhula ndi iye.
  393. Mat 12:47 Kenaka m’modzi adati kwa iye, Tawonani, amayi wanu ndi abale anu ayima panja, kufuna kuyankhula ndi inu.
  394. Mat 12:48 Koma iye adayankha ndipo anati kwa iye amene adamuwuza iye, Amayi wanga ndani? Ndi abale anga ali ayani?
  395. Mat 12:49 Ndipo adatambalitsa dzanja lake kuloza kwa wophunzira ake, ndipo anati, Tawonani amayi wanga ndi abale anga!
  396. Mat 12:50 Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga amene ali kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amayi.
  397. Mat 13:1 Tsiku lomwero Yesu adatuluka m’nyumbamo, ndipo nakhala pansi m’mbali mwa nyanja.
  398. Mat 13:2 Ndipo makamu akulu adasonkhanira pamodzi kwa iye, kotero kuti iye adalowa m’chombo, ndipo anakhala pansi; ndipo khamu lonse lidayima pamtunda.
  399. Mat 13:3 Ndipo iye adayankhula zinthu zambiri kwa iwo m’mafanizo, nanena kuti, Tawonani, wofesa adatuluka kukafesa.
  400. Mat 13:4 Ndipo pamene adafesa, [mbewu] zina zidagwa m’mbali mwa njira, ndipo mbalame zinadza, nizitolatola izo:
  401. Mat 13:5 Zina zinagwa pa malo amiyala, pamene zinalibe dothi lambiri: ndipo pomwepo zidamera; chifukwa zidalibe dothi la kuya:
  402. Mat 13:6 Ndipo m’mene dzuwa lidakwera, izo zidapserera; ndipo chifukwa zidalibe muzu, izo zinafota.
  403. Mat 13:7 Ndipo zina zidagwera pakati paminga; ndipo mingazo zidaphuka, ndipo zinatsamwitsa izo:
  404. Mat 13:8 Koma zina zidagwera m’nthaka yabwino, ndipo zinabala chipatso, zina za zana limodzi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.
  405. Mat 13:9 Iye amene ali ndi makutu akumva, amve.
  406. Mat 13:10 Ndipo wophunzirawo adadza, ndipo anati kwa iye, Chifukwa chiyani inu muyankhula kwa iwo m’mafanizo?
  407. Mat 13:11 Iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za ufumu wa kumwamba, koma kwa iwo sikudapatsidwa.
  408. Mat 13:12 Pakuti aliyense amene ali nazo, kwa iye kudzapatsidwa, ndipo adzakhala nazo zochuluka: koma aliyense amene alibe, chidzachotsedwa kwa iye chingakhale chomwe ali nacho.
  409. Mat 13:13 Choncho ine ndiyankhula kwa iwo m’mafanizo: chifukwa kuti iwo pakuwona sawona ayi; ndi iwo pakumva siamva ayi, kapena iwo samamvetsetsa.
  410. Mat 13:14 Ndipo mwa iwo ukwaniritsidwa uneneri wa Yesaya, umene uti, Pakumva inu mudzamva, ndipo simudzamvetsetsa konse; ndipo pakupenya mudzapenya, ndipo simudzadziwa:
  411. Mat 13:15 Pakuti mtima wa anthu awa udalemera, ndipo makutu [awo] ali wogontha kumva, ndipo maso awo awatseka; kuti mwina pa nthawi ina iliyonse iwo angawone ndi maso [awo] ndi kumva ndi makutu [awo], ndi kuzindikira ndi mtima [wawo], ndi kutembenuka, ndipo ine ndiwachiritse iwo.
  412. Mat 13:16 Koma maso [anu] ali wodala, pakuti apenya; ndi makutu anu, pakuti amva.
  413. Mat 13:17 Pakuti ndithudi ine ndinena kwa inu, Kuti aneneri ambiri ndi [anthu] wolungama adalakalaka kupenya [zinthu zimenezo] zimene inu muziwona, ndipo sadaziwona [izo]; ndi kumva [zinthu zimenezo] zimene inu muzimva, ndipo sadazimva [izo].
  414. Mat 13:18 ¶Choncho imvani inu fanizo la wofesa.
  415. Mat 13:19 Pamene munthu aliyense akumva mawu a ufumu, ndipo osawamvetsetsa [iwo], kenaka adza woyipayo, ndipo akwatula chimene chinafesedwa mu mtima mwake. Uyu ndi iye amene analandira mbewu m’mbali mwa njira.
  416. Mat 13:20 Koma iye amene adalandira mbewu pa malo amiyala, yemweyu ndiye amene akumva mawu, ndipo ndi chimwemwe awalandira nthawi yomweyo;
  417. Mat 13:21 Komatu alibe iye mizu mwa iye yekha, koma akhala kwa kanthawi: pakuti pamene msawutso kapena mazunzo zibuka chifukwa cha mawu, pang’ono ndi pang’ono iye akhumudwa.
  418. Mat 13:22 Iyenso amene adalandira mbewu pakati paminga ndiye amene akumva mawu; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, zitsamwitsa mawu, ndipo iye sabala chipatso.
  419. Mat 13:23 Koma iye amene adalandira mbewu mu nthaka yabwino ndiye amene akumva mawu, ndipo awamvetsetsa [iwo]; amenenso abala chipatso, ndipo afikitsa, ena za zana limodzi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
  420. Mat 13:24 ¶Fanizo lina iye adawafotokozera iwo, nanena kuti, Ufumu wa kumwamba ufanizidwa ndi bambo amene adafesa mbewu zabwino m’munda mwake:
  421. Mat 13:25 Koma pamene abambo adalinkugona, mdani wake anadza nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachoka kupita pa njira yake.
  422. Mat 13:26 Koma pamene mmera udakula, nubala chipatso, kenaka adawonekeranso namsongole.
  423. Mat 13:27 Ndipo anchito ake a mwini nyumbayo adadza ndipo anati kwa iye, Mbuye, kodi inu simudafesa mbewu zabwino m’munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?
  424. Mat 13:28 Iye adanena kwa iwo, Mdani wachichita ichi. Antchito adati kwa iye, Kodi mufuna tsono kuti ife tipite ndi kukasonkhanitsa uyo pamodzi?
  425. Mat 13:29 Koma iye adati, Ayi; kuti mwina m’mene musonkhanitsa namsongoleyo, inu mungazulenso tirigu pamodzi naye.
  426. Mat 13:30 Lolani zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira kholola: ndipo m’nyengo yakukolola ndidzawuza wokololawo, Sonkhanitsani inu pamodzi poyamba namsongole, ndipo mum’mange uyu mitolo kukamtentha: koma musonkhanitse tirigu m’nkhokwe yanga.
  427. Mat 13:31 ¶Fanizo lina iye adawafotokozera iwo, nanena kuti, Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi kambewu kampiru, kamene munthu adakatenga, ndipo anakafesa m’munda wake.
  428. Mat 13:32 Kamene ndithu kali kakang’ono kwa mbewu zonse: koma pamene kakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, ndipo kakhala mtengo, kotero kuti mbalame za mumlengalenga zimadza ndi kubindikira munthambi zake.
  429. Mat 13:33 ¶Fanizo lina adanena kwa iwo; Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi chofufumitsa mkate, chimene mkazi adachitenga, ndipo anachibisa m’miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse udafufuma.
  430. Mat 13:34 Zinthu zonse izi Yesu adaziyankhula kwa makamu m’mafanizo; ndipo kopanda fanizo iye sadayankhula kanthu kwa iwo.
  431. Mat 13:35 Kuti chikhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi mneneri, kunena kuti, Ine ndidzatsegula pakamwa panga m’mafanizo; ine ndidzalankhula zinthu zimene zakhala zosungika zobisika chiyambire kukhazikitsidwa kwa dziko lapansi.
  432. Mat 13:36 Kenaka Yesu adabalalitsa khamulo, ndipo analowa m’nyumbamo: ndipo wophunzira ake adadza kwa iye, nanena kuti, Mutanthawuzire kwa ife fanizo lija la namsongole wa m’munda.
  433. Mat 13:37 Iye adawayankha nati kwa iwo, Iye wofesa mbewu yabwino ndiye Mwana wamwamuna wa munthu;
  434. Mat 13:38 Munda ndiwo dziko lapansi: mbewu yabwino ndiyo ana a ufumuwo; koma namsongole ndiye ana a woyipayo;
  435. Mat 13:39 Mdani amene adafesa uyu ndiye mdiyerekezi; kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya dziko lapansi; ndi wotutawo ndiwo angelo.
  436. Mat 13:40 Choncho monga namsongole asonkhanitsidwa ndi kutenthedwa m’moto; kotero kudzakhala m’chimariziro cha dziko lapansi ili.
  437. Mat 13:41 Mwana wamwamuna wa munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi za mu ufumu wake zinthu zonse zimene zochimwitsa, ndi iwo amene achita kusayeruzika;
  438. Mat 13:42 Ndipo adzawataya iwo m’ng’anjo ya moto: kumene kudzakhala kulira ndi kukuta kwa mano.
  439. Mat 13:43 Kenaka wolungamawo adzawala monga dzuwa mu ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu akumva, amve.
  440. Mat 13:44 ¶Ndiponso ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisidwa m’munda; chimene munthu pamene wachipeza, iye abisa; ndipo chifukwa cha chimwemwe chake apita ndipo agulitsa zonse adali nazo, ndipo agula munda umenewo.
  441. Mat 13:45 ¶Ndiponso, ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wofuna ngale zabwino:
  442. Mat 13:46 Amene, pamene wapeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, adapita ndi kugulitsa zonse adali nazo, ndipo adagula imeneyo.
  443. Mat 13:47 ¶Ndiponso, ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi khoka, limene lidaponyedwa m’nyanja, ndipo lidasonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse:
  444. Mat 13:48 Limene, pamene lidadzaza, iwo adalivuwulira pa mtunda, ndipo adakhala pansi, ndipo adasonkhanitsa zabwino mu zotengera, koma zoyipa adazitaya.
  445. Mat 13:49 Kotero zidzakhala pa chimaliziro cha dziko lapansi pano: angelo adzatuluka, ndipo adzawasankhula woyipa pakati pa abwino,
  446. Mat 13:50 Ndipo adzawataya iwo m’ng’anjo ya moto: komweko kudzakhala kulira ndi kukuta kwa mano.
  447. Mat 13:51 Yesu adati kwa iwo, Kodi inu mwamvetsetsa zinthu zonse izi? Iwo adati kwa iye, Inde, Ambuye.
  448. Mat 13:52 Kenaka iye adati kwa iwo, Choncho mlembi aliyense [amene] wophunzitsidwa ku ufumu wa kumwamba ali wofananizidwa kwa munthu [amene ali] mwini banja, amene atulutsa m’chuma chake [zinthu] zatsopano ndi zakale.
  449. Mat 13:53 ¶Ndipo kudachitika, [kuti] pamene Yesu adamaliza mafanizo awa, iye adanyamuka kumeneko.
  450. Mat 13:54 Ndipo pamene adafika ku dziko la kwawo, iye adaphunzitsa iwo m’masunagoge mwawo, motero mwakuti iwo adazizwa, nanena kuti, [Munthu] uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi, ndi ntchito zamphamvu [izi]?
  451. Mat 13:55 Kodi uyu si mwana wamwamuna wa m’misiri wamatabwa? Kodi dzina la amayi wake si Maria? Ndi abale ake, Yakobo, ndi Yosesi, ndi Simoni, ndi Yudasi?
  452. Mat 13:56 Ndipo alongo ake, Si ali onse ndi ife? Ndipo [munthu] uyu tsono adazitenga zinthu zonsezi kuti?
  453. Mat 13:57 Ndipo iwo adakhumudwa mwa iye. Koma Yesu adati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, kupatula mu dziko la kwawo, ndi m’nyumba mwa iye mwini.
  454. Mat 13:58 Ndipo iye sadachita ntchito zamphamvu zambiri kumeneko chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.
  455. Mat 14:1 Pa Nthawi imeneyo Herode mfumu yayikulu yolamulira gawo lachinayi la dziko adamva za kutchuka kwa mbiri ya Yesu.
  456. Mat 14:2 Ndipo adati kwa antchito ake, Uyu ndi Yohane M’batizi; adawuka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi ntchito zamphamvu zidziwonetsera zokha mwa iye.
  457. Mat 14:3 ¶Pakuti Herode adam’gwira Yohane, ndipo anam’manga iye, ndipo anamuyika [iye] m’ndende chifuwa cha Herodiyasi, mkazi wa mbale wake Filipi.
  458. Mat 14:4 Pakuti Yohane adanena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kumtenga iye.
  459. Mat 14:5 Ndipo pamene iye adafuna kumupha iye, adawopa khamu, chifukwa adamuwerengera iye ngati mneneri.
  460. Mat 14:6 Koma pakukumbukira tsiku la kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiyasi adavina pamaso pawo, ndipo anam’kondweretsa Herode.
  461. Mat 14:7 Pa chimenencho iye adalonjeza ndi lumbiro kumpatsa iye chilichonse chimene akanapempha.
  462. Mat 14:8 Ndipo iye, wokhala atam’pangira amayi wake, adati, Ndipatseni ine kuno mutu wa Yohane M’batizi m’chimbale.
  463. Mat 14:9 Ndipo Mfumuyo adamva chisoni: ngakhale zinali choncho chifukwa cha lumbiro lake, ndi cha iwo adakhala naye pa chakudya, adalamulira kuti upatsidwe kwa [iye].
  464. Mat 14:10 Ndipo iye adatumiza, ndipo anadula mutu wa Yohane m’ndende.
  465. Mat 14:11 Ndipo mutu wake adawutengera m’mbalemo, ndi kupatsidwa kwa mtsikanayo: ndipo iye adawubweretsa [iwo] kwa amayi wake.
  466. Mat 14:12 Ndipo wophunzira ake adadza, ndipo anatenga thupilo, ndipo analiyika m’manda, ndipo adapita ndi kumuwuza Yesu.
  467. Mat 14:13 ¶Pamene Yesu adamva [za ichi], iye adanyamuka kumeneko m’chombo kupita m’malo a chipululu cha mchenga pa yekha: ndipo pamene adamva [zakumeneko], iwo adamtsata iye poyenda pamtunda kuchokera m’mizinda.
  468. Mat 14:14 Ndipo Yesu adatuluka, ndipo anawona khamu lalikulu, ndipo anagwidwa ndi chifundo pa iwo, ndipo anachiritsa wodwala awo.
  469. Mat 14:15 ¶Ndipo pamene panali madzulo, wophunzira ake adafika kwa iye, nanena kuti, Ano ndi malo a chipululu cha mchenga, ndipo nthawi yapita tsopano; liwuzeni khamulo lizipita, kuti iwo akhoze kulowa m’midzi, ndi kukadzigulira okha zakudya.
  470. Mat 14:16 Koma Yesu adati kwa iwo, Iwo sayenera kunyamuka; apatseni inu kuti iwo adye.
  471. Mat 14:17 Ndipo iwo anena kwa iye, Ife tiri nayo pano mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.
  472. Mat 14:18 Iye adati, Mudze nazo kuno kwa ine.
  473. Mat 14:19 Ndipo iye adalamulira khamulo kuti likhale pansi pa udzu; ndipo adatenga mikate isanuyo, ndi nsomba ziwirizo, ndipo akuyang’ana kumwamba, iye anadalitsa, ndipo ananyema, ndipo anapatsa mikateyo kwa wophunzira [ake], ndipo wophunzirawo kwa khamulo.
  474. Mat 14:20 Ndipo adadya onse, ndipo anakhuta: ndipo adatola makombo amene adatsala mitanga khumi ndi iwiri yodzala.
  475. Mat 14:21 Ndipo iwo amene adadyawo adali amuna pafupifupi zikwi zisanu, osawerenga akazi ndi ana.
  476. Mat 14:22 ¶Ndipo pomwepo Yesu adakakamiza wophunzira ake alowe m’chombo, ndi kuti apite patsogolo pa iye ku tsidya lina, pomwe iye ankawuza makamu apite.
  477. Mat 14:23 Ndipo pamene iye adawawuza makamuwo kuti apite, iye adakwera m’phiri pa yekha kukapemphera: ndipo pakufika madzulo, iye adali kumeneko yekha.
  478. Mat 14:24 Koma chombo tsopano chidali pakati pa nyanja, chozunzika ndi mafunde: pakuti mphepo idadza motsutsana nacho.
  479. Mat 14:25 Ndipo pa ulonda wa chinayi wa usiku Yesu adapita kwa iwo alikuyenda pa nyanja.
  480. Mat 14:26 Ndipo m’mene wophunzirawo adamuwona iye, alikuyenda panyanja, adavutika mtima, nanena kuti, Ndi mzukwa; Ndipo adafuwula chifukwa cha mantha.
  481. Mat 14:27 Koma pomwepo Yesu adayankhula kwa iwo, nanena kuti, Limbani mtima; Ndine; musawope.
  482. Mat 14:28 Ndipo Petro adamyankha iye ndipo anati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiwuze ine ndidze kwa inu pamadzi.
  483. Mat 14:29 Ndipo iye adati, Idza. Ndipo pamene Petro adatsika m’chombo, anayenda pamadzi, kuti apite kwa Yesu.
  484. Mat 14:30 Koma m’mene iye adawona mphepo ikuwomba mwamphamvu, iye adawopa; ndipo poyamba kumira, iye anafuwula, nanena kuti, Ambuye, ndipulumutseni ine!
  485. Mat 14:31 Ndipo posakhalitsa Yesu adatansa dzanja [lake], ndipo anamgwira iye, ndipo ananena kwa iye, Iwe wachikhulupiriro chaching’ono, mwa ichi iwe udakayikiranji?
  486. Mat 14:32 Ndipo pamene iwo adalowa m’chombomo, mphepo idaleka.
  487. Mat 14:33 Kenaka iwo amene adali m’chombo adadza ndipo anamlambira iye, nanena kuti, Zowonadi inu ndinu Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  488. Mat 14:34 ¶Ndipo pamene iwo adawoloka, adafika ku dziko la Genesarete.
  489. Mat 14:35 Ndipo m’mene amuna a kumeneko adadziwa za iye, adatumiza ku dziko lonse lozungulira, ndipo anadza nawo kwa iye onse wokhala ndi nthenda;
  490. Mat 14:36 Ndipo adampempha iye kuti angokhudza kokha mphonje ya chovala chake; ndipo ambiri a iwo amene adamkhudza adachiritsidwa.
  491. Mat 15:1 Kenaka adadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, amene anali a ku Yerusalemu, nanena kuti,
  492. Mat 15:2 Kodi chifukwa chiyani wophunzira anu akulumpha miyambo ya akulu? Pakuti sasamba manja awo pakudya mkate?
  493. Mat 15:3 Koma iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Chifukwa chiyani inunso mulumpha lamulo la Mulungu ndi miyambo yanu?
  494. Mat 15:4 Pakuti Mulungu adalamulira, kunena kuti, Lemekeza atate wako ndi amayi wako: ndipo, Iye amene atemberera atate wake ndi amayi ake, iye afe imfayo.
  495. Mat 15:5 Koma inu munena, aliyense amene adzanena kwa atate [wake] kapena kwa amayi [wake, Ili] mphatso, mwa chilichonse chimene iwe ukanakhoza kupindula nacho mwa ine;
  496. Mat 15:6 Ndipo salemekeza atate wake ndi amayi wake, [iye adzakhala wopanda mlandu]. Potero inu mulipangitsa lamulo la Mulungu kukhala lopanda mphamvu ndi miyambo yanu.
  497. Mat 15:7 Wonyenga [inu]! Yesaya adanenera bwino za inu, kunena kuti,
  498. Mat 15:8 Anthu awa ayandikira chifupi ndi ine ndi pakamwa pawo, ndipo andilemekeza ine ndi milomo [yawo]; koma mtima wawo uli kutali ndi ine.
  499. Mat 15:9 Koma kwachabe iwo andilambira ine, kuphunzitsa malangizo a anthu kuti zikhale ziphunzitso.
  500. Mat 15:10 ¶Ndipo iye adayitana khamulo, ndipo anati kwa iwo, Imvani, ndipo mumvetsetse;
  501. Mat 15:11 Si chimene chilowa m’kamwa mwake mwa munthu ndicho chiyipitsa munthu; koma chimene chituluka m’kamwa mwake, ndicho chiyipitsa munthu.
  502. Mat 15:12 Kenaka adadza wophunzira ake, ndipo ananena kwa iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi adakhumudwa, atamva iwo chonena ichi?
  503. Mat 15:13 Koma iye adayankha ndipo anati, Chomera chilichonse, chimene Atate wanga wa kumwamba sadabzala, chidzazulidwa.
  504. Mat 15:14 Alekeni iwo: ali atsogoleri akhungu [otsogolera] akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwera m’dzenje.
  505. Mat 15:15 Kenaka adayankha Petro ndipo anati kwa iye, Mumasulire kwa ife fanizo ili.
  506. Mat 15:16 Ndipo Yesu adati, Kodi inunso mukadali wopanda kumvetsetsa?
  507. Mat 15:17 Kodi inu simumvetsetsa, kuti chilichonse chimene chilowa pakamwa chipita m’mimba, ndipo chitayidwa m’chimbudzi?
  508. Mat 15:18 Koma zinthu zimene zituluka mkamwa zichokera mu mtima; ndipo ziyipitsa munthu.
  509. Mat 15:19 Pakuti kuchokera mu mtima mutuluka maganizo woyipa, kupha, zigololo, ziwerewere, kuba, umboni wonama ndi zonyoza [Mulungu]:
  510. Mat 15:20 Izi ndizo [zinthu zomwe] ziyipitsa munthu: koma kudya wosasamba m’manja sikuyipitsa munthu ayi.
  511. Mat 15:21 ¶Kenaka Yesu adatuluka kumeneko, ndipo ananyamuka kulowa m’malire a Turo ndi Sidoni.
  512. Mat 15:22 Ndipo, Tawonani, mkazi wa ku Kanani adatuluka m’malire omwewo, ndipo anafuwulira kwa iye, nanena kuti, Mundichitire ine chifundo, Ambuye, [inu] Mwana wamwamuna wa Davide; mwana wanga wamkazi wavutidwa kowopsa ndi chiwanda.
  513. Mat 15:23 Koma iye sadamyankha ngakhale mawu amodzi. Ndipo wophunzira ake anadza ndipo anampempha iye, nanena kuti, Mumuwuze apite; pakuti afuwula pambuyo pathu.
  514. Mat 15:24 Koma iye adamyankha ndipo anati, Ine sindidatumidwa [kwa ena] koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Israyeli.
  515. Mat 15:25 Kenaka iye adadza ndipo anamlambira iye, nanena kuti, Ambuye, ndithandizeni ine.
  516. Mat 15:26 Koma iye adayankha ndipo anati, Sikoyenera kutenga chakudya cha ana, ndi kuponyera [icho] agalu.
  517. Mat 15:27 Ndipo iye adati, Zowonadi, Ambuye, pakutinso agalu amadya nyenyeswa zimene zikugwa kuchokera pagome pa ambuye wawo.
  518. Mat 15:28 Kenaka Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako [ndi] chachikulu: chikhale kwa iwe monga momwe iwe ufuna. Ndipo mwana wake wamkazi adachira ora lomwero.
  519. Mat 15:29 Ndipo Yesu adanyamuka kuchoka kumeneko, ndipo anadza ku nyanja ya Galileya; ndipo anakwera m’phiri, ndipo anakhala pansi pamenepo.
  520. Mat 15:30 Ndipo makamu akulu adadza kwa iye, ali nawo [iwo omwe anali] wolumala, akhungu, osayankhula, wowonongeka ziwalo, ndi ena ambiri, ndipo anawakhazika pansi pa mapazi a Yesu; ndipo iye adawachiritsa iwo;
  521. Mat 15:31 Motero mwakuti khamulo lidazizwa, pamene adawona osayankhula nayankhula, ndipo wowonongeka ziwalo nachira, wopunduka nayenda, ndi a khungu napenya: ndipo iwo adalemekeza Mulungu wa Israyeli;
  522. Mat 15:32 ¶Kenaka Yesu adayitana wophunzira ake kwa iye, ndipo anati, Ine ndiri ndi chifundo pa khamuli, chifukwa ali chikhalire ndi ine tsopano masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya: ndipo ine sindifuna kuwawuza iwo apite osadya, kuti mwina angakomoke panjira.
  523. Mat 15:33 Ndipo wophunzira ake anena kwa iye, Tiyitenga kuti ife mikate yotere m’chipululu, yonga yakuti yokhutitsa unyinji wotere wa anthu?
  524. Mat 15:34 Ndipo iye anena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo adati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang’ono.
  525. Mat 15:35 Ndipo iye adalamulira khamulo kuti likhale pansi.
  526. Mat 15:36 Ndipo iye adatenga mikate isanu ndi iwiri ndi nsombazo, ndipo anayamika, ndipo ananyema [izo], ndipo anapatsa kwa wophunzira ake, ndi wophunzirawo kwa khamulo.
  527. Mat 15:37 Ndipo iwo onsewo adadya, ndipo anakhuta: ndipo adatola [za zakudya] zonyemedwa za makombo amene adatsala madengu asanu ndi awiri odzadza.
  528. Mat 15:38 Ndipo iwo onse amene adadyawo adali amuna zikwi zinayi, osawerenga akazi ndi ana.
  529. Mat 15:39 Ndipo iye adawuza khamulo kuti lipite, ndipo adalowa m’chombo, ndipo anafika m’malire a Magadala.
  530. Mat 16:1 Afarisi nawonso pamodzi ndi Asaduki adabwera, ndi kumuyesa kufuna iye kuti awawonetse iwo chizindikiro chochokera kumwamba.
  531. Mat 16:2 Iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Pamene kuli madzulo, inu munena, [kudzakhala] nyengo yabwino: popeza thambo lafiyira.
  532. Mat 16:3 Ndipo m’mawa, [Kudzakhala] nyengo yoyipa lero: popeza thambo lafiyira ndi mlengalenga mwawopsa. Wonyenga [inu] mudziwa kuzindikira za nkhope yake ya thambo; koma inu simungathe [kuzindikira] zizindikiro za nthawizo.
  533. Mat 16:4 Mbadwo woyipa ndi wachigololo ufunafuna chizindikiro; ndipo sichidzaperekedwa chizindikiro [china] kwa uwo, koma chizindikiro cha mneneri Yona. Ndipo iye adawasiya iwo, ndipo ananyamuka.
  534. Mat 16:5 Ndipo pamene wophunzira ake adafika tsidya linalo, iwo adayiwala kutenga mkate.
  535. Mat 16:6 ¶Kenaka Yesu adati kwa iwo, Samalani ndipo chenjerani mupewe chofufumitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.
  536. Mat 16:7 Ndipo iwo adafunsana maganizo pakati pawo, nanena kuti, Ndi chifukwa chakuti sitidatenge mikate.
  537. Mat 16:8 [Chimene] pomwe Yesu adachidziwa, iye adati kwa iwo, Inu a chikhulupiriro chaching’ono, mufunsana maganizo chifukwa chiyani pakati panu, chifukwa inu simudatenge mkate?
  538. Mat 16:9 Kodi inu simumvetsetsabe kufikira tsopano, kapena kukumbukira mikate isanu ija ya zikwi zisanu, ndi madengu angati inu mudatola?
  539. Mat 16:10 Kapenanso mikate isanu ndi iwiri ija ya zikwi zinayi, ndi madengu angati amene inu mudatola?
  540. Mat 16:11 Bwanji nanga inu simukumvetsetsa kuti ine sindidanena [ichi] kwa inu zokhudza mkate, kuti inu musamale chofufumitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki?
  541. Mat 16:12 Kenaka adamvetsetsa iwo momwe mwakuti iye sadawawuza [iwo] kuti achejere za chofufumitsa mkate, koma za chiphunzitso cha Afarisi ndi cha Asaduki.
  542. Mat 16:13 ¶Pamene Yesu adadza m’dziko la Kayisareya wa Filipi, iye adafunsa wophunzira ake, kunena kuti, Anthu anena kuti Mwana wamwamuna wa munthu ndiye yani?
  543. Mat 16:14 Ndipo iwo adati, Ena [ati ndinu] Yohane Mbatizi; koma ena Eliya: ndipo enanso Yeremiya, kapena m’modzi wa aneneri.
  544. Mat 16:15 Iye anena kwa iwo, Koma inu mukuti ndine yani?
  545. Mat 16:16 Ndipo Simoni Petro adayankha ndipo anati, Inu ndinu Khristu Mwana wamwamuna wa Mulungu wamoyo.
  546. Mat 16:17 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Ndiwe wodala iwe, Simoni BarYona: pakuti thupi ndi mwazi sizidawululira [ichi] kwa iwe, koma Atate wanga amene ali kumwamba.
  547. Mat 16:18 Ndiponso ine ndinena kwa iwe, Kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ine ndidzamanga mpingo wanga; ndipo zipata za nyanja ya moto sizidzawugonjetsa uwo.
  548. Mat 16:19 Ndipo ine ndidzakupatsa iwe mafungulo a ufumu wa kumwamba: ndipo chilichonse chimene iwe uchimanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa kumwamba: ndipo chilichonse chimene udzachimasula pa dziko lapansi chidzakhala chomasulidwa kumwamba.
  549. Mat 16:20 Kenaka iye adalamulira wophunzira ake kuti asawuze munthu aliyense kuti iye ndiye Yesu amene ali Khristu.
  550. Mat 16:21 ¶Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kuwawonetsa wophunzira ake, momwe kuyenera kuti iye amuke ku Yerusalemu, ndi kukanzunzidwa ndi zinthu zambiri ndi akulu ndi ansembe akulu ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuwukitsidwa kwa akufa tsiku lachitatu.
  551. Mat 16:22 Kenaka Petro adamtenga iye, ndipo anayamba kumdzudzula iye, kunena kuti, Chikhale kutali ndi inu, Ambuye: ichi sichidzachitika kwa inu.
  552. Mat 16:23 Koma iye adatembenuka, ndipo anati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana: ndiwe chokhumudwitsa kwa ine: pakuti suganizira za Mulungu koma za anthu.
  553. Mat 16:24 ¶Kenaka Yesu adati kwa wophunzira ake, Ngati [munthu] aliyense afuna kudza pambuyo panga, iye adzikane mwini yekha, ndipo atenge mtanda wake, ndi kutsata ine.
  554. Mat 16:25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya: ndipo aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha ine adzawupeza.
  555. Mat 16:26 Pakuti munthu adzapindulanji, ngati iye alandira dziko lonse, ndi kutaya moyo wake? Kapena munthu adzapereka chiyani chosinthana ndi moyo wake?
  556. Mat 16:27 Pakuti Mwana wamwamuna wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo kenaka iye adzapereka mphotho kwa munthu aliyense monga mwa ntchito zake.
  557. Mat 16:28 Ndithudi ndinena kwa inu, Kuti alipo ena akuyima pano, amene sadzalawa imfa, kufikira iwo adzawona Mwana wamwamuna wa munthu akudza mu ufumu wake.
  558. Mat 17:1 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi Yesu adatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mbale wake, ndipo anawatengera iwo pa phiri lalitali pawokha.
  559. Mat 17:2 Ndipo iye adasandulika pamaso pawo: ndipo nkhope yake idawala monga dzuwa, ndi chovala chake chidakhala choyera mbuu monga kuwala.
  560. Mat 17:3 Ndipo, tawonani, adawoneka kwa iwo Mose ndi Eliya alikuyankhula ndi iye.
  561. Mat 17:4 Kenaka Petro adayankha, ndipo anati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kwa ife kuti tikhale pano: ngati inu mulola, tiyeni timange ife pano mahema atatu; imodzi ya inu, ndi imodzi ya Mose, ndi imodzi ya Eliya.
  562. Mat 17:5 Akali kuyankhula iye, ndipo tawonani, mtambo wowala udawaphimba iwo: ndipo tawonani mawu otuluka mumtambo, amene adati, Uyu ndiye Mwana wanga wamwamuna wokondedwa, amene mwa iyeyu ine ndisangalatsidwa bwino; inu mverani iye.
  563. Mat 17:6 Ndipo pamene wophunzira adamva [ichi], iwo adagwa nkhope zawo pansi, ndipo anawopa kwakukulu.
  564. Mat 17:7 Ndipo Yesu adadza ndipo anawakhudza iwo, ndipo anati, Ukani, ndipo musawopa.
  565. Mat 17:8 Ndipo pamene iwo adakweza maso awo, sadawona munthu aliyense, kupatula Yesu yekha.
  566. Mat 17:9 Ndipo pamene adali kutsika pa phiri, Yesu adawalamulira iwo, kunena kuti, Musakawuze masomphenyawo munthu aliyense, kufikira Mwana wamwamuna wa munthu atadzawuka kwa akufa.
  567. Mat 17:10 Ndipo wophunzira ake adamfunsa iye, nanena kuti, Ndipo bwanji alembi anena kuti Eliya ayenera kudza poyamba?
  568. Mat 17:11 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Eliya zowonadi ayenera ayambe kudza, ndi kudzabwezeretsa zinthu zonse.
  569. Mat 17:12 Koma ndinena kwa inu, Kuti Eliya wadza kale, ndipo iwo sadamdziwa iye, koma achitira kwa iye chilichonse chimene iwo adachikhumba. Chimodzimodzinso Mwana wamwamuna wa munthu adzazunzidwa ndi iwo.
  570. Mat 17:13 Kenaka wophunzira adazindikira kuti adayankhula kwa iwo za Yohane Mbatizi.
  571. Mat 17:14 ¶Ndipo pamene iwo adadza ku khamulo, kudafika kwa iye munthu [wina], anam’gwadira iye, ndipo anati,
  572. Mat 17:15 Ambuye, chitirani chifundo mwana wanga wamwamuna: pakuti adwala khunyu, ndipo azunzika koyipa: pakuti kawiri kawiri amagwa pamoto, ndi kawiri kawiri m’madzi.
  573. Mat 17:16 Ndipo ine ndinadza naye kwa wophunzira anu, ndipo iwo sadathe kumchiritsa iye.
  574. Mat 17:17 Kenaka Yesu adayankha ndipo anati, Mbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wamphulupulu, kodi ndidzakhala ndi inu nthawi yayitali bwanji? Ndidzakupirirani inu kwa nthawi yayitali bwanji? M’bweretseni iye kuno kwa ine.
  575. Mat 17:18 Ndipo Yesu adadzudzula chiwandacho; ndipo chidatuluka mwa iye: ndipo mwanayo adachiritsidwa kuyambira ora lomwero.
  576. Mat 17:19 Kenaka wophunzira adadza kwa Yesu ali pa yekha, ndipo anati, Chifukwa chiyani ife sitidakhoza kuchitulutsa icho?
  577. Mat 17:20 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Chifukwa cha kusakhulupirira kwanu: pakuti ndithudi ndinena kwa inu, Ngati inu mukhala nacho chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, inu mudzati kwa phiri ili, Chokapo upite malo aja; ndipo ilo lidzachokapo; ndipo palibe kanthu kadzakhala kosatheka kwa inu.
  578. Mat 17:21 Komabe mtundu uwu sutuluka wamba koma ndi pemphero ndi kusala kudya.
  579. Mat 17:22 ¶Ndipo m’mene adali kukhalabe m’Galileya, Yesu adanena kwa iwo, Mwana wamwamuna wa munthu adzaperekedwa m’manja a anthu:
  580. Mat 17:23 Ndipo iwo adzamupha iye, ndipo tsiku lachitatu iye adzawukitsidwanso. Ndipo iwo adali ndi chisoni chachikulu.
  581. Mat 17:24 ¶Ndipo pamene iwo adafika ku Kaperenamu, iwo amene ankalandira [ndalama] za msonkho adadza kwa Petro, ndipo adati, Kodi Mphunzitsi wanu salipira msonkho?
  582. Mat 17:25 Iye anena, Inde. Ndipo pamene iye analowa m’nyumba, Yesu adatsogola kumlankhula iye, nanena kuti, Uganiza bwanji iwe, Simoni? Alandira msonkho kwa yani mafumu a dziko lapansi? Kwa ana awo kodi, kapena kwa alendo?
  583. Mat 17:26 Petro anena kwa iye, Kwa alendo. Yesu anena kwa iye, Ndiye kuti anawo ali a ufulu.
  584. Mat 17:27 Posawerengera zimenezo, kuti mwina ife tisawakhumudwitse iwo, pita iwe, kunyanja, ndipo ukaponye mbedza, ndipo utenge nsomba yoyamba kuyiwedza; ndipo pamene iwe wayikanula pakamwa pake, iwe udzapezamo ndalama: tenga imeneyo; ndipo uwapatse iwo ya ine ndi iwe.
  585. Mat 18:1 Nthawi yomweyo wophunzira adadza kwa Yesu, nanena kuti, Ndani ali wamkulu mu ufumu wa kumwamba?
  586. Mat 18:2 Ndipo Yesu adayitana kamwana kakang’ono kwa iye, ndipo anakayimika pakati pawo,
  587. Mat 18:3 Ndipo adati, Ndithudi ndinena kwa inu, Pokhapokha ngati inu mutembenuka, ndi kukhala ngati tiana, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.
  588. Mat 18:4 Choncho aliyense amene adzadzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wamkulu kwambiri mu ufumu wa kumwamba.
  589. Mat 18:5 Ndipo aliyense amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka m’dzina langa alandira ine.
  590. Mat 18:6 Koma aliyense amene adzachimwitsa kamodzi ka tiana iti timene tikhulupirira mwa ine, kunali kwabwino kwa iye kuti mphero yamwala ikadakolowekedwa m’khosi mwake, ndi [kuti] iye akadamizidwa kwakuya kwa nyanja.
  591. Mat 18:7 ¶Tsoka kwa dziko lapansi chifukwa cha zochimwitsa! Pakuti kuyenera kuti zochimwitsa zidze; koma tsoka kwa munthu amene chochimwitsacho chidza ndi iye!
  592. Mat 18:8 Mwa ichi ngati dzanja lako kapena phazi lako zikuchimwitsa iwe, uzidule, ndi kuzitaya [izo] kuchoka kwa iwe: n’kwabwino kuti ulowe moyo wolumala kapena wopanda ziwalo, koposa uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri kuponyedwa m’moto wosantha.
  593. Mat 18:9 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulikolowole, ndipo ulitaye [ilo] kulichotsa kwa iwe: n’kwabwino kwa iwe kuti ulowe m’moyo ndi diso limodzi, koposa uli ndi maso awiri kuponyedwa mu nyanja ya moto.
  594. Mat 18:10 Yanga’anirani kuti musanyoza m’modzi wa tating’ono iti; pakuti ine ndinena kwa inu, Kuti kumwamba angelo a ito apenya nthawi zonse chipenyere nkhope ya Atate wanga amene ali kumwamba.
  595. Mat 18:11 Pakuti Mwana wamwamuna wa munthu wadza kudzapulumutsa chimene chinatayikacho.
  596. Mat 18:12 Mukuganiza motani inu? Ngati munthu ali nazo nkhosa zana limodzi, ndipo imodzi ya izo isokera, kodi saleka zija makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, ndipo apita ku mapiri, ndipo afunafuna imene yasokerayo?
  597. Mat 18:13 Ndipo ngati kuli kotero kuti ayipeza iyo, Ndithudi ndinena kwa inu, iye akondwera koposa chifukwa cha [nkhosa] imeneyo, koposa makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi zimene sizinasochera.
  598. Mat 18:14 Chomwecho si chili chifuniro cha Atate wanu amene ali kumwamba, kuti m’modzi wa tating’ono iti atayike.
  599. Mat 18:15 ¶Kupitirira apo ngati mbale wako akadzakuchimwira iwe, pita ndi kukamuwuza iye cholakwa chake pakati pa iwe ndi iye panokha: ngati akumvera iwe, iwe wam’pindula mbale wako.
  600. Mat 18:16 Koma ngati sakumvera [iwe, ndiye] utenge pamodzi ndi iwe wina m’modzi kapena awiri wowonjezapo, kuti pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu atsimikizidwe mawu onse.
  601. Mat 18:17 Ndipo ngati iye anyalanyaza kumvera iwo, uwuze [ichi] mpingo: ndipo ngati iye anyalanyaza kumveranso mpingowo, akhale kwa iwe monga munthu wachikunja ndi wokhometsa msonkho.
  602. Mat 18:18 Ndithudi ndinena kwa inu, Chilichonse chimene inu mukachimanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa kumwamba: ndipo chilichonse chimene inu mukachimasula pa dziko lapansi chidzakhala chomasulidwa kumwamba.
  603. Mat 18:19 Kenanso ine ndinena kwa inu, Kuti ngati awiri a inu adzavomerezana pansi pano mokhudzana ndi chinthu chilichonse chimene iwo adzachipempha, chidzachitidwa kwa iwo ndi Atate wanga amene ali kumwamba.
  604. Mat 18:20 Pakuti pamene pali awiri kapena atatu akasonkhana m’dzina langa, komweko ine ndiri pakati pawo.
  605. Mat 18:21 ¶Kenaka anadza Petro kwa iye, ndipo anati, Ambuye, ndi kangati kamene mbale wanga adzandilakwira ine, ndipo ine ndimkhululukire iye? Kufikira kasanu ndi kawiri?
  606. Mat 18:22 Yesu adanena kwa iye, Ine sindinena kwa iwe, Kufikira kasanu ndi kawiri: koma, Kufikira makumi asanu ndi awiri kuchulukitsidwa kasanu ndi kawiri.
  607. Mat 18:23 ¶Choncho ufumu wa kumwamba ufanizidwa ndi mfumu ina, imene idafuna kuchita chiwerengero cha za antchito ake.
  608. Mat 18:24 Ndipo pamene adayamba kuwerengera, adadza naye kwa iye wina, amene anali naye ngongole ya [ndalama za] matalente zikwi khumi.
  609. Mat 18:25 Koma popeza iye adasowa kanthu kakulipira, mbuye wake adalamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana, ndi zonse zimene adali nazo, ndi kuti kulipira kukachitidwe.
  610. Mat 18:26 Choncho wantchitoyo adagwa pansi, ndipo analambira, nanena kuti, Mbuye, khalani ndi chipiriro ndi ine, ndipo ndidzakulipirani inu zonse.
  611. Mat 18:27 Kenaka mbuye wa wantchitoyo adagwidwa ndi chisoni, ndipo anam’masula iye, ndipo anam’khululukira ngongoleyo.
  612. Mat 18:28 Koma wantchito yemweyu, adatuluka ndipo anapeza wina wa antchito anzake, yemwe adakongola kwa iye ndalama zana limodzi: ndipo iye anam’gwira, ndi kumgwira [iye] pakhosi, nanena kuti, Ndibwezere ine zimene iwe udandikongola.
  613. Mat 18:29 Ndipo wantchito mzakeyo adagwa pansi pa mapazi ake, ndipo anampempha iye, nanena kuti, Khalani ndi chipiriro ndi ine, ndipo ndidzakubwezerani inu zonse.
  614. Mat 18:30 Ndipo iye sadafuna: koma adapita ndi kumponya iye m’nyumba ya ndende, kufikira atadzam’bwezera ngongole.
  615. Mat 18:31 Kotero pamene antchito anzake adawona zochitikazo, adagwidwa ndi chisoni chachikulu, ndipo anadza ndi kufotokozera mbuye wawo zonse zimene zidachitidwa.
  616. Mat 18:32 Kenaka mbuye wake, zitachitika izi adamuyitana iye, nanena kwa iye, Iwe wantchito woyipa, ine ndidakukhululukira iwe ngongole yonse ija, chifukwa iwe udandipempha ine:
  617. Mat 18:33 Kodi iwenso sukadamchitira wantchito mzako chisoni, monga inenso ndidali ndi chisoni ndi iwe?
  618. Mat 18:34 Ndipo mbuye wake adapsa mtima, ndipo anampereka iye kwa azunzi, kufikira atalipira zonse zomwe zinali zoyenera kwa iye.
  619. Mat 18:35 Chomwecho Atate wanga wa kumwamba adzachitanso kwa inu, ngati inu kuchokera m’mitima mwanu simukhululukira aliyense mbale wake machimo awo.
  620. Mat 19:1 Ndipo kudachitika pamene, [kuti] Yesu adatha kunena zonena zimenezi, iye adanyamuka kuchoka ku Galileya, ndipo anadza ku dziko la Yudeya la kupitirira Yordano;
  621. Mat 19:2 Ndipo makamu akulu adamtsata iye; ndipo iye adawachiritsa iwo kumeneko.
  622. Mat 19:3 ¶Afarisi adadzanso kwa iye, kumuyesa iye, ndipo ananena kwa iye, Kodi n’kololedwa kuti bambo asudzule mkazi wake pa chifukwa chilichonse?
  623. Mat 19:4 Ndipo iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Kodi inu simudawerenga kuti iye amene adapanga [iwo] pachiyambi, adawapanga iwo mwamuna ndi mkazi.
  624. Mat 19:5 Ndipo adati, pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake, ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake: ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi?
  625. Mat 19:6 Mwa ichi salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.
  626. Mat 19:7 Iwo anena kwa iye, Nanga n’chifukwa chiyani Mose adalamulira kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumsudzula iye?
  627. Mat 19:8 Iye adanena kwa iwo, Chifukwa cha kuwuma mitima kwanu Mose adakulolezani kusudzula akazi anu: koma kuchokera pachiyambi sizidali choncho.
  628. Mat 19:9 Ndipo ine ndinena kwa inu, Aliyense amene adzasudzula mkazi wake, pokhapokha [chikhale] chifukwa [ichi] cha chiwerewere, ndi kudzakwatira wina, achita chigololo: ndi iye amene akwatira wosudzulidwayo achita chigololo.
  629. Mat 19:10 ¶Wophunzira ake anena kwa iye, Ngati nkhani ili choncho kwa bambo ndi mkazi [wake], sikuli kwabwino kukwatira.
  630. Mat 19:11 Koma iye adati kwa iwo, [Anthu] onse sangathe kulandira chonena ichi, kupatula [iwo] omwe kwa iwo chapatsidwa.
  631. Mat 19:12 Pakuti pali ena osabala, amene anabadwa wotero kuchokera m’mimba ya amayi [awo]: ndipo pali osabala ena, amene adapangidwa ndi anthu: ndipo pali osabala ena amene adadzipanga wokha chifukwa cha ufumu wa kumwamba. Amene angathe kulandira [ichi], achilandire [ichi].
  632. Mat 19:13 ¶Kenaka adadza nato tiana tating’ono kwa iye, kuti iye ayike manja [ake] pa ito, ndi kupemphera: ndipo wophunzirawo adadzudzula iwo.
  633. Mat 19:14 Koma Yesu adati, Lolani tiana, ndipo musatikanize, kudza kwa ine: chifukwa ufumu wa kumwamba uli wa totere.
  634. Mat 19:15 Ndipo iye adayika manja [ake] pa ito, ndipo ananyamuka kumeneko.
  635. Mat 19:16 ¶Ndipo, tawonani, m’modzi adadza ndipo anati kwa iye, Ambuye wabwino, chabwino n’chiti ine ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?
  636. Mat 19:17 Ndipo iye adati kwa iye, Unditcha ine wabwino bwanji? Kulibe wabwino koma m’modzi, [ameneyo ndiye] Mulungu: koma ngati ufuna kulowa m’moyo, sunga malamulo.
  637. Mat 19:18 Iye anena kwa iye, Ati? Yesu adati, Iwe usaphe, Iwe usachite chigololo, Iwe usabe, Iwe usachite umboni wonama,
  638. Mat 19:19 Lemekeza atate wako ndi amayi [wako:] ndipo, Iwe uzikonda woyandikana naye monga udzikonda iwe mwini.
  639. Mat 19:20 Bambo wamng’onoyo adanena kwa iye, Zinthu izi zonse ine ndazisunga kuyambira ku unyamata wanga mpaka kukula: tsono ndisowanso chiyani?
  640. Mat 19:21 Yesu adanena kwa iye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita [ndipo] kagulitse zomwe iwe uli nazo, ndipo upatse aumphawi, ndipo iwe udzakhala ndi chuma kumwamba: ndipo ukadze [ndipo] unditsate.
  641. Mat 19:22 Koma pamene bambo wamng’noyo adamva chonena chimenecho, iye adachoka kupita ali wachisoni: pakuti adali nacho chuma chambiri.
  642. Mat 19:23 ¶Kenaka Yesu adati kwa wophunzira ake, Ndithudi ndinena kwa inu, Kuti munthu wa chuma adzalowa movutika mu ufumu wa kumwamba.
  643. Mat 19:24 Ndipo kenanso ine ndinena kwa inu, N’kwapafupi kuti ngamira ipyole pa diso la singano, koposa munthu wa chuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.
  644. Mat 19:25 Pamene wophunzira ake adamva [ichi], adazizwa kwambiri, nanena kuti, Ndani tsono amene angapulumuke?
  645. Mat 19:26 Koma Yesu adawayang’ana [iwo, ndipo] anati kwa iwo, Ndi anthu ichi sichitheka; koma ndi Mulungu zonse zitheka.
  646. Mat 19:27 ¶Kenaka adayankha Petro ndipo anati kwa iye, Tawonani, ife tidasiya zonse, ndi kutsata inu; kodi choncho tidzakhala ndi chiyani?
  647. Mat 19:28 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ndithudi ine ndinena kwa inu, Kuti inu amene mwanditsata ine, m’kubadwanso pamene Mwana wamwamuna wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso mudzakhala pa mipando yachifumu khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
  648. Mat 19:29 Ndipo aliyense amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena mkazi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zochulukitsidwa ndi zana, nadzalowa moyo wosatha.
  649. Mat 19:30 Koma ambiri [omwe ali] woyamba adzakhala a kumapeto, ndi a kumapeto [adzakhala] woyamba.
  650. Mat 20:1 Pakuti ufumu wa kumwamba ufanana ndi munthu [yemwe ali] mwini banja, amene adatuluka m’mamawa kukalembera antchito m’munda wake wa mphesa.
  651. Mat 20:2 Ndipo pamene adapangana ndi antchito pa ndalama imodzi pa tsiku, iye adawatumiza iwo ku munda wake wa mphesa.
  652. Mat 20:3 Ndipo iye adatuluka pa ora la chitatu, ndipo anawona ena atangoyima pa malo wochitira malonda.
  653. Mat 20:4 Ndipo adati kwa iwo; Pitani inunso ku munda wa mphesa, ndipo chimene chili choyenera ine ndidzakupatsani. Ndipo iwo adapita pa njira yawo.
  654. Mat 20:5 Kenanso iye adatuluka pafupifupi ora la chisanu ndi limodzi ndinso la chisanu ndi chinayi, ndipo anachita chimodzimodzi.
  655. Mat 20:6 Ndipo pa ora la khumi ndi limodzi iye adatuluka, ndipo anapeza ena atangoyima chabe, ndipo adati kwa iwo, Chifukwa chiyani mwangoyima pano chabe tsiku lonse?
  656. Mat 20:7 Iwo adanena kwa iye, Chifukwa palibe munthu adatilemba ntchito. Iye ati kwa iwo, Pitani inunso ku mundawo wa mphesa; ndipo chimene chili choyenera [chimenecho] inu mudzalandira.
  657. Mat 20:8 Ndipo pakufika madzulo, mwini munda adati kwa kapitawo wake, Kayitane antchito, ndipo uwapatse iwo malipiro [awo], kuyambira kwa womalizira kufikira kwa woyamba.
  658. Mat 20:9 Ndipo pamene adafika [iwo wolembedwa] pa ora la khumi ndi limodzi, iwo analandira munthu aliyense khobiri.
  659. Mat 20:10 Koma pamene woyamba adadza, adalingalira kuti adzalandira zambiri; ndipo iwonso adalandira chimodzimodzi munthu aliyense khobiri.
  660. Mat 20:11 Ndipo m’mene iwo adalandira [ilo], iwo anang’ung’udza motsutsana ndi mbuye mwini wa nyumba wabwino,
  661. Mat 20:12 Nanena kuti, Awa omarizira adagwira [chabe] ntchito ora limodzi, ndipo inu mwawalinganiza iwo ndi ife, amene tidapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake kwa tsiku.
  662. Mat 20:13 Koma iye adayankha m’modzi wa iwo, ndipo adati, Mzanga, ine sindikuchitira iwe cholakwa chilichonse: kodi iwe sudagwirizana ndi ine pa khobiri limodzi?
  663. Mat 20:14 Tenga [lomwe liri] lako, ndipo umuke pa njira yako: ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira, monga kwa iwe.
  664. Mat 20:15 Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi za ine mwini? Kodi diso lako ndi loyipa, chifukwa ine ndiri wabwino?
  665. Mat 20:16 Kotero omalizira adzakhala woyamba, ndipo woyamba womalizira: pakuti ambiri akhala woyitanidwa, koma wosankhidwa ndi wochepa.
  666. Mat 20:17 ¶Ndipo pamene Yesu adali kukwera ku Yerusalemu adatenga wophunzira khumi ndi awiri aja napita nawo pa wokha panjira, ndipo adati kwa iwo,
  667. Mat 20:18 Tawonani, tikwera kupita ku Yerusalemu; ndipo Mwana wamwamuna wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi kwa alembi; ndipo iwo adzamuweruza kuti ayenera kufa,
  668. Mat 20:19 Ndipo adzam’pereka kwa anthu Amitundu kuti am’nyoze, ndi kum’kwapula, ndi kum’pachika [iye]: ndipo pa tsiku lachitatu iye adzawuka.
  669. Mat 20:20 ¶Kenaka adadza kwa iye amayi awo a ana a Zebedayo ndi ana ake amuna omwe, anamlambira iye, ndi kumpempha kanthu kena kwa iye.
  670. Mat 20:21 Ndipo adati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye anena kwa iye, Lolani kuti ana anga amuna awiriwa akhoze kukhala, m’modziyo ku dzanja lamanja, ndi wina ku lamanzere, mu ufumu wanu.
  671. Mat 20:22 Koma Yesu adayankha ndipo anati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho chimene ine nditi ndidzamwera, ndikubatizidwa ubatizo umene ine ndibatizidwa nawo? Iwo adanena kwa iye, ife tikhoza.
  672. Mat 20:23 Ndipo iye anena kwa iwo, Chikho changa ndithu inu mudzamweradi, ndikubatizidwa ndi ubatizo umene ine ndibatizidwa nawo: koma kukhala ku dzanja lamanja kwanga ndi ku lamanzere, sikuli kwa ine kupatsa, koma [kudzapatsidwa kwa iwo omwe] kwakonzedweratu ndi Atate wanga.
  673. Mat 20:24 Ndipo m’mene khumiwo adamva [ichi], adapsa mtima ndi abale awiriwo.
  674. Mat 20:25 Koma Yesu adawayitanira iwo [kwa iye], ndipo anati, Mudziwa kuti mafumu Amitundu amachita ufumu pa iwo, ndipo iwo amene ali akulu amachita ulamuliro pa iwo.
  675. Mat 20:26 Koma sikudzakhala chomwecho pakati pa inu: koma aliyense amene akufuna kukhala wamkulu mwa inu, mulole akhale mtumiki wanu;
  676. Mat 20:27 Ndipo aliyense amene adzakhala wolamulira mwa inu, mulole akhale wotumikira wanu;
  677. Mat 20:28 Monga Mwana wamwamuna wa munthu sanadza kuti atumikiridwe, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo chifukwa cha ambiri.
  678. Mat 20:29 Ndipo pamene iwo analikunyamuka ku Yeriko, khamu lalikulu lidamtsata iye.
  679. Mat 20:30 ¶Ndipo tawonani, amuna akhungu awiri adakhala m’mphepete mwa njira, m’mene iwo adamva kuti Yesu adalikupitirapo, adafuwula, nanena kuti, Mutichitire ife chifundo, Ambuye, [inu] Mwana wamwamuna wa Davide.
  680. Mat 20:31 Ndipo khamulo lidawadzudzula iwo, chifukwa adayenera kukhala bata: koma iwo adafuwulitsa, nanena kuti, Mutichitire ife chifundo, Ambuye, [inu] Mwana wamwamuna wa Davide.
  681. Mat 20:32 Ndipo Yesu adayima, ndipo anawayitana iwo, ndipo anati. Kodi inu mufuna kuti ine ndikuchitireni chiyani?
  682. Mat 20:33 Iwo anena kwa iye, Ambuye, kuti maso anthu atseguke.
  683. Mat 20:34 Kotero Yesu adagwidwa ndi chifundo [pa iwo], ndipo adakhudza maso awo: ndipo posakhalitsa maso awo adalandira kupenya, ndipo iwo anamtsata iye.
  684. Mat 21:1 Ndipo pamene iwo adayandikira ku Yerusalemu, ndipo atafika ku Betifage, ku phiri la ma Olivi, kenaka Yesu adatuma wophunzira awiri,
  685. Mat 21:2 Nanena kwa iwo, Mukani ku mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo inu mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye: masulani [izo], ndipo mudze [nazo] kwa ine.
  686. Mat 21:3 Ndipo [munthu] wina aliyense akanena kanthu kwa inu, inu mudzati, Ambuye afuna izo; ndipo pomwepo adzazitumiza.
  687. Mat 21:4 Izi zonse zidachitidwa, kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi mneneri, kunena kuti,
  688. Mat 21:5 Tawuzani inu mwana wamkazi wa Ziyoni, Tawona, Mfumu yako idza kwa iwe, yofatsa, ndi yokwera pa bulu, ndi kamwana kake kakamuna ka bulu.
  689. Mat 21:6 Ndipo wophunzirawo adapita, ndipo anachita monga Yesu adawalamulira iwo;
  690. Mat 21:7 Ndipo anabwera ndi bulu, ndi mwana wake, ndipo anayika pa izo zovala zawo, ndipo anakhazika [iye] pamenepo.
  691. Mat 21:8 Ndipo chikhamu chachikulu kwambiri chidayala zovala zawo m’njiramo; ena anadula nthambi za mitengo, nazimwaza [izo] m’njiramo.
  692. Mat 21:9 Ndipo makamuwo amene adali patsogolo, ndi amene ankatsatira, adafuwula, kunena kuti, Hosana kwa Mwana wamwamuna wa Davide: Wodala [ali] iye amene akudza m’dzina la Ambuye; Hossana m’mwambamwamba!
  693. Mat 21:10 Ndipo m’mene adafika kulowa mu Yerusalemu, mzinda wonse udatekeseka, nanena kuti, Ndani uyu?
  694. Mat 21:11 Ndipo khamulo lidati, Uyu ndi Yesu mneneri wa ku Nazarete wa Galileya.
  695. Mat 21:12 ¶Ndipo Yesu adalowa ku kachisi wa Mulungu, ndipo anatulutsa kunja onse amene ankagulitsa ndi kugula malonda m’kachisimo, ndipo anagubuduza magome a wosintha ndalama, ndi mipando ya iwo amene ankagulitsa nkhunda.
  696. Mat 21:13 Ndipo adati kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo; koma inu mwayipanga kukhala phanga la mbava.
  697. Mat 21:14 Ndipo akhungu ndi wolumala adadza kwa iye ku kachisiko; ndipo iye adachiritsa iwo.
  698. Mat 21:15 Ndipo pamene ansembe akulu ndi alembi adawona zinthu zozizwitsa zimene iye adazichita, ndi ana alinkufuwula m’kachisimo, ndi kunena kuti, Hosana kwa Mwana wamwamuna wa Davide; iwo sadakondweretsedwe ndi pang’no pomwe.
  699. Mat 21:16 Ndipo adati kwa iye, Mulikumva kodi chimene awa ali kunena? Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Inde; kodi simudawerenga, Kutuluka mkamwa mwa makanda ndi woyamwa inu mwapangitsa matamando angwiro?
  700. Mat 21:17 ¶Ndipo iye adawasiya iwo, ndipo anatuluka mu mzinda napita ku Betane; ndipo anagona kumeneko.
  701. Mat 21:18 Ndipo m’mawa pamene iye adali kubwereranso ku mzinda, adamva njala.
  702. Mat 21:19 Ndipo pamene adawona mtengo wa mkuyu panjira, iye adafika pa mtengopo, ndipo anapeza popanda kanthu, koma masamba okha okha, ndipo anati iye kwa uwo, Pasadzabalenso chipatso pa iwe kuyambira tsopano ku nthawi zonse. Ndipo nthawi yomweyo mtengo wa mkuyuwo unafota.
  703. Mat 21:20 Ndipo pamene wophunzira adawona [ichi], iwo adazizwa, nanena kuti, Mtengo wa mkuyu udafota bwanji mwamsanga?
  704. Mat 21:21 Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Ndithudi ndinena kwa inu, Ngati inu mukhala nacho chikhulupiriro, ndi kusakayika ayi, inu simudzachita ichi chokha [chomwe chachitika] pa mtengo wa mkuyu ayi, komanso ngati inu mudzanena ku phiri ili, Tachotsedwa iwe, ndipo uponyedwe m’nyanja; chidzachitidwa.
  705. Mat 21:22 Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m’kupemphera, mukakhulupirira, inu mudzazilandira.
  706. Mat 21:23 ¶Ndipo pamene iye adafika kulowa m’kachisi, ansembe akulu ndi akulu a anthu adadza kwa iye pamene anali kuphunzitsa, ndipo ananena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani adakupatsani ulamuliro umenewu?
  707. Mat 21:24 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Inenso ndikufunsani inu chinthu chimodzi, chimene ngati inu mundiwuza, inenso chimodzimodzi ndikuwuzani inu ndi ulamuliro wotani ndizichita zinthu izi.
  708. Mat 21:25 Ubatizo wa Yohane, kodi udachokera kuti? Udachokera kumwamba, kapena kwa anthu? Koma iwo adafunsana maganizo ndi iwo eni, kunena kuti, Ife tikati, Uchokera kumwamba; iye adzati kwa ife, Chifukwa chiyani inu tsono simudakhulupirira iye?
  709. Mat 21:26 Koma ngati ife tikati, Kwa anthu; tiwopa anthu; pakuti onse amuyesa Yohane monga mneneri.
  710. Mat 21:27 Ndipo iwo adamuyankha Yesu, ndipo anati, Ife sitinganene. Ndipo iyenso adanena kwa iwo, Sindikuwuzani inenso ndi ulamuliro wotani ndichita zinthu izi.
  711. Mat 21:28 ¶Koma muganiza chiyani inu? Munthu [wina] adali nawo ana amuna awiri; ndipo iye anadza kwa woyamba, ndipo anati Mwana wamwamuna, pita kagwire lero ntchito ku munda wanga wa mphesa.
  712. Mat 21:29 Iye adayankha ndipo anati, Ine sindifuna: koma pambuyo pake iye adalapa, ndipo anapita.
  713. Mat 21:30 Ndipo adadza kwa wachiwiriyo, ndipo ananena chimodzimodzi. Ndipo iye adayankha ndipo anati, ine [ndipita], mbuye: koma sadapite ayi.
  714. Mat 21:31 Ndani wa awiriwo adachita chifuniro cha atate [wake]? Iwo anena kwa iye, Woyambayo. Yesu anena kwa iwo, Ndithudi ndinena kwa inu, Kuti wokhometsa misonkho ndi akazi a chiwerewere apita kulowa mu ufumu wa Mulungu patsogolo pa inu.
  715. Mat 21:32 Popeza Yohane adadza kwa inu m’njira ya chilungamo, ndipo inu simudamkhulupirira iye ayi: koma amisonkho ndi akazi a chiwerewere adamukhulupirira iye: ndipo inu, m’mene inu mudachiwona, simudalapa pambuyo pake, kuti mukhoze kukhulupirira iye.
  716. Mat 21:33 ¶Imvani fanizo lina: Padali munthu mwini banja, amene adalima munda wa mphesa, ndipo anawuzunguliza linga, ndipo anakumba umo mofinyiramo mphesa, ndipo anamanga nsanja, ndipo anawubwereketsa kwa wolima munda, ndipo anapita ku dziko lakutali.
  717. Mat 21:34 Ndipo pamene nthawi ya chipatso idayandikira, iye adatumiza antchito ake kwa wolima munda aja, kuti iwo akakhoze kulandirako zipatso zake.
  718. Mat 21:35 Ndipo wolimawo adatenga antchito akewo, ndipo anampanda m’modzi, ndipo wina anamupha, ndipo wina anamponya miyala.
  719. Mat 21:36 Kenanso, adatumiza antchito ena ochuluka kuposa woyambawo: ndipo adawachitira iwo chimodzimodzi.
  720. Mat 21:37 Koma potsiriza pa onse iye adatumiza kwa iwo mwana wake wamwamuna, kunena kuti, Iwo adzalemekeza mwana wanga wamwamuna.
  721. Mat 21:38 Koma pamene wolima mundawo adawona mwana wamwamunayo, adanena pakati pawo, Uyo ndiye wolandira cholowa; bwerani, tiyeni timuphe iye, ndipo ife tiyeni titenge pa cholowa chake.
  722. Mat 21:39 Ndipo adamgwira iye, ndipo anamponya [iye] kunja kwa munda, ndipo anamupha [iye].
  723. Mat 21:40 Choncho pamene mbuye wa munda abwera, kodi iye adzachitira chiyani wolima mundawo?
  724. Mat 21:41 Iwo adanena kwa iye, Iye adzawawononga moyipa anthu woyipawo, ndipo adzapereka munda [wakewo] kwa wolima munda ena, amene adzambwezera iye zipatso mu nyengo zake.
  725. Mat 21:42 Yesu ati kwa iwo, Kodi inu simudawerenga konse m’malemba, Mwala umene womanga nyumba adawukana, womwewo wakhala mutu wa pa ngodya: uku ndi kuchita kwa Ambuye ndipo kuli kozizwitsa m’maso mwathu?
  726. Mat 21:43 Choncho ine ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, ndipo udzapatsidwa kwa fuko la kupatsa zipatso zake.
  727. Mat 21:44 Ndipo aliyense amene adzagwa pa mwala uwu adzaphwanyika: koma pa aliyense amene udzamgwera, udzampera iye monga ufa.
  728. Mat 21:45 Ndipo pamene akulu ansembe ndi Afarisi adali atamva mafanizo ake, iwo adazindikira kuti iye adalankhula za iwo.
  729. Mat 21:46 Ndipo pamene adafuna kumgwira iye, iwo adawopa khamu, chifukwa iwo adamuyesa iye mneneri.
  730. Mat 22:1 Ndipo Yesu adayankha ndipo anayankhulanso kwa iwo m’mafanizo, ndipo anati,
  731. Mat 22:2 Ufumu wa kumwamba ufanana ndi mfumu ina, imene idakonzera ukwati mwana wake wamwamuna.
  732. Mat 22:3 Ndipo anatumiza antchito ake kuti akayitane iwo amene anayitanidwa ku ukwati umenewo: ndipo iwo sadafuna kudza.
  733. Mat 22:4 Kenanso, iye adatumizanso antchito ena, nanena kuti, Uzani iwo amene ali oyitanidwawo, Tawonani, ine ndakonza mgonero wanga: ng’ombe zanga ndi nyama zonenepa [zanga] zaphedwa, ndipo zinthu zonse ziri zokonzedwa: bwerani ku ukwati.
  734. Mat 22:5 Koma iwo adapeputsa za [ichi], ndipo anapita njira zawo, m’modzi ku munda wake, wina ku malonda ake:
  735. Mat 22:6 Ndipo wotsala adagwira antchito ake, ndipo anawachitira [iwo] chipongwe, ndi kuwapha [iwo].
  736. Mat 22:7 Koma pamene mfumu idamva [za zimenezo], iyo idakwiya: ndipo adatuma asirikali ake, ndipo anawononga ambanda aja, ndi kutentha mzinda wawo.
  737. Mat 22:8 Kenaka iyo idanena kwa antchito ake, Za ukwati tsopano zakonzedwa, koma iwo amene anayitanidwa si anali woyenera.
  738. Mat 22:9 Choncho pitani inu ku misewu yaikuluikulu, ndipo ambiri monga mudzawapeza, ayitaneni ku ukwatiwu.
  739. Mat 22:10 Kotero antchitowo adapita ku misewu yaikuluikulu, ndipo anasonkhanitsa onse ambiri monga adawapeza, woyipa ndi abwino: ndipo ukwatiwo udadzala ndi alendo woyitanidwa.
  740. Mat 22:11 ¶Ndipo pamene mfumuyo idabwera kudzawona alendo woyitanidwawo, iye adapenya momwemo munthu amene sadavala chovala cha ukwati;
  741. Mat 22:12 Ndipo adanena kwa iye, Bwenzi, wabwera iwe bwanji muno wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye adalibe mawu.
  742. Mat 22:13 Kenaka mfumu idati kwa antchitowo, Mum’mange iye manja ndi miyendo, ndipo mumtenge, ndi kumponya [iye] ku mdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukuta mano.
  743. Mat 22:14 Pakuti ambiri ayitanidwa, koma wochepa [ndiwo] asankhidwa.
  744. Mat 22:15 ¶Kenaka adapita Afarisi, ndipo anachita upo wa kumkolera iye m’kuyankhula [kwake].
  745. Mat 22:16 Ndipo adatumiza kwa iye wophunzira awo pamodzi ndi Aherode, nanena kuti, Ambuye, ife tidziwa kuti inu muli wowona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu mowona, ndipo simusamala [munthu] aliyense: pakuti, simuyang’ana mawonekedwe a anthu.
  746. Mat 22:17 Choncho mutiwuze ife, Muganiza chiyani inu? Kodi kuloledwa kupatsa msonkho wa Kayisara, kapena iyayi?
  747. Mat 22:18 Koma Yesu adadziwa kuyipa kwawo, ndipo anati, Bwanji inu mundiyesa ine, wonyenga [inu]?
  748. Mat 22:19 Tandiwonetsani ine ndalama ya msonkho. Ndipo iwo adadza nayo kwa iye ndalama imodzi.
  749. Mat 22:20 Ndipo iye adati kwa iwo, N’chayani chithunzithunzi ichi ndikulemba kwake?
  750. Mat 22:21 Iwo anena kwa iye, Cha Kayisara. Kenaka iye adati kwa iwo, Choncho patsani kwa Kayisara zinthu zimene ziri za Kayisara; ndi kwa Mulungu zinthu zimene ziri za Mulungu.
  751. Mat 22:22 Pamene iwo adamva [mawu awa], adazizwa, ndipo anamsiya iye, ndipo ananyamuka kupita pa njira zawo.
  752. Mat 22:23 ¶Tsiku lomwero adadza kwa iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa, ndipo anamfunsa iye,
  753. Mat 22:24 Nanena kuti, Ambuye, Mose adati, Ngati munthu adafa, wopanda ana, mbale wake adzakwatira mkazi wake, ndi kuwukitsira mbewu kwa mbale wake.
  754. Mat 22:25 Tsopano padali ndi ife abale asanu ndi awiri: ndipo woyamba, pamene iye adakwatira mkazi, anamwalira, ndipo, wopanda mbewu, anasiyira mkazi wake mbale wake:
  755. Mat 22:26 Chimodzimodzi wachiwirinso, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiwiri.
  756. Mat 22:27 Ndipo pomaliza pa zonse mkaziyo adamwaliranso.
  757. Mat 22:28 Choncho m’kuwuka kwa akufa iye adzakhala mkazi wa yani pa asanu ndi awiriwo? Pakuti onse adakhala naye.
  758. Mat 22:29 Koma Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Inu mungolakwa, posadziwa malemba, kapena mphamvu ya Mulungu.
  759. Mat 22:30 Pakuti mkuwuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Mulungu a kumwamba.
  760. Mat 22:31 Koma zokhudza kuwuka kwa akufa, kodi inu simudawerenge chomwe chidalankhulidwa kwa inu ndi Mulungu kuti,
  761. Mat 22:32 Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Mulungu sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo.
  762. Mat 22:33 Ndipo pamene khamu lidamva [ichi], adazizwa pa chiphunzitso chake.
  763. Mat 22:34 ¶Koma pamene Afarisi adamva kuti iye adatontholetsa Asaduki, iwo adasonkhana pamodzi.
  764. Mat 22:35 Kenaka m’modzi wa iwo, [amene anali] wa za malamulo, adamfunsa [iye funso], kumuyesa iye, ndi kunena kuti,
  765. Mat 22:36 Ambuye, lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo?
  766. Mat 22:37 Ndipo Yesu adati kwa iye, Iwe uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse ndi maganizo ako onse.
  767. Mat 22:38 Ili ndilo lamulo loyamba ndi lalikulu.
  768. Mat 22:39 Ndipo lachiwiri [ndi] lofanana nalo, Iwe uzikonda woyandikana naye monga udzikonda iwe mwini.
  769. Mat 22:40 Pa malamulo awiri awa pakolowekedwapo chilamulo chonse ndi aneneri.
  770. Mat 22:41 ¶Pamene Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu adawafunsa iwo,
  771. Mat 22:42 Nanena kuti, Muganiza chiyani inu za Khristu? Ali mwana wamwamuna wa yani? Iwo adanena kwa iye [Mwana wamwamuna] wa Davide.
  772. Mat 22:43 Iye ati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula iye bwanji Ambuye, nanena kuti,
  773. Mat 22:44 Ambuye adanena kwa Ambuye wanga, Khala iwe pa dzanja lamanja langa, kufikira ine nditapanga adani ako kukhala chopondera mapazi ako.
  774. Mat 22:45 Ngati Davide tsono amutchula iye Ambuye, ndiye ali mwana wake bwanji?
  775. Mat 22:46 Ndipo padalibe munthu adatha kumuyankha iye mawu, kapena sadalimbika mtima [munthu] aliyense kuyambira tsiku lomwero kumfunsa [mafunso ena].
  776. Mat 23:1 Kenaka Yesu adayankhula kwa khamu, ndi wophunzira ake.
  777. Mat 23:2 Nanena kuti, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose:
  778. Mat 23:3 Choncho zirizonse zimene iwo akawuza inu kuti musunge, [zimenezo] sungani ndipo muchite; koma musachita inu motsata ntchito zawo: pakuti iwo amayankhula, ndipo samachita ayi.
  779. Mat 23:4 Pakuti amanga akatundu wolemera ndi wosawutsa kunyamula, ndipo asenzetsa [izo] pa mapewa a anthu; koma iwo [eni okha] satha kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.
  780. Mat 23:5 Koma ntchito zawo zonse amachita kuti awonedwe kwa anthu: amakulitsa chithando chake cha makoza awo, ndipo akulitsa mphonje za zovala zawo.
  781. Mat 23:6 Ndipo akonda malo a pa gome apamwamba kwambiri pa maphwando, ndi mipando yayikulu [ndi ya ulemu] m’masunagoge,
  782. Mat 23:7 Ndi kulonjeredwa m’malo ochita malonda, ndi kutchulidwa ndi anthu, Mphunzitsi, Mphunzitsi.
  783. Mat 23:8 Koma inu musamatchedwa Mphunzitsi: pakuti Ambuye wanu ali m’modzi, [ndiye] Khristu; ndipo inu nonse muli abale.
  784. Mat 23:9 Ndipo inu musamatchula [munthu] aliyense atate wanu pansi pano: pakuti m’modzi ndiye Atate wanu amene ali kumwamba.
  785. Mat 23:10 Kapena inu musatchulidwa ambuye: pakuti m’modzi ndiye Ambuye wanu, [ndiye] Khristu.
  786. Mat 23:11 Koma iye amene ali wamkulu kopambana pakati pa inu adzakhala mtumiki wanu.
  787. Mat 23:12 Ndipo aliyense amene adzadzikuza yekha adzachepetsedwa; ndipo amene adzichepetsa mwini yekha adzakwezedwa.
  788. Mat 23:13 ¶Koma tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! Pakuti mutsekera ufumu wa kumwamba motsutsana ndi anthu: pakuti inu [eni nokha] simulowamo, kapena kuwalola iwo amene alikulowamo.
  789. Mat 23:14 Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! Pakuti mulikhwira nyumba za amayi amasiye, ndipo monamizira mupemphera pemphero lalitari: choncho mudzalandira chilango chachikulu.
  790. Mat 23:15 Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! Pakuti inu mupitapita ku nyanja ndi mtunda kumpanga munthu m’modzi wotembenukira ku chipembedzo cha Chiyuda; ndipo m’mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa nyanja ya moto kawiri kuposa inu.
  791. Mat 23:16 Tsoka kwa inu, [inu] atsogoleri akhungu, amene munena, Aliyense amene akalumbira kutchula kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa kachisi, iye ali wa ngongole!
  792. Mat 23:17 Wopusa [inu] ndi akhungu; pakuti choposa n’chiti, golide, kapena kachisi amene ayeretsa golidiyo?
  793. Mat 23:18 Ndiponso, Aliyense amene akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mphatso za pamwamba pake, iye ali wochimwa.
  794. Mat 23:19 Wopusa [inu] ndi akhungu: pakuti choposa n’chiti, mphatso, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mphatsoyo?
  795. Mat 23:20 Choncho aliyense wolumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira pa limenero, ndi zonse ziri pamwamba pake.
  796. Mat 23:21 Ndipo aliyense wolumbira kutchula kachisi, alumbira pa ameneyo, ndi iye wokhala momwemo.
  797. Mat 23:22 Ndipo iye amene alumbira kutchula kumwamba, alumbira pa chimpando cha Mulungu, ndi iye wokhala pomwepo.
  798. Mat 23:23 Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! Pakuti mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tomera tonunkhira ta minti tozuna ndi timbewu ta anizi tokometsa zakudya ndi ta kamini tokometsa ndi kununkhiritsa zakudya, ndipo mwasiya zolemera [zofunika] za chilamulo, chiweruzo, chifundo ndi chikhulupiriro: izi inu mudayenera kuzichita, ndi kusasiya zina kuzichita.
  799. Mat 23:24 Inu atsogoleri akhungu, akukuntha udzudzu, ndipo mumeza ngamira.
  800. Mat 23:25 Tsoka pa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! pakuti mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi kwa mbale yayikulu, koma m’katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.
  801. Mat 23:26 [Iwe] mfarisi wakhungu, tsuka poyamba [zimene ziri] mkati mwa chikho ndi mbale yayikulu, kuti kunja kwa izo kukhalenso koyera.
  802. Mat 23:27 Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! pakuti mufanana ndi manda wopaka njereza, amene ndithu awonekera wokongola kunja kwake, koma ali mkatimo wodzala ndi mafupa a [anthu] akufa, ndi zonyansa zonse.
  803. Mat 23:28 Chomwecho inunso muwoneka wolungama kunja pamaso pa anthu, koma mkati inu muli wodzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.
  804. Mat 23:29 Tsoka pa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga inu! pakuti mumanga ziliza za aneneri, ndipo mukongoletsa manda a wolungama,
  805. Mat 23:30 Ndi kunena kuti, ife tikadakhala m’masiku a makolo athu, sitikadakhala woyanjana nawo m’mwazi wa aneneri.
  806. Mat 23:31 Mwa ichi inu mudzichitira umboni nokha, kuti muli ana a iwo amene adapha aneneri.
  807. Mat 23:32 Dzazani inu tsono muyeso wa makolo anu.
  808. Mat 23:33 [Inu] njoka, [inu] mbadwo wa njoka, mudzatha bwanji inu kuthawa kulanga kwake kwa nyanja ya moto?
  809. Mat 23:34 ¶Mwa ichi, tawonani, ine ndituma kwa inu aneneri, ndi anthu anzeru, ndi alembi: ndipo [ena] a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ndi [ena] a iwo mudzawakwapula m’masunagoge mwanu, ndi kuzunza [iwo] kuchokera ku mzinda umodzi kufikira ku mzinda wina.
  810. Mat 23:35 Kuti pa inu ukhoze kufika mwazi wonse wolungama wokhetsedwa pa dziko lapansi, kuyambira pa mwazi wa Abele wolungamayo kufikira mwazi wa Zakariya mwana wamwamuna wa Barakiyasi, amene inu mudamupha pakati pa kachisi ndi guwa la nsembe.
  811. Mat 23:36 Ndithudi ndinena kwa inu, Zinthu izi zonse zidzafika pa mbadwo uwu.
  812. Mat 23:37 Yerusalemu, Yerusalemu, [iwe] amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo amene atumidwa kwa iwe, ndi pafupipafupi motani ine ndidafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake pansi pa mapiko [ake], ndipo inu simudafuna ayi!
  813. Mat 23:38 Tawonani, nyumba yako yasiyidwa kwa iwe yabwinja.
  814. Mat 23:39 Pakuti ine ndinena kwa inu, Inu simudzandiwonanso ine, kuyambira tsopano, kufikira inu mudzanena, Wodala [ali] iye amene akudza m’dzina la Ambuye.
  815. Mat 24:1 Ndipo Yesu adatuluka, ndipo ananyamuka kuchoka ku kachisi: ndipo wophunzira ake adadza kwa [iye] kudzamuwonetsa zomangidwa za kachisiyo.
  816. Mat 24:2 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Simuwona zinthu izi zonse kodi? Ndithudi ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa pansi.
  817. Mat 24:3 ¶Ndipo pamene iye adakhala pansi pa phiri la ma Olivi, wophunzira adadza kwa iye pa yekha, nanena kuti, Mutiwuze ife, zinthu izi zidzachitika liti? Ndipo [chidzakhala chotani] chizindikiro cha kufika kwanu, ndi cha kutha kwa nthawi ya pansi pano.
  818. Mat 24:4 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Chenjerani kuti munthu aliyense asanyenge inu.
  819. Mat 24:5 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nanena kuti, Ine ndine Khristu, ndipo adzanyenga ambiri.
  820. Mat 24:6 Ndipo inu mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo; onani kuti musavutike: pakuti [zinthu izi] zonse ziyenera kuti ziwoneke; koma chitsiriziro sichinafike.
  821. Mat 24:7 Pakuti mtundu udzawukirana ndi mtundu, ndi ufumu udzawukirana ndi ufumu: ndipo kudzakhala njala, ndi miliri, ndi zivomerezi, m’malo mosiyanasiyana.
  822. Mat 24:8 Zinthu zonsezi [ziri] chiyambi cha zisoni.
  823. Mat 24:9 Pa nthawi imeneyo adzakuperekani kuti musawutsidwe, ndipo adzakuphani inu: ndipo idzakudani mitundu yonse, chifukwa cha dzina langa.
  824. Mat 24:10 Ndipo pamenepo ambiri adzakhumudwa, ndipo adzaperekana wina ndi mnzake, ndipo adzadana wina ndi mnzake.
  825. Mat 24:11 Ndipo aneneri wonama ambiri adzawuka, ndipo adzanyenga ambiri.
  826. Mat 24:12 Ndipo chifukwa chakuti mphulupulu idzachuluka, chikondi cha [anthu] ambiri chidzazilala.
  827. Mat 24:13 Koma iye wakupirira kufikira chimariziro, yemweyo adzapulumuka.
  828. Mat 24:14 Ndipo uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo kenaka chidzafika chimaliziro.
  829. Mat 24:15 Choncho pamene inu mudzawona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniel mneneri, chitayima m’malo woyera (iye amene awerenga, amvetsetse.)
  830. Mat 24:16 Tsono iwo amene ali mu Yudeya athawire ku mapiri:
  831. Mat 24:17 Iye amene ali pamwamba pa denga asatsike kukatenga china chilichonse m’nyumba yake.
  832. Mat 24:18 Kapena iye amene ali m’munda asabwerere kukatenga zovala zake.
  833. Mat 24:19 Ndipo tsoka kwa iwo amene ali ndi mwana, ndi kwa iwo woyamwitsa m’masiku amenewo!
  834. Mat 24:20 Koma pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzakhale pa nyengo yozizira, kapena pa tsiku la sabata.
  835. Mat 24:21 Pakuti pamenepo padzakhala masawutso akulu, monga sipadakhala wotero kuyambira chiyambi cha dziko kufikira nthawi ino, ayi, kapena kudzakhalanso.
  836. Mat 24:22 Ndipo pokhapokha masiku awo atafupikitsidwa, sipakadakhala munthu aliyense wopulumuka: koma chifukwa cha wosankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
  837. Mat 24:23 Pamenepo ngati munthu aliyense anena kwa inu, Onani, Khristu [ali] kuno, kapena uko; musakhulupirire [ichi] ayi.
  838. Mat 24:24 Pakuti adzawuka Akhristu wonama, ndi aneneri wonama, ndipo adzawonetsa zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa; motero mwakuti, ngati [zingakhale] zotheka akanyenge wosankhidwa amene.
  839. Mat 24:25 Tawonani, ine ndakuwuziranitu pasadafike.
  840. Mat 24:26 Mwa ichi ngati adzanena kwa inu, Tawonani, iye ali m’chipululu cha mchenga; musamamukeko: tawonani, [iye ali] m’zipinda; musakhulupirire [ichi] ayi.
  841. Mat 24:27 Pakuti monga mphenzi idzera kum’mawa, ndipo iwala ngakhale kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wamwamuna wa munthu.
  842. Mat 24:28 Pakuti kumene kulikonse kumene mtembo uli, kumeneko makungubwe amasonkhana.
  843. Mat 24:29 ¶Posakhalitsa atapita masawutso a masiku awo dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzawonetsa kuwala kwake, ndipo nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za ku miyamba zidzagwedezeka:
  844. Mat 24:30 Ndipo kenaka padzawoneka chizindikiro cha Mwana wamwamuna wa munthu m’thambo: ndipo pamenepo mitundu yonse ya padziko lapansi idzalira, ndipo iwo adzapenya Mwana wamwamuna wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.
  845. Mat 24:31 Ndipo iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake ku mphepo zinayi, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.
  846. Mat 24:32 Tsopano phunzirani fanizo la mtengo wa mkuyu; Pamene nthambi yake ili yanthete, ndi kuphukitsa masamba ake, inu muzindikira kuti chirimwe chayandikira.
  847. Mat 24:33 Chimodzimodzinso inu, pamene inu mudzawona zinthu zonse zimenezi, zindikirani kuti ili pafupi, [inde] ngakhale pamakomo.
  848. Mat 24:34 Ndithudi ine ndinena kwa inu, M’badwo uwu sudzachoka, kufikira zinthu izi zonse zidzakwaniritsidwa.
  849. Mat 24:35 Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga sadzachoka ayi.
  850. Mat 24:36 ¶Koma za tsiku ilo ndi ora sadziwa [munthu] aliyense, ayi, angakhale angelo a kumwamba, koma Atate wanga wokha.
  851. Mat 24:37 Koma monga [kudali] masiku a Nowa, koteronso kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wamwamuna wa munthu.
  852. Mat 24:38 Koma monga m’masiku aja chisadafike chigumula iwo adali nkudya ndi kumwa, adalikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa adalowa m’chingalawa.
  853. Mat 24:39 Ndipo iwo sadadziwe kanthu kufikira pamene chigumula chidadza, ndi kuwatenga iwo onse; koteronso kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wamwamuna wa munthu.
  854. Mat 24:40 Kenaka awiri adzakhala m’munda; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.
  855. Mat 24:41 [Akazi awiri adzakhala] akupera pamphero, m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.
  856. Mat 24:42 ¶Choncho khalani a tcheru: pakuti simudziwa ora liti Ambuye wanu afika.
  857. Mat 24:43 Koma dziwani ichi; kuti mbuye mwini nyumba wabwino akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ithyoledwe.
  858. Mat 24:44 Choncho khalani inunso wokonzekeratu: pakuti mu ora limene simuganizira Mwana wamwamuna wa munthu adza.
  859. Mat 24:45 Ndani kodi tsono amene ali wantchito wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake wampanga woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?
  860. Mat 24:46 Wodala [ndi] wantchito, amene mbuye wake pakufika adzampeza iye ali kuchita chotero.
  861. Mat 24:47 Ndithudi ine ndinena kwa inu, Kuti adzamkhazika iye wolamulira chuma chake chonse.
  862. Mat 24:48 Koma ngati wantchito woyipa ameneyo akanena mu mtima mwake, Mbuye wanga wachedwa kubwera kwake,
  863. Mat 24:49 Ndipo nadzayamba kumenya antchito [anzake], ndi kudya ndi kumwa pamodzi ndi woledzera;
  864. Mat 24:50 Mbuye wa wantchitoyo adzafika pa tsiku limene iye samuyembekezera [iye], ndi mu ora limene iye salidziwa,
  865. Mat 24:51 Ndipo adzamdula m’magawo, ndipo adzapatsa [iye] gawo lake ndi anthu wonyenga: kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
  866. Mat 25:1 Pamenepo ufumu wa kumwamba ufanizidwa ndi anamwali khumi, amene adatenga nyali zawo, ndipo anatuluka kukakomana ndi mkwati.
  867. Mat 25:2 Ndipo asanu a iwo adali anzeru, ndi asanu [adali] wopusa.
  868. Mat 25:3 Iwo amene [anali] wopusa, adatenga nyali zawo, ndipo sadadzitengera mafuta:
  869. Mat 25:4 Koma anzeruwo adatenga mafuta m’zotengera zawo pamodzi ndi nyali zawo.
  870. Mat 25:5 Ndipo pamene mkwati adachedwa, iwo onsewo adawodzera ndipo anagona tulo.
  871. Mat 25:6 Koma pakati pa usiku padali kufuwula, Tawonani, mkwati alinkudza; tulukani inu kukakomana naye.
  872. Mat 25:7 Pamenepo anamwali onse amenewo adawuka, ndipo anakonza nyali zawo.
  873. Mat 25:8 Ndipo wopusa adati kwa anzeruwo, Tipatseniko ena a mafuta anu; pakuti nyali zathu zazima.
  874. Mat 25:9 Koma anzeruwo adayankha, nanena kuti, [Osati titero], kapena mwina sangakhale wokwanira ife ndi inu: koma makamaka mukani kwa iwo amene agulitsa, ndipo mukadzigulire nokha.
  875. Mat 25:10 Ndipo pamene iwo adalikumuka kukagula, mkwati adafika; ndipo iwo amene adali wokonzekawo adalowa naye pamodzi mu ukwati: ndipo chitseko chinatsekedwa.
  876. Mat 25:11 Pambuyo pake adadzanso anamwali enawo; nanena kuti, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife.
  877. Mat 25:12 Koma iye adayankha ndipo anati, Ndithudi ine ndinena kwa inu, sindikudziwani inu.
  878. Mat 25:13 Choncho dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake kapena ora lake limene Mwana wamwamuna wa munthu akudza.
  879. Mat 25:14 ¶Pakuti [ufumu wa kumwamba] ufanana ndi munthu wakunka ulendo ku dziko lakutali, [amene] adayitana antchito ake, ndipo anapereka kwa iwo chuma chake.
  880. Mat 25:15 Ndipo kwa m’modzi iye adampatsa [ndalama za] matalente zisanu, ndi kwa wina ziwiri, ndi kwa wina imodzi; kwa munthu aliyense monga mwa kuthekera kwake; ndipo anamuka iye pa ulendo wake nthawi yomweyo.
  881. Mat 25:16 Kenaka uyo amene adalandira [ndalama za] matalente zisanu adapita ndi kuchita nazo malonda, ndipo anapindula [nazo ndalama za] matalente zina zisanu.
  882. Mat 25:17 Ndipo chimodzimodzi uyo [adalandira] ziwiri, adapindulanso zina ziwiri.
  883. Mat 25:18 Koma iye amene adalandira imodziyo adamuka ndipo anakumba pansi, ndi kubisa ndalama ya mbuye wake.
  884. Mat 25:19 Itapita nthawi yayitali mbuye wa antchito awo anabwera, ndipo anawerengera nawo pamodzi.
  885. Mat 25:20 Ndipo kotero iye amene adalandira [ndalama za] matalente zisanu adadza ndipo adabweretsa [ndalama za] matalente zina zisanu, kunena kuti, Mbuye, inu mudapereka kwa ine [ndalama za] matalente zisanu: tawonani, ndapindulapo pambali pa izo ndalama za matalente zisanu za pamwamba.
  886. Mat 25:21 Mbuye wake adati kwa iye, Wachita bwino, [iwe] wantchito wabwino ndi wokhulupirika: iwe wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa, ine ndidzakhazika iwe wolamulira pa zinthu zambiri: lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.
  887. Mat 25:22 Iyenso amene adalandira [ndalama za] matalente ziwiriyo anadza ndipo anati, Mbuye, mudapereka kwa ine [ndalama za] matalente ziwiri; tawonani, ndapindulapo [ndalama za] matalente zina ziwiri pambali pa izo.
  888. Mat 25:23 Mbuye wake adati kwa iye, Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika; iwe wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakhazika iwe wolamulira pa zinthu zambiri: lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.
  889. Mat 25:24 Kenaka iye amene adalandira [ndalama ya] talente imodzi adadza ndipo anati, Mbuye, ine ndidakudziwani inu kuti ndinu munthu wowuma mtima, wakukolola pamene inu simudafesa, ndi kusonkhanitsa kumene inu simudamwaza:
  890. Mat 25:25 Ndipo ine ndidawopa, ndipo ndidapita ndikubisa ndalama ya talente yanu m’nthaka: onani, siyo [imene muli] nayo [imene ili] yanu.
  891. Mat 25:26 Mbuye wake adayankha ndipo anati kwa iye, [Iwe] wantchito woyipa ndi waulesi, iwe udadziwa kuti ndimakolola pamene sindidafese, ndi kusonkhanitsa kumene ine sindidamwaza;
  892. Mat 25:27 Choncho iwe ukadakhoza kupereka ndalama yanga kwa wosintha ndalama, ndipo [kenaka] ine pa kubwera kwanga ine ndikadalandira za ine mwini ndi phindu lake.
  893. Mat 25:28 Choncho tengani [ndalama ya] talenteyo kwa iye, ndipo muyipereke [iyo] kwa iye amene ali nazo [ndalama za] matalente khumi.
  894. Mat 25:29 Pakuti kwa yense amene ali nazo kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe kudzachotsedwa ngakhale chimene iye ali nacho.
  895. Mat 25:30 Ndipo ponyani wantchito wopanda phindu ku mdima wakunja: kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta kwa mano.
  896. Mat 25:31 ¶Pamene Mwana wamwamuna wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo woyera onse pamodzi naye, pamenepo iye adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake:
  897. Mat 25:32 Ndipo adzasonkhanitsidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse: ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa [zake] ndi mbuzi;
  898. Mat 25:33 Ndipo adzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi ku lamanzere.
  899. Mat 25:34 Kenaka Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani, inu kuno inu wodalitsika a Atate wanga, landirani ufumu wokonzedwera kwa inu, kuyambira pa maziko a dziko lapansi:
  900. Mat 25:35 Pakuti ndidamva njala, ndipo inu mudandipatsa ine chakudya: ine ndidamva ludzu, ndipo inu mudandipatsa ine chakumwa: ndidali mlendo, ndipo mudandilowetsa [m’nyumba] ine.
  901. Mat 25:36 Wamaliseche, ndipo inu mudandiveka ine; ndinadwala ndipo inu munadza kundichezera ine: ine ndidali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa ine,
  902. Mat 25:37 Kenaka wolungama adzayankha iye, kunena kuti, Ambuye, ndi liti limene tidakuwonani mutamva njala; ndi kukudyetsani [inu]? Kapena wa ludzu, ndi kukupatsani kumwa [inu]?
  903. Mat 25:38 Ndi liti ife tidawona inu mlendo, ndi kukulowetsani m’nyumba [inu]? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani [inu]?
  904. Mat 25:39 Kapena ife tidakuwonani inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende; ndipo tidadza kwa inu?
  905. Mat 25:40 Ndipo Mfumuyo idzayankha ndipo idzati kwa iwo, Ndithudi ine ndinena kwa inu, Motero mwakuti inu mudachitira [ichi] m’modzi wa ang’onong’ono a abale anga awa, mudandichitira [ichi] ine.
  906. Mat 25:41 Kenaka adzanena iye kwa iwo akudzanja lamanzere, Chokani kwa ine, inu wotembereredwa, ku moto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:
  907. Mat 25:42 Pakuti ndidali wa njala, ndipo simudandipatsa ine chakudya: ine ndidali ndi ludzu, ndipo inu simudandipatsa ine chakumwa.
  908. Mat 25:43 Ndidali mlendo, ndipo simudandilowetsa m’nyumba ine: wamaliseche, ndipo simudandiveka ine: wodwala, ndi m’nyumba ya ndende, ndipo inu simudadza kundiwona ine.
  909. Mat 25:44 Kenaka iwonso adzayankha iye, kunena kuti, Ambuye, ife tidakuwonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena wodwala, kapena m’nyumba ya ndende, ndipo ife sitidakutumikirani inu?
  910. Mat 25:45 Kenaka iye adzayankha iwo, kunena kuti, Ndithudi ine ndinena kwa inu, Motero mwakuti mudalibe kuchitira [ichi] m’modzi wa ang’onong’ono awa, mudalibe kundichitira [ichi] ine.
  911. Mat 25:46 Ndipo amenewa adzapita ku chilango chosatha: koma wolungama ku moyo wosatha.
  912. Mat 26:1 Ndipo kudachitika, pamene Yesu adatha zonena zonse zimenezi, iye adati kwa wophunzira ake,
  913. Mat 26:2 Inu mudziwa kuti akapita masiku awiri [pakhala phwando] la paskha, ndi Mwana wamwamuna wa munthu adzaperekedwa kukapachikidwa.
  914. Mat 26:3 Kenaka adasonkhana ansembe akulu, ndi alembi, ndi akulu a anthu, ku bwalo la mkulu wa ansembe, amene dzina lake ndi Kayafasi.
  915. Mat 26:4 Ndipo anakambirana kuti akhoze kumtenga Yesu mochenjera, ndi kumupha [iye].
  916. Mat 26:5 Koma iwo adanena, Osati pa [tsiku] la phwando ayi, kuti mwina pangakhale chipolowe pakati pa anthu.
  917. Mat 26:6 ¶Tsopano pamene Yesu adali mu Betane, m’nyumba ya Simoni wakhate,
  918. Mat 26:7 Anadza kwa iye mkazi ali nalo botolo la alabasitara la mafuta wonunkhira a mtengo wapatali, ndipo anawatsanulira pamutu pake, m’mene iye adalikukhala [pachakudya].
  919. Mat 26:8 Koma m’mene wophunzira ake adawona [ichi], adali ndi mkwiyo, nanena kuti, Pali cholinga chotani pa kuwononga kumeneku?
  920. Mat 26:9 Pakuti mafuta awa akadagulitsidwa ndalama zambiri, ndi kupatsa anthu aumphawi.
  921. Mat 26:10 Pamene Yesu adadziwa [ichi], iye adati kwa iwo, Muvutiranji mkaziyu inu? Pakuti wachita ntchito yabwino pa ine.
  922. Mat 26:11 Pakuti muli nawo aumphawi nthawi zonse pamodzi nanu; koma ine si muli nane nthawi zonse.
  923. Mat 26:12 Pakuti mwa ichi kuti mkaziyo wathira mafuta awa pathupi panga, wachitiratu [ichi] pa kuyikidwa kwanga m’manda.
  924. Mat 26:13 Ndithudi ndinena kwa inu, Kumene kulikonse uthenga wabwino uwu udzalalikidwa mdziko lonse lapansi, [kumeneko] ichinso, chimene mkaziyo wachitachi, chidzakambidwanso chifukwa cha chikumbukiro chake.
  925. Mat 26:14 ¶Kenaka m’modzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Isikariyoti, adamuka kwa ansembe akulu,
  926. Mat 26:15 Ndipo anati [kwa iwo], Kodi mudzandipatsa ine chiyani, ndipo ine ndidzampereka iye kwa inu? Ndipo iwo adapangana naye ndalama za siliva makumi atatu.
  927. Mat 26:16 Ndipo kuyambira pamenepo iye adafunafuna mpata wabwino wakuti ampereke iye.
  928. Mat 26:17 ¶Ndipo [tsiku] loyamba [phwando la] mkate wopanda chofufumitsa, wophunzira anadza kwa Yesu, kunena kwa iye, Mufuna ife tikakonzere inu kuti, kuti mukadye paskha?
  929. Mat 26:18 Ndipo iye adati, Mukani kumzinda kwa munthu wakuti, ndipo mukati kwa iye, Ambuye anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya paskha kunyumba kwanu pamodzi ndi wophunzira anga.
  930. Mat 26:19 Ndipo wophunzira adachita monga Yesu adawauza: ndipo anakonzekera paskha.
  931. Mat 26:20 Ndipo pamene madzulo anafika, iye adakhala pansi pamodzi ndi wophunzira khumi ndi awiri.
  932. Mat 26:21 Ndipo m’mene adali akudya, iye adati, Ndithudi ndinena kwa inu, kuti m’modzi wa inu adzandipereka ine.
  933. Mat 26:22 Ndipo iwo adagwidwa ndi chisoni chachikulu, ndipo anayamba aliyense wa iwo kunena kwa iye, Ambuye, kodi ndine?
  934. Mat 26:23 Ndipo iye adayankha ndipo anati, Iye amene asunsa pamodzi ndi ine dzanja [lake] m’mbale, yemweyu adzandipereka ine.
  935. Mat 26:24 Mwana wamwamuna wa munthu achokatu monga kudalembedwa za iye: koma tsoka kwa munthu amene Mwana wamwamuna wa munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati iye akadapanda kubadwa.
  936. Mat 26:25 Kenaka Yudasi, amene adampereka iye, adayankha ndipo anati, Ambuye, kodi ndine? Iye adanena kwa iye, Iwe watero.
  937. Mat 26:26 ¶Ndipo pamene iwo adalinkudya, Yesu adatenga mkate, ndipo anadalitsa [iwo], ndipo anaunyema [iwo], ndipo adapatsa [iwo] kwa wophunzira, ndipo adati, Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.
  938. Mat 26:27 Ndipo adatenga chikho, ndipo anayamika, ndipo anapatsa [icho] kwa iwo, nanena kuti, Mumwere ichi inu nonse.
  939. Mat 26:28 Pakuti uwu ndiwo mwazi wanga wa chipangano chatsopano, umene wakhetsedwa chifukwa cha ambiri ku chikhululukiro cha machimo.
  940. Mat 26:29 Ndipo ndinena kwa inu, Ine sindidzamwanso chipatso ichi cha mphesa kuyambira tsopano, kufikira tsiku limene ine ndidzamwa kwatsopano pamodzi ndi inu mu ufumu wa Atate wanga.
  941. Mat 26:30 Ndipo pamene adayimba nyimbo, iwo adatuluka kumka ku phiri la ma Olivi.
  942. Mat 26:31 Kenaka Yesu anena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha ine usiku uno: pakuti kwalembedwa, Ine ndidzakantha mbusa, ndipo nkhosa za gulu zidzabalalika kudera lalikulu.
  943. Mat 26:32 Ndipo nditawukitsidwanso, ine ndidzatsogolera inu ku Galileya.
  944. Mat 26:33 Petro adayankha ndipo anena kwa iye, Ngakhale [anthu] onse adzakhumudwa chifukwa cha inu, [koma] ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.
  945. Mat 26:34 Yesu adati kwa iye, Ndithudi ndinena kwa iwe, Kuti usiku uno, tambala asadalire, iwe udzandikana ine katatu.
  946. Mat 26:35 Petro adanena kwa iye, Ngakhale ine ndikafe pamodzi ndi inu, komatu ine sindidzakukanani inu ayi. Wophunzira onse adanena chimodzimodzi.
  947. Mat 26:36 ¶Kenaka Yesu anadza ndi iwo ku malo wotchedwa Getsemane, ndipo anena kwa wophunzira ake, Bakhalani inu pompano, pamene ine ndipita ndikapemphere uko.
  948. Mat 26:37 Ndipo iye adatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo pamodzi naye, ndipo anayamba kugwidwa chisoni ndi kulemedwa kwambiri.
  949. Mat 26:38 Kenaka adanena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni, ngakhale cha kufika ku imfa: khalani inu pano, ndipo muchezere pamodzi ndi ine.
  950. Mat 26:39 Ndipo adamuka patsogolo pang’ono, ndipo anagwa nkhope yake pansi, ndipo anapemphera, nanena kuti, Atate wanga, ngati nkutheka, lolani chikho ichi chindipitirire ine: komabe osati monga ndifuna ine, koma monga [mufuna] inu.
  951. Mat 26:40 Ndipo iye adadza kwa wophunzira, ndipo anawapeza iwo akugona, ndipo ananena kwa Petro, Nkutero, kodi simukhoza kukhala maso pamodzi ndi ine ora limodzi?
  952. Mat 26:41 Khalani maso ndi kupemphera, kuti inu musalowe m’kuyesedwa: mzimu ndithu [ali] wakufuna, koma thupi [liri] lofowoka.
  953. Mat 26:42 Adamukanso kachiwiri, ndipo anapemphera, nanena kuti, Atate wanga, ngati chikho ichi sichingakhoze kundipitirira kupatula kuti ine ndimwe icho, kufuna kwanu kuchitidwe.
  954. Mat 26:43 Ndipo anabwera ndipo anawapeza iwo akugonanso: pakuti maso awo adali wolemera.
  955. Mat 26:44 Ndipo iye adawasiya iwo, ndipo anachokanso, ndipo anapemphera kachitatu, kunenanso mawu womwewo.
  956. Mat 26:45 Kenaka iye anadza kwa wophunzira ake, ndipo ananena kwa iwo, Gonani tsopano, ndipo mupumule: tawonani ora layandikira, ndipo Mwana wamwamuna wa munthu aperekedwa m’manja a wochimwa.
  957. Mat 26:46 Nyamukani, tiyeni timuke: tawonani, iye wayandikira amene andipereka ine.
  958. Mat 26:47 ¶Ndipo iye ali chiyankhulire, onani, Yudasi m’modzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu ndi malupanga ndi zindodo, kuchokera kwa ansembe akulu ndi akulu a anthu.
  959. Mat 26:48 Tsopano iye amene wompereka iye adawapatsa iwo chizindikiro, nanena kuti, Aliyense amene ine ndidzampsopsona, ameneyo ndi iye: mumgwire iye msanga.
  960. Mat 26:49 Ndipo pomwepo iye anadza kwa Yesu, ndipo anati, Tikuwoneni, mbuye, ndipo adampsopsona iye.
  961. Mat 26:50 Ndipo Yesu adati kwa iye, Bwenzi, wafikiranji iwe? Kenaka iwo anadza, ndipo anamthira Yesu manja, ndipo anamtenga iye.
  962. Mat 26:51 Ndipo, tawonani, m’modzi wa iwo amene adali pamodzi ndi Yesu adatansa dzanja [lake], ndipo anasolola lupanga lake, ndipo anakantha wantchito wa mkulu wa nsembe, ndipo anadula khutu lake.
  963. Mat 26:52 Kenaka Yesu adanena kwa iye, Tabwezeranso lupanga lako m’chimakemo: pakuti iwo onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.
  964. Mat 26:53 Uganiza iwe kuti ine sindingathe kupemphera tsopano kwa Atate wanga, ndipo iye adzapatsa ine tsopano lomwe lino malegiyoni a angelo woposa khumi ndi awiri?
  965. Mat 26:54 Koma pakutero tsono malembo adzakwaniritsidwa bwanji, pakuti kuyenera kukhala chomwecho?
  966. Mat 26:55 Mu ora lomwero Yesu adati kwa makamuwo, Kodi mudatulukira kundigwira ine ngati mbava ndi malupanga ndi zindodo? Ndimakhala tsiku ndi tsiku pamodzi ndi inu kuphunzitsa m’kachisi, ndipo inu simudandigwira ine.
  967. Mat 26:56 Koma izi zonse zidachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikhoze kukwaniritsidwa. Kenaka wophunzira onse adamsiya iye, ndipo anathawa.
  968. Mat 26:57 ¶Ndipo iwo amene adagwira Yesu adamka [naye] kwa Kayafasi mkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu adasonkhana.
  969. Mat 26:58 Koma Petro adamtsata iye kutali kufikira nyumba ya mkulu wa ansembe, ndipo analowamo, ndipo anakhala pansi ndi antchito, kuti awone chimaliziro.
  970. Mat 26:59 Tsopano ansembe akulu ndi akulu, ndi akulu a milandu onse, adafunafuna mboni zonama zakutsutsa Yesu, kuti amuphe iye;
  971. Mat 26:60 Koma sadawupeza: inde, ngakhale mboni zonama zambiri zidadza, [koma] sadawupeze umboni uli wonse. Pamapeto pake zidadza mboni ziwiri zonama,
  972. Mat 26:61 Ndipo adati, Munthu [uyu] adanena kuti, Ine ndikhoza kupasula kachisi wa Mulungu, ndi kum’manganso masiku atatu.
  973. Mat 26:62 Ndipo mkulu wa ansembe adayimirira, ndipo anati kwa iye, Sukuyankha kanthu kodi? [Nchiyani ichi chimene] awa akunenera iwe?
  974. Mat 26:63 Koma Yesu adangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe adayankha ndi kunena kwa iye, Ine ndikulamulira iwe pa Mulungu wamoyo, kuti iwe utiwuze ife ngati iwe ndiwe Khristu, Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  975. Mat 26:64 Yesu ati kwa iye, Inu mwanena: komabe ine ndinena kwa inu, Kuyambira tsopano mudzawona Mwana wamwamuna wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja lamphamvu, ndi kubwera mu mitambo ya kumwamba.
  976. Mat 26:65 Kenaka mkulu wa ansembe adang’amba zovala zake, nanena kuti, Iye walankhula zonyoza [Mulungu]; tifuniranji ife mboni zina? Tawonani, tsopano inu mwamva zonyoza zakezo.
  977. Mat 26:66 Muganiza bwanji inu? Iwo adayankha ndipo anati, Ali wolakwa koyenera imfa.
  978. Mat 26:67 Kenaka iwo adamlavulira malovu pankhope pake, ndipo anam’bwanyula iye; ndipo ena adampanda [iye] ndi zikhato za manja awo,
  979. Mat 26:68 Nanena kuti, Nenera kwa ife, iwe Khristu, Ndani amene wakumenya iwe?
  980. Mat 26:69 ¶Tsopano Petro adakhala pa bwalo la m’nyumbayo: ndipo mtsikanayo anadza kwa iye, kunena kuti, Iwenso udali ndi Yesu wa ku Galileya.
  981. Mat 26:70 Koma iye adakana pamaso pa [iwo] onse, nanena kuti, Ine sindichidziwa chimene iwe unena.
  982. Mat 26:71 Ndipo pamene iye adatuluka kumka ku chipata, [mtsikana] wina adamuwona iye, ndipo anati kwa iwo amene anali pamenepo, [Munthu] uyunso adali ndi Yesu wa ku Nazarete.
  983. Mat 26:72 Ndipo adakananso ndi chilumbiro, Ine sindidziwa munthuyo.
  984. Mat 26:73 Ndipo popita nthawi yayin’gono anadza kwa [iye] iwo akuyimapo, ndipo anati kwa Petro, Zowonadi iwenso uli [m’modzi] wa iwo; pakuti mayankhulidwe ako akupereka iwe.
  985. Mat 26:74 Kenaka adayamba iye kutemberera ndi kulumbira, [kunena kuti], Ine sindikumdziwa munthuyo ayi. Ndipo posakhalitsa tambala adalira.
  986. Mat 26:75 Ndipo Petro adakumbukira mawu a Yesu, amene adanena kwa iye, Asadalire tambala, iwe udzandikana ine katatu. Ndipo iye adatuluka kunja, ndipo analira ndi kuwawa mtima.
  987. Mat 27:1 Pamene m’mawa unadza, ansembe akulu ndi akulu a anthu onse adachita upo wakumtsutsa Yesu kuti amuphe iye:
  988. Mat 27:2 Ndipo iwo atam’manga iye, anamuka [naye], ndipo anampereka iye kwa Pontiyasi Pilato kazembeyo.
  989. Mat 27:3 ¶Kenaka Yudasi, yemwe adampereka iye, pamene iye adawona kuti iye adatsutsidwa, adalapa iye mwini, ndipo anabweretsanso ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akulu ndi akulu.
  990. Mat 27:4 Nanena kuti, Ine ndachimwa kuti ndapereka mwazi wosalakwa. Ndipo iwo adati, Kodi [ichi chili chiyani] kwa ife? Udziwonere iwe wekha [ku icho].
  991. Mat 27:5 Ndipo iye adataya pansi ndalamazo m’kachisi, ndipo anachokapo, ndipo anapita ndipo anadzimangirira yekha.
  992. Mat 27:6 Ndipo ansembe akulu adatenga ndalamazo, ndipo anati, Sikuloledwa kuziyika izi m’chosungiramo ndalama, chifukwa ziri mtengo wa mwazi.
  993. Mat 27:7 Ndipo iwo adapangana, ndipo anazigulira izo munda wa wowumba mbiya, ukhale manda a alendo.
  994. Mat 27:8 Mwa ichi munda umenewu adautcha Munda wa mwazi, kufikira tsiku la lero.
  995. Mat 27:9 Pamenepo chidakwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi Yeremiya m’neneri, kunena kuti, Ndipo iwo adatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa iye umene udawerengeredwa, amene iwo ana a Israyeli adawerengera mtengo wake.
  996. Mat 27:10 Ndipo adazipereka izo kugula munda wa wowumba mbiya, monga Ambuye adandikonzera ine.
  997. Mat 27:11 Ndipo Yesu adayimirira pamaso pa kazembe: ndipo kazembeyo adamfunsa iye, kunena kuti, Kodi iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu adati kwa iye, Inu mwanena.
  998. Mat 27:12 Ndipo pamene adam’nenera iye ansembe akulu ndi akulu, iye sadayankha kanthu.
  999. Mat 27:13 Kenaka Pilato adanena kwa iye, Sukumva iwe kodi zinthu zambiri bwanji akunenera iwe?
  1000. Mat 27:14 Ndipo sadayankha iye ngakhale mawu amodzi; motero mwakuti kazembe adazizwa kwambiri.
  1001. Mat 27:15 Tsopano pa phwando [ilo] kazembe adazolowera kumasulira anthu wandende m’modzi, amene iwo adafuna.
  1002. Mat 27:16 Ndipo iwo adali ndi wandende wodziwika, wotchedwa Barabasi.
  1003. Mat 27:17 Choncho pamene iwo adasonkhana pamodzi, Pilato adanena kwa iwo, Ndani amene inu mufuna kuti ine ndikumasulireni inu? Barabasi, kapena Yesu amene atchedwa Khristu?
  1004. Mat 27:18 Pakuti iye adadziwa chifukwa chanjiru adampereka iye.
  1005. Mat 27:19 ¶Ndipo pamene Pilato adali atakhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake adatumiza mawu kwa iye, nanena kuti, Musachite kanthu kalikonse ndi munthu wolungamayo: pakuti ine ndasawuka kwambiri lero m’kulota chifukwa cha iye.
  1006. Mat 27:20 Koma ansembe akulu adakopa khamu kuti lipemphe Barabasi, ndi kuwononga Yesu.
  1007. Mat 27:21 Kazembe adayankha ndipo anati kwa iwo, Ndi uti wa awa awiri mufuna inu kuti ndikumasulireni inu? Iwo adati, Barabasi.
  1008. Mat 27:22 Pilato adanena kwa iwo, Ndidzachita chiyani tsono ndi Yesu amene atchedwa Khristu? [Iwo] onse adati kwa iye, Iye apachikidwe.
  1009. Mat 27:23 Ndipo kazembe adati, Chifukwa chiyani, choyipa chotani chimene iye wachita? Koma iwo adafuwulitsa kopambana, kunena kuti, Iye apachikidwe.
  1010. Mat 27:24 ¶Pamene Pilato adawona kuti iye sadakhoza kupambana kulikonse, koma [kuti] makamaka lidachitika phokoso, iye adatenga madzi, ndipo anasamba manja [ake] pamaso pa khamulo, nanena kuti, Ine ndiribe kuchimwira mwazi wa munthu wolungama uyu: mudziwonere inu nokha [ku ichi].
  1011. Mat 27:25 Kenaka anthu onse adayankha, ndipo anati, Mwazi wake [ukhale] pa ife, ndi pa ana athu.
  1012. Mat 27:26 ¶Kenaka iye adamasulira iwo Barabasi: ndipo pamene anamkwapula Yesu, iye anampereka [iye] kuti akapachikidwe.
  1013. Mat 27:27 Kenaka asirikali a kazembe adamuka naye Yesu ku bwalo la milandu, ndipo anasonkhanitsa kwa iye gulu la [asirikali] lonse.
  1014. Mat 27:28 Ndipo adamvula iye, ndipo anamveka mkanjo wofiyira wa chifumu.
  1015. Mat 27:29 ¶Ndipo pamene adaluka korona waminga, iwo anamveka iye pamutu pake, ndipo anamugwiritsa bango m’dzanja lake lamanja: ndipo iwo adapinda bondo pamaso pake, ndipo anamchitira chipongwe, nanena kuti, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda!
  1016. Mat 27:30 Ndipo anamulavulira malovu iye, ndipo anatenga bango, ndi kumpanda iye pamutu.
  1017. Mat 27:31 Ndipo pamene adatha kumchitira iye chipongwe, iwo adamuvula mkanjo uja, ndipo anamveka iye chovala chake, ndipo adamtsogolera iye kupita kukampachika [iye].
  1018. Mat 27:32 Ndipo pakutuluka iwo, adapeza munthu wa ku Kurene, dzina lake Simoni: iwo anamkangamiza iye kuti anyamule mtanda wake.
  1019. Mat 27:33 Ndipo pamene adadza kumalo dzina lake Gologota, ndiko kunena kuti, malo a bade.
  1020. Mat 27:34 ¶Adampatsa iye viniga kuti amwe wosanganiza ndi ndulu: ndipo pamene iye adalawa [za zimenezo], iye sadafuna kumwa.
  1021. Mat 27:35 Ndipo iwo adampachika iye, ndipo anagawana zovala zake, anachita mayere: kuti chikhoze kukwaniritsidwa chimene chinanenedwa ndi mneneriyo, Iwo adagawana zovala zanga pakati pawo, ndipo pa malaya anga anachita mayere.
  1022. Mat 27:36 Ndipo atakhala iwo pansi anamdikira iye pamenepo;
  1023. Mat 27:37 Ndipo adayika pamwamba pa mutu wake mawu a mlandu wolembedwa; UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.
  1024. Mat 27:38 Kenaka pamenepo adapachika mbava ziwiri pamodzi ndi iye, m’modzi ku dzanja lamanja, ndi wina ku lamanzere.
  1025. Mat 27:39 ¶Ndipo iwo amene ankadutsapo adamchitira mwano iye, ndi kupukusa mitu yawo,
  1026. Mat 27:40 Ndi kunena kuti, Iwe amene uwononga kachisi ndi kum’manganso [iye] m’masiku atatu, dzipulumutse wekha. Ngati uli Mwana wamwamuna wa Mulungu, tatsika pa mtandapo.
  1027. Mat 27:41 Chomwechonso ansembe akulu kumchitira [iye] chipongwe, pamodzi ndi alembi ndi akulu, ananena kuti,
  1028. Mat 27:42 Iye adapulumutsa ena; yekha sangathe kudzipulumutsa. Ngati ndiye Mfumu ya Israyeli, atsike tsopano pa mtandapo, ndipo ife tidzamkhulupirira iye.
  1029. Mat 27:43 Iye amadalira mwa Mulungu; iye ampulumutse tsopano, ngati iye afuna kutero naye: pakuti iye adati, Ine ndine Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  1030. Mat 27:44 Mbalazonso, zimene zidapachikidwa pamodzi ndi iye, zidamlalatira iye mawu omwewo.
  1031. Mat 27:45 Tsopano kuyambira ora lachisanu ndi chimodzi padali mdima padziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinayi.
  1032. Mat 27:46 Ndipo pafupifupi pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu adafuwula ndi mawu okwera, nanena kuti, Eli Eli, lama sabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?
  1033. Mat 27:47 Ena a iwo akuyimirira pomwepo, pamene adamva [ichi], adanena kuti, [Munthu] uyu ayitana Eliya.
  1034. Mat 27:48 Ndipo pomwepo m’modzi wa iwo adathamanga, ndipo anatenga chinkhupule, ndipo anachidzaza [icho] ndi viniga, ndipo anachiyika [icho] pa bango, ndipo anampatsa iye kuti amwe.
  1035. Mat 27:49 Enawo adati, Taleka, tiyeni tiwone ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa iye.
  1036. Mat 27:50 ¶Yesu, pamene adafuwulanso ndi mawu okwera, adamwalira.
  1037. Mat 27:51 Ndipo, tawonani, chinsalu chotchinga cha m’kachisi chidang’ambika pakati m’magawo awiri kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko lapansi lidagwedezeka, ndipo miyala idang’ambika;
  1038. Mat 27:52 Ndipo manda adatseguka; ndi matupi ambiri a anthu woyera mtima amene adagona adawuka,
  1039. Mat 27:53 Ndipo adatuluka m’mandamo pambuyo pa kuwuka kwa iye, ndipo analowa mu mzinda woyerawo, ndipo anawonekera kwa ambiri.
  1040. Mat 27:54 Tsopano pamene kenturiyoni, ndi iwo amene adali naye, akuyang’anira Yesu, adawona chivomerezi, ndi zinthu zimene zidachitidwa, adawopa kwambiri, nanena kuti, Zowonadi uyu anali Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  1041. Mat 27:55 Ndipo akazi ambiri adali pomwepo akuyang’anira patali amene adatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira kwa iye;
  1042. Mat 27:56 Mwa iwo amene mudali Mariya wa Mmagidalene, ndi Mariya amayi wake a Yakobo ndi Yosesi, ndi amayi wa ana a Zebedayo.
  1043. Mat 27:57 Ndipo pakufika madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe, amene adalinso iye wophunzira wa Yesu:
  1044. Mat 27:58 Iyeyo adapita kwa Pilato, ndipo anapempha thupi la Yesu. Kenaka Pilato adalamulira kuti thupilo liperekedwe.
  1045. Mat 27:59 Ndipo pamene Yosefe adatenga thupilo, adalikulunga ilo m’nsalu yabafuta yoyeretsetsa,
  1046. Mat 27:60 Ndipo analiyika m’manda ake atsopano, amene iye adasema m’mwala: ndipo anakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, ndipo ananyamukapo.
  1047. Mat 27:61 Ndipo padali Mariya Mmagidalene pamenepo, ndi Mariya winayo, atakhala pansi popenyana ndi mandawo.
  1048. Mat 27:62 ¶Tsopano tsiku lotsatira, limene lidali lotsatana ndi tsiku lokonzekera, ansembe akulu ndi Afarisi adasonkhana kwa Pilato.
  1049. Mat 27:63 Nanena kuti, Mfumu, ife tikukumbukira kuti wonyenga amene uja adati, pamene adali ndi moyo, Pakutha masiku atatu ine ndidzawuka.
  1050. Mat 27:64 Choncho mulamule kuti asindikize pamandapo kufikira tsiku lachitatulo, kuti mwina wophunzira ake angadze usiku, ndi kudzamuba kuchoka naye, ndipo adzanena kwa anthu, Iye wawuka kwa akufa: kotero cholakwika chomaliza chidzaposa choyambacho.
  1051. Mat 27:65 Pilato adati kwa iwo, Inu ikani alonda: mukani pa njira yanu, kalondereni [awo] motsimikiza monga inu mungathere.
  1052. Mat 27:66 Kotero iwo adamuka, ndipo anasunga manda, ndipo anasindikizapo chizindikiro pamwalapo, ndi kuyika woyang’anira.
  1053. Mat 28:1 Ndipo kumathero kwake kwa [tsiku la] sabata, m’mene kudayamba kucha kwa [tsiku] loyamba la sabata, anadza Mariya Mmagadalene ndi Mariya winayo kudzawona manda.
  1054. Mat 28:2 Ndipo, tawonani, padali chivomerezi chachikulu: pakuti mngelo wa Ambuye adatsika kuchokera kumwamba, ndipo anafika ndi kukunkhuniza mwalawo kuwuchotsa pakhomopo, ndipo anakhala pamwamba pake.
  1055. Mat 28:3 Nkhope yake idali ngati mphezi, ndi chovala chake choyera ngati matalala;
  1056. Mat 28:4 Ndipo chifukwa cha mantha ndi iye alondawo adanthunthumira, ndipo anakhala ngati [anthu] akufa.
  1057. Mat 28:5 Ndipo mngelo adayankha ndipo anati kwa akaziwo, Musawopa inu: pakuti ine ndidziwa kuti inu mulikufunafuna Yesu, amene adapachikidwa.
  1058. Mat 28:6 Iye mulibe muno: pakuti iye adawuka, monga iye adanena, Idzani, onani malo amene Ambuye adagonamo.
  1059. Mat 28:7 Ndipo pitani msanga, ndipo muwuze wophunzira ake kuti iye wawuka kwa akufa; ndipo, tawonani, apita patsogolo panu ku Galileya; kumeneko inu mudzamuwona iye: onani, ine ndakuwuzani inu.
  1060. Mat 28:8 Ndipo iwo adanyamuka msanga kuchoka kumanda ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu; ndipo anathamanga kukawuza wophunzira ake.
  1061. Mat 28:9 ¶Ndipo pamene amamka kukawuza wophunzira ake, tawonani, Yesu adakomana nawo, nanena kuti, Tikuwoneni. Ndipo iwo anadza ndipo anamgwira iye mapazi ake, ndipo anamlambira iye.
  1062. Mat 28:10 Kenaka adanena Yesu kwa iwo, Musawope: pitani kawuzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo kumeneko adzandiwona ine.
  1063. Mat 28:11 ¶Tsopano pamene iwo adalikupita, tawonani, ena a alonda adafika mu mzinda; ndipo anawuza ansembe akulu zonse zimene zidachitidwa.
  1064. Mat 28:12 Ndipo pamene adasonkhana pamodzi ndi akulu, ndipo adachita upo, iwo anapatsa ndalama zambiri kwa asirikaliwo.
  1065. Mat 28:13 Nanena kuti, Kazinenani inu, Wophunzira ake anadza usiku, ndipo anamuba iye [kumchotsa] m’mene ife tidali mtulo.
  1066. Mat 28:14 Ndipo ngati ichi chidzamveka ku makutu a kazembe, ife tidzamukakamiza iye, ndi kukutetezani inu.
  1067. Mat 28:15 Kotero iwo adalandira ndalamazo, ndipo anachita monga adawuzidwa: ndipo chonena ichi chimafotokozedwabe pakati pa Ayuda kufikira tsiku la lero.
  1068. Mat 28:16 ¶Kenaka wophunzira khumi ndi m’modziyo adanyamukapo kulowa mu Galileya, kulowa m’phiri limene Yesu adawasonyeza iwo.
  1069. Mat 28:17 Ndipo pamene adamuwona iye, iwo adamlambira iye: koma ena adakayika.
  1070. Mat 28:18 Ndipo Yesu anadza ndipo anayankhula nawo, nanena kuti, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi dziko lapansi.
  1071. Mat 28:19 ¶Choncho inu mukani, ndipo phunzitsani mitundu yonse, kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana wamwamuna, ndi la Mzimu Woyera:
  1072. Mat 28:20 Kuwaphunzitsa iwo kuti asunge zinthu zonse zimene ine ndidakulamulirani inu: ndipo, onani ine ndiri pamodzi ndi inu nthawi zonse, [ngakhale] kufikira ku kutha kwa dziko. Amen.
  1073. Mrk 1:1 Chiyambi cha uthenga wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wamwamuna wa Mulungu;
  1074. Mrk 1:2 Monga mwalembedwa mwa aneneri. Tawonani, Ine ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu patsogolo panu.
  1075. Mrk 1:3 Mawu a wina wofuwula m’chipululu, Konzani inu njira ya Ambuye, lungamitsani makwalala ake.
  1076. Mrk 1:4 Yohane adabatiza m’chipululu, ndi kulalikira ubatizo wa kutembenuka mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo.
  1077. Mrk 1:5 Ndipo adatuluka kudza kwa iye dziko lonse la Yudeya, ndi iwo a ku Yerusalemu, ndipo onse anabatizidwa ndi iye mu mtsinje wa Yordano, akuwulula machimo awo.
  1078. Mrk 1:6 Ndipo Yohane ankavala ubweya wa ngamira, ndi lamba wa chikopa m’chiwuno mwake: ndipo iye amadya dzombe ndi uchi wakuthengo;
  1079. Mrk 1:7 Ndipo adalalikira, kunena kuti, Akudza wina wondipambana ine mphamvu pambuyo panga, chingwe cha nsapato zake sindiyenera kuwerama ndi kumasula.
  1080. Mrk 1:8 Ine zowonadi ndikubatizani inu ndi madzi; koma iye adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera.
  1081. Mrk 1:9 Ndipo kudachitika m’masiku amenewo, kuti Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, ndipo anabatizidwa ndi Yohane m’Yordano.
  1082. Mrk 1:10 Ndipo nthawi yomweyo potuluka m’madzi, iye adawona miyamba itatseguka, ndipo Mzimu monga nkhunda adatsikira pa iye:
  1083. Mrk 1:11 Ndipo padadza mawu wochokera kumwamba, [wonena], Iwe uli Mwana wanga wamwamuna wokondedwa, amene mwa iye ndikondwera bwino.
  1084. Mrk 1:12 Ndipo posakhalitsa Mzimu adampititsa iye kulowa kuchipululu.
  1085. Mrk 1:13 Ndipo iye adakhala m’menemo m’chipululu masiku makumi anayi, kuyesedwa ndi Satana; ndipo adali ndi nyama zakuthengo; ndipo angelo adamtumikira iye.
  1086. Mrk 1:14 Tsopano Yohane atayikidwa m’ndende, Yesu anadza kulowa mu Galileya, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.
  1087. Mrk 1:15 Ndikunena, Nthawi yakwaniritsidwa, ndipo ufumu wa Mulungu wayandikira: lapani inu, ndipo khulupirirani uthenga wabwino.
  1088. Mrk 1:16 Tsopano pamene iye anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, iye adawona Simoni ndi Anduru, mbale wake alinkuponya khoka m’nyanja: pakuti adali asodzi.
  1089. Mrk 1:17 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Idzani inu pambuyo panga, ndipo ine ndidzakupangani inu kuti mukhale asodzi a anthu.
  1090. Mrk 1:18 Ndipo nthawi yomweyo iwo adasiya makhoka awo, ndipo anamtsata iye.
  1091. Mrk 1:19 Ndipo pamene iye adapita patsogolo pang’ono, iye adawona Yakobo, mwana [wamwamuna] wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wake, amene iwonso adali m’chombo kusoka makhoka awo.
  1092. Mrk 1:20 Ndipo nthawi yomweyo iye adawayitana iwo: ndipo iwo adasiya atate wawo Zebedayo m’chombo pamodzi ndi antchito wolembedwa, ndipo anamtsata iye.
  1093. Mrk 1:21 Ndipo iwo adapita kulowa m’Kaperenamu; ndipo nthawi yomweyo pa tsiku la sabata iye adalowa m’sunagoge, ndipo anaphunzitsa.
  1094. Mrk 1:22 Ndipo iwo adazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti iye adaphunzitsa iwo monga iye amene adali ndi ulamuliro, ndipo osati monga alembi.
  1095. Mrk 1:23 Ndipo padali m’sunagoge mwawo bambo [amene] adali ndi mzimu wonyansa; ndipo iye adafuwula,
  1096. Mrk 1:24 Kunena kuti, Tisiyeni [ife]; kodi tiri ndi chiyani ife ndi inu, inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzatiwononga ife? Ine ndikudziwani inu amene muli, Woyerayo wa Mulungu.
  1097. Mrk 1:25 Ndipo Yesu adamdzudzula iye, kunena kuti, Khala chete, ndipo tatuluka mwa iye.
  1098. Mrk 1:26 Ndipo pamene mzimu wonyansawo unamung’amba iye, ndipo anafuwula ndi mawu okwera, iwo udatuluka mwa iye.
  1099. Mrk 1:27 Ndipo iwo onse adazizwa, kotero kuti adafunsana mwa iwo wokha, kunena kuti, Chinthu ichi nchiyani? Kodi chiphunzitso chatsopano chotani [ichi]? Pakuti ndi ulamuliro alamula iye ngakhale mizimu yonyansa, ndipo imumvera iye.
  1100. Mrk 1:28 Ndipo posakhalitsa kutchuka kwake kudabuka mofalikira ku dziko lonse lozungulira Galileya.
  1101. Mrk 1:29 Ndipo posakhalitsa, atatuluka m’sunagoge, iwo adalowa m’nyumba ya Simoni ndi Anduru, pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.
  1102. Mrk 1:30 Koma amayi ake a mkazi wa Simoni adali gone wodwala kutentha thupi, ndipo nthawi yomweyo iwo adamuwuza za iye.
  1103. Mrk 1:31 Ndipo iye anadza ndipo anamgwira iye pa dzanja, ndipo anamuwutsa; ndipo nthawi yomweyo kutentha thupi kudamleka iye, ndipo iye adatumukira kwa iwo.
  1104. Mrk 1:32 Ndipo madzulo, pamene dzuwa litalowa, anadza nawo kwa iye onse amene adali wodwala, ndi iwo amene adali wogwidwa ndi ziwanda.
  1105. Mrk 1:33 Ndipo mzinda wonse udasonkhana pamodzi pakhomo,
  1106. Mrk 1:34 Ndipo iye adachiritsa anthu ambiri amene adali wodwala nthenda za mitundumitundu, ndipo anatulutsa ziwanda zambiri; ndipo sadalole ziwandazo kuti ziyankhule, chifukwa izo zidamdziwa iye.
  1107. Mrk 1:35 Ndipo m’mawa adawuka, m’bandakucha kwenikweni, iye anatuluka, ndipo ananyamuka kupita pa malo a payekha, ndipo kumeneko anapemphera.
  1108. Mrk 1:36 Ndipo Simoni ndi iwo amene adali ndi iye adamtsata iye.
  1109. Mrk 1:37 Ndipo pamene adampeza iye, adanena kwa iye, [Anthu] onse afunafuna inu.
  1110. Mrk 1:38 Ndipo iye adanena kwa iwo, Tiyeni tipite kulowa ku mizinda ili pafupipa, kuti ine ndikalalikire kumenekonso: pakuti chifukwa cha ichi ine ndadzera.
  1111. Mrk 1:39 Ndipo adalalikira m’masunagoge mwawo m’Galileya monse, ndipo anatulutsa ziwanda.
  1112. Mrk 1:40 Ndipo adadza wodwala khate kwa iye, kumpempha iye, ndi kugwadira kwa iye, ndi kunena kwa iye. Ngati inu mufuna, inu mukhoza kundiyeretsa ine.
  1113. Mrk 1:41 Ndipo Yesu, mogwidwa ndi chifundo, anatambasula dzanja [lake], ndipo anamkhudza iye, ndi kunena kwa iye, Ine ndifuna; khala iwe wokonzedwa.
  1114. Mrk 1:42 Ndipo pamene atangoyankhula, posakhalitsa khate lidachoka kwa iye, ndipo iye adayeretsedwa.
  1115. Mrk 1:43 Ndipo iye mosachedwetsa adalamulira iye, ndipo nthawi yomweyo anamtumiza iye kumchotsa;
  1116. Mrk 1:44 Ndipo adanena kwa iye, Ona iwe kuti usanene kanthu kwa munthu aliyense: koma pita pa njira yako, ukadziwonetse wekha kwa wansembe, ndipo upereke chifukwa cha makonzedwe ako zinthu zimene Mose adalamulira, zikhale mboni kwa iwo.
  1117. Mrk 1:45 Koma iye adatuluka, ndipo anayamba kulengeza [ichi] kwambiri, ndi kubukitsa mofalikira nkhaniyo, kotero kuti Yesu sakadakhoza kulowanso poyera mu mzindamo, koma adakhala kunja m’malo a zipululu za mchenga: ndipo iwo anadza kwa iye wochokera ku madera onse.
  1118. Mrk 2:1 Ndipo iye adalowanso m’Kaperenamu atapita masiku [ena]; ndipo kudamveka kuti iye adali m’nyumba.
  1119. Mrk 2:2 Ndipo posakhalitsa ambiri adasonkhana pamodzi, kotero kuti adasowa malo wowalandirirapo [iwo], ayi, ngakhale cha pakhomo pomwe: ndipo adalalikira mawu kwa iwo.
  1120. Mrk 2:3 Ndipo iwo anadza kwa iye, kubweretsa wina wodwala matenda akufa ziwalo, amene adanyamulidwa ndi anthu anayi.
  1121. Mrk 2:4 Ndipo pamene iwo sakadakhoza kufika moyandikira kwa iye chifukwa cha khamu la anthu, iwo adasasula denga pamene padali iye: ndipo pamene iwo adatha kulibowola [ilo], iwo adatsitsa kama amene wodwala matenda akufa ziwaloyo adagona.
  1122. Mrk 2:5 Pamene Yesu adawona chikhulupiriro chawo, iye adanena kwa wodwala matenda akufa ziwaloyo, Mwana wamwamuna, machimo ako akhululukidwira iwe.
  1123. Mrk 2:6 Koma padali ena a alembi adakhala pamenepo, ndipo adasinkhasinkha m’mitima mwawo,
  1124. Mrk 2:7 Kodi [munthu] uyu alankhula chotero zonyoza [Mulungu]? Ndani akhoza kukhululukira machimo koma Mulungu yekha?
  1125. Mrk 2:8 Ndipo posakhalitsa pamene Yesu adazindikira mu mzimu wake kuti alikusinkhasinkha chomwecho pakati pa iwo wokha, iye adanena kwa iwo, Bwanji inu musinkhasinkha zinthu izi m’mitima yanu?
  1126. Mrk 2:9 Kodi chapafupi n’chiti kumuwuza wodwala matenda akufa ziwalo, Machimo [ako] akhululukidwa; kapena kunena kuti; Nyamuka, ndipo tenga kama wako, ndipo uyende?
  1127. Mrk 2:10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wamwamuna wa munthu ali ndi mphamvu pa dziko lapansi zakukhululukira machimo, (adanena kwa wodwala matenda akufa ziwaloyo,)
  1128. Mrk 2:11 Ine ndinena kwa iwe, Nyamuka, ndipo tenga kama wako, ndipo umuke pa njira ya kulowa kunyumba yako.
  1129. Mrk 2:12 Ndipo posakhalitsa iye adanyamuka, natenga kamayo, ndipo ananyamuka kupita pamaso pa iwo onse; kotero kuti onse anadabwa, ndipo analemekeza Mulungu, kunena kuti, Ife sitidaziwonepo zikuchitika motere.
  1130. Mrk 2:13 Ndipo iye adapitanso kumka m’mbali mwa nyanja; ndipo khamu lonse la anthu linadza kwa iye; ndipo iye adawaphunzitsa iwo.
  1131. Mrk 2:14 Ndipo pamene iye ankadutsa, iye adawona Levi mwana [wamwamuna] wa Alafeyasi atakhala pamalo polandirira msonkho, ndipo adanena kwa iye, Tsata ine. Ndipo iye adanyamuka ndi kumtsata iye.
  1132. Mrk 2:15 Ndipo kudachitika, kuti, pamene Yesu adakhala pa chakudya m’nyumba mwake, wokhometsa misonkho ambiri ndi wochimwanso adakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi wophunzira ake: pakuti padali ambiri, ndipo adamtsata iye.
  1133. Mrk 2:16 Ndipo pamene alembi ndi Afarisi adawona iye kuti alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi wochimwa, iwo adanena kwa wophunzira ake, Motani kuti uyu akudya ndi kumwa nawo amisonkho ndi wochimwa?
  1134. Mrk 2:17 Pamene Yesu adamva [ichi], iye adanena kwa iwo, iwo amene ali wolimba safuna dotolo, koma iwo amene ali wodwala: Ine sindidadza kudzayitana wolungama, koma wochimwa ku kulapa.
  1135. Mrk 2:18 Ndipo wophunzira a Yohane ndi Afarisi adazolowera kusala kudya: ndipo iwo anadza ndi kunena kwa iye, Bwanji wophunzira a Yohane ndi Afarisi asala kudya koma wophunzira anu sasala kudya?
  1136. Mrk 2:19 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, kodi ana a nyumba ya ukwati angathe kusala kudya, pamene mkwati ali pamodzi ndi iwo? Pokhala iwo nthawi imene mkwati akhala pamodzi ndi iwo, iwo sangathe kusala.
  1137. Mrk 2:20 Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo nthawi imeneyo adzasala kudya m’masiku amenewo.
  1138. Mrk 2:21 Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yatsopano pa chovala chakale: kapena chigamba chatsopanocho chimene chinakwanapo chikhoza kuzomoka kuchotsako ku yakaleyo, ndipo chibowo chake chikhala chokulirapo.
  1139. Mrk 2:22 Ndipo palibe munthu amayika vinyo watsopano m’mabotolo azikopa akale: kapena vinyo watsopanoyo adzaphulitsa mabotolo azikopawo, ndipo vinyoyo akhuthuka, ndipo mabotolo azikopa kuwonongeka: koma vinyo watsopano ayenera kuyikidwa m’mabotolo azikopa atsopano.
  1140. Mrk 2:23 Ndipo kudachitika, kuti adapita iye pakati pa minda ya tirigu tsiku la sabata; ndipo wophunzira ake, pamene ankayenda, adayamba kubudula ngala za tirigu.
  1141. Mrk 2:24 Ndipo Afarisi adanena kwa iye, Tawonani, kodi achitiranji iwo pa tsiku la sabata chili chosaloleka mwa lamulo kuchitika?
  1142. Mrk 2:25 Ndipo iye adanena kwa iwo, Kodi inu simudawerenga konse chimene adachichita Davide, pamene adali ndi chosowa, ndipo adamva njala, iye, ndi iwo amene adali pamodzi ndi iye?
  1143. Mrk 2:26 Momwe iye adalowera m’nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara wansembe wamkulu, ndipo anadya mikate yowonetsera, imene ili yosaloleka kudya koma kwa ansembe, ndipo adaperekanso kwa iwo amene adali pamodzi ndi iye?
  1144. Mrk 2:27 Ndipo iye adanena kwa iwo, Sabata lidayikidwa chifukwa cha munthu, ndipo osati munthu chifukwa cha sabata:
  1145. Mrk 2:28 Choncho Mwana wamwamuna wa munthu alinso Mbuye wa sabata.
  1146. Mrk 3:1 Ndipo iye adalowanso msunagoge; ndipo mudali bambo m’menemo amene adali ndi dzanja lake lopuwala.
  1147. Mrk 3:2 Ndipo adamulondalonda iye, ngati iye akadamuchiritsa iye pa tsiku la sabata; kuti iwo amuyimbe mlandu womtsutsa iye.
  1148. Mrk 3:3 Ndipo iye adanena kwa bambo amene adali ndi dzanja lopuwala, Imirira.
  1149. Mrk 3:4 Ndipo iye adanena kwa iwo, N’kololedwa mwa lamulo kuchita zabwino pa masiku a sabata, kapena kuchita zoyipa? Kupulumutsa moyo, kapena kupha? Koma iwo adakhala chete.
  1150. Mrk 3:5 Ndipo m’mene adayang’ana mozungulira pa iwo ndi mkwiyo, pomvetsedwa chisoni chifukwa cha kuwuma mitima yawo, iye adanena kwa bamboyo, Tambasula dzanja lako, Ndipo iye adalitambasula [ilo]: ndipo dzanja lake lidakhala bwino monga linzake.
  1151. Mrk 3:6 Ndipo Afarisi adatuluka, ndipo pomwepo adamchitira upo ndi Aherode wa kumtsutsa iye, momwe angamuwonongere iye.
  1152. Mrk 3:7 Koma Yesu iye mwini adachokapo pamodzi ndi wophunzira ake kupita ku nyanja: ndipo khamu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya lidamtsata iye, ndi lochokera ku Yudeya,
  1153. Mrk 3:8 Ndi wochokera ku Yerusalemu, ndi lochokera ku Idumeya, ndi [lochokera] kupitirira ku Yordano; ndi a kufupi ndi ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikulu, pamene iwo adamva zazikulu zimene adazichita, linadza kwa iye.
  1154. Mrk 3:9 Ndipo iye adayankhula kwa wophunzira ake, kuti chombo chaching’ono chidikire pa iye chifukwa cha khamulo, kuti iwo angamkanikize iye.
  1155. Mrk 3:10 Pakuti adachiritsa ambiri; kotero kuti iwo adakanikizana pa iye kuti amkhudze iye, ambiri a iwo wokhala nayo miliri.
  1156. Mrk 3:11 Ndipo mizimu yonyasa, m’mene iyo inamuwona iye, idagwa pansi pamaso pake, ndi kufuwula, kunena kuti, Inu ndinu Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  1157. Mrk 3:12 Ndipo iye mosachedwetsa adayilamulira kuti iyo isampangitse iye kudziwika.
  1158. Mrk 3:13 Ndipo iye akwera kupita m’phiri, ndipo anadziyitanira [kwa iye] omwe iye adafuna: ndipo anadza kwa iye.
  1159. Mrk 3:14 Ndipo adadzoza khumi ndi awiriwo, kuti iwo akhale ndi iye, ndi kuti iye akhoze kuwatuma kukalalikira,
  1160. Mrk 3:15 Ndi kuti akhale ndi mphamvu zakuchiritsa matenda, ndi kutulutsa ziwanda.
  1161. Mrk 3:16 Ndipo Simoni adamutcha Petro;
  1162. Mrk 3:17 Ndi Yakobo [mwana wamwamuna] wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo; iwo adawatcha Bowanagesi, ndiko kuti, Ana amuna a bingu:
  1163. Mrk 3:18 Ndi Anduru, ndi Filipi ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo [mwana wamwamuna] wa Alifeyasi, ndi Tadeyasi, ndi Simoni Mkanani,
  1164. Mrk 3:19 Ndi Yudase Iskariyote, amenenso adampereka iye: ndipo iwo adapita kulowa m’nyumba.
  1165. Mrk 3:20 Ndipo khamulo lidasonkhananso pamodzi, kotero kuti iwo sakadatha kuti adye konse mkate.
  1166. Mrk 3:21 Ndipo pamene abwenzi ake adamva [za ichi], iwo adapita kuti amgwire iye: pakuti iwo adati, Iye ali woyaluka.
  1167. Mrk 3:22 ¶Ndipo alembi amene adatsika kuchokera ku Yerusalemu adati, Iye ali ndi Belezebule, ndipo ndi kalonga wawo wa ziwanda iye atulutsa ziwanda.
  1168. Mrk 3:23 Ndipo adawayitana iwo [kwa iye], ndipo ananena kwa iwo m’mafanizo, Angathe bwanji Satana kutulutsa Satana?
  1169. Mrk 3:24 Ndipo ngati ufumu ugawanika pa iwo wokha, ufumu umenewo sukhoza kukhazikika.
  1170. Mrk 3:25 Ndipo ngati nyumba igawika motsutsana iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kukhazikika.
  1171. Mrk 3:26 Ndipo ngati Satana adziwukira mwini yekha, ndi kukhala wogawanika, iye sangathe kuyima, koma ali ndi mathero.
  1172. Mrk 3:27 Palibe munthu akhoza kulowa m’nyumba ya munthu wamphamvu; ndi kuwononga katundu wake, pokhapokha iye ayambe wamanga munthu wamphamvuyo; ndipo pamenepo iye adzawononga nyumba yake.
  1173. Mrk 3:28 Ndithudi ndinena kwa inu, Machimo onse adzakhululukidwa kwa ana amuna a anthu, ndi zonena zamwano zirizonse iwo adzanena.
  1174. Mrk 3:29 Koma iye amene adzanenera zonyoza Mzimu Woyera sadzakhala ndi kukhululukidwa nthawi yonse, koma ali m’ngozi ya chiweruzo chosatha:
  1175. Mrk 3:30 Chifukwa iwo adanena, Iye ali ndi mzimu wonyansa.
  1176. Mrk 3:31 ¶Kenaka panadza abale ake ndi amayi ake, ndipo, atayima kunja, anatumiza uthenga kwa iye, kuyitana iye.
  1177. Mrk 3:32 Ndipo khamu lidakhala pansi momzungulira iye; ndipo ananena kwa iye, Onani, amayi anu ndi abale anu ali kunja akukufunani inu.
  1178. Mrk 3:33 Ndipo iye adawayankha iwo, kunena kuti, Amayi wanga ndani, kapena abale anga?
  1179. Mrk 3:34 Ndipo iye adawayang’ana mozungulira pa iwo amene adakhala mozungulira iye, ndipo ananena, Tawonani amayi wanga ndi abale anga!
  1180. Mrk 3:35 Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndi mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi.
  1181. Mrk 4:1 Ndipo iye adayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja: ndipo lidasonkhana kwa iye khamu lalikulu kwambiri, kotero kuti iye adalowa m’chombo, ndipo anakhala m’nyanja; ndipo khamu lonse lidali m’mbali mwa nyanja pamtunda.
  1182. Mrk 4:2 Ndipo iye adawaphunzitsa iwo zinthu zambiri mwa mafanizo, ndipo ananena kwa iwo chiphunzitso chake.
  1183. Mrk 4:3 Mverani; Tawonani, padatuluka wofesa kukafesa:
  1184. Mrk 4:4 Ndipo kudachitika, kuti pamene anali kufesa, zina zidagwa m’mbali mwa njira, ndi mbalame zamum’lengalenga zinadza ndi kudya iyo.
  1185. Mrk 4:5 Ndipo zina zinagwa panthaka ya miyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo posakhalitsa zinamera, chifukwa idalibe dothi lakuya:
  1186. Mrk 4:6 Ndipo pamene dzuwa lidakwera, idapserezedwa; ndipo chifukwa idalibe muzu, idafota.
  1187. Mrk 4:7 Ndipo zina zidagwa pakati pa minga, ndipo mingayo idakula, ndipo inayitsamwitsa iyo, ndipo siyinabala chipatso.
  1188. Mrk 4:8 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo idapatsa chipatso chimene chidaphuka n’kukula ndi kuchuluka; ndipo inabala, zina makumi atatu, ndi zina makumi asanu ndi limodzi, ndi zina makumi khumi.
  1189. Mrk 4:9 Ndipo iye adanena kwa iwo, Iye amene ali nawo makutu akumva amve.
  1190. Mrk 4:10 Ndipo pamene iye adali payekha, iwo amene adali pafupi ndi iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo adamfunsa kwa iye za fanizolo.
  1191. Mrk 4:11 Ndipo iye adanena kwa iwo, Kwa inu kwapatsidwa kudziwa chinsinsi cha ufumu wa Mulungu: koma kwa iwo amene ali kunja, zonse zinthu [izi] zichitidwa m’mafanizo:
  1192. Mrk 4:12 Kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva akhoza kumva, koma asamvetsetse; pena pa nthawi ina iliyonse iwo angatembenuke mtima, ndi machimo [awo] kukhululukidwa.
  1193. Mrk 4:13 Ndipo iye adanena nawo, Simudziwa inu kodi fanizo ili? Ndipo kotero inu mudzazindikira bwanji mafanizo onse?
  1194. Mrk 4:14 ¶Wofesa afesa mawu.
  1195. Mrk 4:15 Ndipo awa ndiwo a m’mbali mwa njira, malo amene mawu afesedwa; koma pamene iwo amva; Satana amadza posakhalitsa, ndipo amachotsa mawu amene anafesedwa m’mitima mwawo.
  1196. Mrk 4:16 Ndipo awa ndiwo momwemonso amene afesedwa panthaka yamiyala; amene, pamene iwo amva mawu, posakhalitsa awalandira ndi kukondwera;
  1197. Mrk 4:17 Ndipo alibe mizu mwa iwo wokha, ndipo kotero apirira kwa kanthawi: pambuyo pake, pamene masawutso kapena mazunzo abuka chifukwa cha mawu, posakhalitsa iwo akhumudwitsidwa.
  1198. Mrk 4:18 Ndipo awa ndiwo amene afesedwa pakati pa minga; monga iwo amene amva mawu,
  1199. Mrk 4:19 Ndipo chisamaliro cha dziko lapansili, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina polowamo, zitsamwitsa mawu, ndipo ikhala yopanda chipatso.
  1200. Mrk 4:20 Ndipo awa ndiwo amene afesedwa panthaka yabwino; monga iwo otere amva mawu, ndipo awalandira [iwo], ndipo abala chipatso, ena makumi atatu, ena makumi asanu ndi limodzi, ndi ena makumi khumi.
  1201. Mrk 4:21 ¶Ndipo adanena kwa iwo, Kodi nyali itengedwa kuti ikayikidwe pansi pa mbiya, kapena pansi pa kama? Osati kuti iyikidwe pa choyikapo nyali?
  1202. Mrk 4:22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, kamene sikadzawonetsedwa; kapena panali kanthu kena kalikonse kosungidwa mwachinsinsi, koma kuti kadzawululidwe.
  1203. Mrk 4:23 Ngati munthu aliyense ali ndi makutu akumva, iye amve.
  1204. Mrk 4:24 Ndipo iye adanena kwa iwo, Samalirani chimene inu mukumva: ndi muyeso omwewo inu muyesa nawo, udzayesedwa kwa inu: ndipo kwa inu amene mukumva zambiri kudzapatsidwa.
  1205. Mrk 4:25 Pakuti kwa iye amene ali nako, kwa iye kudzapatsidwa: ndipo iye amene alibe, kuchokera kwa iye kudzatengedwa ngakhale chimene ali nacho.
  1206. Mrk 4:26 ¶Ndipo iye adanena, Moteromo ndi momwe uli ufumu wa Mulungu, monga ngati munthu angaponye mbewu mu nthaka;
  1207. Mrk 4:27 Ndipo agone, ndi kuwuka usiku ndi usana, ndipo mbewu zimere ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.
  1208. Mrk 4:28 Pakuti dziko libala chipatso chake lokha; poyamba m’mera, kenaka ngala, pakutha apo maso wokhwima m’ngalamo.
  1209. Mrk 4:29 Koma pamene zipatso zabereka, posakhalitsa iye ayika zenga, pakuti kholola lafika.
  1210. Mrk 4:30 ¶Ndipo iye adanena, Tidzafanizira ndi chiyani ufumu wa Mulungu? Kapena tidzawulinganiza ife ndi chilinganizo chotani?
  1211. Mrk 4:31 [Uli] ngati mbewu ya mpiru, imene, pamene ifesedwa m’nthaka, ili yaying’ono mwa mbewu zonse zikhala m’dziko lapansi:
  1212. Mrk 4:32 Koma pamene ifesedwa, iyo ikula, ndipo iposa zitsamba zonse, ndipo itulutsa nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za mum’lengalenga zikhoza kubindikira pansi pa m’nthunzi wake.
  1213. Mrk 4:33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri iye adayankhula mawu kwa iwo, monga iwo adali nako kuthekera kwa kumva [iwo].
  1214. Mrk 4:34 Koma sadayankhule ndi iwo iye wopanda fanizo: ndipo pamene iwo anali pa wokha, iye adatanthawuzira zinthu zonse kwa wophunzira ake.
  1215. Mrk 4:35 Ndipo tsiku lomwero, atafika madzulo, iye adanena kwa iwo, Tiyeni tiwolokere ku tsidya lina.
  1216. Mrk 4:36 Ndipo pamene adalitumiza khamulo, iwo adamtenga iye ngakhale momwe iye adali m’chombo. Ndipo padali pamodzi ndi iye zombo zina zazing’ono.
  1217. Mrk 4:37 Ndipo padawuka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde adagavira chombo, kotero kuti chombo chidadzaza.
  1218. Mrk 4:38 Ndipo iye adali kumbuyo kwa chombo, kugona tulo pa mtsamiro: ndipo iwo adamudzutsa iye, ndipo ananena kwa iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti ife tiwonongeke?
  1219. Mrk 4:39 Ndipo iye adadzuka, ndipo anadzudzula mphepo, ndipo anati kwa nyanja, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo idaleka, ndipo kudali bata lalikulu.
  1220. Mrk 4:40 Ndipo adanena kwa iwo, Kodi inu muchitiranji mantha chotere? Zikutheka bwanji kuti inu mulibe chikhulupiriro?
  1221. Mrk 4:41 Ndipo iwo adachita mantha koposa, ndipo ananena wina kwa mzake, Kodi munthu uyu ndi wotani, kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera iye?
  1222. Mrk 5:1 Ndipo iwo adadza ku tsidya lina la nyanja, kulowa m’dziko la Agadarene.
  1223. Mrk 5:2 Ndipo pamene adatuluka m’chombomo, posakhalitsa adakomana naye wotuluka ku manda bambo wogwidwa ndi mzimu wonyansa,
  1224. Mrk 5:3 Amene adali ndi nyumba [yake] pakati pa mitumbira; ndipo padalibe munthu akadakhoza kum’manga, ayi, ngakhale ndi maunyolo:
  1225. Mrk 5:4 Chifukwa kuti iye ankamangidwa kawirikawiri ndi zingwe zachitsulo ndi maunyolo, ndipo maunyolo anadulidwa mbwee ndi iye, ndi zingwe zachitsulo kudulidwa m’magawo: kapena [panalibe munthu] aliyense amene akadakhoza kumsunga iye.
  1226. Mrk 5:5 Ndipo nthawi zonse, usiku ndi usana, iye adali m’mapiri, ndi m’mitumbira, nafuwula, ndi kudzitematema yekha ndi miyala.
  1227. Mrk 5:6 Koma pamene adamuwona Yesu patali, iye adathamanga namlambira iye.
  1228. Mrk 5:7 Ndipo adafuwula ndi mawu okwera, ndipo ananena, Ndiri ndi chiyani ndi inu, Yesu, [inu] Mwana wamwamuna wa Mulungu wam’mwambamwamba? Ndikulamulirani mwa Mulungu, kuti inu musandizunze ine ayi.
  1229. Mrk 5:8 Pakuti iye adanena kwa iye, Tuluka mwa munthuyu, [iwe] mzimu wonyansa.
  1230. Mrk 5:9 Ndipo iye adamfunsa iye, Dzina lako ndani? Ndipo iye adayankha, kunena kuti, Dzina langa [ndi] Legiyoni: pakuti tiri ambiri.
  1231. Mrk 5:10 Ndipo adampempha iye kwambiri kuti iye asayitumize iyo kunja kwake kwa dzikolo.
  1232. Mrk 5:11 Tsopano padali kufupi ndi mapiri gulu lalikulu la nkhumba zidali kudya.
  1233. Mrk 5:12 Ndipo mizimu yonse yoyipa idampempha iye, kunena kuti, Titumuzeni ife mu nkhumbazo, kuti ife tilowe mu izo.
  1234. Mrk 5:13 Ndipo nthawi yomweyo Yesu adayilola kuti ichoke. Ndipo mizimu yonyansa idatuluka, ndi kulowa mukhumba: ndipo gululo lidathamanga mwa chiwawa potsetsereka kulowa m’nyanja; (izo zidali ngati zikwi ziwiri;) ndipo zidatsamwitsidwa m’nyanja.
  1235. Mrk 5:14 Ndipo iwo amene amaweta nkhumbazo adathawa, ndipo anakanena [ichi] mu mzinda, ndi m’dzikolo. Ndipo iwo adatuluka kukawona chomwe chidali chimene chochitikacho.
  1236. Mrk 5:15 Ndipo iwo anadza kwa Yesu, ndipo anapenya iye amene adali wogwidwa ndi mzimu woyipayo, ndipo adali ndi legiyoni; atakhala pansi, ndipo wovala, ndi wa maganizo abwinobwino: ndipo iwo adawopa.
  1237. Mrk 5:16 Ndipo iwo amene adapenya [ichi] adawafotokozera iwo umo zidachitikira kwa iye amene adali wogwidwa ndi mzimu woyipayo, ndiponso zokhudzana ndi nkhumbazo.
  1238. Mrk 5:17 Ndipo adayamba kupempha iye kuti atuluke m’dziko lawo.
  1239. Mrk 5:18 Ndipo m’mene iye adalowa m’chombo, iye amene adali wogwidwa ndi mzimu woyipayo uja adampempha kuti akhoze kukhala ndi iye.
  1240. Mrk 5:19 Komabe Yesu sadamulola iye, koma adanena kwa iye, Pita kwanu kwa abwenzi ako, ndipo uwawuze iwo zinthu zazikulu motani Ambuye adakuchitira iwe, ndipo adali ndi chifundo pa iwe.
  1241. Mrk 5:20 Ndipo iye adanyamuka, ndipo anayamba kulalikira ku Dekapolisi momwe ukulu wa zinthu Yesu adamchitira iye: ndipo [anthu] onse adazizwa.
  1242. Mrk 5:21 Ndipo pamene Yesu adawolokanso m’chombo kupita tsidya lina, anthu ambiri adasonkhana kwa iye: ndipo iye anali pafupi ndi nyanja.
  1243. Mrk 5:22 Ndipo, tawonani, adadzako m’modzi wa olamulira a sunagoge, dzina lake Jayirasi; ndipo pamene anawona iye, iye adagwa pa mapazi ake,
  1244. Mrk 5:23 Ndipo nampempha iye kwambiri, kunena kuti, Kamwana kanga kakakazi kalikugona kali pafupi kufa: [ine ndikupemphani inu] mubwere ndi kuyika manja anu pa iko, kuti kakhoze kuchiritsidwa; ndipo adzakhala ndi moyo.
  1245. Mrk 5:24 Ndipo [Yesu] adamka naye pamodzi; ndipo anthu ambiri adamtsata iye, ndi kumkanikiza iye.
  1246. Mrk 5:25 Ndipo mkazi wina, amene adali ndi nthenda ya mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri,
  1247. Mrk 5:26 Ndipo adamva zinthu zowawa zambiri mwa adotolo ambiri, ndipo anagulitsa zonse anali nazo kulipira, ndipo osasintha kupeza bwino konse, koma m’malo mwake nthenda idakula.
  1248. Mrk 5:27 Pamene iye adamva za Yesu, anadza kumbuyo m’khamu la anthu, ndipo anakhudza chovala chake.
  1249. Mrk 5:28 Pakuti iye adanena, Ngati ine ndingakhudze maka zovala zake, ine ndidzachiritsidwa.
  1250. Mrk 5:29 Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake ya mwazi adawuma; ndipo iye adazindikira m’thupi [lake] kuti adachiritsidwa ku mliri wake.
  1251. Mrk 5:30 Ndipo Yesu, posakhalitsa pozindikira mwa iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa iye, adatembenukira iye mu khamu la anthulo, ndipo ananena, Ndani anakhudza zovala zanga?
  1252. Mrk 5:31 Ndipo wophunzira ake adanena kwa iye, Inu mukuwona kuti khamu liri kukanikiza inu, ndipo munena inu, Wandikhudza ine ndani?
  1253. Mrk 5:32 Ndipo iye adawunguzawunguza kuti awone iye amene adachita chinthu ichi.
  1254. Mrk 5:33 Koma mkaziyo powopa ndi kunthunthumira, podziwa chimene chidachitidwa mwa iye, adadza ndipo anagwa pamaso pa iye, ndipo anamuwuza iye chowona chonse.
  1255. Mrk 5:34 Ndipo iye adati kwa iye, Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe; pita mu mtendere, ndipo ukhale wochira ku mliri wako.
  1256. Mrk 5:35 M’mene iye adali chiyankhulire, adadza [ena] kuchokera [kunyumba] ya wolamulira wa sunagoge amene ananena kuti, Mwana wako wamkazi wafa: iwe upitiriziranji kuvutitsa Mphunzitsiyu?
  1257. Mrk 5:36 Mwamsanga atangomva Yesu mawu anayankhulidwawo, iye adanena kwa wolamulira wa sunagoge, Usawope, khulupilira kokha.
  1258. Mrk 5:37 Ndipo iye sadalole munthu aliyense kumtsatira iye, kupatula Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo.
  1259. Mrk 5:38 Ndipo adadza kunyumba kwake kwa wolamulira wa sunagoge, ndipo adawona chipiringu, ndi iwo wobuma ndi wolira kwambiri.
  1260. Mrk 5:39 Ndipo m’mene iye adalowa, iye adanena kwa iwo, Kodi muchita inu ichi bwanji, ndi kulira? Mtsikanayu sadafe, koma akugona.
  1261. Mrk 5:40 Ndipo iwo adamseka iye monyogodola, Koma pamene iye adawatulutsa kunja iwo onse, iye adatenga atate ndi amayi ake a mtsikanayo ndi aja amene adali ndi iye, ndipo analowa m’mene mudali mtsikanayo.
  1262. Mrk 5:41 Ndipo iye adagwira mtsikanayo ndi dzanja, ndipo ananena kwa iye, Talita kumi; kumene kutanthawuza kwake kuli, Mtsikana, Ine ndinena kwa iwe, uka.
  1263. Mrk 5:42 Ndipo pomwepo mtsikanayo adawuka, ndipo anayenda; pakuti iye adali [wa zaka] khumi ndi ziwiri. Ndipo iwo anadabwa ndi kudabwa kwakukulu.
  1264. Mrk 5:43 Ndipo iye adawalamulira iwo monenetsa kuti munthu wina aliyense asadziwe ichi; ndipo analamulira kuti china chake chipatsidwe kwa iye kuti adye.
  1265. Mrk 6:1 Ndipo iye adatuluka kuchoka kumeneko, ndipo anadza kulowa m’dziko la kwawo; ndipo wophunzira ake adamtsata iye.
  1266. Mrk 6:2 Ndipo pamene tsiku la sabata linafika, iye adayamba kuphunzitsa m’sunagoge: ndipo ambiri akumva [iye] anazizwa, kunena kuti, Kuchokera kuti kumene [munthu] uyu adazitenga izi? Ndipo ndi nzeru yanji iyi imene yapatsidwa kwa iyeyu? Kuti ngakhale ntchito zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?
  1267. Mrk 6:3 Kodi uyu si m’misiri wa matabwa, mwana wamwamuna wa Mariya, mbale wawo wa Yakobo, ndi Josesi, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ake si ali nafe pano kodi? Ndipo adakhumudwa ndi iye.
  1268. Mrk 6:4 Koma Yesu adanena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwawo ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m’nyumba yake.
  1269. Mrk 6:5 Ndipo iye sadakhoza kumeneko kuchita ntchito zamphamvu konse, kupatula kuti iye adayika manja ake pa anthu wodwala wochepa, ndipo anawachiritsa [iwo].
  1270. Mrk 6:6 Ndipo iye adazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Ndipo adayendayenda kuzungulira m’midzi, kuphunzitsa.
  1271. Mrk 6:7 ¶Ndipo iye adadziyitanira [kwa iye] khumi ndi awiriwo, ndipo anayamba kuwatumiza iwo awiri awiri; ndipo anawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa.
  1272. Mrk 6:8 Ndipo adawalamulira iwo kuti asatenge kanthu ka pa ulendo [wawo], kupatula ndodo yokha; opanda chikwama, mkate, kapena ndalama m’matumba [awo]:
  1273. Mrk 6:9 Koma [akhale] wovekedwa ndi nsapato; ndipo asavale malaya awiri.
  1274. Mrk 6:10 Ndipo iye adanena kwa iwo, Mu malo ena aliwonse mukalowa m’nyumba, momwemo mukhale kufikira mutanyamuka kuchoka ku malo amenewo.
  1275. Mrk 6:11 Ndipo wina aliyense amene sadzakulandirani inu, kapena kumvera inu, pamene inu muchoka kumeneko, sansani fumbi liri pansi pa mapazi anu likhale umboni wotsutsa iwo, Ndithudi ndinena kwa inu, Kudzakhala kulolera kwakukulu kwa Sodomu ndi Gomora mu tsiku la chiweruzo kuposa kwa mzinda umenewo.
  1276. Mrk 6:12 Ndipo iwo adatuluka, ndipo analalikira kuti anthu alape.
  1277. Mrk 6:13 Ndipo iwo adatulutsa mizimu yoyipa yambiri, ndipo anadzoza ndi mafuta anthu ambiri amene adali wodwala, ndipo anawachiritsa [iwo].
  1278. Mrk 6:14 Ndipo mfumu Herode adamva [za iye]; (pakuti dzina lake lidafalikira kutali:) ndipo iye adanena, Kuti Yohane Mbatizi anawuka kwa akufa, ndipo choncho ntchito za mphamvuzi zidziwonetsera zokha mwa iye.
  1279. Mrk 6:15 Ena adati, Ameneyu ndi Eliya. Ndipo ena adati, Ameneyo ndi mneneri, kapena monga m’modzi wa aneneriwo.
  1280. Mrk 6:16 Koma pamene Herode adamva [za izo], iye adanena, Ndi Yohane, amene ine ndinamdula mutu: wawuka kwa akufa.
  1281. Mrk 6:17 Pakuti Herode mwini yekha adatuma anthu ndipo anamgwira Yohane, ndipo anam’manga iye m’ndende chifukwa cha Herodiyas, mkazi wa Filipi mbale wake: pakuti iye adamkwatira iye.
  1282. Mrk 6:18 Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Sikuloledwa mwa lamulo kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.
  1283. Mrk 6:19 Choncho Herodiyas adachita mkangano womtsutsa iye, ndipo akanamupha iye; koma iye sadathe:
  1284. Mrk 6:20 Pakuti Herode adawopa Yohane, podziwa kuti adali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo adamyang’anira iye; ndipo pamene iye adamumva iye, iye adachita zinthu zambiri, ndipo anamumva iye mokondwera.
  1285. Mrk 6:21 Ndipo pamene lidafika tsiku loyenera, kuti pa tsiku la kubadwa kwake kwa Herode adakonzera phwando akulu ake, akazembe akulu, ndi anthu akulu [wotchuka] a ku Galileya;
  1286. Mrk 6:22 Ndipo pamene mwana wamkazi wa iye wotchedwa Herodiyas adalowa, ndipo anavina, ndipo anakondweretsa Herode ndi iwo amene adakhala ndi iye; mfumuyo idati kwa mtsikanayo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndipo ine ndidzakupatsa iwe [icho].
  1287. Mrk 6:23 Ndipo adalumbirira kwa iye, Chilichonse iwe ukapempha kwa ine, ine ndidzakupatsa iwe [icho], kufikira theka la ufumu wanga.
  1288. Mrk 6:24 Ndipo adatuluka, ndipo ananena kwa amayi wake, Kodi ine ndidzapempha chiyani? Ndipo iye adati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi.
  1289. Mrk 6:25 Ndipo pomwepo adalowa mwachangu kwa mfumu, ndipo anapempha, kunena kuti, Ine ndifuna mundipatse kamodzi nkamodzi, mutu wa Yohane Mbatizi m’mbale.
  1290. Mrk 6:26 Ndipo mfumu idamva chisoni chachikulu, [komatu] chifukwa cha lumbiro lake, ndi chifukwa cha iwo amene adakhala ndi iye, iye sakadamkana iye.
  1291. Mrk 6:27 Ndipo posakhalitsa mfumu idatuma wokamupha, ndipo analamulira akabweretse mutu wake: ndipo iye adapita namdula mutu m’ndende.
  1292. Mrk 6:28 Ndipo adabweretsa mutu wake m’mbale, ndipo anawupereka kwa mtsikanayo; ndipo mtsikanayo adawupereka kwa amayi ake.
  1293. Mrk 6:29 Ndipo m’mene wophunzira ake adamva [za ichi], iwo anadza ndi kunyamula mtembo wake, ndipo anawuyika m’manda.
  1294. Mrk 6:30 Ndipo atumwi adasonkhana pamodzi mwa iwo wokha kwa Yesu; ndipo anamuwuza zinthu zonse, zimene adazichita ndi kuziphunzitsa.
  1295. Mrk 6:31 Ndipo iye adanena kwa iwo, Idzani inu nokha padera kulowa ku malo a chipululu cha mchenga, ndipo mupumule kanthawi: pakuti padali ambiri akudza ndi akuchoka ndipo adalibe nthawi yopumula yokwanira yakuti adye.
  1296. Mrk 6:32 Ndipo adachoka nakwera chombo kupita ku malo a chipululu cha mchenga mwa chinsinsi.
  1297. Mrk 6:33 Ndipo anthu adawawona iwo ali kunyamuka, ndipo ambiri adamdziwa iye, ndipo anathamangira pa mapazi nadza kwa iye wochokera m’mizinda yonse, ndipo anawapitirira iwo, ndipo anabwera pamodzi kwa iye.
  1298. Mrk 6:34 Ndipo Yesu, pamene adatuluka, anawona anthu ambiri, ndipo anagwidwa ndi chifundo ndi iwo, pakuti adali ngati nkhosa zimene ziri zopanda mbusa: ndipo iye adayamba kuwaphunzitsa iwo zinthu zambiri.
  1299. Mrk 6:35 Ndipo pamene tsiku lidapita ndithu, wophunzira ake anadza kwa iye, ndipo ananena, Malo ano ndi a chipululu cha mchenga, ndipo tsopano nthawi yatha ndithu:
  1300. Mrk 6:36 Muwatumize iwo kuti apite, kuti alowe m’dziko lozungulira, ndi kulowa m’midzi, ndi kudzigulira wokha mkate: pakuti alibe kanthu kakuti adye.
  1301. Mrk 6:37 Iye adayankha ndi kunena kwa iwo, Apatseni ndinu kuti adye. Ndipo iwo adanena kwa iye, Kodi ife tipite ndi kugula mikate yokwana makobiri mazana awiri, ndipo kuwapatsa kuti adye?
  1302. Mrk 6:38 Iye adanena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Pitani ndipo mukawone. Ndipo m’mene adadziwa, iwo adanena, Isanu, ndi nsomba ziwiri.
  1303. Mrk 6:39 Ndipo iye adawalamulira kuti awakhalitse pansi onse magulumagulu pawudzu wobiriwira.
  1304. Mrk 6:40 Ndipo iwo adakhala pansi mabungwemabungwe, a mazana, ndi makumi asanu.
  1305. Mrk 6:41 Ndipo pamene iye adatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, iye anayang’ana kumwamba, ndipo anadalitsa, ndipo ananyema mikateyo; ndipo anapatsa [iyo] kwa wophunzira kuti ayike pamaso pawo; ndi nsomba ziwirizo adagawa iye pakati pa onsewo.
  1306. Mrk 6:42 Ndipo iwo onse anadya, ndipo anakhuta.
  1307. Mrk 6:43 Ndipo adatola madengu khumi ndi awiri wodzaza ndi makombo, ndipo a nsombazo.
  1308. Mrk 6:44 Ndipo iwo amene adadya mikateyo adali pafupifupi amuna zikwi zisanu.
  1309. Mrk 6:45 Ndipo pomwepo iye adakakamiza wophunzira ake alowe m’chombo, ndi kutsogola kupita ku tsidya lina ku Betsayida, pamene iye adali kuwuza khamulo kuti lizipita.
  1310. Mrk 6:46 Ndipo pamene iye anawawuza kuti apite, iye adanyamuka kulowa m’phiri kukapemphera.
  1311. Mrk 6:47 Ndipo atafika madzulo, chombo chidali pakati pa nyanja, ndi iye yekha adali pamtunda.
  1312. Mrk 6:48 Ndipo pamene adawawona iwo ali kuvutika ndi kupalasa; pakuti mphepo idadza motsutsana ndi iwo: ndipo pa ulonda wachinayi wa usiku iye anadza kwa iwo, alikuyenda panyanja, ndipo akadapitirira iwo.
  1313. Mrk 6:49 Koma pamene iwo adamuwona iye alikuyenda panyanja, iwo adayesa kuti udali mzukwa, ndipo anafuwula:
  1314. Mrk 6:50 Pakuti iwo onse adamuwona iye, ndipo anavutika. Ndipo posakhalitsa iye adayankhula ndi iwo, Khalani wolimbika mtima: ndinetu, musawope.
  1315. Mrk 6:51 Ndipo iye adakwera kupita kwa iwo kulowa m’chombo; ndipo mphepo idaleka: ndipo iwo anazizwa kwakulu mwa iwo wokha koposa muyeso, ndipo anadabwa.
  1316. Mrk 6:52 Pakuti sadalingalire za [chozizwitsa cha] mikateyo: pakuti mitima yawo idawumitsidwa.
  1317. Mrk 6:53 Ndipo pamene iwo adawoloka, adadza kulowa m’dziko la Genesarete, ndipo anakocheza padoko.
  1318. Mrk 6:54 Ndipo pamene iwo adatuluka m’chombo, nthawi yomweyo adamdziwa iye,
  1319. Mrk 6:55 Ndipo adathamanga dziko lonselo lozungulira, ndipo anayamba kunyamula anthu wodwala pamakama iwo amene adali wodwala, kufikira nawo kumene adamva kuti iye anali.
  1320. Mrk 6:56 Ndipo kumene kulikonse iye adalowa, kulowa m’midzi, kapena mizinda, kapena dziko, iwo adagoneka wodwala m’misewu, ndipo anampempha iye kuti akhoze kukhudza ngakhale ikadakhala mphonje ya chovala chake: ndipo ambiri a iwo amene adamkhudza iye adachiritsidwa.
  1321. Mrk 7:1 Kenaka adasonkhana kwa iye Afarisi, ndi ena a alembi, amene adachokera ku Yerusalemu.
  1322. Mrk 7:2 Ndipo pamene adawona ena a wophunzira ake akudya mkate ndi m’manja mwakuda, kutanthawuza kuti, ndi m’manja mosasamba, iwo adapezerapo chifukwa.
  1323. Mrk 7:3 Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse, pokhapokha asambe m’manja [mwawo] mwakawirikawiri, samadya, posunga mwambo wa akulu.
  1324. Mrk 7:4 Ndipo [pomwe iwo abwera] kuchokera ku msika, pokhapokha asambe, iwo sakudya ayi. Ndipo zinthu zina zambiri ziripo, zimene adazilandira kuti azisunge, monga matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa, ndi za magome.
  1325. Mrk 7:5 Kenaka Afarisi ndi alembi adamfunsa iye, Chifukwa chiyani wophunzira anu sakhala molingana ndi mwambo wa akulu, koma akudya mkate ndi m’manja mosasamba?
  1326. Mrk 7:6 Iye adawayankha ndipo anati kwa iwo, Yesaya adanenera bwino za inu wonyenga, monga kwalembedwa, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo [yawo], koma mtima wawo uli kutali ndi ine.
  1327. Mrk 7:7 Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa [kuti zikhale] ziphunzitso malamulowo a anthu.
  1328. Mrk 7:8 Pakusiya lamulo la Mulungu, inu musunga mwambo wa anthu, monga kutsuka miphika ndi zikho: ndi zinthu zina zotero zambiri zimene inu muchita.
  1329. Mrk 7:9 Ndipo iye adanena kwa iwo, Mwabwino kwambiri inu mukana lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wa inu eni.
  1330. Mrk 7:10 Pakuti Mose adati, Lemekeza atate wako ndi amayi wako; ndipo, iye amene atemberera atate wake kapena amayi wake, iye afe imfayo:
  1331. Mrk 7:11 Koma inu munena, Ngati munthu akati kwa atate wake, kapena amayi wake, [Iyi ndi] Korbani, ndiko kunena kuti, mphatso, mwa imene mwanjira iliyonse iwe ukakhoza kuthandizidwa nayo mwa ine; [iye adzakhala mfulu].
  1332. Mrk 7:12 Ndipo inu simulolanso iye kuti achitire kanthu atate wake kapena amayi wake;
  1333. Mrk 7:13 Kuwapanga mawu a Mulungu opanda kuchitachita kudzera mu mwambo wanu, umene inu mwawupereka: ndi zinthu zotere zambiri inu muzichita.
  1334. Mrk 7:14 ¶Ndipo pamene iye adadziyitanira anthu onse [kwa iye], iye adanena kwa iwo, Mvetserani kwa ine wina aliyense [wa inu], ndipo mumvetsetse;
  1335. Mrk 7:15 Kulibe kanthu kochokera kunja kwa munthu, kamene kakalowa mwa iye kangathe kumdetsa iye: koma zinthu zimene zituluka mwa iye, ndizo zimene zimdetsa munthu.
  1336. Mrk 7:16 Ngati munthu ali nawo makutu akumva, muloleni amve.
  1337. Mrk 7:17 Ndipo m’mene iye adalowa m’nyumba kuchokera kwa anthuwo, wophunzira ake adamfunsa iye zokhudza fanizolo.
  1338. Mrk 7:18 Ndipo iye adanena kwa iwo, Inunso muli wotero wopanda kumvetsetsanso? Kodi inu simuzindikira, kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kulowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
  1339. Mrk 7:19 Chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma kalowa m’mimba, ndipo katuluka kupita m’chimbudzi, kuyeretsa zakudya zonse?
  1340. Mrk 7:20 Ndipo iye adati, Chimene chituluka mwa munthu, chimenecho chidetsa munthu.
  1341. Mrk 7:21 Pakuti kuchokera mkati, kutuluka mu mtima wa anthu, mutuluka maganizo woyipa, zigololo, chiwerewere, kupha,
  1342. Mrk 7:22 Kuba, kusirira, kuchita zoyipa, chinyengo, chilakolako chonyansa, diso loyipa, zamwano, kudzikuza, kupusa:
  1343. Mrk 7:23 Zinthu zonse zoyipa izi zichokera mkati, ndipo zidetsa munthu.
  1344. Mrk 7:24 ¶Ndipo kuchokera kumeneko iye adanyamuka, ndipo anamka m’madera a ku Turo ndi Sidoni, ndipo iye adalowa m’nyumba, ndipo adafuna kuti asadziwe [ichi] munthu aliyense: koma sakadatha kubisika.
  1345. Mrk 7:25 Pakuti mkazi [wina], amene mwana wake wamng’ono wamkazi adali ndi mzimu wonyansa, adamva za iye, ndipo anadza ndi kugwa pa mapazi ake:
  1346. Mrk 7:26 Koma mkaziyo adali Mherene, mtundu wake Msurofonika; ndipo iye adampempha iye kuti iye atulutse chiwanda mwa mwana wake wamkazi.
  1347. Mrk 7:27 Koma Yesu adanena kwa iye, Baleka ana ayambe akhuta: pakuti sikoyenera kutenga mkate wa ana, ndi kuwutayira [iwo] kwa agalu.
  1348. Mrk 7:28 Ndipo iye adayankha ndi kunena kwa iye, Inde, Ambuye: angakhale agalu ali pansi pa gome amadya za nyenyeswa za ana.
  1349. Mrk 7:29 Ndipo iye adati kwa iye, Chifukwa cha kunena kumeneku pita pa njira yako; chiwanda chatuluka mwa mwana wako wamkazi.
  1350. Mrk 7:30 Ndipo pamene adadza kunyumba kwake, adapeza chiwanda chitatuluka kuchoka, ndi mwana wake wamkaziyo atamgoneka pakama.
  1351. Mrk 7:31 ¶Ndipo kenanso, kunyamuka kuchoka ku madera a Turo ndi Sidoni, iye adadza ku nyanja ya Galileya, kupyola pakati pa madera a Dekapolisi.
  1352. Mrk 7:32 Ndipo iwo anadza naye kwa iye munthu wogontha, ndipo anali ndi vuto mu kulankhula kwake; ndipo iwo adampempha iye kuti ayike dzanja lake pa iye.
  1353. Mrk 7:33 Ndipo adamtengera pambali kuchoka pa khamu la anthu, ndipo analonga zala zake m’makutu mwake, ndipo analavula malovu, ndipo anakhudza lirime lake;
  1354. Mrk 7:34 Ndipo pakuyang’ana kumwamba, adawusa moyo, ndipo ananena kwa iye Efufata, ndiko kuti, Tatseguka.
  1355. Mrk 7:35 Ndipo pomwepo makutu ake adatseguka, ndipo chingwe cha lirime lake chidamasulidwa, ndipo iye adayankhula molunjika.
  1356. Mrk 7:36 Ndipo iye adawalamulira iwo kuti asawuze munthu aliyense: koma pamene iye adawalamulira kwambiri, ndi pomwe iwo amalengeza [icho] kwambiri.
  1357. Mrk 7:37 Ndipo anadabwa kwakukulu koposa muyeso, kunena kuti, Iye wachita zinthu zonse bwino: iye apangitsa onse wogontha kuti amve, ndi wosayankhula, kuti ayankhule.
  1358. Mrk 8:1 M’masiku amenewo khamulo pokhala lalikulu kwambiri, ndipo kukhala wopanda kanthu kakuti adye, Yesu anadziyitanira wophunzira ake [kwa iye], ndipo ananena kwa iwo.
  1359. Mrk 8:2 Ine ndiri ndi chifundo pa khamulo, chifukwa iwo tsopano akhala ndi ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakuti adye.
  1360. Mrk 8:3 Ndipo ngati ine ndiwawuza iwo kuti azipita osadya kanthu ku nyumba zawo, iwo adzakomoka panjira: pakuti osiyanasiyana a iwo achokera kutali.
  1361. Mrk 8:4 Ndipo wophunzira ake adamuyankha iye, Kuchokera kuti munthu angathe kukhutitsa [anthu] awa ndi mikate m’chipululu muno?
  1362. Mrk 8:5 Ndipo iye adawafunsa iwo, Kodi inu muli ndi mikate ingati? Ndipo iwo adati, Isanu ndi iwiri.
  1363. Mrk 8:6 Ndipo iye adalamulira anthu kuti akhale pansi pa dothi: ndipo anatenga mikate isanu ndi iwiriyo, ndipo anayamika, ndi kunyema, ndipo anapatsa kwa wophunzira ake kuti apereke kwa [iwo]; ndipo [iwo] adaziyika pamaso pa anthuwo.
  1364. Mrk 8:7 Ndipo adali nato tinsomba tochepa: ndipo iye anadalitsa, ndipo analamulira kuti iwo atiyikenso pamaso pa [iwo].
  1365. Mrk 8:8 Kotero iwo adadya, ndipo anakhuta: ndipo adatola makombo [a chakudya] chonyemedwa madengu asanu ndi awiri.
  1366. Mrk 8:9 Ndipo iwo amene adadya adali ngati zikwi zinayi: ndipo iye adawatumiza apite.
  1367. Mrk 8:10 ¶Ndipo nthawi yomweyo iye adalowa m’chombo ndi wophunzira ake, ndipo adafika ku madera a ku Dalimanuta.
  1368. Mrk 8:11 Ndipo Afarisi adabwera, ndipo anayamba kufunsana ndi iye, kufuna kwa iye chizindikiro chochokera kumwamba, kumuyesa iye.
  1369. Mrk 8:12 Ndipo adawusa moyo kwambiri mu mzimu wake, ndipo ananena, Chifukwa chiyani m’badwo uwu ufunafuna chizindikiro? Ndithudi ndinena kwa inu, Sipadzakhala chizindikiro chopatsidwa ku m’badwo uwu.
  1370. Mrk 8:13 Ndipo iye adawasiya iwo, ndipo analowanso m’chombomo ananyamuka kupita tsidya lina,
  1371. Mrk 8:14 ¶Tsopano [wophunzirawo] adayiwala kutenga mkate, kapena iwo kukhala ndi iwo mkate m’chombo woposa umodzi.
  1372. Mrk 8:15 Ndipo iye adawalamulira iwo, kunena kuti, Samalani, chenjerani ndi chofufumitsa mkate cha Afarisi, ndi chofufumitsa mkate cha Herode.
  1373. Mrk 8:16 Ndipo adafunsana maganizo pakati pawo, kunena kuti, [Ichi ndi] chifukwa chakuti tiribe mkate.
  1374. Mrk 8:17 Ndipo pamene Yesu adadziwa [ichi], iye adanena kwa iwo, Bwanji mukufunsana maganizo inu, chifukwa inu mulibe mkate? Kodi inu simuzindikira, kapena kumvetsetsa? Kodi inu muli nawo mtima wakuti wowumitsidwa kale?
  1375. Mrk 8:18 Pokhala nawo maso, simupenya kodi? Ndi pokhala nawo makutu, simumva kodi? Ndipo inu simukumbukira kodi?
  1376. Mrk 8:19 Pamene ine ndidanyema mikate isanu pakati pa anthu zikwi zisanu, kodi ndi madengu angati odzala ndi makombo amene mudatola? Iwo adanena kwa iye, Khumi ndi awiri.
  1377. Mrk 8:20 Ndipo pamene isanu ndi iwiri pakati pa [anthu] zikwi zinayi, ndi madengu angati wodzala ndi makombo mudatola? Ndipo iwo adanena, Asanu ndi awiri.
  1378. Mrk 8:21 Ndipo iye adanena kwa iwo. Nanga n’chifukwa chiyani inu simumvetsetsa?
  1379. Mrk 8:22 ¶Ndipo iye anadza ku Betsaida; ndipo anadza naye munthu wakhungu kwa iye, ndipo anampempha iye kuti amkhudze iye.
  1380. Mrk 8:23 Ndipo adamgwira munthu wakhunguyo padzanja, ndipo anamtsogolera iye kutuluka naye kunja kwa mzinda; ndipo pamene anamthira malovu pamaso ake, ndipo anayika manja ake pa iye, iye adamfunsa iye ngati anawona kanthu.
  1381. Mrk 8:24 Ndipo adayang’ana kumwamba, ndipo adanena, Ndikuwona anthu ngati mitengo, ikuyenda.
  1382. Mrk 8:25 Patatha izi adayikanso manja [ake] pamaso ake, ndipo adampenyetsa kumwamba: ndipo anachiritsidwa, ndipo anawona munthu aliyense bwinobwino.
  1383. Mrk 8:26 Ndipo iye adamtumiza apite ku nyumba yake, kunena kuti, Usalowe konse mu mzinda, kapena kuwuza [ichi] wina aliyense mumzinda.
  1384. Mrk 8:27 ¶Ndipo Yesu adatuluka, ndi wophunzira ake, kulowa mu mizinda ya Kayisareya wa Filipi: ndipo panjira iye adawafunsa wophunzira ake, kunena kwa iwo, Kodi anthu amanena kuti ine ndine yani?
  1385. Mrk 8:28 Ndipo iwo adayankha, Yohane Mbatizi: koma ena [anena] Eliya; ndipo ena M’modzi wa aneneri.
  1386. Mrk 8:29 Ndipo iye adati kwa iwo, Koma inu munena kuti ndine yani? Ndipo Petro adayankha ndipo ananena naye, Inu ndinu Khristu.
  1387. Mrk 8:30 Ndipo iye adawalamulira iwo kuti asawuze munthu ndi m’modzi yemwe za iye.
  1388. Mrk 8:31 Ndipo iye adayamba kuwaphunzitsa iwo, kuti kuyenera Mwana wamwamuna wa munthu kuti akamve zinthu zowawa zambiri, ndi kukakanidwa ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndipo pakutha masiku atatu kuwukanso kwa akufa.
  1389. Mrk 8:32 Ndipo mawuwo adanena poyera. Ndipo Petro adamtenga iye, nayamba kumdzudzula iye.
  1390. Mrk 8:33 Koma pamene iye adazungulira kutembenuka ndi kupenya pa wophunzira ake, iye adadzudzula Petro, kunena kuti, Pita iwe kumbuyo kwanga, Satana: popeza susamalira zinthu zimene ziri za Mulungu, koma zinthu zimene ziri za anthu.
  1391. Mrk 8:34 ¶Ndipo pamene iye adadziyitanira anthu [kwa iye] pamodzinso ndi wophunzira ake, iye adati kwa iwo, Wina aliyense wofuna kudza pambuyo panga, iye adzikanize yekha, ndipo anyamule mtanda wake, ndipo anditsate ine.
  1392. Mrk 8:35 Pakuti aliyense adzafuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya; koma aliyense adzataya moyo wake chifukwa cha ine ndi chifukwa cha uthenga wabwino, yemweyo adzawupulumutsa.
  1393. Mrk 8:36 Pakuti chidzapindulira munthu nchiyani, ngati iye akalandira dziko lonse lapansi, ndi kutaya moyo wake?
  1394. Mrk 8:37 Kapena munthu adzapereka chiyani chosinthanitsa ndi moyo wake?
  1395. Mrk 8:38 Choncho aliyense amene adzachita manyazi chifukwa cha ine ndi cha mawu anga mu m’badwo uwu wachigololo ndi wochimwa; kwa iyenso Mwana wamwamuna wa munthu adzachitanso manyazi, pamene iye adzadza mu ulemerero wa Atate wake pamodzi ndi angelo ake woyera.
  1396. Mrk 9:1 Ndipo iye adanena kwa iwo, Ndithudi, ine ndinena kwa inu, Kuti alipo ena a iwo amene ayimirira pano, amene sadzalawa imfa, kufikira iwo atawona ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.
  1397. Mrk 9:2 ¶Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi Yesu adatenga [pamodzi ndi iye] Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndipo awatsogolera iwo kukwera pa phiri lalitali padera pa iwo wokha: ndipo adasinthika pamaso pawo.
  1398. Mrk 9:3 Ndipo zovala zake zidakhala zonyezimira, zoyera mbu koposa matalala; monga ngati makina wochapa nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsa izo.
  1399. Mrk 9:4 Ndipo adawoneka kwa iwo Eliya ndi Mose: ndipo anali kuyankhula ndi Yesu.
  1400. Mrk 9:5 Ndipo Petro adayankha ndi kunena kwa Yesu, Ambuye, n’kwabwino kwa ife kukhala pano: ndipo ife timange mahema atatu; m’modzi wa inu, ndi m’modzi wa Mose, ndi m’modzi wa Eliya.
  1401. Mrk 9:6 Pakuti sadadziwa chimene akadanena; popeza adali ndi mantha akulu.
  1402. Mrk 9:7 Ndipo padadza mtambo umene udaphimba iwo: ndipo mawu adatuluka kuchoka mu mtambowo, kunena kuti, Uyu ndi Mwana wanga wamwamuna wokondedwa: mverani iye.
  1403. Mrk 9:8 Ndipo mwadzidzidzi, pamene iwo adayang’ana powazungulira, iwo sadapenyanso munthu wina aliyense, kupatula Yesu yekha, ndi iwo eni.
  1404. Mrk 9:9 Ndipo pakutsika iwo kuchoka paphiri, iye adawalamulira iwo kuti asawuze munthu aliyense zinthu zimene adaziwona, kufikira pamene Mwana wamwamuna wa munthu akadzawuka kwa akufa.
  1405. Mrk 9:10 Ndipo adasunga chonenedwa chimenecho mwa iwo wokha, kufunsana wina ndi mzake kuti kuwuka kwa akufa kungatanthawuzenji?
  1406. Mrk 9:11 ¶Ndipo iwo adamfunsa iye, kunena kuti, Kodi alembi anena bwanji kuti Eliya adzayamba kufika?
  1407. Mrk 9:12 Ndipo iye adayankha ndi kuwawuza iwo, Eliya ndithudi adza moyamba, ndipo abwezeretsa zinthu zonse; ndipo momwe zalembedwera za Mwana wamwamuna wa munthu, kuti ayenera kumva zinthu zowawa zambiri, ndi kuyikidwa kukhala wachabe.
  1408. Mrk 9:13 Koma ine ndinena kwa inu, Kuti Eliya ndithu wadza, ndipo iwo achita kwa iye zirizonse iwo adaziyika pa mndandanda, monga zalembedwa za iye.
  1409. Mrk 9:14 ¶Ndipo pamene iye anadza kwa wophunzira [ake], iye adawona khamu lalikulu lozungulira iwo, ndi alembi alimkufunsana ndi iwo.
  1410. Mrk 9:15 Ndipo nthawi yomweyo anthu onse, pamene iwo adamuwona iye, adadabwa kwambiri, ndipo anathamangira kwa [iye] namulonjera iye.
  1411. Mrk 9:16 Ndipo iye adafunsa alembi, Kodi inu mufunsa iwo chiyani?
  1412. Mrk 9:17 Ndipo m’modzi wa khamulo adayankha ndi kunena kuti, Mbuye, ine ndadza naye kwa inu mwana wanga wamwamuna, amene ali nawo mzimu wosayankhula;
  1413. Mrk 9:18 Ndipo kulikonse kumene umtengera iye, iwo ung’amba iye: ndipo achita thovu, ndipo akukuta mano ake, ndipo ananyololoka: ndipo ine ndidayankhula kwa wophunzira anu kuti awutulutse; ndipo iwo sadakhoza.
  1414. Mrk 9:19 Iye adamuyankha iye, ndipo ananena, Mbadwo wosakhulupirira, kodi ine ndidzakhala nthawi yayitali bwanji ndi inu? Ine ndidzakulekererani inu nthawi yayitali bwanji? Mbweretse iye kwa ine.
  1415. Mrk 9:20 Ndipo anambweretsa iye kwa iye: ndipo pamene anamuwona iye, nthawi yomweyo mzimuwo udam’ng’amba iye; ndipo iye adagwa pansi, ndipo anamvimvinizika kuchita thovu.
  1416. Mrk 9:21 Ndipo iye adafunsa atate wake, Kodi papita nthawi yayitali bwanji kuyambira pomwe ichi chidadza kwa iye? Ndipo iye adati, Ali mwana.
  1417. Mrk 9:22 Ndipo kawirikawiri wakhala ukumamtaya m’moto, ndi m’madzi, kuti umuwononge iye: koma ngati inu mukhoza kuchita kanthu kalikonse, tichitireni ife chifundo, ndi kutithandiza ife.
  1418. Mrk 9:23 Yesu adanena kwa iye, Ngati iwe ungakhulupirire, zinthu zonse [ziri] zotheka kwa iye amene akhulupirira.
  1419. Mrk 9:24 Ndipo nthawi yomweyo atate wa mwanayo adafuwula, ndipo ananena ndi misozi, Ambuye, Ine ndikhulupirira; thandizani inu kusakhulupirira kwanga.
  1420. Mrk 9:25 Pamene Yesu adawona kuti anthu anabwera akuthamanga pamodzi, iye adadzudzula mzimu wonyansa, ndi kunena kwa iye, [Iwe] mzimu wosalankhula ndi wogontha, Ine ndikulamulira iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.
  1421. Mrk 9:26 Ndipo [mzimuwo] udafuwula, num’ng’amba kwambiri, ndipo udatuluka mwa iye: ndipo iye adakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Iye wamwalira.
  1422. Mrk 9:27 Koma Yesu adamgwira ndi dzanja lake, ndipo anamnyamutsa iye; ndipo iye adayimirira.
  1423. Mrk 9:28 Ndipo pamene iye adalowa m’nyumba, wophunzira ake adamfunsa mseri kuti, Kodi ife sitinakhoza bwanji kuwutulutsa?
  1424. Mrk 9:29 Ndipo iye adanena kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi pemphero ndi kusala kudya.
  1425. Mrk 9:30 ¶Ndipo adanyamuka iwo kumeneko, ndipo anadutsa pakati pa Galileya; ndipo iye sadafune kuti munthu aliyense adziwe [ichi].
  1426. Mrk 9:31 Pakuti adaphunzitsa wophunzira ake, ndipo ananena kwa iwo, Mwana wamwamuna wa munthu waperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo iwo adzamupha iye; ndipo ataphedwa iye, iye adzawukanso tsiku lachitatu.
  1427. Mrk 9:32 Koma iwo sadamvetsetsa chonenedwa chimenecho, ndipo anawopa kumfusa iye.
  1428. Mrk 9:33 ¶Ndipo iye anadza ku Kaperenamu: ndipo pamene iye adakhala m’nyumba iye adawafunsa iwo, Kodi ndi chiyani chimene mudali kutsutsana pakati panu panjira?
  1429. Mrk 9:34 Koma iwo adakhala chete: pakuti panjira adatsutsana pakati pawo, kodi wamkulu kwambiri [angakhale] ndani?
  1430. Mrk 9:35 Ndipo iye adakhala pansi, ndipo anayitana khumi ndi awiriwo, ndipo ananena kwa iwo, Ngati munthu aliyense akhumba kukhala woyamba, [yemweyo] adzakhala womaliza kwa onse, ndi mtumiki wa onse.
  1431. Mrk 9:36 Ndipo adatenga kamwana, ndipo anakayika pakati pa iwo: ndipo pamene adakayangata m’manja mwake, iye adanena kwa iwo,
  1432. Mrk 9:37 Wina aliyense amene adzalandira m’modzi wa tiana totere m’dzina langa, andilandira ine: ndipo aliyense amene adzalandira ine, salandira ine, koma iye amene anandituma ine.
  1433. Mrk 9:38 ¶Ndipo Yohane adamuyankha iye, kunena kuti; Ambuye, ife tidawona wina alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndipo satsata ife: ndipo ife tidamletsa, chifukwa iye satsata ife.
  1434. Mrk 9:39 Koma Yesu adati, Musamletsa iye: pakuti palibe munthu adzachita chozizwa m’dzina langa, amene akhoza kulankhula zoyipa zopeputsa ine.
  1435. Mrk 9:40 Pakuti iye amene satsutsana nafe ali kumbali yathu.
  1436. Mrk 9:41 Pakuti aliyense adzakupatsani inu chikho cha madzi kuti mumwe m’dzina langa, chifukwa muli ake a Khristu, Ndithudi ndinena kwa inu, iye sadzataya konse mphotho yake.
  1437. Mrk 9:42 Ndipo aliyense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana [iti] timene tikhulupirira mwa ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wa mphero ukadakolowekedwa m’khosi mwake, ndipo akadaponyedwa m’nyanja.
  1438. Mrk 9:43 Ndipo ngati dzanja lako likuchimwitsa iwe, ulidule: kuli kwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wolumala dzanja, koposa kukhala ndi manja awiri kuti ulowe mu nyanja ya moto, kulowa m’moto umene sudzakhoza kuzimitsidwa.
  1439. Mrk 9:44 Kumene mphutsi yawo simafa, ndipo moto suzimitsidwa.
  1440. Mrk 9:45 Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa iwe, ulidule: kuli kwabwino kwa iwe kulowa wolumala m’moyo, kuposa kukhala ndi mapazi awiri kuti ukaponyedwe mu nyanja ya moto, moto umene sudzazimitsidwa.
  1441. Mrk 9:46 Kumene mphutsi yawo simafa, ndiponso moto suzimitsidwa.
  1442. Mrk 9:47 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa iwe, ulikolowole: kuli kwabwino kwa iwe kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, koposa kukhala ndi maso awiri kuti ukuponyedwe m’moto wa nyanja ya moto.
  1443. Mrk 9:48 Kumeneko mphutsi yawo simafa, ndipo moto suzimitsidwa.
  1444. Mrk 9:49 Pakuti aliyense adzathiridwa ndi mchere ndi moto, ndi nsembe iliyonse idzathiridwa ndi mchere.
  1445. Mrk 9:50 Mchere [ndi] wabwino: koma ngati mchere usukuluka, kodi inu mudzawukoleretsa ndi chiyani? Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mzake.
  1446. Mrk 10:1 Ndipo iye adanyamuka kuchokera kumeneko, ndipo adadza m’madera a Yudeya ku tsidya lotalikirapo la Yordano: ndipo anthu adasonkhananso kwa iye; ndipo, monga adazolowera, adawaphunzitsanso.
  1447. Mrk 10:2 ¶Ndipo Afarisi anadza kwa iye, ndipo adamfunsa iye, kodi nkololedwa mwa lamulo kuti bambo asudzule mkazi [wake]? Kumuyesa iye.
  1448. Mrk 10:3 Ndipo iye adayankha nati kwa iwo, Kodi Mose adakulamulirani chiyani inu?
  1449. Mrk 10:4 Ndipo iwo adati Mose adalola kulembera kalata wachilekaniro, ndi kumsudzula iye.
  1450. Mrk 10:5 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Chifukwa cha kuwuma kwa mtima wanu adakulemberani lamulo ili.
  1451. Mrk 10:6 Koma kuchokera pachiyambi cha chilengedwe Mulungu adawapanga iwo mwamuna ndi mkazi.
  1452. Mrk 10:7 Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake, ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake;
  1453. Mrk 10:8 Ndipo iwo awiriwo adzakhala thupi limodzi: kotero pamenepo si alinso awiri, koma thupi limodzi.
  1454. Mrk 10:9 Chifukwa chake chimene Mulungu adachimanga pamodzi, munthu asalekanitse.
  1455. Mrk 10:10 Ndipo m’nyumbamo wophunzira ake adamfunsanso za chinthu [ichi].
  1456. Mrk 10:11 Ndipo iye adanena kwa iwo, Aliyense amene adzasudzula mkazi wake, ndi kukwatira wina, achita chigololo kulakwira iye.
  1457. Mrk 10:12 Ndipo ngati mkazi adzasudzula mwamuna wake, ndi kukwatiwa ndi wina, achita chigololo.
  1458. Mrk 10:13 ¶Ndipo adadza nawo ana aang’ono kwa iye, kuti iye akhudze iwo: ndipo wophunzira [ake] adawadzudzula [iwo] amene adadza [nawo].
  1459. Mrk 10:14 Koma pamene Yesu adawona [ichi], adakhumudwa kwambiri, ndipo adati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa ine, ndipo musatiletse ito ayi: pakuti kwa wotere uli ufumu wa Mulungu.
  1460. Mrk 10:15 Ndithudi ndinena kwa inu, Aliyense [amene] sadzalandira ufumu wa Mulungu ngati kamwana kakang’ono, iye sadzalowamo ayi.
  1461. Mrk 10:16 Ndipo iye adatiyangata m’manja mwake, anayika manja [ake] pa ito, ndi kutidalitsa ito.
  1462. Mrk 10:17 ¶Ndipo pamene iye adatuluka kulowa m’njiramo, panadza wina akuthamanga, ndipo anagwada kwa iye, ndipo anamfunsa iye, Ambuye wabwino, ine ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
  1463. Mrk 10:18 Ndipo Yesu adati kwa iye, Unditcha ine wabwino bwanji? [Palibe] wina wabwino koma m’modzi, [ameneyo ndiye], Mulungu.
  1464. Mrk 10:19 Iwe udziwa malamulo, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachita umboni wonama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amayi wako.
  1465. Mrk 10:20 Ndipo iye adayankha nati kwa iye, Ambuye, zinthu zonsezi izi ine ndidazisunga kuyambira unyamata wanga.
  1466. Mrk 10:21 Kenaka Yesu pomuyang’ana iye anamkonda iye, ndipo anati kwa iye, Chinthu chimodzi iwe uchisowa: pita pa njira yako, gulitsa chilichonse chimene uli nacho, ndipo uzipereke kwa aumphawi, ndipo iwe udzakhala nacho chuma kumwamba: ndipo udze, tenga mtanda, ndipo unditsate ine.
  1467. Mrk 10:22 Ndipo adali wachisoni ndi chonenedwa chimenecho, ndipo adachoka wokhumudwa: pakuti adali ndi chuma chambiri.
  1468. Mrk 10:23 ¶Ndipo Yesu adayang’anayang’ana mozungulira, ndipo ananena kwa wophunzira ake, Movutika motani iwo amene ali ndi chuma adzalowa ufumu wa Mulungu!
  1469. Mrk 10:24 Ndipo wophunzirawo adazizwa ndi mawu ake. Koma Yesu adayankhanso, ndipo ananena kwa iwo, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu!
  1470. Mrk 10:25 Ndi kwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa kwa munthu wolemera kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.
  1471. Mrk 10:26 Ndipo iwo anadabwa koposa muyeso, kunena pakati pa iwo wokha, Ndipo ndani tsono angathe kupulumuka?
  1472. Mrk 10:27 Yesu poyang’ana pa iwo anati, Ndi anthu [ziri] zosatheka, koma osati ndi Mulungu: pakuti ndi Mulungu zinthu zonse ziri zotheka.
  1473. Mrk 10:28 ¶Kenaka Petro adayamba kunena kwa iye, Onani, ife tasiya zonse, ndipo takutsatani inu.
  1474. Mrk 10:29 Ndipo Yesu adayankha ndi kunena kuti, Ndithudi ndinena kwa inu, Palibe munthu amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate wake, kapena amayi wake, kapena mkazi wake, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi uthenga wabwino,
  1475. Mrk 10:30 Koma iye adzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo m’dziko limene liri nkudza moyo wosatha.
  1476. Mrk 10:31 Koma ambiri [omwe ali] woyamba adzakhala akumapeto; ndi a kumapeto adzakhala woyamba.
  1477. Mrk 10:32 ¶Ndipo iwo adali m’njira kukwera kupita kumka ku Yerusalemu; ndipo Yesu adapita patsogolo pa iwo: ndipo iwo adazizwa; ndipo pamene adalikutsatira, iwo adachita mantha. Ndipo iye adatenganso khumi ndi awiriwo, ndipo anayamba kuwawuza zinthu zimene ziyenera kumchitikira iye.
  1478. Mrk 10:33 [Kunena kuti], Tawonani, ife tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wamwamuna wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi; ndipo iwo adzamuweruza kuti ayenera imfa, ndipo adzampereka iye kwa Amitundu:
  1479. Mrk 10:34 Ndipo iwo adzamnyoza iye, ndi kumthira malovu iye, ndi kumkwapula iye, ndipo adzamupha; ndipo tsiku la chitatu iye adzawukanso.
  1480. Mrk 10:35 ¶Ndipo Yakobo ndi Yohane ana amuna a Zebedayo, anadza kwa iye, kunena kuti, Ambuye, ife tifuna kuti inu mutichitire ife chilichonse chimene tidzakhumba.
  1481. Mrk 10:36 Ndipo iye adati kwa iwo, Kodi inu mufuna kuti ine ndikuchitireni chiyani inu?
  1482. Mrk 10:37 Iwo adati kwa iye, Mutipatse ife tikhoze kukhala, m’modzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina ku dzanja lamanzere, mu ulemerero wanu.
  1483. Mrk 10:38 Koma Yesu adati kwa iwo, Inu simudziwa chimene inu muchipempha: kodi mukhoza kumwera chikho chimene ndimwera? Ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene ine ndidzabatizidwa nawo?
  1484. Mrk 10:39 Ndipo adati kwa iye, Ife tikhoza. Ndipo Yesu adati kwa iwo, Inu mudzamweradi chikho chimene ine ndimwera; ndipo ndi ubatizo umene ndibatizidwa nawo mudzakhala wobatizidwa nawo inu:
  1485. Mrk 10:40 Koma kukhala ku dzanja langa lamanja ndi ku dzanja lamanzere si kuli kwanga kupatsa; [koma kudzapatsidwa kwa iwo] amene kudakonzedweratu kwa iwo.
  1486. Mrk 10:41 Ndipo pamene khumiwo adamva [ichi], adayamba kukhumudwa kwambiri ndi Yakobo ndi Yohane.
  1487. Mrk 10:42 Koma Yesu adawayitanira iwo [kwa iye] nanena nawo, ndipo ananena kwa iwo, Inu mudziwa kuti iwo amene awerengedwa wolamulira pa Amitundu amachita umbuye pa iwo, ndipo akulu awo amachita ulamuliro pa iwo.
  1488. Mrk 10:43 Koma sikudzatero ayi pakati pa inu: koma aliyense amene adzakhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu:
  1489. Mrk 10:44 Ndipo aliyense wa inu amene adzakhala wamkulu kwambiri, adzakhala mtumiki wa onse.
  1490. Mrk 10:45 Pakuti ngakhale Mwana wamwamuna wa munthu sanadza kuti atumikiridwe, koma kuti atumikire, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa ambiri.
  1491. Mrk 10:46 ¶Ndipo iwo adadza ku Yeriko: ndipo pamene iye adalikutuluka mu Yeriko ndi wophunzira ake ndi chiwerengero chachikulu cha anthu, Bartimeyasi wakhungu, mwana wamwamuna wa Timeyasi, adakhala pansi m’mbali mwa msewu kupempha.
  1492. Mrk 10:47 Ndipo pamene iye adamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, iye adayamba kufuwula, ndi kunena, Yesu, [inu] Mwana wamwamuna wa Davide, mundichitire ine chifundo.
  1493. Mrk 10:48 Ndipo ambiri adamlamula iye kuti akhale bata: koma iye makamaka adafuwula koposa, [Inu] Mwana wamwamuna wa Davide, mundichitire ine chifundo.
  1494. Mrk 10:49 Ndipo Yesu adayima chiliri nati, ndipo analamula kuti iye ayitanidwe. Ndipo iwo ayitana munthu wakhunguyo, kunena kwa iye, Khala olimbika mtima; nyamuka; iye akuyitana iwe.
  1495. Mrk 10:50 Ndipo iye, kutaya chovala chake, anadzuka, ndi kudza kwa Yesu.
  1496. Mrk 10:51 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Kodi iwe ufuna kuti ine ndichite chiyani kwa iwe? Munthu wakhunguyo adati kwa iye, Ambuye, kuti ndikhoze kulandira kuwona kwanga.
  1497. Mrk 10:52 Ndipo Yesu adati kwa iye, Pita pa njira yako; chikhulupiriro chako chakupangitsa iwe wamphumphu. Ndipo posakhalitsa adalandira kupenya kwake, ndipo anatsata Yesu pa njira.
  1498. Mrk 11:1 Ndipo pamene iwo adayandikira ku Yerusalemu, ku Betifage ndi Betane, pa phiri la ma Olivi, iye adatuma awiri mwa wophunzira ake.
  1499. Mrk 11:2 Ndipo adati kwa iwo, Pitani pa njira yanu lowani m’mudzi wapandunji ndi inu: ndipo pamene inu mutangolowa m’menemo, inu mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, pamene munthu sadakhalapo kale lonse; m’masuleni iye, ndipo mum’bweretse [iye].
  1500. Mrk 11:3 Ndipo munthu akanena kwa inu, Bwanji inu muchita ichi? Munene inu kuti Ambuye akumfuna iye; ndipo pomwepo iye adzamtumiza iye kuno.
  1501. Mrk 11:4 Ndipo adapita pa njira yawo, ndipo anapeza mwana wa bulu womangidwa panja pafupi ndi khomo pamalo pamene njira ziwiri zidakumana; ndipo iwo anam’masula iye.
  1502. Mrk 11:5 Ndipo ena a iwo amene adayimirira kumeneko adanena kwa iwo, Muchita chiyani inu, kumasula mwana wa bulu?
  1503. Mrk 11:6 Ndipo iwo adanena kwa iwo monga momwe Yesu adawalamulira: ndipo iwo adawalola iwo apite.
  1504. Mrk 11:7 Ndipo iwo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, ndipo anayala zovala zawo pa iye; ndipo iye adakhala pa [mwana wa buluyo].
  1505. Mrk 11:8 Ndipo ambiri adayala zovala zawo panjira: ndipo ena anadula nthambi za mitengo, ndipo anazimwaza [izo] m’njira.
  1506. Mrk 11:9 Ndipo iwo amene adatsogola, ndi iwo amene ankamutsata, adafuwula kunena kuti, Hosana; wodalitsika [ali] iye amene akudza m’dzina la Ambuye:
  1507. Mrk 11:10 Wodalitsika [ukhale] ufumu wa atate wathu Davide, umene ukudza m’dzina la Ambuye: Hosana m’mwambamwamba.
  1508. Mrk 11:11 Ndipo Yesu adalowa mu Yerusalemu, ndipo analowa m’kachisi; ndipo m’mene adayang’ana mozungulira pa zinthu zonse, ndipo tsopano adafika madzulo, iye adatuluka kupita ku Betane pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
  1509. Mrk 11:12 ¶Ndipo tsiku lotsatira, pamene adadza kuchokera ku Betane, iye adamva njala:
  1510. Mrk 11:13 Ndipo pakuwona mtengo wa mkuyu patali uli ndi masamba, iye anadza, kuti mwina iye akhoza kupeza kanthu pamenepo: ndipo m’mene adafikako, iye adapeza palibe kanthu koma masamba; pakuti nthawi ya nkhuyu idali isadakwane.
  1511. Mrk 11:14 Ndipo Yesu adayankha nanena kwa iwo, Palibe munthu adzadyanso zipatso zako kuyambira tsopano mpaka nthawi zonse. Ndipo wophunzira ake adamva [izi].
  1512. Mrk 11:15 ¶Ndipo iwo adadza ku Yerusalemu: ndipo Yesu adalowa m’kachisi, ndipo anayamba kutulutsa iwo amene amagulitsa ndi kugula m’kachisimo, ndipo anagubuduza magome a wosinthana ndalama, ndi mipando ya wogulitsa nkhunda;
  1513. Mrk 11:16 Ndipo sadalole kuti munthu aliyense anyamule chotengera [chilichonse] kupyola pakati pa kachisi.
  1514. Mrk 11:17 Ndipo iye adaphunzitsa, kunena kwa iwo, Sikudalembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa kwa anthu a mitundu yonse nyumba yopemphereramo? Koma inu mwayisandutsa phanga la mbava.
  1515. Mrk 11:18 Ndipo alembi ndi akulu ansembe adamva [ichi], ndipo anafunafuna momwe iwo akhoza kumuwonongera iye: pakuti iwo adamuwopa iye, chifukwa anthu onse adazizwa ndi chiphunzitso chake.
  1516. Mrk 11:19 Ndipo atafika madzulo, iye adatuluka mumzindamo.
  1517. Mrk 11:20 ¶Ndipo m’mawa, m’mene adapyolapo, iwo adawona mtengo wa mkuyuwo utawuma kuyambira ku mizu.
  1518. Mrk 11:21 Ndipo Petro pakukumbukira anena kwa iye, Ambuye, tawonani, mtengo wa mkuyu umene inu mudawutemberera wafota.
  1519. Mrk 11:22 Ndipo Yesu poyankha anena kwa iwo, Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.
  1520. Mrk 11:23 Pakuti ndithudi ndinena kwa inu, Kuti aliyense [amene] adzanena ku phiri ili, Tachotsedwa iwe, ndipo iwe uponyedwe m’nyanja; ndipo wosakayika mumtima mwake, koma nadzakhulupirira kuti zinthu zimene iye azinena zidzachitika; iye adzakhala nazo zimene iye azinena.
  1521. Mrk 11:24 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Zinthu zirizonse inu muzikhumba, pamene inu mupemphera, khulupirirani kuti inu mwalandira [izo], ndipo inu mudzakhala nazo.
  1522. Mrk 11:25 Ndipo pamene inu muyimirira kupemphera, khululukirani, ngati inu muli ndi chifukwa ndi wina: kutinso Atate wanu amene ali kumwamba akhoze kukukhululukirani inu zolakwa zanu.
  1523. Mrk 11:26 Koma ngati inu simukhululukira, Atate wanu amene ali kumwamba sadzakhululukiranso zolakwa zanu.
  1524. Mrk 11:27 ¶Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu: ndipo pamene iye adali kuyenda m’kachisi, adadza kwa iye ansembe akulu, ndi alembi, ndi akulu,
  1525. Mrk 11:28 Ndipo adati kwa iye, Ndi ulamuliro wotani inu muzichita nawo zinthu izi? Ndipo ndani adakupatsani inu ulamuliro uwu wakuchita zinthu izi?
  1526. Mrk 11:29 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Ine ndikufunsaninso inu funso limodzi, ndipo mundiyankhe ine, ndipo ine ndikuwuzani inu ulamuliro umene ine ndichitira nawo zinthu zimenezi.
  1527. Mrk 11:30 Ubatizo wa Yohane, kodi [unali] wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiyankheni ine.
  1528. Mrk 11:31 Ndipo adafunsana maganizo iwo eni wokha, kunena kuti, Ife tikanena kuti, Udachokera kumwamba; iye adzanena, Chifukwa chiyani tsono inu simudamukhulupirira iye?
  1529. Mrk 11:32 Koma ife tikati, Kwa anthu; iwo adawawopa anthuwo: pakuti [anthu] onse adamuyesa Yohane, kuti iye adali mneneri ndithu.
  1530. Mrk 11:33 Ndipo iwo adayankha nati kwa Yesu, Ife sitinganene, Ndipo Yesu kuwayankha anena kwa iwo, Inenso sindikuwuzani inu ulamuliro umene ine ndichitira nawo zinthu izi.
  1531. Mrk 12:1 Ndipo iye adayamba kuyankhula kwa iwo m’mafanizo, Munthu [wina] adalima munda wa mphesa, ndipo anayika linga lozunguzulira [iwo], ndipo anakumba [malo] a moponderamo mphesa, ndipo anamanga nsanja, ndipo anawubwereketsa kwa wolima munda, ndipo anapita ku dziko lakutali.
  1532. Mrk 12:2 Ndipo pa nyengo yake iye adatuma wantchito kwa wolima mundawo, kuti iye akakhoze kulandirako kwa wolima mundawo zipatso za munda wa mphesa.
  1533. Mrk 12:3 Ndipo iwo adamugwira [iye], ndipo anam’menya iye, ndipo anampirikitsa [iye] wopanda kanthu.
  1534. Mrk 12:4 Ndipo adatumanso kwa iwo wantchito wina; ndipo kwa iye iwo adamponya miyala, ndipo anamuvulaza [iye] m’mutu, ndipo anampirikitsa [iye] mochititsa manyazi.
  1535. Mrk 12:5 Ndipo iye adatumanso wina; ndipo iye iwo adamupha, ndi ena ambiri; kumenya ena, ndi kupha ena.
  1536. Mrk 12:6 Choncho pokhala naye mwana wamwamuna m’modzi, wokondedwa bwino wake, iye adamtumizanso iye potsiriza kwa iwo, kunena kuti, Iwo adzalemekeza mwana wanga wamwamuna.
  1537. Mrk 12:7 Koma wolima mundawo adanena pakati pa iwo wokha, Ameneyu ndiye wolandira cholowa; bwerani, tiyeni ife timuphe iye, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.
  1538. Mrk 12:8 Ndipo iwo adamtenga iye, ndipo anamupha [iye], ndipo anamtaya [iye] kunja kwa munda wa mphesa.
  1539. Mrk 12:9 Kodi choncho mbuye wa munda wa mphesa adzachita chiyani? Iye adzadza ndi kuwononga wolima mundawo, ndipo adzapereka munda wa mphesawo kwa ena.
  1540. Mrk 12:10 Kodi inu simudawerenga lembo ili, Mwala umene womanga nyumba adawukana wasanduka mutu wa pa ngodya:
  1541. Mrk 12:11 Uku kudali kuchita kwa Ambuye, ndipo kuli kodabwitsa m’maso athu?
  1542. Mrk 12:12 Ndipo iwo adafuna kuti amgwire iye; koma adawopa anthu: pakuti adadziwa kuti iye adakamba fanizolo pakutsutsa iwo: ndipo iwo adamsiya iye, ndipo anapita pa njira yawo.
  1543. Mrk 12:13 ¶Ndipo iwo adatuma kwa iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole iye m’mawu [ake].
  1544. Mrk 12:14 Ndipo pamene iwo adadza, iwo adanena kwa iye, Ambuye, ife tidziwa kuti inu muli wowona, ndipo simusamala za munthu: pakuti inu simuganizira za [mawonokedwe a] umunthu wa anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu m’chowona: Kodi nkololeka mwa lamulo kupereka msonkho kwa Kayisara, kapena iyayi?
  1545. Mrk 12:15 Kodi ife tipereke, kapena ife tisapereke? Koma iye, podziwa chinyengo chawo, adati kwa iwo, Chifukwa chiyani inu mundiyesa ine? Ndibweretsereni ine khobiri latheka, kuti ine ndiliwone [ilo].
  1546. Mrk 12:16 Ndipo adambweretsera [ilo]. Ndipo iye adati kwa iwo, Kodi chithunzi ichi ndi chilembo chake ziri za yani? Ndipo adati kwa iye, za Kayisara.
  1547. Mrk 12:17 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iwo, Perekani kwa Kayisara zinthu zimene ziri za Kayisara, ndi kwa Mulungu zinthu zimene ziri za Mulungu. Ndipo iwo adazizwa pa iye.
  1548. Mrk 12:18 ¶Kenaka anadza kwa iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; ndipo adamfunsa iye kunena kuti,
  1549. Mrk 12:19 Ambuye, Mose adalembera kwa ife kuti, Ngati afa mbale wake wa munthu, ndipo asiya mkazi [wake m’mbuyo mwake], ndipo wosasiyapo mwana, kuti mbale wake atenge mkazi wake, ndi kuwukitsira mbale wake mbewu.
  1550. Mrk 12:20 Tsopano adalipo abale asanu ndi awiri: woyamba adatenga mkazi, ndipo pakufa sadasiye mbewu.
  1551. Mrk 12:21 Ndipo wachiwiri adamtenga iye, ndipo anafa, sadasiyenso iye mbewu iliyonse ayi: ndipo wachitatunso chimodzimodzi.
  1552. Mrk 12:22 Ndipo wachisanu ndi chiwiriyo adakhala naye, ndipo sadasiye mbewu: pomaliza pa zonse mkaziyo adamwaliranso.
  1553. Mrk 12:23 Choncho m’chiwukitso, pomwe iwo adzawuka, kodi adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adakhala naye monga mkazi wawo.
  1554. Mrk 12:24 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iwo, Kodi inu choncho simulakwitsa, chifukwa inu simudziwa malembo, kapena mphamvu ya Mulungu?
  1555. Mrk 12:25 Pakuti pamene iwo adzawuka kwa akufa, iwo sakwatira, kapena saperekedwa mu ukwati; koma akhala ngati angelo amene ali kumwamba.
  1556. Mrk 12:26 Koma pa zokhudza akufa, kuti iwo amawuka: kodi inu simudawerenga m’buku la Mose, momwe m’thengo Mulungu adalankhula kwa iye, kunena kuti, Ine [ndine] Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?
  1557. Mrk 12:27 Iye sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: choncho inu mulakwitsa kwakulu.
  1558. Mrk 12:28 ¶Ndipo m’modzi wa alembi anadza, ndipo atawamva iwo alikufunsana maganizo pamodzi, ndipo podziwa kuti iye adawayankha bwino, adamfunsa iye, Kodi ndi lamulo liti loyamba la onse?
  1559. Mrk 12:29 Ndipo Yesu adamuyankha iye, Lamulo loyamba la onse [ndi ili], Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu ndi Ambuye m’modzi:
  1560. Mrk 12:30 Ndipo iwe uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi malingaliro ako onse, ndi mphamvu zako zonse; ili [ndi] lamulo loyamba.
  1561. Mrk 12:31 Ndipo lachiwiri [ndi] lofanana, ili [litchedwa], Uzikonda woyandikana naye monga udzikonda iwe mwini. Palibe lamulo lina loposa awa.
  1562. Mrk 12:32 Ndipo mlembiyo adati kwa iye, Chabwino, Ambuye, inu mwanena zowona: pakuti pali Mulungu m’modzi; ndipo palibe wina koma iye:
  1563. Mrk 12:33 Ndipo kumkonda iye ndi mtima wonse, ndi kumvetsetsa konse, ndi moyo wonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda woyandikana naye monga adzikonda iye mwini, ziri zoposa zopereka za nsembe zopsereza zamphumphu zonse ndi nsembe.
  1564. Mrk 12:34 Ndipo Yesu pakuwona kuti adayankha mwa nzeru, iye adati kwa iye, Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu patatha pamenepo amene adalimba mtima kumfunsa [funso lina lirilonse].
  1565. Mrk 12:35 ¶Ndipo Yesu adayankha nati, pamene adali kuphunzitsa m’kachisi, Bwanji alembi anena kuti Khristu ndiye mwana wamwamuna wa Davide?
  1566. Mrk 12:36 Pakuti Davide mwini yekha adati mwa Mzimu Woyera, AMBUYE adati kwa Ambuye wanga, Khala iwe ku dzanja langa lamanja, kufikira ine nditapanga adani ako choponderapo cha mapazi ako.
  1567. Mrk 12:37 Kotero Davide mwini yekha amtchula iye Ambuye; ndipo kuchokera kuti [tsono] ali mwana wake wamwamuna? Ndipo anthu a wamba adamumva iye mokondwera.
  1568. Mrk 12:38 ¶Ndipo iye adati kwa iwo m’chiphunzitso chake, Chenjerani ndi alembi, amene akonda kuvala mwinjiro ndi [kukonda] kulandira ulemu m’malo a misika,
  1569. Mrk 12:39 Ndi mipando ya ulemu m’masunagoge, ndi malo a pamwamba kwambiri pa maphwando:
  1570. Mrk 12:40 Amene alusira nyumba za akazi amasiye, ndipo chifukwa cha chinyengo apemphera mapemphero atali, awa adzalandira kulanga koposa.
  1571. Mrk 12:41 ¶Ndipo Yesu adakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, ndipo anapenya momwe anthu adali kuponyera ndalama mosungiramo: ndipo ambiri amene adali wolemera adaponyamo zambiri.
  1572. Mrk 12:42 Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye adaponyamo tindalama tiwiri tating’ono, tokwanira ndalama imodzi.
  1573. Mrk 12:43 Ndipo iye adayitanira [kwa iye] wophunzira ake, ndipo anati kwa iwo, Ndithudi ndinena kwa inu, Kuti mkazi wamasiye waumphawi waponyamo zambiri, koposa onse iwo amene aponya mosungiramo ndalama:
  1574. Mrk 12:44 Pakuti onse [iwo] adaponyamo mwa zochuluka zawo; koma iye mwa kusowa kwake adaponya zonse adali nazo, [inde] ngakhale za moyo wake wonse.
  1575. Mrk 13:1 Ndipo pamene iye adalikutuluka m’kachisi, m’modzi wa wophunzira ake adanena kwa iye, Ambuye, onani miyala ya mtundu wotere ndi nyumba [ziri pano].
  1576. Mrk 13:2 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iye, Kodi wawona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa pansi.
  1577. Mrk 13:3 Ndipo pamene iye adakhala pa phiri la ma Olivi popenyana ndi kachisi, Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane ndi Anduru adamfunsa iye mseri,
  1578. Mrk 13:4 Tiwuzeni ife, kodi zinthu izi zidzachitika liti? Ndipo [chidzakhala] chotani chizindikiro chake pamene zinthu izi zonse zidzakwaniritsidwa?
  1579. Mrk 13:5 Ndipo Yesu powayankha iwo adayamba kunena nawo, Chenjerani kuti mwina [munthu] aliyense asakunyengeni inu:
  1580. Mrk 13:6 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, kunena kuti, Ine ndine [Khristu]; ndipo adzanyenga ambiri.
  1581. Mrk 13:7 Ndipo pamene inu mudzamva za nkhondo ndi mphekesera za nkhondo, inu musavutike: pakuti [zinthu zoterezi] ziyenera kukhalapo; koma chimaliziro [chidzakhala] chisadafike.
  1582. Mrk 13:8 Pakuti mtundu udzawukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzawukira ufumu: ndiponso padzakhala zivomerezi m’malo osiyanasiyana, ndiponso padzakhala njala ndi mavuto: izi [ndi] zoyambira za zisoni.
  1583. Mrk 13:9 ¶Koma inu chenjerani kwa inu nokha: pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo m’masunagoge inu mudzakwapulidwa: ndipo inu mudzatengeredwa pamaso pa olamulira ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala umboni wowatsutsa iwo.
  1584. Mrk 13:10 Ndipo uthenga wabwino uyenera uyambe walalikidwa pakati pa mitundu yonse.
  1585. Mrk 13:11 Koma pamene iwo adzapita [nanu], ndi kukuperekani inu, musachiganiziretu chimene inu mudzayankhula, kapena kulingaliriratu: koma chilichonse chimene chidzapatsidwa kwa inu mu ora lomwero, chimenecho inu mudzayankhule inu: pakuti simudzakhala inu amene muyankhula, koma Mzimu Woyera.
  1586. Mrk 13:12 Tsopano m’bale adzapereka m’bale wake kuti aphedwe, ndi atate mwana wake wamwamuna, ndi ana adzawukira akuwabala [awo], ndipo adzawapangitsa kuti aphedwe.
  1587. Mrk 13:13 Ndipo inu mudzadedwa ndi anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wopirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.
  1588. Mrk 13:14 ¶Koma pamene inu mudzawona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidayankhulidwa ndi Danieli mneneri, chitayimirira pomwe sichiyenera, (iye amene awerenga amvetsetse,) kenaka muwalole iwo ali mu Yudeya athawire ku mapiri:
  1589. Mrk 13:15 Ndipo iye amene ali pamwamba pa denga asatsike kulowa m’nyumba, kapena asalowe m’menemo, kuti atenge kanthu kalikonse kutulutsa m’nyumba mwake,
  1590. Mrk 13:16 Ndi iye amene ali kumunda asabwerere kuti adzatenge malaya ake.
  1591. Mrk 13:17 Koma tsoka kwa iwo amene ali ndi mwana, ndi kwa iwo amene adzayamwitsa m’masiku amenewo!
  1592. Mrk 13:18 Ndipo pempherani inu kuti kuthawa kwanu kusadzakhale m’nyengo yozizira.
  1593. Mrk 13:19 Pakuti [mu] masiku amenewo padzakhala mazunzo, wonga asadakhalepo kuchokera pa chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu adachilenga kufikira nthawi yino, kapena sichidzakhalanso.
  1594. Mrk 13:20 Ndipo pokhapokha kuti Ambuye adafupikitsa masiku amenewo, palibe amene akadapulumuka: koma chifukwa cha wosankhidwa, amene iye wawasankha, iye adafupikitsa masikuwo.
  1595. Mrk 13:21 Ndipo pamenepo ngati munthu wina aliyense adzanena kwa inu, Onani, Khristu [ali] pano; kapena, Onani, [ali] uko; musakhulupirire [iye] ayi.
  1596. Mrk 13:22 Pakuti Akhristu wonyenga ndi aneneri wonyenga adzawuka, ndipo adzawonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa, kuti akope, ngati [kukadakhala] kotheka, ngakhale wosankhidwa omwe.
  1597. Mrk 13:23 Koma chenjereni inu: tawonani, ine ndakuwuziranitu zinthu zonse [zisadafike].
  1598. Mrk 13:24 ¶Koma m’masiku amenewo, chitatha chisawutso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzapereka kuwunika kwake,
  1599. Mrk 13:25 Ndipo nyenyezi za kumwamba zidzagwa ndipo mphamvu zimene ziri kumwamba zidzagwedezeka.
  1600. Mrk 13:26 Ndipo pamenepo adzawona Mwana wamwamuna wa munthu alinkudza m’mitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero.
  1601. Mrk 13:27 Ndipo pamenepo adzatuma angelo ake, ndipo adzasonkhanitsa wosankhidwa ake wochokera ku mphepo zinayi, kuchokera ku malakezero a dziko lapansi kufikira ku malakezero a thambo.
  1602. Mrk 13:28 Tsopano phunzirani fanizo la mtengo wa mkuyu; Pamene pafika kuti nthambi yake ikali yanthete, ndipo uphuka masamba, inu muzindikira kuti chayandikira chirimwe:
  1603. Mrk 13:29 Chomwecho inunso motero momwemo, pamene inu mudzawona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti ili pafupi, [inde] ngakhale pamakomo.
  1604. Mrk 13:30 Ndithudi ndinena kwa inu, kuti m’badwo uwu sudzapita, kufikira zinthu izi zonse zitachitika.
  1605. Mrk 13:31 Thambo ndi dziko lapansi zidzapita: koma mawu anga sadzapita.
  1606. Mrk 13:32 ¶Koma za tsiku ilo ndi ora limenelo sadziwa munthu aliyense, ayi, ngakhale angelo amene ali kumwamba, kapena Mwana wamwamuna, koma Atate.
  1607. Mrk 13:33 Chenjerani inu, dikirani ndipo pempherani: pakuti inu simudziwa pamene nthawi iyi ili.
  1608. Mrk 13:34 [Pakuti Mwana wamwamuna wa munthu ali] monga munthu woyenda ulendo wawutali, amene [adanyamuka] kuchoka kunyumba kwake, ndipo adapatsa ulamuliro antchito ake, ndi kwa munthu aliyense ntchito yake, ndipo adalamulira wapakhomo kuti adikire.
  1609. Mrk 13:35 Choncho dikirani: pakuti inu simudziwa nthawi imene mbuye wa nyumba abwera, madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena pakulira tambala, kapena m’mamawa:
  1610. Mrk 13:36 Kuti mwina pobwera mwadzidzidzi iye apeza inu mukugona.
  1611. Mrk 13:37 Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.
  1612. Mrk 14:1 Ndipo patapita masiku awiri kudali [phwando la] paskha, ndi la mikate yopanda chofufumitsa: ndipo ansembe akulu ndi alembi adafunafuna momwe angamgwirire iye momchenjerera, ndi kumupha [iye].
  1613. Mrk 14:2 Koma iwo adati, Osati pa [tsiku] la phwando ayi, kuti mwina pangakhale chipolowe cha anthu.
  1614. Mrk 14:3 ¶Ndipo pakukhala iye ku Betane m’nyumba ya Simoni wakhate, pamene adakhala kuseyama pa chakudya, panadza mkazi ali nalo botolo la alabasitara la mafuta wonunkhira bwino a nardo a mtengo wapatali; ndipo anaswa botololo, ndipo anawatsanulira [awo] pamutu pake.
  1615. Mrk 14:4 Ndipo adalipo ena amene adali ndi mkwiyo mkati pa iwo wokha, ndipo ananena, Kodi kutaya uku kwa mafutawo kwachitika chifukwa chiyani?
  1616. Mrk 14:5 Pakuti akadakhoza kugulitsidwa pa mtengo wa ndalama zoposa mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa aumphawi. Ndipo adang’ung’udza motsutsa iye.
  1617. Mrk 14:6 Ndipo Yesu adati, Mulekeni iye; inu mumvutiranji iye? Iye wachita ntchito yabwino pa ine.
  1618. Mrk 14:7 Pakuti muli nawo aumphawi pamodzi ndi inu nthawi zonse, ndipo pa nthawi ina iliyonse inu mufuna mukhoza kuwachitira zabwino: koma ine simuli nane inu nthawi zonse.
  1619. Mrk 14:8 Iye wachita chimene akadakhoza: iye wadza kudzandidzozeratu thupi langa ku kuyikidwa m’manda.
  1620. Mrk 14:9 Ndithudi ndinena kwa inu, Paliponse pamene uthenga wabwino uwu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, [ichinso] chimene iye wachita chidzanenedwa chikhale chikumbukiro cha iye.
  1621. Mrk 14:10 ¶Ndipo Yudasi Isikariyote, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, adapita kwa ansembe akulu, kuti akampereke iye kwa iwo.
  1622. Mrk 14:11 Ndipo pamene iwo adamva [ichi], iwo adakondwera, ndipo analonjeza kuti adzampatsa iye ndalama. Ndipo iye adafunafuna momwe angamperekere iye bwino.
  1623. Mrk 14:12 ¶Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chofufumitsa, pamene iwo adapha paskha, wophunzira ake adanena kwa iye, Ndi kuti kumene mufuna ife tipite ndi kukonza kuti inu mukhoze kukadyako paskha?
  1624. Mrk 14:13 Ndipo iye adatuma awiri a wophunzira ake, ndipo ananena kwa iwo, Mukani inu kulowa mu mzinda, ndipo adzakomana nanu bambo wosenza mtsuko wa madzi: tsatani iye.
  1625. Mrk 14:14 Ndipo kulikonse kumene adzalowako iye, munene inu kwa mwini nyumba wabwino, Ambuye anena, Chili kuti chipinda cha alendo, m’mene ndidzadyera paskha ndi wophunzira anga?
  1626. Mrk 14:15 Ndipo iye adzakusonyezani inu chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo [ndi] chokonzedwa: m’menemo mutikonzere ife.
  1627. Mrk 14:16 Ndipo wophunzira adatuluka kupita, ndipo anadza mu mzinda, ndipo anapeza monga iye adanena kwa iwo: ndipo iwo adakonza paskha.
  1628. Mrk 14:17 Ndipo madzulo iye adabwera ndi khumi ndi awiriwo.
  1629. Mrk 14:18 Ndipo pamene iwo adakhala pansi ndi kudya, Yesu adati, Ndithudi ndinena kwa inu, M’modzi wa inu amene akudya ndi ine adzandipereka ine.
  1630. Mrk 14:19 Ndipo iwo adayamba kukhala ndi chisoni, ndi kunena kwa iye m’modzi m’modzi, [Kodi] ndine? Ndipo wina, [ananena, Kodi] ndine?
  1631. Mrk 14:20 Ndipo iye anayankha nati kwa iwo, [Ndi] m’modzi wa khumi ndi awiriwo, amene wosunsa pamodzi ndi ine m’mbale.
  1632. Mrk 14:21 Mwana wamwamuna wa munthu ndithu amukadi; monga kwalembedwa za iye: koma tsoka kwa munthuyo amene Mwana wamwamuna wa munthu aperekedwa [naye]! Kukadakhala kwabwino kwa munthu ameneyo akadakhala kuti sadabadwe.
  1633. Mrk 14:22 ¶Ndipo pamene analikudya, Yesu adatenga mkate, ndipo anadalitsa, ndipo anawunyema [iwo], ndipo anapereka kwa iwo, ndipo anati, Tengani, idyani: ili ndi thupi langa.
  1634. Mrk 14:23 Ndipo adatenga chikho, ndipo pamene iye adapereka mayamiko, iye adapereka [icho] kwa iwo, ndipo iwo onse adamweramo.
  1635. Mrk 14:24 Ndipo iye adati kwa iwo, Uwu ndi mwazi wanga wa pangano latsopano, umene wakhetsedwa chifukwa cha ambiri.
  1636. Mrk 14:25 Ndithudi ndinena kwa inu, ine sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo limene ndidzamwa icho chatsopano mu ufumu wa Mulungu.
  1637. Mrk 14:26 ¶Ndipo atayimba nyimbo, iwo adatuluka napita kulowa m’phiri la ma Olivi.
  1638. Mrk 14:27 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Inu nonsenu mudzakhumudwa chifukwa cha ine usiku uno: pakuti kwalembedwa, Ine ndidzakantha mbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.
  1639. Mrk 14:28 Koma ndikadzawuka [kwa akufa] ine, ndidzatsogolera inu ku Galileya.
  1640. Mrk 14:29 Koma Petro adati kwa iye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine [sindidzatero] ayi.
  1641. Mrk 14:30 Ndipo Yesu adati kwa iye, Ndithudi ine ndinena kwa iwe, Kuti lero, ngakhale usiku uwu, tambala asadalire kawiri, iwe udzandikana ine katatu.
  1642. Mrk 14:31 Koma iye adayankhula molimbitsa mawu kuti, Ngati ine ndidzayenera kufa ndi inu, ine sindidzakana inu mwina mulimonse. Chimodzimodzinso adanena iwo onsewo.
  1643. Mrk 14:32 Ndipo iwo anadza ku malo amene adatchedwa Getsemane: ndipo iye adanena kwa wophunzira ake, Khalani inu pano, pamene ine ndipemphera.
  1644. Mrk 14:33 Ndipo adatenga pamodzi ndi iye Petro ndi Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kudabwa kwambiri, ndi kulemedwa ndithu.
  1645. Mrk 14:34 Ndipo adati kwa iwo, Moyo wanga uli wachisoni chambiri kufikira imfa: bakhalani inu pano, ndipo mudikire.
  1646. Mrk 14:35 Ndipo iye anapita m’tsogolo pang’ono, ndipo anagwa pansi, ndipo anapemphera kuti, ngati kuli kotheka oralo likhoze kumpitirira kuchoka kwa iye.
  1647. Mrk 14:36 Ndipo iye adati, Abba, Atate, zinthu zonse [ziri] zotheka kwa inu; chotsani chikho ichi kwa ine: komatu si chimene ine ndifuna, koma chimene inu mufuna.
  1648. Mrk 14:37 Ndipo iye anadza, ndipo anawapeza iwo akugona, ndipo ananena kwa Petro, Simoni, ugona kodi? Sukadatha iwe kodi kudikira ora limodzi?
  1649. Mrk 14:38 Khalani maso inu ndi kupemphera, kuti mwina mungalowe m’kuyesedwa. Mzimutu zowonadi ali wokonzeka, koma thupi [liri] lofowoka.
  1650. Mrk 14:39 Ndipo iye adapitanso, ndipo anapemphera, ndipo analankhula mawu womwewo.
  1651. Mrk 14:40 Ndipo pamene anabwerera, iye adawapeza akugonanso, (pakuti maso awo adali wolemera,) ndipo sanadziwe iwo chomwe akadamuyankha iye.
  1652. Mrk 14:41 Ndipo iye anadza kachitatu, ndipo ananena kwa iwo, Gonani tsopano, ndipo mupumule: chakwanira; ora lija lafika; tawonani Mwana wamwamuna wa munthu akuperekedwa m’manja a wochimwa.
  1653. Mrk 14:42 Ukani, tiyeni ife tizipita; onani iye amene andipereka ine ali pafupi.
  1654. Mrk 14:43 ¶Ndipo posakhalitsa, pamene iye ali chiyankhulire, anadza Yudasi, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu ali ndi malupanga ndi zibonga, wochokera kwa ansembe akulu ndi alembi ndi akulu.
  1655. Mrk 14:44 Ndipo iye amene adampereka iye adawapatsa iwo chizindikiro, kunena kuti, Aliyense amene ine ndidzampsopsona, yemweyo ndi iye; mtengeni iye, ndipo munke naye [iye] mosamala.
  1656. Mrk 14:45 Ndipo pamene iye atangofika, pomwepo iye anapita kwa iye, ndipo ananena Ambuye, ambuye; ndipo anampsopsona iye.
  1657. Mrk 14:46 ¶Ndipo iwo adamgwira iye, ndi kumtenga iye.
  1658. Mrk 14:47 Ndipo m’modzi wa iwo amene adayimirira pamenepo adasolola lupanga, ndipo anakantha wantchito wa mkulu wa ansembe, ndipo anamdula khutu lake.
  1659. Mrk 14:48 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka, monga molimbana ndi mbava, ndi malupanga ndi zibonga kudzatenga ine?
  1660. Mrk 14:49 Ine ndidali tsiku lirilonse ndi inu m’kachisi kuphunzitsa, ndipo inu simudanditenge ine ayi, koma malembo ayenera kukwaniritsidwa.
  1661. Mrk 14:50 Ndipo iwo onse adamsiya iye, ndipo anathawa.
  1662. Mrk 14:51 Ndipo adamtsata iye m’nyamata wina, adafundira [pathupi] bafuta yekha kubisa umaliseche [wake]; ndipo anyamatawo adamugwira iye:
  1663. Mrk 14:52 Ndipo iye adasiya nsalu ya bafutayo, ndipo anathawa kuchoka kwa iwo wamaliseche.
  1664. Mrk 14:53 ¶Ndipo adamka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe: ndipo pamodzi ndi iye adasonkhana ansembe akulu onse ndi akulu a anthu ndi alembi.
  1665. Mrk 14:54 Ndipo Petro adamtsata iye chapatali, ngakhale kufikira kulowa m’bwalo la mkulu wa ansembe: ndipo adakhala pansi pamodzi ndi antchito, ndipo anadzifunditsa yekha pakuwotha moto.
  1666. Mrk 14:55 Ndipo ansembe akulu ndi akulu a milandu onse adafunafuna umboni womtsutsa nawo Yesu kuti amuphe iye; ndipo sadawupeze uliwonse.
  1667. Mrk 14:56 Pakuti ambiri adamchitira umboni wonama, koma umboni wawo sudagwirizane.
  1668. Mrk 14:57 Ndipo adanyamukapo ena, ndipo anamchitira umboni wonama, kunena kuti,
  1669. Mrk 14:58 Ife tidamva iye alikunena, Ine ndidzawononga kachisi uyu amene ali wopangidwa ndi manja, ndi mu masiku atatu ndidzamanga wina wosamangidwa ndi manja.
  1670. Mrk 14:59 Koma ngakhale momwemo umboni wawo sudagwirizane.
  1671. Mrk 14:60 Ndipo mkulu wa ansembe adayimirira pakati, ndipo anamfunsa Yesu, kunena kuti, Suyankha kanthu iwe kodi? Nchiyani [ichi chimene] awa alikuchitira umboni mokutsutsa iwe?
  1672. Mrk 14:61 Ndipo iye adakhala chete, ndipo sadayankhe kanthu. Adamfunsanso iye mkulu wa ansembe, ndi kunena kwa iye, Kodi iwe ndiwe Khristu, Mwana wamwamuna wa Wodala?
  1673. Mrk 14:62 Ndipo Yesu adati, Ine ndine; ndipo mudzawona Mwana wamwamuna wa munthu atakhala pa dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza m’mitambo ya kumwamba.
  1674. Mrk 14:63 Ndipo mkulu wa ansembe adang’amba malaya ake, ndipo ananena, Tifuniranjinso ife mboni zina?
  1675. Mrk 14:64 Mwamva zonyoza [Mulunguzo]: inu muganiza bwanji? Ndipo onse adamuweruza iye kuti ali ndi mlandu woyenera imfa.
  1676. Mrk 14:65 Ndipo ena adayamba kumthira malovu iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kum’bwanyula iye, ndi kunena kwa iye, Nenera: ndipo atchitowo adampanda iye ndi zikhato za manja awo.
  1677. Mrk 14:66 ¶Ndipo pamene Petro adali pansi m’bwalomo, anadza pamenepo m’modzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe:
  1678. Mrk 14:67 Ndipo pamene adamuwona Petro alikuwotha moto, adayang’ana pa iye, ndipo adanena, Ndi iwenso udali naye Yesu wa ku Nazarete.
  1679. Mrk 14:68 Koma iye adakana, kunena kuti, Ine sindimudziwa, kapena kumvetsetsa chimene iwe uchinena. Ndipo iye adatuluka kupita kuchipata; ndipo tambala adalira.
  1680. Mrk 14:69 Ndipo mdzakazi adamuwonanso iye, ndipo anayamba kunena ndi iwo amene adalikuyimirirapo, Uyu ndi [m’modzi] wa iwo.
  1681. Mrk 14:70 Ndipo iye adakananso. Ndipo patapita nthawi yochepa, iwo amene adalikuyimirirapo adanenanso kwa Petro, Zowonadi uli [m’modzi] wa iwo: pakuti iwe uli Mgalileya, ndipo mayankhulidwe ako agwirizana [ndi iwo].
  1682. Mrk 14:71 Koma iye adayamba kutemberera ndi kulumbira, [kunena kuti], Ine sindidziwa za munthu uyu amene inu muyankhula za iye.
  1683. Mrk 14:72 Ndipo tambala adalira kachiwiri. Ndipo Petro adakumbukira mawu omwe Yesu adanena kwa iye, Asanalire tambala kawiri, iwe udzandikana ine katatu. Ndipo pamene iye adaganizira pa ichi, adalira iye.
  1684. Mrk 15:1 Ndipo pamenepo m’mawa ansembe akulu adakambirana ndi akulu a anthu ndi alembi ndi akulu a milandu onse, ndipo anamanga Yesu, ndipo anamtenga [iye], ndipo anampereka [iye] kwa Pilato.
  1685. Mrk 15:2 Ndipo Pilato adamfunsa iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo iye poyankha adati kwa iye, Inu mwanena [ichi].
  1686. Mrk 15:3 Ndipo ansembe akulu adamnenera iye zinthu zambiri: koma iye sadayankhe kanthu.
  1687. Mrk 15:4 Ndipo Pilato adamfunsanso iye, kunena kuti, Suyankha kanthu iwe kodi? Tawona zinthu zambiri zotere iwo akuchitira umboni mokutsutsa iwe.
  1688. Mrk 15:5 Koma Yesu osayankhabe kanthu; kotero kuti Pilato adazizwa.
  1689. Mrk 15:6 Tsopano paphwando [ilo] iye ankamasulira kwa iwo wa m’ndende m’modzi, aliyense amene iwo adamfuna.
  1690. Mrk 15:7 Ndipo adalipo [wina] dzina lake Barabasi, [amene adagona] womangidwa pamodzi ndi ena amene adachita mpanduko, amene adapha munthu mumpandukowo.
  1691. Mrk 15:8 Ndipo khamu pofuwula lidayamba kupempha [iye kuti achite] monga adali kuwachitira iwo.
  1692. Mrk 15:9 Koma Pilato adawayankha iwo, kunena kuti, Kodi inu mufuna ine ndimasulire kwa inu Mfumu ya Ayuda?
  1693. Mrk 15:10 Pakuti iye adadziwa kuti ansembe akulu adampereka iye mwa kaduka.
  1694. Mrk 15:11 Koma ansembe akulu adasonkhezera anthu, kuti iye bola awamasulire Barabasi kwa iwo.
  1695. Mrk 15:12 Ndipo Pilato adayankha natinso kwa iwo, Kodi ine tsono ndidzachita chiyani [kwa iye] amene inu mumtchula Mfumu ya Ayuda?
  1696. Mrk 15:13 Ndipo iwo adafuwulanso. Mpachikeni iye.
  1697. Mrk 15:14 Kenaka Pilato adanena kwa iwo, Chifukwa chiyani, iye wachita choyipa chotani? Koma iwo adafuwula kopambana, Mpachikeni iye.
  1698. Mrk 15:15 ¶Ndipo [potero] Pilato, pofuna kuwakhazikitsa mtima anthuwo, adawamasulira iwo Barabasi, ndipo anampereka Yesu, atamkwapula [iye], kuti akapachikidwe.
  1699. Mrk 15:16 Ndipo asirikali adachoka naye nalowa m’bwalo, ndilo Pratoriyamu; nasonkhanitsa gulu lawo lonse.
  1700. Mrk 15:17 Ndipo adamveka iye ndi chovala cha [mtundu wa] pepo, naluka korona wa minga, namveka pa [mutu] pake.
  1701. Mrk 15:18 Ndipo adayamba kumulonjera iye, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda!
  1702. Mrk 15:19 Ndipo adampanda iye pamutu pake ndi bango, ndipo anamlavulira iye malovu, pompindira mawondo [awo] anamlambira iye.
  1703. Mrk 15:20 Ndipo atatha kum’nyoza iye, adavula chovala chapepocho pa iye, ndipo anamveka zovala zake, ndipo adatuluka naye kuti akampachike iye.
  1704. Mrk 15:21 Ndipo adamkangamiza wina Simoni Mkurene, amene amadutsapo, wotuluka kuchokera m’dzikomo, atate wawo wa Alekizanda ndi Rufus, kuti anyamule mtanda wake.
  1705. Mrk 15:22 Ndipo adabwera naye ku malo Gologota, amene ali, pakutanthawuzidwa, Malo a bade.
  1706. Mrk 15:23 Ndipo adampatsa kuti amwe vinyo wosanganiza ndi mure: koma iye sadalandire [uyo] ayi.
  1707. Mrk 15:24 Ndipo pamene adampachika iye, adagawana zovala zake, kuchita mayere pa izo, kuti adziwe chimene munthu aliyense adzatenga.
  1708. Mrk 15:25 Ndipo lidali ora lachitatu, ndipo iwo adampachika iye.
  1709. Mrk 15:26 Ndipo lemba la mlandu wake lidalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.
  1710. Mrk 15:27 Ndipo pamodzi ndi iye adapachika mbava ziwiri; m’modzi kudzanja lake lamanja, ndi wina ku lamanzere lake.
  1711. Mrk 15:28 Ndipo lemba lidakwaniritsidwa, limene lidati, Ndipo iye adawerengedwa pamodzi ndi wophwanya malamulo.
  1712. Mrk 15:29 Ndipo iwo amene ankadutsapo adachitira mwano pa iye, kupukusa mitu yawo, ndi kunena, Ha, iwe amene uwononga kachisi, ndi kum’manga [iye] m’masiku atatu,
  1713. Mrk 15:30 Udzipulumutse wekha, ndipo utsike pamtandapo.
  1714. Mrk 15:31 Chimodzimodzinso ansembe akulu kumtonza ndi kunena pakati pawo pamodzi ndi alembi, Iye adapulumutsa ena; iye yekha sangadzipulumutse.
  1715. Mrk 15:32 Atsike tsono Khristu Mfumu ya Israyeli kuchoka pa mtanda, kuti ife tiwone ndi kukhulupirira. Ndipo iwo amene adapachikidwa pamodzi ndi iye adamlalatira iye.
  1716. Mrk 15:33 Ndipo litafika ora lachisanu ndi limodzi, padali mdima pa dziko kufikira ora lachisanu ndi chinayi.
  1717. Mrk 15:34 Ndipo pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu adafuwula ndi mawu wokweza, kunena kuti Eloi, Eloi, lama sabakitani? Amene ali pakutanthawuzidwa, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji ine?
  1718. Mrk 15:35 Ndipo ena amene adayimirirapo, pamene adamva [ichi], adanena, Tawonani, iye ayitana Eliya.
  1719. Mrk 15:36 Ndipo m’modzi adathamanga ndi kudzaza chinkhupule ndi viniga, ndipo anachiyika [icho] pa bango, ndipo anampatsa kuti amwe, kunena kuti, Lekeni; tiyeni ife tiwone ngati Eliya adza kuti adzamtsitse iye.
  1720. Mrk 15:37 Ndipo Yesu adafuwula ndi mawu wokweza, ndipo anamwalira.
  1721. Mrk 15:38 Ndipo chinsalu chotchinga cha m’kachisi chidang’ambika pakati magawo awiri, kuyambira kumwamba kufikira pansi.
  1722. Mrk 15:39 ¶Ndipo pamene kenturiyoni, amene adayimirira popenyana ndi iye, adawona kuti adafuwula mokweza chotero, ndipo adamwalira, iye adati, Zowonadi munthu uyu adali Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  1723. Mrk 15:40 Padalinso pamenepo akazi akuyang’anira patali: amene pakati pa iwo padali Mariya Mmagidalene, ndi Mariya amayi ake a Yakobo wam’ng’ono ndi wa Yoses, ndi Salome;
  1724. Mrk 15:41 (Amenenso pamene adali mu Galileya, adamtsata iye, ndipo anamtumikira iye;) ndi akazi ena ambiri amene adadza kukwera ndi iye ku Yerusalemu.
  1725. Mrk 15:42 ¶Ndipo tsopano pamene madzulo adafika, chifukwa linali tsiku la chikonzekero, ndiko kuti, tsiku la pambuyo pa sabata,
  1726. Mrk 15:43 Yosefe wa ku Arimateya, mlangizi wolemekezeka, amenenso adali kuyembekezera ufumu wa Mulungu, adadza, ndipo analowa molimba mtima kwa Pilato, ndipo anapempha mtembo wa Yesu.
  1727. Mrk 15:44 Ndipo Pilato adazizwa ngati adali atamwalira kale: ndipo anayitana [kwa iye] kenturiyoni, iye anamfunsa iye ngati iye adali atamwalira kwa kathawi ndithu.
  1728. Mrk 15:45 Ndipo pamene iye adadziwa za [ichi] kuchokera kwa kenturiyoni, iye adampatsa mtembowo kwa Yosefe.
  1729. Mrk 15:46 Ndipo iye adagula nsalu ya bafuta, ndipo anamtsitsa kumtenga iye, ndipo anamkulunga m’salu yabafutamo, ndipo anamuyika m’manda amene adali wosemedwa m’thanthwe, ndipo anakunkhunizira mwala pa khomo lamanda.
  1730. Mrk 15:47 Ndipo Mariya Mmagidalene ndi Mariya [amayi wake] a Yoses adapenya pamalo pomwe iye adayikidwapo.
  1731. Mrk 16:1 Ndipo pamene sabata linali litapita, Mariya Mmagidalene, ndi Mariya amayi wake a Yakobo, ndi Salome, adagula zonunkhira, kuti akadze ndi kumdzoza iye.
  1732. Mrk 16:2 Ndipo m’mamawa kwambiri [tsiku] loyamba la sabata, anadza kumanda pakutuluka dzuwa.
  1733. Mrk 16:3 Ndipo adanena pakati pa iwo wokha, Ndani adzatikunkhunizira mwalawo kuwuchotsa pakhomo la manda?
  1734. Mrk 16:4 Ndipo pamene iwo adayang’ana, iwo adawona kuti mwala wakunkhunizidwa: pakuti udali waukulu kwambiri.
  1735. Mrk 16:5 Ndipo pakulowa m’manda, iwo adawona mnyamata atakhala kumbali ya kumanja, wovala mwinjiro wawutali woyera; ndipo iwo adachititsidwa mantha.
  1736. Mrk 16:6 Ndipo iye adanena kwa iwo, Inu musachite mantha: inu muli kufuna Yesu wa ku Nazarete, amene adapachikidwa: iye wawuka; iye sali pano: tawonani malo amene adayikamo iye.
  1737. Mrk 16:7 Koma inu mukani pa njira yanu, uzani wophunzira ake ndi Petro kuti akutsogolerani inu ku Galileya: kumeneko inu mudzamuwona iye, monga iye adanena kwa inu.
  1738. Mrk 16:8 Ndipo iwo adatuluka mwamsanga, ndipo anathawa kuchokera kumanda; pakuti iwo ananthunthumira ndipo anali wodabwa; kapena kunena kanthu kalikonse kwa [munthu] aliyense; pakuti iwo adachita mantha.
  1739. Mrk 16:9 ¶Ndipo pamene [Yesu] adawuka m’mamawa [tsiku] loyamba la sabata, iye adawonekera koyamba kwa Mariya Mmagidalene amene mwa iye adamtulutsa ziwanda zisanu ndi ziwiri.
  1740. Mrk 16:10 [Ndipo] iye adapita ndi kukawawuza iwo amene adakhala naye, pamene iwo anali ndi kubuma ndi kulira.
  1741. Mrk 16:11 Ndipo iwowo, pamene adamva kuti iye ali ndi moyo, ndi kuti adawonekera kwa iye, sadakhulupirire ayi.
  1742. Mrk 16:12 ¶Ndipo zitatha izi; adawonekeranso iye m’mawonekedwe ena kwa awiri a iwo amene, pamene adali kuyenda, ndi kupita kulowa m’dzikomo.
  1743. Mrk 16:13 Ndipo iwowa adapita ndi kuwuza [ichi] kwa wotsala: komanso iwo sadakhulupirira iwo.
  1744. Mrk 16:14 ¶Ndipo pambuyo pake iye adawonekera kwa khumi ndi m’modzi pamene iwo adalikuseyama pa chakudya, ndipo adawadzudzula iwo ndi kusakhulupirira kwawo ndi kuwuma kwa mtima, chifukwa sadakhulupirira iwo amene adamuwona iye atawuka iye.
  1745. Mrk 16:15 Ndipo iye adanena kwa iwo, Mukani ku dziko lonse lapansi, ndipo lalikirani uthenga wabwino kwa cholengedwa chilichonse.
  1746. Mrk 16:16 Iye amene akhulupirira ndipo abatizidwa adzapulumuka; koma iye amene sakhulupirira adzalangidwa.
  1747. Mrk 16:17 Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupirira; M’dzina langa adzatulutsa ziwanda; iwo adzayankhula ndi malirime atsopano;
  1748. Mrk 16:18 Iwo adzatenga njoka; ndipo ngati amwa kanthu kalikonse kakufa nako, iko sikadzawapweteka iwo; adzayika manja awo pa wodwala, ndipo iwo adzachira.
  1749. Mrk 16:19 ¶Kotero kenaka Ambuye atatha kuyankhula kwa iwo, iye adalandiridwa kumwamba, ndipo anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.
  1750. Mrk 16:20 Ndipo iwowa adapita, ndipo analalikira ponseponse, Ambuye akugwira ndi [iwo] ntchito pamodzi, ndipo anatsimikiza mawu ndi zizindikiro zakutsatirapo. Amen.
  1751. Luk 1:1 Monga kuli kwakuti ambiri adayesa kulongosola mwatsatanetsatane nkhani ya zinthu izo zimene ziri zowonadi zokhulupiridwa pakati pa ife,
  1752. Luk 1:2 Monga adazipereka izo kwa ife, iwo amene kuyambira pachiyambi adakhala mboni zowona ndi maso, ndi atumiki a mawu;
  1753. Luk 1:3 Zidawoneka zokoma kwa inenso, nditakhala ndi kumvetsetsa kwangwiro kwa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe mwa tsatanetsatane, Teyofilasi wolemekezeka kwambiri.
  1754. Luk 1:4 Kuti iwe ukhoze kudziwa zowona zake za zinthu izo, zimene iwe waphunzitsidwa.
  1755. Luk 1:5 ¶Mudali m’masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, wansembe wina, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya: ndi mkazi wake [anali] wa ana akazi a Aroni, ndipo dzina lake [linali] Elizabeti.
  1756. Luk 1:6 Ndipo onse awiri adali wolungama pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoyikika za Ambuye wopanda banga.
  1757. Luk 1:7 Ndipo iwo adalibe mwana, chifukwa chakuti Elizabeti adali wosabala, ndipo iwo onse awiri adali [tsopano] zaka zawo zochuluka.
  1758. Luk 1:8 Ndipo zidachitika kuti, pamene iye anali kugwira ntchito ya unsembe pamaso pa Mulungu mu dongsolo la gulu lake,
  1759. Luk 1:9 Monga mwa mwambo wa ntchito ya mkulu wansembe, mayere a pa iye anali akufukizira zonunkhira pamene iye alowa m’kachisi ya Ambuye.
  1760. Luk 1:10 Ndipo khamu lonse la anthu lidali kupemphera kunja pa nthawi ya zonunkhira.
  1761. Luk 1:11 Ndipo adawonekera kwa iye mngelo wa Ambuye atayimirira ku dzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.
  1762. Luk 1:12 Ndipo pamene Zakariya adamuwona [iye], anavutika, ndipo mantha adam’gwira iye.
  1763. Luk 1:13 Koma mngelo adati kwa iye, Usawope Zakariya: chifukwa kuti pemphero lako lamveka; ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira iwe mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
  1764. Luk 1:14 Ndipo iwe udzakhala nacho chimwemwe ndi chisangalalo; ndipo ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.
  1765. Luk 1:15 Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena chakumwa cha ukali; ndipo adzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ngakhale kuyambira m’mimba mwa amayi wake.
  1766. Luk 1:16 Ndipo ambiri ana a Israyeli iye adzawatembenuzira kwa Ambuye Mulungu wawo.
  1767. Luk 1:17 Ndipo iye adzamtsogolera iye mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kuti atembenuzire mitima ya atate kwa ana, ndi wosamvera ku nzeru ya wolungama mtima; kuti awakonzekeretse anthu kukhala okonzekera Ambuye.
  1768. Luk 1:18 Ndipo Zakariya adati kwa mngelo, Ndidzadziwa ichi ndi chiyani? Pakuti ine ndine munthu wokalamba, ndipo mkazi wanga zaka zake nzochuluka ndithu.
  1769. Luk 1:19 Ndipo mngelo poyankha adati kwa iye, Ine ndine Gabrieli, amene amayimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndidatumidwa kudzayankhula kwa iwe, ndikuwuza iwe uthenga wabwino uwu.
  1770. Luk 1:20 Ndipo, tawona, iwe udzakhala bububu, ndi wosakhoza kuyankhula, kufikira tsiku limene zinthu izi zidzachitika; chifukwa iwe sukhulupirira mawu anga, amene adzakwaniritsidwa pa nyengo yake.
  1771. Luk 1:21 Ndipo anthu analindira Zakariya, ndipo anazizwa kuti anachedwa kwambiri m’kachisimo.
  1772. Luk 1:22 Ndipo pamene iye adatulukamo, sadathe kuyankhula kwa iwo: ndipo iwo adazindikra kuti iye adawona masomphenya m’kachisimo: ndipo iye adalinkukodola iwo, ndipo anakhalabe wosayankhula.
  1773. Luk 1:23 Ndipo kudachitika, kuti, masiku a utumiki wake atamalizidwa, adanyamuka kupita kunyumba kwake.
  1774. Luk 1:24 Ndipo atatha masiku awa, mkazi wake Elizabeti adayima; ndipo anadzibisa miyezi isanu, nanena kuti,
  1775. Luk 1:25 Chotero Ambuye wachita ndi ine m’masiku omwe iye adapenyera pa [ine], kuchotsa chitonzo changa pakati pa anthu.
  1776. Luk 1:26 Ndipo mwezi wa chisanu ndi umodzi mngelo Gabrieli adatumidwa ndi Mulungu kupita ku mzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete.
  1777. Luk 1:27 Kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna amene dzina lake linali Yosefe, wa nyumba ya Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo [linali] Mariya.
  1778. Luk 1:28 Ndipo mngelo adalowa kwa iye, ndipo adati, Tikuwoneni, [inu amene muli] wokonderedwa mwapamwamba, Ambuye [ali] ndi iwe: wodala [iwe] pakati pa amayi.
  1779. Luk 1:29 Ndipo pamene adamuwona [iye], adavutika ndi kunena uku, ndipo anasinkhasinkha m’malingaliro mwake kuti kuyankhula uku nkotani.
  1780. Luk 1:30 Ndipo mngelo adati kwa iye, Usawope, Mariya: pakuti iwe wapeza kukonderedwa ndi Mulungu.
  1781. Luk 1:31 Ndipo, tawona, udzakhala ndi pakati m’mimba mwako, ndipo udzabala mwana wamwamuna, ndipo adzatchedwa dzina lake YESU.
  1782. Luk 1:32 Iye adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba: ndipo Ambuye Mulungu adzapatsa kwa iye mpando wachifumu wa atate wake Davide.
  1783. Luk 1:33 Ndipo iye adzachita ufumu pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ndipo za ufumu wake sipadzakhala mapeto.
  1784. Luk 1:34 Kenaka Mariya adati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?
  1785. Luk 1:35 Ndipo mngelo adayankha ndipo anati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba iwe: chonchonso choyeracho chimene chidzabadwa kwa iwe chidzatchedwa Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  1786. Luk 1:36 Ndipo, tawona, msuwani wako Elizabeti, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake: ndipo uno ndi mwezi wachisanu ndi umodzi wa iye, amene adatchedwa wosabala.
  1787. Luk 1:37 Popeza ndi Mulungu palibe zinthu zidzakhala zosatheka.
  1788. Luk 1:38 Ndipo Mariya adati, Onani mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mawu anu. Ndipo mngelo adanyamuka kumchokera iye.
  1789. Luk 1:39 Ndipo Mariya adanyamuka masiku amenewo, ndipo anapita kulowa ku dziko la ku phiri ndi changu, mu mzinda wa Yuda;
  1790. Luk 1:40 Ndipo adalowa m’nyumba ya Zakariya, ndipo anayankhula kwa Elizabeti.
  1791. Luk 1:41 Ndipo kudachitika, kuti, pamene Elizabeti adamva kuyankhula kwake kwa Mariya, mwana adalumpha m’mimba mwake; ndipo Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera.
  1792. Luk 1:42 Ndipo adayankhula ndi mawu okweza, ndipo anati, Wodala [iwe] pakati pa akazi, ndipo chodalitsika [chili] chipatso cha mimba yako.
  1793. Luk 1:43 Ndipo [ichi] chichokera kuti kudza kwa ine, kuti amayi wake wa Ambuye wanga adze kwa ine?
  1794. Luk 1:44 Pakuti, tawona, kumveka kwa mawu atangolankhulidwa atalowa m’makutu anga, mwana adalumpha ndi msangalalo m’mimba mwanga.
  1795. Luk 1:45 Ndipo wodala [ali] iye amene adakhulupirira: chifukwa padzakhala kuchitidwa kwa zinthu izo zimene zidanenedwa kwa iye kuchokera kwa Ambuye,
  1796. Luk 1:46 Ndipo Mariya adati, Moyo wanga ukuza Ambuye.
  1797. Luk 1:47 Ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.
  1798. Luk 1:48 Pakuti iye wayang’anira kuchepa kwa mdzakazi wake: pakuti, tawonani, kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditchula ine wodala.
  1799. Luk 1:49 Pakuti iye amene ali wamphamvuyo wachitira kwa ine zinthu zazikulu; ndipo dzina lake [liri] loyera.
  1800. Luk 1:50 Ndipo chifundo chake [chili] pa iwo akumuwopa iye kuchokera m’badwo kufikira m’badwo.
  1801. Luk 1:51 Iye wawonetsa mphamvu ndi mkono wake; iye wabalalitsa wodzitama m’malingaliro a mitima yawo.
  1802. Luk 1:52 Iye watsitsa pansi amphamvu kuchokera pa mipando [yawo], ndipo wakweza iwo apansi.
  1803. Luk 1:53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino; ndipo eni chuma wawachotsa wopanda kanthu.
  1804. Luk 1:54 Iye wathandiza Israyeli mtumiki wake, m’kukumbukira kwa chifundo [chake];
  1805. Luk 1:55 Monga iye adayankhula kwa atate athu, kwa Abrahamu, ndi kwa mbewu yake ku nthawi zonse.
  1806. Luk 1:56 Ndipo Mariya adakhala ndi iye ngati miyezi itatu, ndipo anabwereranso kunyumba kwake.
  1807. Luk 1:57 Tsopano nthawi ya Elizabeti idafika yakuti iye abale, ndipo iye anabala mwana wamwamuna.
  1808. Luk 1:58 Ndipo anansi ake ndi asuwani ake adamva momwe Ambuye adawonetsera chifundo chachikulu pa iye; ndipo iwo anakondwera pamodzi ndi iye.
  1809. Luk 1:59 Ndipo kudachitika, kuti pa tsiku lachisanu ndi chitatu iwo adadza kudzachita mdulidwe kamwanako; ndipo adamutcha iye Zakariya, dzina la atate wake.
  1810. Luk 1:60 Ndipo amayi wake adayankha ndipo anati, Ayi [osati choncho]; koma iye adzatchedwa Yohane.
  1811. Luk 1:61 Ndipo iwo adati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili.
  1812. Luk 1:62 Ndipo iwo adachita zizindikiro kwa atate wake, momwe iye afuna dzina loti amutche?
  1813. Luk 1:63 Ndipo iye adafunsa gome lolembapo, ndipo analemba, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo iwo adazizwa onse.
  1814. Luk 1:64 Ndipo posakhalitsa pakamwa pake padatseguka, ndi lirime lake [lidamasuka], ndipo iye adayankhula, ndipo analemekeza Mulungu.
  1815. Luk 1:65 Ndipo mantha adafika pa iwo onse amene amakhala mozungulira iwo: ndipo zonena izi zonse zidayankhulidwa mofalikira m’dziko lonse la phiri la Yudeya.
  1816. Luk 1:66 Ndipo onse iwo amene adazimva [izo] adazikhazikitsa [izo] m’mitima mwawo, nanena kuti, Mwana uyu adzakhala wotani! Ndipo dzanja la Ambuye lidali pamodzi ndi iye.
  1817. Luk 1:67 Ndipo atate wake Zakariya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo ananenera, nanena kuti,
  1818. Luk 1:68 Wodalitsika [akhale] Ambuye, Mulungu wa Israyeli; pakuti iye wayendera ndi kuwombola anthu ake.
  1819. Luk 1:69 Ndipo wakweza nyanga ya chipulumutso kwa ife m’nyumba ya mtumiki wake Davide.
  1820. Luk 1:70 Monga iye adayankhula ndi m’kamwa mwa aneneri ake woyera, amene akhala kuyambira pamene dziko lidayamba:
  1821. Luk 1:71 Kuti ife tipulumutsidwe kwa adani athu, ndi kuchokera ku dzanja la onse amene atida ife;
  1822. Luk 1:72 Kuti achitire chifundo [cholonjezedwa] kwa atate wathu, ndi kukumbukira pangano lake loyera;
  1823. Luk 1:73 Lumbiro limene iye adalumbira kwa atate wathu Abrahamu,
  1824. Luk 1:74 Kuti iye akhoze kupatsa kwa ife, kuti ife powomboledwa kutuluka m’manja mwa adani athu tikhoze kutumikira iye mopanda mantha,
  1825. Luk 1:75 M’chiyero ndi m’chilungamo pamaso pake, masiku onse a moyo wathu.
  1826. Luk 1:76 Ndipo iwetu, mwana, udzatchedwa mneneri wa Wam’mwambamwamba: pakuti iwe udzatsogolera pamaso pa Ambuye kukonza njira zake;
  1827. Luk 1:77 Kuti apereke chidziwitso cha chipulumutso kwa anthu ake kudzera m’chikhululukiro cha machimo awo,
  1828. Luk 1:78 Kudzera mu chifundo chokoma cha Mulungu wathu; mwa ichi m’bandakucha wochokera kumwamba watichezera ife,
  1829. Luk 1:79 Kuti apereke kuwala kwa iwo akukhala mu mdima ndi [mu] mthunzi wa imfa, kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.
  1830. Luk 1:80 Ndipo mwanayo adakula, ndipo analimbika mu mzimu, ndipo iye adali m’zipululu kufikira tsiku la kuwonetsera kwake kwa Israyeli.
  1831. Luk 2:1 Ndipo kudachitika m’masiku aja, kuti lidatuluka lamulo kwa Kayisara Augustasi, kuti dziko lonse lokhalamo anthu litichidwe chiwerengero.
  1832. Luk 2:2 ([Ndipo] chiwerengro cha anthu ichi chidachitika koyamba nthawi imene Sayireniyasi anali kazembe wa Siriya.)
  1833. Luk 2:3 Ndipo onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mzinda wake.
  1834. Luk 2:4 Ndipo Yosefe yemwe adakwera kuchokera ku Galileya, kuchokera mu mzinda wa Nazarete, kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide, umene utchedwa Betelehemu; (chifukwa iye adali wa banja lake la Davide:)
  1835. Luk 2:5 Kukalembedwa iye pamodzi ndi Mariya wopalidwa ubwenzi, ali ndi pakati potsala pang’ono kubereka.
  1836. Luk 2:6 Ndipo padali kotero, kuti, pamene adali komweko, masiku ake a kubala adakwanira kuti iye abereke.
  1837. Luk 2:7 Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba, ndipo anamukulunga iye mu nsalu za mbereko, ndipo anamgoneka iye modyera ng’ombe; chifukwa kuti padalibe malo a iwo m’nyumba ya alendo.
  1838. Luk 2:8 Ndipo padali abusa m’dziko lomwero, okhala kobusa kuyang’anira zoweta zawo usiku.
  1839. Luk 2:9 Ndipo, tawonani, mngelo wa Ambuye adafika pa iwo, ndipo ulemerero wa Ambuye udawala mozungulira iwo: ndipo iwo adali ndi mantha akulu.
  1840. Luk 2:10 Ndipo mngelo adati kwa iwo, Musawope: pakuti tawonani, ine ndibweretsera inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse.
  1841. Luk 2:11 Pakuti kwa inu wakubadwirani tsiku la lero, mu mzinda wa Davide Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.
  1842. Luk 2:12 Ndipo ichi [chidzakhala] chizindikiro kwa inu; Mudzapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu za mbereko, atagona modyera ng’ombe.
  1843. Luk 2:13 Ndipo mwadzidzidzi padali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la kumwamba natamanda Mulungu, nanena kuti,
  1844. Luk 2:14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu m’mwambamwamba, ndi pansi pano mtendere, kufuna kwabwino kwa anthu.
  1845. Luk 2:15 Ndipo padachitika, pamene angelo adachoka kwa iwo kupita kumwamba, abusa adati wina kwa mzake, Tipitiretu tsopano ku Betelehemu, ndipo tikawone chinthu ichi chimene chachitika, chimene Ambuye atidziwitsa ife.
  1846. Luk 2:16 Ndipo iwo anadza mwachangu, ndipo anapeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera ng’ombe.
  1847. Luk 2:17 Ndipo pamene iwo adawona [ichi], iwo adachidziwitsa kufalikira kutali kudera lalikulu za mawu adayankhulidwa kwa iwo okhudza mwana uyu.
  1848. Luk 2:18 Ndipo anthu onse iwo amene adamva [ichi] adazizwa ndi zinthu zimene adawuzidwa ndi abusawo.
  1849. Luk 2:19 Koma Mariya adasunga zinthu izi, ndipo anazilingalira [izo] mumtima mwake.
  1850. Luk 2:20 Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zinthu zonse zimene iwo adazimva ndi kuziwona, monga zidawuzidwa kwa iwo.
  1851. Luk 2:21 Ndipo pamene adakwanira masiku asanu ndi atatu a kumchita mdulidwe iye, adamutcha dzina lake YESU, limene adatchula motero ndi mngeloyo iye asanalandiridwe m’mimba.
  1852. Luk 2:22 Ndipo pamene masiku a kuyeretsa iye monga mwa chilamulo cha Mose adakwanira, iwo adakwera naye kupita ku Yerusalemu, kukamsonyeza [iye] kwa Ambuye;
  1853. Luk 2:23 (Monga mwalembedwa m’chilamulo cha Ambuye, Mwamuna aliyense wotsegula mimba ya amayi wake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye;)
  1854. Luk 2:24 Ndikupereka nsembe monga mwanenedwa m’chilamulo cha Ambuye, Njiwa ziwiri, kapena mawunda awiri.
  1855. Luk 2:25 Ndipo, tawonani, mudali munthu mu Yerusalemu, amene dzina lake [linali] Simiyoni; ndipo munthu uyu [anali] wolungama mtima ndi wopembedza, adalikulindira matonthozedwe a Israyeli: ndipo Mzimu Woyera adali pa iye.
  1856. Luk 2:26 Ndipo adamuwululira Mzimu Woyera, kuti iye sadzawona imfa, iye asadawone Khristu wa Ambuye.
  1857. Luk 2:27 Ndipo mwa Mzimu iye adalowa ku kachisi; ndipo pamene makolo adalowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira iye motsatira mwambo wa chilamulo;
  1858. Luk 2:28 Kenaka iye adamtenga iye m’manja mwake, ndipo analemekeza Mulungu, ndipo anati,
  1859. Luk 2:29 Ambuye, tsopano lolani mtumiki wanu ndichoke mu mtendere, monga mwa mawu anu:
  1860. Luk 2:30 Pakuti maso anga awona chipulumutso chanu.
  1861. Luk 2:31 Chimene inu mwakonza pamaso pa anthu onse;
  1862. Luk 2:32 Kuwunika kukawalire anthu Amitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.
  1863. Luk 2:33 Ndipo Yosefe ndi amayi ake adazizwa ndi zinthu zoyankhulidwa za iye.
  1864. Luk 2:34 Ndipo Simiyoni adawadalitsa iwo, ndipo anati kwa Mariya amayi ake, Tawona, [mwana] uyu wayikidwa akhale kugwa ndi kuwuka kwa ambiri mu Israyeli; ndi chizindikiro chimene adzalankhula motsutsana nacho;
  1865. Luk 2:35 (Eya, ndipo lupanga lidzapyoza moyo wako womwenso,) kuti maganizo a mitima yambiri ikhoze kuvumbulutsidwa.
  1866. Luk 2:36 Ndipo padali wina Anna, mneneri wamkazi, mwana wamkazi wa Fanuweli, wa fuko la Aseri: adali wokalamba ndithu, ndipo adakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri kuyambira pa unamwali wake;
  1867. Luk 2:37 Ndipo iye [adali] wamasiye kufikira zaka makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi, amene sadachoke ku kachisi, koma adatumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.
  1868. Luk 2:38 Ndipo iye polowa pa nthawi yomweyo adapereka mayamiko chimodzimodzi kwa Ambuye, ndipo anayankhula za iye kwa onse amene woyembekezera chiwombolo cha Yerusalemu.
  1869. Luk 2:39 Ndipo pamene iwo adatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, iwo anabwerera kulowa ku Galileya, ku mzinda wawo Nazarete.
  1870. Luk 2:40 Ndipo mwanayo adakula, ndipo analimbika mu mzimu, wodzala ndi nzeru: ndi chisomo cha Mulungu chidali pa iye.
  1871. Luk 2:41 Tsopano makolo ake ankapita chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku phwando la Paskha.
  1872. Luk 2:42 Ndipo pamene iye adali ndi zaka khumi ndi ziwiri, iwo adakwera ku Yerusalemu motsata machitidwe a phwando.
  1873. Luk 2:43 Ndipo iwo adamaliza masikuwo, pakubwerera iwo, mwanayo Yesu adatsalira m’mbuyo ku Yerusalemu; ndipo Yosefe ndi amayi wake sadadziwa [za ichi].
  1874. Luk 2:44 Koma iwo, poganiza kuti iye adali m’chipiringu [cha ulendo], adayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo iwo adamfunafuna iye mwa abale [awo] ndi mwa anansi awo.
  1875. Luk 2:45 Ndipo pamene sadampeza iye, adabwereranso ku Yerusalemu, kukamfunafuna iye.
  1876. Luk 2:46 Ndipo kudachitika, pakupita masiku atatu adampeza iye ali m’kachisi, alikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, ndi kuwafunsa mafunso.
  1877. Luk 2:47 Ndipo onse amene adamva iye anadabwa ndi kuzindikira kwake ndi mayankho [ake].
  1878. Luk 2:48 Ndipo m’mene adamuwona iye, iwo anadabwa: ndipo amayi wake adati kwa iye, Mwana wamwamuna, wachitiranji ndi ife chotero? Tawona, atate wako ndi ine tidali kufunafuna iwe ndi kuda nkhawa.
  1879. Luk 2:49 Ndipo iye adati kwa iwo, Kuli bwanji kuti mudali kundifuna ine? Simudziwa inu kodi kuti kundiyenera ine ndikhale mu ntchito za Atate wanga?
  1880. Luk 2:50 Ndipo iwo sadadziwitsa kunena kumene iye adayankhula kwa iwo.
  1881. Luk 2:51 Ndipo iye adatsika nawo pamodzi, ndipo anadza ku Nazarete, ndipo anawamvera iwo: koma amayi wake adasunga zonena izi zonse mumtima mwake.
  1882. Luk 2:52 Ndipo Yesu adakulabe mu nzeru ndi msinkhu, ndi m’kukonderedwa ndi Mulungu ndi munthu.
  1883. Luk 3:1 Tsopano m’chaka chakhumi ndi chisanu cha ulamuliro wa Tiberiyasi Kayisara, Pontiyasi Pilato pokhala kazembe wa Yudeya, ndi Herode wokhala wolamulira gawo lachinayi wa dziko ali wolamulira wa Galileya, ndi Filipi mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi chigawo cha Trakonitisi, ndi Lusaniyasi chiwanga cha Abilene,
  1884. Luk 3:2 Annasi ndi Kayafasi pakukhala ansembe akulu, mawu a Mulungu anadza kwa Yohane mwana wamwamuna wa Zakariya m’chipululu.
  1885. Luk 3:3 Ndipo iye anadza kulowa mu dziko lonse la m’mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;
  1886. Luk 3:4 Monga mwalembedwa m’buku la mawu a Yesaya mneneri, kunena kuti, Mawu a wofuwula m’chipululu, Konzani inu njira ya Ambuye, wongolani makwalala ake.
  1887. Luk 3:5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lirilonse ndi mtunda uliwonse zidzachepetsedwa; ndipo zokhota zidzawongoledwa, ndipo njira za zigolowondo [zidzakhala] zosalazidwa.
  1888. Luk 3:6 Ndipo anthu onse adzawona chipulumutso cha Mulungu.
  1889. Luk 3:7 Kenaka iye adati kwa makamu amene anadza kudzabatizidwa ndi iye, Mbadwo wa njoka inu, ndani wakuchenjezani inu kuti muthawe mkwiyo ulinkudza?
  1890. Luk 3:8 Choncho balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, tiri naye Atate [wathu] ndiye Abrahamu: pakuti ine ndinena kwa inu, Kuti Mulungu ali ndi mphamvu mwa miyala iyi kuwukitsira Abrahamu ana.
  1891. Luk 3:9 Ndipo tsopano lino nkhwangwa yayikidwa pamizu ya mitengo: choncho mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, ndipo uponyedwa pamoto.
  1892. Luk 3:10 Ndipo anthu adamfunsa iye, nanena kuti, Ndipo tsono ife tidzachita chiyani?
  1893. Luk 3:11 Iye adayankha nati kwa iwo, Iye amene ali nawo malaya awiri agawireko iye amene alibe; ndi iye amene ali nacho chakudya achite chimodzimodzi.
  1894. Luk 3:12 Kenaka anadzanso wokhometsa misonkho kwa iye kudzabatizidwa, ndipo anati kwa iye, Ambuye, ife tidzachita chiyani?
  1895. Luk 3:13 Ndipo iye adati kwa iwo, Musamawonjezerapo kanthu konse kakuposa chimene chidalamulidwa kwa inu.
  1896. Luk 3:14 Ndipo asirikali chimodzimodzi adamfunsa iye, nanena kuti, Nanga ife tidzachita chiyani? Ndipo iye adati kwa iwo, Musamawopseze, kapena musamanamizire munthu aliyense; khalani wokhutitsidwa ndi malipiro anu.
  1897. Luk 3:15 Ndipo pamene anthu adali m’chiyembekezo, ndipo onse adaganizaganiza m’mitima yawo za Yohane, ngati kapena iye adali Khristu, kapena ayi;
  1898. Luk 3:16 Yohane adayankha, nanena kwa [iwo] onse, Inetu inde ndikubatizani inu ndi madzi; koma wina wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene chingwe cha nsapato zake ine sindiyenera kumasula: iye adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
  1899. Luk 3:17 Amene chokupizira chake [chili] m’dzanja lake, ndipo adzayeretsa kwathunthu padwale pake, ndipo adzasonkhanitsa tirigu m’nkhokwe yake; koma mankhusu adzatenthedwa m’moto wosazimitsika.
  1900. Luk 3:18 Ndi zinthu zina zambiri mukuwalimbikitsa kwake iye analalikira kwa anthuwo.
  1901. Luk 3:19 Koma Herode wolamulira gawo lachinayi la dzikolo, podzudzulidwa ndi iye chifukwa cha Herodiyasi mkazi wa mbale wake Filipi, ndi cha zinthu zonse zoyipa Herode adazichita.
  1902. Luk 3:20 Adawonjeza ichinso pamwamba pa zonsezi, kuti adatsekera Yohane m’nyumba yandende.
  1903. Luk 3:21 Tsopano pamene anthu onse anabatizidwa, kudachitika, kuti Yesu pobatizidwanso, ndipo ali kupemphera, kumwamba kudatseguka,
  1904. Luk 3:22 Ndipo Mzimu Woyera adatsika ndi mawonekedwe athupi ngati nkhunda kudza pa iye; ndipo kudatuluka mawu kumwamba, amene adati, Iwe ndiwe Mwana wanga wamwamuna wokondedwa; mwa iwe ndikondwera bwino.
  1905. Luk 3:23 Ndipo Yesuyo mwini adali kufikira zaka makumi atatu, wokhala (monga momwe kudayerekezera) mwana wamwamuna wa Yosefe, amene adali mwana wamwamuna wa Heli,
  1906. Luk 3:24 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Matati, amene adali [mwana wamwamuna] wa Levi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Melki, amene adali [mwana wamwamuna] wa Jana, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yosefe.
  1907. Luk 3:25 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Matatiyasi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Amosi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Naumi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Esli, amene adali [mwana wamwamuna] wa Nagge,
  1908. Luk 3:26 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Maati, amene adali [mwana wamwamuna] wa Matatiyasi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Semei, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yosefe, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yuda,
  1909. Luk 3:27 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Joanna, amene adali [mwana wamwamuna] wa Resa, amene adali [mwana wamwamuna] wa Zorobabeli, amene [adali mwana wamwamuna wa] Selatiyeli, amene adali [mwana wamwamuna] wa Neri,
  1910. Luk 3:28 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Melki, amene adali [mwana wamwamuna] wa Addi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Kosamu, amene adali [mwana wamwamuna] wa Elmodam, amene adali [mwana wamwamuna] wa Ere,
  1911. Luk 3:29 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Jose, amene adali [mwana wamwamuna] wa Eliezere, amene adali [mwana wamwamuna] wa Jorimu, amene adali [mwana wamwamuna] wa Matati, amene adali [mwana wamwamuna] wa Levi,
  1912. Luk 3:30 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Simiyoni, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yuda, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yosefe, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yonan, amene adali [mwana wamwamuna] wa Eliyakimu,
  1913. Luk 3:31 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Melea, amene adali [mwana wamwamuna] wa Menan, amene adali [mwana wamwamuna] wa Matata, amene adali [mwana wamwamuna] wa Natani, amene adali [mwana wamwamuna] wa Davide,
  1914. Luk 3:32 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Jese, amene adali [mwana wamwamuna] wa Obede, amene adali [mwana wamwamuna] wa Boazi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Salmoni, amene adali [mwana wamwamuna] wa Naasoni,
  1915. Luk 3:33 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Aminadabu, amene adali [mwana wamwamuna] wa Aram, amene adali [mwana wamwamuna] wa Ezirom, amene adali [mwana wamwamuna] wa Farese, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yuda,
  1916. Luk 3:34 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Yakobo, amene adali [mwana wamwamuna] wa Isake, amene adali [mwana wamwamuna] wa Abrahamu, amene adali [mwana wamwamuna] wa Tera, amene adali [mwana wamwamuna] wa Nakori,
  1917. Luk 3:35 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Saruki, amene adali [mwana wamwamuna] wa Ragau, amene adali [mwana wamwamuna] wa Phaleke, amene adali [mwana wamwamuna] wa Hebere, amene adali [mwana wamwamuna] wa Sala,
  1918. Luk 3:36 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Kainane, amene adali [mwana wamwamuna] wa Arfaksadi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Semu, amene adali [mwana wamwamuna] wa Nowa, amene adali [mwana wamwamuna] wa Lameke,
  1919. Luk 3:37 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Matusala, amene adali [mwana wamwamuna] wa Enoke, amene adali [mwana wamwamuna] wa Yaredi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Malaleeli, amene adali [mwana wamwamuna] wa Kayinane,
  1920. Luk 3:38 Amene adali [mwana wamwamuna] wa Enosi, amene adali [mwana wamwamuna] wa Seti, amene adali [mwana wamwamuna] wa Adamu, amene adali [mwana wamwamuna] wa Mulungu.
  1921. Luk 4:1 Ndipo Yesu wodzala ndi Mzimu Woyera adabwerera kuchokera ku Yordano, ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu kupita kukalowa m’chipululu,
  1922. Luk 4:2 Pakukhala masiku makumi anayi kuyesedwa ndi mdierekezi. Ndipo m’masiku amenewo iye sanadye kanthu kena kalikonse: ndipo pamene adatha, pambuyo pake iye adamva njala.
  1923. Luk 4:3 Ndipo mdierekezi adati kwa iye, Ngati muli Mwana wamwamuna wa Mulungu, lamulirani mwala uwu kuti usanduke mkate.
  1924. Luk 4:4 Ndipo Yesu adayankha iye, nanena kuti, Kwalembedwa, Kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu aliwonse a Mulungu.
  1925. Luk 4:5 Ndipo mdierekezi, adamtenga iye nakwera naye pa phiri, anamuwonetsa iye maufumu onse a dziko lonse lapansi m’kamphindi kakang’ono.
  1926. Luk 4:6 Ndipo mdierekezi adati kwa iye, Ulamuliro uwu wonse ine ndidzapatsa inu, ndi ulemerero wawo: pakuti udaperekedwa kwa ine; ndipo ndiwupereka kwa wina aliyense amene ine ndifuna.
  1927. Luk 4:7 Choncho ngati inu mudzandirambira ine, wonsewo udzakhala wanu.
  1928. Luk 4:8 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Pita iwe kumbuyo kwanga Satana: pakuti kwalembedwa, Iwe udzamlambira Ambuye Mulungu wako ndipo iye yekha udzamtumikira.
  1929. Luk 4:9 Ndipo adabwera naye ku Yerusalemu, ndipo anamuyika iye pamwamba pa nsonga ya kachisi, ndipo anati kwa iye, Ngati inu muli Mwana wamwamuna wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi kuchokera pano:
  1930. Luk 4:10 Pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamulira angelo ake za inu, kuti akusungeni inu.
  1931. Luk 4:11 Ndipo m’manja [awo] adzakunyamulani inu, kuti mwina pa nthawi ina iliyonse mungagunde konse phazi lanu pa mwala.
  1932. Luk 4:12 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Kwanenedwa, Iwe usamuyese Ambuye Mulungu wako.
  1933. Luk 4:13 Ndipo pamene mdierekezi adamaliza mayesero onse, adamchokera iye kwa kanyengo.
  1934. Luk 4:14 ¶Ndipo Yesu adabwerera mu mphamvu ya Mzimu ku Galileya: ndipo mbiri yake ya iye inabuka dziko lonse lozungulira.
  1935. Luk 4:15 Ndipo iye adaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalemekezedwa ndi onse.
  1936. Luk 4:16 ¶Ndipo anadza ku Nazarete, kumene iye adaleredwa: ndipo, monga chizolowezi chake chidali, iye adalowa m’sunagoge tsiku la sabata, ndipo adayimiriramo kuti awerenge.
  1937. Luk 4:17 Ndipo lidaperekedwa kwa iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m’mene iye adatsegula bukulo, adapeza pomwe padalembedwa,
  1938. Luk 4:18 Mzimu wa Ambuye [ali] pa ine, chifukwa iye wandidzoza ine ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osawuka; wandituma ine kukachiritsa a mtima wosweka, kulalikira mamasulidwe kwa am’singa, ndi kupenyanso kwa akhungu, kupatsa ufulu iwo amene ali wovulazidwa.
  1939. Luk 4:19 Kulalikira chaka cholandirika cha Ambuye.
  1940. Luk 4:20 Ndipo iye adatseka bukulo, ndipo adaliperekanso [ilo] kwa mtumiki, ndipo anakhala pansi. Ndipo maso awo a anthu onse m’sunagogemo adayang’anitsa pa iye.
  1941. Luk 4:21 Ndipo iye adayamba kunena kwa iwo, Lero lemba ili lakwaniritsidwa m’makutu anu.
  1942. Luk 4:22 Ndipo onse adamchitira iye umboni, ndipo anazizwa ndi mawu a chisomo amene adatuluka m’kamwa mwake. Ndipo iwo ananena, Kodi uyu simwana wamwamuna wa Yosefe?
  1943. Luk 4:23 Ndipo iye adati kwa iwo, Inu zowona mudzati kwa ine mwambi uwu, Dotolo, dzichiritse wekha: ziri zonse zimene tazimva zidachitidwa ku Kaperenamu, muzichitenso zomwezo kuno m’dziko lanu.
  1944. Luk 4:24 Ndipo iye adati, Ndithudi, ine ndinena kwa inu, Palibe mneneri alandiridwa ku dziko la kwawo.
  1945. Luk 4:25 Koma ine ndikuwuzani mwa chowona, mudali akazi a masiye ambiri mu Israyeli masiku ake a Eliya, pamene kudatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene padakhala njala yayikulu pa dziko lonselo;
  1946. Luk 4:26 Koma Eliya sadatumidwa kwa m’modzi wa iwo, kupatula ku Sarepta, [mzinda] wa ku Sidoni, kwa mkazi [yemwe anali] wamasiye.
  1947. Luk 4:27 Ndipo mudali akhate ambiri mu Israyeli masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe m’modzi wa iwo adakonzedwa, koma Namani yekha wa ku Siriya.
  1948. Luk 4:28 Ndipo onse a m’sunagoge, pamene adamva zinthu izi, adadzala ndi mkwiyo;
  1949. Luk 4:29 Ndipo adanyamuka, ndipo anamtulutsira iye kunja kwa mzindawo, ndipo anapita naye pamwamba pa phiri pamene padamangidwa mzinda wawo, kuti akamponye pansi chotsogoza mutu.
  1950. Luk 4:30 Koma iye mopyola pakati pawo anapita pa njira yake.
  1951. Luk 4:31 Ndipo iye adatsika kudza ku Kaperenamu, ndiwo mzinda wa ku Galileya, ndipo adali kuwaphunzitsa iwo masiku a pa sabata.
  1952. Luk 4:32 Ndipo iwo adadabwa ndi chiphunzitso chake: pakuti mawu ake adali ndi mphamvu.
  1953. Luk 4:33 ¶Ndipo m’sunagoge mudali munthu, amene adali nacho chiwanda cha mzimu wonyansa; ndipo anafuwula ndi mawu wokwera.
  1954. Luk 4:34 Nanena kuti, Tilekeni [ife] tokha; kodi tiri ndi chiyani ndi inu, [inu] Yesu wa ku Nazarete? Kodi inu mwadza kudzatiwononga ife? Ine ndikudziwani inu muli yani; Woyera wake wa Mulungu.
  1955. Luk 4:35 Ndipo Yesu adamdzudzula iye, nanena kuti, Tonthola, ndipo utuluke mwa iye. Ndipo m’mene chiwandacho chidam’gwetsa iye pakati [pawo], chidatuluka mwa iye, ndipo sichidampweteka iye ayi.
  1956. Luk 4:36 Ndipo anthu onse adadabwa, ndipo anayankhula pakati pawo, nanena kuti, Mawu amenewa [ali] wotani! Pakuti ndi ulamuliro ndi mphamvu iye alamulira mizimu yonyansa, ndipo ituluka.
  1957. Luk 4:37 Ndipo mbiri yake ya iye idafikira ku malo onse a dziko lozunguira.
  1958. Luk 4:38 ¶Ndipo iye adanyamuka kuchokera m’sunagoge, ndipo analowa m’nyumba ya Simoni. Ndipo amayi wake a mkazi wake wa Simoni adagwidwa ndi nthenda yayikulu ya kutentha thupi, ndipo iwo adampempha iye chifukwa cha iye.
  1959. Luk 4:39 Ndipo iye adayimirira pa iye, ndipo anadzudzula kutentha nthupiko; ndipo idamleka iye: ndipo posakhalitsa adawuka ndipo anawatumikira iwo.
  1960. Luk 4:40 ¶Ndipo pamene limalowa dzuwa, iwo onse amene adali nawo wodwala ndi nthenda za mitundumitundu anadza nawo kwa iye; ndipo iye adayika manja ake pa wina aliyense wa iwo, ndipo anawachiritsa iwo.
  1961. Luk 4:41 Ndipo ziwanda zomwe zidatuluka mwa ambiri, kufuwula, ndi kunena kuti, Inu ndinu Khristu Mwana wamwamuna wa Mulungu! Ndipo iye adazidzudzula [izo] wosazilola kuti ziyankhule: pakuti zidadziwa kuti iye anali Khristu.
  1962. Luk 4:42 Ndipo pamene kudacha, iye adanyamuka ndipo anapita ku malo a chipululu cha mchenga: ndipo anthu adalikumfunafuna iye, ndipo anadza kwa iye, ndipo anamletsa iye, kuti asanyamuke kuwachokera iwo.
  1963. Luk 4:43 Ndipo iye adati kwa iwo, Ine ndikuyenera kulalikira ufumu wa Mulungu ku mizinda yinanso: pakuti choncho ine ndatumidwa.
  1964. Luk 4:44 Ndipo iye adalalikira m’masunagoge aku Galileya.
  1965. Luk 5:1 Ndipo padachitika, kuti, pamene anthu anali kumkanikiza iye kudzamva mawu a Mulungu, iye adayimirira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete,
  1966. Luk 5:2 Ndipo adawona zombo ziwiri zitayima m’mbali mwa nyanja: koma asodzi adali atatuluka m’menemo, ndipo analikutsuka makhoka [awo].
  1967. Luk 5:3 Ndipo iye adalowa m’chimodzi cha zombozo, chimene chinali chake cha Simoni, ndipo anampempha iye akankhe pang’ono kuchoka kumtunda. Ndipo iye adakhala, ndipo anaphunzitsa anthuwo kuchokera m’chombomo.
  1968. Luk 5:4 Tsopano pamene iye adaleka kuyankhula, adati kwa Simoni, Kankhira kwakuya, ndipo muponye makoka anu ku kusodza.
  1969. Luk 5:5 Ndipo Simoni pakuyankha anati kwa iye, Ambuye, ife tidagwiritsa ntchito usiku wonse, ndipo osakola kanthu: ngakhale ziri choncho pa mawu anu ndidzaponya khoka.
  1970. Luk 5:6 Ndipo pamene adachita ichi, adazinga unyinji waukulu wa nsomba: ndipo khoka lawo lidang’ambika.
  1971. Luk 5:7 Ndipo iwo adakodola [anzawo], amene adali m’chombo china, kuti adze ndi kuwathandiza iwo. Ndipo iwo anadza, ndipo anadzaza zombo zonse ziwiri, kotero kuti zidayamba kumira.
  1972. Luk 5:8 Ndipo pamene Simoni Petro adawona [ichi], adagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena kuti, Muchoke kwa ine; popeza ndine munthu wochimwa, Ambuye.
  1973. Luk 5:9 Pakuti iye adazizwa, ndi onse amene adali naye, pa kasodzedwe kansomba zodzaza khoka zimene adazikola:
  1974. Luk 5:10 Ndipo chomwechonso [anali] Yakobo, ndi Yohane, ana amuna a Zebedayo, amene adali anzake a Simoni. Ndipo Yesu adati kwa Simoni, Usawope; kuyambira tsopano udzakhala iwe msodzi wa anthu.
  1975. Luk 5:11 Ndipo m’mene iwo adakocheza zombo zawo pamtunda, adasiya zonse, ndipo anamtsata iye.
  1976. Luk 5:12 ¶Ndipo padachitika, pamene iye adali mu mzinda wina, tawonani munthu wodzala ndi khate: amene pakuwona Yesu adagwa ndi nkhope [yake] pansi, ndipo anampempha iye, nanena kuti, Ambuye, ngati mufuna, mungathe kundiyeretsa ine.
  1977. Luk 5:13 Ndipo iye adatambalitsa dzanja [lake], ndipo anamkhudza iye, nanena kuti, Ine ndifuna: tayeretsedwa. Ndipo posakhalitsa khate lidachoka kwa iye.
  1978. Luk 5:14 Ndipo iye adamulamulira kuti asanene kwa munthu aliyense: koma pita, ndipo udziwonetse wekha kwa wansembe, ndipo upereke nsembe ya pa chiyeretsedwe chako, monga Mose adalamulira, chifukwa cha umboni kwa iwo.
  1979. Luk 5:15 Koma makamaka mbiri inabuka dera lalikulu ya iye: ndipo makamu akulu adasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa ndi iye nthenda zawo.
  1980. Luk 5:16 ¶Ndipo iye adachoka mwini yekha napita kuchipululu, ndipo anapemphera.
  1981. Luk 5:17 Ndipo padachitika pa tsiku lina, pamene iye adali kuphunzitsa, kuti padali Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo akukhalapo, amene adali wochokera ku mizinda iliyonse ya ku Galileya, ndi Yudeya, ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye idali [pamenepo] kuwachiritsa iwo.
  1982. Luk 5:18 ¶Ndipo, tawonani, anthu adabweretsa kulowa naye munthu wamwamuna pakama wogwidwa matenda akufa ziwalo: ndipo anafunafuna [njira] yobweretsera iye mkati, ndi kumugoneka [iye] pamaso pa iye.
  1983. Luk 5:19 Ndipo pamene iwo sadapeza njira imene angakhoze kumulowetsera iye mkati, chifukwa cha khamu, iwo adakwera pamwamba pa denga, ndipo anamtsitsira iye [pobowola] pa denga ndi kama [wake] namfikitsa pakati pamaso pa Yesu.
  1984. Luk 5:20 Ndipo iye pamene adawona chikhulupiriro chawo, iye adati kwa iye, Mwamuna, machimo ako akhululukidwa.
  1985. Luk 5:21 Ndipo alembi ndi Afarisi adayamba kufunsana maganizo, kunena kuti, Ndani uyu amene ayankhula zonyoza [Mulungu]? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?
  1986. Luk 5:22 Koma pamene Yesu adadziwa malingaliro awo, iye anayankha, ndipo anati kwa iwo mukusinkhasinkha chiyani m’mitima yanu?
  1987. Luk 5:23 Chapafupi n’chiti, kunena kuti, Machimo ako akhululukidwa kwa iwe; kapena kunena kuti, Tawuka ndipo uyende?
  1988. Luk 5:24 Koma kuti mukhoze kudziwa kuti Mwana wamwamuna wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira machimo, (adati iye kwa wodwala matenda akufa ziwaloyo). Ine ndinena kwa iwe, Tawuka, ndipo utenge kama wako, ndipo umuke kunyumba kwako.
  1989. Luk 5:25 Ndipo posakhalitsa adayimirira pamaso pawo, ndipo anatenga chimene iye adagonapo, ndipo ananyamuka kupita kunyumba kwake, ali kulemekeza Mulungu.
  1990. Luk 5:26 Ndipo iwo onse adazizwa, ndipo iwo adalemekeza Mulungu, ndipo anadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Ife tawona zodabwitsa lero.
  1991. Luk 5:27 ¶Ndipo zitatha zinthu izi iye adatuluka, ndipo anawona munthu wokhometsa msonkho, dzina lake Levi, atakhala pamalo polandirira msonkho: ndipo iye anati kwa iye, Unditsate ine.
  1992. Luk 5:28 Ndipo iye adasiya zonse, nanyamuka, ndipo anamtsata iye.
  1993. Luk 5:29 Ndipo Levi adamkonzera iye phwando lalikulu m’nyumba mwake: ndipo padali khamu lalikulu la a misonkho ndi enanso amene adakhala pansi pamodzi nawo.
  1994. Luk 5:30 Koma Afarisi ndi alembi awo adang’ung’udza kwa wophunzira ake, nanena kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi wochimwa?
  1995. Luk 5:31 Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Iwo amene ali wolimba safuna dotolo; koma iwo amene ali wodwala.
  1996. Luk 5:32 Ine sindinadza kuyitana wolungama, koma wochimwa ku kulapa.
  1997. Luk 5:33 ¶Ndipo iwo adati kwa iye, Chifukwa chiyani wophunzira a Yohane asala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso [wophunzira] a Afarisi; koma anu amangodya ndi kumwa?
  1998. Luk 5:34 Koma iye adati kwa iwo, Mungathe inu kuwapanga ana a ukwati kuti asale, pamene mkwati ali nawo pamodzi?
  1999. Luk 5:35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo kenaka iwo adzasala kudya masiku amenewo.
  2000. Luk 5:36 ¶Ndipo iye adayankhulanso fanizo kwa iwo; Palibe munthu ayika chigamba cha malaya chatsopano nachiphatika pa [malaya] akale; chifukwa ngati atero, pamenepo chatsopanocho chingong’ambitsa, ndipo chigamba chimene [chinatengedwa] kwa atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.
  2001. Luk 5:37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’mabotolo azikopa akale; ngati atero vinyo watsopanoyo adzaphulitsa mabotolo azikopawo, ndipo adzatayika, ndipo mabotolo azikopawo adzawonongeka.
  2002. Luk 5:38 Koma vinyo watsopano ayenera atsanulidwe m’mabotolo azikopa atsopano; ndipo zonse ziwiri zisungika.
  2003. Luk 5:39 Ndipo palibe munthu atamwa [vinyo] wakale nthawi yomweyo afuna watsopano: pakuti iye anena, Wakale ali woposa [watsopano].
  2004. Luk 6:1 Ndipo kudachitika kuti tsiku la sabata yachiwiri itapita yoyamba, kuti iye adalinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo wophunzira ake adabudula ngala za tirigu, nazifikisa [izo] m’manja mwawo, ndipo anadya.
  2005. Luk 6:2 Ndipo ena a Afarisi adati kwa iwo, Muchitiranji chosaloledwa mwachilamulo kuchitika m’masiku a sabata?
  2006. Luk 6:3 Ndipo Yesu poyankha iwo anati, Kodi simunawerenga kotero zambiri zonga izi, chimene adachita Davide, pamene iye mwini adamva njala, ndi iwo amene adali naye pamodzi;
  2007. Luk 6:4 Momwe iye adalowa m’nyumba ya Mulungu, ndipo anatenga ndi kudya mikate yowonetsera, ndipo anapatsanso kwa iwo amene adali pamodzi ndi iye; imeneyi yosaloledwa mwachilamulo kudya koma ansembe wokha?
  2008. Luk 6:5 Ndipo iye adati kwa iwo, Kuti Mwana wamwamuna wa munthu ali Mbuyenso wa tsiku la sabata.
  2009. Luk 6:6 Ndipo kudachitikanso pa tsiku lina lasabata, kuti iye adalowa m’sunagoge ndipo anaphunzitsa: ndipo mudali munthu momwemo amene dzanja lake lamanja lidali lopuwala.
  2010. Luk 6:7 Ndipo alembi ndi Afarisi adamlondalonda iye, ngati adzachiritsa pa tsiku la sabata; kuti akapeze choneneza motsutsa iye.
  2011. Luk 6:8 Koma iye adadziwa maganizo awo, ndipo anati kwa munthuyo wa dzanja lopuwala, Nyamuka, ndipo uyimirire pakatipo. Ndipo iye adanyamuka ndikuyimirira.
  2012. Luk 6:9 Kenaka Yesu adati kwa iwo, Ndikufunsani inu chinthu chimodzi; Kodi kuloleka mwachilamulo pa masiku a sabata kuchita zabwino, kapena kuchita zoyipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuwuwononga [uwo]?
  2013. Luk 6:10 Ndipo pamene adayang’ana mozungulira pa iwo onse, iye adati kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo iye adatero: ndipo dzanja lake lidabwezeretsedwa monga linzake.
  2014. Luk 6:11 Ndipo iwo [adapsa mtima] ndiponso anasokonezeka; ndipo anayankhulana wina ndi mzake zimene akhoza kumchitira Yesu.
  2015. Luk 6:12 Ndipo kudachitika m’masiku amenewo, kuti iye adatuluka napita kuphiri kukapemphera, ndipo anapitiriza usiku wonse m’kupemphera kwa Mulungu.
  2016. Luk 6:13 ¶Ndipo pamene kunacha, iye adayitana [kwa iye] wophunzira ake: ndipo mwa iwo anasankha khumi ndi awiri, amene iye adawatchanso atumwi;
  2017. Luk 6:14 Simoni, (amene iye adamutchanso Petro,) ndi Anduru mbale wake, Yakobo ndi Yohane, Filipi ndi Bartolomeyo,
  2018. Luk 6:15 Mateyu ndi Tomasi, Yakobo mwana [wamwamuna] wa Alifeyasi, ndi Simoni wotchedwa Zelotesi,
  2019. Luk 6:16 Ndi Yudasi [mbale] wa Yakobo, ndi Yudasi Isikariyote, amene adali wompereka.
  2020. Luk 6:17 ¶Ndipo iye adatsika nawo, ndipo anayima pachidikha, ndi gulu la wophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku madera a m’mbali mwa nyanja a Turo ndi Sidoni, amene adadza kudzamva iye, ndi kudzachiritsidwa ku nthenda zawo.
  2021. Luk 6:18 Ndipo iwo amene adavutika ndi mizimu yonyansa: ndipo iwo adachiritsidwa.
  2022. Luk 6:19 Ndipo khamu lonse lidafuna kumkhudza iye: popeza mudatuluka mphamvu mwa iye, ndi kuchiritsidwa [iwo] onse.
  2023. Luk 6:20 ¶Ndipo iye adakweza maso ake kwa wophunzira ake, ndipo ananena kuti, Wodala [muli inu] wosawuka: pakuti uli wanu ufumu wa Mulungu.
  2024. Luk 6:21 Wodala [muli inu] amene mukumva njala tsopano: pakuti mudzakhuta, Wodala [muli inu] amene mulira tsopano: pakuti inu mudzasekerera.
  2025. Luk 6:22 Wodala muli inu, pamene anthu adzada inu, ndi pamene adzapatula inu [ku gulu lawo], ndipo adzatonza [inu], nadzalitaya dzina lanu monga loyipa, chifukwa cha Mwana wamwamuna wa munthu.
  2026. Luk 6:23 Kondwerani inu m’tsiku limenero, ndipo tumphani chifukwa cha chimwemwe: pakuti tawonani, mphotho yanu [ili] yayikulu kumwamba: pakuti mu njira yomweyo makolo awo adawachitira aneneri.
  2027. Luk 6:24 Koma tsoka inu eni chuma! Pakuti mwalandiriratu chosangalatsa chanu.
  2028. Luk 6:25 Tsoka kwa inu amene muli wokhuta! Pakuti inu mudzamva njala. Tsoka kwa inu amene musekerera tsopano! Pakuti mudzachita maliro ndi kulira misozi.
  2029. Luk 6:26 Tsoka kwa inu, pamene anthu onse adzanena zabwino za inu! Pakuti motero adachita makolo awo kwa aneneri wonama.
  2030. Luk 6:27 ¶Koma ndinena kwa inu akumva, Kondani adani anu, chitirani zabwino iwo akuda inu,
  2031. Luk 6:28 Dalitsani iwo amene atemberera inu, ndi kupempherera iwo amene akukugwiritsani inu ntchito monyazitsa.
  2032. Luk 6:29 Ndipo kwa iye amene akupanda iwe pa tsaya [limodzi] umpatsenso linalo; ndi iye amene alanda chofunda chako usamkanize [kuti atenge] malaya akonso.
  2033. Luk 6:30 Patsani kwa munthu aliyense apempha kwa iwe; ndi kwa iye amene alanda zinthu zako usazifunsanso [izo] ayi.
  2034. Luk 6:31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu akuchitireni inu, muchite inunso kwa iwo motero momwemo.
  2035. Luk 6:32 Pakuti ngati muwakonda iwo amene akonda inu, mudzalandira chiyamiko chotani inu? Pakuti wochimwanso akonda iwo amene akonda iwo.
  2036. Luk 6:33 Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani inu? Pakuti wochimwa amachitanso chomwecho.
  2037. Luk 6:34 Ndipo ngati mukongoletsa kanthu [kwa iwo] amene muyembekezera kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani inu? Pakuti wochimwa amakongoletsa wochimwa, kuti alandirenso mochuluka.
  2038. Luk 6:35 Koma kondani adani anu, ndikuchita zabwino, ndipo kongoletsani, osayembekezera kanthu konse; ndipo mphotho yanu idzakhala yayikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba: pakuti iye ali wochitira zokoma osayamika ndi [kwa] woyipa.
  2039. Luk 6:36 Choncho khalani inu a chifundo monga Atate wanunso ali wachifundo.
  2040. Luk 6:37 Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa: musamatsutse ayi, ndipo inu simudzatsutsidwa: khululukirani, ndipo inu mudzakhululukidwa:
  2041. Luk 6:38 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsenderedwa, wokhutchumulidwa, ndi wosefukira, anthu adzakupatsani pa chifuwa chanu. Pakuti ndi muyeso womwewo inu muyesa nawo udzayesedwanso kwa inu.
  2042. Luk 6:39 Ndipo iye adawayankhula fanizo. Kodi wakhungu angatsogolere wakhungu? Kodi iwo sadzagwa onse awiri m’dzenje?
  2043. Luk 6:40 Wophunzira sali pamwamba pa mphunzitsi wake: koma aliyense amene ali wangwiro adzafanana ndi mphunzitsi wake.
  2044. Luk 6:41 Ndipo chifukwa chiyani uyang’ana iwe kafumbi kamene kali m’diso la mbale wako, koma siwuzindikira chipika chimene chili m’diso la iwe mwini?
  2045. Luk 6:42 Kapena iwe ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale, ndilole ndikoke kutulutsa kafumbi kamene kali m’diso lako, pamene iwe mwini wosayang’ana chipika chimene chili m’diso lako lomwe? Wonyenga iwe, chotsa poyamba chipikacho m’diso lako, ndipo kenaka udzayang’anitsitsa bwino kuchotsa kafumbi ka m’diso la mbale wako.
  2046. Luk 6:43 Pakuti mtengo wabwino supatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woyipa supatsa zipatso zabwino.
  2047. Luk 6:44 Pakuti mtengo uliwonse udziwika ndi chipatso chake. Pakuti paminga anthu samatchera nkhuyu, kapena pamtungwi samatchera mphesa.
  2048. Luk 6:45 Munthu wabwino kuchokera m’chuma chokoma cha mtima wake atulutsa chimene chili chabwino; ndi munthu woyipa kuchokera m’chuma choyipa cha mtima wake atulutsa chimene chili choyipa; pakuti mwa kuchuluka kwa mtima wake m’kamwa mwake muyankhula.
  2049. Luk 6:46 ¶Ndipo munditchuliranji ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ine ndizinena?
  2050. Luk 6:47 Aliyense wakudza kwa ine, ndi kumva zonena zanga, ndi kuzichita, ine ndidzakusonyezani kwa amene iye afanana naye:
  2051. Luk 6:48 Iye afanana ndi munthu amene adamanga nyumba, ndipo adakumba pansi mwakuya, ndipo anamanga maziko pa thanthwe: ndipo pamene madzi anasefukira, mtsinje udagunda mwamphamvu pa nyumbayo, ndipo sudakhoza kuyigwedeza iyo: chifukwa idamangidwa pa thanthwe.
  2052. Luk 6:49 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanana ndi munthu amene popanda maziko anamanga nyumba pa nthaka; pa imeneyo mtsinje udagunda mwamphamvu, ndipo posakhalitsa iyo idagwa; ndipo kugwa kwake kwa nyumbayo kudali kwakukulu.
  2053. Luk 7:1 Tsopano pamene adatsiriza zonena zake zonse m’makutu a anthu, iye adalowa m’Kaperenamu.
  2054. Luk 7:2 Ndipo wantchito wina wake wa kenturiyoni, amene adali wokondedwa kwa iye, anadwala, ndipo adali wokonzeka kufa.
  2055. Luk 7:3 Ndipo pamene iye adamva za Yesu, adatuma kwa iye akulu a Ayuda, kumpempha iye kuti adze ndi kuchiritsa wantchito wake.
  2056. Luk 7:4 Ndipo pamene iwo adafika kwa Yesu, adampempha iye mowona mtima, nanena, Kuti iye anali woyenera kwakuti ndi amene anayenera kumchitire ichi:
  2057. Luk 7:5 Pakuti akonda dziko lathu, ndipo adatimangira ife sunagoge.
  2058. Luk 7:6 Kenaka Yesu adapita ndi iwo. Ndipo pamene iye anayandikira kufika tsono pafupi panyumba yake, kenturiyoni adatuma kwa iye abwenzi ake, kunena kwa iye, Ambuye, musadzivute inu nokha: pakuti ine sindiyenera kuti inu mudzalowe pansi pa denga langa:
  2059. Luk 7:7 Mwa ichi ine sindidadziyesera ndekha woyenera kudza kwa inu: koma nenani m’mawu, ndipo wanchito wanga adzachiritsidwa.
  2060. Luk 7:8 Pakuti inenso ndiri munthu woyikidwa pansi pa ulamuliro, ndiri nawo asirikali a pansi pa ine; ndipo ine ndinena kwa wina, Pita, ndipo apita; ndi kwa wina, Idza, ndipo adza; ndipo kwa wanchito wanga, Tachita ichi, ndipo achita.
  2061. Luk 7:9 Pamene Yesu adamva zinthu zimenezi, adazizwa naye, ndipo anapotoloka, ndipo ananena kwa anthu amene adali kumutsata iye, Ine ndinena kwa inu, sindidapeze chikhulupiriro chachikulu chotere, ayi, osati mu Israyeli.
  2062. Luk 7:10 Ndipo iwo wotumidwawo, pakubwera kunyumba, adapeza wantchitoyo atachira ndithu yemwe adali nkudwala.
  2063. Luk 7:11 ¶Ndipo kudachitika litapita tsiku ili, kuti iye adapita kumzinda dzina lake Nayini; ndipo ambiri a wophunzira ake adapita naye ndi anthu ambiri.
  2064. Luk 7:12 Ndipo pamene adayandikira ku chipata cha mzindawo, tawonani, pamenepo padali munthu wakufa wonyamulidwa, mwana wamwamuna m’modzi yekha wa amayi wake, ndipo adali mkazi wamasiye: ndipo anthu ambiri a mumzindawo adali pamodzi naye.
  2065. Luk 7:13 Ndipo pamene Ambuye adamuwona iye, adagwidwa ndi chifundo pa iye, ndipo ananena kwa iye, Usalire ayi.
  2066. Luk 7:14 Ndipo iye adayandikira nakhudza chithatha: ndipo iwo amene womunyamula [iye] adayima. Ndipo iye adati, Mnyamata iwe, ndinena kwa iwe, Tawuka.
  2067. Luk 7:15 Ndipo iye amene adali wakufayo adakhala tsonga, ndipo anayamba kuyankhula. Ndipo iye adampereka kwa amayi wake.
  2068. Luk 7:16 Ndipo panadza mantha pa onsewo: ndipo onse adalemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wawuka pakati pa ife; ndipo, Kuti Mulungu wayendera anthu ake.
  2069. Luk 7:17 Ndipo mbiri yake imeneyi inabuka ku Yudeya konse, ndi ku dziko lonse lozungulira.
  2070. Luk 7:18 Ndipo wophunzira a Yohane adamuwuza iye za zinthu izi zonse.
  2071. Luk 7:19 ¶Ndipo Yohane adayitana [kwa iye] awiri a wophunzira ake nawatuma [iwo] kwa Yesu, nanena kuti, Kodi ndinu amene munayenera kudzayo? Kapena tiyang’anire wina?
  2072. Luk 7:20 Pamene anthuwo adafika kwa iye, iwo adati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa inu, kunena kuti, Kodi ndinu amene munayenera kudzayo? Kapena tiyang’anire wina?
  2073. Luk 7:21 Ndipo nthawi yomweyo iye adachiritsa ambiri zofowoka [zawo] ndi miliri, ndi ku mizimu yoyipa; ndi kwa ambiri amene anali akhungu anawapenyetsanso.
  2074. Luk 7:22 Kenaka Yesu adayankha nati kwa iwo, Pitani pa njira yanu, ndipo muwuze Yohane zimene mwaziwona ndi kuzimva; m’mene anthu akhungu alandirira kuwona, wolumala miyendo akuyenda, akhate ayeretsedwa, wogontha akumva, akufa awukitsidwa, kwa aumphawi uthenga wabwino walalikidwa.
  2075. Luk 7:23 Ndipo wodala [ali] iye, yense amene sakhumudwa mwa ine.
  2076. Luk 7:24 ¶Ndipo amithenga ake a Yohane atanyamuka, iye adayamba kulankhula kwa anthu zokhudzana ndi Yohane, Kodi mudatuluka kupita kuchipululu kukawona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?
  2077. Luk 7:25 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Tawonani, iwo wovala zolemera, ndi wokhala modyerera, ali m’mabwalo a mafumu.
  2078. Luk 7:26 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Mneneri kodi? Eya, ine ndinena kwa inu, ndipo woposa mneneri.
  2079. Luk 7:27 Uyu ndi [iye] uja, amene za iye zidalembedwa, Tawona, ine ndituma mthenga wanga akutsogolere, amene adzakonzera njira yako pamaso pako.
  2080. Luk 7:28 Pakuti ine ndinena kwa inu, Mwa iwo wobadwa mwa akazi palibe m’modzi mneneri wamkulu woposa Yohane Mbatizi: koma iye amene ali wamng’ono mu ufumu wa Mulungu ali wamkulu kumposa iye.
  2081. Luk 7:29 Ndipo anthu onse amene adamva [iye], ndi wokhometsa misonkho, adavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza adabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.
  2082. Luk 7:30 Koma Afarisi ndi achilamulo adakana uphungu wa Mulungu kwa iwo wokha, posabatizidwa ndi iye.
  2083. Luk 7:31 ¶Ndipo Ambuye adati, Ndidzafanizira ndi chiyani tsono anthu a m’badwo uwu? Ndipo afanana ndi chiyani?
  2084. Luk 7:32 Iwo ali ofanana ndi ana wokhala mu msika, ndi kuyitanizana wina ndi mzake, ndi kunena kuti, Ife tidalizira kwa inu chitoliro, ndipo inu simudavine ayi; ife tinabuma maliro kwa inu, ndipo inu simudalire ayi.
  2085. Luk 7:33 Pakuti Yohane Mbatizi adafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo inu munena, Ali ndi chiwanda.
  2086. Luk 7:34 Mwana wamwamuna wa munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo inu munena, Tawonani, munthu wadyera, ndi kumwayimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu wochimwa!
  2087. Luk 7:35 Koma nzeru ilungamitsidwa ndi ana ake onse.
  2088. Luk 7:36 ¶Ndipo m’modzi wa Afarisi adakhumba iye kuti akadye naye. Ndipo iye adalowa m’nyumba ya Mfarisi, ndipo anakhala pansi kuseyama pa chakudya.
  2089. Luk 7:37 Ndipo, tawonani, mkazi wa mu mzindamo, amene adali wochimwa, pamene adadziwa kuti [Yesu] adali kuseyama pa chakudya m’nyumba ya Mfarisi, adabwera nayo nsupa ya alabastara ya mafuta wonunkhira bwino.
  2090. Luk 7:38 Ndipo adayimirira pa mapazi ake kumbuyo [kwake] alikulira, ndipo anayamba kusambitsa mapazi ake ndi misozi, ndipo anawapukuta [iwo] ndi tsitsi la kumutu kwake, ndipo anapsopsona mapazi ake, ndipo anawadzoza ndi mafutawo.
  2091. Luk 7:39 Tsopano Mfarisi amene adamuyitana iye adawona [ichi], iye adanena mwa iye yekha, nanena kuti, Munthu uyu, ngati akadakhala kuti ali mneneri, akadadziwa ali yani ndi kuti mkaziyo ali wotani amene anamkhudza iye: pakuti ali wochimwa.
  2092. Luk 7:40 Ndipo Yesu adayankha nanena kwa iye, Simoni, ine ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye adati, Ambuye, nenani.
  2093. Luk 7:41 Padali wokongoletsa ndalama wina amene adali nawo angongole awiri: m’modziyo adali ndi ngongole yake ya makobiri mazana asanu, ndi winayo makumi asanu.
  2094. Luk 7:42 Ndipo pamene adalibe chobwezera, iye adawakhululukira mwa ulere onse awiri. Choncho tandiwuza, ndi ndani wa iwo adzakonda koposa?
  2095. Luk 7:43 Simoni adayankha ndipo anati, Ndiyesa kuti [iye], kwa amene adamkhululukira zoposa. Ndipo adanena kwa iye, Iwe wayankha molondola.
  2096. Luk 7:44 Ndipo iye adachewukira kwa mkaziyo, ndipo anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ine ndidalowa m’nyumba yako, iwe sudandipatse madzi a mapazi anga: koma iye wasambitsa mapazi anga ndi misozi ndi kuwapukuta [iwo] ndi tsitsi la kumutu kwake.
  2097. Luk 7:45 Iwe sudandipsopsone ine: koma mkazi uyu kuyambira nthawi yomwe ine ndalowa sadaleka kupsopsona mapazi anga.
  2098. Luk 7:46 Mutu wanga iwe sudawudzoza ndi mafuta; koma mkazi uyu wadzoza mapazi anga ndi mafuta.
  2099. Luk 7:47 Mwa ichi ine ndinena kwa iwe, Machimo ake, amene ali ambiri, akhululukidwa; pakuti adakonda kwambiri: koma kwa iye yemwe wakhululukidwa pang’ono, [yemweyo] akonda pang’ono.
  2100. Luk 7:48 Ndipo adati kwa [mkaziyo], Machimo ako akhululukidwa.
  2101. Luk 7:49 Ndipo iwo amene adakhala kuseyama pa chakudya ndi iye adayamba kunena mwa iwo wokha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?
  2102. Luk 7:50 Ndipo iye adati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; pita mu mtendere.
  2103. Luk 8:1 Ndipo kudachitika pambuyo pake, kuti iye adayendayenda ku mzinda ndi ku mudzi uliwonse, kulalikira ndi kuwawuza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu: ndi khumi ndi awiriwo [anali] pamodzi naye,
  2104. Luk 8:2 Ndi akazi ena, amene adachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi nthenda, Mariya wotchedwa Mmagidalene, amene zidatuluka mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri,
  2105. Luk 8:3 Ndi Jowana mkazi wake wa Kuza kapitawo wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene adatumikira iye ndi chuma chawo.
  2106. Luk 8:4 ¶Ndipo pamene anthu ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo adadza kwa iye wochokera ku mzinda uliwonse, iye adayankhula mwa fanizo:
  2107. Luk 8:5 Wofesa adatuluka kukafesa mbewu zake: ndipo pamene adali kufesa, zina zinagwera m’mbali mwa njira; ndipo zidapondedwa, ndi mbalame za mu mlengalenga zidadya iyo.
  2108. Luk 8:6 Ndipo yina yidagwera pathanthwe; ndipo itangomera, idafota, chifukwa idalibe m’nyontho.
  2109. Luk 8:7 Ndipo yina yidagwa pakati pa minga; ndi mingayo idaphuka pamodzi nayo, ndipo inayitsamwitsa.
  2110. Luk 8:8 Ndipo yina yidagwa pa nthaka yabwino, ndipo zidamera, ndipo idapatsa chipatso chochulukitsa ndi zana. Ndipo pamene ananena iye zinthu izi, iye adafuwula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.
  2111. Luk 8:9 Ndipo wophunzira ake adamfunsa iye, kunena kuti, Kodi fanizo ili likhoza kukhala lotani?
  2112. Luk 8:10 Ndipo iye adati, Kwa inu kwapatsidwa kuzindikira zinsinsi za ufumu wa Mulungu: koma kwa ena m’mafanizo; kuti pakuwona iwo asakhoze kuwona, ndi pakumva iwo asakhoze kumva.
  2113. Luk 8:11 Tsopano fanizolo ndi ili: Mbewu ndiyo mawu a Mulungu.
  2114. Luk 8:12 Iyo ya m’mbali mwa njira ndiwo amene amamva; kenaka akudza mdierekezi, ndipo achotsa mawu m’mitima yawo, kuti mwina angakhulupirire ndi kupulumutsidwa.
  2115. Luk 8:13 Iyo ya pathanthwe [ndiwo], amene, pamene akumva, alandira mawu ndi chimwemwe; ndipo awa alibe muzu, amene akhulupirira kwa kanthawi, ndipo mu nthawi ya mayesero amagwa.
  2116. Luk 8:14 Ndipo yija imene zidagwa pakati pa mingazi ndiwo, amene, pamene atamva, apita kwawo, ndipo atsamwitsidwa ndi nkhawa ndi chuma ndi zokondweretsa za moyo [uno], ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.
  2117. Luk 8:15 Koma yija ya panthaka yabwino ndiwo, amene mu mtima wowona ndi wabwino, atamva mawu, awasunga [iwo], ndipo abala chipatso mwa chipiriro.
  2118. Luk 8:16 ¶Palibe munthu, pamene iye atayatsa nyali, ayivundikira ndi chotengera, kapena kuyiyika [iyo] pansi pa kama; koma ayiyika pa choyikapo chake, kuti iwo amene alowamo akhoze kuwona kuwalako.
  2119. Luk 8:17 Pakuti palibe chobisika, chimene sichidzawonetsedwa; kapena [china chilichonse] chobisidwa, chimene sichidzadziwika ndi kufalitsidwa.
  2120. Luk 8:18 Choncho samalirani momwe inu mumvera: pakuti kwa iye amene ali nacho, kwa iye kudzapatsidwa; ndipo amene alibe, kwa iye chidzachotsedwa chingakhale chimene awoneka ngati ali nacho.
  2121. Luk 8:19 ¶Kenaka adadza kwa iye amayi [ake] ndi abale ake, ndipo sadathe kufika kwa iye chifukwa cha khamu la anthu.
  2122. Luk 8:20 Ndipo adamuwuza iye ndi [ena] amene adati, Amayi anu ndi abale anu ayima kunja, akufuna kuwona inu.
  2123. Luk 8:21 Ndipo iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Amayi anga ndi abale anga ndi awa amene akumva mawu a Mulungu, ndi kuwachita.
  2124. Luk 8:22 ¶Tsopano zidachitika pa tsiku lina, kuti iye adalowa m’chombo ndi wophunzira ake: ndipo anati kwa iwo, Tiyeni tiwolokere ku tsidya lina la nyanja. Ndipo adanyamuka kupita.
  2125. Luk 8:23 Ndipo m’mene iwo adali kupita pamadzi iye adagona tulo: ndipo padatsikira namondwe wa mphepo pa nyanja; ndipo iwo anadzazidwa [ndi madzi], ndipo adali pa chiwopsezo.
  2126. Luk 8:24 Ndipo iwo adadza kwa iye, ndipo anamudzutsa iye, nanena kuti, Ambuye, ambuye, ife tiwonongeka. Kenaka iye adadzuka, ndipo anadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi: ndipo zidaleka, ndipo padagwa bata.
  2127. Luk 8:25 Ndipo iye adati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo iwo m’kuchita mantha adazizwa, nanena wina kwa mzake. Munthu uyu ndi wotani! Pakuti alamula ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimvera iye.
  2128. Luk 8:26 ¶Ndipo iwo adafika ku dziko la Agadala, limene liri lopenyana ndi Galileya.
  2129. Luk 8:27 Ndipo pamene iye adatuluka nafika pamtunda, adakomana naye mwamuna wina kunja kwa mzinda, amene adali nazo ziwanda kwa nthawi yayitali, ndipo samavala zovala, kapena kukhala m’nyumba [ina] iliyonse, koma mkati mwa manda.
  2130. Luk 8:28 Pamene adamuwona Yesu, iye adafuwula, ndipo anagwa pansi pamaso pake, ndipo ndi mawu wokwera anati, Ndiri nacho chiyani ndi inu, Yesu, [inu] Mwana wamwamuna wa Mulungu Wam’mwambamwamba? Ndikupemphani inu, musandizunze ine ayi.
  2131. Luk 8:29 (Pakuti iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri umam’ngwira iye: ndipo amasungidwa womangidwa ndi unyolo ndi malamba achitsulo; ndipo adadula zomangazo, ndipo anatengedwa ndi woyipayo kupita kuchipululu.)
  2132. Luk 8:30 Ndipo Yesu adamfunsa iye, kunena kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo iye adati, Legiyoni: chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.
  2133. Luk 8:31 Ndipo zidampempha iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa kwakuya.
  2134. Luk 8:32 Ndipo pamenepo padali gulu la nkhumba zambiri zimadya m’phiri: ndipo zidapempha iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo iye adazilola.
  2135. Luk 8:33 Kenaka ziwandazo zidatuluka mwa munthuyo, ndipo zinalowa mu nkhumba: ndipo gululo lidatsika mwachiwawa pamalo potsetsereka kulowa m’nyanjamo, ndipo zidatsamwitsidwa.
  2136. Luk 8:34 Pamene iwo woweta [izo] m’mene adawona chimene chidachitika, adathawa, ndipo anawuza [ichi] a mu mzinda ndi a m’mudzi.
  2137. Luk 8:35 Kenaka iwo adatuluka kukawona chimene chidachitika; ndipo adadza kwa Yesu, ndipo anampeza munthuyo, amene mwa iye ziwanda zidatuluka, atakhala pansi pa mapazi a Yesu, wovala, ndi woganiza bwinobwino: ndipo iwo adawopa.
  2138. Luk 8:36 Iwonso amene adawona [ichi] adawawuza za momwe adali machiritsidwe ake a wogwidwa ndi ziwandayo.
  2139. Luk 8:37 ¶Kenaka khamu lonse la dziko lonse la Agerasa lozungulira lidampempha iye achoke kwa iwo; pakuti adagwidwa ndi mantha akulu: ndipo iye adapita kulowa m’chombo nabwereranso.
  2140. Luk 8:38 Tsopano munthu amene ziwanda zidatuluka mwa iye adampempha iye akhoze kukhala ndi iye: koma Yesu adamuwuza kuti apite, nanena kuti,
  2141. Luk 8:39 Bwerera kunyumba kwako, ndipo ukafotokoze zinthu zazikuluzo Mulungu adakuchitira iwe. Ndipo iye adapita pa njira yake, ndipo analalikira ku mzinda wonse momwe Yesu adamchitira iye zinthu zazikuluzo.
  2142. Luk 8:40 Ndipo kudachitika, kuti, pamene Yesu anabwerera, anthu adamulandira iye [mokondwera]: pakuti onse adali kumuyembekezera iye.
  2143. Luk 8:41 ¶Ndipo, tawonani, panadza munthu dzina lake Jayirasi, ndipo iye ndiye wolamula wa sunagoge: ndipo adagwa pamapazi ake a Yesu, ndipo anampempha iye adze ku nyumba kwake;
  2144. Luk 8:42 Pakuti adali naye mwana wamkazi m’modzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo adali atagona ali pafupi kumwalira iye. Koma pakupita iye anthu adamkanikiza iye.
  2145. Luk 8:43 ¶Ndipo mkazi wokhala nayo nthenda yotaya mwazi zaka khumi ndi ziwiri, amene adalipira kwa a dotolo za moyo wake zonse, ndipo sadathe kuchiritsidwa ndi m’modzi yense,
  2146. Luk 8:44 Anadza pambuyo [pake], ndipo anakhudza mphonje ya chovala chake: ndipo posakhalitsa nthenda idaleka.
  2147. Luk 8:45 Ndipo Yesu adati, Wandikhudza ine ndani? Pamene onse adakana, Petro ndi iwo adali naye adati, Ambuye, khamu likukankhana pa inu ndi kukanikiza [inu], ndipo inu munena kuti, Ndani wandikhudza ine?
  2148. Luk 8:46 Ndipo Yesu adati, Wina wandikhudza ine: pakuti ndazindikira ine kuti mphamvu yatuluka mwa ine.
  2149. Luk 8:47 Ndipo pamene mkaziyo adawona kuti sakadabisika, anadza ali kunthunthumira, ndipo anagwa pamaso pake, iye anafotokoza kwa iye pamaso pa anthu onsewo chifukwa chimene anamkhudzira iye, ndi momwe adachiritsidwira mosakhalitsa.
  2150. Luk 8:48 Ndipo iye adati kwa iyeyu, Mwana wamkaziwe, khala wolimba mtima: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; pita mu mtendere.
  2151. Luk 8:49 ¶Akadali iye chiyankhulire, anadza wina wochokera [kunyumba] kwa wolamulira wa sunagoge, nanena kwa iye, Mwana wako wamkazi wafa; usamvute Mphunzitsi.
  2152. Luk 8:50 Koma pamene Yesu adamva [izi], adamuyankha iye, kunena kuti, Usawope: khulupirira kokha, ndipo iye adzachiritsidwa.
  2153. Luk 8:51 Ndipo pamene iye adafika kunyumbako, sadaloleza munthu wina aliyense kulowa, kupatula Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate ndi amayi wake a buthulo.
  2154. Luk 8:52 Ndipo onse adalira, ndipo adamlirira iye: koma iye adati, Musalire ayi; iye sadafe, koma wagona tulo.
  2155. Luk 8:53 Ndipo adamseka iye pwepwete, podziwa kuti adafa.
  2156. Luk 8:54 Ndipo iye adawatulutsa onse kubwalo, ndipo anamgwira iye pa dzanja, ndipo anayitana, nanena kuti, Buthu, tawuka.
  2157. Luk 8:55 Ndipo mzimu wake udabweranso, ndipo adawuka pomwepo: ndipo iye adalamulira kuti ampatse iye chakudya.
  2158. Luk 8:56 Ndipo makolo ake anadabwa: ndipo iye adalamulira iwo kuti asawuze munthu aliyense chimene chidachitika.
  2159. Luk 9:1 Kenaka iye adayitana pamodzi khumi ndi awiriwo, ndipo anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.
  2160. Luk 9:2 Ndipo adawatuma kukalalikira ufumu wa Mulungu, ndi kuti achiritse matenda.
  2161. Luk 9:3 Ndipo iye adati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka pa ulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nawo malaya awiri.
  2162. Luk 9:4 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowemo, khalani m’menemo, ndipo muzikachokera kumeneko.
  2163. Luk 9:5 Ndipo onse amene sadzalandira inu, m’mene mutuluka mzinda umenewo, sansani fumbi ku mapazi anu likhale umboni wakutsutsa iwo.
  2164. Luk 9:6 Ndipo iwo adatuluka, ndipo anapita kudutsa m’mizinda, kulalikira uthenga wabwino, ndi kuchiritsa paliponse.
  2165. Luk 9:7 ¶Tsopano Herode mfumu yolamulira gawo limodzi la anayi adamva mbiri yake ya zonse zidachitika ndi iye: ndipo iye anathedwa nzeru, chifukwa chakuti kudanenedwa ndi ena, kuti Yohane adawuka kwa akufa;
  2166. Luk 9:8 Ndipo kwa ena, kuti Eliya adawoneka; ndipo kwa ena, kuti m’modzi wa aneneri akale aja adawuka.
  2167. Luk 9:9 Ndipo Herode adati, Yohane ndidamdula mutu ine: koma uyu ndani, amene ndikumva zotere za iye? Ndipo adakhumba kumuwona iye.
  2168. Luk 9:10 ¶Ndipo atumwiwo, pamene atabwerera, adamfotokozera iye zonse zimene iwo adazichita. Ndipo iye adawatenga, ndipo anapita nawo pa wokha kunka ku malo a chipululu cha mchenga a ku mzinda dzina lake Betsayida.
  2169. Luk 9:11 Ndipo anthu, pamene adadziwa [izi], adamtsata iye: ndipo iye adawalandira iwo, ndipo anayankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndipo anachiritsa amene adasowa kuchiritsidwa.
  2170. Luk 9:12 Ndipo pamene tsiku linapita kumapeto, pamenepo anadza khumi ndi awiriwo, ndipo anati kwa iye, Tawuzani khamu limuke, kuti iwo apite ku mizinda ndi dziko lozungulira, ndi kugona, ndi kupeza zakudya: chifukwa tiri kuno ku malo a chipululu cha mchenga.
  2171. Luk 9:13 Koma iye adati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Ndipo iwo adati, ife tiribe mikate yochuluka koma isanu yokha ndi nsomba ziwiri zokha; pokhapo timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.
  2172. Luk 9:14 Pakuti adali amuna pafupifupi zikwi zisanu. Ndipo iye adati kwa wophunzira ake, Khalitsani iwo pansi m’magulu, a makumi asanu asanu.
  2173. Luk 9:15 Ndipo adatero, nawakhalitsa pansi onsewo.
  2174. Luk 9:16 Kenaka iye m’mene adatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri, ndipo adayang’ana kumwamba, iye anazidalitsa, ndi kunyema, ndipo anapatsa wophunzira apereke kwa makamuwo.
  2175. Luk 9:17 Ndipo iwo anadya, ndipo anakhuta onsewo: ndipo panatoledwa makombo kwa iwo mitanga khumi ndi iwiri.
  2176. Luk 9:18 ¶Ndipo kudachitika, pamene iye adali payekha kupemphera wophunzira adali naye: ndipo iye adawafunsa iwo, kunena kuti, Anthu anena kuti ine ndine yani?
  2177. Luk 9:19 Iwo adayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena [ati], Eliya; ndi ena [ati], kuti m’modzi wa aneneri akale adawuka.
  2178. Luk 9:20 Iye adati kwa iwo, koma inu munena kuti ine ndine yani? Petro adayankha nati, Khristu wa Mulungu.
  2179. Luk 9:21 Ndipo iye adawawuzitsa iwo, nawalamulira [iwo] kuti asanene kwa munthu aliyense chinthu ichi.
  2180. Luk 9:22 Nanena kuti, Mwana wamwamuna wa munthu ayenera kuti amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu ndi ansembe akulu ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuwukitsidwa tsiku la chitatu.
  2181. Luk 9:23 ¶Ndipo iye adanena kwa [iwo] onse, Ngati [munthu] afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, ndipo anyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, ndipo anditsate ine.
  2182. Luk 9:24 Pakuti aliyense amene adzapulumutsa moyo wake adzawutaya: koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha ine, yemweyo adzawupulumutsa.
  2183. Luk 9:25 Pakuti munthu adzapindulanji, akadzilemeretsa dziko lonse lapansi, nadziwononga iye mwini, kapena kudzitaya kunja?
  2184. Luk 9:26 Pakuti aliyense amene adzachita manyazi chifukwa cha ine ndi mawu anga, kwa iye Mwana wamwamuna wa munthu adzachita manyazi, pamene iye adzafika mu ulemerero wake, ndi [mwa Atate ake], ndi wa angelo woyera.
  2185. Luk 9:27 Koma ine ndinena ndi inu za zowonadi, pali ena a iwo ayima pano, amene sadzalawa imfa, kufikira kuti adzawona ufumu wa Mulungu.
  2186. Luk 9:28 ¶Ndipo padachitika pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu pambuyo pa zonena izi, iye adatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo, ndipo adapita nawo kukwera m’phiri kukapemphera.
  2187. Luk 9:29 Ndipo pamene anali kupemphera, mawonekedwe a nkhope yake adasandulidwa, ndipo chovala chake [chidali] choyera [ndi] chonyezimira.
  2188. Luk 9:30 Ndipo, tawonani, adalikuyankhulana naye amuna awiri, amene anali Mose ndi Eliya:
  2189. Luk 9:31 Amene adawonekera mu ulemerero, ndipo ananena za imfa yake imene iye ayenera kukwaniritsa ku Yerusalemu.
  2190. Luk 9:32 Koma Petro ndi iwo adali naye adalemedwa ndi tulo: ndipo pamene iwo adadzuka, adawona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo amene adayima ndi iye.
  2191. Luk 9:33 Ndipo panachitika, pamene amachoka kwa iye aja, Petro adati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tikhale pano: ndipo tiyeni timange mahema atatu; imodzi ya inu, ndi imodzi ya Mose, ndi imodzi ya Eliya; wosadziwa chimene iye adalikunena.
  2192. Luk 9:34 Pamene anali chiyankhulire, panadza mtambo, ndipo unawaphimba iwo: ndipo anachita mantha pakulowa iwo mumtambowo.
  2193. Luk 9:35 Ndipo mudatuluka mawu mu mtambo, kunena kuti, Uyu ndi Mwana wanga wamwamuna wokondedwa: mverani iye.
  2194. Luk 9:36 Ndipo pakutha mawuwo, Yesu adapezeka ali yekha. Ndipo iwo adasunga ichi osawulula, ndipo sadawuza munthu aliyense masiku aja za chimodzi cha zinthu izo zimene iwo adaziwona.
  2195. Luk 9:37 ¶Ndipo panachitika, tsiku lotsatira, atatsika m’phiri, anthu ambiri adakomana naye.
  2196. Luk 9:38 Ndipo, tawonani, munthu wa gululo adafuwula, nanena kuti, Mbuye, ine ndikupemphani yang’anani pa mwana wanga wamwamuna: pakuti iye ndiye yekhayo wa ine;
  2197. Luk 9:39 Ndipo, onani, mzimu umamgwira iye, ndipo mwadzidzidzi amafuwula; ndipo umam’ng’amba kwakuti iye amachitanso thovu [pakamwa], ndi kumuvulaza iye osachoka mwa iye.
  2198. Luk 9:40 Ndipo ndawapempha wophunzira anu kuti awutulutse; ndipo iwo sadathe ayi.
  2199. Luk 9:41 Ndipo Yesu adayankha nanena kuti, Mbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wokhotakhota, ndidzakhala ndi inu nthawi yayitali bwanji, ndikulekerera inu? Mbweretse kuno mwana wako wamwamuna.
  2200. Luk 9:42 Ndipo pamene iye adalinkudza, chiwandacho chidam’gwetsa pansi, ndi kumung’amba [iye]. Ndipo Yesu adadzudzula mzimu wonyansawo, ndipo anachiritsa mwanayo, ndipo anam’bwezera iye kwa atate wake.
  2201. Luk 9:43 ¶Ndipo onse anadabwa ndi mphamvu yayikulu ya Mulungu. Koma pamene aliyense adalikuzizwa pa zinthu zonse zimene Yesu adazichita, iye adati kwa wophunzira ake,
  2202. Luk 9:44 Lolani zonena izi zilowe pansi m’makutu anu: pakuti Mwana wamwamuna wa munthu adzaperekedwa m’manja a anthu.
  2203. Luk 9:45 Koma iwo sadamvetsetsa chonena ichi, ndipo chinabisidwa kwa iwo, kotero kuti iwo sadachizindikire ayi: ndipo iwo adawopa kumfunsa za chonenedwacho.
  2204. Luk 9:46 ¶Kenaka adayamba kufunsana maganizo mwa iwo wokha, kuti ndani wa iwo amene ayenera kukhala wamkulu kwambiri.
  2205. Luk 9:47 Koma Yesu, pakuzindikira kulingalira kwa mtima wawo, adatenga kamwana, ndipo anakayimika pambali pake,
  2206. Luk 9:48 Ndipo iye adati kwa iwo, Aliyense amene adzalandira kamwana aka m’dzina langa alandira ine: ndipo amene aliyense andilandira ine alandira iye amene adandituma ine: pakuti iye wakukhala wamng’onong’ono wa inu nonse, yemweyu ndiye adzakhala wamkulu.
  2207. Luk 9:49 ¶Ndipo Yohane adayankha ndipo anati, Ambuye, ife tidawona wina ali kutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tidamletsa iye, chifukwa sadatsatana pamodzi ndi ife.
  2208. Luk 9:50 Ndipo Yesu adati kwa iye, Musamletse [iye] ayi, pakuti iye amene satsutsana nafe athandizana nafe.
  2209. Luk 9:51 ¶Ndipo padachitika, pamene nthawi idafika yakuti iye alandiridwe kumwamba, iye adatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu.
  2210. Luk 9:52 Ndipo adatumiza a mithenga patsogolo pake: ndipo iwo adamka, ndipo analowa m’mudzi wa Asamariya, kukamkonzera iye.
  2211. Luk 9:53 Ndipo iwo sadamlandire iye, chifukwa nkhope yake idali yowoneka ngati ayenera kunka ku Yerusalemu.
  2212. Luk 9:54 Ndipo pamene wophunzira ake Yakobo ndi Yohane adawona [izi], iwo adati, Ambuye, kodi mufuna kuti ife tiwuze moto utsike kumwamba, ndi kuwanyeketsa iwo, monga Eliya adachitira?
  2213. Luk 9:55 Koma iye adatembenuka, ndipo anawadzudzula iwo, ndipo anati, Inu simukudziwa za mtundu wa mzimu umene inu muli.
  2214. Luk 9:56 Pakuti Mwana wamwamuna wa munthu sadadza kudzawononga miyoyo ya anthu, koma kuwapulumutsa [iwo]. Ndipo adapita kumudzi wina.
  2215. Luk 9:57 ¶Ndipo kudachitika, kuti, m’mene iwo adalikuyenda m’njira, [munthu] wina adati kwa iye, Ambuye, Ine ndidzakutsatani inu kumene kulikonse kumene mupitako.
  2216. Luk 9:58 Ndipo Yesu adati kwa iye, Nkhandwe ziri nawo mayenje, ndi mbalame za mlengalenga [ziri nazo] zisa; koma Mwana wamwamuna wa munthu alibe pogoneka mutu wake.
  2217. Luk 9:59 Ndipo adati kwa wina, Unditsate ine, Koma iye adati, Ambuye, mundilole ine; choyamba ndiyambe ndapita kukayika maliro a atate wanga.
  2218. Luk 9:60 Koma Yesu adati kwa iye, Leka akufa ayike akufa awo: koma muka iwe ndi kukalalikira ufumu wa Mulungu.
  2219. Luk 9:61 Ndipo winanso adati, Ambuye ndidzakutsatani inu; koma muyambe mwandilola kulawirana nawo, amene ali kwathu kunyumba kwanga.
  2220. Luk 9:62 Ndipo Yesu adati kwa iye, Palibe munthu, atagwira chikhasu, nayang’ana kumbuyo, ali woyenera ufumu wa Mulungu.
  2221. Luk 10:1 Zitatha izi Ambuye adasankha enanso makumi asanu ndi awiri, ndipo anawatuma iwo awiri awiri pamaso pake ku mzinda uliwonse, ndi malo aliwonse, kumene ati afikeko mwini yekha.
  2222. Luk 10:2 Choncho iye adanena kwa iwo, Zokolola zowona zachulukadi, koma antchito ali wochepa: choncho pempherani kwa Mbuye wa zokolola, kuti iye atumize antchito ku kholola lake.
  2223. Luk 10:3 Mukani njira zanu: tawonani, ine ndituma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu.
  2224. Luk 10:4 Musanyamula thumba la ndalama, kapena thumba la kamba, kapena nsapato: ndipo musayankhule munthu panjira.
  2225. Luk 10:5 Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowamo, muyambe mwanena, Mtendere [ukhale] pa nyumba iyi.
  2226. Luk 10:6 Ndipo ngati mwana wamwamuna wa mtendere ali m’menemo, mtendere wanu udzapumula pa iyo: ngati mulibe, udzabwereranso kwa inu.
  2227. Luk 10:7 Ndipo m’nyumba yomweyo khalani, ndi kudya ndi kumwa zinthu zotero monga akupatsani: pakuti wantchito ayenera kulandira mphotho yake. Musamachoka nyumba ina kupita m’nyumba ina.
  2228. Luk 10:8 Ndipo mumzinda uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zinthu zotero monga iwo akupatsani:
  2229. Luk 10:9 Ndipo chiritsani wodwala amene ali momwemo, ndipo munene kwa iwo, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.
  2230. Luk 10:10 Koma kumzinda uli wonse mukalowako, ndipo iwo salandira inu, pitani kunjira za kumakwalala ake a kumeneko ndi kunena kuti,
  2231. Luk 10:11 Lingakhale fumbi la kumzinda kwanu, limene limamatika pa ife, tirisansira motsutsana ndi inu: ngakhale ziri choncho tsimikizikani za ichi, kuti ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.
  2232. Luk 10:12 Koma ine ndinena kwa inu, kuti kudzapiririka tsiku lijalo kwa Sodomu, kuposa mzinda umenewo.
  2233. Luk 10:13 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Pakuti ntchito zamphamvu zimene zidachitika m’Turo ndi Sidoni zimene zachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe, ndi kukhala pansi wovala chiguduli ndi phulusa.
  2234. Luk 10:14 Koma kudzakhala kopiririka kwa Turo ndi ku Sidoni pachiweruziro, koposa inu.
  2235. Luk 10:15 Ndipo iwe, Kaperenamu, amene wakwezedwa kufikira kumwamba, udzatsitsidwa kufikira ku nyanja ya moto.
  2236. Luk 10:16 Iye amene amvera inu andimvera ine; ndipo iye amene anyoza inu andinyoza ine; ndipo iye amene wonyoza ine am’nyoza iye amene adandituma ine.
  2237. Luk 10:17 ¶Ndipo makumi asanu ndi awiriwo anabwerera mokondwera, nanena kuti, Ambuye, ngakhale ziwanda zigonjera kwa ife kudzera m’dzina lanu.
  2238. Luk 10:18 Ndipo iye adati kwa iwo, Ine ndidawona Satana alinkugwa ngati mphezi kuchokera kumwamba.
  2239. Luk 10:19 Tawonani, ine ndakupatsani inu mphamvu yoponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo: ndipo kulibe kanthu kadzakupwetekani mwanjira iliyonse.
  2240. Luk 10:20 Posasamalira mu izi musakondwera nako, kuti mizimu ikugonjerani inu; koma makamaka kondwerani, chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.
  2241. Luk 10:21 ¶Mu ora limenero Yesu adakondwera mu mzimu, ndipo anati, Ndiyamika inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira zinthu izi kwa anzeru ndi wosamalitsa machitidwe awo, ndipo mwaziwululira izo kwa ana amakanda: ngakhale choncho, Atate; pakuti kotero kudawoneka kwabwino m’kuwona kwanu.
  2242. Luk 10:22 Zinthu zonse zaperekedwa kwa ine ndi Atate wanga: ndipo palibe munthu azindikira Mwana wamwamuna ali yani, koma Atate; ndi kwa [iye] amene Mwana wamwamuna afuna kumuwululira [iye].
  2243. Luk 10:23 ¶Ndipo iye adatembenukira kwa ophunzira [ake], ndipo ali pa wokha adati, Wodala [ali] maso amene akuwona zimene inu muwona.
  2244. Luk 10:24 Pakuti ine ndikuwuzani inu, kuti aneneri ndi mafumu ambiri akhumba kuwona zimene inu muziwona, ndipo sadaziwona [izo]; ndi kumva zinthu zimene inu mukumva, ndipo sanazimve [izo].
  2245. Luk 10:25 ¶Ndipo, tawonani, wachilamulo wina adayimirira, ndi kumuyesa iye, kunena kuti, Ambuye, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
  2246. Luk 10:26 Adati kwa iye, Kodi m’chilamulo mwalembedwa chiyani? Iwe uwerenga bwanji?
  2247. Luk 10:27 Ndipo iye poyankha anati, Iwe uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi maganizo ako onse; ndi woyandikana naye monga iwe mwini.
  2248. Luk 10:28 Ndipo iye adati kwa iye, Iwe wayankha molondola: chita ichi, ndipo iwe udzakhala ndi moyo.
  2249. Luk 10:29 Koma iye, pofuna kudziyesa wolungama yekha, adati kwa Yesu, Ndipo woyandikana naye wanga ndani?
  2250. Luk 10:30 Ndipo Yesu poyankha anati, [Munthu] wina adatsika kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko, ndipo anagwa mwa achifwamba, amene adamvula iye zovala zake, ndipo anamvulaza [iye], ndipo anachoka, atamsiya [iye] ali pafupi kufa.
  2251. Luk 10:31 Ndipo mwa mwayi padali kubwera wansembe wina akutsika pa njirayo: ndipo pamene anamuwona iye, anadutsa mbali yina.
  2252. Luk 10:32 Momwemonso Mlevi, pamene anali pamalopo, anadza ndi kuyang’ana pa [iye], ndipo anadutsa ku mbali yina.
  2253. Luk 10:33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo, adafika pamene padali iye: ndipo pamene anamuwona iye, adagwidwa chifundo ndi iye,
  2254. Luk 10:34 Ndipo anadza kwa [iye], ndipo anamanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo, ndipo adamuyika pa nyama yake ya iye yekha, ndipo anadza naye ku nyumba yogona alendo, ndipo anamsamalira iye.
  2255. Luk 10:35 Ndipo pa tsiku linalo pomwe iye ananyamuka, iye adatulutsa makobiri awiri, ndipo anapatsa [iwo] mwini nyumba ya alendo, ndipo anati kwa iye, Msamalireni iye; ndipo chilichonse uwononga koposa, pobweranso ine, ndidzakubwezera iwe.
  2256. Luk 10:36 Ndi uti wa atatu awa, uganiza iwe, amene adali woyandikana naye wa iye uja adagwa mwa achifwamba?
  2257. Luk 10:37 Ndipo iye adati, Iye amene adawonetsa chifundo pa iye. Kenaka Yesu adati kwa iye, Pita, ndipo uchite iwe momwemo.
  2258. Luk 10:38 ¶Tsopano padachitika, pamene anali kupita pa ulendo, kuti iye adalowa m’mudzi wina: ndipo mkazi wina dzina lake Marita adamlandira iye m’nyumba mwake.
  2259. Luk 10:39 Ndipo iye adali ndi mbale wake wotchedwa Mariya, amene adakhalanso pa mapazi a Yesu, ndipo anamva mawu ake.
  2260. Luk 10:40 Koma Marita adatanganidwa ndi kutumikira kwambiri, ndipo adadza kwa iye, ndipo anati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga wandisiya ine kutumikira ndekha? Choncho mumuwuze kuti andithandize ine.
  2261. Luk 10:41 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Marita, Marita, iwe uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri:
  2262. Luk 10:42 Koma chinthu chimodzi chifunika: ndipo Mariya wasankha dera labwino limenero, limene silidzachotsedwa kwa iye.
  2263. Luk 11:1 Ndipo kunachitika, kuti, pamene iye anali kupemphera pamalo pena, m’mene iye adaleka, wina wa wophunzira ake adati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monganso Yohane adaphunzitsa wophunzira ake.
  2264. Luk 11:2 Ndipo iye adati kwa iwo, Pamene mupemphera, nenani kuti, Atate wathu amene muli kumwamba, Liyeretsedwe dzina lanu. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba, chomwecho pa dziko lapansi.
  2265. Luk 11:3 Mutipatse ife tsiku ndi tsiku mkate wathu wa patsiku.
  2266. Luk 11:4 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira aliyense amene ali ndi mangawa kwa ife. Ndipo musatitengere ife m’mayesero; koma mutipulumutse ife kwa choyipa.
  2267. Luk 11:5 Ndipo iye adati kwa iwo, Ndani wa inu amene adzakhala ndi bwenzi, ndipo adzapita kwa iye usiku, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;
  2268. Luk 11:6 Popeza bwenzi langa lochokera pa ulendo wandidzera ine, ndipo ndiribe chompatsa iye?
  2269. Luk 11:7 Ndipo iyeyu kuchokera m’katimo adzayankha ndi kunena kuti, Usandivute ine ayi; chitseko nchotseka tsopano, ndipo ana anga alinane pamodzi pakama; sindingathe kuwuka ndi kukupatsa iwe.
  2270. Luk 11:8 Ine ndinena kwa inu, Ngakhale iye sadzawuka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha kulimbika kwake iye adzawuka ndipo adzampatsa iye mochuluka monga azifuna.
  2271. Luk 11:9 Ndipo ine ndinena kwa inu, Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.
  2272. Luk 11:10 Pakuti aliyense amene apempha alandira; ndipo iye amene afunafuna apeza; ndi kwa iye amene agogodayo chidzatsegulidwa.
  2273. Luk 11:11 Ngati mwana wamwamuna adzampempha mkate kwa wina wa inu amene muli tate, kodi adzampatsa iye mwala? Kapena ngati [apempha] nsomba, kodi adzam’patsa njoka m’malo mwa nsomba?
  2274. Luk 11:12 Kapena ngati adzampempha dzira, kodi adzampatsa chinkhanira?
  2275. Luk 11:13 Ngati inu tsono, wokhala woyipa, mudziwa momwe mungapatsire mphatso zabwino kwa ana anu: koposa kotani Atate [wanu] wakumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha iye.
  2276. Luk 11:14 ¶Ndipo adali kutulutsa chiwanda, ndipo chinali chosayankhula. Ndipo kunachitika, pamene chiwanda chitatuluka, wosayankhulayo adayankhula; ndipo anthu adadabwa.
  2277. Luk 11:15 Koma ena mwa iwo adati, Iye amatulutsa ziwanda kudzera mwa Belezebule mkulu wa ziwanda.
  2278. Luk 11:16 Ndipo ena, pomuyesa [iye], anafuna kwa iye chizindikiro chochokera kumwamba.
  2279. Luk 11:17 Koma iye, podziwa zolingalira zawo, adati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanikana motsutsana mwa iwo wokha umafika ku chiwonongeko; ndipo nyumba [ikagawanikana] motsutsana ndi nyumba imagwa.
  2280. Luk 11:18 Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa iye mwini, udzayima bwanji ufumu wake? Popeza inu munena kuti ine nditulutsa ziwanda kudzera mwa Belezebule.
  2281. Luk 11:19 Ndipo ngati ine ndimatulutsa ziwanda kudzera mwa Belezebule, ana anu amuna atulutsa [izo] mwa yani? Choncho iwo adzakhala woweruza anu.
  2282. Luk 11:20 Koma ngati ine ndi chala cha Mulungu ndimatulutsa ziwanda, popanda kukayika ufumu wa Mulungu wafika pa inu.
  2283. Luk 11:21 Koma pamene munthu wamphamvu wokhala ndi zida alonda panyumba pake, zinthu zake ziri mumtendere:
  2284. Luk 11:22 Koma pamene wakumposa mphamvu adza pa iye, ndipo akamlaka iye, amchotsera iye zida zake zonse zimene adazidalira, ndipo agawa zofunkha zake.
  2285. Luk 11:23 Iye amene sali ndi ine atsutsana ndi ine: ndipo iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi ine amwaza.
  2286. Luk 11:24 Pamene mzimu wonyansa utuluka mwa munthu, umayenda kudutsa malo owuma, kufunafuna mpumulo; ndipo posawupeza, iwo unena kuti, ine ndibwerera ku nyumba kwanga konkuja kumene ndidatulukako,
  2287. Luk 11:25 Ndipo pamene ufika, uyipeza yosesa ndi yokonzedwa.
  2288. Luk 11:26 Kenaka upita, ndipo utenga [kwa iye] mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa yoposa mwini yekhayo; ndipo ilowamo, ndipo ikhala m’menemo: ndipo [makhalidwe] wotsiriza a munthu uyo ali woyipa koposa woyambawo.
  2289. Luk 11:27 ¶Ndipo kunachitika, pamene iye anali kunena zinthu izi, mkazi wina wa khamu la anthulo adakweza mawu ake, ndipo anati kwa iye, Yodala [ili] mimba imene idakubalani inu, ndi mawere amene inu mudayamwa.
  2290. Luk 11:28 Koma iye adati, Inde makamaka, wodala [ali] iwo amene akumva mawu a Mulungu, ndipo awasunga.
  2291. Luk 11:29 ¶Ndipo pamene adasonkhana anthu mothinana, iye adayamba kunena, Uwu ndi mbadwo woyipa: iwo afuna chizindikiro; ndipo sipadzaperekedwa chizindikiro china kwa uwo, koma chizindikiro cha Yona mneneri.
  2292. Luk 11:30 Pakuti monga Yona adali chizindikiro kwa Anineve, chotero adzakhalanso Mwana wamwamuna wa munthu kwa mbadwo uwu.
  2293. Luk 11:31 Mfumu yayikazi ya kumwera idzayimirira pa chiweruzo chotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uwu, ndipo adzawatsutsa iwo: pakuti anadza kuchokera ku malekezero adziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo, tawonani, wamkulu woposa Solomoni [ali] pano.
  2294. Luk 11:32 Amuna aku Nineve adzayimirira pakuweruza kotsiriza pamodzi ndi mbadwo uwu, ndipo adzawutsutsa uwo: pakuti iwo adalapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo, tawonani, wamkulu woposa Yona [ali] pano.
  2295. Luk 11:33 Palibe munthu, atayatsa nyali, ayiyika [iyo] malo obisika, kapena pansi pa choyezera, koma pa choyikapo chake, kuti iwo akulowamo awone kuwala.
  2296. Luk 11:34 Nyali yathupi ndiyo diso: choncho pamene diso lako liri langwiro, thupi lako lonse lidzala ndi kuwunika; koma ngati [diso lako] liri loyipa, thupi lakonso [liri] lodzala ndi mdima.
  2297. Luk 11:35 Choncho yang’anira kuti kuwunika kuli mwa iwe kusakhale mdima.
  2298. Luk 11:36 Choncho ngati thupi lako lonse [likhala] lowunukidwa, losakhala nalo dera lina la mdima, lonsero lidzakhala lodzala ndi kuwunika, monga ngati pamene kuwala kwake kwa nyali kuwunikira iwe.
  2299. Luk 11:37 ¶Ndipo pamene iye anali kuyankhula, Mfarisi wina adampempha iye kuti adye naye: ndipo pamene iye adalowa, ndipo anakhala pansi ku chakudya.
  2300. Luk 11:38 Ndipo pamene Mfarisiyo adawona [izi], iye adazizwa pakuwona kuti adayamba kudya asadasambe.
  2301. Luk 11:39 Ndipo Ambuye adati kwa iye, Tsopano inu Afarisi mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale yayikulu; koma m’kati mwanu muli modzala ndi kuba ndi zoyipa.
  2302. Luk 11:40 Wopusa [inu], kodi iye amene anapanga chimene chili kunja [sanathe] kupanga chimene chili mkatinso?
  2303. Luk 11:41 Koma makamaka patsani mphatso zachifundo monga mwa zinthu zimene inu muli nazo; ndipo, tawonani, zinthu zonse zili zoyera kwa inu.
  2304. Luk 11:42 Koma tsoka inu, Afarisi! Pakuti mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tomera tonunkhira ta minti tozuna ndi tizitsamba tokometsa chakudya ta ruwe ndi zitsamba za mitundu yonse, ndipo muleka chiweruziro ndi chikondi cha Mulungu: izi munayenera inu mutachita, ndi kusasiya zinazo osazichita.
  2305. Luk 11:43 Tsoka kwa inu, Afarisi! Pakuti inu mukonda mipando ya ulemu m’masunagoge, ndi kuyankhulidwa m’misika.
  2306. Luk 11:44 Tsoka kwa inu, alembi ndi Afarisi, wonyenga! Pakuti muli ngati manda amene sawoneka, ndipo anthu amene ayenda pamwamba [pawo] sadziwa [za iwo].
  2307. Luk 11:45 ¶Kenaka adayankha m’modzi wa a chilamulo, ndipo ananena kwa iye, Mphunzitsi, kunena izi inu mutitonza ifenso.
  2308. Luk 11:46 Ndipo iye adati, Tsoka kwa inunso, inu a chilamulo! Pakuti musenzetsa anthu akatundu wosawutsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.
  2309. Luk 11:47 Tsoka inu! Pakuti muwaka manda a aneneri, ndipo makolo anu adawapha.
  2310. Luk 11:48 Zowona inu muchita umboni kuti muvomereza zochita za makolo anu: pakuti iwo ndithu adawapha iwo, ndipo inu muwawakira manda.
  2311. Luk 11:49 Chonchonso idanena nzeru ya Mulungu, Ine ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo [ena] a iwo adzawapha ndi kuwazunza:
  2312. Luk 11:50 Kuti mwazi wa aneneri onse, umene udakhetsedwa kuyambira kukhazikika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uwu.
  2313. Luk 11:51 Kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zakariya, amene adaphedwa pakati pa guwa la nsembe ndi kachisi: ndithudi ine ndinena kwa inu, Udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uwu.
  2314. Luk 11:52 Tsoka kwa inu, a chilamulo! Pakuti mwachotsa chifungulo cha chidziwitso: inu simudalowamo eni nokha, ndipo iwo amene adalinkulowa inu mudawaletsa.
  2315. Luk 11:53 Ndipo pamene iye adanena zinthu izi kwa iwo, alembi ndi Afarisi adayamba kumkakamiza [iye] kolimba, ndi kumputa iye kuti ayankhule zinthu zambiri:
  2316. Luk 11:54 Nadikira iye, ndikufuna kuti akakole kanthu kotuluka m’kamwa mwake, ndi kuti akampezere chifukwa iye.
  2317. Luk 12:1 Pa Nthawi imeneyi, pamene adasonkhana pamodzi khamu la anthu osawerengeka, kotero kuti adapondana wina pa mzake, iye adayamba kunena kwa wophunzira ake poyamba pa zonse, Tachenjerani inu ndi chofufumitsa cha Afarisi, chimene chili chinyengo.
  2318. Luk 12:2 Pakuti kulibe kanthu kovundikiridwa, kamene sikadzavumbulutsidwa; kapena kobisika, kamene sikadzadziwika.
  2319. Luk 12:3 Choncho chilichonse chimene mwachinena mu mdima chidzamveka powala; ndipo chimene inu mwayankhula m’khutu m’zipinda za mkati [zotsekedwa] chidzalalikidwa pa madenga a nyumba.
  2320. Luk 12:4 Ndipo ndinena kwa inu abwenzi anga, Musawope iwo amene akupha thupi, ndipo pambuyo pa ichi alibe kanthu kena kamene angathe kuchita.
  2321. Luk 12:5 Koma ine ndidzakuchenjezeranitu inu iye amene muzimuwopa: Wopani iye, amene atapha ali ndi mphamvu yakutaya ku nyanja ya moto; inde, ine ndinena kwa inu, Wopani iye.
  2322. Luk 12:6 Kodi mpheta zisanu sizigulitsidwa tindalama tiwiri, ndipo palibe imodzi ya izo iyiwalika pamaso pa Mulungu?
  2323. Luk 12:7 Komatu ngakhale tsitsi lonse la pamutu panu liri lowerengedwa. Choncho musawopa: inu muli a mtengo woposa wa mpheta ziwiri.
  2324. Luk 12:8 Ndiponso ine ndinena kwa inu, Aliyense adzavomereza ine pamaso pa anthu, iyeyo Mwana wamwamuna wa munthu adzamvomerezanso iye pamaso pa angelo a Mulungu:
  2325. Luk 12:9 Koma iye amene andikana ine pamaso pa anthu adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.
  2326. Luk 12:10 Ndipo aliyense amene adzanenera zoyipa Mwana wamwamuna wa munthu, zidzakhlulukidwa kwa iye: koma kwa iye amene adzanenera zamwano Mzimu Woyera sizidzakhululukidwa ayi.
  2327. Luk 12:11 Ndipo pamene adzapita nanu ku masunagoge, ndi [kwa] woweruza milandu, ndi maulamuliro, musalingalire inu kuti mukadzikanira bwanji ndipo motani kapena chinthu chimene inu mukanena;
  2328. Luk 12:12 Pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene inu muyenera kuzinena.
  2329. Luk 12:13 ¶Ndipo m’modzi wa gululo adati kwa iye, Mphunzitsi, lankhulani kwa mbale wanga, kuti agawane ndi ine chuma cha masiye.
  2330. Luk 12:14 Ndipo adati kwa iye, Munthu [iwe], ndani adandiyika ine ndikhale woweruza kapena ogawira pa inu?
  2331. Luk 12:15 Ndipo iye adati kwa iwo, Yang’anirani, ndipo mudzisungire kupewa msiliro uliwonse: pakuti moyo wake wa munthu supangidwa ndi kuchuluka kwa zinthu ali nazo.
  2332. Luk 12:16 Ndipo iye adanena fanizo kwa iwo, kunena kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma udapatsa zambiri:
  2333. Luk 12:17 Ndipo iye adaganiza mwa iye yekha, nanena kuti, Ndidzachita chiyani ine, chifukwa ndiribe mosungiramo zipatso zanga?
  2334. Luk 12:18 Ndipo iye adati, Ndidzachita ichi: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu; ndipo m’menemo ndidzasungiramo zipatso zanga zonse ndi katundu wanga.
  2335. Luk 12:19 Ndipo ine ndidzati kwa moyo wanga, Moyo, iwe uli ndi katundu wambiri wosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, udye, umwe, [ndipo] ukhale wokondwera,
  2336. Luk 12:20 Koma Mulungu adati kwa iye, Wopusa [iwe], usiku uno moyo wako udzafunidwa kwa iwe: tsono zidzakhala za yani zinthu izo, zimene iwe wazisunga?
  2337. Luk 12:21 Chomwecho akhala iye amene adziwunjikira chuma mwini yekha, ndipo wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.
  2338. Luk 12:22 ¶Ndipo iye adati kwa wophunzira ake, Choncho ine ndinena kwa inu, musade nkhawa za moyo wanu, chimene mudzadya; kapena za thupi lanu, chimene inu mudzavala.
  2339. Luk 12:23 Moyo uli woposa chakudya, ndi thupi [liri loposa] chovala.
  2340. Luk 12:24 Lingalirani makungubwe: kuti samafesayi kapena kukolola; zimene ziribe nyumba yosungiramo kapena nkhokwe; ndipo Mulungu amazidyetsa izo: koposa kotani nanga inu muli woposa mbalame?
  2341. Luk 12:25 Ndipo ndani wa inu ndi kuda nkhawa angathe kuwonjeza kutalika kwa phazi ndi theka pa msinkhu wake?
  2342. Luk 12:26 Ngati inu simungathe kuchita ngakhale chimene chili chaching’onong’ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?
  2343. Luk 12:27 Lingalirani maluwa momwe akulira iwo: sagwira ntchito, sapota ayi; koma ine ndinena kwa inu, kuti Solomoni mu ulemerero wake wonse sadavala ngati limodzi la awa.
  2344. Luk 12:28 Ngati tsono Mulungu aveka kotere udzu, umene lero ukhala m’thengo, ndipo mawa uponyedwa pamoto; koposa kotani nanga [iye sadzakuvekani] inu, inu a chikhulupiriro chochepa?
  2345. Luk 12:29 Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa, ndipo musakhale ndi mtima wokayika.
  2346. Luk 12:30 Pakuti zinthu izi zonse mitindu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna: ndipo Atate wanu adziwa kuti musowa zinthu zimenezi inu.
  2347. Luk 12:31 ¶Koma makamaka funafunani inu ufumu wa Mulungu; ndipo zinthu izi zonse zidzawonjezeredwa kwa inu.
  2348. Luk 12:32 Musawopa ayi, kagulu kankhosa; pakuti chili chisangalalo chabwino kwa Atate wanu kukupatsani ufumu.
  2349. Luk 12:33 Gulitsani zimene muli nazo, ndipo mupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere eni nokha matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha m’mwamba chimene sichilephera, kumene mbala siziyandikira, kapena njenjete sizichiwononga.
  2350. Luk 12:34 Pakuti kumene chuma chanu chili, komweko mtima wanu udzakhalanso.
  2351. Luk 12:35 Dzimangireni m’chiwuno mwanu, ndipo nyali [zanu] zikhale zoyaka;
  2352. Luk 12:36 Ndipo inu nokha khalani wofanana ndi anthu amene ayembekezera mbuye wawo, pamene ati adzabwerera kuchokera ku ukwati; kuti pamene akudza iye ndi kugogoda, iwo akamtsegulire iye mofulumira.
  2353. Luk 12:37 Wodala [ali] antchitowo, amene mbuye wawo, pakudza iye adzawapeza akudikira: ndithudi ndinena ndi inu, kuti iye adzadzimangira m’chiwuno yekha, ndipo adzawakhalitsa pansi kudya, ndipo adzafika ndi kuwatumikira.
  2354. Luk 12:38 Ndipo ngati angadze ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, ndipo awapeza [iwo] atero, wodala antchito amenewa.
  2355. Luk 12:39 Ndipo zindikirani ichi, kuti ngati mwini nyumba wabwinoyo akadadziwa ora limene ikudza mbala, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibowoledwe.
  2356. Luk 12:40 Choncho khalani wokonzeka inunso: pakuti Mwana wamwamuna wa munthu adzadza nthawi imene simulingalira.
  2357. Luk 12:41 ¶Kenaka Petro adati kwa iye, Ambuye, inu mwalinena fanizo ili kwa ife, kapena kwa onse?
  2358. Luk 12:42 Ndipo Ambuye adati, Ndani tsono amene ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeruyo, amene mbuye [wake] adzamuyika wolamulira wa pa nyumba yake, kuwapatsa [iwo] gawo la chakudya [lawo] pa nyengo yake?
  2359. Luk 12:43 Wodala [ali] wantchitoyo, amene mbuye wake pamene afika adzampeza alikuchita chotero.
  2360. Luk 12:44 Mwa zowona ndinena kwa inu, kuti adzamuyika iye wolamulira wa pa zonse ali nazo.
  2361. Luk 12:45 Koma ndipo ngati wantchito uyo akanena mu mtima mwake, Mbuye wanga achedwa kudza kwake; ndipo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi, ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;
  2362. Luk 12:46 Mbuye wa wantchito uyo adzafika m’tsiku lakuti samuyembekezera [iye], ndi pa ora lakuti iye salidziwa, ndipo adzamdula iye m’magawo, ndipo adzamuyika dera lake pamodzi ndi anthu wosakhulupirira.
  2363. Luk 12:47 Ndipo wantchito uyo, amene adadziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sadakonzekera [mwini yekha], kapena kuchita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa [mikwapulo] yambiri.
  2364. Luk 12:48 Koma iye amene sadachidziwa, ndipo adazichita zinthu zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa [ndi mikwapulo] pang’ono. Pakuti kwa aliyense wapatsidwa zambiri, kwa iye kudzafunidwa zambiri: ndipo kwa amene anthu adamuyikizira zambiri, kwa iye iwo adzamfunsa zoposa.
  2365. Luk 12:49 ¶Ine ndidadzera kutumiza moto pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji ine, ngati uli woyatsidwa kale?
  2366. Luk 12:50 Koma ine ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nawo; ndipo ine ndiletsedwa motani kufikira ukatsirizidwa!
  2367. Luk 12:51 Muyesa inu kuti ndidadzera kupatsa mtendere pa dziko lapansi? Ine ndiwuza inu, Ayitu; koma makamaka kugawanikana:
  2368. Luk 12:52 Pakuti kuyambira tsopano adzakhala asanu m’nyumba imodzi ogawanikana, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.
  2369. Luk 12:53 Atate adzagawanikana kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wamwamuna kutsutsana ndi atatewo; amayi adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amayi wake, mpongozi wamkazi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake wamwamuna, ndi mkaziyo wa mwana wake wamwamuna ndi mpongozi wake wamkazi.
  2370. Luk 12:54 ¶Ndipo iye adatinso kwa anthu, Pamene inu muwona mtambo ukukwera kutuluka kumadzulo, pomwepo inu munena kuti, Ikudza mivumbi; ndipo kuli kotero.
  2371. Luk 12:55 Ndipo pamene [inu muwona] mphepo ya kumwera iwomba; munena kuti, Kudzakhala kotenthatu; ndipo kuterodi.
  2372. Luk 12:56 Inu wonyenga, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya thambo ndi ya dziko lapansi; koma bwanji simudziwa kuzindikira nthawi yino?
  2373. Luk 12:57 Inde, ndipo chifukwa chiyani ngakhale inunso pa inu nokha simuweruza zomwe ziri zolungama?
  2374. Luk 12:58 ¶Pamene iwe uli kupita naye woyimbana naye mlandu kwa woweruza, [pomwe uli] panjira, fulumira, kuti ukhoze kumasulidwa kwa iye; kuti mwina angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msirikali, ndi msirikali angaponye iwe m’nyumba yandende.
  2375. Luk 12:59 Ine ndikuwuza iwe, iwe sudzatulukamo konse m’menemo, kufikira utalipira kandalama komaliza.
  2376. Luk 13:1 Adalipo pa nyengo imeneyo ena amene adamuwuza iye za Agalileya, amene mwazi wawo Pilato adasanganiza ndi nsembe zawo.
  2377. Luk 13:2 Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Muyesa inu kuti Agalileya awa adali wochimwa koposa Agalileya onse, chifukwa adamva zinthu zowawa izi?
  2378. Luk 13:3 Ine ndinena kwa inu, Iyayitu: pokhapo ngati inu mulapa, mudzawonongeka inu nonse chimodzimodzi.
  2379. Luk 13:4 Kapena aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yayitali ya m’Siloamu idawagwera, ndi kuwapha iwo; kodi muganiza kuti iwo adali wochimwa koposa anthu onse amene akhala m’Yerusalemu?
  2380. Luk 13:5 Ine ndiwuza inu, Iyayitu: koma, pokhapo ngati mulapa, inu mudzawonongeka chimodzimodzi.
  2381. Luk 13:6 ¶Iye adanenanso fanizo ili, [Munthu] wina adali ndi mtengo wa mkuyu wobzyalidwa m’munda wake wa mphesa; ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, ndipo adapeza popanda.
  2382. Luk 13:7 Ndipo iye adati kwa wosamalira munda wake wa mphesa, Tawona, zaka zitatu izi ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mtengo wa mkuyu uwu; ndipo ndimapeza popanda; tawudula; iwo uyipangitsiranji nthaka yopanda pake?
  2383. Luk 13:8 Ndipo iye poyankha anati kwa iye, Mbuye, bawulekani chaka chinonso, kufikira ine ndidzawukumbira kwete, ndi kuthiramo [umo] ndowe.
  2384. Luk 13:9 Ndipo ngati udzabala chipatso, [chabwino]: ndipo ngati ayi, [kenaka] pambuyo pake mudzawudulatu.
  2385. Luk 13:10 Ndipo alikuphunzitsa mu imodzi ya masunagoge pa sabata.
  2386. Luk 13:11 ¶Ndipo, tawonani, padali mkazi amene adali nawo mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, ndipo anakhala wopeteka, ndipo sakadatha konse [iye mwini] kuweramuka.
  2387. Luk 13:12 Ndipo pamene Yesu adamuwona, adamuyitanira [iye kwa iye], ndipo ananena kwa iye, Mkaziwe, iwe wamasulidwa kuzopweteka zako.
  2388. Luk 13:13 Ndipo adayika manja [ake] pa iye: ndipo posakhalitsa adawongoledwa, ndipo analemekeza Mulungu.
  2389. Luk 13:14 Ndipo wolamulira wa sunagoge adayankha movutika mtima, chifukwa chakuti Yesu adachiritsa tsiku la sabata, ndipo ananena kwa anthuwo, Alipo masiku asanu ndi limodzi amene anthu ayenera kugwira ntchito: choncho mu amenewo idzani kudzachiritsidwa, ndipo osati tsiku la sabata ayi.
  2390. Luk 13:15 Ambuye kenaka adamyankha iye, ndipo anati, [Iwe] wonyenga, kodi munthu aliyense wa inu pa tsiku la sabata samayimasula ng’ombe yake kapena bulu [wake] m’khola, kupita [nayo] kukayimwetsa madzi?
  2391. Luk 13:16 Ndipo nanga sikuyenera kuti mkazi uyu, wokhala mwana wamkazi wa Abrahamu, amene Satana wam’manga, onani, zaka izi khumi ndi zisanu ndi zitatu, kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la sabata?
  2392. Luk 13:17 Ndipo pamene iye adanena zinthu izi, onse wotsutsana naye adachita manyazi: ndipo anthu onse adakondwera ndi zinthu zonse za ulemerero zidachitidwa ndi iye.
  2393. Luk 13:18 ¶Kenaka iye adanena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ine ndidzawufanizira ndi chiyani?
  2394. Luk 13:19 Ufanana ndi kambewu ka mpiru, kamene munthu adatenga, ndi kukaponya m’munda wake; ndipo kadakula, ndikukhala mtengo waukulu; ndipo mbalame za mum’lengalenga zinabindikira mu nthambi zake.
  2395. Luk 13:20 Ndipo iye adatinso, Ndidzafanizira ufumu wa Mulungu ndi chiyani?
  2396. Luk 13:21 Ufanana ndi chofufumitsa mikate, chimene mkazi adatenga nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira udafufumitsidwa wonsewo.
  2397. Luk 13:22 Ndipo iye adapita pakati pa mizinda ndi midzi, kuphunzitsa, ndi kuyenda ulendo kuloza ku Yerusalemu.
  2398. Luk 13:23 Kenaka m’modzi adati kwa iye, Ambuye, wopulumutsidwa ali wowerengeka kodi? Ndipo iye adati kwa iwo,
  2399. Luk 13:24 ¶Yesetsani kulowa umo pa chipata chopapatiza: pakuti ambiri, ine ndikuwuzani inu, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.
  2400. Luk 13:25 Pamene atawuka mwini nyumba, ndipo watseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuyima kunja, ndi kugogoda pachitseko, kunena kuti, Ambuye, Ambuye, titsegulireni ife; ndipo iye adzayankha ndipo adzati kwa inu; sindidziwa inu kumene muchokerako:
  2401. Luk 13:26 Kenaka mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo mudaphunzitsa m’makwalala athu.
  2402. Luk 13:27 Koma iye adzati, Ine ndikuwuzani inu, Ine sindikudziwani kumene inu muchokera; chokani kwa ine, inu nonse akuchita kusaweruzika.
  2403. Luk 13:28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzawona Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo ndi aneneri onse mu ufumu wa Mulungu, koma inu mukutulutsidwa kunja.
  2404. Luk 13:29 Ndipo iwo adzachokera kum’mawa, ndi kuchokera kumadzulo, ndi kuchokera kumpoto, ndi [kuchokera] kumwera, ndipo adzakhala pansi mu ufumu wa Mulungu.
  2405. Luk 13:30 Ndipo, tawonani, alipo akumapeto amene adzakhala woyamba, ndipo alipo woyamba adzakhala akumapeto.
  2406. Luk 13:31 ¶Tsiku lomwero padadzapo Afarisi ena, nanena kwa iye, Tulukani, ndipo chokani kuno: chifukwa Herode afuna kupha inu.
  2407. Luk 13:32 Ndipo iye adati kwa iwo, Pitani inu, ndipo kawuzeni nkhandwe imeneyo, Tawonani, ine nditulutsa ziwanda, ndipo ine ndichiritsa lero ndi mawa, ndipo [tsiku] la chitatu ndidzakhalitsidwa wangwiro.
  2408. Luk 13:33 Ngakhale ziri choncho ine ndiyenera ndiyende lero, ndipo mawa, ndi [tsiku] lotsatira: pakuti sikuyenera kutero kuti mneneri awonongeke kunja kwa Yerusalemu.
  2409. Luk 13:34 Yerusalemu, Yerusalemu, amene ukupha aneneri, ndi woponya miyala iwo atumidwa kwa iwe; Kawiri kawiri ndidafuna kusonkhanitsa pamodzi ana ako, monga ngati thadzi [lisonkhanitsa] anapiye kuwafungatira m’mapiko [ake], ndipo inu simudafuna ayi!
  2410. Luk 13:35 Tawonani, nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja: ndipo ndithudi ine ndinena kwa inu, Inu simudzandiwona ine, kufikira [pa nthawi] idzadza pomwe inu mudzati, Wodala [ali] iye amene akudza m’dzina la Ambuye.
  2411. Luk 14:1 Ndipo padachitika, pamene iye adalowa m’nyumba ya m’modzi wa akulu Afarisi kukadya pa tsiku lasabata, kuti iwo adali kumzonda iye.
  2412. Luk 14:2 Ndipo, tawonani, padali munthu wina pamaso pake adali wa mbulu.
  2413. Luk 14:3 Ndipo Yesu poyankha anati kwa a chilamulo ndi Afarisi, nanena kuti, Kodi nkuloledwa mwachilamulo kuchiritsa pa tsiku la sabata?
  2414. Luk 14:4 Koma iwo adakhala chete. Ndipo adamtenga [iye], ndi kumchiritsa iye, ndipo anamuwuza apite;
  2415. Luk 14:5 Ndipo adayankha iwo, nanena kuti, Ndani wa inu amene adzakhala ndi bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’dzenje, ndipo sadzayitulutsa pomwepo pa tsiku lasabata kodi?
  2416. Luk 14:6 Ndipo iwo sadatha kumuyankhanso pa zinthu izi.
  2417. Luk 14:7 ¶Ndipo iye adapereka fanizo kwa iwo amene adali woyitanidwa, pamene iye adapenya momwe amadzisankhira malo a pa gome a ulemu; kunena kwa iwo,
  2418. Luk 14:8 Pamene iwe wayitanidwa ndi [munthu] wina ku ukwati, usakhale pa mpando wa pamwamba kwambiri; kuti mwina wina wa ulemu woposa iwe adzayitanidwa ndi iye;
  2419. Luk 14:9 Ndipo iye amene adayitana iwe ndi iye afika ndi kunena kwa iwe, Mpatse munthu uyu malo; ndipo iwe udzayamba kuchita manyazi kukakhala pa mpando wa pansipansi.
  2420. Luk 14:10 Koma pamene iwe wayitanidwa, pita nukhale pansi pa malo a pansipansi; kuti pamene iye adakuyitana iwe adza, akhoze kunena kwa iwe, Bwenzi, pita kukwera: kenaka udzakhala ndi ulemu pamaso pa onse akukhala kuseyama pa chakudya pamodzi ndi iwe.
  2421. Luk 14:11 Pakuti aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo iye amene adzichepetsa adzakwezedwa.
  2422. Luk 14:12 ¶Kenaka iye adanenanso kwa iye amene adamuyitana, Pamene ukonza chakudya cha pa usana kapena cha madzulo, usayitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena afuko lako, kapena anansi [ako] eni chuma; kuti mwina iwonso angabwezere kuyitana iwe, ndipo kubwezera kudzachitika kwa iwe.
  2423. Luk 14:13 Koma pamene ukonza phwando, uyitane a umphawi, wolumala, wotsimphina, akhungu:
  2424. Luk 14:14 Ndipo udzakhala wodalitsika; pakuti iwo sangakubwezere iwe: pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuwuka kwa wolungama.
  2425. Luk 14:15 ¶Ndipo pamene wina wa iwo amene adakhala pachakudya pamodzi ndi iye adamva zinthu izi, adati kwa iye, Wodala [ali] iye amene adzadya mkate mu ufumu wa Mulungu.
  2426. Luk 14:16 Kenaka iye adati kwa iye, Munthu wina adakonza phwando lalikulu; ndipo anayitana anthu ambiri:
  2427. Luk 14:17 Ndipo adatuma wantchito wake pa nthawi ya phwando kukanena kwa iwo amene adayitanidwawo, Idzani; pakuti zonse zakonzedwa tsopano.
  2428. Luk 14:18 Ndipo onse ndi [mgwirizano] umodzi adayamba kupereka zifukwa. Woyamba adati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ine ndiyenera ndipite ndikawuwone: ndikupempha iwe undilole ine ndisafike.
  2429. Luk 14:19 Ndipo wina adati, Ine ndagula ng’ombe za magoli asanu, ndipo ndinka kukaziyesa: ndikupempha iwe undilole ine ndisafike.
  2430. Luk 14:20 Ndipo wina adati, Ine ndakwatira mkazi, ndipo choncho sindingathe kudza.
  2431. Luk 14:21 Kotero wantchitoyo anabwera, ndipo adawuza mbuye wake zinthu izi. Kenaka mwini nyumba atakwiya anati kwa wantchito wakeyo, Tuluka pita msanga kumakwalala ndi kunjira za mudzi, ndipo ubwere nawo muno aumphawi ndi wolumala ndi wotsimphina ndi akhungu.
  2432. Luk 14:22 Ndipo wantchitoyo adati, Ambuye, zachitika monga inu mwalamulira, ndipo malo tsono akadalipobe.
  2433. Luk 14:23 Ndipo mbuye adanena kwa wantchitoyo, Tuluka kupita ku misewu ndi njira za kuminda, ndipo uwawumirize [iwo] kuti alowe, kuti nyumba yanga ikhoze kudzala.
  2434. Luk 14:24 Pakuti ndinena kwa inu, Kuti kulibe m’modzi wa amuna amene adayitanidwa aja adzalawa mgonero wanga.
  2435. Luk 14:25 ¶Ndipo khamu lalikulu lidapita naye: ndipo iye adatembenuka, ndipo anati kwa iwo,
  2436. Luk 14:26 Ngati munthu aliyense adza kwa ine, wosada atate wake ndi amayi wake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo, inde, ndiponso moyo wake wa iye mwininso, iye sangathe kukhala wophunzira wanga.
  2437. Luk 14:27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake, ndi kudza pambuyo panga, sangathe kukhala wophunzira wanga.
  2438. Luk 14:28 Pakuti ndani wa inu, amene akufuna kumanga nsanja yayitali, sayamba wakhala kaye pansi, ndipo nawerengera mtengo wake, ngati ali nazo [zokwanira] zakuyimaliza [iyo]?
  2439. Luk 14:29 Kuti mwina zingachitike, pamene iye atayala maziko, ndipo sali wakutha kuyimaliza [iyo], ndipo anthu onse amene ayang’ana [iyo] ayamba kum’nyogodola iye.
  2440. Luk 14:30 Kunena kuti, Munthu uyu adayamba kumanga, ndipo sadathe kumaliza.
  2441. Luk 14:31 Kapena mfumu yanji, pakupita kumenyana ndi nkhondo ndi mfumu inzake, siyiyamba yakhala pansi, ndi kufunsafunsa ngati akhoza ndi asirikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alinkudza kukomana naye ndi asirikali zikwi makumi awiri?
  2442. Luk 14:32 Kapena ngati sakhoza, pokhala winayo ali kutalitali, atumize akazembe, ndipo afunse dongosolo la za mtendere.
  2443. Luk 14:33 Kotero chomwechonso, aliyense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.
  2444. Luk 14:34 ¶Mchere [uli] wabwino: koma ngati ukasukuluka, udzakolereretsedwa ndi chiyani?
  2445. Luk 14:35 Suyenera kuwuthira pamunda, kapena padzala la ndowe; [koma] anthu awutaya kunja. Amene ali nawo makutu akumva, iye amve.
  2446. Luk 15:1 Kenaka adayandikira kwa iye onse wokhometsa misonkho ndi anthu wochimwa kudzamva iye.
  2447. Luk 15:2 Ndipo Afarisi ndi alembi adang’ung’udza, nanena kuti, Munthu uyu alandira wochimwa, ndipo adya nawo.
  2448. Luk 15:3 ¶Ndipo iye adayankhula fanizo ili kwa iwo, nanena kuti,
  2449. Luk 15:4 Munthu ndani wa inu, ali nazo nkhosa zana limodzi, ngati ataya imodzi ya izo, sasiya nanga makumi asanu ndi anayi ndi mphambu zisanu ndi zinayi zinazo m’chipululu, ndipo alondola imene yotayikayo, kufikira iye atayipeza iyo?
  2450. Luk 15:5 Ndipo pamene ayipeza [iyo], iye ayiyika [iyo] pa mapewa ake, akukondwera.
  2451. Luk 15:6 Ndipo pamene afika kunyumba kwake, amema abwenzi [ake] ndi anansi ake, nanena kwa iwo, Kondwerani ndi ine; pakuti ndayipeza nkhosa yanga imene inatayikayo.
  2452. Luk 15:7 Ine ndinena kwa inu, kuti chimodzimodzi chimwemwe chidzakhala kumwamba chifukwa cha wochimwa m’modzi amene alapa, koposa anthu wolungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene sasowa kulapa.
  2453. Luk 15:8 ¶Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama za siliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, ndipo asesa m’nyumba yake, ndipo afunafuna mosamalitsa kufikira atayipeza [iyo]?
  2454. Luk 15:9 Ndipo m’mene ayipeza [iyo], amema abwenzi [ake] ndi anansi [ake], nanena kuti, Kondwerani ndi ine, pakuti ndayipeza ndalama imene ine ndidatayayo.
  2455. Luk 15:10 Chimodzimodzinso, ine ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa m’modzi amene alapa.
  2456. Luk 15:11 ¶Ndipo iye adati, Bambo wina adali ndi ana amuna awiri:
  2457. Luk 15:12 Ndipo wam’ng’onoyo adati kwa atate [wake], Atate, ndigawirenitu ine gawo la pa chuma chanu limene liri la [kwa ine]. Ndipo iye adawagawira iwo za moyo [wake].
  2458. Luk 15:13 Ndipo pasanathe masiku ambiri mwana wamwamuna wam’ng’ono adasonkhanitsa zonse pamodzi, ndipo anayenda ulendo wake kupita ku dziko lakutali; ndipo komweko adasakaza chuma chake ndi makhalidwe osalabadira zotsatira zake.
  2459. Luk 15:14 Ndipo pamene adatha zonse, padakhala njala yayikulu m’dziko muja; ndipo iye adayamba kusowa.
  2460. Luk 15:15 Ndipo iye adapita ndi kudziphatika kwa mbadwa imodzi yadziko limenero; ndipo iye adamtumiza kubusa kwake kukadyetsa nkhumba.
  2461. Luk 15:16 Ndipo akadakondwera kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya: ndipo palibe munthu adam’patsa kanthu.
  2462. Luk 15:17 Ndipo pamene adalingalira mumtima za iye, iye adati, Ndi angati a antchito wolipidwa a atate wanga ali nacho chakudya chokwanira ndi china chotsala, ndipo ine ndiwonongeka ndi njala?
  2463. Luk 15:18 Ine ndidzanyamuka ndi kupita kwa atate wanga, ndipo ndidzanena kwa iye, Atate, ine ndinachimwira kumwamba, ndi pamaso panu.
  2464. Luk 15:19 Ndipo sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu wamwamuna: mundiyese ine monga m’modzi wa antchito anu.
  2465. Luk 15:20 Ndipo iye adanyamuka, ndipo anadza kwa atate wake. Koma pamene anali kudza iye kutali, atate wake adamuwona iye, ndipo anagwidwa chifundo, ndipo anathamanga, ndipo anamkupatira pakhosi pake, ndipo anampsopsona.
  2466. Luk 15:21 Ndipo mwana wamwamunayo adati kwa iye, Atate, ndidachimwira kumwamba, ndi pamaso panu, ndipo sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu wamwamuna.
  2467. Luk 15:22 Koma atateyo adati kwa antchito ake, Bweretsani mwinjiro wokometsetsa, ndipo mumveke iye [uwo]; ndipo mumveke mphete ku dzanja lake, ndi nsapato ku mapazi [ake]:
  2468. Luk 15:23 Ndipo idzani naye mwana wa ng’ombe wonenepa, ndipo mumuphe [iye], ndipo tiyeni ife tidye, ndipo tisangalale:
  2469. Luk 15:24 Chifukwa mwana wanga wamwamuna uyu adali wakufa, ndipo alinso ndi moyo; anali wotayika, ndipo wapezeka. Ndipo adayamba kusangalala.
  2470. Luk 15:25 Tsopano mwana wake wamwamuna wamkulu adali kumunda: ndipo pamene adali kubwera iye ndi kuyandikira kunyumbayo, adamva nyimbo ndi kuvina.
  2471. Luk 15:26 Ndipo iye adayitana m’modzi wa antchito, ndipo anamfunsa zimene zinthu izi zitanthawuza.
  2472. Luk 15:27 Ndipo iye adati kwa iye, Mng’ono wako wafika; ndipo atate wako wapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa iye wamlandira iye wotetezedwa ndi wamoyo.
  2473. Luk 15:28 Ndipo iye adakwiya, ndipo sadafuna kulowamo: choncho atate wake adatuluka, ndipo anamdandawulira iye.
  2474. Luk 15:29 Koma iye poyankha anati kwa atate [wake], Onani, zaka zambiri zotere ine ndikutumikirani inu, kapena kulakwira lamulo lanu nthawi iliyonse: ndipo tsono inu simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisangalale ndi abwenzi anga:
  2475. Luk 15:30 Koma pamene mwana wanu wamwamuna uyu atangodza, amene watha za moyo zanu ndi akazi achiwerewere, inu mudaphera iye mwana wa ng’ombe wonenepa.
  2476. Luk 15:31 Koma iye adanena kwa iye, Mwana wanga wamwamuna, iwe uli ndi ine nthawi zonse, ndipo zonse zimene ndiri nazo ziri zako.
  2477. Luk 15:32 Kudayenera kuti ife tisangalale, ndi kukondwera: pakuti m’ng’ono wako uyu adali wakufa, ndipo alinso ndi moyo; ndipo adatayika, ndipo wapezeka.
  2478. Luk 16:1 Ndipo iye adanenanso kwa wophunzira ake, Padali munthu wina mwini chuma, amene adali ndi kapitawo; ndipo yemweyu adanenezedwa kwa iye kuti adali kumwaza chuma chake.
  2479. Luk 16:2 Ndipo adamuyitana iye, ndipo anati kwa iye, Zitheka bwanji kuti ndikumva izi za iwe? Undiwerengere za ukapitawo wako; pakuti iwe ukhoza kusakhalabe kapitawo.
  2480. Luk 16:3 Kenaka kapitawo uyu adati mwa iye yekha, Ndidzachita chiyani ine? Pakuti mbuye wanga wandichotsera ukapitawo: Sindingalime; kupemphapempha ine ndichita manyazi.
  2481. Luk 16:4 Ndikonza chimene ine ndidzachita, kuti, pamene andichotsa pa ukapitawo, [anthu] akandilandire ine m’nyumba zawo.
  2482. Luk 16:5 Kotero adadziyitanira [kwa iye] aliyense wa mangawa a mbuye wake, ndipo anati kwa woyamba, Udakongola zochuluka bwanji kwa ambuye wanga?
  2483. Luk 16:6 Ndipo iye adati, mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye adati kwa iye, Tenga polembedwa ngongole, ndipo ukhale pansi msanga, ndipo ulembe makumi asanu.
  2484. Luk 16:7 Kenaka iye adati kwa wina, Ndipo iwe uli nawo mangawa wotani? Ndipo iye adati, Miyeso ya [mitanga] ya tirigu zana. Ndipo iye adanena kwa iye, Tenga polembedwa ngongole yako, ndipo ulembe makumi asanu ndi atatu.
  2485. Luk 16:8 Ndipo mbuyeyo adatama kapitawo wonyengayo, chifukwa iye adachita mwanzeru: pakuti ana a dziko lapansili ali mu mbadwo wawo anzeru koposa ana a kuwunika.
  2486. Luk 16:9 Ndipo ine ndinena kwa inu, Mudzipange nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti, pamene inu chikakusowani; iwo akalandira inu m’mahema wosatha.
  2487. Luk 16:10 Iye amene ali wokhulupirika mu chimene chili chaching’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu: ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’ono alinso wosalungama m’chachikulu.
  2488. Luk 16:11 Choncho ngati simunakhala wokhulupirika m’chuma chosalungama, ndani adzakudalirani kuyikiza kwa inu [chuma] chowona?
  2489. Luk 16:12 Ndipo ngati simudakhala wokhulupirika mu chimene chili chake cha munthu wina, adzakupatsani inu ndani zimene ziri za inu eni?
  2490. Luk 16:13 ¶Palibe wantchito angakhoze kutumikira ambuye awiri: pakuti kapena adzamuda mmodzi; ndi kukonda winayo; kapena adzakangamira kwa m’modzi, ndipo adzapeputsa winayo. Inu simungatumikire Mulungu ndi chuma.
  2491. Luk 16:14 Ndipo Afarisinso, amene adali wokonda ndalama, adamva zinthu izi zonse: ndipo iwo adamseka iye.
  2492. Luk 16:15 Ndipo iye adati kwa iwo, Inu ndinu iwo amene mudziyesera nokha wolungama pamaso pa anthu; koma Mulungu adziwa mitima yanu: pakuti chimene chilemekezedwa koposa pakati pa anthu ndi chonyansa pamaso pa Mulungu.
  2493. Luk 16:16 Chilamulo ndi aneneri [zidalipo] kufikira pa Yohane: kuyambira nthawi imeneyo ufumu wa Mulungu ulalikidwa, ndipo munthu aliyense akangamiza kulowamo.
  2494. Luk 16:17 Ndipo kuli kwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke, kusiyana ndikuti kansonga kalembo kamodzi kachilamulo kalephere.
  2495. Luk 16:18 Aliyense wosudzula mkazi wake, ndi kukwatira wina, achita chigololo: ndipo aliyense wokwatira amene wosudzulidwayo kwa mwamuna [wake], achita chigololo.
  2496. Luk 16:19 ¶Ndipo padali munthu wina mwini chuma, amene amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, ndipo anasekera nadyerera tsiku lirilonse:
  2497. Luk 16:20 Ndipo padali wopemphapempha wina dzina lake Lazarasi, amene adayikidwa pa chipata chake, wodzala ndi zilonda,
  2498. Luk 16:21 Ndipo adafuna kukhuta ndi nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pagome la mwini chumayo: koma sipokhapo agalunso anadza ndipo ananyambita zilonda zake;
  2499. Luk 16:22 Ndipo kudachitika, kuti wopemphayo adafa, ndipo adatengedwa ndi angelo kupita ku chifuwa cha Abrahamu: ndipo mwini chumayo adafanso, ndipo anayikidwa m’manda;
  2500. Luk 16:23 Ndipo mu nyanja ya moto adakweza maso ake, pokhala ali m’mazunzo, ndipo anawona Abrahamu patali, ndi Lazarasi m’chifuwa mwake.
  2501. Luk 16:24 Ndipo adakweza mawu ndipo anati, Atate Abrahamu, mundichitire ine chifundo, ndipo mutume Lazarasi, kuti aviyike nsonga ya chala chake m’madzi, ndi kuziziritsa lirime langa, pakuti ine ndizunzidwa m’lawi ili lamoto.
  2502. Luk 16:25 Koma Abrahamu adati, Mwana wamwamuna, kumbukira kuti iwe m’nthawi ya moyo wako udalandira zinthu zokoma zako, ndipo chimodzimodzinso Lazarasi zinthu zoyipa; koma tsopano iye atonthozedwa, koma iwe uzunzidwa.
  2503. Luk 16:26 Ndipo pambali pa izi zonse, pakati pa ife ndi inu pali phompho lalikulu lakhazikidwa: kotero kuti iwo wofuna kuwoloka kuchokera kuno kupita kwa inu sangathe; kapena sangawolokere kwa ife amene [angafune kubwera] kuchokera kwanuko.
  2504. Luk 16:27 Kenaka iye adati, choncho ine ndikupemphani inu, atate, kuti mumtume iye kunyumba ya atate wanga:
  2505. Luk 16:28 Pakuti ndiri nawo abale asanu; kuti achitire umboni kwa iwo, kuti mwina iwonso angadze ku malo ano a mazunzo.
  2506. Luk 16:29 Abrahamu adati kwa iye, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.
  2507. Luk 16:30 Ndipo iye adati, Iyayi, atate Abrahamu: koma ngati wina apita kwa iwo wochokera kwa akufa, iwo adzalapa.
  2508. Luk 16:31 Ndipo adati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, iwo sadzakopeka mtima, ngakhale wina akawuka kwa akufa.
  2509. Luk 17:1 Kenaka adati iye kwa wophunzira ake, Sikutheka koma kuti zolakwitsa zidzadza: koma tsoka [kwa iye], amene zidza kudzera mwa iye.
  2510. Luk 17:2 Kukadakhala kwabwino kwa iye kukolowekedwa mwala wa mphero mkhosi mwake, ndi kuponyedwa m’nyanja, kusiyana ndi kuti iye akhumudwitse m’modzi wa ang’ono awa.
  2511. Luk 17:3 ¶Kadzichenjerani mwa inu nokha: Ngati mbale wako akakuchimwira iwe, umdzudzule iye; ndipo ngati alapa, umkhululukire iye.
  2512. Luk 17:4 Ndipo ngati akuchimwira iwe kasanu ndi kawiri pa tsiku limodzi, ndipo nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena kuti, Ine ndalapa; Iwe uzimkhululukira iye.
  2513. Luk 17:5 Ndipo atumwi adati kwa Ambuye, Wonjezerani chikhulupiriro chathu.
  2514. Luk 17:6 Ndipo Ambuye adati, Ngati inu mukadakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu ka mpiru, mukadakhoza kunena kwa mtengo uwu wa mabulosi, Uzulidwe iwe ndi ku mizu, ndipo uwokedwe iwe m’nyanja; ndipo uyenera kumvera inu.
  2515. Luk 17:7 Koma ndani wa inu ali naye wantchito wolima, kapena woweta ng’ombe, adzanena kwa iye, pamene abwera iye nthawi yomweyo kuchokera kumunda, Pita ndi kukhala pansi kudya?
  2516. Luk 17:8 Ndipo makamaka wosanena naye, Undikonzere chimene ndiyenera kuti ndidye ine, ndipo udzimangire iwe mwini, ndipo unditumikire ine, kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya ndi kumwa iwe?
  2517. Luk 17:9 Kodi iye ayamika wantchitoyo chifukwa adachita zinthu zimene adalamulidwa iye? Ine sindiganiza choncho ayi.
  2518. Luk 17:10 Chotero chimodzimodzi inunso, m’mene inu mutachita zonse zimene adakulamulirani inu, nenani, Ife ndife antchito wosapindula: tangochita zimene zinali ntchito yathu yakuti tichite.
  2519. Luk 17:11 ¶Ndipo kudachitika, pamene amapita ku Yerusalemu, kuti iye adalikudutsa pakati pa Samariya ndi Galileya.
  2520. Luk 17:12 Ndipo m’mene adalowa iye m’mudzi wina, adakomana naye amuna khumi amene adali akhate, amene adayima kutali:
  2521. Luk 17:13 Ndipo iwo adakweza mawu [awo], ndipo ananena, Yesu, Mbuye, mutichitire ife chifundo.
  2522. Luk 17:14 Ndipo iye pakuwawona [iwo], adati kwa iwo, Pitani kadziwonetseni inu nokha kwa ansembe. Ndipo kudachitika, kuti, m’kupita kwawo, adayeretsedwa.
  2523. Luk 17:15 Ndipo m’modzi wa iwo, pamene anawona kuti adachiritsidwa, anabwerera m’mbuyo, ndipo ndi mawu akulu analemekeza Mulungu;
  2524. Luk 17:16 Ndipo adagwa nkhope [yake] pansi kumapazi ake, namyamika iye: ndipo iye adali Msamariya.
  2525. Luk 17:17 Ndipo Yesu poyankha anati, Kodi sadayeretsedwa khumi? Koma [ali] kuti asanu ndi anayi aja?
  2526. Luk 17:18 Sadapezeka wobwerera kudzalemekeza Mulungu, kupatula mlendo uyu.
  2527. Luk 17:19 Ndipo adati kwa iye, Nyamuka, nupite pa njira yako: chikhulupiriro chako chakupangitsa iwe kukhala wamphumphu.
  2528. Luk 17:20 ¶Ndipo pamene adamfunsa iye Afarisi, nthawi imene ufumu wa Mulungu uyenera kudza; iye adawayankha iwo ndipo anati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi mawonekedwe:
  2529. Luk 17:21 Kapena sadzanena, Onani [uli] pano! Kapena, onani [uwo] uko! Pakuti, tawonani, ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu.
  2530. Luk 17:22 Ndipo iye adati kwa wophunzirawo, Masiku adzadza, amene mudzakhumba kuwona limodzi la masiku a Mwana wamwamuna wa munthu, ndipo inu simudzaliwona [ilo].
  2531. Luk 17:23 Ndipo iwo adzanena kwa inu, Tawonani kuno; kapena, tawonani uko: musapita pambuyo pawo, kapena kuwatsata [iwo].
  2532. Luk 17:24 Pakuti monga mphenzi ing’anima kuchokera [mbali] imodzi ya pansi pa thambo, iwunika kufikira [mbali] ina pansi pa thambo; kotero adzakhalanso Mwana wamwamuna wa munthu m’tsiku lake.
  2533. Luk 17:25 Koma poyamba ayenera kumva zinthu zowawa zambiri; ndipo nakanidwa ndi m’badwo uwu.
  2534. Luk 17:26 Ndipo monga kudakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso m’masiku a Mwana wamwamuna wa munthu.
  2535. Luk 17:27 Iwo anadya, iwo adamwa, iwo adakwatira akazi, iwo adaperekedwa ku ukwati, kufikira tsiku lija Nowa adalowa m’chombo, ndipo chigumula chinadza, ndipo chinawawononga iwo onsewo.
  2536. Luk 17:28 Chimodzimodzinso kudakhala m’masiku a Loti; iwo anadya, iwo adamwa, iwo anagula, iwo adagulitsa, iwo adabzala, iwo adamanga nyumba;
  2537. Luk 17:29 Koma tsiku lomwero limene Loti adatuluka m’Sodomu udavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba, ndipo zidawawononga [iwo] onsewo.
  2538. Luk 17:30 Momwemo kudzakhala m’tsiku limene Mwana wamwamuna wa munthu adzavumbulutsidwa.
  2539. Luk 17:31 M’tsiku limenero, iye amene adzakhala pamwamba pa denga, ndi akatundu ake m’nyumba, asatsike kukazitenga: ndipo iye amene ali m’munda, chimodzimodzinso iye asabwere m’mbuyo.
  2540. Luk 17:32 Kumbukirani mkazi wa Loti.
  2541. Luk 17:33 Aliyense amene adzafuna kusunga moyo wake adzawutaya; koma aliyense adzataya moyo wake adzawusunga.
  2542. Luk 17:34 Ine ndikuwuzani inu, mu usiku umenewo padzakhala amuna awiri pakama m’modzi; m’modzi adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa.
  2543. Luk 17:35 Akazi awiri adzakhala akupera pamodzi; m’modzi adzatengedwa, ndipo wina adzasiyidwa.
  2544. Luk 17:36 Amuna [awiri] adzakhala m’munda; m’modzi adzatengedwa, ndipo wina adzasiyidwa.
  2545. Luk 17:37 Ndipo iwo adayankha ndipo ananena kwa iye, Kuti, Ambuye? Ndipo iye adati kwa iwo, Kulikonse kumene mtembo [uli], komwekonso miimba idzasonkhana pamodzi.
  2546. Luk 18:1 Ndipo iye adanena fanizo kwa iwo kumapeto ake, lakuti anthu ayenera kupemphera nthawi zonse, ndipo osafowoka mtima;
  2547. Luk 18:2 Nanena kuti, Mudali mumzinda woweruza, amene samawopa Mulungu, ndipo wosasamala munthu:
  2548. Luk 18:3 Ndipo mudali mkazi wamasiye mumzindamo; ndipo anadza kwa iye, nanena kuti, Mundiweruzire ine pa woyimbana nane mlandu.
  2549. Luk 18:4 Ndipo sadafuna kwa kanthawi: koma pambuyo pake iye adati mwa iye yekha, Ndingakhale ine sindiwopa Mulungu, kapena kusasamala munthu;
  2550. Luk 18:5 Tsono chifukwa chakuti mkazi wamasiye ameneyu akundivutitsa, ine ndidzamuweruzira mlandu, kuti mwina ndi kubwerabwera kwake angandilemetse ine.
  2551. Luk 18:6 Ndipo Ambuye adati, Tamverani chimene woweruza wosalungama anena.
  2552. Luk 18:7 Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo wosankhidwa ake, amene alirira usana ndi usiku kwa iye, ngakhale iye awalezera iwo mtima?
  2553. Luk 18:8 Ine ndikuwuzani inu kuti adzawachitira chilungamo mwachangu. Ngakhale ziri choncho pamene akudza Mwana wamwamuna wa munthu, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?
  2554. Luk 18:9 Ndipo adanenanso fanizo ili kwa ena amene adadzikhulupirira mwa iwo wokha kuti adali wolungama, ndipo anapeputsa ena:
  2555. Luk 18:10 Anthu awiri adakwera kupita ku kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi, ndi mzake wokhometsa msonkho.
  2556. Luk 18:11 Mfarisi adayimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ine ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu ena [ali], wopambapamba, wosalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu.
  2557. Luk 18:12 Ine ndimasala chakudya kawiri mu sabata, ine ndimapereka limodzi la khumi la zonse zimene ndikhala nazo.
  2558. Luk 18:13 Ndipo wa msonkhoyo, adayima patali, sadafuna kukweza koposa kotero maso [ake] kumwamba; koma adadziguguda pachifuwa pake, nanena kuti, Mulungu mundichitire chifundo ine wochimwa.
  2559. Luk 18:14 Ine ndikuwuzani inu, munthu uyu adatsikira kunyumba kwake wolungamitsidwa [osati] wina uja ayi: pakuti yense amene adzikuza yekha adzachepetsedwa; ndipo amene adzichepetsa yekha adzakwezedwa.
  2560. Luk 18:15 Ndipo anadza nawo kwa iye ana amakanda kuti iye awakhudze: koma pamene wophunzira [ake] adawona [izi], adawadzudzula iwo.
  2561. Luk 18:16 Koma Yesu adawayitanira [kwa iye], ndipo ananena, Lolani ana aang’ono adze kwa ine, ndipo musawaletsa iwo ayi: pakuti kwa wotere uli ufumu wa Mulungu.
  2562. Luk 18:17 Ndithudi ndinena kwa inu, Aliyense amene sadzalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono mwa njira iliyonse sadzalowamo ndithu.
  2563. Luk 18:18 Ndipo wolamulira wina adamfunsa iye, nanena kuti, Ambuye wabwino, kodi ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
  2564. Luk 18:19 Ndipo Yesu adati kwa iye, Unditcha ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, kupatula m’modzi, [ameneyo ndiye], Mulungu.
  2565. Luk 18:20 Iwe udziwa malamulo, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amayi wako.
  2566. Luk 18:21 Ndipo iye adati, Izi zonse ndazisunga kuyambira pa ubwana wanga.
  2567. Luk 18:22 Tsopano pamene Yesu adamva zinthu izi, adati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zonse zimene iwe uli nazo, ndipo uzigawire kwa osawuka; ndipo iwe udzakhala nacho chuma kumwamba: ndipo udze, unditsate ine.
  2568. Luk 18:23 Koma pamene adamva izi, adagwidwa ndi chisoni chambiri: pakuti adali wolemera kwambiri.
  2569. Luk 18:24 Ndipo pamene Yesu anawona kuti iye adali ndi chisoni chambiri, iye adati, Movutika motani kwa anthu eni chuma kulowa ufumu wa Mulungu!
  2570. Luk 18:25 Pakuti n’kwapafupi kwa ngamira kuti ipyole pa diso la singano, koposa kwa munthu wa chuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.
  2571. Luk 18:26 Ndipo iwo amene adamva [izi] adati, Ndani tsono angathe kupulumutsidwa?
  2572. Luk 18:27 Ndipo iye adati, Zinthu zimene ziri zosatheka ndi anthu ziri zotheka ndi Mulungu.
  2573. Luk 18:28 Pamenepo Petro adati, Onani, ife tasiya zonse, ndipo takutsatani inu.
  2574. Luk 18:29 Ndipo iye adati kwa iwo, Ndithudi ine ndinena kwa inu, Palibe munthu amene wasiya nyumba, kapena makolo, kapena abale, kapena mkazi, kapena ana, chifukwa cha ufumu wa Mulungu,
  2575. Luk 18:30 Amene sadzalandira zobwezedwa koposatu m’nthawi yino; ndipo m’nthawi iri nkudza moyo wosatha.
  2576. Luk 18:31 ¶Ndipo adadzitengera [kwa iye] khumi ndi awiriwo, ndipo anati kwa iwo, Tawonani, ife tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zinthu zonse zolembedwa ndi aneneri zokhudza Mwana wamwamuna wa munthu zidzakwaniritsidwa.
  2577. Luk 18:32 Pakuti iye adzaperekedwa kwa Amitundu, ndipo adzamnyoza, ndi kumchitira chipongwe, ndipo adzamthira malovu.
  2578. Luk 18:33 Ndipo adzamkwapula [iye], ndipo adzamupha iye: ndipo pa tsiku la chitatu iye adzawukanso.
  2579. Luk 18:34 Ndipo sadamvetsetsa kalikonse ka zinthu izi: ndi chonena ichi chidabisika kwa iwo, kapena sadadziwa iwo zinthu zimene zinalankhulidwazo.
  2580. Luk 18:35 ¶Ndipo kunachitika, kuti pamene iye adayandikira ku Yeriko, munthu wina wosawona adakhala m’mbali mwa njira napemphapempha:
  2581. Luk 18:36 Ndipo pakumva khamu la anthu lirinkudutsapo, iye adafunsa chimene chikutanthawuza?
  2582. Luk 18:37 Ndipo iwo adamuwuza iye, kuti Yesu wa ku Nazarete ali kudutsa apa.
  2583. Luk 18:38 Ndipo iye adafuwula, nanena kuti, Yesu, [inu] Mwana wamwamuna wa Davide, mundichitire ine chifundo.
  2584. Luk 18:39 Ndipo iwo wotsogolera adamdzudzula iye, kuti akhale bata: koma iye adafuwulitsa kwambiri, [Inu] Mwana wamwamuna wa Davide, mundichitire ine chifundo.
  2585. Luk 18:40 Ndipo Yesu adayima, ndipo analamulira kuti abwere naye kwa iye: ndipo m’mene adafika pafupi, adamfunsa iye,
  2586. Luk 18:41 Nanena kuti, Kodi ufuna kuti ine ndikuchitire chiyani iwe? Ndipo iye adati, Ambuye, kuti ndikhoze kulandira kupenya kwanga.
  2587. Luk 18:42 Ndipo Yesu adati kwa iye, Landira kupenya kwako: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.
  2588. Luk 18:43 Ndipo posakhalitsa iye adalandira kupenya kwake, ndipo anamtsata iye, nalemekeza Mulungu: ndipo anthu onse, pamene anawona [izi], adapereka matamando kwa Mulungu.
  2589. Luk 19:1 Ndipo [Yesu] adalowa ndipo anapyola kudutsa Yeriko.
  2590. Luk 19:2 Ndipo, tawonani, [padali] mwamuna wotchedwa Zakeyasi; amene adali mkulu wa wokhometsa misonkho, ndipo adali wachuma.
  2591. Luk 19:3 Ndipo iye adafuna kuwona Yesu amene iye adali; ndipo sadathe chifukwa cha khamu la anthu, chifukwa adali wamfupi msinkhu.
  2592. Luk 19:4 Ndipo adathamanga natsogola, ndipo anakwera mu mkuyu kuti amuwone iye; pakuti anali wakuti apita njira yomweyo.
  2593. Luk 19:5 Ndipo m’mene Yesu anadza pamalopo, adayang’ana m’mwamba, ndipo anamuwona iye, ndipo anati kwa iye, Zakeyasi, fulumira, ndipo utsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m’nyumba mwako.
  2594. Luk 19:6 Ndipo adafulumira, ndipo anatsika, ndi kumlandira iye wokondwera.
  2595. Luk 19:7 Ndipo m’mene iwo adachiwona [ichi], onse adang’ung’udza, nanena kuti, Iye adalowa kukhala mlendo kwa munthu amene ali wochimwa.
  2596. Luk 19:8 Ndipo Zakeyasi adayimirira, ndipo anati kwa Ambuye; Tawonani, Ambuye, theka limodzi la zanga zonse ine ndipatsa kwa osawuka; ndipo ngati ndidatenga kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ine ndidzambwezera [iye] kanayi.
  2597. Luk 19:9 Ndipo Yesu adati kwa iye, Lero chipulumutso chafika ku nyumba iyi, monga muli kwakuti iyenso ndiye mwana wamwamuna wa Abrahamu.
  2598. Luk 19:10 Pakuti Mwana wamwamuna wa munthu wadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.
  2599. Luk 19:11 Ndipo pamene iwo adamva izi, iye adawonjeza ndipo ananena fanizo, chifukwa adali iye pafupi ndi Yerusalemu, ndi chifukwa iwo adaganiza kuti ufumu wa Mulungu uyenera kuwoneka nthawi yomweyo.
  2600. Luk 19:12 Choncho iye adati, Munthu wina womveka adanka ku dziko lakutali kukadzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerera.
  2601. Luk 19:13 Ndipo adayitana antchito ake khumi, ndipo anawapatsa iwo ndalama khumi, ndipo anati kwa iwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.
  2602. Luk 19:14 Koma mbadwa za pa mudzi pake zidamuda iye, ndipo zinatumiza uthenga kumtsata m’mbuyo, kunena kuti, Ife sitifuna [munthu] uyu atilamulire ife.
  2603. Luk 19:15 Ndipo kunachitika, kuti iye atabwerera, atalandira ufumuwo, kenaka adalamula antchito aja ayitanidwe kwa iye, kwa iwo amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo aliyense adapindulira pochita malonda.
  2604. Luk 19:16 Pamenepo adafika woyamba, nanena kuti, Mbuye ndalama yanu yapindula ndalama khumi,
  2605. Luk 19:17 Ndipo iye adati kwa iye, Chabwino, iwe mtumiki wabwino: chifukwa iwe udakhala wokhulupirika m’chachin’gono, khala nawo ulamuliro pa mizinda khumi.
  2606. Luk 19:18 Ndipo wachiwiri adadza, nanena kuti, Mbuye ndalama yanu yapindula ndalama zisanu.
  2607. Luk 19:19 Ndipo adanena chimodzimodzi kwa iyenso, Khala iwenso woweruza mizinda isanu.
  2608. Luk 19:20 Ndipo wina adadza, nanena kuti, Mbuye, tawonani, [siyi] ndalama yanu imene ine ndayisunga m’kansalu:
  2609. Luk 19:21 Pakuti ndidakuwopani, chifukwa inu ndinu munthu wowuma mtima: inu munyamula chimene simudachiyika pansi, ndipo mututa chimene simudafesa.
  2610. Luk 19:22 Ndipo adanena kwa iye, Kuchokera pakamwa pako ine ndikuweruza iwe, [iwe] mtumiki woyipa. Iwe udadziwa kuti ine ndine munthu wowuma mtima, wonyamula chimene sindinachiyika pansi, ndi kututa chimene sindinafesa:
  2611. Luk 19:23 Mwa ichi tsono sudapereka bwanji ndalama yanga kosungitsa ndalama, kuti pakudza kwanga ine ndikhoze kukayitenga ndi phindu lake?
  2612. Luk 19:24 Ndipo adati kwa iwo akuyimirapo, Tengani kwa iye ndalamayo, ndipo mupatse [iyo] kwa iye ali nazo ndalama khumi.
  2613. Luk 19:25 (Ndipo iwo adati kwa iye, Ambuye, ali nazo ndalama khumi.)
  2614. Luk 19:26 Pakuti ine ndinena kwa inu, Kuti aliyense amene adzakhala nacho kudzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, ngakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.
  2615. Luk 19:27 Koma adani anga awo, amene wosafuna kuti ine ndidzakhale mfumu yawo, bwerani nawo kuno, ndipo muwaphe [iwo] pamaso panga.
  2616. Luk 19:28 ¶Ndipo m’mene adanena motero, iye adawatsogolera nakwera kunka ku Yerusalemu.
  2617. Luk 19:29 Ndipo kudachitika, pamene iye adayandikira ku Betefage ndi Betane, pa phiri lotchedwa [phiri la] ma Olivi, iye adatuma awiri a wophunzira ake.
  2618. Luk 19:30 Nanena kuti, Pitani ku mudzi uli pandunji [panu]; m’menemo pakulowa kwanu mudzapeza mwana wabulu womangidwa, amene pa iye palibe munthu adakhalapo: mum’masule iye, ndipo mubwere [naye kuno].
  2619. Luk 19:31 Ndipo munthu aliyense afunsa inu, Mum’masuliranji [iye]? Mudzatero kunena naye, Chifukwa Ambuye amfuna iye.
  2620. Luk 19:32 Ndipo iwo amene adatumidwawo anapita pa njira yawo, ndipo anapeza monga adanena kwa iwo.
  2621. Luk 19:33 Ndipo pamene anali kum’masula mwana wa buluyo, eni ake adati kwa iwo, Mum’masuliranji mwana wa bulu?
  2622. Luk 19:34 Ndipo iwo adati, Ambuye amfuna iye.
  2623. Luk 19:35 Ndipo adadza naye kwa Yesu; ndipo adayalika zovala zawo pa mwana wa buluyo, ndipo anakwezapo Yesu.
  2624. Luk 19:36 Ndipo pamene anali kupita iye, iwo adayala zovala zawo m’njiramo.
  2625. Luk 19:37 Ndipo pamene iye anayandikira, ngakhale tsopano potsetsereka pake pa phiri la Azitona, khamu lonse la wophunzira lidayamba kukondwera ndi kutamanda Mulungu ndi mawu akulu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu adaziwona;
  2626. Luk 19:38 Nanena kuti, Wodalitsika [akhale] Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye: mtendere kumwamba, ndi ulemerero m’mwambamwamba.
  2627. Luk 19:39 Ndipo Afarisi ena a m’khamu la anthu adati kwa iye, Ambuye, dzudzulani wophunzira anu.
  2628. Luk 19:40 Ndipo iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Ine ndikuwuzani inu kuti, ngati awa akhala chete, miyala idzafuwula nthawi yomweyo.
  2629. Luk 19:41 ¶Ndipo m’mene adayandikira, adawona mzindawo, ndipo analirira pa iwo.
  2630. Luk 19:42 Nanena kuti, Ngati iwe ukadadziwa, ngakhale iwe, m’tsiku lako ili, zinthu [zomwe] ziri zako za mtendere wako! Koma tsopano zibisika pamaso pako.
  2631. Luk 19:43 Pakuti masiku adzadza pa iwe, kuti adani ako adzakuzingira dzenje lokuzungulira iwe, ndipo adzakuzungulira iwe, ndipo adzakutsekerezera iwe mkati mbali zonse,
  2632. Luk 19:44 Ndipo adzakugoneka iwe ngakhale pansi, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala umodzi pa unzake; chifukwa iwe sudazindikira nyengo yakuyenderedwa kwako.
  2633. Luk 19:45 Ndipo iye adalowa m’kachisi, ndipo anayamba kutulutsa iwo akugulitsamo ndi iwo amene amagula;
  2634. Luk 19:46 Nanena kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga ndi nyumba yakupemphereramo: koma inu mwapanga iyo phanga la mbava.
  2635. Luk 19:47 Ndipo iye adalikuphunzitsa m’kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe akulu ndi alembi ndi akulu a anthu adafunafuna kumuwononga iye,
  2636. Luk 19:48 Ndipo sadapeza chimene iwo akadakhoza kuchita: pakuti anthu onse adali ndi chidwi chakumva iye.
  2637. Luk 20:1 Ndipo kudachitika, [kuti] pa limodzi la masiku awo, m’mene iye adalikuphunzitsa anthu m’kachisi, ndi kulalikira uthenga wabwino, ansembe akulu ndi alembi adadza kwa [iye] ndi akulu a anthu.
  2638. Luk 20:2 Ndipo adalankhula kwa iye, nanena kuti, Mutiwuze ife, muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene adakupatsani ulamuliro umenewu?
  2639. Luk 20:3 Ndipo iye adayankha ndipo anati kwa iwo, Ine ndidzakufunsani inenso chinthu chimodzi, ndipo mundiyankhe ine.
  2640. Luk 20:4 Ubatizo wa Yohane, udachokera kumwamba kodi, kapena kwa anthu?
  2641. Luk 20:5 Ndipo adafunsana mwa iwo wokha, nanena kuti, Ngati ife tidzanena, Udachokera kumwamba; iye adzati, chifukwa ninji inu simudamkhulupirira?
  2642. Luk 20:6 Koma ngati tinena, Kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala ife: pakuti iwo adakopeka mtima kuti Yohane adali mneneri.
  2643. Luk 20:7 Ndipo iwo adayankha, kuti iwo sakadatha kunena kumene [udachokera].
  2644. Luk 20:8 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ndingakhale inenso sindikuwuzani za ulamuliro ndichita zinthu izi.
  2645. Luk 20:9 Kenaka iye adayamba kunena kwa anthu fanizo ili; Munthu wina adalima munda wa mphesa, ndipo anawukongoletsa kwa wolima munda, ndipo anapita kudziko la kutali nagonerako nthawi yayitali.
  2646. Luk 20:10 Ndipo pa nyengoyo adatumiza wantchito kwa wolima mundawo, kuti ampatseko chipatso chamunda wa mphesawo: koma wolimawo adampanda iye, ndipo anampitikitsa [iye] wopanda kanthu.
  2647. Luk 20:11 Ndipo adatumizanso wantchito wina: ndipo iyenso adampanda, ndipo anamchitira [iye] mwachipongwe, ndipo nampitikitsa [iye] wopanda kanthu.
  2648. Luk 20:12 Ndipo adatumizanso wina wa chitatu: ndipo iyenso adamvulaza, ndipo anamtaya [iye] kunja.
  2649. Luk 20:13 Kenaka adati mbuye wa munda wa mphesawo, Ine ndidzachita chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna amene ndimkonda: zikhoza kukhala kuti iwo kapena adzamchitira [iye] ulemu pamene amuwona iye.
  2650. Luk 20:14 Koma pamene wolimawo mundawo adamuwona iye, adafunsana maganizo pakati pawo, nanena kuti, Uyu ndiye wolandira cholowa: tiyeni ife timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.
  2651. Luk 20:15 Kotero iwo adamponya iye kunja kwa mundawo, ndipo anamupha [iye]. Choncho mwini munda wa mphesawo adzawachitira chiyani?
  2652. Luk 20:16 Iye adzafika ndipo adzawononga wolima munda aja, ndipo adzapatsa munda wa mphesa kwa ena. Ndipo pamene iwo adamva izi, adati, Mulungu akukaniza.
  2653. Luk 20:17 Koma iye adawapenya iwo, ndipo anati, Nchiyani ichi tsono chimene chidalembedwa, Mwala umene womanga nyumba adawukana, womwewo udakhala mutu wa pangodya.
  2654. Luk 20:18 Aliyense adzagwa pa mwala umenewo, adzaphwanyika; koma pa aliyense amene udzamgwera, udzamupera iye monga ufa.
  2655. Luk 20:19 ¶Ndipo alembi ndi ansembe akulu ora lomwero adafunafuna kumgwira iye; ndipo iwo adawopa anthu: pakuti adazindikira kuti adanena fanizo ili kutsutsa iwo.
  2656. Luk 20:20 Ndipo adamyang’anira [iye], ndipo anatumiza azondi, amene adadziwonetsera ngati anthu wolungama mtima, kuti akakhoze kumkola pa mawu ake, kotero kuti akampereke iye kwa akulu ndi a ulamuliro wa kazembe.
  2657. Luk 20:21 Ndipo iwo adamfunsa iye, nanena kuti, Ambuye, ife tidziwa kuti inu munena ndi kuphunzitsa kolondola, komanso kusasamalira nkhope ya munthu [aliyense], koma muphunzitsa njira ya Mulungu mowona:
  2658. Luk 20:22 Kodi nkuloledwa mwachilamulo kwa ife kupereka msonkho kwa Kayisara, kapena ayi?
  2659. Luk 20:23 Koma iye adazindikira chinyengo chawo, ndipo anati kwa iwo, Chifukwa chiyani inu mukundiyesa ine?
  2660. Luk 20:24 Tandiwonetsani ine khobiri. Chithunzithunzi ndi cholemba chake nchayani? Iwo adayankha ndipo anati, cha Kayisara.
  2661. Luk 20:25 Ndipo iye adati kwa iwo, choncho perekani kwa Kayisara zinthu zimene ziri zake za Kayisara, ndi kwa Mulungu zinthu zimene ziri zake za Mulungu.
  2662. Luk 20:26 Ndipo iwo sadakhoza kugwira mawu ake pamaso pa anthu: ndipo adazizwa ndi yankho lake, ndipo anakhala bata.
  2663. Luk 20:27 ¶Ndipo anadza kwa [iye] ena a Asaduki, amene amakana kuti pali kuwuka kwa akufa; ndipo adamfunsa iye,
  2664. Luk 20:28 Nanena kuti, Ambuye, Mose adalembera kwa ife, Ngati mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo afa alibe ana iye, kuti mbale wake azitenga mkazi wakeyo, ndi kuwukitsira mbewu kwa mbale wakeyo.
  2665. Luk 20:29 Choncho padali abale asanu ndi awiri: ndipo woyamba adatenga mkazi, ndipo anafa wopanda ana.
  2666. Luk 20:30 Ndipo wachiwiri adamtenga mkaziyo kukhala mkazi wake, ndipo adafa, wopanda ana.
  2667. Luk 20:31 Ndipo wachitatu adamtenga mkaziyo; ndipo choteronso wachisanu ndi chiwirinso: ndipo iwo sadasiya ana, ndipo anamwalira.
  2668. Luk 20:32 Pomaliza pa zonse adamwaliranso mkaziyo.
  2669. Luk 20:33 Choncho pa kuwuka kwa akufa iye adzakhala mkazi wayani wa iwo? Pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.
  2670. Luk 20:34 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira, ndipo aperekedwa ku ukwati;
  2671. Luk 20:35 Koma iwo akuyesedwa woyenera kulandira dziko lijalo, ndi kuwuka kwa akufa, sakwatira, kapena kukwatiwa;
  2672. Luk 20:36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse: pakuti afanana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuwuka kwa akufa.
  2673. Luk 20:37 Tsopano popeza kuti akufa awuka, ngakhale Mose adasonyeza pa chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.
  2674. Luk 20:38 Pakuti iye sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.
  2675. Luk 20:39 ¶Ndipo ena a alembi adayankha nati, Mphunzitsi, inu mwanena bwino.
  2676. Luk 20:40 Ndipo pakutha pa izi iwo sadalimbanso mtima kumfunsanso iye [funso] lina.
  2677. Luk 20:41 Koma iye adati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristu ali Mwana wamwamuna wa Davide?
  2678. Luk 20:42 Ndipo Davide mwini yekha anena m’buku la Masalmo, Ambuye adanena kwa Ambuye wanga, Khala iwe pa dzanja langa lamanja,
  2679. Luk 20:43 Kufikira ine ndidzayika adani ako poyika pa mapazi ako.
  2680. Luk 20:44 Choncho Davide adamtchula iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake wamwamuna bwanji?
  2681. Luk 20:45 ¶Kenaka anthu onse adalinkumva iye adati kwa wophunzira ake,
  2682. Luk 20:46 Chenjerani nawo alembi, amene afuna kuyendayenda wovala mwinjiro, ndipo akonda kulonjeredwa m’misika, ndi mipando ya ulemu m’masunagoge, ndi malo a magome apamwamba kwambiri pa maphwando;
  2683. Luk 20:47 Amene alusira nyumba za akazi amasiye, ndipo mwachiwonetsero achita mapemphero atali: omwewo adzalandira kulanga koposa.
  2684. Luk 21:1 Ndipo iye adayang’ana kumwamba, ndipo anawona anthu eni chuma alikuyika mphatso zawo mosungiramo ndalama.
  2685. Luk 21:2 Ndipo iye adawona mkazi wina wamasiye waumphawi akuyika momwemo tindalama tiwiri.
  2686. Luk 21:3 Ndipo iye adati, Zowonadi ndinena kwa inu, kuti wamasiye waumphawi uyu wayikamo koposa iwo onse:
  2687. Luk 21:4 Pakuti onse amenewa mwa kuchuluka kwawo adayika pa zoperekazo za Mulungu: koma iye mwa kusowa kwake wayikamo zonse za moyo wake zimene adali nazo.
  2688. Luk 21:5 ¶Ndipo pamene ena adalikunena za kachisi, momwe adakongoletsedwera ndi miyala yabwino ndi mphatso, iye adati,
  2689. Luk 21:6 [Za] zinthu izi zimene mukuziwona, masiku adzafika, amene sudzasiyidwa mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa pansi.
  2690. Luk 21:7 Ndipo iwo adamfunsa iye, nanena kuti, Ambuye, koma nanga zidzawoneka liti zinthu izi? Ndipo chizindikiro chake [chidzakhala] chiyani pamene zinthu izi ziti zidzachitike?
  2691. Luk 21:8 Ndipo iye adati, Yang’anirani kuti musanyengedwe; pakuti ambiri adzadza m’dzina langa, nadzanena kuti, Ine ndine [Khristu], ndipo nthawi yayandikira: choncho inu musawatsate iwo pambuyo pawo.
  2692. Luk 21:9 Koma pamene inu mudzamva za nkhondo ndi kuwukira a maulamuliro, musawopsedwe: pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.
  2693. Luk 21:10 Kenaka adanena iye kwa iwo, Mtundu udzawukira mtundu, ndipo ufumu kuwukira ufumu.
  2694. Luk 21:11 Ndipo zivomezi zazikulu zidzakhala m’malo osiyanasiyana, ndi njala ndi miliri: ndipo kudzakhala zowopsa zowoneka ndi zizindikiro zazikulu zidzakhala zochokera kumwamba.
  2695. Luk 21:12 Koma zisadachitike zonse izi, iwo adzakuthirani manja inu, ndipo adzakuzunzani [inu], kukuperekani [inu] ku masunagoge, ndi ku ndende, nadzakuperekani inu kwa mafumu ndi wolamula chifukwa cha dzina langa.
  2696. Luk 21:13 Ndipo zidzasandulika kwa inu chifukwa cha umboni.
  2697. Luk 21:14 Choncho tsimikizani [izi] mumtima mwanu, kuti musalingalire chimene inu mudzayankha:
  2698. Luk 21:15 Pakuti ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzitsutsa kapena kuzikaniza.
  2699. Luk 21:16 Ndipo mudzaperekedwa ndi akukubalani, ndi abale, ndi afuko lanu, ndi abwenzi; ndipo [ena] a inu adzakupangitsani kuti muphedwe.
  2700. Luk 21:17 Ndipo inu adzakudani anthu onse chifukwa cha dzina langa.
  2701. Luk 21:18 Koma sipadzakhala tsitsi limodzi la pamutu panu lidzawonongeka.
  2702. Luk 21:19 M’chipiriro chanu sungani inu moyo wanu.
  2703. Luk 21:20 Ndipo pamene mudzawona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a nkhondo, pamenepo zindikirani kuti chipulumutso chake chayandikira.
  2704. Luk 21:21 Pamenepo iwo amene ali m’Yudeya athawire kumapiri; ndi iwo ali mkati mwa uwo anyamuke kutuluka; ndi iwo amene ali kumilaga asalowemo.
  2705. Luk 21:22 Pakuti amenewa akhala masiku akubwezera, kuti zinthu zonse zimene zalembedwa zikwaniritsidwe.
  2706. Luk 21:23 Koma tsoka iwo akukhala ndi mwana, ndi iwo amene akuyamwitsa, m’masiku awo! Pakuti padzakhala chisawuko chachikulu m’dziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.
  2707. Luk 21:24 Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, ndipo adzagwidwa undende kumka ku mitundu yonse: ndipo Yerusalemu adzaponderezedwa ndi mapazi a anthu Amitundu, kufikira nthawi zawo za Amitundu zakwaniritsidwa.
  2708. Luk 21:25 ¶Ndipo kudzakhala zizindikiro mu dzuwa, ndi mu mwezi, ndi mu nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisawuko cha mitundu ya anthu, ndi othedwa nzeru; ndi pa nyanja ndi mafunde mkokomo;
  2709. Luk 21:26 Mitima ya anthu kukomoka ndi mantha, ndi chifukwa cha kuyembekezera zinthu zirinkundza pa dziko lapansi; pakuti mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.
  2710. Luk 21:27 Ndipo kenaka adzawona Mwana wamwamuna wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero wawukulu.
  2711. Luk 21:28 Ndipo pamene zinthu izi ziyamba kuchitika, pamenepo yang’anani kumwamba, ndipo tukulani mitu yanu; pakuti chiwomboledwe chanu chayandikira.
  2712. Luk 21:29 Ndipo adanena kwa iwo fanizo; Onani mtengo wa mkuyu ndi mitengo yonse;
  2713. Luk 21:30 Pamene iyo iphuka tsopano, inu muyipenya ndi kudziwa pa inu eni kuti nyengo yotentha ili pafupi tsopano.
  2714. Luk 21:31 Kotero chimodzimodzi inunso, pamene muwona zinthu izi zirikuchitika, dziwani inu kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.
  2715. Luk 21:32 Ndithudi ndinena kwa inu, Mbadwo uwu sudzapita, kufikira zonse zitakwaniritsidwa.
  2716. Luk 21:33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mawu anga sadzapita.
  2717. Luk 21:34 ¶Ndipo mudziyang’anire inu nokha, kuti mwina mitima yanu ingalemetsedwe kwambiri ndi kukhuta moposera, ndi kuledzera, ndi zisamaliro za moyo uno, ndipo [kotero] kuti tsiku ilo lingafikire pa inu modzidzimutsa.
  2718. Luk 21:35 Pakuti ngati msampha lidzafikira anthu onse amene akukhala pa nkhope pa dziko lonse lapansi.
  2719. Luk 21:36 Choncho dikirani, ndipo pempherani nthawi zonse, kuti inu mudzakhoze kukhala woyesedwa woyenera kupulumuka ku zinthu izi zonse zimene zidzachitika, ndi kuyimirira pamaso pa Mwana wamwamuna wa munthu.
  2720. Luk 21:37 Ndipo usana iye adalikuphunzitsa m’kachisi; ndi usiku amatuluka, ndi kugona pa phiri lotchedwa [phiri la] ma Olivi.
  2721. Luk 21:38 Ndipo anthu onse adalawirira m’mamawa kudza kwa iye m’kachisi kudzamvera iye.
  2722. Luk 22:1 Tsopano phwando la mikate yopanda chofufumitsa lidayandikira, limene litchedwa Paskha.
  2723. Luk 22:2 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adafunafuna momwe akadamuphera iye; pakuti adawopa anthuwo.
  2724. Luk 22:3 ¶Kenaka Satana adalowa mwa Yudasi wonenedwa Isikariyote, pokhala mmodzi wa khumi ndi awiriwo.
  2725. Luk 22:4 Ndipo iye adapita pa njira yake, ndipo anayankhulana ndi ansembe akulu ndi akazembe, momwe iye akadakhoza kumperekera kwa iwo.
  2726. Luk 22:5 Ndipo iwo adakondwera, ndipo anapangana naye kumpatsa iye ndalama.
  2727. Luk 22:6 Ndipo iye adalonjeza, ndipo anafunafuna mpata wakumpereka iye kwa iwo palibe khamulo.
  2728. Luk 22:7 ¶Kenaka lidafika tsiku la mikate yopanda chofufumitsa, pamene paskha ayenera kuphedwa.
  2729. Luk 22:8 Ndipo iye adatumiza Petro ndi Yohane, nanena kuti, Pitani ndipo mutikonzere ife paskha, kuti ife tidye.
  2730. Luk 22:9 Ndipo iwo adanena kwa iye, Mufuna tikakonzere kuti?
  2731. Luk 22:10 Ndipo iye adati kwa iwo, Tawonani, pamene mutalowa mumzinda, adzakomana ndi inu bambo atasenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.
  2732. Luk 22:11 Ndipo mukanene kwa mbuye wa nyumbayo, Mphunzitsi anena kwa iwe, chipinda cha alendo chili kuti, kumene ndikadya paskha pamodzi ndi wophunzira anga?
  2733. Luk 22:12 Ndipo iyeyo adzakuwonetsani chipinda chachikulu chapamwamba chokonzeka: mukakonzere kumeneko.
  2734. Luk 22:13 Ndipo adapita iwo, ndipo anapeza monga iye adanena kwa iwo: ndipo iwo adakonzekera paskha.
  2735. Luk 22:14 Ndipo ora lake litadza, iye adakhala pansi, ndi atumwi khumi ndi awiri pamodzi naye.
  2736. Luk 22:15 Ndipo iye adati kwa iwo, Ndichilakolako ine ndalakalaka kudya paskha uyu pamodzi ndi inu ine ndisanasawutsidwe:
  2737. Luk 22:16 Pakuti ine ndinena kwa inu, Ine sindidzadyakonso izo, kufikira udzakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.
  2738. Luk 22:17 Ndipo adatenga chikho, ndipo adayamika, ndipo adati; Tengani ichi, ndipo mugawane [ichi] pakati pa inu nokha.
  2739. Luk 22:18 Pakuti ine ndinena kwa inu, Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira ufumu wa Mulungu udzafika.
  2740. Luk 22:19 ¶Ndipo iye adatenga mkate, ndipo anayamika, ndipo adawunyema [uwo], ndipo anapereka kwa iwo, nanena kuti, Ili ndi thupi langa limene lapatsidwa chifukwa cha inu: ichi chitani kukumbukira ine.
  2741. Luk 22:20 Chimodzimodzinso chikho atatha mgonero, nanena kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga, umene wathiridwa chifukwa cha inu.
  2742. Luk 22:21 ¶Koma, tawonani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ine [liri] pamodzi ndi ine pagome pano.
  2743. Luk 22:22 Ndipo zowonadi Mwana wamwamuna wa munthu amukatu, monga kudayikidwiratu: koma tsoka kwa munthuyo amene mwa iye adzaperekedwa!
  2744. Luk 22:23 Ndipo adayamba kufunsana mwa iwo wokha, ndiye yani mwa iwo amene anayenera kuchita ichi.
  2745. Luk 22:24 ¶Ndipo kudakhalanso kutsutsana pakati pa iwo, ndani wa iwo ayenera kuyesedwa wamkulu.
  2746. Luk 22:25 Ndipo iye adati kwa iwo, Mafumu a anthu Amitundu achitira ufumu pa iwo; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa ochitira ena zabwino.
  2747. Luk 22:26 Koma inu simudzakhala wotero: koma iye amene ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali mfumu, ngati iye amene atumikira.
  2748. Luk 22:27 Pakuti [ali] wamkulu ndani, iye wakukhala pa chakudya, kapena wotumikirapo? Si [ndiye] wakukhala pa chakudya kodi? Koma ine ndiri pakati pa inu monga ngati iye wotumikira.
  2749. Luk 22:28 Inu ndinu amene mudakhala ndi ine m’mayesero anga.
  2750. Luk 22:29 Ndipo ine ndiyika kwa inu ufumu, monganso Atate wanga adayikira kwa ine,
  2751. Luk 22:30 Kuti mukadye ndi kumwa pa gome langa mu ufumu wanga; ndi kukhala pa mipando ya chifumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
  2752. Luk 22:31 ¶Ndipo Ambuye adati, Simoni, Simoni, tawona, Satana wakhumba [kukutenga iwe], kuti akusefe [iwe] ngati tirigu:
  2753. Luk 22:32 Koma ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chingazime: ndipo pamene iwe watembenuka ulimbikitse abale ako.
  2754. Luk 22:33 Ndipo iye adati kwa iye, Ambuye, ine ndiri wokonzeka kupita ndi inu, kulowa kundende, ndi ku imfa.
  2755. Luk 22:34 Ndipo iye adati, Ine ndikuwuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino, m’mbuyo mwakuti iwe utandikana ine katatu, kuti sundidziwa ine.
  2756. Luk 22:35 Ndipo iye adati kwa iwo, Pamene ine ndidakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, ndi thumba, ndi nsapato, mudasowa kanthu kalikonse kodi? Ndipo iwo adanena, Palibe.
  2757. Luk 22:36 Kenaka iye adati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, iye alitenge [ilo], ndipo chimodzimodzi thumba la kamba [lake]: ndipo iye amene alibe lupanga, iye agulitse chovala chake, ndipo agule limodzi.
  2758. Luk 22:37 Pakuti ine ndinena kwa inu, kuti ichi ndi chimene chidalembedwa chiyenera kukhala chokwaniritsidwa mwa ine, Ndipo iye adawerengedwa ndi anthu wophwanya lamulo: pakuti zinthu zokhudza ine ziri ndi mapeto.
  2759. Luk 22:38 Ndipo iwo adati, Ambuye, tawonani, awa malupanga awiri, Ndipo iye adati kwa iwo, Chakwanira.
  2760. Luk 22:39 ¶Ndipo iye adatuluka, ndipo anapita, monga iye adazolowera, ku phiri la ma Olivi; ndipo wophunzira ake adamtsatanso iye.
  2761. Luk 22:40 Ndipo pamene anali pamalopo, iye adati kwa iwo, Pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa.
  2762. Luk 22:41 Ndipo iye adadzipatula kuchoka kwa iwo kutalika kwake ngati kuponya mwala, ndipo anagwada pansi, ndipo anapemphera.
  2763. Luk 22:42 Nanena kuti, Atate, ngati inu mufuna, chotsani chikho ichi kwa ine: chomwechobe sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu, kuchitike.
  2764. Luk 22:43 Ndipo adawonekera mngelo kwa iye wochokera kumwamba, kumlimbikitsa iye.
  2765. Luk 22:44 Ndipo pokhala iye mu ululu wowopsa adapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake lidakhala ngati madontho akulu a mwazi ali nkugwa pansi.
  2766. Luk 22:45 Ndipo pamene adanyamuka kuchoka pakupemphera, ndipo anadza kwa wophunzira ake, anawapeza iwo akugona chifukwa cha chisoni,
  2767. Luk 22:46 Ndipo adati kwa iwo, Inu mugoneranji? Nyamukani ndipo pempherani, kuti mwina inu mungalowe m’kuyesedwa.
  2768. Luk 22:47 ¶Ndipo iye ali chiyankhulire, tawonani khamu, ndipo iye wotchedwa Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, adawatsogolera, ndipo anayandikira kwa Yesu kumpsopsona iye.
  2769. Luk 22:48 Koma Yesu adati kwa iye, Yudasi, ulikupereka Mwana wamwamuna wa munthu ndi chimpsopsono?
  2770. Luk 22:49 Pamene iwo amene adali kumzinga iye adawona chimene chiti chitsatire, adati kwa iye, Ambuye, ife tikanthe ndi lupanga kodi?
  2771. Luk 22:50 ¶Ndipo m’modzi wa iwo adakantha wantchito wa mkulu wansembe, ndipo anamdula khutu lake lamanja.
  2772. Luk 22:51 Ndipo Yesu adayankha ndipo anati, Lolani inu kufikira kumene. Ndipo adakhudza khutu lake, ndipo anamchiritsa iye.
  2773. Luk 22:52 Kenaka Yesu adati kwa ansembe akulu, ndi akapitawo a kachisi, ndi akulu, amene anadza kwa iye, Inu mudatuluka kudza, monga ngati mugwira wakuba, ndi malupanga ndi zindodo kodi?
  2774. Luk 22:53 Pamene ine ndidali ndi inu masiku onse m’kachisi, inu simudatansa manja anu kundigwira ine; koma ili ndi ora lanu, ndi ulamuliro wa mdima.
  2775. Luk 22:54 ¶Kenaka iwo adamtenga iye, ndipo anapita naye [iye], ndipo anabwera naye kulowa m’nyumba ya mkulu wa ansembe. Ndipo Petro adamtsata patali.
  2776. Luk 22:55 Ndipo pamene adasonkha moto m’kati mwa bwalo, ndipo atakhala pansi pamodzi, Petro adakhala pansi pakati pawo.
  2777. Luk 22:56 Ndipo mdzakazi wina adamuwona iye alikukhala pafupi ndi moto, ndipo anampenyetsetsa iye, ndipo anati, Munthu uyunso adali naye.
  2778. Luk 22:57 Koma iye adamkana iye, nanena kuti, Mkaziwe, ine sindimudziwa iye.
  2779. Luk 22:58 Ndipo patapita kamphindi wina adamuwona, ndipo anati, Iwenso uli wa iwo. Ndipo Petro adati, Munthu iwe, sindine ayi.
  2780. Luk 22:59 Ndipo patapita ngati ora limodzi wina motsimikiza adanenetsa, nanena kuti, Zowonadi [munthu] uyunso adali naye: pakuti ndiye Mgalileya.
  2781. Luk 22:60 Ndipo Petro adati, Munthu iwe, ine sindidziwa chimene iwe uchinena. Ndipo posakhalitsa, iye ali chiyankhulire tambala adalira.
  2782. Luk 22:61 Ndipo Ambuye adatembenuka, ndipo anayang’ana pa Petro. Ndipo Petro adakumbukira mawu a Ambuye, momwe adanena kwa iye, Asadalire tambala, iwe udzandikana ine katatu.
  2783. Luk 22:62 Ndipo Petro adatuluka, ndipo analira mowawidwa [mtima].
  2784. Luk 22:63 ¶Ndipo amuna amene adalikusunga Yesu adam’nyoza iye, ndipo anampanda [iye].
  2785. Luk 22:64 Ndipo pamene iwo adammanga iye m’maso, anampanda iye kumaso, ndipo anamfunsa iye, nanena kuti, Nenera, ndani amene wakupanda iwe?
  2786. Luk 22:65 Ndipo zinthu zina zambiri momchitira mwano adam’nenera iye.
  2787. Luk 22:66 ¶Ndipo pamene kudangocha, akulu a anthu ndi ansembe akulu ndi alembi adasonkhana pamodzi, ndipo adapita naye ku bwalo lawo, nanena kuti,
  2788. Luk 22:67 Kodi iwe uli Khristuyo? Utiwuze ife. Ndipo iye adati kwa iwo, Ngati ine ndikuwuzani inu, inu simukhulupirira ayi;
  2789. Luk 22:68 Ndipo ngati nditakufunsaninso [inu], inu simundiyankha ine, kapena kundilola [ine] kupita.
  2790. Luk 22:69 Kuyambira tsopano Mwana wamwamuna wa munthu adzakhala pa dzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.
  2791. Luk 22:70 Kenaka iwo onse adati, Kodi tsono iwe uli Mwana wamwamuna wa Mulungu? Ndipo iye adati kwa iwo, Inu munena kuti Ine ndine.
  2792. Luk 22:71 Ndipo iwo adati, Chifukwa chiyani ife tifunanso umboni wina? Pakuti ife tokha tamva za m’kamwa mwa iye mwini.
  2793. Luk 23:1 Ndipo khamu lonsero la iwo lidanyamuka, ndi kupita naye iye kwa Pilato.
  2794. Luk 23:2 Ndipo iwo adayamba kum’nenera iye, kunena kuti, Ife tidapeza [munthu] uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kayisara, kunena kuti iye mwini ndiye Khristu Mfumu.
  2795. Luk 23:3 Ndipo Pilato adamfunsa iye, nanena kuti, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo iye adamyankha iye ndipo anati, Inu mwanena ichi.
  2796. Luk 23:4 Ndipo Pilato adati kwa ansembe akulu ndi a kwa anthu, Ine sindidapeza chifukwa cha mlandu mwa munthu uyu.
  2797. Luk 23:5 Ndipo iwo adawopseza kwambiri, nanena kuti, Iye amasonkhezera anthuwo, kuphunzitsa m’Yudeya monse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira malo ano.
  2798. Luk 23:6 Pamene Pilato adamva za Galileya, iye anafunsa ngati munthuyu adali wa ku Galileya.
  2799. Luk 23:7 Ndipo m’mene adangodziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, adamtumiza iye kwa Herode, amene adali iye mwini ku Yerusalemu mu nthawi imeneyo.
  2800. Luk 23:8 ¶Ndipo pamene Herode adawona Yesu, adakondwa kopambana: pakuti iye adali kufuna kumpenya iye kwa nthawi yayitali, chifukwa adamva zinthu zambiri za iye; ndipo anayembekeza kuwona chozizwitsa china chochitidwa ndi iye.
  2801. Luk 23:9 Kenaka iye adamfunsa iye mu mawu ambiri; koma iye sadayankha kanthu.
  2802. Luk 23:10 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adayimirira ndipo anam’nenera iye kolimba.
  2803. Luk 23:11 Ndipo Herode ndi asirikali ake ankhondo adampeputsa iye, ndipo anam’nyoza [iye], ndipo anamveka iye chofunda chonyezimira, ndipo anam’bwezeranso iye kwa Pilato.
  2804. Luk 23:12 ¶Ndipo tsiku lomwero Pilato ndi Herode adakhala abwenzi: pakuti anali pa udani pakati pawo.
  2805. Luk 23:13 ¶Ndipo Pilato, pamene adayitanira pamodzi ansembe akulu ndi olamulira ndi anthu,
  2806. Luk 23:14 Nanena kwa iwo, Inu mudadza ndi munthu uyu kwa ine, ngati munthu wopandutsa anthu: ndipo, tawonani, ine, nditamfunsafunsa [iye] za mlanduwu pamaso panu, sindidapeza chifukwa mwa munthuyu chokhudza zinthu zimene inu mum’nenera iye.
  2807. Luk 23:15 Ayi, ngakhale Herode yemwe: pakuti ine ndidatumiza inu kwa iye; ndipo, onani, palibe chilichonse choyenera imfa chachitika pa iye.
  2808. Luk 23:16 Choncho ine ndidzamkwapula iye, ndi kum’masula [iye].
  2809. Luk 23:17 (Popeza kuti iye ankayenera kuwamasulira iwo munthu m’modzi pa phwando.)
  2810. Luk 23:18 Ndipo iwo onse adafuwula pamodzi, nanena kuti, Chotsani [munthu] uyu, ndipo mutimasulire ife Barabasi.
  2811. Luk 23:19 (Amene chifukwa cha mpanduko wochitika mu mzinda, ndi cha kupha munthu adaponyedwa m’ndende.)
  2812. Luk 23:20 Choncho Pilato, wofuna kumasula Yesu, adayankhulanso kwa iwo.
  2813. Luk 23:21 Koma iwo adafuwula, nanena kuti, Mpachikeni [iye], mpachikeni iye.
  2814. Luk 23:22 Ndipo iye adati kwa iwo nthawi yachitatu, Chifukwa chiyani, wachita choyipa chotani? Ine sindinapeza chifukwa choyenera imfa mwa iye: choncho ine ndidzamkwapula iye, ndi [kum’masula] kuti [iye] apite.
  2815. Luk 23:23 Ndipo iwo anali wofulumira ndi mawu wokweza, kupempha kuti iye akhoze kupachikidwa. Ndipo mawu a iwo ndi a akulu a ansembe adapambana.
  2816. Luk 23:24 Ndipo Pilato adaweruza kuti zikhale monga iwo adali kufunsa.
  2817. Luk 23:25 Ndipo iye adamasulira iwo amene chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu adaponyedwa m’ndende, amene iwo adampempha; koma adapereka Yesu ku chifuniro chawo.
  2818. Luk 23:26 Ndipo pamene amapita naye, adagwira munthu Simoni, Mkurene, alinkudza kuchokera kumidzi, ndipo iwo anamsenzetsa iye mtanda, kuti awunyamule [iwo] pambuyo pake pa Yesu.
  2819. Luk 23:27 ¶Ndipo lidamtsata iye gulu lalikulu la anthu, ndi la akazi, amene anadziguguda pachifuwa namlirira iye.
  2820. Luk 23:28 Koma Yesu adatembenukira kwa iwo anati, Ana akazi a Yerusalemu, musandiririre ine, koma mudziririre nokha ndi ana anu.
  2821. Luk 23:29 Pakuti, tawonani, masiku alinkudza, amene iwo adzati, Wodala [ali] wowuma, ndi mimba yosabala, ndi mawere amene sanayamwitsapo.
  2822. Luk 23:30 Kenaka adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.
  2823. Luk 23:31 Pakuti ngati achita zinthu izi mu mtengo wawuwisi, nanga kudzachitidwa zotani mu mtengo wowuma?
  2824. Luk 23:32 Ndipo adaliponso awiri ena, wochita zoyipa, adatengedwa pamodzi ndi iye kukaphedwa.
  2825. Luk 23:33 Ndipo pamene adafika ku malo, dzina lake Kalivari, pamenepo adampachika iye pa mtanda, ndi wochita zoyipa womwe, m’modzi ku dzanja lamanja, ndi wina ku dzanja lamanzere.
  2826. Luk 23:34 ¶Kenaka Yesu adanena, Atate, muwakhululukire iwo; pakuti sadziwa chimene iwo achita. Ndipo adagawana zovala zake, ndipo anachita mayere.
  2827. Luk 23:35 Ndipo anthuwo adayimirira nawonerera. Ndi wolamuliranso adamlalatira [iye], nanena kuti, Adapulumutsa ena; adzipulumutse yekha, ngati iye ndiye Khristu, wosankhidwa wake wa Mulungu.
  2828. Luk 23:36 Ndipo asirikalinso adamnyoza, nadza kwa iye, ndi kumpatsa iye viniga.
  2829. Luk 23:37 Ndipo nanena kuti, Ngati iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha.
  2830. Luk 23:38 Ndipo chilembonso chidalembedwa pamwamba pa iye m’zilembo za Chigriki, ndi Chilatini, ndi Chihebri, UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.
  2831. Luk 23:39 ¶Ndipo m’modzi wa wochita zoyipa amene adapachikidwayo adamchitira iye mwano, nanena kuti, Ngati iwe uli Khristu; udzipulumutse iwe wekha ndi ife.
  2832. Luk 23:40 Koma winayo poyankha anamdzudzula iye, nanena kuti, Kodi iwe suwopa Mulungu, powona uli m’kulangika komweku?
  2833. Luk 23:41 Ndipo ifetu kuyenera pakuti tiri kulandira mphotho zoyenera zochita zathu: koma munthu uyu sadachita kanthu molakwa.
  2834. Luk 23:42 Ndipo iye adati kwa Yesu, Ambuye, mundikumbukire ine pamene mukudza mu ufumu wanu.
  2835. Luk 23:43 Ndipo Yesu adanena kwa iye, Ndithudi ndinena kwa iwe, Lero lino iwe udzakhala ndi ine m’Paradayiso.
  2836. Luk 23:44 Ndipo lidali ngati ora lake la chisanu ndi chimodzi pamenepo, ndipo padali mdima padziko lonse lapansi kufikira ora la chisanu ndi chinayi;
  2837. Luk 23:45 Ndipo dzuwa linadetsedwa, ndipo chinsalu chotchinga cha mkachisi chidang’ambika pakati.
  2838. Luk 23:46 ¶Ndipo pamene Yesu adafuwula ndi mawu okwera, iye adati, Atate, m’manja mwanu ine ndipereka mzimu wanga: ndipo atanena motero, iye adamwalira.
  2839. Luk 23:47 Ndipo pamene kenturiyoni adawona chimene chidachitikacho, iye adalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zowonadi uyu adali munthu wolungama.
  2840. Luk 23:48 Ndipo anthu onse amene adabwera pamodzi kudzapenya ichi, powona zinthu zimene zidachitikazo, anadziguguda pachifuwa, ndipo adapita kwawo.
  2841. Luk 23:49 Ndipo wonse womdziwa iye, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, adayima kutali, nawona zinthu izi.
  2842. Luk 23:50 ¶Ndipo, tawonani, [padali munthu] dzina lake Yosefe, mlangizi; [ndipo adali] munthu wabwino, ndi wolungama:
  2843. Luk 23:51 (Amene sadavomereza kuweruza kwawo ndi ntchito yawo;) [adali wa] ku Arimateya, mzinda wa Ayuda: amene iyenso anayembekezera ufumu wa Mulungu.
  2844. Luk 23:52 [Munthu] uyu adapita kwa Pilato, ndipo anapempha mtembo wake wa Yesu.
  2845. Luk 23:53 Ndipo iye adawutsitsa, ndipo anawukulunga m’salu ya bafuta, ndipo anawuyika m’manda wosemedwa m’mwala, m’menemo sadayika munthu ndi kale lonse.
  2846. Luk 23:54 Ndipo tsiku limenero lidali la chikonzekero, ndipo sabata lidayandika.
  2847. Luk 23:55 Ndipo akazinso, amene adachokera naye ku Galileya, adamtsata m’mbuyo, ndipo anawona mandawo, ndi momwe mtembo wake unayikidwira.
  2848. Luk 23:56 Ndipo adabwerera, ndipo anakonza zonunkhira ndi mafuta onunkhira bwino; ndipo adapumula pa tsiku la sabata monga mwa lamulo.
  2849. Luk 24:1 Tsopano pa [tsiku] loyamba la sabata, m’bandakucha, iwo anadza kumanda, kubweretsa zonunkhira zimene iwo adazikonza, ndi [ena] pamodzi nawo.
  2850. Luk 24:2 Ndipo iwo adapeza mwala utakunkhunizidwa kuchotsedwa pamanda.
  2851. Luk 24:3 Ndipo iwo adalowamo, ndipo sadapeza mtembo wa Ambuye Yesu.
  2852. Luk 24:4 Ndipo kudachitika, m’mene iwo adathedwa nzeru kwakukulu pamenepopo, tawonani, amuna awiri adayimirira pafupi pawo atavala zonyezimira:
  2853. Luk 24:5 Ndipo m’mene iwo adali ndi mantha, naweramitsa pansi nkhope [zawo], adati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pakati pa akufa?
  2854. Luk 24:6 Iye si ali kuno, koma wawuka: kumbukirani momwe iye adayankhulira kwa inu pamene iye adali m’Galileya.
  2855. Luk 24:7 Kunena kuti, Mwana wamwamuna wa munthu ayenera kuperekedwa m’manja a anthu wochimwa, ndi kupachikidwa, ndi kuwukanso tsiku la chitatu.
  2856. Luk 24:8 Ndipo adakumbukira mawu ake,
  2857. Luk 24:9 Ndipo anabwerera kuchokera kumanda, ndipo anafotokoza zinthu izi zonse kwa khumi ndi m’modziyo, ndi ena onse.
  2858. Luk 24:10 Adali Mariya Mmagidalene, ndi Jowana, ndi Mariya [amayi ake] a Yakobo, ndi [akazi] ena amene adali [pamodzi] nawo, amene adanena zinthu izi kwa atumwiwo.
  2859. Luk 24:11 Ndipo mawu awo adawoneka pamaso pawo ngati nkhani chabe, ndipo iwo sadawakhulupirire iwo ayi.
  2860. Luk 24:12 Kenaka Petro adanyamuka, ndipo anathamangira kumanda; ndipo poweramira pansi, iye adawona nsalu zoyera zitayikidwa izo pazokha, ndipo adanyamuka, ali nkudabwa mwa iye yekha ndi chimene chidachitikacho.
  2861. Luk 24:13 ¶Ndipo, tawonani, awiri a mwa iwo adapita tsiku lomwero ku mudzi dzina lake Emausi, umene udali wotalikana ndi Yerusalemu mitunda [pafupifupi] isanu ndi iwiri ndi theka.
  2862. Luk 24:14 Ndipo adali kukambirana onse pamodzi za izi zonse zimene zidachitika.
  2863. Luk 24:15 Ndipo kudachitika, kuti ali m’kukambirana [kwawo] pamodzi ndi kufunsana maganizo, Yesu mwini adayandikira, ndipo anatsagana nawo.
  2864. Luk 24:16 Koma maso awo adagwidwa kuti iwo asamdziwa iye.
  2865. Luk 24:17 Ndipo iye adati kwa iwo, Mawu [awa] ndi wotani muli kukambirana wina ndi mnzake, pamene mukuyenda, ndipo muli ndi chisoni?
  2866. Luk 24:18 Ndipo m’modzi wa iwo, dzina lake Kleopasi, adayankha ndipo anati kwa iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo mu Yerusalemu, ndi kuti sudadziwa zinthu zidachitika kumeneko masiku awa?
  2867. Luk 24:19 Ndipo iye adati kwa iwo, Zinthu ziti? Ndipo iwo adati kwa iye, Zokhudza Yesu wa ku Nazarete, amene adali mneneri wamphamvu m’ntchito ndi mawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse:
  2868. Luk 24:20 Ndi momwe ansembe akulu ndi olamulira athu adampereka iye kuti aweruzidwe ndi chilango cha imfa, ndipo ampachika iye.
  2869. Luk 24:21 Koma ife tidadalira kuti iye ndiye amene wakudzayo amene anayenera kuwombola Israyeli: komanso pambali pa izi zonse, lero ndi tsiku la chitatu kuyambira pamene zinthu izi zidachitika.
  2870. Luk 24:22 Inde, ndipo akazi enanso a gulu la ife anatidabwitsa, ndiwo amene adalawirira m’mamawa ku manda;
  2871. Luk 24:23 Ndipo m’mene iwo sadawupeza mtembo wake, anadza, nanena, kuti iwo adawona masomphenya a angelo, amene adanena kuti iye anali ndi moyo.
  2872. Luk 24:24 Ndipo ena mwa iwo amene adali nafe adapita ku manda, napeza motero monga momwe akazi adanena; koma iyeyo sadamuwona.
  2873. Luk 24:25 Ndipo iye adati kwa iwo, Opusa, ndi a mtima wochedwa kukhulupirira zonse zimene aneneri aziyankhula!
  2874. Luk 24:26 Kodi sadayenera Khristu kumva zinthu zowawa izi, ndi kulowa mu ulemerero wake?
  2875. Luk 24:27 Ndipo kuyambira pa Mose ndi aneneri onse, iye adatanthawuzira kwa iwo m’malembo onse zinthu zokhudza iye yekha.
  2876. Luk 24:28 Ndipo adayandikira ku mudzi, umene adalikupitako: ndipo adachita ngati adafuna kupitirira.
  2877. Luk 24:29 Koma iwo adamuwumiriza iye, nanena kuti, Khalani ndi ife: pakuti kuli kuyandikira madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo adalowa kukhala nawo.
  2878. Luk 24:30 Ndipo kudachitika, m’mene iye adakhala nawo pa chakudya, iye adatenga mkate, ndipo anawudalitsa [iwo], ndipo ananyema, ndipo anapatsa iwo.
  2879. Luk 24:31 Ndipo maso awo adatseguka, ndipo adamdziwa iye; ndipo adawasowera iwo m’maso mwawo.
  2880. Luk 24:32 Ndipo iwo adati wina kwa mnzake, Kodi mtima wathu si udali wotentha m’kati mwathu, m’mene iye adali kuyankhula nafe m’njira, ndi m’mene iye adatitsegulira ife malembo?
  2881. Luk 24:33 Ndipo adanyamuka ora lomwero, ndipo anabwerera ku Yerusalemu, ndipo anapeza khumi ndi m’modziwo atasonkhana pamodzi, ndi iwo adali nawo,
  2882. Luk 24:34 Nanena kuti, Ambuye adawuka ndithu, ndipo wawonekera kwa Simoni.
  2883. Luk 24:35 Ndipo iwo adawafotokozera [zomwe zinachitidwa] m’njira, ndi umo adadziwikira kwa iwo m’kunyema kwa mkate.
  2884. Luk 24:36 ¶Ndipo pamene iwo analikuyankhula kotero, Yesu mwini yekha adayimirira pakati pawo, ndipo ananena kwa iwo, Mtendere ukhale kwa inu.
  2885. Luk 24:37 Koma iwo adawopsedwa ndi kuchititsidwa mantha, ndipo anayesa kuti adalikuwona mzimu.
  2886. Luk 24:38 Ndipo iye adati kwa iwo, Chifukwa chiyani inu muvutika? Ndipo chifukwa chiyani maganizo awuka m’mitima mwanu?
  2887. Luk 24:39 Tawonani manja anga ndi mapazi anga, kuti ine ndine mwini yekha: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu alibe m’nofu ndi mafupa, monga muwona ine ndiri nazo.
  2888. Luk 24:40 Ndipo m’mene adanena motero, iye adawawonetsa iwo manja [ake] ndi mapazi [ake].
  2889. Luk 24:41 Ndipo pokhala iwo tsono wosakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, ndi kudabwa, iye anati kwa iwo, Kodi muli nacho chakudya chilichonse kuno?
  2890. Luk 24:42 Ndipo adampatsa iye chidutswa cha nsomba yowotcha, ndi chisa cha uchi.
  2891. Luk 24:43 Ndipo iye adachitenga [icho], ndipo anadya pamaso pawo.
  2892. Luk 24:44 Ndipo iye adati kwa iwo, Awa [ndi] mawuwo amene ine ndidayankhula kwa inu, pamene ine ndidali ndi inu, kuti zinthu zonse ziyenera kukwaniritsidwa, zomwe zidalembedwa m’chilamulo cha Mose, ndi [mwa] aneneri, ndi m’masalmo, zokhudza ine.
  2893. Luk 24:45 Ndipo adatsegula kumvetsetsa kwawo, kuti akhoze kumvetsetsa malembo,
  2894. Luk 24:46 Ndipo iye adati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, ndipo kotero kuyenera kuti Khristu amve zowawa, ndi kuwuka kwa akufa tsiku la chitatu:
  2895. Luk 24:47 Ndi kuti kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kulalikidwe m’dzina lake pakati pa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.
  2896. Luk 24:48 Ndipo inu ndinu mboni za zinthu izi.
  2897. Luk 24:49 ¶Ndipo, tawonani, Ine nditumiza lonjezano la Atate wanga kwa inu: koma khalani inu mu mzinda wa Yerusalemu, kufikira inu mutakhala wovekedwa ndi mphamvu yochokera kumwamba.
  2898. Luk 24:50 ¶Ndipo iye adatuluka nawo kuwatsogolera kufikira ku Betane; ndipo iye nakweza manja ake, ndi kuwadalitsa iwo.
  2899. Luk 24:51 Ndipo kudachitika, pamene anali kuwadalitsa iwo, iye adalekanitsidwa kuchoka kwa iwo, ndipo anatengedwa kupita kumwamba.
  2900. Luk 24:52 Ndipo iwo adamlambira iye, ndipo nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu:
  2901. Luk 24:53 Ndipo adakhala chikhalire m’kachisi, kutamanda ndi kudalitsa Mulungu. Amen.
  2902. Jhn 1:1 Mu chiyambi munali Mawu, ndipo Mawu adali ndi Mulungu, ndipo Mawu adali Mulungu.
  2903. Jhn 1:2 Omwewa adali mu chiyambi ndi Mulungu.
  2904. Jhn 1:3 Zinthu zonse zidapangidwa ndi iye; ndipo popanda iye sikadalengedwa kanthu kena kalikonse kamene kadalengedwa.
  2905. Jhn 1:4 Mwa iye mudali moyo; ndi moyowu udali kuwunika kwa anthu.
  2906. Jhn 1:5 Ndipo kuwunikaku kuwala mu mdima; ndi mdimawu sudakuzindikira ayi.
  2907. Jhn 1:6 ¶Padali munthu, wotumidwa kuchokera kwa Mulungu, amene dzina lake [lidali] Yohane.
  2908. Jhn 1:7 Yemweyu adadza chifukwa cha umboni, kudzachita umboni za Kuwunika kumeneko, kuti [anthu] onse kudzera mwa iye akhoze kukhulupirira.
  2909. Jhn 1:8 Iye sanali Kuwunika kumeneku, koma [adatumidwa] kukachita umboni wa Kuwunika kumeneku.
  2910. Jhn 1:9 [Kumeneko] kunali Kuwunika kwenikweni, kumene kuwunikira munthu aliyense amene adza kulowa m’dziko lapansi.
  2911. Jhn 1:10 Iye adali m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi lidalengedwa ndi iye, ndipo dziko lapansi silidamdziwa iye.
  2912. Jhn 1:11 Anadza kwa ake a iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sadamlandira iye.
  2913. Jhn 1:12 Koma ambiri iwo amene anamlandira iye, kwa iwo iye adapatsa mphamvu kuti akhale ana amuna a Mulungu, [ngakhale] kwa iwotu amene akhulupirira dzina lake.
  2914. Jhn 1:13 Amene anabadwa, osati mwa mwazi, kapena mwa chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.
  2915. Jhn 1:14 Ndipo Mawu adasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, (ndipo ife tidawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate), wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.
  2916. Jhn 1:15 ¶Yohane achita umboni za iye, ndipo anafuwula, kunena kuti, Uyu ndi iye amene ine ndidanena za iye, Iye wakudzayo pambuyo panga adalipo ndisanabadwe ine: pakuti adali woyamba wa ine.
  2917. Jhn 1:16 Ndipo mwa kudzala kwake ife tonse talandira, chisomo kwa chisomo.
  2918. Jhn 1:17 Pakuti chilamulo chidapatsidwa mwa Mose, [koma] chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
  2919. Jhn 1:18 Palibe munthu adawona Mulungu nthawi ina iliyonse; Mwana wamwamuna wobadwa yekha, amene ali m’chifukwato cha Atate, iyeyu walengeza [iye].
  2920. Jhn 1:19 ¶Ndipo uwu ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda adatuma ansembe ndi Alevi ochokera ku Yerusalemu kuti akamfunse iye, Iwe ndiwe yani?
  2921. Jhn 1:20 Ndipo iye adavomera, ndipo sadakane ayi; koma anavomera, Ine sindine Khristuyo.
  2922. Jhn 1:21 Ndipo iwo adamfunsa iye, Nanga bwanji tsono? Kodi ndiwe Eliya? Iye adanena, Sindine ayi. Kodi ndiwe mneneriyo? Ndipo iye anayankha, Iyayi.
  2923. Jhn 1:22 Kenaka iwo adati kwa iye, Iwe ndiwe yani? Kuti tikhoze kubwezera yankho kwa iwo amene adatituma ife. Unena chiyani iwe za iwe mwini wekha?
  2924. Jhn 1:23 Iye adati, Ine [ndine] mawu a wofuwula m’chipululu, Wongola njira ya Ambuye, monga adanena mneneri Yesaya.
  2925. Jhn 1:24 Ndipo iwo amene adatumidwawo adali a kwa Afarisi.
  2926. Jhn 1:25 Ndipo iwo adamfunsa iye, ndipo anati kwa iye, Nanga iwe ukubatiza bwanji tsono, ngati iwe suli Khristu ameneyo, kapena Eliya, kapena mneneriyo?
  2927. Jhn 1:26 Yohane adawayankha iwo, kunena kuti, Ine ndibatiza ndi madzi: koma pakuyimirira wina pakati pa inu, amene simumdziwa.
  2928. Jhn 1:27 Iye ndiye amene, amene akudza pambuyo panga adalipo ndisanabadwe ine, amene chingwe cha nsapato zake ine sindiri woyenera kumasula.
  2929. Jhn 1:28 Zinthu izi zidachitika mu Betabara kupitirira Yordano, komwe Yohane adalikubatiza.
  2930. Jhn 1:29 ¶Tsiku lotsatira Yohane awona Yesu alinkudza kwa iye, ndipo ananena, Tawonani Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi!
  2931. Jhn 1:30 Uyu ndi iye amene ine ndidati za iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene adalipo ndisanabadwe ine: pakuti adali woyamba wa ine.
  2932. Jhn 1:31 Ndipo ine sindidamdziwa iye: koma kuti iye awonetsedwe kwa Israyeli, choncho ine ndadza kudzabatiza ndi madzi.
  2933. Jhn 1:32 Ndipo Yohane adachita umboni, kunena kuti, Ine ndidawona Mzimu alikutsika kuchokera kumwamba monga nkhunda, ndipo anakhala pa iye.
  2934. Jhn 1:33 Ndipo ine sindidamdziwa iye: koma iye amene ananditumayo kudzabatiza ndi madzi, yemweyo adanena kwa ine, Pa iye amene iwe udzawona Mzimu atsikira, ndi kukhala pa iye, yemweyu ndi iye amene abatiza ndi Mzimu Woyera.
  2935. Jhn 1:34 Ndipo ine ndidawona, ndipo ndichita umboni kuti uyu ndiye Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  2936. Jhn 1:35 ¶Kenanso tsiku lotsatira Yohane atayimirira, ndi awiri a wophunzira ake;
  2937. Jhn 1:36 Ndipo poyang’ana pa Yesu pamene analikuyenda, iye adati, Tawonani Mwanawankhosa wa Mulungu!
  2938. Jhn 1:37 Ndipo wophunzira awiriwo adamumva iye alinkuyankhula, ndipo anatsata Yesu.
  2939. Jhn 1:38 Kenaka Yesu adatembenuka, ndipo anapenya iwo alikutsatira, ndipo ananena kwa iwo, Mufuna chiyani inu? Ndipo adati kwa iye, Ambuye (ndiko kunena kuti, potanthawuzidwa, Mphunzitsi), inu mumakhala kuti?
  2940. Jhn 1:39 Iye adati kwa iwo, Idzani ndipo muwone. Iwo anadza ndipo anawona kumene amakhala; ndipo anakhala ndi iye tsiku limenero: popeza kuti linali pafupifupi ora lakhumi.
  2941. Jhn 1:40 M’modzi wa awiriwo amene adamva Yohane [akuyankhula], ndipo anamtsata iye, adali Anduru, mbale wake wa Simoni Petro.
  2942. Jhn 1:41 Iye poyamba adapeza mbale wake Simoni, ndipo ananena kwa iye, Ife tampeza Mesiya, amene ali, potanthawuzidwa [ndi], Khristu.
  2943. Jhn 1:42 Ndipo iye anadza naye kwa Yesu. Ndipo pamene Yesu adamuyang’ana iye, iye adati, Iwe ndiwe Simoni mwana wamwamuna wa Yona: iwe udzatchedwa Kefasi, amene potanthawuzidwa, Mwala.
  2944. Jhn 1:43 ¶Tsiku lotsatira Yesu adafuna kutuluka kupita kulowa m’Galileya, ndipo anapeza Filipi, ndipo adanena kwa iye, Unditsate ine.
  2945. Jhn 1:44 Tsopano Filipi adali wa ku Betisayida, mzinda wa Anduru ndi Petro.
  2946. Jhn 1:45 Filipi adapeza Nataniyeli, ndipo ananena kwa iye, Ife tampeza iye, amene za iye Mose m’chilamulo, ndi aneneri, adalemba, Yesu wa ku Nazarete mwana wamwamuna wa Yosefe.
  2947. Jhn 1:46 Ndipo Nataniyeli adati kwa iye, Kungakhale kanthu kena kalikonse kabwino kuchokera ku Nazarete? Filipi adanena kwa iye, Idza ndipo uwone.
  2948. Jhn 1:47 Yesu adawona Nataniyeli alinkudza kwa iye, ndipo ananena za iye, Tawonani, mu Israyeli ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!
  2949. Jhn 1:48 Nataniyeli adanena kwa iye, Inu mudandidziwira kuti ine? Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Asadakuyitane iwe Filipi, pamene udali iwe pansi pa mtengo wa mkuyu, Ine ndidakuwona iwe.
  2950. Jhn 1:49 Nataniyeli adayankha ndipo ananena kwa iye, Ambuye, inu ndinu Mwana wamwamuna wa Mulungu; inu ndinu Mfumu ya Israyeli.
  2951. Jhn 1:50 Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Chifukwa ine ndidati kwa iwe, Ine ndidakuwona iwe pansi pa mtengo wa mkuyu, kodi iwe ukhulupirira? Iwe udzawona zinthu zazikulu zoposa izi.
  2952. Jhn 1:51 Ndipo iye adanena kwa iye, Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Kuchokera tsopano [lino] inu mudzawona kumwamba kotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera ndi kutsikira pa Mwana wamwamuna wa munthu.
  2953. Jhn 2:1 Ndipo tsiku la chitatu padali ukwati mu Kana wa Galileya; ndipo amayi wake a Yesu adali komweko:
  2954. Jhn 2:2 Ndipo Yesu yemwe adayitanidwa, ndi wophunzira ake, ku ukwatiwo.
  2955. Jhn 2:3 Ndipo pamene adafuna vinyo, amayi wake a Yesu adanena kwa iye, Iwo alibe vinyo.
  2956. Jhn 2:4 Yesu adanena kwa iye, Mkazi, kodi ine ndiri ndi chiyani chochita ndi inu? Ora langa silidafike.
  2957. Jhn 2:5 Amayi wake adanena kwa antchito, Kalikonse chimene iye anena kwa inu, chitani [chimenecho].
  2958. Jhn 2:6 Ndipo padali pamenepo yoyikidwapo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi, monga mwa mwambo wa mayeretsedwe a Ayuda, yokwanira miyeso iwiri kapena itatu ya malita makumi atatu ndi mphambu zinayi.
  2959. Jhn 2:7 Yesu adanena kwa iwo, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Ndipo iwo adayidzadza mpaka m’milomo.
  2960. Jhn 2:8 Ndipo iye adanena kwa iwo, Tungani tsopano, ndipo mupite naye kwa mkulu wa phwando. Ndipo adapita [naye].
  2961. Jhn 2:9 Pamene wolamulira wa phwandoyo adalawa madzi amene adasandulika vinyowo, ndipo sadadziwa kumene adachokera: (koma antchito amene adatunga madzi adadziwa;) mkulu wa phwandoyo adayitana mkwati,
  2962. Jhn 2:10 Ndipo ananena naye, Munthu aliyense amayamba kuyika vinyo wabwino; ndipo pomwe anthu amwa bwino lomwe, pamenepo amene ali woyipa: [koma] iwe wasunga vinyo wabwino kufikira tsopano lino.
  2963. Jhn 2:11 Chiyambi ichi cha zozizwa Yesu adazichita mu Kana wa Galileya, ndipo adawonetsera ulemerero wake; ndipo wophunzira ake adakhulupirira iye.
  2964. Jhn 2:12 ¶Zitapita izi adatsikira ku Kaperenamu, iye, ndi amayi wake, ndi abale ake, ndi wophunzira ake: ndipo anakhala komweko osati masiku ambiri.
  2965. Jhn 2:13 ¶Ndipo Paskha wa Ayuda adayandikira, ndipo Yesu adakwera kupita ku Yerusalemu.
  2966. Jhn 2:14 Ndipo adapeza m’kachisi iwo amene ankagulitsa ng’ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi osintha ndalama atakhala pansi:
  2967. Jhn 2:15 Ndipo pamene adapanga mkwapulo wa zingwe zazing’ono, iye adatulutsa iwo onse m’kachisimo, ndi nkhosazo, ndi ng’ombezo; ndipo anakhuthula ndalama za wosinthawo, ndi kugubuduza magome;
  2968. Jhn 2:16 Ndipo anati kwa iwo amene ankagulitsa nkhundawo; Chotsani zinthu izi muno; musayipange nyumba ya Atate wanga [kukhala] nyumba ya malonda.
  2969. Jhn 2:17 Ndipo wophunzira ake adakumbukira kuti kudalembedwa, Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine.
  2970. Jhn 2:18 ¶Kenaka Ayuda adayankha ndi kunena kwa iye, Chizindikiro chanji chimene mutiwonetse ife, powona kuti inu muchita izi?
  2971. Jhn 2:19 Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Gumulani kachisi uyu, ndipo m’masiku atatu ndidzamuwutsa.
  2972. Jhn 2:20 Kenaka Ayuda adati, Zaka makumi anayi kudza zisanu ndi chimodzi adali kumanga kachisiyu, ndipo inu mudzamuwutsa m’masiku atatu?
  2973. Jhn 2:21 Koma iye adanena za kachisi wa thupi lake.
  2974. Jhn 2:22 Choncho iye atawuka kwa akufa, wophunzira ake adakumbukira kuti adanena ichi kwa iwo; ndipo iwo adakhulupirira lembalo, ndi mawu amene Yesu adanena.
  2975. Jhn 2:23 ¶Tsopano pamene iye adali mu Yerusalemu pa Paskha, mu [tsiku] la phwando, ambiri adakhulupirira m’dzina lake, pamene adawona zozizwa zimene adachitazi.
  2976. Jhn 2:24 Koma Yesu sadadzipereka mwini yekha kwa iwo, chifukwa iye adadziwa [anthu] onse.
  2977. Jhn 2:25 Ndipo sadasowa wina achite umboni za munthu: pakuti adadziwa iye chimene chidali mwa munthu.
  2978. Jhn 3:1 Padali munthu wa Afarisi, wotchedwa Nikodemasi, wolamulira wa Ayuda:
  2979. Jhn 3:2 Yemweyu adadza kwa Yesu usiku, ndipo anati kwa iye, Ambuye, tidziwa kuti inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu: pakuti palibe munthu akhoza kuchita zozizwa izi zimene inu muchita, pokhapokha Mulungu akhala ndi iye.
  2980. Jhn 3:3 Yesu adayankha ndipo ananena kwa iye, Ndithudi, ndithudi ndinena kwa iwe, Pokhapokha munthu abadwe mwatsopano, iye sangawone ufumu wa Mulungu.
  2981. Jhn 3:4 Nikodemasi adanena kwa iye, Kodi munthu akhoza bwanji kubadwa pamene iye wakalamba? Kodi iye akhoza kulowanso kachiwiri m’mimba ya amayi wake, ndi kubadwa?
  2982. Jhn 3:5 Yesu adayankha, Ndithudi, ndithudi ine ndinena kwa iwe, Pokhapokha munthu atabadwa mwa madzi ndi [mwa] Mzimu, iye sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.
  2983. Jhn 3:6 Chimene chili chobadwa mwa thupi chili thupi; ndipo chimene chili chobadwa mwa Mzimu chili mzimu.
  2984. Jhn 3:7 Usadabwe chifukwa ine ndidati kwa iwe, Uyenera kubadwanso mwatsopano.
  2985. Jhn 3:8 Mphepo iwomba komwe ifuna, ndipo iwe ukumva liwu lake, koma sunganene kumene ichokera, ndi kumene ipita: chotero aliyense amene abadwa mwa Mzimu.
  2986. Jhn 3:9 Nikodemasi adayankha ndipo anati kwa iye, Kodi zinthu izi zingatheke bwanji?
  2987. Jhn 3:10 Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Iwe uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa zinthu izi?
  2988. Jhn 3:11 Ndithudi, ndithudi ndinena kwa iwe, Ife tiyankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni chimene ife tachiwona; ndipo inu simulandira umboni wathu.
  2989. Jhn 3:12 Ngati ine ndakuwuzani zinthu za dziko lapansi, ndipo inu simukhulupirira, kodi mudzakhulupirira bwanji, ngati ine ndikuwuzani [za] kumwamba?
  2990. Jhn 3:13 Ndipo kulibe munthu adakwera [kupita] kumwamba, koma iye amene adatsikayo kuchokera kumwamba, [ndiye] Mwana wamwamuna wa munthu amene ali kumwamba.
  2991. Jhn 3:14 ¶Ndipo monga Mose adakweza njoka m’chipululu, choteronso Mwana wamwamuna wa munthu ayenera kukwezekedwa:
  2992. Jhn 3:15 Kuti aliyense wakukhulupirira mwa iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.
  2993. Jhn 3:16 ¶Pakuti Mulungu adakondetsetsa dziko lapansi, kotero iye adapatsa Mwana wake wamwamuna wobadwa yekha, kuti aliyense wakukhulupirira mwa iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.
  2994. Jhn 3:17 Pakuti Mulungu sadatume Mwana wake wamwamuna ku dziko lapansi kuti akatsutse dziko lapansi; koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe kudzera mwa iye.
  2995. Jhn 3:18 ¶Iye amene akhulupirira pa iye satsutsidwa: koma iye amene sakhulupirira watsutsidwa kale, chifukwa iye sadakhulupirira mu dzina la Mwana wamwamuna wobadwa yekha wa Mulungu.
  2996. Jhn 3:19 Ndipo ichi ndicho chiweruzocho, kuti kuwunika kwadza m’dziko lapansi, ndipo anthu adakonda mdima koposa kuwunika; chifukwa zochita zawo zidali zoyipa.
  2997. Jhn 3:20 Pakuti aliyense wochita zoyipa adana ndi kuwunika, kapenanso sabwera ku kuwunika, kuti mwina zochita zake zingatsutsidwe.
  2998. Jhn 3:21 Koma iye amene achita chowonadi abwera ku kuwunikaku, kuti zochita zake ziwonetsedwe, kuti ziri zochitidwa mwa Mulungu.
  2999. Jhn 3:22 ¶Zitapita zinthu izi anadza Yesu ndi wophunzira ake m’dziko la Yudeya; ndipo kumeneko adakhala nawo pamodzi, ndipo anabatiza.
  3000. Jhn 3:23 ¶Ndipo Yohane adalinkubatizanso mu Ayinoni pafupi ndi ku Salimu, chifukwa padali madzi ambiri pamenepo: ndipo iwo adaza, ndipo anabatizidwa.
  3001. Jhn 3:24 Pakuti Yohane adali asadayikidwe m’ndende.
  3002. Jhn 3:25 ¶Kenaka padawuka funso pakati pa [ena] a wophunzira a Yohane ndi Ayuda zokhudza mayeretsedwe.
  3003. Jhn 3:26 Ndipo iwo anadza kwa Yohane, ndipo anati kwa iye, Ambuye, iye amene adali ndi inu tsidya lija la Yordano, kwa iye amene inu mumchitira umboni, tawonani, yemweyu akubatiza, ndipo [anthu] onse alinkudza kwa iye.
  3004. Jhn 3:27 Yohane adayankha ndipo anati, Munthu sangalandire kanthu, pokhapokha kakapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba.
  3005. Jhn 3:28 Inu nomwe mundichitira ine umboni, kuti ine ndidati, Ine sindine Khristuyo, koma kuti ndiri wotumidwa m’tsogolo mwake mwa iye.
  3006. Jhn 3:29 Iye amene ali naye mkwatibwi ndiye mkwati: koma bwenzi lake la mkwatiyo, amene akuyimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mawu a mkwatiyo: choncho mwa ichi chimwemwe changa chikwaniritsidwa.
  3007. Jhn 3:30 Iyeyo ayenera kukula, koma ine [ndiyenera] ndichepe.
  3008. Jhn 3:31 Iye amene achokera kumwamba ali pamwamba pa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, ndipo alankhula za dziko lapansi: iye amene achokera kumwamba ali pamwamba pa onse.
  3009. Jhn 3:32 Ndipo chimene iye wachiwona ndi kuchimva, chimenecho achita umboni; ndipo palibe munthu alandira umboni wake.
  3010. Jhn 3:33 Iye amene walandira umboni wake wayika ku chisindikizo chake kuti Mulungu ali wowona.
  3011. Jhn 3:34 Pakuti iye amene Mulungu wamtuma alankhula mawu a Mulungu: pakuti Mulungu sapatsa Mzimu mwa muyeso [kwa iye].
  3012. Jhn 3:35 Atate akonda Mwana wamwamuna, ndipo wapatsa zinthu zonse m’dzanja lake.
  3013. Jhn 3:36 Iye amene akhulupirira pa Mwana wamwamunayo ali nawo moyo wosatha: ndipo iye amene sakhulupirira Mwana wamwamunayo sadzawona moyo; koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.
  3014. Jhn 4:1 Choncho pamene Ambuye adadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu adapanga ndi kubatiza wophunzira ambiri koposa Yohane,
  3015. Jhn 4:2 (Angakhale Yesu mwiniyo sanabatiza ayi koma wophunzira ake,)
  3016. Jhn 4:3 Iye adachoka ku Yudeya, ndipo adanyamukanso kupita ku Galileya.
  3017. Jhn 4:4 Ndipo iye adasowekera kuyenera kudutsa pakati pa Samariya.
  3018. Jhn 4:5 Kenaka adadza ku mudzi wa Samariya, umene utchedwa Sikara, pafupi pa kamalo kamene Yakobo adapatsa mwana wake wamwamuna Yosefe.
  3019. Jhn 4:6 Tsopano chitsime cha Yakobo chidali pamenepo. Choncho Yesu, atatopa ndi ulendo [wake], adakhala pa chitsimecho: [ndipo] kunali pafupifupi ora la chisanu ndi chimodzi.
  3020. Jhn 4:7 Kunadza mkazi wa ku Samariya kudzatunga madzi: Yesu adanena kwa iye, Undipatse ine kuti ndimwe.
  3021. Jhn 4:8 (Pakuti wophunzira ake adachoka kupita ku mzinda kuti akagule chakudya.)
  3022. Jhn 4:9 Kenaka adanena mkazi wa ku Samariyayo kwa iye, Kodi zichitika bwanji kuti inu, wokhala Myuda, mupempha kumwa kwa ine, amene ndiri mkazi wa ku Samariya? Pakuti Ayuda sachita kalikonse ndi a Samariya.
  3023. Jhn 4:10 Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Ngati iwe ukadadziwa mphatso ya Mulungu, ndi amene ali iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse ine kuti ndimwe; iwe ukadapempha kwa iye, ndipo iye akadakupatsa iwe madzi a moyo.
  3024. Jhn 4:11 Mkaziyo adanena kwa iye, Ambuye, inu mulibe chakuti mutungire nacho madzi, ndi chitsime chili chakuya: kuchokera kuti tsono kumene inu muli ndi madzi a moyo?
  3025. Jhn 4:12 Kodi muli wamkulu koposa atate wathu Yakobo, amene adatipatsa ife chitsimechi, ndipo anamwa a m’menemo iye mwini ndi ana ake, ndi ng’ombe zake?
  3026. Jhn 4:13 Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Aliyense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu:
  3027. Jhn 4:14 Koma aliyense wakumwako madzi amene ine ndidzampatsa iye sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene ine ndidzampatsa iye adzakhala mwa iye chitsime cha kasupe wa madzi otumphukira kulowa m’moyo wosatha.
  3028. Jhn 4:15 Mkaziyo adanena kwa iye, Ambuye, ndipatseni ine madzi amenewa, kuti ndisamve ludzu, kapena kubwera kuno kudzatunga.
  3029. Jhn 4:16 Yesu adanena kwa iye, Pita, kamuyitane mwamuna wako, ndipo ubwere kuno.
  3030. Jhn 4:17 Mkaziyo adayankha ndipo anati kwa iye, ine ndiribe mwamuna. Yesu adanena naye, Iwe wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe:
  3031. Jhn 4:18 Pakuti iwe wakhala nawo amuna asanu; ndipo iye amene ukukhala naye tsopano sali mwamuna wako; mu icho wanena iwe zowona.
  3032. Jhn 4:19 Mkazi adanena kwa iye, Ambuye, ine ndazindikira kuti inu ndinu mneneri.
  3033. Jhn 4:20 Atate athu analambira m’phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu ndiwo malo amene anthu ayenera kulambiramo.
  3034. Jhn 4:21 Yesu adanena kwa iye, Mkazi, khulupirira ine, ora likudza, limene inu simudzalambira Atate m’phiri ili, kapena mu Yerusalemu.
  3035. Jhn 4:22 Inu mulambira chimene simuchidziwa: ife tichidziwa chimene tichilambira: pakuti chipulumutso ncha kwa Ayuda.
  3036. Jhn 4:23 Koma ora likudza, ndipo tsopano liripo, limene olambira wowona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi: pakuti Atate afuna wotere kumulambira iye.
  3037. Jhn 4:24 Mulungu ndi Mzimu: ndipo iwo amene amlambira [iye] ayenera kumlambira [iye] mu mzimu ndi m’chowonadi.
  3038. Jhn 4:25 Mkazi adanena kwa iye, Ine ndidziwa kuti Mesiya abwera, amene atchedwa Khristu: pamene iyeyu adzabwera, iye adzatiwuza ife zinthu zonse.
  3039. Jhn 4:26 Yesu adanena kwa iye, Ine amene ndikulankhula kwa iwe ndine [amene].
  3040. Jhn 4:27 ¶Ndipo pamenepo adabwera wophunzira ake, ndipo anazizwa kuti iye adalinkulankhula ndi mkazi: koma panalibe munthu adati, Kodi inu mukufuna chiyani? Kapena, Chifukwa chiyani mukulankhula ndi iye?
  3041. Jhn 4:28 Mkaziyo kenaka adasiya mtsuko wake wa madzi, ndipo anapita panjira yake kulowa mu mzinda, ndipo ananena kwa anthu,
  3042. Jhn 4:29 Idzani, mudzawone munthu, amene adandiwuza zinthu zirizonse zimene ine ndidazichita: kodi uyu sindiye Khristuyo?
  3043. Jhn 4:30 Kenaka iwo adatuluka mu mzinda, ndipo anabwera kwa iye.
  3044. Jhn 4:31 ¶Pa nthawi imene izi zimachitika wophunzira ake adampempha iye, kunena kuti, Mphunzitsi, idyani.
  3045. Jhn 4:32 Koma iye adati kwa iwo, Ine ndiri nacho chakudya chimene inu simuchidziwa.
  3046. Jhn 4:33 Choncho wophunzira adanena wina kwa mzake, Kodi munthu wina adamtengera iye [kanthu] kakuti adye?
  3047. Jhn 4:34 Yesu adanena kwa iwo, Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha iye amene adandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.
  3048. Jhn 4:35 Simunena inu, kuti, Kuli miyezi inayi, ndipo [kenaka] kudza kukolola? Tawonani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, ndipo muyang’ane pa minda; pakuti ili kale yakucha kuti ikololedwe.
  3049. Jhn 4:36 Ndipo iye amene akolola alandira malipiro, ndipo asonkhanitsira chipatso ku moyo wosatha: kuti onse awiri iye amene afesa ndi iye amene akololayo akhoze kukondwera pamodzi.
  3050. Jhn 4:37 Ndipo m’menemo ndi momwe chonenedwacho chili chowona, Wina afesa, ndipo wina akolola.
  3051. Jhn 4:38 Ine ndidatuma inu kukamweta pa chimene inu simudagwirirapo ntchito: anthu ena adagwira ntchito, ndipo inu mwalowa mu ntchito zawo.
  3052. Jhn 4:39 ¶Ndipo ambiri a Asamariya mu mzinda umenewo adakhulupirira pa iye, chifukwa cha mawu a mkazi, amene adachita umboniyo, Iye adandiwuza ine zonse ndidazichita.
  3053. Jhn 4:40 Kotero pamene Asamariya anadza kwa iye, iwo adamfunsa iye kuti akhale ndi iwo: ndipo adakhala komweko masiku awiri.
  3054. Jhn 4:41 Ndipo ena ambiri adakhulupirira chifukwa cha mawu ake;
  3055. Jhn 4:42 Ndipo adanena kwa mkaziyo, Tsopano ife tikhulupirira, osati chifukwa cha zoyankhula zako: pakuti ife tamva [iye] tokha, ndipo tidziwa kuti uyu ndithu ndi Khristu, Mpulumutsi wa dziko lapansi.
  3056. Jhn 4:43 ¶Tsopano atapita masiku awiriwo adanyamuka kumeneko, ndipo adapita ku Galileya.
  3057. Jhn 4:44 Pakuti Yesu mwini adachita umboni, kuti mneneri alibe ulemu ku dziko la kwawo.
  3058. Jhn 4:45 Kenaka pamene iye adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira iye, atawona zinthu zonse zimene adazichita ku Yerusalemu pa phwando: pakuti iwonso adapita ku phwandolo.
  3059. Jhn 4:46 Kotero Yesu adabweranso ku Kana wa ku Galileya, kumene adasandutsa madzi [kukhala] vinyo. Ndipo kudali munthu wina wolemekezeka amene mwana wake wamwamuna adadwala mu Kaperenamu.
  3060. Jhn 4:47 Pamene iyeyu adamva kuti Yesu wachoka ku Yudeya kulowa mu Galileya, iye adapita kwa iye, ndipo anampempha kuti atsike, ndi kuchiritsa mwana wake wamwamuna: pakuti adali pafupi imfa.
  3061. Jhn 4:48 Kenaka Yesu adati kwa iye, Pokhapokha inu muwone zizindikiro ndi zozizwa, inu simudzakhulupirira ayi.
  3062. Jhn 4:49 Munthu wolemekezekayo adanena kwa iye, Ambuye, bwerani mwana wanga asanafe.
  3063. Jhn 4:50 Yesu adanena kwa iye, Pita pa njira yako, mwana wako wamwamuna ali ndi moyo. Ndipo munthuyo adakhulupirira mawu amene Yesu adanena kwa iye, ndipo iye anapita pa njira yake.
  3064. Jhn 4:51 Ndipo m’mene iye adali kupita, antchito ake adakumana naye, ndipo anamuwuza [iye], kunena kuti, Mwana wanu wamwamuna ali ndi moyo.
  3065. Jhn 4:52 Kenaka iye adawafunsa iwo ora limene adayamba kuchira. Ndipo iwo adati kwa iye, Dzulo pa ora la chisanu ndi chiwiri malungo adamsiya iye.
  3066. Jhn 4:53 Kotero atateyo adadziwa kuti [lidali] ora lomwero, limene Yesu adati kwa iye, Mwana wako wamwamuna ali ndi moyo: ndipo iye yekha adakhulupirira, ndi nyumba yake yonse.
  3067. Jhn 4:54 Ichinso [ndi] chozizwa chachiwiri [chimene] Yesu adachita, pamene iye atachoka ku Yudeya kulowa mu Galileya.
  3068. Jhn 5:1 Zitapita izi padali phwando la Ayuda; ndipo Yesu adakwera kupita ku Yerusalemu.
  3069. Jhn 5:2 Tsopano pali thamanda mu Yerusalemu pa chipata cha [msika] wa nkhosa, limene litchedwa mu lirime la Chihebri, Betesida, lokhala ndi makumbi asanu.
  3070. Jhn 5:3 M’menemo munagona khamu lalikulu la anthu wopanda mphamvu, akhungu, wosayenda, opuwala, kudikira kuvundulidwa kwa madzi.
  3071. Jhn 5:4 Ndipo mngelo amatsika nyengo yina kulowa mu thamandalo, ndi kuvundula madzi: aliyense tsono amene amayambirira atavundulidwa madzi kulowamo amakhala wokonzedwa kumatenda aliwonse iye adali nawo.
  3072. Jhn 5:5 Ndipo munthu wina adali pamenepo, amene adali ndi nthenda kwa zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.
  3073. Jhn 5:6 Pamene Yesu adamuwona iye atagona, ndipo adadziwa kuti adakhala kufikira tsopano kwa nthawi yayitali [moteromo], iye adanena kwa iye, Ufuna iwe ukhale wochiritsidwa kodi?
  3074. Jhn 5:7 Munthu wopanda mphamvuyo adayankha iye, Ambuye, ine ndiribe munthu, pamene madzi avundulidwa, kuti andiyike ine muthamanda: koma pamene ine ndikudza, wina amatsika ndisadatsike ine.
  3075. Jhn 5:8 Yesu adanena kwa iye, Uka, nyamula kama wako, ndipo uyende.
  3076. Jhn 5:9 Ndipo posakhalitsa munthuyo adachiritsidwa, ndipo ananyamula kama wake, ndipo anayenda; ndipo tsiku lomwero lidali la sabata.
  3077. Jhn 5:10 ¶Choncho Ayuda adanena kwa munthu amene adachiritsidwayo, Ndi tsiku lasabata: ndipo sikuloledwa mwa lamulo kwa iwe kunyamula kama [wako].
  3078. Jhn 5:11 Iye adayankha iwo, Iye amene adandichiritsa, yemweyo adati kwa ine, Nyamula kama wako, ndipo uyende.
  3079. Jhn 5:12 Kenaka iwo adamfunsa iye, Munthuyo ndani amene adanena kwa iwe, Nyamula kama wako, ndipo uyende?
  3080. Jhn 5:13 Ndipo iye amene adachiritsidwayo sanadziwa kuti anali ndani: pakuti Yesu adadzichotsapo yekha, khamu lidali pa malo [paja].
  3081. Jhn 5:14 Zitapita izi Yesu adampeza iye m’kachisi, ndipo anati kwa iye, Tawona, iwe wachiritsidwa: usachimwenso, kuti mwina choyipa choposa chingakugwere iwe.
  3082. Jhn 5:15 Munthuyo adanyamuka, ndipo anawuza Ayuda kuti anali Yesu, amene adamchiritsa iye.
  3083. Jhn 5:16 Ndipo choncho Ayuda adalondalonda Yesu, ndipo anafuna kumupha iye, chifukwa adachita zinthu izi patsiku la sabata.
  3084. Jhn 5:17 ¶Koma Yesu adayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, ndipo ine ndigwira ntchito.
  3085. Jhn 5:18 Choncho Ayuda adawonjeza kufuna kumupha iye, osati chifukwa cha kuswa tsiku lasabata kokha, koma adanenanso kuti Mulungu ndi Atate wake, kudzipanga iye wofanana ndi Mulungu.
  3086. Jhn 5:19 Kenaka Yesu adayankha nati kwa iwo, Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Mwana wamwamuna sangathe kuchita kanthu ka iye yekha, koma chimene awona Atate achichita: pakuti zinthu zirizonse zimene iye azichita, izinso achitanso Mwana wamwamuna.
  3087. Jhn 5:20 Pakuti Atate akonda Mwana wamwamuna, ndipo amuwonetsa iye zinthu zonse zimene azichita yekha: ndipo adzamuwonetsa iye ntchito zazikulu zoposa izi, kuti inu mukhoze kuzizwa.
  3088. Jhn 5:21 Pakuti monga Atate awukitsa akufa, ndipo awapatsa moyo [iwo]; momwemonso Mwana wamwamunayo apatsa moyo iye amene iye afuna.
  3089. Jhn 5:22 Pakuti Atate saweruza munthu, koma wapereka kuweruza konse kwa Mwana wamwamuna:
  3090. Jhn 5:23 Kuti [anthu] onse alemekeze Mwana wamwamuna, monga iwo alemekeza Atate. Iye amene salemekeza Mwana wamwamuna salemekeza Atate amene wamtuma iye.
  3091. Jhn 5:24 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Iye amene akumva mawu anga, ndi kukhulupirira pa iye amene adatuma ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo iye sadza mu kutsutsidwa, koma wachokera ku imfa kulowa m’moyo.
  3092. Jhn 5:25 Ndithudi, ndithudi, ndinena kwa inu, Ora likudza, ndipo liripo tsopano, limene akufa adzamva mawu a Mwana wamwamuna wa Mulungu: ndipo iwo amene adzamva adzakhala ndi moyo.
  3093. Jhn 5:26 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha; koteronso iye wapatsa kwa Mwana wamwamuna kuti akhale ndi moyo mwa iye yekha;
  3094. Jhn 5:27 Ndipo wampatsa iye ulamuliro woweruza, chifukwa iye ali Mwana wamwamuna wa munthu.
  3095. Jhn 5:28 Musazizwe ayi pa ichi: pakuti likudza ora, mu limene onse amene ali m’manda adzamva mawu ake,
  3096. Jhn 5:29 Ndipo adzatuluka; iwo amene achita zabwino, ku kuwuka kwa moyo; ndipo iwo amene achita zoyipa ku kuwuka kwa chiwonongeko.
  3097. Jhn 5:30 Ine sindingachite kanthu mwa ine ndekha: monga momwe ine ndimva, ine ndiweruza: ndipo kuweruza kwanga kuli kolungama; chifukwa ine sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Atate amene wandituma Ine.
  3098. Jhn 5:31 Ngati ndichita umboni mwa ine ndekha, umboni wanga si uli wowona.
  3099. Jhn 5:32 ¶Alipo wina amene achita umboni wa ine; ndipo ine ndidziwa kuti umboni umene iye andichitira ine uli wowona.
  3100. Jhn 5:33 Inu mudatuma kwa Yohane, ndipo iye achitira umboni kwa chowonadi.
  3101. Jhn 5:34 Koma ine sindilandira umboni wochokera kwa munthu: koma zinthu izi ine ndinena, kuti inu mukhoze kupulumutsidwa.
  3102. Jhn 5:35 Iye adali nyali yoyaka ndi yowala: ndipo inu mudali wofuna kukondwera kwa kanthawi m’kuwunika kwake.
  3103. Jhn 5:36 ¶Koma ine ndiri nawo umboni waukulu woposa [uwo] wa Yohane: pakuti ntchito zimene Atate wandipatsa ine kuti ndizitsirize, ntchito zomwezo zimene ine ndizichita, zichitira umboni kwa ine, kuti Atate wandituma ine.
  3104. Jhn 5:37 Ndipo Atate mwini yekha, amene wandituma ine, wandichitira umboni ine. Inu simudamva mawu ake nthawi iliyonse, kapena kuwona mawonekedwe ake.
  3105. Jhn 5:38 Ndipo mulibe mawu ake wokhala mwa inu: chifukwa kuti amene iye wamtuma, iyeyu inu simumkhulupirira ayi.
  3106. Jhn 5:39 ¶Santhulani malembo; pakuti m’menemo inu muganiza kuti inu muli nawo moyo wosatha: ndipo iwo ndiwo amene akundichitira ine umboni;
  3107. Jhn 5:40 Ndipo inu simudzabwera kwa ine, kuti mukhoze kukhala ndi moyo.
  3108. Jhn 5:41 Ine sindilandira ulemu wochokera kwa anthu.
  3109. Jhn 5:42 Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu.
  3110. Jhn 5:43 Ine ndadza m’dzina la Atate wanga, ndipo inu simundilandira ine ayi: ngati wina abwera m’dzina lake la iye mwini, iyeyu inu mudzamulandira.
  3111. Jhn 5:44 Mungathe inu kukhulupirira bwanji, amene mulandira ulemu wina kwa mzake, ndipo osafunafuna ulemu umene [uchokera] kwa Mulungu yekha?
  3112. Jhn 5:45 Musaganize kuti Ine ndidzakutsutsani inu kwa Atate; pali [m’modzi] amene akukutsutsani inu, [ndiye] Mose, amene mwa iye inu mukhulupirira.
  3113. Jhn 5:46 Pakuti inu mukadakhulupirira Mose; inu mukadakhulupirira ine: pakuti iyeyu adalembera za ine.
  3114. Jhn 5:47 Koma ngati simukhulupirira malembo ake, inu mudzakhulupirira bwanji mawu anga?
  3115. Jhn 6:1 Zitapita zinthu izi Yesu adapita kutsidya la nyanja ya Galileya, imene ili [nyanja] ya Tiberiyasi.
  3116. Jhn 6:2 Ndipo khamu lalikulu lidamtsata iye, chifukwa iwo adawona zozizwa zake zimene iye adachita pa iwo amene adali wodwala.
  3117. Jhn 6:3 Ndipo Yesu adakwera kuphiri, ndipo kumeneko anakhala pansi pamodzi ndi wophunzira ake.
  3118. Jhn 6:4 Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, lidayandikira.
  3119. Jhn 6:5 ¶Pamene Yesu kenaka adakweza maso [ake], ndi kuwona kuti khamu lalikulu lirinkudza kwa iye, iye adanena kwa Filipi, Tidzagula kuti ife mikate, kuti awa akhoze kudya?
  3120. Jhn 6:6 Ndipo ichi adanena kuti amuyese iye: pakuti iye yekha adadziwa chimene iye adzachita.
  3121. Jhn 6:7 Filipi adayankha iye, Mikate ya ndalama mazana awiri siyikwanira iwo, kuti aliyense wa iwo atenge pang’ono.
  3122. Jhn 6:8 M’modzi wa wophunzira ake, Anduru, mbale wake wa Simoni Petro, adanena kwa iye.
  3123. Jhn 6:9 Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate ya balere isanu, ndi nsomba zazing’ono ziwiri: koma nanga izi zingatani pa ambiri otere?
  3124. Jhn 6:10 Ndipo Yesu adati, Akhalitseni anthu pansi. Tsopano padali udzu wambiri pamalopo. Kotero amunawo adakhala pansi, mu chiwerengero cha pafupifupi zikwi zisanu.
  3125. Jhn 6:11 Ndipo Yesu adatenga mikateyo; ndipo pamene iye adayamika, iye adagawira kwa wophunzira; ndipo wophunzira kwa iwo amene adakhala pansi; momwemo ndi nsomba monga mwa kuchuluka komwe iwo adafuna.
  3126. Jhn 6:12 Pamene iwo adakhuta, iye adanena kwa wophunzira ake, Sonkhanitsani makombo, kuti pasakhale kotayika.
  3127. Jhn 6:13 Choncho iwo adasonkhanitsa [makombowo] pamodzi, ndipo anadzadza mitanga khumi ndi iwiri ndi makombo a mikate isanuyo ya balere, imene idatsalira koposera ndi pamwamba kwa iwo amene adadyawo.
  3128. Jhn 6:14 Kenaka anthu awo, pamene adawona chozizwa chimene Yesu adachita, adanena, Ichi ndicho chowonadi chakuti mneneriyo ayenera kudza m’dziko lapansi.
  3129. Jhn 6:15 ¶Choncho pamene Yesu adazindikira kuti iwo alikufuna kubwera kudzamtenga iye mokakamiza, kuti amlonge iye ufumu, iye adachokanso kupita m’phiri pa yekha.
  3130. Jhn 6:16 Koma pamene [tsopano] adafika madzulo, wophunzira ake adatsikira kulowa m’nyanja;
  3131. Jhn 6:17 Ndipo adalowa m’chombo, ndipo anawoloka nyanja kupita ku Kaperenamu. Ndipo tsopano kunada, ndipo Yesu adali asanadze kwa iwo.
  3132. Jhn 6:18 Ndipo nyanja idawuka chifukwa cha mphepo yayikulu imene idawomba.
  3133. Jhn 6:19 Ndipo pamene adapalasa pafupifupi mitunda itatu kapena inayi, iwo awona Yesu akuyenda pamwamba pa nyanja, ndi kuyandikira chombo: ndipo iwo adachita mantha.
  3134. Jhn 6:20 Koma iye adati kwa iwo, Ndine; musakhala ndi mantha.
  3135. Jhn 6:21 Kenaka iwo mwakufuna kwawo adamlandira iye m’chombo: ndipo posakhalitsa chombo chidafika kumtunda kumene adalikunkako.
  3136. Jhn 6:22 ¶Tsiku lotsatira, pamene anthu amene adayima tsidya lina la nyanja adawona kuti padalibe chombo china pamenepo, kupatula chimodzi chokhacho chimene m’mene wophunzira ake adalowamo, ndi kuti Yesu sadapite pamodzi ndi wophunzira m’chombomo, koma [kuti] wophunzira ake adapita pawokha;
  3137. Jhn 6:23 (Ngakhale zinali choncho padadza zombo zina zidabwera kuchokera ku Tiberiyasi pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate, pamene atatha Ambuye kupereka mayamiko:)
  3138. Jhn 6:24 Choncho pamene anthu adawona kuti Yesu sadali pamenepo, kapenanso wophunzira ake, iwonso adalowa m’zombomo, ndipo anadza ku Kaperenamu, kumfunafuna Yesu.
  3139. Jhn 6:25 Ndipo pamene iwo adampeza iye tsidya lina la nyanja, iwo adati kwa iye, Mphunzitsi, munadza kuno liti?
  3140. Jhn 6:26 Yesu adayankha iwo ndipo anati, Ndithudi, ndithudi ndinena kwa inu, Inu mundifuna ine, sichifukwa inu mudawona zozizwa, koma chifukwa inu mudadya mkate, ndipo mudakhuta.
  3141. Jhn 6:27 Musagwira ntchito chifukwa cha chakudya chimene chitayika, koma chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha, chimene Mwana wamwamuna wa munthu adzakupatsani inu: pakuti ameneyo Mulungu Atate wamsindikiza chizindikiro.
  3142. Jhn 6:28 Kenaka iwo adati kwa iye, Tichite chiyani kuti tikhoze kuchita ntchito za Mulungu?
  3143. Jhn 6:29 Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Iyi ndiyo ntchito ya Mulungu, kuti inu mukhulupirire pa iye amene iyeyo wamtuma.
  3144. Jhn 6:30 Choncho iwo adati kwa iye, Chizindikiro chotani muwonetsa inu tsono, kuti ife tiwone ndi kukhulupirira inu? Kodi inu muchita ntchito yanji?
  3145. Jhn 6:31 Atate athu anadya mana m’chipululu cha mchenga; monga kwalembedwa, Iye adawapatsa iwo mkate wochokera kumwamba kuti adye.
  3146. Jhn 6:32 Kenaka Yesu adati kwa iwo, Ndithudi, ndithudi ndinena kwa inu, Mose sadakupatseni inu mkate umene uja wochokera kumwamba; koma Atate wanga amakupatsani inu mkate wowona wa kumwamba.
  3147. Jhn 6:33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye iye amene watsika pansi kuchoka kumwamba, ndipo apatsa moyo ku dziko lapansi.
  3148. Jhn 6:34 Kenaka iwo adati kwa iye, Ambuye, nthawi zonse tipatseni ife mkate umenewo.
  3149. Jhn 6:35 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo: iye amene adza kwa ine sadzamva njala, ndi iye amene akukhulupirira ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
  3150. Jhn 6:36 Koma ine ndidati kwa inu, Kuti inu mwandiwonanso ine, ndipo simukhulupirira ayi.
  3151. Jhn 6:37 Onse amene Atate andipatsa ine adzadza kwa ine; ndipo iye amene akudza kwa ine sindidzamtaya mwa njira ina iliyonse kunja.
  3152. Jhn 6:38 Pakuti ine ndidatsika kuchokera kumwamba, sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha iye amene adandituma ine.
  3153. Jhn 6:39 Ndipo ichi ndicho chifuniro cha Atate amene anandituma ine, kuti mwa zonse za zimene iye wandipatsa ine ndisatayeko kalikonse, koma kuti ndichiwukitsenso ichi pa tsiku lomaliza.
  3154. Jhn 6:40 Ndipo ichi ndicho chifuniro cha iye amene anandituma ine, kuti aliyense amene awona Mwana wamwamuna, ndi kukhulupirira pa iye, akhoze kukhala nawo moyo wosatha: ndipo ine ndidzamuwukitsa iye pa tsiku lomaliza.
  3155. Jhn 6:41 Kenaka Ayuda adang’ung’udza pa iye, chifukwa iye adati, Ine ndine mkate umene udatsika kuchokera kumwamba.
  3156. Jhn 6:42 Ndipo iwo adanena, Si Yesu uyu, Mwana wamwamuna wa Yosefe, amene atate wake ndi amayi wake ife tiwadziwa? Nanga tsono iye anena bwanji kuti, Ine ndidatsika kuchokera kumwamba?
  3157. Jhn 6:43 Choncho Yesu adayankha nati kwa iwo, Musang’ung’udze ayi pakati pa inu nokha.
  3158. Jhn 6:44 Palibe munthu angathe kudza kwa ine, pokhapokha ngati Atate amene wandituma ine amkoka iye: ndipo ine ndidzamuwukitsa pa tsiku lomaliza.
  3159. Jhn 6:45 Zalembedwa mwa aneneri, Ndipo iwo onse adzakhala wophunzitsidwa za Mulungu. Choncho munthu aliyense amene wamva ndipo waphunzira kwa Atate, adza kwa ine.
  3160. Jhn 6:46 Sikuti munthu wina aliyense wawona Atate, kupatula iye amene ali wa kwa Mulungu, iye wawona Atate.
  3161. Jhn 6:47 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Iye amene akhulupirira pa ine ali nawo moyo wosatha.
  3162. Jhn 6:48 Ine ndine mkate wa moyo.
  3163. Jhn 6:49 Atate anu adadya mana m’chipululu, ndipo adamwalira.
  3164. Jhn 6:50 Uwu ndiye mkate wotsika kuchokera kumwamba, kuti munthu akhoze kudyako, ndi kusamwalira.
  3165. Jhn 6:51 Ine ndine mkate wamoyo wotsika kuchokera kumwamba: ngati munthu aliyense akadyako mkate umenewu, iye adzakhala ndi moyo kwamuyaya: ndipo mkate umene ndidzapatsa ine ndiwo thupi langa, limene ine ndidzapereka chifukwa cha moyo wa dziko lapansi.
  3166. Jhn 6:52 Choncho Ayuda adatetana pakati pawo, kunena kuti, Kodi munthu uyu angathe kutipatsa ife thupi [lake] kuti tidye?
  3167. Jhn 6:53 Kenaka Yesu adati kwa iwo, Ndithudi, ndithudi, ine ndinena ndi inu, Pokhapokha inu mukadya thupi la Mwana wamwamuna wa munthu, ndi kumwa mwazi wake, inu mulibe moyo mwa inu.
  3168. Jhn 6:54 Iye amene akudya thupi langa, ndi kumwa mwazi wanga, ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuwukitsa iye pa tsiku lomaliza.
  3169. Jhn 6:55 Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.
  3170. Jhn 6:56 Iye amene akudya thupi langa, ndi kumwa mwazi wanga, akhala mwa ine, ndi ine mwa iye.
  3171. Jhn 6:57 Monga Atate wamoyo wandituma ine, ndipo inenso ndiri ndi moyo mwa Atate: kotero iye amene adya ine, ngakhale iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha ine.
  3172. Jhn 6:58 Uwu ndiwo mkate wotsika kuchokera kumwamba: osati monga atate wanu, adadya mana, ndipo anamwalira: iye amene adyako mkate uwu adzakhala ndi moyo nthawi zonse.
  3173. Jhn 6:59 Zinthu izi iye adanena m’sunagogemo, pamene iye ankaphunzitsa mu Kaperenamu.
  3174. Jhn 6:60 Choncho ambiri a wophunzira ake, pamene iwo adamva [izi], adati, Ichi ndi chonena chosawutsa; ndani akhoza kumva ichi?
  3175. Jhn 6:61 Pamene Yesu adadziwa mwa iye yekha kuti wophunzira ake adang’ung’udza pa ichi, iye adati kwa iwo, Kodi ichi chikhumudwitsa inu?
  3176. Jhn 6:62 [Nanga] bwanji ndipo ngati inu mukadzawona Mwana wamwamuna wa munthu alikukwera kumene iye adali kale?
  3177. Jhn 6:63 Mzimu ndiye amene apatsa moyo; thupi silipindulitsa kalikonse: mawu amene ine ndilankhula kwa inu, [ali] mzimu, ndipo [ali] moyo.
  3178. Jhn 6:64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira ayi. Pakuti Yesu adadziwa kuyambira pochiyambi iwo amene adali amene sadakhulupirire ayi, ndi amene adzampereka iye.
  3179. Jhn 6:65 Ndipo iye adanena, Choncho ndidati kwa inu, kuti palibe munthu angadze kwa ine, pokhapokha ngati kudakhala kopatsidwa kwa iye ndi Atate wanga.
  3180. Jhn 6:66 ¶Kuyambira pa [nthawi] imeneyo ambiri wophunzira ake adabwerera m’mbuyo, ndipo sadayendenso pamodzi ndi iye.
  3181. Jhn 6:67 Kenaka Yesu adati kwa khumi ndi awiriwo, Kodi inu mufunanso kuchoka?
  3182. Jhn 6:68 Kenaka Simoni Petro adamuyankha iye, Ambuye, kwa yani kumene ife tidzapita? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.
  3183. Jhn 6:69 Ndipo ife tikhulupirira ndipo titsimikiza kuti inu ndinu Khristu, Mwana wamwamuna wa Mulungu wamoyo.
  3184. Jhn 6:70 Yesu adawayankha iwo, Kodi sindidakusankhani inu khumi ndi awiri, ndipo m’modzi wa inu ali mdierekezi?
  3185. Jhn 6:71 Iye adanena za Yudase Iskariyote, [mwana wamwamuna] wa Simoni: pakuti iye ndiye amene adzampereka iye, wokhala m’modzi wa khumi ndi awiri.
  3186. Jhn 7:1 Ndipo zitapita izi Yesu adayenda mu Galileya: pakuti sadafuna kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda adafuna kumupha iye.
  3187. Jhn 7:2 Tsopano phwando la Ayuda la misasa, lidali pafupi.
  3188. Jhn 7:3 Choncho abale ake adati kwa iye, Chokani pano, ndipo mupite kulowa m’Yudeya, kuti wophunzira anunso akhoze kupenya ntchito zanu zimene mukuchita.
  3189. Jhn 7:4 Pakuti [palibe] munthu aliyense [amene] amachita kanthu kalikonse mwa m’seri, ndipo iye yekha nafuna kudziwika poyera. Ngati inu mukuchita zinthu izi, dziwonetsereni eni nokha ku dziko lapansi.
  3190. Jhn 7:5 Pakuti angakhale abale ake sadakhulupirira mwa iye.
  3191. Jhn 7:6 Kenaka Yesu adanena kwa iwo, Nthawi yanga siyidafike: koma nthawi yanu ili yokonzeka nthawi zonse.
  3192. Jhn 7:7 Dziko lapansi silingakudeni inu; koma ine lindida, chifukwa ine ndichitira umboni za ilo, kuti ntchito zake ziri zoyipa.
  3193. Jhn 7:8 Kwerani inu kupita ku phwando: Ine sindikwera tsono ku phwando ili: pakuti nthawi yanga siyidakwanire kwathunthu.
  3194. Jhn 7:9 Pamene adanena mawu awa kwa iwo, iye adakhalabe mu Galileya.
  3195. Jhn 7:10 ¶Koma pamene abale ake adakwera kupita, kenaka adapitanso iye kukwera ku phwando, osati mowonekera, koma monga mobisika.
  3196. Jhn 7:11 Kenaka Ayuda adalikumfuna iye ku phwando, ndipo ananena, Ali kuti iye?
  3197. Jhn 7:12 Ndipo padali kung’ung’udza kwambiri pakati pa anthu zokhudza iye: popeza ena adanena kuti, Ali munthu wabwino: ena adanena, Iyayi: koma iye asocheretsa anthu.
  3198. Jhn 7:13 Ngakhale zidali choncho padalibe munthu adalankhula za iye poyera chifukwa cha kuwopa Ayuda.
  3199. Jhn 7:14 ¶Tsopano cha pakatikati pa phwando Yesu adakwera nalowa m’kachisi, ndipo anaphunzitsa.
  3200. Jhn 7:15 Ndipo Ayuda adazizwa, nanena kuti, Munthu uyu adziwa bwanji zilemba, pokhala wosaphunzira?
  3201. Jhn 7:16 Yesu adayankha iwo, ndipo anati, Chiphunzitso changa si chili changa, koma cha iye amene adandituma ine.
  3202. Jhn 7:17 Ngati munthu aliyense adzachita chifuniro chake, adzadziwa za chiphunzitsocho, ngati chili cha kwa Mulungu, kapena [ngati] ndilankhula zochokera kwa ine ndekha.
  3203. Jhn 7:18 Iye amene alankhula za iye yekha afunafuna ulemu wa mwini yekha: koma iye amene afunafuna ulemerero wa iye amene adamtuma iye, yemweyu ali wowona, ndipo mulibe chosalungama mwa iye.
  3204. Jhn 7:19 Kodi Mose sadakupatsani inu chilamulo, ndipo palibe ndi m’modzi [yemwe] mwa inu asunga chilamulocho? Chifukwa chiyani mufuna kundipha ine?
  3205. Jhn 7:20 Anthuwo adayankha ndipo anati, Inu muli ndi chiwanda: ndani akufunafuna kukuphani inu?
  3206. Jhn 7:21 Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Ine ndachita ntchito imodzi, ndipo inu nonse muzizwa.
  3207. Jhn 7:22 Choncho Mose adakupatsani inu mdulidwe; (osati chifukwa chakuti uli wa Mose, koma wa atate;) ndipo muchita munthu mdulidwe tsiku lasabata.
  3208. Jhn 7:23 Ngati munthu pa tsiku la sabata alandira mdulidwe, kuti chilamulo cha Mose chisaphwanyidwe; kodi inu muli wokwiya ndi ine, chifukwa ndamchiritsa munthu kwathunthu tsiku lasabata?
  3209. Jhn 7:24 Musaweruze monga mwamawonekedwe, koma weruzani chiweruzo cholungama.
  3210. Jhn 7:25 Kenaka adanena ena a iwo a ku Yerusalemu, Kodi uyu si iye, amene iwo afuna kumupha?
  3211. Jhn 7:26 Koma, tawona, iye ayankhula molimba mtima, ndipo iwo sadanena kanthu kwa iye. Kodi olamulira akudziwa ndithu kuti uyu ndi Khristu amene?
  3212. Jhn 7:27 Ngakhale ziri choncho ife tidziwa kumene munthu uyu akuchokera: koma pamene Khristu adzabwera, palibe munthu m’modzi adziwa kumene adzachokera.
  3213. Jhn 7:28 Kenaka Yesu adafuwula m’kachisi pamene iye analikuphunzitsa, kunena kuti, Inu nonse mudziwa ine, ndiponso inu mudziwa kumene ine ndichokera: ndipo ine sindidadza kwa ine ndekha, koma iye amene anandituma ine ali wowona, amene inu simumdziwa ayi.
  3214. Jhn 7:29 Koma ine ndimdziwa iye: pakuti ndiri wochokera kwa iye, ndipo iye wandituma ine.
  3215. Jhn 7:30 Kenaka adafuna kumgwira iye: koma padalibe munthu aliyense adamgwira iye, chifukwa ora lake lidali lisadafike.
  3216. Jhn 7:31 Ndipo ambiri a anthuwo adakhulupirira pa iye; ndipo adanena, Pamene Khristu abwera, kodi iye adzachita zozizwa zambiri zoposa zimene [munthu] uyu wazichita?
  3217. Jhn 7:32 ¶Afarisi adamva kuti anthu ali kung’ung’udza zinthu zotere zokhudza iye; ndipo Afarisi ndi ansembe akulu adatuma asirikali kuti akamgwire iye.
  3218. Jhn 7:33 Kenaka Yesu adati kwa iwo, Tsono kwa kanthawi kochepa ine ndiri ndi inu, ndipo [kenaka] ine ndimuka kwa iye amene anandituma ine.
  3219. Jhn 7:34 Inu mudzafunafuna ine, ndipo simudzandipeza [ine]: ndipo komwe ndiri ine, [kumeneko] inu simungathe kudzako.
  3220. Jhn 7:35 Kenaka Ayuda adati pakati pa iwo wokha, Kodi adzapita kuti iye, kuti ife sitikangampeze iye? Kodi iye adzapita kwa wobalalikawo pakati pa Amitundu, ndi kuphunzitsa Amitunduwo?
  3221. Jhn 7:36 Kodi ndi kunena [kotani] uku kumene iye wanena, Inu mudzandifunafuna ine, ndipo simudzandipeza [ine]: ndipo komwe ndiri ine, [kumeneko] inu simungathe kudzako?
  3222. Jhn 7:37 Mu [tsiku] lomaliza la phwando, tsiku lalikulu la phwandolo, Yesu adayimirira nafuwula, kunena kuti, Ngati munthu wina aliyense akumva ludzu, iye abwere kwa ine, ndi kumwa.
  3223. Jhn 7:38 Iye amene akhulupirira pa ine, monga malembo anena, kutuluka mkati mwake idzayenda mitsinje ya madzi a moyo.
  3224. Jhn 7:39 (Koma ichi adanena za Mzimu, amene iwo amene akhulupirira pa iye ayenera kulandira: pakuti Mzimu Woyera adali asadaperekedwe [pamenepo]; chifukwa chakuti Yesu adali asadalemekezedwe.)
  3225. Jhn 7:40 ¶Choncho ambiri a anthuwo, pamene adamva kunena uku, adanena, Mwa chowonadi uyu ndi Mneneriyo.
  3226. Jhn 7:41 Ena adanena, Uyu ndi Khristu, Koma ena adanena, kodi Khristu abwera kutuluka mu Galileya?
  3227. Jhn 7:42 Kodi malembo sadati, Kuti Khristu adzabwera mwa mbewu ya Davide, ndi kuchokera mu mzinda wa Betelehemu, kumene Davide adali?
  3228. Jhn 7:43 Kotero kudakhala kugawikana [pawiri] pakati pa anthuwo chifukwa cha iye.
  3229. Jhn 7:44 Ndipo ena a iwo adafuna kumgwira iye; koma munthu aliyense sadamgwira iye.
  3230. Jhn 7:45 ¶Kenaka anadza asirikaliwo kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwo adati kwa iwo, Chifukwa chiyani inu simudamtenga iye?
  3231. Jhn 7:46 Asirikaliwo adayankha, Palibe munthu adayankhulapo mofanana ndi munthu uyu.
  3232. Jhn 7:47 Kenaka Afarisi adayankha iwo, Kodi inunso mwanyengedwa?
  3233. Jhn 7:48 Kodi wina wa olamulira kapena wa Afarisi adakhulupirira pa iye?
  3234. Jhn 7:49 Koma anthu awa amene sadziwa chilamulo ali wotembereredwa.
  3235. Jhn 7:50 Nikodemasi adanena kwa iwo, (iye amene adadza kwa Yesu ndi usiku, pokhala m’modzi wa iwo,)
  3236. Jhn 7:51 Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu [aliyense], osayamba kumva iye, ndi kudziwa chimene iye achita?
  3237. Jhn 7:52 Iwo adayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wa ku Galileya? Fufuza, ndipo uyang’ane: pakuti kuchokera m’Galileya simuwuka mneneri ayi.
  3238. Jhn 7:53 Ndipo munthu aliyense adapita ku nyumba yake.
  3239. Jhn 8:1 Yesu adapita ku phiri la Azitona.
  3240. Jhn 8:2 Ndipo m’mamawa adabweranso m’kachisi, ndipo anthu adadza kwa iye; ndipo iye anakhala pansi, ndipo adaphunzitsa iwo.
  3241. Jhn 8:3 Ndipo alembi ndi Afarisi adabwera naye kwa iye mkazi wogwidwa m’chigololo; ndipo pamene adamuyimika iye pakati,
  3242. Jhn 8:4 Iwo adanena kwa iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa, ali mkati mochita chigololo.
  3243. Jhn 8:5 Tsopano Mose m’chilamulo adatilamulira ife, kuti otere tiwaponye miyala: koma inu munena chiyani?
  3244. Jhn 8:6 Ichi iwo adanena, kumuyesa iye, kuti akhoze kumtsutsa iye. Koma Yesu adawerama pansi, ndipo ndi chala [chake] adalemba pansi [ngati kuti iye sadawamve iwo ayi].
  3245. Jhn 8:7 Kotero pamene adapitiriza kufunsabe iye, iye adadziweramutsa yekha, ndipo anati kwa iwo, Iye amene ali wopanda tchimo pakati pa inu, ayambe iye kuponya mwala pa iye.
  3246. Jhn 8:8 Ndipo kenanso adawerama, ndipo adalemba pansi.
  3247. Jhn 8:9 Ndipo iwo amene adamva [ichi], potsutsika ndi chikumbumtima [chawo chomwe], anatulukamo m’modzim’modzi, kuyambira wamkulu kwambiri, [ngakhale] kufikira wotsiriza: ndipo Yesu adatsala yekha, ndi mkazi akuyimirira pakati.
  3248. Jhn 8:10 Pamene Yesu adadziweramutsa yekha, ndipo sanawona wina aliyense koma mkaziyo, iye adati kwa iye, Mkazi, kodi ali kuti aja otsutsa iwe? Kodi palibe munthu adakutsutsa iwe?
  3249. Jhn 8:11 Iye adati, Palibe munthu [aliyense], Ambuye. Ndipo Yesu adati kwa iye, Inenso sindikutsutsa iwe: pita, ndipo usakachimwenso ayi.
  3250. Jhn 8:12 ¶Kenaka Yesu adalankhulanso kwa iwo, kunena kuti, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi: iye amene anditsata ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwunika kwa moyo.
  3251. Jhn 8:13 Choncho Afarisi adati kwa iye, Inu muchita umboni wa inu nokha; umboni wanu suli wowona.
  3252. Jhn 8:14 Yesu adayankha ndipo anati kwa iwo, Ngakhale ine ndichita umboni wa ine ndekha, [komatu] umboni wanga uli wowona: pakuti ndidziwa kumene ndichokerako, ndi komwe ndimukako; koma inu simunganene kumene ine ndichokera, ndi kumene ine ndipita.
  3253. Jhn 8:15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.
  3254. Jhn 8:16 Ndipo ngati ine ndiweruza, chiweruzo changa chili chowona: pakuti sindiri ndekha, koma ine ndi Atate amene adandituma ine.
  3255. Jhn 8:17 Zidalembedwanso m’chilamulo chanu, kuti umboni wa anthu awiri uli wowona.
  3256. Jhn 8:18 Ine ndine amene ndichita umboni wa ine ndekha, ndi Atate amene adandituma ine achita umboni wa ine.
  3257. Jhn 8:19 Kenaka iwo adanena kwa iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu adayankha, Inu simudziwa ine, kapena Atate wanga: inu mukadadziwa ine, inu mukadadziwanso Atate wanga.
  3258. Jhn 8:20 Mawu awa adalankhula Yesu ali m’nyumba yosungira chuma, pamene iye amaphunzitsa m’kachisi: ndipo palibe munthu adagwira iye; pakuti ora lake lidali lisadafike.
  3259. Jhn 8:21 Kenaka Yesu adatinso kwa iwo, Ine ndipita njira yanga, ndipo inu mudzandifuna ine, ndipo inu mudzafa m’machimo anu: kumene ine ndipita, inu simungafikeko.
  3260. Jhn 8:22 Kenaka Ayuda adanena, Kodi iye adzadzipha yekha? Pakuti iye akunena, Kumene ine ndipita, inu simungafikeko.
  3261. Jhn 8:23 Ndipo iye adanena kwa iwo, Inu ndinu wochokera pansi; Ine ndine wochokera kumwamba: inu ndinu a dziko lapansili; Ine sindiri wadziko lapansili.
  3262. Jhn 8:24 Choncho ndidati kwa inu, kuti inu mudzafa m’machimo anu, pakuti ngati inu simukhulupirira kuti ine [ndi iye], inu mudzafa m’machimo anu.
  3263. Jhn 8:25 Kenaka adanena iwo kwa iye, Inu ndinu yani? Yesu anena kwa iwo, Ngakhale [chomwecho] chimene ndidanena kwa inu kuyambira pachiyambi.
  3264. Jhn 8:26 Ine ndiri nazo zinthu zambiri kuti ndinene ndi zoweruza inu: koma iye amene anandituma ine ali wowona; ndipo ine ndilankhula kwa dziko lapansi zinthu izo zimene ndazimva kwa iye.
  3265. Jhn 8:27 Iwo sadamvetsetsa kuti iye adalikunena kwa iwo za Atate.
  3266. Jhn 8:28 Kenaka Yesu adati kwa iwo, Pamene inu mwakweza Mwana wamwamuna wa munthu, pamenepo inu mudzadziwa kuti ine [ndine iye], ndi [kuti] ine sindichita kanthu kwa ine ndekha; koma monga Atate wandiphunzitsa ine, ine ndilankhula zinthu izi.
  3267. Jhn 8:29 Ndipo iye amene anandituma ine ali ndi ine: Atate sadandisiye ine ndekha; chifukwa ine nthawi zonse ndichita zinthu zimene zimkondweretsa iye.
  3268. Jhn 8:30 Pamene iye adali kulankhula mawu awa, ambiri adakhulupirira pa iye.
  3269. Jhn 8:31 Kenaka Yesu adanena kwa Ayuda amene adakhulupirira pa iye, Ngati inu mupitirira kukhala m’mawu anga, [pamenepo] muli wophunzira anga ndithu;
  3270. Jhn 8:32 Ndipo inu mudzazindikira chowonadi ndipo chowonadi chidzakumasulani inu.
  3271. Jhn 8:33 ¶Iwo adamuyankha iye, Ife tiri mbewu ya Abrahamu, ndipo sitidakhalapo akapolo a munthu: munena bwanji inu, Inu mudzayesedwa mfulu?
  3272. Jhn 8:34 Yesu adayankha iwo, Ndithudi, ndithudi, ndinena kwa inu kuti aliyense wochita tchimo ali kapolo wa tchimo.
  3273. Jhn 8:35 Ndipo kapolo sakhala m’nyumba nthawi yonse: [koma] Mwana wamwamuna akhala nthawi zonse.
  3274. Jhn 8:36 Choncho ngati Mwana wamwamuna adzakuyesani inu aufulu, inu mudzakhala mfulu ndithu.
  3275. Jhn 8:37 Ine ndikudziwa kuti inu muli mbewu ya Abrahamu; koma mukufuna kundipha ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu.
  3276. Jhn 8:38 Ine ndilankhula zimene ndawona ziri ndi Atate wanga: ndipo inu muchita chimene mudawona kwa atate wanu.
  3277. Jhn 8:39 Iwo adamuyankha ndipo anati kwa iye, Abrahamu ndi atate wathu. Yesu adanena kwa iwo, Ngati inu mukadakhala ana a Abrahamu, inu mukadachita ntchito za Abrahamu.
  3278. Jhn 8:40 Koma tsopano mufuna kundipha ine, munthu amene wakuwuzani inu chowonadi, chimene ine ndidamva kwa Mulungu: ichi sadachita Abrahamu.
  3279. Jhn 8:41 Inu muchita ntchito za atate wanu. Kenaka iwo adati kwa iye, Ife sitinabadwe m’chiwerewere; tiri ndi Atate m’modzi, [ndiye] Mulungu.
  3280. Jhn 8:42 Yesu adati kwa iwo, Ngati Mulungu akadakhala Atate wanu, inu mukadakonda ine: pakuti ine ndidatuluka ndi kuchokera kwa Mulungu; ine sindidadza mwa ine ndekha, koma iyeyu adandituma ine.
  3281. Jhn 8:43 Chifukwa chiyani simuzindikira malankhulidwe anga? [Ngakhale] chifukwa inu simungathe kumva mawu anga.
  3282. Jhn 8:44 Inu muli wa atate [wanu] mdierekezi, ndipo zilakolako za atate wanu inu mufuna kuchita. Iyeyu adali wakupha kuyambira pachiyambi, ndipo sadakhale m’chowonadi, chifukwa mulibe chowonadi mwa iye. Pamene alankhula bodza, iye alankhula za mwini yekha: pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa ilo.
  3283. Jhn 8:45 Ndipo chifukwa ine ndinena ndi [inu] chowonadi, inu simukhulupirira ine ayi.
  3284. Jhn 8:46 Ndani wa inu anditsutsa ine za tchimo? Ndipo ngati ine ndinena chowonadi, chifukwa chiyani simukhulupirira ine?
  3285. Jhn 8:47 Iye amene ali wa kwa Mulungu akumva mawu a Mulungu: inu choncho simumva [awo], chifukwa chakuti inu simuli a kwa Mulungu.
  3286. Jhn 8:48 Kenaka Ayuda adayankha ndipo anati kwa iye, Kodi ife sitinenetsa bwino kuti inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?
  3287. Jhn 8:49 Yesu adayankha, Ine ndiribe chiwanda; koma ine ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu simundilemekeza ine.
  3288. Jhn 8:50 Ndipo ine sindifunafuna ulemerero wa ine mwini: alipo m’modzi amene afunafuna ndipo aweruza.
  3289. Jhn 8:51 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Ngati munthu asunga zonena zanga, iye sadzawona imfa nthawi yonse.
  3290. Jhn 8:52 Kenaka Ayuda adati kwa iye, Tsopano ife tadziwa kuti inu muli ndi chiwanda. Abrahamu adamwalira, ndi aneneri; ndipo inu munena, Ngati munthu asunga zonena zanga, iye sadzalawa imfa ku nthawi yonse.
  3291. Jhn 8:53 Kodi inu ndinu wamkulu koposa atate wathu Abrahamu, amene adamwalira? Ndi aneneri adamwalira: mudziyeserera inu nokha muli yani?
  3292. Jhn 8:54 Yesu adayankha, Ngati ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wanga uli chabe: ndi Atate wanga amene andilemekeza ine; za amene inu munena, kuti ali Mulungu wanu:
  3293. Jhn 8:55 Komatu inu simunamudziwe iye; koma ine ndimdziwa iye: ndipo ngati ine ndiyenera kunena, ine sindimdziwa ayi, ine ndidzakhala wonama wofanana ndi inu: koma ine ndimdziwa iye, ndi kusunga zonena zake.
  3294. Jhn 8:56 Atate wanu Abrahamu adakondwera kuwona tsiku langa: ndipo iye adawona [ilo], ndipo anasangalala.
  3295. Jhn 8:57 Kenaka adanena Ayuda kwa iye, Inu simudafike zaka zakubadwa makumi asanu, ndipo inu mudawona Abrahamu?
  3296. Jhn 8:58 Yesu adati kwa iwo, Ndithudi, ndithudi, ndinena kwa inu, Asadakhale Abrahamu, Ine ndine.
  3297. Jhn 8:59 Kenaka iwo adatola miyala kuti amponye iye: koma Yesu anadzibisa mwini yekha, ndipo anatuluka m’kachisi, kudutsa pakati pa iwo, ndipo kotero anawadutsapo.
  3298. Jhn 9:1 Ndipo pamene [Yesu] amadutsapo, iye adawona munthu amene adali wosawona chibadwire.
  3299. Jhn 9:2 Ndipo wophunzira ake adamfunsa iye, kunena kuti, Mphunzitsi, kodi adachimwa ndani, munthu uyu, kapena makolo ake, kuti iye adabadwa wosawona?
  3300. Jhn 9:3 Yesu adayankha, Sadachimwa munthu uyu, kapena makolo ake: koma kuti ntchito za Mulungu zikawonetsedwe mwa iye.
  3301. Jhn 9:4 Ine ndiyenera kugwira ntchito za iye amene adandituma ine, akadali masana: usiku ukudza, pamene palibe munthu angagwire ntchito.
  3302. Jhn 9:5 Pa nthawi yonse yakukhala ine m’dziko lapansi, ine ndiri kuwunika kwa dziko lapansi.
  3303. Jhn 9:6 Pamene iye adanena motero, iye adalavulira pansi, ndipo anapanga thope ndi malovuwo, ndipo anadzoza maso a munthu wosawonayo ndi thopelo,
  3304. Jhn 9:7 Ndipo adati kwa iye, Pita, ukasambe mu thamanda la Siloamu (limene liri lotanthawuzidwa, Wotumidwa.) Choncho iye adapita pa njira yake, ndipo anasamba, ndipo anabwera akuwona.
  3305. Jhn 9:8 ¶Choncho anansi ake, ndi iwo amene adamuwona kale kuti adali wosawona, adanena, Kodi si uyu uja amene adalikukhala ndi kupemphapempha?
  3306. Jhn 9:9 Ena adanena, Ndi iyeyu: ena [adanena], Iye afanana ndi iye: [koma] iye adati, Ine ndine [amene].
  3307. Jhn 9:10 Choncho adanena kwa iye, Nanga maso ako adatseguka bwanji?
  3308. Jhn 9:11 Iye adayankha ndipo anati, Munthu wotchedwa Yesu adapanga thope, ndipo anadzoza maso anga, ndipo anati kwa ine, Pita ku thamanda la Siloamu, ndipo ukasambe: ndipo ine ndidapita ndikukasamba, ndipo ndinalandira kuwona.
  3309. Jhn 9:12 Kenaka iwo adati kwa iye, Ali kuti iyeyo? Iye adati, Ine sindikudziwa ayi.
  3310. Jhn 9:13 ¶Iwo adambweretsa kwa Afarisi iye amene adali wosawona kale.
  3311. Jhn 9:14 Ndipo lidali tsiku lasabata limene Yesu adapanga thopelo, ndi kutsegula maso ake.
  3312. Jhn 9:15 Kenaka Afarisi adamfunsanso iye m’mene iye adawonera. Iye adati kwa iwo, Iye adapaka thope pa maso anga, ndipo ine ndidasamba, ndipo ndikuwona.
  3313. Jhn 9:16 Choncho adanena ena a Afarisi, Munthu uyu si ali wa kwa Mulungu, chifukwa sasunga tsiku lasabata. Ena adanena, Munthu ngati ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zozizwa zotere? Ndipo padali kugawikana pawiri pakati pa iwo.
  3314. Jhn 9:17 Iwo adanenanso kwa wosawonayo, Iwe unenanji za iye, kuti iye wakutsegula maso ako. Iye adati, Iye ali mneneri.
  3315. Jhn 9:18 Koma Ayuda sadakhulupirira zokhudza iye, kuti iye adali wosawona, ndipo analandira kuwona kwake, kufikira pamene adayitana makolo ake a iye amene adalandira kuwona kwake.
  3316. Jhn 9:19 Ndipo iwo adawafunsa iwo, kunena kuti, Kodi mwana wamwamuna uyu ndi wanu, amene inu munena kuti adabadwa wosawona? Kodi tsono iye awona bwanji tsopano?
  3317. Jhn 9:20 Makolo ake adayankha iwo ndipo anati, Ife tikudziwa kuti mwana wamwamuna uyu ndi wathu, ndi kuti iye anabadwa wosawona.
  3318. Jhn 9:21 Koma momwe umo wawonera tsopano, ife sitidziwa ayi; kapena iye amene adamtsegula maso ake, ife sitimdziwa ayi, iye ali wamsinkhu; mumfunse iye: iye adzadzilankhulira mwini yekha.
  3319. Jhn 9:22 [Mawu] awa adalankhula makolo ake, chifukwa iwo adawopa Ayuda: pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzavomereza iye kuti ndiye Khristu, iye adzachotsedwa m’sunagoge.
  3320. Jhn 9:23 Choncho makolo ake adati, iye ali wamsinkhu; mufunse iye.
  3321. Jhn 9:24 Kenaka iwo adamuyitananso munthu amene adali wosawonayo, ndipo anati kwa iye, Pereka kwa Mulungu matamando: ife tidziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.
  3322. Jhn 9:25 Iye adayankha ndipo anati, Kaya iye ndi wochimwa [kapena ayi], ine sindikudziwa ayi: chinthu chimodzi ndichidziwa, kuti, pakale ine ndidali wosawona, tsopano ndiwona.
  3323. Jhn 9:26 Kenaka iwo adatinso kwa iye, Kodi iye anachita chiyani kwa iwe? Kodi adatsegula motani iye maso ako?
  3324. Jhn 9:27 Iye adayankha iwo, Ine ndakuwuzani kale, ndipo inu simudamve: bwanji nanga mufuna kumvanso [izi]? Kodi inunso mufuna kukhala wophunzira ake?
  3325. Jhn 9:28 Kenaka iwo adamulalatira iye, ndipo anati, Iwe ndiwe wophunzira wake; koma ife ndife wophunzira a Mose.
  3326. Jhn 9:29 Ife tidziwa kuti Mulungu adalankhula kwa Mose: [koma za] munthu ameneyu, ife sitikudziwa kumene achokera iye.
  3327. Jhn 9:30 Munthuyo adayankha ndipo anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mwa iye muli chinthu chozizwitsa, kuti inu simudziwa kumene iye achokera, ndipo [tsono] iye watsegula maso anga.
  3328. Jhn 9:31 Tsopano tidziwa kuti Mulungu samvera wochimwa: koma ngati munthu aliyense akhala wolambira wa Mulungu, ndipo achita chifuniro chake, iye amvera iyeyo.
  3329. Jhn 9:32 Kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi sikudamveka kuti munthu wina adatsegulira maso munthu amene adali wosawona chibadwire.
  3330. Jhn 9:33 Ngati munthuyu sadali wa kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kalikonse.
  3331. Jhn 9:34 Ndipo iwo adayankha ndipo anati kwa iye, Iwe unabadwa konsekonse m’machimo, ndipo kodi iwe utiphunzitse ife? Ndipo iwo adamponya iye kunja.
  3332. Jhn 9:35 Yesu adamva kuti iwo adamponya kunja; ndipo iye atampeza iye, iye adati kwa iye, Kodi iwe ukhulupirira pa Mwana wamwamuna wa Mulungu?
  3333. Jhn 9:36 Iye adayankha ndipo anati, Iyeyo ndani, Ambuye, kuti ine ndikhulupirire pa iye?
  3334. Jhn 9:37 Ndipo Yesu adati kwa iye, Iwe wamuwona iye, ndiponso ndi iye amene akulankhula ndi iwe.
  3335. Jhn 9:38 Ndipo iye adati, Ambuye, ine ndikhulupirira. Ndipo iye adamulambira iye.
  3336. Jhn 9:39 ¶Ndipo Yesu adati, Chifukwa cha chiweruzo ine ndadza ku dziko lino lapansi, kuti iwo amene sapenya akhoze kupenya; ndi kuti iwo amene apenya akhoze kusanduka wosawona.
  3337. Jhn 9:40 Ndipo [ena] a Afarisi amene adali ndi iye adamva mawu awa, ndipo adati kwa iye, Kodi ifenso ndife wosawona?
  3338. Jhn 9:41 Yesu adati kwa iwo, inu mukadakhala wosawona, inu simukadakhala ndi tchimo: koma tsopano inu munena, kuti, Ife tipenya; choncho tchimo lanu likhala chikhalire.
  3339. Jhn 10:1 Ndithudi, ndithudi, ndinena kwa inu, Iye amene salowera pakhomo mkhola la nkhosa, koma akwerera pa njira ina, yemweyu ndi wakuba ndi wolanda.
  3340. Jhn 10:2 Koma iye wolowera pakhomo ndiye mbusa wa nkhosazo.
  3341. Jhn 10:3 Kwa iyeyu wapakhomo amtsegulira; ndipo nkhosa zimva mawu ake: ndipo iye ayitana nkhosa za iye yekha ndi mayina awo, ndipo azitsogolera [kutuluka] kunja.
  3342. Jhn 10:4 Ndipo pamene atulutsa nkhosa za iye yekha, iye azitsogolera izo; ndi nkhosazo zimtsata iye: pakuti zidziwa mawu ake.
  3343. Jhn 10:5 Ndipo mlendo, izo sizidzamtsata ayi, koma zidzamthawa iye: pakuti sizidziwa mawu a alendo.
  3344. Jhn 10:6 Fanizo ili Yesu adanena kwa iwo: koma iwo sadazindikire ayi zinthu zimene iye adayankhula kwa iwo.
  3345. Jhn 10:7 Kenaka Yesu adanenanso kwa iwo, Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Ine ndine khomo la nkhosa.
  3346. Jhn 10:8 Onse amene adadza mtsogolo mwa ine ali akuba ndi wolanda: koma nkhosazo sizidamva iwo.
  3347. Jhn 10:9 Ine ndine khomo: mwa ine ngati munthu wina alowerapo, iye adzapulumutsidwa, ndipo adzalowa ndi kutuluka, ndipo adzapeza msipu.
  3348. Jhn 10:10 Mbala siyikudza, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuwononga: Ine ndadza kuti iwo akhoze kukhala ndi moyo, ndi kuti akhoze kukhala nawo wochuluka.
  3349. Jhn 10:11 Ine ndine mbusa wabwino: mbusa wabwino apereka moyo wake chifukwa cha nkhosa.
  3350. Jhn 10:12 Koma iye amene ali wolipidwa, ndipo osati mbusayo, amene nkhosa zake zomwe sizikhala za iye ayi, akawona mmbulu ulinkudza, ndipo amasiya nkhosazo, ndipo amathawa: ndipo mmbulu uzigwira izo, ndi kubalalitsa nkhosa;
  3351. Jhn 10:13 Wolipidwa amathawa, chifukwa iye ali wolipidwa, ndipo sasamalira za nkhosazo.
  3352. Jhn 10:14 Ine ndine mbusa wabwino; ndipo ndizindikira [nkhosa] zanga, ndipo ine ndidziwika ndi zanga.
  3353. Jhn 10:15 Monga Atate andidziwa ine, motero momwemo ine ndimdziwa Atate: ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosazo.
  3354. Jhn 10:16 Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili: izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo izo zidzamva mawu anga; ndipo padzakhala khola limodzi, [ndi] mbusa m’modzi.
  3355. Jhn 10:17 Choncho Atate andikonda ine, chifukwa ine nditaya moyo wanga, kuti ndikhoze kuwutenganso.
  3356. Jhn 10:18 Palibe munthu wina awutenga kuchokera kwa ine, koma ine ndiwutaya mwa ine ndekha. Ine ndiri ndi mphamvu yakuwutaya, ndiponso ndiri nayo mphamvu yakuwutenganso. Lamulo ili ndalandira ine kwa Atate wanga.
  3357. Jhn 10:19 ¶Choncho padakhalanso kugawanika pawiri pakati pa Ayuda chifukwa cha zonena izi.
  3358. Jhn 10:20 Ndipo ambiri a iwo adanena, Iye ali ndi chiwanda, ndipo wachita misala; bwanji inu mukumvera iye?
  3359. Jhn 10:21 Ena adanena, Awa sali mawu a munthu amene ali ndi chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kutsegula maso a wosawona?
  3360. Jhn 10:22 ¶Ndipo kudali ku Yerusalemu, pa phwando la kudzipereka, ndipo idali nyengo yozizira.
  3361. Jhn 10:23 Ndipo Yesu adayenda m’kachisi m’khumbi la Solomoni.
  3362. Jhn 10:24 Kenaka anadza Ayuda namzungulira iye, ndipo ananena kwa iye, kwa nthawi yayitali bwanji inu mutipangitsa ife kuti tikayike? Ngati inu ndinu Khristuyo, tiwuzeni ife momveka.
  3363. Jhn 10:25 Yesu adayankha iwo, Ine ndinakuwuzani, ndipo inu simudakhulupirira ayi: ntchito zimene ine ndizichita m’dzina la Atate wanga, zichita umboni kwa ine.
  3364. Jhn 10:26 Koma inu simukhulupirira ayi, chifukwa inu simuli a mwa nkhosa zanga, monga ine ndidanena kwa inu.
  3365. Jhn 10:27 Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo ine ndizidziwa izo, ndipo zinditsata ine:
  3366. Jhn 10:28 Ndipo ine ndipereka moyo wosatha kwa izo; ndipo izo sizidzawonongeka ku nthawi yonse, kapena munthu [aliyense] kuzikwatula izo kuzitulutsa m’dzanja langa.
  3367. Jhn 10:29 Atate wanga, amene adazipereka [izo] kwa ine ali wamkulu koposa onse; ndipo palibe [munthu] aliyense angathe kuzikwatula [izo] m’dzanja la Atate wanga.
  3368. Jhn 10:30 Ine ndi Atate [wanga] ndife amodzi.
  3369. Jhn 10:31 Kenaka Ayuda adatolanso miyala kuti amponye iye.
  3370. Jhn 10:32 Yesu adayankha iwo, Ntchito zambiri zabwino ndakuwonetsani zochokera kwa Atate; chifukwa cha iti mwa ntchito izo mundiponyera miyala ine?
  3371. Jhn 10:33 Ayuda adamuyankha iye, kunena kuti, Chifukwa cha ntchito yabwino ife sitikuponyerani miyala inu ayi; koma chifukwa cha kuchitira mwano Mulungu; ndi chifukwa chakuti inu; pokhala muli munthu, mudzipanga nokha kukhala Mulungu.
  3372. Jhn 10:34 Yesu adayankha iwo, Kodi sizidalembedwa m’chilamulo chanu, Ine ndidati, Inu muli milungu?
  3373. Jhn 10:35 Ngati adawatcha iwo milungu, kwa iwo amene mawu a Mulungu adawadzera, ndipo malembo sangathe kuthyoledwa;
  3374. Jhn 10:36 Kodi inu munena za iye, amene Atate adampatula, ndipo anamtuma m’dziko lapansi, Uchitira mwano Mulungu; chifukwa ine ndidati, Ine ndine Mwana wamwamuna wa Mulungu?
  3375. Jhn 10:37 Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira ine ayi.
  3376. Jhn 10:38 Koma ngati ndichita, mungakhale inu simukhulupirira ine ayi, khulupirirani ntchitozo: kuti inu mukhoze kudziwa, ndi kukhulupira, kuti Atate [ali] mwa ine, ndi ine mwa iwo.
  3377. Jhn 10:39 Choncho iwo adafunafunanso kuti amtenge iye: koma adapulumuka kuchoka m’dzanja lawo.
  3378. Jhn 10:40 Ndipo adachokanso napita kupitirira Yordano, kulowa ku malo kumene Yohane adalikubatiza poyamba; ndipo komweko adakhala.
  3379. Jhn 10:41 Ndipo ambiri anadza kwa iye, ndipo ananena, Yohane sadachita chozizwa: koma zinthu zonse Yohane adanena za munthu uyu zidali zowona.
  3380. Jhn 10:42 Ndipo ambiri adakhulupirira pa iye komweko.
  3381. Jhn 11:1 Tsopano munthu [wina] adadwala, [dzina lake] Lazarasi wa ku Betane, mzinda wa Mariya ndi mbale wake Marita.
  3382. Jhn 11:2 (Adali Mariya [uja] adadzoza Ambuye ndi mafuta, ndi kupukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazarasi adadwala.)
  3383. Jhn 11:3 Choncho alongo ake adatumiza [uthenga] kwa iye, kunena kuti, Ambuye, tawonani, iye amene inu mumkonda wadwala.
  3384. Jhn 11:4 Pamene Yesu adamva [izi], iye adati, Kudwala uku sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wamwamuna wa Mulungu alemekezedwe nako.
  3385. Jhn 11:5 Tsopano Yesu adakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazarasi.
  3386. Jhn 11:6 Choncho pamene iye adamva kuti iye akudwala, iye adakhalabe masiku awiri pa malo pomwepo pamane iye adali.
  3387. Jhn 11:7 Kenaka zitachitika kuti atanena kwa wophunzira [ake], Tiyeni ife tipitenso ku Yudeya.
  3388. Jhn 11:8 Wophunzira [ake] anena kwa iye, Ambuye, Ayuda posachedwa apa adalikufuna kukuponyerani inu miyala; ndipo inu mupitanso komweko kodi?
  3389. Jhn 11:9 Yesu adayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu aliyense ayenda usana, iye saphunthwa ayi, chifukwa iye apenya kuwunika kwa dziko ili lapansi.
  3390. Jhn 11:10 Koma ngati munthu ayenda usiku, iye aphunthwa, chifukwa mulibe kuwunika mwa iye.
  3391. Jhn 11:11 Zinthu izi adanena iye: ndipo zitachitika izi iye adanena kwa iwo, Bwenzi lathu Lazarasi ali m’tulo; koma ine ndipita, kuti ndikhoze kukamuwukitsa iye ku tulo.
  3392. Jhn 11:12 Kenaka wophunzira ake adati, Ambuye, ngati iye ali m’tulo, iye adzakhala bwino.
  3393. Jhn 11:13 Ngakhale ziri choncho Yesu adanena za imfa yake: koma iwowa adaganiza kuti iye adanena za mpumulo wa tulo.
  3394. Jhn 11:14 Kenaka Yesu adati kwa iwo momveka, Lazarasi wamwalira.
  3395. Jhn 11:15 Ndipo ine ndikondwera chifukwa cha inu kuti ine kudalibe kumeneko, ndi cholinga chakuti mukhoze kukhulupirira; komabe tiyeni tipite kwa iye.
  3396. Jhn 11:16 Kenaka adanena Tomasi, wotchedwa Didimasi, kwa wophunzira anzake, Ifenso tiyeni tipite, kuti tikakhoze kufera naye pamodzi.
  3397. Jhn 11:17 Kenaka pamene Yesu adadza, iye adapeza kuti iye adali [atagona] kale m’manda kwa masiku anayi.
  3398. Jhn 11:18 Tsopano Betane adali pafupi [ndi] ku Yerusalemu, kutalika kwake pafupifupi mitunda iwiri:
  3399. Jhn 11:19 Ndipo ambiri a Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa zokhudza mlongo wawo.
  3400. Jhn 11:20 Kenaka Marita, iye atangomva mosakhalitsa kuti Yesu alinkudza, adapita ndi kukomana ndi iye: koma Mariya adakhala [chikhalire] m’nyumba.
  3401. Jhn 11:21 Kenaka Marita adati kwa Yesu, Ambuye, inu mukadakhala kuno mlongo wanga sakadamwalira.
  3402. Jhn 11:22 Koma ine ndidziwa, kuti ngakhale tsopano lino, china chilichonse inu mudzapempha kwa Mulungu, Mulungu adzakupatsani inu [ichi].
  3403. Jhn 11:23 Yesu adanena kwa iye, Mlongo wako adzawukanso.
  3404. Jhn 11:24 Marita adanena kwa iye, Ine ndidziwa kuti adzawuka m’chiwukitso pa tsiku lomaliza.
  3405. Jhn 11:25 Yesu adati kwa iye, Ine ndine kuwuka, ndi moyo: iye amene akhulupirira mwa ine, angakhale anali atamwalira, komatu adzakhalabe ndi moyo:
  3406. Jhn 11:26 Ndipo aliyense wakukhala ndi moyo ndi kukhulupirira mwa ine sadzamwalira nthawi yonse. Kodi iwe ukhulupirira ichi?
  3407. Jhn 11:27 Iye adanena kwa iye, Inde, Ambuye; ine ndikhulupirira kuti inu ndinu Khristu, Mwana wamwamuna wa Mulungu, amene ayenera kudza m’dziko lapansi.
  3408. Jhn 11:28 Ndipo m’mene adanena motero, iye adapita pa njira yake, ndipo anayitana Mariya mbale wake m’seri, kunena kuti, Mphunzitsi wafika, ndipo akuyitana iwe.
  3409. Jhn 11:29 Atangomva [izi] mosakhalitsa, iye adanyamuka msanga, ndipo anabwera kwa iye.
  3410. Jhn 11:30 Tsopano Yesu adali asadafike mu mzinda, koma adali pamalo pomwe Marita adakomana ndi iye.
  3411. Jhn 11:31 Kenaka Ayuda amene adali naye m’nyumba, ndi kumtonthoza iye, pamene adawona Mariya, kuti adanyamuka mwamsanga ndi kutuluka, iwo anamtsata iye, kunena kuti, Iye alikupita kumanda kukalira komweko.
  3412. Jhn 11:32 Kenaka pamene Mariya adafika pamene Yesu adali, ndi kumuwona iye, iye adagwa pa mapazi ake, kunena kwa iye, Ambuye, inu mukadakhala kuno, mlongo wanga sakadamwalira.
  3413. Jhn 11:33 Choncho pamene Yesu adamuwona iye alikulira, ndiponso Ayuda akulira amene adadza ndi iye, iye adadzuma mumzimu, ndipo anavutika.
  3414. Jhn 11:34 Ndipo adati, Kodi mwamuyika kuti iye? Iwo adanena kwa iye, Ambuye, tiyeni ndipo mukawone.
  3415. Jhn 11:35 Yesu adalira.
  3416. Jhn 11:36 Kenaka Ayuda adanena, Tawonani momwe adamkondera iye!
  3417. Jhn 11:37 Ndipo ena a iwo adati, Sakadatha munthu uyu, amene adatsegula maso wosawona, kupangitsa kuti ngakhale munthu uyu kuti asafe?
  3418. Jhn 11:38 Choncho Yesu anadzumanso mwa iye yekha nafika kumanda. Lidali phanga, ndipo mwala udayikidwa pamenepo.
  3419. Jhn 11:39 Yesu adanena, Chotsani inu mwala. Marita, mlongo wake wa iye amene adamwalirayo, adanena kwa iye, Ambuye, panthawi ino iye akununkha: pakuti wakhala masiku anayi [atamwalira].
  3420. Jhn 11:40 Yesu adanena kwa iye, Kodi ine sindinati kwa iwe, kuti, ngati iwe ukhulupirira, iwe udzayenera kuwona ulemerero wa Mulungu?
  3421. Jhn 11:41 Kenaka iwo adachotsa mwalawo, [kuchoka pa malo] pamene womwalirayo adagonekedwa. Ndipo Yesu adakweza maso [ake], ndipo anati, Atate, Ine ndiyamika inu kuti mwandimva ine.
  3422. Jhn 11:42 Ndipo ine ndidadziwa kuti mumandimva ine nthawi zonse: koma chifukwa cha anthu amene alikuyimirirapo ine ndidanena [ichi], kuti iwo akhoze kukhulupirira kuti inu mwandituma ine.
  3423. Jhn 11:43 Ndipo m’mene iye adali atanena kotero, iye adafuwula ndi mawu okwera, Lazarasi, [tuluka] bwera kuno.
  3424. Jhn 11:44 Ndipo iye amene adali womwalirayo adatuluka kubwera, womangidwa dzanja ndi mwendo ndi nsalu za kumanda: ndi nkhope yake idamangidwa mozungulira ndi kansalu. Yesu adati kwa iwo, M’masuleni iye, ndipo mlekeni iye apite.
  3425. Jhn 11:45 Ndipo ambiri a Ayuda amene adadza kwa Mariya, ndipo adali atawona zinthu zimene Yesu adazichita, adakhulupirira pa iye.
  3426. Jhn 11:46 Koma ena a iwo adapita pa njira zawo kwa Afarisi, ndipo anawawuza iwo zinthu zimene Yesu adazichita.
  3427. Jhn 11:47 ¶Kenaka adasonkhanitsa ansembe akulu, ndi Afarisi, ndi akulu a bwalo, ndipo ananena, Kodi titani ife? Pakuti munthu uyu akuchita zozizwa zambiri.
  3428. Jhn 11:48 Ife ngati timleka iye kotero, [anthu] onse adzakhulupirira pa iye: ndipo Aroma adzabwera ndipo adzatenga malo athu ndi fuko lathu.
  3429. Jhn 11:49 Ndipo m’modzi wa iwo, [dzina lake] Kayefasi, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho, adati kwa iwo, Simudziwa kanthu kalikonse inu.
  3430. Jhn 11:50 Kapena simuganiza kuti nkokoma kwa ife kuti munthu m’modzi ayenera kufera anthu, ndi kuti fuko lonse lisawonongeke.
  3431. Jhn 11:51 Ndipo ichi iye sadanene kwa iye yekha: koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chimenecho, iye adanenera kuti Yesu adzafera fukolo;
  3432. Jhn 11:52 Ndipo osati chifukwa cha fuko ilo lokha ayi; koma kuti iye akasonkhanitse pamodzi mu m’modzi ana a Mulungu amene anabalalitsidwa kutaliwo.
  3433. Jhn 11:53 Kenaka kuyambira tsiku limenero iwo adapangana pamodzi kuti amuphe iye.
  3434. Jhn 11:54 Choncho Yesu sadayendayendanso mowonekera pakati pa Ayuda; koma adapita kumeneko m’dziko loyandikira ku chipululu, mu mzinda wotchedwa Efraimu, ndipo anapitirira kukhala komweko pamodzi ndi wophunzira ake.
  3435. Jhn 11:55 ¶Ndipo paskha wa Ayuda adali pafupi: ndipo ambiri adanyamuka kuchokera m’dzikolo kukwera kupita ku Yerusalemu asanafike paskha, kuti akadziyeretse iwo wokha.
  3436. Jhn 11:56 Kenaka iwo adali kumfuna Yesu, ndipo analankhulana pakati pawo, pamene iwo anayimirira m’kachisi, Muganiza motani inu, kuti iye sabwera kuphwando?
  3437. Jhn 11:57 Tsopano ansembe akulu ndi Afarisi adapereka lamulo, kuti, ngati munthu aliyense akudziwa kumene anali iye, iye awulule [ichi], kuti iwo akhoze kumtenga iye.
  3438. Jhn 12:1 Kenaka atatsala masiku asanu ndi limodzi lisanafike phwando la paskha Yesu adabwera ku Betane, kumene kudali Lazarasi amene adamwalirayo, amene iye adamuwukitsa kwa akufa.
  3439. Jhn 12:2 Kumeneko iwo adamkozera iye chakudya chamadzulo; ndipo Marita adatumikira: koma Lazarasi adali m’modzi wa iwo amene adakhala pa chakudya pamodzi ndi iye.
  3440. Jhn 12:3 Kenaka Mariya adatenga muyeso umodzi wa mafuta wonunkhira bwino a nardo, a mtengo wapatali, ndipo adadzodza mapazi a Yesu, ndipo anapukuta mapazi ake ndi tsitsi lake: ndipo nyumba idadzazidwa ndi m’nunkhiro wa mafutawo.
  3441. Jhn 12:4 Kenaka adanena m’modzi wa wophunzira ake Yudasi Isikariyote, [mwana wamwamuna] wa Simoni, amene adzayenera kumpereka iye,
  3442. Jhn 12:5 Bwanji mafuta wonunkhirawa sadagulitsidwe kwa ndalama mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa wosawuka?
  3443. Jhn 12:6 Ichi iye adanena, osati chifukwa chakuti adalikusamalira wosawuka; koma chifukwa iye adali mbala, ndipo amakhala ndi thumbalo, ndipo amaba zimene zimayikidwa m’menemo.
  3444. Jhn 12:7 Kenaka Yesu adati, Mlekeni iye: poyandikira tsiku la kuyikidwa kwanga iye anandisungira ichi.
  3445. Jhn 12:8 Pakuti wosawuka muli nawo pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma ine simuli nane inu nthawi zonse.
  3446. Jhn 12:9 Anthu ambiri a Ayuda choncho adadziwa kuti iye adali kumeneko: ndipo adabwera osati chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti akhoze kukawonanso Lazarasi, amene iye adamuwukitsa kwa akufa.
  3447. Jhn 12:10 ¶Koma ansembe akulu adapangana kuti akhoze kuphanso Lazarasi;
  3448. Jhn 12:11 Chifukwa chakuti pa chifukwa cha iye ambiri a Ayuda adachoka, ndipo anakhulupirira pa Yesu.
  3449. Jhn 12:12 ¶Pa tsiku lotsatira anthu ambiri amene adabwera ku phwando, pamene adamva kuti Yesu alikubwera ku Yerusalemu,
  3450. Jhn 12:13 Adatenga nthambi za mitengo ya kanjedza, ndipo anatuluka kukakomana ndi iye, ndipo anafuwula, Hosanna: Wodalitsika [ndiye] Mfumu ya Israyeli amene akudza m’dzina la Ambuye.
  3451. Jhn 12:14 Ndipo Yesu, m’mene adapeza kabulu, adakhala pamenepo; monga kwalembedwa,
  3452. Jhn 12:15 Usawope, mwana wamkazi wa Ziyoni: tawona, Mfumu yako idza, yokhala pa mwana wa bulu.
  3453. Jhn 12:16 Zinthu izi sadazimvetsetsa wophunzira ake poyamba: koma pamene Yesu adalemekezedwa, kenaka adakumbukira iwo kuti izi zidalembedwa kwa iye, ndi [kuti] iwo adamchitira zinthu izi iye.
  3454. Jhn 12:17 Choncho anthuwo amene adali pamodzi ndi iye pa nthawi imene adayitana Lazarasi kutuluka m’manda ake, ndi kumuwukitsa kwa akufa, achitira umboni.
  3455. Jhn 12:18 Pa chifukwa ichi anthuwo adakomananso ndi iye, pakuti iwo adamva kuti iye adachita chozizwa ichi.
  3456. Jhn 12:19 Choncho Afarisiwo adanena pakati pawo, Simuzindikira inu momwe simupindulirapo kanthu? Tawonani, dziko latsatira pambuyo pa iye.
  3457. Jhn 12:20 ¶Ndipo padali Ahelene ena pakati pa iwo amene adakwera kubwera kukalambira pa phwando.
  3458. Jhn 12:21 Choncho omwewo adabwera kwa Filipi, amene adali wa ku Betesayida wa m’Galileya, ndipo anamfunsa iye, kunena kuti, Mbuye, ife tifuna kuwona Yesu.
  3459. Jhn 12:22 Filipi adabwera ndipo anawuza Anduru: ndipo kenanso Anduru ndi Filipi awuza Yesu.
  3460. Jhn 12:23 ¶Ndipo Yesu adayankha iwo, kunena kuti, Ora lafika, kuti Mwana wamwamuna wa munthu alemekezedwe.
  3461. Jhn 12:24 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Pokhapokha ngati mbewu ya tirigu igwa m’nthaka ndi kufa, iyo ikhala yokha: koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.
  3462. Jhn 12:25 Iye amene akonda moyo wake adzawutaya; ndipo iye amene adana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha.
  3463. Jhn 12:26 Ngati munthu aliyense atumikira ine, iye anditsate ine; ndipo kumene ine ndiri, komwekonso kudzakhala wantchito wanga: ngati wina anditumikira ine, iyeyo Atate [wanga] adzamchitira ulemu.
  3464. Jhn 12:27 Tsopano moyo wanga uli wovutika; ndipo ine ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni ine ku ora ili: koma pa chifukwa ichi ine ndidadzera ora ili.
  3465. Jhn 12:28 Atate, Lemekezani dzina lanu. Kenaka adadza pamenepo mawu wochokera kumwamba [kunena kuti], Ine ndalilemekeza [ilo], ndipo ndirilemekezanso [ilo].
  3466. Jhn 12:29 Choncho anthu amene adayimirirapo, ndi kumva [izi], adanena kuti kudagunda: ena adanena, Mngelo adayankhula kwa iye.
  3467. Jhn 12:30 Yesu adayankha ndipo anati, Mawu awa sadafike chifukwa cha ine, koma chifukwa cha inu.
  3468. Jhn 12:31 Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi: tsopano kalonga wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja.
  3469. Jhn 12:32 Ndipo ine, ngati ine ndikwezedwa kuchoka kudziko, ndidzakoka [anthu] onse kwa ine.
  3470. Jhn 12:33 Ichi iye adanena, kuzindikiritsa imfa imene iye ayenera kufa.
  3471. Jhn 12:34 Anthuwo adayankha iye, Tidamva ife kuchokera m’chilamulo kuti Khristu akhala ku nthawi yonse: ndipo inu munena bwanji, Mwana wamwamuna wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wamwamuna wa munthu ameneyu ndani?
  3472. Jhn 12:35 Kenaka Yesu adati kwa iwo, Komatu ka nthawi kakang’ono kuwunikaku kuli ndi inu. Yendani pokhala muli nako kuwunika, kuti mwina mdima ungafike pa inu: pakuti iye amene ayenda mumdima sadziwa kumene apita.
  3473. Jhn 12:36 Pamene muli nako kuwunika, khulupirirani mu kuwunikako, kuti mukakhoze kukhala ana a kuwunika. Zinthu izi Yesu adalankhula, ndipo anadzibisa mwini yekha kwa iwo.
  3474. Jhn 12:37 ¶Koma ngakhale adachita zozizwa zambiri zotere pamaso pawo iwo, komabe iwo sadakhulupirira pa iye.
  3475. Jhn 12:38 Kuti chonena cha Yesaya mneneri chikhoze kukwaniritsidwa, chimene iye adalankhula, Ambuye kodi ndani wakhulupirira uthenga wathu? Ndipo ndi kwa ndani mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa iye?
  3476. Jhn 12:39 Choncho sadathe kukhulupirira, chifukwa chakuti Yesaya adatinso,
  3477. Jhn 12:40 Iye wachititsa khungu maso awo, ndi kuwumitsa mtima wawo; kuti iwo asawone ndi maso [awo], kapena kumvetsetsa ndi mtima [wawo], ndi kukhala wotembenuka, ndi kuti ine ndingawachiritse iwo.
  3478. Jhn 12:41 Zinthu izi adanena Yesaya, pamene adawona ulemerero wake, ndi kuyankhula za iye.
  3479. Jhn 12:42 ¶Ngakhale kudali kotero pakati pa akulu olamulira ambirinso adakhulupirira pa iye, koma chifukwa cha Afarisi iwo sadavomereza [iye], kuti mwina iwo angachotsedwe m’sunagoge:
  3480. Jhn 12:43 Pakuti adakonda ulemerero wa anthu koposa ulemu wa Mulungu.
  3481. Jhn 12:44 ¶Yesu adafuwula ndipo anati, Iye amene akhulupirira pa ine, sakhulupirira pa ine ayi, koma pa iye amene adandituma ine.
  3482. Jhn 12:45 Ndipo iye amene awona ine awona iye amene adandituma ine.
  3483. Jhn 12:46 Ine ndadza muwuni m’dziko lapansi, kuti aliyense amene akhulupirira pa ine asakhale mumdima.
  3484. Jhn 12:47 Ndipo ngati munthu aliyense amva mawu anga, ndi kusakhulupirira, Ine sindimuweruza ayi; pakuti ine sindinabwera kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.
  3485. Jhn 12:48 Iye amene andikana ine, ndipo salandira mawu anga, ali naye m’modzi amene aweruza iye: mawu amene ine ndayankhula, omwewa adzamuweruza iye m’tsiku lomariza.
  3486. Jhn 12:49 Pakuti ine sindinayankhula za ine ndekha; koma Atate amene anandituma ine, iye adandipatsa ine lamulo, zimene ine ndiyenera kunena, ndi zimene ine ndiyenera kuyankhula.
  3487. Jhn 12:50 Ndipo ine ndidziwa kuti lamulo lake liri moyo wosatha: choncho chilichonse chimene ndiyankhula, monga momwe Atate ananena kwa ine, motero ine ndiyankhula.
  3488. Jhn 13:1 Tsopano lisadafike phwando la paskha, pamene Yesu adadziwa kuti ora lake lidafika lakuti iye anyamuke kutuluka m’dziko lino lapansi kupita kwa Atate, m’mene adakonda ake a iye yekha amene adali m’dziko lapansi, iye adawakonda iwo kufikira mapeto.
  3489. Jhn 13:2 Ndipo mgonero utatha, mdierekezi atayika kale mu mtima wa Yudase Isikariyote, [mwana wamwamuna] wa Simoni, kuti akampereke iye;
  3490. Jhn 13:3 Yesu podziwa kuti Atate adapereka zinthu zonse m’manja mwake, ndi kuti iye adachokera kwa Mulungu, ndi kupita kwa Mulungu.
  3491. Jhn 13:4 Iye adanyamuka kuchoka pa mgonero, ndipo [anavula] nayika pambali zovala zake; ndipo adatenga chopukutira, ndipo anadzimanga yekha m’chiwuno.
  3492. Jhn 13:5 Atachita ichi iye adathira madzi mu chosambira, ndipo anayamba kusambitsa mapazi a wophunzira ake, ndi kuwapukuta [iwo] ndi chopukutira chimene iye adadzimanga nacho.
  3493. Jhn 13:6 Kenaka iye adadza kwa Simoni Petro: ndipo Petro adanena kwa iye, Ambuye, kodi inu mundisambitsa ine mapazi anga?
  3494. Jhn 13:7 Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Chimene ine ndichita iwe suchidziwa tsopano; koma iwe udzadziwa mtsogolo mwake.
  3495. Jhn 13:8 Petro adanena kwa iye, Inu simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu adayankha iye, Ngati ine sindikusambitsa iwe, iwe ulibe gawo ndi ine.
  3496. Jhn 13:9 Simoni Petro adanena kwa iye, Ambuye, osati mapazi anga wokha ayi, komanso manja [anga] ndi mutu [wanga].
  3497. Jhn 13:10 Yesu adanena kwa iye, Iye amene wasamba alibe kusowekera kupatula kusamba mapazi [ake], koma ayera monsemonse: ndipo inu ndinu woyera, koma osati nonse ayi.
  3498. Jhn 13:11 Pakuti iye adadziwa amene adzampereka iye; choncho iye adati. Inu simuli nonse woyera.
  3499. Jhn 13:12 Kotero atatha iye kusambitsa mapazi awo, ndi kuti adatenga zovala zake, ndipo adali atakhalanso pansi, iye anati kwa iwo, Mudziwa inu chimene ine ndachita kwa inu?
  3500. Jhn 13:13 Inu munditcha ine Mphunzitsi ndi Ambuye: ndipo inu munena bwino; pakuti [wotero] ndi ine.
  3501. Jhn 13:14 Ngati ine tsono, Ambuye ndi Mphunzitsi [wanu], ndasambitsa mapazi anu; inunso muyenera kusambitsa mapazi a wina ndi mnzake.
  3502. Jhn 13:15 Pakuti ine ndakupatsani inu chitsanzo, kuti inu muchite monga ine ndakuchitirani inu.
  3503. Jhn 13:16 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Wantchito sali wamkulu kuposa mbuye wake; kapena iye amene watumidwa kuposa iye amene wamtuma iye.
  3504. Jhn 13:17 Ngati inu mudziwa zinthu izi, wosangalala muli inu ngati muzichita izo.
  3505. Jhn 13:18 ¶Ine sindinena za inu nonse: ine ndikudziwa amene ndasankha: koma kuti malemba akhoze kukwaniritsidwa, Iye amene akudya mkate ndi ine wanyamula chidendene chake molimbana ndi ine.
  3506. Jhn 13:19 Tsopano ine ndinena kwa inu chisadadze, kuti, pamene chichitika, inu mukhoze kukhulupirira kuti [ndine] amene.
  3507. Jhn 13:20 Ndithudi, ndithudi, ndinena kwa inu, Iye amene alandira aliyense amene ndimtuma alandira ine; ndipo iye amene alandira ine alandira amene wandituma ine.
  3508. Jhn 13:21 Pamene Yesu adanena motero, iye adavutika mu mzimu, ndipo anachitira umboni, ndipo anati, Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, kuti m’modzi wa inu adzandipereka ine.
  3509. Jhn 13:22 Kenaka wophunzira adalinkupenyana wina ndi mnzake, ndi kukayikira za iye amene adanena.
  3510. Jhn 13:23 Tsopano padali amene adatsamira pa chifuwa cha Yesu m’modzi wa wophunzira ake, amene Yesu adamkonda.
  3511. Jhn 13:24 Choncho Simoni Petro adamkodolera kwa iye, kuti iye afunse amene ayenera kukhala yani amene iye adalankhula.
  3512. Jhn 13:25 Iyeyu tsono potsamira pa chifuwa cha Yesu adanena kwa iye, Ambuye, ndiye yani?
  3513. Jhn 13:26 Yesu adayankha, Iyeyu ndi, amene ine ndidzampatsa nthongo, pamenepo ine ndasunsa [iyo]. Ndipo m’mene adasunsa nthongoyo, iye adayipereka [iyo] kwa Yudase Isikariyote, [mwana wamwamuna] wa Simoni.
  3514. Jhn 13:27 Ndipo pambuyo pa nthongoyo Satana adalowa mwa iyeyu. Kenaka Yesu adanena kwa iye, Chimene iwe uchita, chita msanga.
  3515. Jhn 13:28 Tsopano padalibe munthu aliyense wa iwo pa gomepo adadziwa cholinga chotani chimene iye adanena ichi kwa iye.
  3516. Jhn 13:29 Pakuti ena a [iwo] adaganiza, chifukwa Yudase adali nalo thumba, kuti Yesu adanena kwa iye, Gula [zinthu izo] zimene ife zitisowa pokonzekera phwandolo; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.
  3517. Jhn 13:30 Iye tsono atalandira nthongo adatuluka kunja mosakhalitsa: ndipo udali usiku.
  3518. Jhn 13:31 ¶Choncho, pamene iye adatuluka kunja, Yesu adanena, Tsopano Mwana wamwamuna wa munthu walemekezedwa, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa iye;
  3519. Jhn 13:32 Ngati Mulungu alemekezedwa mwa iye, Mulungu adzamlemekeza iye mwa iye mwini, ndipo pomwepo adzamlemekeza iye.
  3520. Jhn 13:33 Tiana, tsono kwa kanthawi pang’ono ndikhala ndi inu. Inu mudzandifunafuna ine: ndipo monga ndidanena kwa Ayuda, Kumene ndinkako ine, inu simungathe kudza; motero tsopano ndinena kwa inu.
  3521. Jhn 13:34 Lamulo latsopano ine ndikupatsani inu, Kuti inu mukondane wina ndi mnzake; monga ine ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.
  3522. Jhn 13:35 Mwa ichi [anthu] onse adzadziwa kuti inu muli wophunzira anga, ngati muli ndi chikondi wina ndi mnzake.
  3523. Jhn 13:36 ¶Simoni Petro adanena kwa iye, Ambuye, inu mupita kuti? Yesu adayankha iye, Kumene ine ndipita, iwe sungathe kunditsata ine tsopano; koma iwe udzanditsata ine pambuyo pake.
  3524. Jhn 13:37 Petro adanena kwa iye, Ambuye, kodi ine sindingathe kukutsatani inu tsopano chifukwa ninji? Ine ndidzataya moyo wanga chifukwa cha inu.
  3525. Jhn 13:38 Yesu adayankha iye, Kodi iwe udzataya moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi, ndithudi, ndinena kwa iwe, Tambala sadzalira, kufikira iwe utandikana ine katatu.
  3526. Jhn 14:1 Mtima wanu usakhale wovutika: inu mukhulupirira mwa Mulungu, khulupiriraninso mwa ine.
  3527. Jhn 14:2 M’nyumba ya Atate wanga muli zipinda zokhalamo zambiri: ngati [sikudali kotero], ine ndikadakuwuzani inu. Ine ndipita kuti ndikakonze malo a inu.
  3528. Jhn 14:3 Ndipo ngati ndipita kukakonza malo a inu, ine ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, [kumeneko] inu mukakhoze kukhalanso.
  3529. Jhn 14:4 Ndipo kumene ine ndipita inu mudziwa, ndipo njira yake inu muyidziwa.
  3530. Jhn 14:5 Tomasi adanena kwa iye, Ambuye, ife sitidziwa kumene mukupita; ndipo ife tiyidziwa njira bwanji?
  3531. Jhn 14:6 Yesu adanena kwa iye, Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo: palibe munthu abwera kwa Atate, koma mwa ine.
  3532. Jhn 14:7 Ngati inu mukadandidziwa ine, mukadadziwanso Atate wanga; ndipo kuyambira tsopano mumdziwa iye, ndipo inu mwamuwona iye.
  3533. Jhn 14:8 Filipi adanena kwa iye, Ambuye, tiwonetseni ife Atate, ndipo chitikwanira ife.
  3534. Jhn 14:9 Yesu adanena kwa iye, Kodi ine ndakhala ndi inu nthawi yayikulu yotere, ndipo tsono inu simudandidziwa ine, Filipi? Iye amene wandiwona ine wawona Atate; ndipo iwe unena bwanji [tsono], Mutiwonetse ife Atate?
  3535. Jhn 14:10 Sukhulupirira iwe kodi kuti ine ndiri mwa Atate, ndi Atate mwa ine? Mawu amene ndinena ine kwa inu sindiyankhula za ine ndekha: koma Atate amene akhala mwa ine, iye achita ntchito.
  3536. Jhn 14:11 Khulupirirani ine, kuti ine [ndiri] mwa Atate, ndi Atate mwa ine: kapena china, kapena khulupirirani ine chifukwa cha ntchito zomwezi.
  3537. Jhn 14:12 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Iye amene akhulupirira pa ine, ntchito zimene ine ndichita iyeyu adzazichitanso; ndipo [ntchito] zazikulu zoposa izi iye adzachitanso; chifukwa ine ndipita kwa Atate wanga.
  3538. Jhn 14:13 Ndipo kalikonse inu mudzafunsa m’dzina langa, chimenecho ine ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana wamwamuna.
  3539. Jhn 14:14 Ngati mudzapempha kalikonse m’dzina langa, ine ndidzachita [ichi].
  3540. Jhn 14:15 ¶Ngati inu mukonda ine, sungani malamulo anga.
  3541. Jhn 14:16 Ndipo ine ndidzapempha Atate, ndipo iye adzakupatsani inu Mtonthozi wina, kuti iye akhoze kukhala ndi inu nthawi yonse;
  3542. Jhn 14:17 [Ndiye] Mzimu wa chowonadi: amene dziko lapansi silingathe kumlandira, chifukwa silimuwona iye, kapena kumdziwa iye: koma inu mumdziwa iye; pakuti akhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
  3543. Jhn 14:18 Sindidzakusiyani inu mukhale amasiye: ine ndidzabwera kwa inu.
  3544. Jhn 14:19 Tsono kwa kanthawi kochepa, ndipo dziko lapansi silindiwonanso ine; koma inu mundiwona ine: chifukwa ine ndiri moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.
  3545. Jhn 14:20 Tsiku limenero inu mudzadziwa kuti ine [ndiri] mwa Atate wanga, ndi inu mwa ine, ndi ine mwa inu.
  3546. Jhn 14:21 Iye amene ali nawo malamulo anga, ndipo awasunga, iyeyu ndiye amene andikonda ine: ndipo iye amene andikonda ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo ine ndidzamkonda, ndi kudziwonetsa ndekha kwa iye.
  3547. Jhn 14:22 Yudase anati kwa iye, osati Isikariyote, Ambuye, zitheka bwanji kuti inu mudziwonetsa nokha kwa ife, ndipo osati kwa dziko lapansi?
  3548. Jhn 14:23 Yesu adayankha ndipo anati kwa iye, Ngati munthu akonda ine, iye adzasunga mawu anga: ndipo Atate wanga adzamkonda iye, ndipo tidzabwera kwa iye, ndipo tidzapanga mokhala mwathu ndi iye.
  3549. Jhn 14:24 Iye amene sakonda ine sasunga zonena zanga: ndipo mawu amene inu mumva sali mawu anga, koma a Atate amene anandituma ine.
  3550. Jhn 14:25 Zinthu izi ine ndalankhula kwa inu, pakukhala [tsono] ndi inu.
  3551. Jhn 14:26 Koma Nkhosweyo, [amene ali] Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, iyeyo adzaphunzitsa inu zinthu zonse, ndipo adzakumbutsa inu zinthu zonse, zirizonse zimene ine ndanena kwa inu.
  3552. Jhn 14:27 Mtendere ine ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani inu: osati monga dziko lapansi lipatsa, ndipatsa ine kwa inu. Musalole kuti mtima wanu uvutike, kapena kulola kuti uchite mantha.
  3553. Jhn 14:28 Inu mwamva momwe ine ndidanenera kwa inu, ine ndichoka, ndipo ndibweranso kwa inu. Ngati inu mukadakonda ine, inu mukadakondwera, chifukwa ndinanena, ine ndipita kwa Atate: pakuti Atate ali wamkulu koposa ine.
  3554. Jhn 14:29 Ndipo tsopano ine ndakuwuzani chisadachitike, kuti, pamene chikhala chitachitika, inu mukhoze kukhulupirira.
  3555. Jhn 14:30 Kuyambira tsopano ine sindidzayankhulanso zambiri ndi inu: pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kalikonse mwa ine;
  3556. Jhn 14:31 Koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate wanga; ndipo monga Atate adandipatsa ine lamulo, chotero ine ndichita. Imirirani, tiyeni ife tinyamukepo pano.
  3557. Jhn 15:1 Ine ndine mpesa wowonadi, ndipo Atate wanga ndiye mlimi.
  3558. Jhn 15:2 Nthambi iliyonse mwa ine imene siyibala chipatso iye ayichotsa: ndi [nthambi] iliyonse imene ibala chipatso iye ayisadza, kuti ikhoze kubweretsa chipatso chochuluka.
  3559. Jhn 15:3 Tsopano inu mwayeretsedwa kudzera m’mawu amene ine ndayankhula kwa inu.
  3560. Jhn 15:4 Khalani mwa ine, ndi ine mwa inu. Monga nthambi siyingathe kubala chipatso pa iyo yokha, pokhapokha ikhale mwa mphesa; koposera simungachite inu, pokhapokha inu mukhale mwa ine.
  3561. Jhn 15:5 Ine ndine mphesa, inu [ndinu] nthambi: Iye amene akhala mwa ine, ndi ine mwa iye, yemweyo abweretsa chipatso chambiri: pakuti kopanda ine simungathe kuchita kanthu kalikonse.
  3562. Jhn 15:6 Ngati munthu sakhala mwa ine, iye watayika monga nthambi, ndipo wafota; ndipo anthu azisonkhanitsa izo, ndipo azitaya [izo] m’moto, ndipo zitenthedwa.
  3563. Jhn 15:7 Ngati mukhala mwa ine, ndipo mawu anga akhala mwa inu, inu mudzapempha chimene inu muchifuna, ndipo chidzachitidwa kwa inu.
  3564. Jhn 15:8 Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti inu mubale chipatso chambiri; kotero inu mudzakhala wophunzira anga.
  3565. Jhn 15:9 Monga Atate wandikonda ine, kotero ine ndakonda inu: khalanibe inu m’chikondi changa.
  3566. Jhn 15:10 Ngati musunga malamulo anga, mudzakhala m’chikondi changa; monga ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake.
  3567. Jhn 15:11 Zinthu izi ndalankhula kwa inu, kuti chimwemwe changa chikhalebe mwa inu, ndi [kuti] chimwemwe chanu chikhoze kukhala chodzadza.
  3568. Jhn 15:12 Ili ndi lamulo langa, Kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ine ndakonda inu.
  3569. Jhn 15:13 Chikondi chachikulu choposa ichi palibe munthu ali nacho, kuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
  3570. Jhn 15:14 Inu muli abwenzi anga, ngati muzichita zirizonse zimene ine ndakulamulirani inu.
  3571. Jhn 15:15 Kuyambira tsopano sinditcha inu antchito; pakuti wantchito sadziwa chimene mbuye wake achita: koma ine ndatcha inu abwenzi; chifukwa zinthu zonse zimene ine ndazimva kwa Atate wanga ine ndakudziwitsani inu.
  3572. Jhn 15:16 Inu simudandisankha ine, koma ine ndidakusankhani inu, ndipo ndidakuyikani inu, kuti inu mupite ndikubweretsa chipatso, ndi [kuti] chipatso chanu chikhale: kuti chilichonse chimene mukapempha Atate m’dzina langa, akhoze iye kukupatsani inu.
  3573. Jhn 15:17 Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzake.
  3574. Jhn 15:18 Ngati dziko lapansi lida inu, inu mudziwa kuti linada ine lisanadane ndi inu.
  3575. Jhn 15:19 Ngati inu mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda za ilo lokha: koma chifukwa inu simuli a dziko lapansi, koma ine ndidakusankhani inu kuchokera m’dziko lapansi, choncho dziko lapansi likudani inu.
  3576. Jhn 15:20 Kumbukirani mawu amene ine ndidanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati iwo adandisawutsa ine, iwo adzakusawutsani inunso; ngati iwo adasunga zonena zanga, adzasunga zanunso.
  3577. Jhn 15:21 Koma zinthu izi zonse iwo adzakuchitirani inu chifukwa cha dzina langa; chifukwa sadziwa iye amene anandituma ine.
  3578. Jhn 15:22 Ngati ine sindikadadza ndi kulankhula kwa iwo, iwo sakadakhala wokhala nalo tchimo: koma tsopano alibe chobisira cha tchimo lawo.
  3579. Jhn 15:23 Iye amene andida ine adanso Atate wanga.
  3580. Jhn 15:24 Ngati ine sindikadachita pakati pa iwo ntchito zimene palibe munthu wina adazichita, iwo sakadakhala wokhala nalo tchimo: koma tsopano iwo onse awona ndipo adandida ine ndi Atate wanga.
  3581. Jhn 15:25 Koma [ichi chidzachitika], kuti mawu akhoze kukwaniritsidwa amene ali wolembedwa m’chilamulo chawo, Adandida ine kopanda chifukwa.
  3582. Jhn 15:26 Koma pamene Nkhosweyo wafika, amene ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, [ndiye] Mzimu wa chowonadi, amene atuluka kuchokera kwa Atate, iyeyu adzachitira umboni za ine.
  3583. Jhn 15:27 Ndipo inunso mudzachitira umboni, chifukwa inu mudali ndi ine kuyambira pachiyambi.
  3584. Jhn 16:1 Zinthu izi ndayankhula kwa inu, kuti inu musakhumudwitsidwe.
  3585. Jhn 16:2 Iwo adzakutulutsani m’masunagoge: inde, nthawi ikudza, imene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti iye achitira Mulungu utumiki.
  3586. Jhn 16:3 Ndipo zinthu izi iwo adzachita kwa inu, chifukwa iwo sadadziwe Atate, kapena ine.
  3587. Jhn 16:4 Koma zinthu izi ine ndakuwuzani inu, kuti pamene nthawiyo idza, inu mukhoze kukumbukira kuti ine ndidakuwuzani za izo. Ndipo zinthu izi ine sindidanena kwa inu pa chiyambi, chifukwa ine ndidali pamodzi ndi inu.
  3588. Jhn 16:5 Koma tsopano ndipita kwa iye amene anandituma ine; ndipo palibe wa inu andifunsa ine, Mupita kuti inu?
  3589. Jhn 16:6 Koma chifukwa ndanena zinthu izi kwa inu, chisoni chadzadza mtima wanu.
  3590. Jhn 16:7 Ngakhale ziri motero ine ndikuwuzani inu chowonadi; Kuti kuli phindu kwa inu kuti ine ndichoke: pakuti ngati ine sindichoka, Mtonthoziyo sadzabwera kwa inu; koma ngati ine ndinyamuka, ine ndidzamtuma iye kwa inu.
  3591. Jhn 16:8 Ndipo akadza iyeyo, iye adzatsutsa dziko lapansi za tchimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro:
  3592. Jhn 16:9 Za machimo, chifukwa iwo sakhulupirira pa ine ayi;
  3593. Jhn 16:10 Za chilungamo, chifukwa ine ndipita kwa Atate wanga, ndipo inu simudzandiwonanso ine;
  3594. Jhn 16:11 Za chiweruzo, chifukwa kalonga wa dziko lino lapansi waweruzidwa.
  3595. Jhn 16:12 Ine ndiri nazo tsono zambiri kuti ndinene kwa inu, koma inu simungathe kuzimvetsa izo tsopano [lino].
  3596. Jhn 16:13 Komabe akabwera iyeyu, Mzimu wa chowonadi, akadza, iye adzakutsogolerani inu m’chowonadi chonse: pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma kalikonse iye adzamva; [chimenecho] iye adzachilankhula: ndipo iye adzakuwonetserani zinthu zirinkudza.
  3597. Jhn 16:14 Iyeyu adzalemekeza ine: chifukwa adzalandira za kwa ine, ndipo adzawonetsera [izo] kwa inu.
  3598. Jhn 16:15 Zinthu zonse zimene Atate ali nazo ndi zanga: choncho ine ndidati, kuti iye adzatenga za kwa ine, ndipo adzaziwonetsera [izo] kwa inu.
  3599. Jhn 16:16 Kwa kanthawi kochepa, ndipo inu simundiwonanso ine: ndipo kenanso, kwa kanthawi, ndipo inu mudzandiwona ine, chifukwa ine ndipita kwa Atate.
  3600. Jhn 16:17 Kenaka adanena [ena] a wophunzira ake pakati pa iwo wokha. Kodi ichi ndi chiyani chimene iye anena kwa ife, Kwa kanthawi kochepa inu simundiwona ine: ndipo kenanso, kwa kanthawi kochepa, inu mudzandiwona ine: ndi, Chifukwa ine ndipita kwa Atate?
  3601. Jhn 16:18 Choncho iwo adanena, Kodi ichi ndi chiyani chimene iye anena, Kanthawi? Ife sitinganene chimene iye ayankhula.
  3602. Jhn 16:19 Tsopano Yesu adadziwa kuti iwo adalikufuna kumfunsa iye, ndipo adati kwa iwo, Kodi muli kufunsana pakati panu za kuti ine ndanena, Kwa kanthawi kochepa, ndipo inu simundiwona ine: ndipo kenanso, kwa kanthawi kochepa inu mudzandiwona ine?
  3603. Jhn 16:20 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Kuti inu mudzalira ndi kubuma, koma dziko lapansi lidzakondwera: ndipo inu mudzachita chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.
  3604. Jhn 16:21 Mkazi pamene ali mu zowawa ali ndi chisoni, chifukwa ora lake lafika: koma pamene iye wangobala mwana, sakumbukiranso chisawutsocho, chifukwa cha chimwemwe kuti munthu wabadwa ku dziko lapansi.
  3605. Jhn 16:22 Choncho inu tsopano muli nacho chisoni: koma ine ndidzakuwonaninso inu, ndipo mtima wanu, udzakondwera, ndipo chimwemwe chanu palibe munthu adzachotsa kwa inu.
  3606. Jhn 16:23 Ndipo m’tsiku limenero inu simudzandifunsa ine kanthu, Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa inu, Chilichonse chimene inu mudzapempha Atate m’dzina langa adzakupatsani inu [icho].
  3607. Jhn 16:24 Kufikira tsopano inu simudapempha kanthu m’dzina langa: pemphani, ndipo inu mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chodzadza.
  3608. Jhn 16:25 Zinthu izi ndiyankhula kwa inu m’miyambi: koma ikudza nthawi, imene ine sindidzalankhula kwa inu m’miyambi, koma ine ndidzakuwonetsani inu momveka bwino za Atate.
  3609. Jhn 16:26 Pa tsiku limenero inu mudzapempha m’dzina langa: ndipo ine sindinena kwa inu, kuti ine ndidzapemphera kwa Atate chifukwa cha inu.
  3610. Jhn 16:27 Pakuti Atate mwini yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda ine, ndipo mwakukhulupirira kuti ine ndidatuluka kuchokera kwa Mulungu.
  3611. Jhn 16:28 Ine ndidatuluka kuchokera kwa Atate, ndipo ine ndabwera m’dziko lapansi: kenanso, ine ndilisiya dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.
  3612. Jhn 16:29 Wophunzira ake adanena kwa iye, Onani, tsopano inu muyankhula momveka bwino, ndipo simulankhula miyambi.
  3613. Jhn 16:30 Tsopano ife tatsimikizika kuti inu mudziwa zinthu zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina afunse inu: mwa ichi ife tikhulupirira kuti mudatuluka kuchokera kwa Mulungu.
  3614. Jhn 16:31 Yesu adayankha iwo, Kodi tsopano inu mukhulupirira?
  3615. Jhn 16:32 Tawonani, ora likudza, inde, tsopano lafika, kuti inu mubalalitsidwe, munthu aliyense kuzake za iye yekha, ndipo ine mudzandisiya ndekha: ndipo tsono sindiri ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi ine.
  3616. Jhn 16:33 Zinthu izi ndayankhula kwa inu, kuti mwa ine mukhoze kukhala nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chisawutso: koma khalani wokondwera; ine ndalilaka dziko lapansi.
  3617. Jhn 17:1 Mawu awa adayankhula Yesu; ndipo adakweza maso ake kumwamba, ndipo adati, Atate, ora lafika; lemekezani Mwana wanu wamwamuna, kuti Mwana wanu wamwamuna akalemekeze inu:
  3618. Jhn 17:2 Monga mwampatsa iye ulamuliro pa thupi lirilonse, kuti apereke kwa iwo moyo wosatha kwa ambiri a iwo monga inu mwampatsa iye.
  3619. Jhn 17:3 Ndipo uwu ndi moyo wosatha, kuti akhoze kudziwa inu Mulungu yekha wowona, ndi Yesu Khristu, amene inu mwamtuma.
  3620. Jhn 17:4 Ine ndalemekeza inu pa dziko lapansi: Ine ndatsiriza ntchito imene inu mudandipatsa ine kuti ndichite.
  3621. Jhn 17:5 Ndipo tsopano, Atate, inu lemekezani ine pamodzi ndi inu mwini ndi ulemerero umene ine ndidali nawo ndi inu lisadakhale dziko lapansi.
  3622. Jhn 17:6 Ine ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene inu mwandipatsa ine kuchoka m’dziko lapansi: iwo adali anu, ndipo inu mwandipatsa ine iwo; ndipo iwo asunga mawu anu.
  3623. Jhn 17:7 Tsopano iwo azindikira kuti zinthu zirizonse zimene inu mwandipatsa ine ziri za kwa inu.
  3624. Jhn 17:8 Pakuti ine ndapatsa kwa iwo mawu amene inu mudandipatsa ine; ndipo iwo adalandira [mawuwo], ndipo tsopano adziwa ndithu kuti ine ndidatuluka kuchokera kwa inu, ndipo iwo akhulupirira kuti inu mudandituma ine.
  3625. Jhn 17:9 Ine ndipempherera iwo: ine sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene inu mwandipatsa ine; pakuti iwo ali anu.
  3626. Jhn 17:10 Ndipo onse anga ali anu, ndi anu ali anga; ndipo ine ndilemekezedwa mwa iwo.
  3627. Jhn 17:11 Ndipo tsopano sindirinso m’dziko lapansi, koma awa ali mdziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa inu. Atate Woyera, sungani kudzera m’dzina lanu nokha amene inu mwandipatsa ine, kuti akhale m’modzi, monga ife [tiri].
  3628. Jhn 17:12 Pamene ine ndidakhala nawo m’dziko lapansi, ine ndidawasunga iwo m’dzina lanu: iwo amene inu mwandipatsa ine ndidawasunga, ndipo palibe m’modzi yense wa iwo watayika, koma mwana wamwamuna wa chitayiko; kuti lembo likhoze kukwaniritsidwa.
  3629. Jhn 17:13 Ndipo tsopano ine ndidza kwa inu; ndipo zinthu izi ine ndiyankhula m’dziko lapansi, kuti iwo akhoze kukhala nacho chimwemwe changa chokwaniritsidwa mwa iwo wokha.
  3630. Jhn 17:14 Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi lawada iwo, chifukwa sali a dziko lapansi, monga ine sindiri wa dziko lapansi.
  3631. Jhn 17:15 Ine sindipemphera kuti inu muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuwateteza ku choyipacho.
  3632. Jhn 17:16 Iwo sali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.
  3633. Jhn 17:17 Patulani iwo kudzera m’chowonadi chanu; mawu anu ndi chowonadi.
  3634. Jhn 17:18 Monga momwe inu mwandituma ine m’dziko lapansi, momwenso ine ndawatuma iwo m’dziko lapansi.
  3635. Jhn 17:19 Ndipo chifukwa cha iwo, ine ndidzipatula ndekha, kuti iwonso akhoze kukhala wopatulidwa kudzera m’chowonadi.
  3636. Jhn 17:20 Kapena sindipempherera awa wokha, koma iwonso amene adzakhulupirira pa ine kudzera m’mawu awo;
  3637. Jhn 17:21 Kuti onse akhoze kukhala amodzi; monga inu, Atate, [muli] mwa ine, ndi ine mwa inu, kuti iwonso akhoze kukhala amodzi mwa ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti inu mwandituma ine.
  3638. Jhn 17:22 Ndipo ulemerero umene inu mwandipatsa ine, ine ndawapatsa iwo; kuti iwo akhale amodzi, monga ife tiri amodzi:
  3639. Jhn 17:23 Ine mwa iwo, ndi inu mwa ine, kuti akhoze kukhala angwiro mwa m’modzi; kuti dziko lapansi lidziwe kuti inu mwandituma ine, ndipo mwawakonda iwo, monga momwe inu mudakonda ine,
  3640. Jhn 17:24 Atate, ine ndifuna kuti iwonso, amene mwandipatsa, akhale pamodzi ndi ine kumene ine ndiri, kuti akhoze kuwona ulemerero wanga, umene inu mwandipatsa ine: pakuti inu mudandikonda ine asadakhazikike maziko a dziko lapansi.
  3641. Jhn 17:25 Atate wolungama, dziko lapansi silidadziwa inu; koma ine ndadziwa inu; ndipo awa adziwa kuti inu mwandituma ine.
  3642. Jhn 17:26 Ndipo ine ndidazindikiritsa kwa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa [ilo]: kuti chikondi chimene inu mwakonda nacho ine chikhoze kukhala mwa iwo, ndi ine mwa iwo.
  3643. Jhn 18:1 Pamene Yesu adalankhula mawu awa, iye adatuluka ndi wophunzira ake kupita tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kudali munda, m’mene iye adalowamo ndi wophunzira ake.
  3644. Jhn 18:2 Ndi Yudasinso amene adampereka iye, adadziwa malowa: pakuti Yesu ankapitako kawirikawiri kukapuma ndi wophunzira ake.
  3645. Jhn 18:3 Kenaka Yudasi, atalandira gulu la [anthu] ndi asirikali ochokera kwa ansembe akulu ndi Afarisi, adafika komweko ndi nyali ndi miwuni ndi zida.
  3646. Jhn 18:4 Choncho Yesu, podziwa zinthu zonse zimene zinayenera kudza pa iye, adatuluka, ndipo anati kwa iwo, Mufuna yani inu?
  3647. Jhn 18:5 Iwo adamyankha iye, Yesu wa ku Nazarete, Yesu adanena kwa iwo, Ine ndine [iye]. Ndipo Yudasinso, amene adampereka iye, adayima nawo pamodzi.
  3648. Jhn 18:6 Nthawi yomweyo tsono pamene iye adangonena kwa iwo, Ine ndine [iye], iwo adabwerera m’mbuyo, ndipo anagwa pansi.
  3649. Jhn 18:7 Kenaka iye adawafunsanso iwo, Ndi yani amene mufuna? Ndipo iwo adati, Yesu wa ku Nazarete.
  3650. Jhn 18:8 Yesu adayankha, Ine ndakuwuzani kuti ndine [iye]: choncho ngati inu mufuna ine, lekani awa apite pa njira yawo;
  3651. Jhn 18:9 Kuti chonenedwa chikhoze kukwaniritsidwa, chimene iye adayankhula, A iwo amene inu mwandipatsa ine sindidataya ine wina aliyense.
  3652. Jhn 18:10 Kenaka Simoni Petro pokhala nalo lupanga, adalisolola ilo, ndipo anakantha wantchito wa mkulu wansembe, ndi kudula khutu lake lamanja. Dzina la wantchitoyo lidali Malikasi.
  3653. Jhn 18:11 Kenaka Yesu adati kwa Petro, Longa lupanga lako m’chimake: chikho chimene Atate wandipatsa ine, kodi ine sindimwa ichi?
  3654. Jhn 18:12 Kenaka gululo ndi kapitawo ndi asirikali a Ayuda adatenga Yesu, ndipo anam’manga iye.
  3655. Jhn 18:13 Ndipo anamtsogolera iye kupita naye kwa Anasi poyamba; pakuti adali mpongozi wa Kayafasi, amene adali mkulu wa ansembe chaka chomwecho.
  3656. Jhn 18:14 Tsopano Kayafasi anali iye, amene adapereka langizo kwa Ayuda, kuti kudali koyenera kuti munthu m’modzi ayenera kufera anthu.
  3657. Jhn 18:15 ¶Ndipo Simoni Petro adatsatira Yesu, ndipo [chotero adachitanso] wophunzira wina: koma wophunzira ameneyo adali wodziwika kwa mkulu wansembe, ndipo analowa pamodzi ndi Yesu kunyumba [yachifumu] ya mkulu wansembe.
  3658. Jhn 18:16 Koma Petro adayima pakhomo kunja, Kenaka wophunzira winayo adatuluka, amene adadziwika kwa mkulu wansembe, ndipo anayankhula kwa iye amene amayang’anira pakhomo, ndipo analowetsa Petro.
  3659. Jhn 18:17 Kenaka mtsikana amene amayang’anira pakhomoyo anati kwa Petro; Kodi iwe si uli [mmodzi] wa wophunzira a munthu uyu? Iye adanena, Sindine ayi.
  3660. Jhn 18:18 Ndipo antchito ndi asirikali adalikuyimirira pamenepo; amene adasonkha moto wamakala; pakuti kudali kukuzizira: ndipo iwo adalikuwotha moto: ndipo Petro adalikuyimirira pamodzi ndi iwo kuwotha moto.
  3661. Jhn 18:19 ¶Mkulu wansembe kenaka adafunsa Yesu za wophunzira ake, ndi za chiphunzitso chake.
  3662. Jhn 18:20 Yesu adayankha iye, Ine ndinayankhula mosabisa ku dziko lapansi; ine nthawi zonse ndidaphunzitsa m’sunagoge, ndi m’kachisi, kumene amasonkhana Ayuda; ndipo mobisika ine sindiyankhula kanthu.
  3663. Jhn 18:21 Undifunsiranji ine? Funsa iwo amene adamva ine, chimene ine ndidanena kwa iwo, tawonani, iwo adziwa chimene ine ndidanena.
  3664. Jhn 18:22 Ndipo m’mene iye adalankhula motero, m’modzi wa asirikali amene adalikuyimirirapo adapanda Yesu khofi ndi chikhato cha dzanja lake, kunena kuti, Kodi uyankha mkulu wansembe chomwecho?
  3665. Jhn 18:23 Yesu adayankha iye, Ngati ine ndayankhula choyipa; pereka umboni wa choyipacho: koma ngati chabwino, iwe undipandiranji ine?
  3666. Jhn 18:24 Tsopano Anasi adamtumiza iye womangidwa kwa Kayafasi mkulu wansembe.
  3667. Jhn 18:25 Ndipo Simoni Petro adalikuyimirira ndi kuwotha moto. Choncho iwo adati kwa iye, Si uli iwenso kodi [m’modzi] wa wophunzira ake? Iyeyu adakana [ichi], ndipo anati, Sindiri ayi.
  3668. Jhn 18:26 M’modzi wa antchito a mkulu wansembe wokhala mbale [wake] wa amene khutu lake Petro adamdula, anena, Kodi ine sindidakuwona iwe kodi m’munda pamodzi ndi iye?
  3669. Jhn 18:27 Kenaka Petro adakananso: ndipo posakhalitsa tambala adalira.
  3670. Jhn 18:28 ¶Kenaka iwo adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafasi kupita ku nyumba yoweruzira milandu: ndipo kudali mamawa; ndipo iwo wokha sadalowa ku nyumba yoweruzira milandu, kuti mwina angadetsedwe; koma kuti akhoze kudya paskha.
  3671. Jhn 18:29 Kenaka Pilato adatuluka kunja kupita kwa iwo, ndipo anati, Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?
  3672. Jhn 18:30 Iwo adayankha nati kwa iye, Akadakhala kuti si wochita zoyipa, ife sitikadampereka iye kwa inu.
  3673. Jhn 18:31 Kenaka Pilato adati kwa iwo, Mutengeni inu iye, ndipo mumuweruze iye monga mwa chilamulo chanu. Choncho Ayuda adati kwa iye, Sikuli kololedwa mwa lamulo kwa ife kupha munthu aliyense:
  3674. Jhn 18:32 Kuti chonena cha Yesu chikhoze kukwaniritsidwa, chimene iye adalankhula, kuzindikiritsa za imfa imene ayenera kufa.
  3675. Jhn 18:33 Kenaka Pilato adalowanso m’nyumba yoweruzira milandu, ndipo anayitana Yesu, ndipo anati kwa iye, Iwe kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?
  3676. Jhn 18:34 Yesu adayankha iye, Munena inu ichi mwa inu nokha kapena ena adakuwuzani [ichi] inu za ine?
  3677. Jhn 18:35 Pilato adayankha, Kodi ndiri Myuda? Fuko lako lomwe ndi ansembe akulu adakupereka iwe kwa ine: wachita chiyani iwe?
  3678. Jhn 18:36 Yesu adayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lapansili: ufumu wanga ukadakhala wa dziko lapansili, pamenepo atumiki anga akadamenya nkhondo, kuti ine ndisaperekedwe kwa Ayuda: koma tsopano ufumu wanga si uli wochokera kuno.
  3679. Jhn 18:37 Choncho Pilato adati kwa iye, Kodi iwe ndiwe Mfumu tsono? Yesu adayankha, Inu munena kuti ine ndine Mfumu. Kudzachita ichi ine ndidabadwa, ndipo pa chifukwa ichi ine ndidadzera m’dziko lapansi, kuti ndikachite umboni kwa chowonadi. Aliyense amene ali wa chowonadi amva liwu langa.
  3680. Jhn 18:38 Pilato adanena kwa iye, Chowonadi ndi chiyani? Ndipo pamene adanena ichi, adatulukiranso kupita kwa Ayudawo, ndipo ananena kwa iwo, ine sindikupeza mwa iye chifukwa [chilichonse].
  3681. Jhn 18:39 Koma muli nawo mwambo, kuti ine ndiyenera kumamasulira kwa inu m’modzi pa paskha: choncho mufuna tsono kuti ine ndimasulire kwa inu Mfumu ya Ayuda?
  3682. Jhn 18:40 Kenaka adafuwulanso iwo onse, kunena kuti, Osati munthu uyu ayi, koma Barabasi. Tsopano Barabasi adali wolanda.
  3683. Jhn 19:1 Choncho kenaka Pilato adatenga Yesu, ndipo anamkwapula [iye].
  3684. Jhn 19:2 Ndipo asirikali adaluka chisoti chaminga, naveka [icho] pamutu pake, ndipo anamveka iye mwinjiro wa [mtundu] wofiyirira.
  3685. Jhn 19:3 Ndipo anati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda! Ndipo adampanda iye ndi manja awo.
  3686. Jhn 19:4 Choncho Pilato adatulukanso kunja, ndipo ananena kwa iwo, Tawonani, ine ndidza naye kwa inu kunja, kuti inu mudziwe kuti sindipeza chifukwa chilichonse mwa iye.
  3687. Jhn 19:5 Kenaka Yesu adatuluka kunja, atavala chisoti cha minga, ndi mwinjiro wa [mtundu] wofiyirira. Ndipo [Pilato] adanena kwa iwo, Tawonani munthuyu!
  3688. Jhn 19:6 Choncho pamene ansembe akulu ndi asirikali adamuwona iye, iwo adafuwula, kunena kuti, Mpachikeni [iye], mpachikeni [iye]. Pilato adanena kwa iwo. Mtengeni inu iye, ndipo mumpachike [iye], pakuti ine sindikupeza chifukwa mwa iye.
  3689. Jhn 19:7 Ayuda adayankha iye, Ife tiri nacho chilamulo, ndipo monga mwa chilamulo chathu ayenera kufa, chifukwa adadziyesera yekha Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  3690. Jhn 19:8 ¶Choncho pamene Pilato adamva mawu awa, adachita mantha koposa;
  3691. Jhn 19:9 Ndipo adalowanso ku nyumba yoweruzira milandu, ndipo ananena kwa Yesu, Muchoka kuti inu? Koma Yesu sadamyankha kanthu.
  3692. Jhn 19:10 Kenaka Pilato adanena kwa iye, Simulankhula kwa ine kodi? Simudziwa kodi kuti ine ndiri ndi ulamuliro wakukupachikani, ndipo ndiri nawo ulamuliro wakukumasulani?
  3693. Jhn 19:11 Yesu adayankha, Inu simukadakhala nawo ulamuliro [uliwonse] wonditsutsa ine, pokhapokha ngati ukadapatsidwa kwa inu kuchokera kumwamba: choncho iye amene anandipereka ine kwa inu ali nalo tchimo lalikulu.
  3694. Jhn 19:12 Ndipo kuchokera pa nthawi iyi Pilato adafuna kum’masula iye: koma Ayuda adafuwula, kunena kuti, Ngati inu mumasula munthu ameneyu, inu simuli bwenzi la Kayisara: wina aliyense amene adzipanga yekha mfumu alankhula motsutsana ndi Kayisara.
  3695. Jhn 19:13 ¶Choncho pamene Pilato adamva chonena chimenecho, iye adatuluka ndi Yesu, ndipo anakhala pansi pa mpando woweruzira m’malo amene amatchedwa Baelo la miyala, koma m’Chihebri, Gabata.
  3696. Jhn 19:14 Ndipo lidali tsiku lokonzekera paskha; pafupifupi ora la chisanu ndi chimodzi: ndipo adanena kwa Ayuda, Tawonani mfumu yanu!
  3697. Jhn 19:15 Koma iwo adafuwula, Chotsani [iye], chotsani [iye], mpachikeni iye! Pilato adanena kwa iwo, Kodi ndidzapachika Mfumu yanu? Ansembe akulu adayankha, Ife tiribe mfumu koma Kayisara.
  3698. Jhn 19:16 Choncho kenaka adampereka iye kwa iwo kuti apachikidwe. Ndipo iwo adamtenga Yesu, ndipo iwo anamutsogolera [iye] m’njira kuchoka naye.
  3699. Jhn 19:17 Ndipo iye atasenza mtanda wake anatuluka kupita [ku malo] wotchedwa malo a bade, amene atchedwa m’Chihebri Gologota:
  3700. Jhn 19:18 Kumene iwo adampachika iye, ndi awiri ena pamodzi ndi iye, ku mbali iliyonse m’modzi, ndi Yesu pakati.
  3701. Jhn 19:19 ¶Ndipo Pilato adalemba mawu, nawayika [iwo] pa mtanda. Ndipo cholemba chidali, YESU WA KU NAZARETE MFUMU YA AYUDA.
  3702. Jhn 19:20 Ndipo chilembo icho adachiwerenga ambiri a Ayuda: pakuti malo amene Yesu adapachikidwapo adali pafupi pa mzindawo: ndipo chidalembedwa m’Chihebri, [ndi] m’Chigriki, [ndi] m’Chilatini.
  3703. Jhn 19:21 Kenaka adanena ansembe akulu a Ayuda kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti iyeyu adati, Ine ndine Mfumu ya Ayuda.
  3704. Jhn 19:22 Pilato adayankha, Chimene ine ndalemba, ndalemba.
  3705. Jhn 19:23 ¶Kenaka asirikaliwo, pamene anampachika Yesu, adatenga zovala zake, ndipo anazigawa panayi, kwa msirikali aliyense gawo; ndiponso ndi chovala pamwamba [chake]: koma chovala pamwamba chidalibe msoko, chowombedwa monsemo kuyambira pamwamba.
  3706. Jhn 19:24 Choncho iwo adati pakati pawo, Tisang’ambe awa, koma tiwachitire mayere awa, kuti akhale a yani: kuti lemba likhoze kukwaniritsidwa, limene linena, Iwo adagawana zovala zanga pakati pawo, ndi chifukwa cha malaya anga adachita mayere. Choncho zinthu izi asirikali adachita.
  3707. Jhn 19:25 ¶Tsopano padayimirirapo pa mtanda wa Yesu amayi wake ndi mbale wa amayi wake, Mariya [mkazi] wa Kleyopasi, ndi Mariya Mmagidalene.
  3708. Jhn 19:26 Choncho pamene Yesu adawona amayi wake ndi wophunzira amene adamkonda alikuyimirapo, iye adanena kwa amayi wake, Mkazi, tawonani mwana wanu wamwamuna!
  3709. Jhn 19:27 Kenaka iye adanena kwa wophunzirayo, Tawona amayi wako! Ndipo kuyambira ora lomweri wophunzira ameneyo adawatenga kupita nawo kunyumba [kwake].
  3710. Jhn 19:28 ¶Chitapita ichi, Yesu podziwa kuti zonse tsopano zidatha, kuti lemba likhoze kukwaniritsidwa, anena, Ine ndimva ludzu.
  3711. Jhn 19:29 Tsopano padayikidwa chotengera chodzala ndi viniga: ndipo iwo adadzadza chinkhupule ndi viniga, ndipo anayika pa hisope, ndipo anachiyika [icho] kukamwa kwake.
  3712. Jhn 19:30 Choncho pamene Yesu adalandira viniga, iye adati, Kwatha: ndipo iye adaweramitsa mutu wake, ndipo anamwalira.
  3713. Jhn 19:31 Choncho Ayuda, chifukwa padali pa chikonzekero, kuti mitembo isatsale pa mtanda pa tsiku lasabata, (pakuti tsiku la sabata limenero lidali la pamwamba,) adapempha Pilato kuti miyendo yawo ikhoze kuthyoledwa, ndipo [kuti] iwo akhoze kuchotsedwa.
  3714. Jhn 19:32 Kenaka adabwera asirikali, ndipo anathyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo amene adapachikidwa pamodzi ndi iye:
  3715. Jhn 19:33 Koma pamene anafika kwa Yesu, ndi kuwona kuti iye, kuti adali atafa kale, iwo sadathyole miyendo yake:
  3716. Jhn 19:34 Koma m’modzi wa asirikali ndi nthungo adamgwaza m’nthiti mwake, ndipo mudatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.
  3717. Jhn 19:35 Ndipo iye amene adawona [izi] achita umboni, ndi umboni wake uli wowona: ndipo iyeyu adziwa kuti iye anena zowona: kuti inu mukhoze kukhulupirira.
  3718. Jhn 19:36 Pakuti zinthu izi zidachitika kuti lemba likwaniritsidwe, Fupa la iye silidzathyoledwa.
  3719. Jhn 19:37 Ndipo lemba lina linenanso. Iwo adzayang’ana pa iye amene adamgwaza.
  3720. Jhn 19:38 ¶Ndipo chitatha ichi Yosefe wa ku Arimateya, pokhala wophunzira wa Yesu, koma mobisika chifukwa cha kuwopa Ayuda, adapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu: ndipo Pilato adalola [iye]. Choncho iye adadza ndipo anatenga mtembo wa Yesu.
  3721. Jhn 19:39 Ndipo adadzanso Nikodemasi, amene poyamba adabwera kwa Yesu usiku, ndipo adabweretsa chisanganizo cha mule ndi aloye, [zolemera] pafupifupi miyeso zana.
  3722. Jhn 19:40 Kenaka adatenga mtembo wa Yesu, ndipo anawukulunga iwo mu nsalu za bafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa mwambo wa a Ayuda wa mayikidwe a maliro.
  3723. Jhn 19:41 Tsopano pamene iye adapachikidwapo padali munda; ndi m’mundamo manda a tsopano, m’mene munthu aliyense sadayikidwamo ndi kale lonse.
  3724. Jhn 19:42 Choncho m’menemo adayika Yesu chifukwa cha [tsiku] lokonzekera la Ayuda, pakuti mandawo adali pafupi.
  3725. Jhn 20:1 Tsiku loyamba la sabata adadza Mariya Mmagidalene m’mamawa, kukadali mdima, ku mandawo, ndipo apenya mwala utachotsedwa pamanda.
  3726. Jhn 20:2 Kenaka iye adathamanga, ndipo anadza kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu adamkonda, ndipo ananena kwa iwo, Amchotsa Ambuye m’manda, ndipo ife sitidziwa kumene adamuyika iye.
  3727. Jhn 20:3 Choncho Petro adapita, ndi wophunzira winayo, ndipo anafika kumanda.
  3728. Jhn 20:4 Kotero adathamanga onse awiri pamodzi: ndipo wophunzira winayo adathamanga naposa Petro, ndipo anayamba kufika kumandako.
  3729. Jhn 20:5 Ndipo iye m’mene adawerama pansi, [ndipo posuzumiramo], adawona nsalu zabafuta zitakhala, komatu iye sadalowamo ayi.
  3730. Jhn 20:6 Kenaka adadza Simoni Petro alinkutsata iye, ndipo analowa m’manda; ndipo adawona nsalu zabafuta zitakhala.
  3731. Jhn 20:7 Ndipo kansalu, kamene kadali mozungulira kumutu wake, kosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma kokulungika pamodzi pamalo pena pakokha.
  3732. Jhn 20:8 Kenaka tsono adalowanso wophunzira winayo, amene adayamba kufika kumanda, ndipo iye adawona, ndipo anakhulupirira.
  3733. Jhn 20:9 Pakuti kufikira pa nthawi imeneyi iwo sadadziwa malemba, kuti iye ayenera kuwuka kwa akufa.
  3734. Jhn 20:10 Kenaka wophunzirawo adachokanso, kupita kwawo.
  3735. Jhn 20:11 ¶Koma Mariya adayimirira kunja kwa manda alikulira: ndipo m’mene adalikulira, iye adawerama, ndipo [anayang’ana] m’manda,
  3736. Jhn 20:12 Ndipo adawona angelo awiri atavala zoyera atakhala, m’modzi kumutu, ndi wina kumiyendo, pamalo pamene mtembo wa Yesu udagona.
  3737. Jhn 20:13 Ndipo iwowa adanena kwa iye, Mkazi, ulira chiyani iwe? Iye adanena kwa iwo, Chifukwa adachotsa Ambuye wanga, ndipo ine sindidziwa kumene adamuyika iye.
  3738. Jhn 20:14 Ndipo m’mene iye adanena motero, iye adachewuka m’mbuyo, ndipo anawona Yesu ali chiliri, ndipo sadadziwa kuti anali Yesu.
  3739. Jhn 20:15 Yesu adanena kwa iye, Mkazi, ulira chiyani iwe? Ufuna yani iwe? Iyeyu, poyesa iye kuti ndi wosunga munda, anena kwa iye, Mbuye, ngati mwamunyamula iye kuno, ndiwuzeni ine kumene inu mwamuyika iye, ndipo ine ndidzakamtengako.
  3740. Jhn 20:16 Yesu adanena kwa iye, Mariya. Iyeyu adachewuka, ndipo adanena kwa iye Rabboni; kumene kuli kunena kuti, Mphunzitsi.
  3741. Jhn 20:17 Yesu adanena kwa iye, Usandikhudza ine ayi; pakuti ine sindinakwere kupita kwa Atate wanga: koma pita kwa abale anga, ndipo ukati kwa iwo, Ine ndikwera kupita kwa Atate wanga, ndi Atate wanu; ndi [kwa] Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.
  3742. Jhn 20:18 Mariya Mmagidalene adabwera ndipo anawuza wophunzirawo kuti iye adawona Ambuye; ndi [kuti] adalankhula zinthu izi kwa iye.
  3743. Jhn 20:19 ¶Kenaka tsiku lomwero pokhala madzulo, pokhala [tsiku] loyamba la sabata, pamene makomo adatsekedwa kumene wophunzira adasonkhana chifukwa cha kuwopa Ayuda, adadza Yesu ndipo anayimirira pakati pawo, ndipo ananena kwa iwo, Mtendere [ukhale] kwa inu.
  3744. Jhn 20:20 Ndipo pamene iye adanena motero, iye adawonetsa kwa iwo manja [ake] ndi m’nthiti mwake. Kenaka wophunzira adakondwera, pamene iwo adawona Ambuye.
  3745. Jhn 20:21 Kenaka Yesu adatinso kwa iwo, Mtendere [ukhale] kwa inu: monga Atate [wanga] wandituma ine, koteronso ine ndituma inu.
  3746. Jhn 20:22 Ndipo pamene iye adanena ichi, iye adawapumira pa [iwo], ndipo anena kwa iwo, Landirani inu Mzimu Woyera.
  3747. Jhn 20:23 Wina aliyense amene machimo ake inu mukhululukira, adzakhululukidwa kwa iwo; [ndipo] a wina aliyense amene [machimo] ake muwasunga, asungidwa.
  3748. Jhn 20:24 ¶Koma Tomasi, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimasi, sadali pamodzi ndi iwo pamene Yesu adadza.
  3749. Jhn 20:25 Choncho wophunzira ena adanena kwa iye, Tamuwona Ambuye. Koma iye adati kwa iwo, Pokhapokha ine ndidzawona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuyika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuyika dzanja langa m’nthiti mwake; ine sindidzakhulupirira ayi.
  3750. Jhn 20:26 ¶Ndipo patapita masiku asanu ndi atatu wophunzira ake adalinso m’kati, ndi Tomasi pamodzi nawo: [Kenaka] Yesu adadza, makomo ali otseka, ndipo anayimirira pakati, ndipo anati, Mtendere [ukhale] kwa inu.
  3751. Jhn 20:27 Kenaka iye adanena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, ndipo uwone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, ndipo uliyike [ilo] m’nthiti mwanga: ndipo usakhale wopanda chikhulupiriro, koma wokhulupirira.
  3752. Jhn 20:28 Ndipo Tomasi adayankha nati kwa iye, Ambuye wanga ndi Mulungu wanga.
  3753. Jhn 20:29 Yesu anena kwa iye, Tomasi, chifukwa iwe wawona ine, ndipo [tsono] wakhulupirira: wodala [ali] iwo amene sadawona, koma tsono adakhulupirira.
  3754. Jhn 20:30 ¶Ndipo zizindikiro zina zambiri ndithudi adachitadi Yesu pamaso pa wophunzira ake, zimene sizidalembedwa m’buku ili:
  3755. Jhn 20:31 Koma izi zidalembedwa, kuti inu mukhoze kukhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu, Mwana wamwamuna wa Mulungu; ndi kuti pakukhulupirira inu mukhale nawo moyo kupyolera m’dzina lake.
  3756. Jhn 21:1 Zitapita zinthu izi Yesu adadziwonetseranso iye yekha kwa wophunzira ake pa nyanja ya Tiberiyasi; ndipo motere adadziwonetsera [mwini yekha].
  3757. Jhn 21:2 Adali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimasi, ndi Nataniyeli wa ku Kana wa ku Galileya, ndi [ana amuna] a Zebedayo, ndi ena awiri a wophunzira ake.
  3758. Jhn 21:3 Simoni Petro adenena kwa iwo, ine ndinka kokasodza. Iwo anena kwa iye, Ifenso tipita pamodzi nawe, Iwo adatuluka, ndipo posakhalitsa analowa m’chombo; ndipo mu usiku umenewo iwo sadagwira kanthu.
  3759. Jhn 21:4 Koma pamene m’mawa tsopano unafika, Yesu adayimirira pambali pa nyanja: koma wophunzira sadadziwa kuti anali Yesu.
  3760. Jhn 21:5 Kenaka Yesu adanena kwa iwo, Ananu, kodi muli ndi chakudya chilichonse? Iwo adayankha iye, Ayi.
  3761. Jhn 21:6 Ndipo iye adati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja la chombo, ndipo inu mudzapeza. Choncho iwo adaponya, ndipo tsopano adalibenso kuthekera kwakulikoka ilo chifukwa cha kuchuluka nsomba.
  3762. Jhn 21:7 Choncho wophunzira amene Yesu adamkonda adanena kwa Petro, Ndi Ambuye. Tsopano pamene Simoni Petro adamva kuti adali Ambuye, iye adadziveka malaya [ake] osodzera, (pakuti adali wamaliseche,) ndipo anadziponya yekha m’nyanja.
  3763. Jhn 21:8 Ndipo wophunzira ena adabwera m’chombo chaching’ono; (pakuti sadali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri,) akukoka khoka lomwe linali ndi nsomba.
  3764. Jhn 21:9 Ndipo pamene iwo adali atangofika ku mtunda, iwo adapenya moto wa makala pomwepo, ndi nsomba zoyikidwapo, ndi mkate.
  3765. Jhn 21:10 Yesu adanena kwa iwo, Bweretsani nsomba za zimene inu mwazigwira tsopano.
  3766. Jhn 21:11 Simoni Petro adakwera [m’chombo] nakokera khoka ku mtunda lodzala ndi nsomba zazikulu, zana limodzi ndi makumi asanu ndi zitatu: ndipo mwa zonse panali zochuluka kwambiri; koma khoka silidang’ambika.
  3767. Jhn 21:12 Yesu adanena kwa iwo, Idzani [ndipo] mudye. Koma palibe m’modzi wa wophunzira adatha kumfunsa iye, Kodi ndinu yani? Podziwa kuti anali Ambuye.
  3768. Jhn 21:13 Yesu kenaka adadza, ndipo atenga mkate ndi kuwapatsa iwo, ndi nsomba chimodzimodzinso.
  3769. Jhn 21:14 Imeneyi ndi nthawi yachitatu imene Yesu adadziwonetsera iye yekha kwa wophunzira ake, m’mene adali atawuka kwa akufa.
  3770. Jhn 21:15 ¶Kotero pamene iwo atadya, Yesu adanena kwa Simoni Petro, Simoni [mwana wamwamuna] wa Yonasi, iwe undikonda ine kodi koposa awa? Iye adanena kwa iye, Inde, Ambuye; inu mudziwa kuti ine ndikukondani inu. Iye adanena kwa iye, Dyetsa ana a nkhosa anga.
  3771. Jhn 21:16 Iye adanena kwa iyenso kwachiwiri, Simoni, [mwana wamwamuna] wa Yonasi, iwe undikonda ine kodi? Iye adanena ndi iye, Inde, Ambuye; inu mudziwa kuti ine ndikukondani inu. Iye adanena kwa iye, Dyetsa nkhosa zanga.
  3772. Jhn 21:17 Iye adanena kwa iye kachitatu, Simoni, [mwana wamwamuna] wa Yonasi, iwe undikonda ine kodi? Petro adamva chisoni chifukwa iye adati kwa iye kachitatu, Iwe undikonda ine kodi? Ndipo iye adanena kwa iye, Ambuye, inu mudziwa zinthu zonse; inu mudziwa kuti ine ndikukondani inu. Yesu adanena kwa iye, Dyetsa nkhosa zanga.
  3773. Jhn 21:18 Ndithudi, ndithudi, ine ndinena kwa iwe, Pamene iwe udali wamng’ono, iwe udadzimangira wekha m’chiwuno [lamba], ndipo iwe udayenda kumene iwe udafuna: koma pamene udzakhala okalamba, iwe udzatambasula manja ako, ndipo wina adzakumanga iwe, ndipo adzakunyamula iwe kumene sudafuna.
  3774. Jhn 21:19 Ichi adalankhula iye, kuzindikiritsa mwa imfa imene iye adzayenera kulemekeza Mulungu. Ndipo m’mene iye adalankhula ichi, iye anena kwa iye, Nditsate ine.
  3775. Jhn 21:20 Kenaka Petro, pakutembenuka, adapenya wophunzira amene Yesu adamkonda alikutsatira; amenenso adamtsamira pachifuwa pake pa mgonero, ndipo anati, Ambuye, ndani iye amene apereka inu?
  3776. Jhn 21:21 Petro pakumuwona adanena kwa Yesu, Ambuye, ndipo ndi [chiyani] munthu uyu [adzachita]?
  3777. Jhn 21:22 Yesu anena kwa iye, Ngati ine ndifuna uyu akhale kufikira ndidza ine, [chili] chiyani kwa iwe? Iwe nditsate ine.
  3778. Jhn 21:23 Kenaka chonena ichi chidatuluka kufikira pakati pa abale, kuti wophunzira uyu asafe ayi: koma Yesu sadanena kwa iye, Iye sadzafa; koma, ngati ine ndifuna kuti iye akhale kufikira ndidza, [ichi chili] chiyani kwa iwe?
  3779. Jhn 21:24 Uyu ndiye wophunzira amene achita umboni za zinthu izi, ndipo adalemba zinthu izi: ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi wowona.
  3780. Jhn 21:25 Ndipo palinso zina zambiri zimene Yesu adazichita, zimene, ngati chilichonse chikadalembedwa, ine ndilingalira kuti dziko lapansi palokha silikadakhoza kukwanira kusunga mabuku amene akadakhala wolembedwa. Amen.
  3781. Act 1:1 Zolemba za m’mbuyomo ine ndidakulembera, Teofilasi, za zonse zomwe Yesu adayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,
  3782. Act 1:2 Kufikira m’tsiku limene iye adatengedwera m’mwamba, atatha iye mwa Mzimu Woyera kupereka maulamuliro kwa atumwi amene iye adawasankha:
  3783. Act 1:3 Kwa iwonso amene adadziwonetsera yekha wamoyo atatha masawutso ake ndi zitsimikizo zosalakwika zambiri, nawonekera kwa iwo masiku makumi anayi, ndi kunena za zinthu zolingana ndi ufumu wa Mulungu:
  3784. Act 1:4 Ndipo, posonkhana [nawo] pamodzi, adawalamulira kuti asachoke ku Yerusalemu, koma adikire lonjezano la Atate, limene, [anena iye], mudamva kwa ine.
  3785. Act 1:5 Pakuti Yohane zowonadi adabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera asadapite masiku ambiri.
  3786. Act 1:6 Choncho pamene iwo atasonkhana pamodzi, adafunsa za iye, kunena kuti, Ambuye, kodi inu pa nthawi ino mubwezeranso ufumu kwa Israyeli?
  3787. Act 1:7 Ndipo Iye adati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate adaziyika mu ulamuliro wake wa iye mwini.
  3788. Act 1:8 Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni kwa ine m’Yerusalemu ndi Yudeya yense, ndi m’Samariya, ndi ku malekezero a dziko lapansi.
  3789. Act 1:9 Ndipo m’mene adanena zinthu izi, ali chipenyerere iwo, iye adanyamulidwa; ndipo mtambo udamlandira iye kumchotsa pamaso pawo.
  3790. Act 1:10 Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba iye alinkupita kumwamba, tawonani, amuna awiri adayimirira pambali pawo wovala zoyera.
  3791. Act 1:11 Amenenso adati, Inu amuna a ku Galileya, muyimiriranji inu ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu yemweyu, amene wanyamulidwa kuchokera kwa inu kumka kumwamba, adzabwera motero momwemo monga mudamuwona ali nkupita kumwamba.
  3792. Act 1:12 Kenaka anabwerera iwo ku Yerusalemu kuchokera ku phiri lonenedwa Azitona, limene kuchokera ku Yerusalemu ndi ulendo woyenda kwa tsiku la Sabata.
  3793. Act 1:13 Ndipo pamene adalowa, adakwera ku chipinda cha pamwamba, kumene adali kukhalako Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Anduru, Filipi, ndi Tomasi, Batolomeyo, ndi Mateyu, Yakobo [mwana wamwamuna] wa Alifeyasi, ndi Simoni Zelotesi, ndi Yuda [mbale wake] wa Yakobo.
  3794. Act 1:14 Awa onse adali kupitirira ndi mtima umodzi m’kupemphera ndi kupembedzera, pamodzi ndi akazi, ndi Mariya amayi wake a Yesu, ndi abale ake.
  3795. Act 1:15 ¶Ndipo m’masiku awo adayimirira Petro pakati pa wophunzira, ndipo adati (chiwerengero cha mayina [onse] pamodzi chinali pafupifupi zana limodzi ndi makumi awiri,)
  3796. Act 1:16 Amuna [ndi] abale, lemba ili kudayenera kuti likwaniritsidwe, limene Mzimu Woyera kudzera mkamwa mwa Davide adanena kale zokhudza Yudasi, amane adali mtsogoleri wa iwo amene adagwira Yesu.
  3797. Act 1:17 Pakuti iye adali wowerengedwa pamodzi nafe, ndipo adalandira gawo la utumiki uwu.
  3798. Act 1:18 Tsopano munthu uyu adagula munda ndi mphotho ya zoyipa; ndipo pakugwa chamutu, anaphulika pakati, ndipo zam’mimba mwake zonse zidakhuthuka;
  3799. Act 1:19 Ndipo chidadziwika kwa onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti mundawo umatchedwa m’chinenedwe chawo choyenera, Akeldama, uko ndi kunena kuti, Munda wamwazi.
  3800. Act 1:20 Pakuti kwalembedwa m’buku la Masalmo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wokhalamo; ndipo udindo wake woyang’anira wina awutenge.
  3801. Act 1:21 Mwa ichi kwa amuna awa amene adakhala nafe nthawi yonseyi imene Ambuye Yesu adalowa ndikutuluka mwa ife,
  3802. Act 1:22 Kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lomwe lija iye adatengedwa kumka kumwamba kuchokera kwa ife, ayenera m’modzi kusankhidwa akhale mboni pamodzi ndi ife ya kuwuka kwake.
  3803. Act 1:23 Ndipo adasankhapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene adatchedwanso dzina la bambo wake Yustasi, ndi Matiyasi.
  3804. Act 1:24 Ndipo iwo adapemphera, ndipo anati, Inu, Ambuye, amene muzindikira mitima ya [anthu] onse, sonyezani mwa awa awiri amene inu mwamsankha.
  3805. Act 1:25 Kuti iye akhoze kutenga gawo la utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera ku umene Yudase ndi tchimo adagwa, kuti akhoze kupita ku malo a iye yekha.
  3806. Act 1:26 Ndipo adayesa mayere awo; ndipo mayere adagwera Matiyasi, ndipo adawerengedwa pamodzi ndi atumwi khumi ndi m’modziwo.
  3807. Act 2:1 Ndipo pamene tsiku la Pentekoste lidafika kwathunthu, iwo onse adali a mtima umodzi m’malo amodzi.
  3808. Act 2:2 Ndipo mwadzidzidzi padadza phokoso lochokera kumwamba monga ngati la mphepo yothamanga yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene iwo adakhalamo.
  3809. Act 2:3 Ndipo padawonekera kwa iwo malirime wogawanika wonga ngati a moto, ndipo udakhala pa yense wa iwo.
  3810. Act 2:4 Ndipo iwo onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo anayamba kuyankhula ndi malirime ena, monga Mzimu anawapatsa iwo mayankhulidwe.
  3811. Act 2:5 Ndipo adali wokhalako Ayuda mu Yerusalemu, amuna wopembedza, wochokera ku mtundu uliwonse pansi pa thambo.
  3812. Act 2:6 Tsopano pamene izi zinalengezedwa mofalikira kudera lalikulu, khamulo lidasonkhana pamodzi, ndipo lidadodometsedwa, chifukwa chakuti munthu aliyense adamva iwowa alikuyankhula m’chiyankhulidwe chake cha iye mwini.
  3813. Act 2:7 Ndipo anadabwa onse ndipo anazizwa, nanena wina ndi mzake, Tawonani, kodi awa onse ayankhulawa sali Agalileya?
  3814. Act 2:8 Ndipo nanga tikumva bwanji ife munthu aliyense m’chiyankhulidwe chathu, chimene ife tinabadwa nacho?
  3815. Act 2:9 Apartiyani ndi Amedes, ndi Ayelami, ndi iwo wokhala m’Mesopotamiya, ndi m’Yudeya ndi m’Kapadosiya, m’Pontasi, ndi Asiya,
  3816. Act 2:10 M’Frugiya, ndi Pamfiliya, mu Igupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo a ku Roma, Ayuda ndi wotembenukira kuchipembedzo cha Chiyuda,
  3817. Act 2:11 Akrete ndi Aarabu, ife tikuwamva iwo alikuyankhula m’malirime athu ntchito zodabwitsa za Mulungu.
  3818. Act 2:12 Ndipo iwo onse anadabwa, ndipo anali m’chikayiko, kunena wina ndi mzake, Kodi ichi chitanthawuza chiyani?
  3819. Act 2:13 Ena adanyoza kunena, Anthu awa ali wokhuta vinyo walero.
  3820. Act 2:14 ¶Koma Petro, adayimirira pamodzi ndi khumi ndi m’modziwo, anakweza mawu ake, ndi kunena kwa iwo, nati, Inu amuna a ku Yudeya, ndi [inu] nonse wokhala m’Yerusalemu, ichi chidziwike kwa inu, ndipo tcherani khutu ku mawu anga:
  3821. Act 2:15 Pakuti awa sadaledzere, monga muganiza inu; powona kuti ndi ora lachitatu [lokha] la tsiku;
  3822. Act 2:16 Komatu ichi ndi chimene chidanenedwa ndi mneneri Yoweli;
  3823. Act 2:17 Ndipo kudzali m’masiku wotsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lirilonse: ndipo ana anu amuna ndi ana anu akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzawona masomphenya, ndipo abambo akulu anu adzalota maloto:
  3824. Act 2:18 Ndipo pa antchito anga ndi pa adzakazi anga ine ndidzathira m’masiku awo cha Mzimu wanga; ndipo iwo adzanenera.
  3825. Act 2:19 Ndipo ndidzawonetsa zodabwitsa kumwamba m’mwamba, ndi zizindikiro pansi pa dziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi:
  3826. Act 2:20 Dzuwa lidzasandulika mdima, ndi mwezi udzasandulika mwazi, tsiku lalikulu ndi lodziwika la Ambuye lisanadze;
  3827. Act 2:21 Ndipo kudzali, [kuti] wina aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
  3828. Act 2:22 Inu amuna a ku Israyeli, mverani mawu awa; Yesu Mnazareti, mwamuna wovomerezedwa ndi Mulungu pakati pa inu mwa zozizwa ndi zodabwitsa ndi zizindikiro, zimene Mulungu adazichita mwa iye pakati pa inu, monga inu eninso mudziwa.
  3829. Act 2:23 Iye, pokhala woperekedwa ndi uphungu woyikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwamtenga, ndipo ndi manja oyipa mwampachika [pa mtanda] ndi kumupha.
  3830. Act 2:24 Amene Mulungu wamuwukitsa, atamasula zowawa za imfa: chifukwa sikudali kotheka kuti iye agwidwe ndi iyo.
  3831. Act 2:25 Pakuti Davide anena zokhudza iye, ndidawona Ambuye nthawi zonse pamaso panga, pakuti ali pa dzanja langa lamanja, kuti ine ndisasunthike:
  3832. Act 2:26 Choncho udakondwera mtima wanga, ndipo lirime langa lidasangalala; kuwonjezera aponso thupi langanso lidzapuma m’chiyembekezo.
  3833. Act 2:27 Chifukwa inu simudzasiya moyo wanga ku manda, kapena simudzalola Woyera wanu awone chivundi.
  3834. Act 2:28 Inu munadziwitsa ine njira za moyo; inu mudzandipanga ine wodzala ndi chikondwerero ndi nkhope yanu.
  3835. Act 2:29 Amuna [ndi] abale, lolani ine ndilankhule kwa inu mwa ufulu za kholo [lija] Davide, kuti adamwalira ndipo anayikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.
  3836. Act 2:30 Choncho pokhala mneneri, ndi kudziwa kuti Mulungu adalumbira ndi lumbiro kwa iye, kuti mwa chipatso cha m’chiwuno mwake, molingana ndi thupi, adzamuwukitsira Khristu kuti adzakhale pa mpando wake wachifumu.
  3837. Act 2:31 Iye powona ichi kale adayankhula za kuwuka kwa Khristu, kuti moyo wake sudasiyidwe m’manda, kapena thupi lake kuwona chivundi.
  3838. Act 2:32 Yesu ameneyo Mulungu wamuwukitsa, za ichi ife tonse tiri mboni.
  3839. Act 2:33 Choncho pokwezedwa mwa dzanja lamanja la Mulungu, ndi kulandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, watsanulira ichi, chimene inu tsopano mupenya ndi kumva.
  3840. Act 2:34 Pakuti Davide sadakwera kulowa kumwamba ayi: koma iye mwini yekha adati, AMBUYE adati kwa Mbuye wanga, Khala iwe kudzanja lamanja langa,
  3841. Act 2:35 Kufikira ndikayike adani ako chopondapo mapazi ako.
  3842. Act 2:36 Choncho lolani nyumba yonse ya Israyeli idziwitse ndithu, kuti Mulungu wam’panga Yesu yemweyo, amene inu mudampachika, Ambuye ndiponso Khristu.
  3843. Act 2:37 ¶Tsopano pamene adamva [ichi], adalaswa mu mtima mwawo, ndipo adati kwa Petro ndi atumwi enawo, Amuna [ndi] abale, tidzachita chiyani?
  3844. Act 2:38 Kenaka Petro adati kwa iwo, Lapani, ndipo mubatizidwe yense wa inu m’dzina la Yesu Khristu chifukwa cha chikhululukiro cha machimo anu, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
  3845. Act 2:39 Pakuti lonjezano liri kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse amene ali kutali, [ngakhale] ambiri monga Ambuye Mulungu wathu adzayitana.
  3846. Act 2:40 Ndipo ndi mawu ena ambiri iye adachita umboni ndi kudandawulira, kunena kuti, Mudzipulumutse nokha ku m’badwo uwu wosaweruzika.
  3847. Act 2:41 ¶Kenaka iwo amene adalandira mawu ake mokondwera anabatizidwa: ndipo tsiku lomwero idawonjezeka [kwa iwo] miyoyo ngati zikwi zitatu.
  3848. Act 2:42 Ndipo iwo adakhalabe chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano, ndi m’kunyema mkate ndi m’mapemphero.
  3849. Act 2:43 Ndipo mantha adadza pa moyo uliwonse: ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zidachitidwa ndi atumwi.
  3850. Act 2:44 Ndipo onse amene adakhulupirira adali pamodzi, ndipo adali nazo zinthu zonse zofanana.
  3851. Act 2:45 Ndipo adagulitsa zinthu zawo ndi katundu, nazigawira kwa [anthu] onse, monga aliyense adasowa.
  3852. Act 2:46 Ndipo iwo, pokhalabe chikhalire tsiku ndi tsiku ndi mtima umodzi m’kachisi, ndi kunyema mkate kuchokera nyumba [ina] kumka ku nyumba [ina], anadya chakudya chawo ndi chisangalalo ndi mtima umodzi.
  3853. Act 2:47 Nalemekeza Mulungu, ndi kukhala ndi kukonderedwa ndi anthu onse. Ndipo Ambuye adawonjezera ku mpingo tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
  3854. Act 3:1 Tsopano Petro ndi Yohane adakwera kupita pamodzi m’kachisi kukapemphera pa ora la kupemphera, [ndilo ora] la chisanu ndi chinayi.
  3855. Act 3:2 Ndipo munthu wina wolumala chibadwire adanyamulidwa, amene ankamuyika tsiku ndi tsiku pa khomo la kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zachifundo kwa iwo amene ankalowa m’kachisi;
  3856. Act 3:3 Amene pakuwona Petro ndi Yohane akuti alowe m’kachisi, adapempha alandire zachifundo.
  3857. Act 3:4 Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, adati, Yang’ana pa ife.
  3858. Act 3:5 Ndipo iye adamvera iwo, nayembekeza kulandira kanthu kuchokera kwa iwo.
  3859. Act 3:6 Kenaka Petro adati, Siliva ndi golide ine ndiribe; koma chimene ndiri nacho ichi ndikupatsa iwe: M’dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, imirira nuyende.
  3860. Act 3:7 Ndipo adamgwira iye ku dzanja lake lamanja, nam’nyamutsa [iye]: ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi mfundo za ku mapazi zidalandira mphamvu.
  3861. Act 3:8 Ndipo iye adalumpha nayimirira, ndipo anayenda, ndipo adalowa pamodzi nawo m’kachisi, akuyenda, ndi kulumpha, ndi kulemekeza Mulungu.
  3862. Act 3:9 Ndipo anthu onse adamuwona iye alikuyenda ndi kulemekeza Mulungu:
  3863. Act 3:10 Ndipo iwo adadziwa kuti adali iye amene ankakhala chifukwa cha zachifundo pa khomo Lokongola la kachisi: ndipo iwo adadzazidwa ndi kudabwa ndi mantha kwambiri pa ichi chimene chidamchitikira iye.
  3864. Act 3:11 Ndipo pamene munthu wolumala amene adachiritsidwa uja adagwira Petro ndi Yohane, anthu onse adawathamangira pamodzi kukhumbi lotchedwa la Solomon, alikudabwa kwakukulu.
  3865. Act 3:12 ¶Koma pamene Petro adawona [ichi], adayankha kwa anthu, Inu amuna a Israyeli, muzizwa bwanji inu pa ichi? Kapena mutipenyetsetsa kwambiri ife bwanji, monga ngati ndi mphamvu kapena ndi chiyero chathu ife tidapangitsa munthu uyu kuti ayende?
  3866. Act 3:13 Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo, Mulungu wa makolo athu, adalemekeza Mwana wake wamwamuna Yesu; amene inu munampereka, ndi kumkana iye pamaso pa Pilato, pamene iyeyu adafuna kum’masula [iye].
  3867. Act 3:14 Koma inu mudam’kana Woyera ndi Wolungamayo, ndipo mudakhumba munthu wakupha kuti apatsidwe kwa inu;
  3868. Act 3:15 Ndi kupha Kalonga wa moyo, amene Mulungu wamuwukitsa kwa akufa; za ichi ife tiri mboni.
  3869. Act 3:16 Ndipo mu dzina lake kupyolera mu chukhulupiriro mu dzina lake zapangitsa munthu uyu kukhala ndi mphamvu, iye amene inu mumuwona ndi kumumdziwa: inde, chikhulupiriro chimene cha mwa iye champatsa iye kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.
  3870. Act 3:17 Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti mwakusadziwa inu mudachita [ichi], monganso [adachita] wolamulira anu.
  3871. Act 3:18 Koma zinthu zimenezo, zimene Mulungu kale adaziwonetsera kudzera m’kamwa mwa aneneri ake onse, kuti Khristu ayenera kumva zowawa, iye kotero wakwaniritsa.
  3872. Act 3:19 ¶Choncho inu lapani, ndi kutembenuka, kuti machimo anu akhoze kufafanizidwa, pamene nthawi zakutsitsimutsa zidzadze zochokera m’kupezeka kwa Ambuye;
  3873. Act 3:20 Ndipo adzatuma Yesu Khristu, amene poyamba adalalikidwa kwa inu:
  3874. Act 3:21 Amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi za kubwezera kwa eni zinthu zonse, zimene Mulungu adayankhula kudzera m’kamwa mwa aneneri ake onse woyera chiyambire cha dziko lapansi.
  3875. Act 3:22 Pakuti Mose zowonadi adati kwa makolo, Ambuye Mulungu wanu adzawukitsira kwa inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; iyeyo mudzamvera inu m’zinthu zonse adzayankhula kwa inu.
  3876. Act 3:23 Ndipo kudzali, [kuti] moyo uliwonse, umene sudzamvera m’neneri ameneyo, udzawonongedwa kuchotsedwa pakati pa anthu.
  3877. Act 3:24 Inde, ndipo aneneri onse kuyambira Samueli ndi wobwera pambuyo pake [atamwalira iye], ambiri monga adayankhula, adalosera chimodzimodzi za masiku awa.
  3878. Act 3:25 Inu ndinu ana a aneneri, ndi apanganolo limene Mulungu adapangana ndi makolo athu, kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.
  3879. Act 3:26 Kwa inu Mulungu choyamba, atawukitsa Mwana wake wamwamuna Yesu, adamutuma iye kukudalitsani inu, mwa kubweza wina aliyense wa inu ku zoyipa zake.
  3880. Act 4:1 Ndipo pamene adali kuyankhula kwa anthu, ansembe ndi m’dindo wa ku kachisi, ndi Asaduki, anadza pa iwo,
  3881. Act 4:2 Ali wovutika mtima pakuti iwo adaphunzitsa anthuwo, ndipo analalikira kudzera mwa Yesu kuwuka kwa akufa.
  3882. Act 4:3 Ndipo adawagwira, nawayika [iwo] m’malo akuwasungamo kufikira tsiku lotsatira: pakuti tsopano idali nthawi yamadzulo.
  3883. Act 4:4 Ngakhale ziri motero chomwecho ambiri a iwo amene adamva mawu adakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chidali ngati zikwi zisanu.
  3884. Act 4:5 ¶Ndipo zidachitika izi tsiku lotsatira, kuti olamula awo, ndi akulu, ndi alembi,
  3885. Act 4:6 Ndi Anasi wansembe wamkulu, Kayefasi, ndi Yohane, ndi Alekezanda, ndipo ambiri amene ali a fuko la wamkulu wa ansembe, adasonkhana pamodzi ku Yerusalemu.
  3886. Act 4:7 Ndipo m’mene adawayimika iwo pakati, adafunsa; Mwa mphamvu yanji, kapena m’dzina lanji, mwachita ichi inu?
  3887. Act 4:8 Kenaka Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera adati kwa iwo, Inu oweruza a anthu, ndi akulu a Israyeli,
  3888. Act 4:9 Ngati ife tsiku ili tiyesedwa chifukwa cha chochita chabwino chimene chachitika pa munthu wopanda mphamvuyo, ndi njira yomwe wachiritsidwira iye;
  3889. Act 4:10 Chidziwike kwa inu nonse, ndi kwa anthu onse a Israyeli, kuti m’dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, amene inu mudampachika, amene Mulungu adamuwukitsa kwa akufa, [ngakhale] mwa iyeyu munthuyu ayimirira pamaso panu wangwiro.
  3890. Act 4:11 Uwu ndiwo mwalawo udayikidwa kukhala wopanda pake ndi inu womanga [nyumba], umene wakhala mwala wa pangodya.
  3891. Act 4:12 Kapena palibe chipulumutso mwa wina wake: pakuti palibe dzina lina pansi pa kumwamba lopatsidwa pakati pa anthu, mwa limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.
  3892. Act 4:13 ¶Tsopano pamene adawona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo kuzindikira iwo anali amuna wosaphunzira ndi wosazindikira, adazizwa ndipo adawadziwa iwo, kuti iwo adakhala pamodzi ndi Yesu.
  3893. Act 4:14 Ndipo pakuwona munthu amene adachiritsidwayo alikuyimirira pamodzi nawo, iwo sakadatha kunena kanthu kotsutsa ichi.
  3894. Act 4:15 Koma pamene adawalamulira iwo kuti apite pambali kuchoka m’bwalo la akulu, adakambirana pakati pawo.
  3895. Act 4:16 Kunena kuti, Tidzachita chiyani kwa anthu awa? Pakuti ndithu chozizwa chodziwika chachitidwa ndi iwo [chili] chowonetsedwa kwa onse akukhala m’Yerusalemu; ndipo ife sitingakane [ichi].
  3896. Act 4:17 Komatu kuti chisafalikire kuposera apa pakati pa anthu, tiyeni tiwawopseze molimbika iwo, kuti asayankhulenso kuyambira tsopano kwa munthu aliyense m’dzina ili.
  3897. Act 4:18 Ndipo adawayitana iwo, ndipo anawalamulira iwo kuti asalankhule konse kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu.
  3898. Act 4:19 Koma Petro ndi Yohane adayankha ndi kunena kwa iwo, Ngati kuli kwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa kwa Mulungu, weruzani inu.
  3899. Act 4:20 Pakuti ife sitingathe kuleka koma kuyankhula zinthu zimene taziwona ndi kumva.
  3900. Act 4:21 Kotero m’mene iwo adapitirira kuwawopseza iwo, adawamasula iwo amuke, osapeza kanthu ka momwe akhoza kuwalangira iwo, chifukwa cha anthu: pakuti [anthu] onse adapereka ulemerero kwa Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.
  3901. Act 4:22 Pakuti munthuyo adali wa zaka zoposa makumi anayi, amene chozizwa ichi chakumchiritsa chidawonetsedwa.
  3902. Act 4:23 ¶Ndipo m’mene adamasulidwa, anapita kwa anzawo a iwo wokha, nawawuza zirizonse woweruza ndi akulu adanena kwa iwo.
  3903. Act 4:24 Ndipo m’mene adamva zimenezo, adakweza mawu kwa Mulungu ndi mtima umodzi, ndipo anati, Ambuye inu [ndinu] Mulungu, amene mwalenga kumwamba, ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi zonse zomwe ziri momwemo:
  3904. Act 4:25 Amene mwa pakamwa pa mtumiki wanu Davide mwanena, Kodi achikunja adapseranji mtima, ndi anthu alingalira zopanda pake?
  3905. Act 4:26 Mafumu a dziko lapansi anayimirira, ndipo wolamula adasonkhanitsidwa pamodzi kutsutsana ndi Ambuye, ndi kutsutsana ndi Khristu wake.
  3906. Act 4:27 Pakuti zowonadi kutsutsana mwana woyera Yesu, amene inu mwam’dzoza, Herode, ndi Pontiyasi Pilato, ndi Amitundu, ndi anthu a Israyeli, adasonkhana pamodzi.
  3907. Act 4:28 Kuti achite chilichonse chimene dzanja lanu ndi uphungu wanu mudazikonzeratu kale kuti zidzachitike.
  3908. Act 4:29 Ndipo tsopano, Ambuye, penyani zowopseza zawo: ndipo patsani kwa atumiki anu, kuti ndi kulimbika mtima konse iwo akhoze kuyankhula mawu anu.
  3909. Act 4:30 Pa kutambasula dzanja lanu kuchiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zodabwitsa zikhoze kuchitidwa mwa dzina la mwana wanu woyera Yesu.
  3910. Act 4:31 ¶Ndipo m’mene iwo adapemphera, pamalopo padagwedezeka pamene iwo adasonkhanirapo pamodzi; ndipo iwo onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo iwo anayankhula mawu a Mulungu ndi kulimbika mtima.
  3911. Act 4:32 Ndipo unyinji wa iwo wokhulupirira adali a mtima umodzi ndi moyo umodzi: kapena sadanena wina aliyense [wa iwo] kuti kanthu kazinthu kamene adali nako ndi kake ka iye yekha; koma adali nazo zonse zofanana.
  3912. Act 4:33 Ndipo ndi mphamvu yayikulu atumwi adapereka umboni za kuwuka kwa Ambuye Yesu: ndipo chisomo chachikulu chidali pa iwo onse.
  3913. Act 4:34 Kapena adalipo wina pakati pawo amene adasowa: pakuti ambiri amene adali nayo minda kapena nyumba adazigulitsa, nabwera nawo mtengo wake wa zinthu zimene zidagulitsidwa.
  3914. Act 4:35 Ndipo adaziyika [izi] pansi pa mapazi a atumwi: ndipo kugawa kudachitika kwa munthu aliyense monga iye adali ndi chosowa.
  3915. Act 4:36 Ndipo Yoses, amene adatchedwa ndi atumwi Barnabas, (limene liri, lotanthawuzidwa, Mwana wa chisangalalo,) Mlevi, [ndi] wa ku dziko la Sayipulasi,
  3916. Act 4:37 Pokhala nawo munda, adagulitsa [uwo], nabwera nazo ndalama, ndipo anaziyika [izo] pa mapazi a atumwi.
  3917. Act 5:1 KOMA munthu wina dzina lake Ananiyasi pamodzi ndi Safira mkazi wake, adagulitsa chomwe chinali chawo,
  3918. Act 5:2 Ndipo anasunga kumbuyo [gawo] la mtengowo, mkazi wakenso kukhala wa chinsinsi [ku ichi], ndipo anabweretsa gawo lina, ndi kuliyika [ilo], pa mapazi a atumwi.
  3919. Act 5:3 Koma Petro adati, Ananiyasi, kodi Satana wadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanama kwa Mzimu Woyera, ndi kusunga kumbuyo [gawo] la mtengo wake wa mundawo?
  3920. Act 5:4 Pamene udalipo, sudali wa iwe mwini kodi? Ndipo pamene udagulitsidwa, kodi sudali mu mphamvu ya iwe mwini? Chifukwa chiyani udaganiza chinthu ichi mu mtima mwako? Iwe sudaname kwa anthu, koma kwa Mulungu.
  3921. Act 5:5 Ndipo Ananiyasi pakumva mawu awa adagwa pansi, ndipo anamwalira: ndipo mantha akulu adafikira pa iwo onse amene adamva zinthu izi.
  3922. Act 5:6 Ndipo anyamata adanyamuka, namkulunga iye, ndipo anam’nyamula kutuluka [naye] kunja, ndipo anamuyika [m’manda iye].
  3923. Act 5:7 Ndipo panali patapita mpata pafupifupi wa maora atatu, pamene mkazi wake, wosadziwa chimene chidachitidwacho, adalowa.
  3924. Act 5:8 Ndipo Petro adayankha kwa iye, Undiwuze ngati mudagulitsa mundawo pa mtengo wakuti? Ndipo iye adanena, Inde, pa mtengo wakuti.
  3925. Act 5:9 Kenaka Petro adati kwa iye, Zatani kuti inu mwapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Tawona, mapazi awo a iwo amene ayika mwamuna wako [ali] pakhomo, ndipo adzanyamula iwe kukutulutsa.
  3926. Act 5:10 Ndipo iye adagwa pansi nthawi yomweyo pa mapazi ake, ndipo anamwalira: ndipo anyamatawo adalowa, ndipo anampeza iye atafa, ndipo, adam’nyamula [iye] kutuluka naye, namuyika [iye] pambali pa mwamuna wake.
  3927. Act 5:11 Ndipo mantha akulu adafikira pa mpingo wonse, ndi pa ambiri womwe adamva zinthu izi.
  3928. Act 5:12 ¶Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zidachitidwa pakati pa anthu; (ndipo adali onse ndi mtima umodzi m’khumbi la Solomon.
  3929. Act 5:13 Ndipo pa wotsalawo palibe m’modzi adalimba mtima kuphatikana nawo: komatu anthu adawakuzitsa iwo.
  3930. Act 5:14 Ndipo wokhulupirira adachuluka kuwonjezekabe kwa Ambuye, makamu a amuna ndi akazi).
  3931. Act 5:15 Kotero kuti adabweretsa wodwala m’makwalala, nawayika [iwo] pamakama ndi pamphasa, kuti popita m’nthunzi wa Petro ungakhoze kuwafikira ena a iwo.
  3932. Act 5:16 Panadzanso khamu [lochokera] ku mizinda yozungulira Yerusalemu, kubweretsa anthu wodwala, ndi iwo amene adali wovutitsidwa ndi mizimu yonyansa: ndipo iwo adachiritsidwa aliyense.
  3933. Act 5:17 ¶Kenaka mkulu wa ansembe adayimirira, ndi onse amene adali naye, (amene ali a mpatuko wa Asaduki,) ndipo adali wodzazidwa ndi mkwiyo.
  3934. Act 5:18 Ndipo adathira manja awo pa atumwi, ndipo anawayika m’ndende ya anthu wamba.
  3935. Act 5:19 Koma mngelo wa Ambuye usiku adatsegula makomo a ndende, ndipo anawatulutsa iwo, ndipo anati,
  3936. Act 5:20 Pitani, ndipo imirirani ndi kuyankhula m’kachisi kwa anthu mawu onse a moyo umenewu.
  3937. Act 5:21 Ndipo pamene adamva [icho], adalowa m’kachisi m’bandakucha, ndipo adaphunzitsa. Koma mkulu wa ansembe adadza, ndi iwo amene adali ndi iye, ndipo anasonkhanitsa abwalo la akulu, ndi akulu onse a ana a Israyeli, ndipo anatuma kundende kuti abweretsedwe iwo.
  3938. Act 5:22 Koma asirikali amene adabwera, ndipo sadawapeza iwo m’ndende, iwo anabwerera, ndipo adafotokoza.
  3939. Act 5:23 Kunena kuti, Nyumba ya ndende zowonadi ife tidapeza chitsekere ndi chitetezo chonse, ndi olondera ali chiyimire kunja pambali pamaso pa makomo: koma pamene ife tidatsegula, tidapeza mopanda munthu aliyense mkati.
  3940. Act 5:24 Tsopano m’mene mkulu wansembe ndi mdindo wa Kachisi ndi ansembe akulu adamva zinthu izi, iwo adakayikira za iwo kuti ichi chidzakula kufikira pati.
  3941. Act 5:25 Kenaka padadza wina ndipo anawafotokozera iwo, kunena kuti, Tawonani, amuna aja amene inu mudawayika m’ndende alikuyimirira m’Kachisi, ndi kuphunzitsa anthu.
  3942. Act 5:26 Kenaka adapita mdindo ndi asirikali, ndipo anabwera nawo iwo mopanda chiwawa: pakuti iwo adawopa anthu, kuti mwina iwo angaponyedwe miyala.
  3943. Act 5:27 Ndipo m’mene adadza nawo iwo, adawayika [iwo] pamaso pa bwalo la akulu: ndipo mkulu wansembe adawafunsa iwo,
  3944. Act 5:28 Kunena kuti, Kodi sitidakulamulani molimbika inu kuti musaphunzitse m’dzina ili? Ndipo, tawonani mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera mwazi wa munthu uyu pa ife.
  3945. Act 5:29 ¶Kenaka Petro ndi atumwi [ena] adayankha ndipo anati, Ife tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.
  3946. Act 5:30 Mulungu wa makolo athu adawukitsa Yesu, amene inu mudamupha ndi kumpachika pa mtengo.
  3947. Act 5:31 Ameneyo Mulungu wamkweza ndi dzanja lake lamanja [kuti akhale] Kalonga ndi Mpulumutsi, kuti apatse kulapa kwa Israyeli, ndi chikhululukiro cha machimo.
  3948. Act 5:32 Ndipo ife tiri mboni za iye za zinthu izi; ndi [chotero ali] Mzimu Woyeranso, amene Mulungu wapereka kwa iwo akumvera iye.
  3949. Act 5:33 ¶Nthawi imene adamva [ichi], iwo adapsa mtima, ndipo adatenga upangiri kuti awaphe.
  3950. Act 5:34 Kenaka adayimirirapo wina m’bwalo la akulu, Mfarisi, wotchedwa Gamaliyeli, mphunzitsi wa chilamulo, adali wopatsidwa ulemu pakati pa anthu onse, ndipo analamula kuti atumwiwo akhale patali pang’ono;
  3951. Act 5:35 Ndipo adati kwa iwo, Inu amuna a Israyeli, samalirani kwa inu nokha chimene inu mufuna muchite zokhudza anthu awa.
  3952. Act 5:36 Pakuti asadafike masiku ano adawuka Tewudasi, nadzikuza iye mwini kuti ali munthu wina wake; amene kwa iye anthu owerengeka, pafupifupi mazana anayi adadziphatika wokha eni: amene adaphedwa; ndipo onse, ambiri amene adamvera iye, adamwazika, nakhala achabe.
  3953. Act 5:37 Atapita munthu ameneyo adawuka Yudas wa ku Galileya m’masiku a kalembera, ndipo anakopa anthu ambiri kumtsata iye: iyenso adawonongeka; ndi onse, [ngakhale] ambiri amene adamvera iye, adabalalitsidwa.
  3954. Act 5:38 Ndipo tsopano ine ndinena kwa inu, Dzileketseni kwa anthu amenewa, ndipo muwasiye wokha: pakuti ngati uphungu umenewu kapena ntchito iyi ikhala ya kwa anthu, idzakhala yachabe;
  3955. Act 5:39 Koma ngati ili ya kwa Mulungu simungathe kuyigonjetsa, kuti mwina inu mungapezeke ngakhale wotsutsana ndi Mulungu.
  3956. Act 5:40 Ndipo kwa iye adavomereza: ndipo m’mene adayitana atumwi, ndi kuwakwapula [iwo], analamulira kuti iwo asayankhule m’dzina la Yesu, ndipo adalola iwo amuke.
  3957. Act 5:41 ¶Ndipo iwo adanyamuka kuchokera pamaso pa bwalo la akulu, akukondwera kuti iwo adawerengedwa woyenera kunzunzidwa mwa manyazi chifukwa cha dzina lake.
  3958. Act 5:42 Ndipo tsiku ndi tsiku m’kachisi, ndi m’nyumba iliyonse, sadaleka kuphunzitsa ndi kulalika Khristu Yesu.
  3959. Act 6:1 Ndipo m’masiku awo, pamene chiwerengero cha wophunzira chidachulukitsidwa, padabuka madandawulo a Ahelene kudandawula pa Ahebri, chifukwa amasiye awo adayiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.
  3960. Act 6:2 Kenaka khumi ndi awiri adayitana khamu la wophunzira [kwa iwo], ndipo anati, Ichi sichifukwa chakuti ife tisiye mawu a Mulungu, ndi kutumikira pamagome.
  3961. Act 6:3 Mwa ichi, abale, yang’anani pakati pa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, wodzala ndi Mzimu Woyera ndi nzeru, amene ife tikawayike pa ntchito iyi.
  3962. Act 6:4 Koma ife tidzadzipereka tokha kupitiriza ku pemphero, ndi ku utumuki wa mawu.
  3963. Act 6:5 ¶Ndipo mawu amenewa adakondweretsa khamu lonse: ndipo iwo adasankha Stefano, munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipi, ndi Prokorasi, ndi Nikanora, ndi Timon, ndi Pamenasi, ndi Nikolasi wotembenukira kuchipembedzo cha Chiyuda wa ku Antiyoki:
  3964. Act 6:6 Amene adawayika pamaso pa atumwi: ndipo m’mene adapemphera, adayika manja [awo] pa iwo.
  3965. Act 6:7 Ndipo mawu a Mulungu adakula; ndipo chiwerengero cha wophunzira chidachulukitsidwa kwakukulu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe lidakhala lomvera ku chikhulupirirocho.
  3966. Act 6:8 Ndipo Stefano, wodzala ndi chikhulupiriro ndi mphamvu, adachita zodabwitsa zazikulu ndi zozizwa pakati pa anthu.
  3967. Act 6:9 ¶Kenaka padawuka ena a m’sunagoge imene itchedwa [sunagoge] ya Amsinga Womasulidwa, ndi Asayireniya, ndi Alekezandiriya, ndi a iwo a ku Silisiya ndi a ku Asiya, kutsutsana ndi Stefano.
  3968. Act 6:10 Ndipo sadathe kuyitsutsa nzeru ndi mzimu amene iye adayankhula kudzera mwa iye.
  3969. Act 6:11 Kenaka iwo adapereka ziphuphu kwa anthu, amene adati, Tidamumva iye ali kunenera mawu amwano motsutsana ndi Mose, ndi [motsutsana ndi] Mulungu.
  3970. Act 6:12 Ndipo iwo adatakasa anthu, ndi akulu, ndi alembi, ndipo anafika pa [iye], ndipo anamgwira [iye], ndipo anam’bweretsa [iye] kubwalo la akulu,
  3971. Act 6:13 Ndipo anayika mboni zonama, zimene zinanena, Munthu uyu saleka kulankhula mawu amwano motsutsana ndi malo ano woyera, ndi chilamulo:
  3972. Act 6:14 Pakuti ife tamumva iye ali kunena, kuti Yesu uyu wa ku Nazareti adzawononga malo awa, ndipo adzasintha miyambo imene Mose adatipatsa ife.
  3973. Act 6:15 Ndipo onse wokhala m’bwalo la akulu, akuyang’anitsitsa mwachidwi pa iye, anawona nkhope yake ngati kuti idali nkhope ya mngelo.
  3974. Act 7:1 Kenaka mkulu wansembe adati, Ziri chonchi kodi zinthu izi?
  3975. Act 7:2 Ndipo iye adati, Amuna, abale, ndi atate, mverani; Mulungu wa ulemerero adawonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pamene adali iye m’Mesopotamiya, asadakhale iye m’Haran,
  3976. Act 7:3 Ndipo adati kwa iye, Tuluka iwe ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo bwera iwe ku dziko limene ine ndidzakusonyeza iwe.
  3977. Act 7:4 Kenaka iye adatuluka m’dziko la Akaldiyani, nakhala m’Haran: ndipo kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, iye adamsuntha kulowa m’dziko lino, m’mene inu mukhalamo tsopano.
  3978. Act 7:5 Ndipo sadampatsa cholowa chake m’menemo, ayi, osati [chachikulu chotero] ngati popondapo phazi lake: komatu iye adalonjeza kuti iye akadampatsa ili likhale lake, ndi kwa mbewu yake yomtsatira iye, panthawiyo [monga] adalibe mwana.
  3979. Act 7:6 Ndipo Mulungu adalankhula chotero, Kuti mbewu yake idzakhala nthawi yayitali m’dziko la chilendo; ndi kuti iwo adzabweretsa iwo mu ukapolo, ndi kuwachitira choyipa [iwo], zaka mazana anayi.
  3980. Act 7:7 Ndipo mtundu wa anthu umene iwo adzakhala akapolo ine ndidzawuweruza, adatero Mulungu: ndipo pambuyo pa izi adzatuluka, nadzanditumikira ine pamalo ano.
  3981. Act 7:8 Ndipo adampatsa iye pangano la mdulidwe: ndipo kotero [Abrahamu] anabala Isake, namchita mdulidwe tsiku la chisanu ndi chitatu; ndi Isake [adabala] Yakobo; ndi Yakobo [adabala] makolo akulu aja khumi ndi awiri.
  3982. Act 7:9 Ndipo makolo akuluwa, mosunthidwa ndi nsanje, adamgulitsa Yosefe ku Igupto: koma Mulungu adali ndi iye.
  3983. Act 7:10 Ndipo anamlanditsa iye kumtulutsa m’zisawutso zake zonse, ndipo anampatsa kukonderedwa ndi nzeru pamaso pa Farawo mfumu ya ku Igupto; ndipo adamuyika iye kazembe pa Igupto ndi nyumba yake yonse.
  3984. Act 7:11 Tsopano padadza njala pa dziko lonse la Igupto ndi Kanani, ndi chisawutso chachikulu: ndipo makolo athu sadapeza chakudya.
  3985. Act 7:12 Koma pamene Yakobo adamva kuti muli tirigu mu Igupto, iye adatuma makolo athu poyamba.
  3986. Act 7:13 Ndipo [nthawi] yachiwiri Yosefe adazindikiritsidwa kwa abale ake; ndipo a pa banja la Yosefe lidazindikiritsidwa kwa Farawo.
  3987. Act 7:14 Kenaka Yosefe adatumiza, ndi kuyitana Yakobo atate wake kwa [iye], ndi a pa banja lake lonse, anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.
  3988. Act 7:15 Potero Yakobo adapita kutsikira ku Igupto, ndipo adamwalira, iye, ndi makolo athu.
  3989. Act 7:16 Ndipo adanyamulidwa kupita mu Sekemu, ndipo anawayika m’manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana amuna a Emori [atate] wa Sekemu.
  3990. Act 7:17 Koma m’mene nthawi idayandikira ya lonjezo limene Mulungu adalumbira kwa Abrahamu, anthuwo adakula ndi kuchuluka mu Igupto,
  3991. Act 7:18 Kufikira mfumu yina idawuka, imene siyidamdziwa Yosefe.
  3992. Act 7:19 Yomweyo idachita mochenjera ndi fuko lathu, ndi kuwachitira moyipa makolo athu, kotero kuti anataya kunja ana awo, kuti mapeto ake tisakhoze kukhala ndi moyo.
  3993. Act 7:20 Mu nyengo imene anabadwa Mose, ndipo anaposa kukongola ndithu, ndipo adamlera m’nyumba ya atate wake miyezi itatu:
  3994. Act 7:21 Ndipo pamene anamtaya iye kunja, mwana wa mkazi wa Farawo adamtola iye, namlera akhale mwana wake wamwamuna.
  3995. Act 7:22 Ndipo Mose adaphunzira mu nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu m’mawu ndi m’ntchito.
  3996. Act 7:23 Koma pamene zaka zake zidafika kwathunthu makumi anayi, mudalowa mu mtima mwake kukayendera abale ake ana a Israyeli.
  3997. Act 7:24 Ndipo pamene anawona wina [wa iwo] alikuchita choyipa, iye adamchinjiriza [iye], ndipo anam’bwezerera chilango iye wozunzidwayo, ndipo anakantha M’Igupto:
  3998. Act 7:25 Pakuti iye adayesa kuti abale ake akadazindikira za momwe Mulungu mwa dzanja lake akadakhoza kuwapulumutsa iwo; koma iwo sadazindikira ayi.
  3999. Act 7:26 Ndipo tsiku lotsatira iye adadziwonetsera yekha kwa iwo pamene anali kulimbana ndewu, ndipo akadafuna kuti awayanjanitsenso pamodzi iwo, kunena kuti, Amuna, muli abale; kodi muchitirana choyipa kwa wina ndi mzake bwanji?
  4000. Act 7:27 Koma iye wakumchitira woyandikana naye choyipa adamkankha, kunena kuti, Ndani wakuyika iwe wolamula ndi woweruza pa ife?
  4001. Act 7:28 Ufuna kundipha ine kodi, monga muja iwe udachitira M’Igupto dzulo?
  4002. Act 7:29 Kenaka adathawa Mose pa mawu awa, ndipo anakhala mlendo mdziko la Midiyani, kumene adabala ana amuna awiri.
  4003. Act 7:30 Ndipo zitatha zaka makumi anayi, padawonekera kwa iye m’chipululu cha Sina mngelo wa Ambuye m’lawi la moto m’chitsamba.
  4004. Act 7:31 Pamene Mose adawona [ichi], iye adazizwa pachowonekachi: ndipo pamene adayandikira iye kukawona [ichi], mawu a Ambuye adadza kwa iye,
  4005. Act 7:32 Kunena kuti, Ine [ndine] Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose adanthunthumira, ndipo sadalimbika mtima kuwonetsetsako.
  4006. Act 7:33 Kenaka Ambuye adati kwa iye, Vula nsapato zako ku mapazi ako: pakuti pa malo pamene uyimapo m’pamalo woyera.
  4007. Act 7:34 Ine ndawona, ine ndawona chisawutso cha anthu anga chimene chili M’Igupto, ndipo ndamva kubuwula kwawo, ndipo ndabwera kuwalanditsa iwo. Ndipo tsopano bwera, ine ndikutuma iwe ku Igupto.
  4008. Act 7:35 Mose uyu amene iwo adamkana, kunena kuti, Ndani wakuyika iwe wolamula ndi woweruza? Yemweyo Mulungu adamtuma [kuti] akhale wolamula ndi mombolo ndi dzanja la mngelo amene anamuwonekera m’chitsamba.
  4009. Act 7:36 Iye adawatulutsa, atatha kuwonetsa zodabwitsa ndi zizindikiro m’dziko la Igupto, ndi m’nyanja Yofiyira, ndi m’chipululu zaka makumi anayi.
  4010. Act 7:37 ¶Uyu ndi Mose uja, amene adati kwa ana a Israyeli, Ambuye Mulungu wanu adzawukitsira kwa inu mneneri wa mwa abale anu, wonga ine, iyeyo inu mudzamvere.
  4011. Act 7:38 Uyu ndi iye, amene adali mu mpingo m’chipululu ndi mngelo amene anayankhula kwa iye m’phiri la Sina, [pamodzi] ndi makolo athu: amene adalandira maneno amoyo kuti apatse kwa ife:
  4012. Act 7:39 Kwa iye amene makolo athu sadafuna kumvera, koma adamkankha [iye] achoke kwa iwo, ndipo m’mitima mwawo anabwereranso m’mbuyo ku Igupto.
  4013. Act 7:40 Kunena kwa Aroni, Tipangireni ife milungu yopita patsogolo pa ife: pakuti [za] Mose uyu, amene adatitulutsa ife m’Igupto, ife sitidziwa chomwe chamgwera iye.
  4014. Act 7:41 Ndipo adapanga mwana wa ng’ombe masiku amenewo, ndipo anapereka nsembe kwa fanolo, ndipo anakondwerera ndi ntchito za manja awo.
  4015. Act 7:42 Kenaka Mulungu adatembenuka, ndipo anawapereka iwo alambire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m’buku la aneneri, Inu nyumba ya Israyeli, kodi mwapereka kwa ine nyama zophedwa ndi nsembe [kwa nthawi ya zaka] makumi anayi m’chipululu?
  4016. Act 7:43 Inde, inu mudatenga chihema cha Moloki, ndi nyenyezi ya mulungu wanu Remfani, zithunzi zimene inu mudazipanga kuzilambira izo: ndipo ndidzakutengani kumka nanu mopitirira Babuloni.
  4017. Act 7:44 Makolo athu adali ndi chihema cha umboni m’chipululu, monga adalamula iye, kuyankhula kwa Mose, kuti achipange ichi monga mwa mapangidwe amene iye adawawona.
  4018. Act 7:45 Chimenenso makolo athu adadza m’mbuyo adachibweretsa kulowa nacho ndi Yesu m’kulandira cholowa chawo cha kwa Amitundu, amene Mulungu adawapitikitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;
  4019. Act 7:46 Amene adapeza kukonderedwa pamaso pa Mulungu, ndipo anakhumba kupeza chihema cha Mulungu wa Yakobo.
  4020. Act 7:47 Koma Solomon adam’mangira iye nyumba.
  4021. Act 7:48 Ngakhale ziri motero chomwecho Wam’wambamwamba sakhala m’makachisi wopangidwa ndi manja; monga anena mneneri,
  4022. Act 7:49 Kumwamba [ndiko] mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi [liri] popondapo mapazi anga: mudzandimangira inu nyumba yotani ine? Atero Ambuye: kapena [ali] wotani malo a mpumulo wanga?
  4023. Act 7:50 Kodi dzanja langa silidapanga zinthu izi zonse?
  4024. Act 7:51 ¶Inu owuma makosi ndi osadulidwa mu mtima ndi makutu, inu nthawi zonse mukaniza Mzimu Woyera: monga makolo anu [adachita, momwemo muchita] inu.
  4025. Act 7:52 Ndi yani wa aneneri amene makolo anu sadamzunza? Ndipo adawapha iwo amene adawawonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa iye amene mwakhala tsopano wompereka ndi akupha:
  4026. Act 7:53 Amene mwalandira chilamulo monga chidayikidwa ndi angelo, ndipo simudachisunga [ichi].
  4027. Act 7:54 ¶Pamene adamva zinthu izi, adapsa mtima, ndipo iwo adakukutira pa iye ndi mano [awo].
  4028. Act 7:55 Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, adapenyetsetsa m’mwamba, ndipo anawona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuyimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.
  4029. Act 7:56 Ndipo adati, Tawonani, ine ndipenya miyamba yotseguka, ndi Mwana wamwamuna wa munthu ali kuyimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.
  4030. Act 7:57 Kenaka iwo adafuwula ndi mawu okwera, ndipo anatseka m’makutu mwawo, nathamangira pa iye ndi mtima umodzi.
  4031. Act 7:58 Ndipo adamtaya [iye] kunja kwa mzinda, ndipo anamponya miyala [iye]: ndipo mbonizo zidayika zovala zawo pa mapazi a mnyamata, amene dzina lake linali Saulo.
  4032. Act 7:59 Ndipo adamponya miyala Stefano, akuyitana pa [Mulungu], ndi kunena kuti, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.
  4033. Act 7:60 Ndipo iye adagwada pansi, nafuwula ndi mawu okwera, Ambuye, musawayikire tchimo ili kwa iwo. Ndipo m’mene adanena ichi, iye adagona tulo.
  4034. Act 8:1 Ndipo Saulo adalikuvomerezana nawo ku imfa yake. Ndipo pa nthawi imeneyo padali kuzunza kwakukulu kotsutsa mpingo umene udali mu Yerusalemu; ndipo iwo onse adabalalitsidwa mudera lalikulu m’mayiko a Yudeya ndi Samariya, kupatula atumwiwo.
  4035. Act 8:2 Ndipo anthu wopembedza adamtengera Stefano [kokamuyika iye], ndipo kulira [kwa maliro] kwakukulu kudachitika pa iye.
  4036. Act 8:3 Zokhudza Saulo, iye adawononga kwambiri mpingo, kulowa m’nyumba iliyonse, nakokamo mwachiwawa amuna ndi akazi nawayika [iwo] m’ndende.
  4037. Act 8:4 Choncho iwo wobalalitsidwa mudera lalikuluwo adapita kulikonse nalalikira mawuwo.
  4038. Act 8:5 Pamenepo Filipi adapita kutsikira ku mzinda wa Samariya, ndipo analalikira Khristu kwa iwo.
  4039. Act 8:6 Ndipo anthuwo ndi mtima umodzi adasamalira ku zinthu zimene Filipi adanena, kumva ndi kupenya zozizwa zimene iye adazichita.
  4040. Act 8:7 Pakuti mizimu yonyansa, yofuwula ndi mawu okwera, idatuluka mwa ambiri amene adali wogwidwa [ndi iyo]: ndipo ambiri a manjenje, ndi amene adali wolumala, adachiritsidwa.
  4041. Act 8:8 Ndipo padali chimwemwe chachikulu mu mzinda umenewo.
  4042. Act 8:9 Koma padali munthu wina, wotchedwa Simoni, amene kale mu mzinda womwewo adagwiritsa ntchito matsenga, ndi kuwalodza anthu a ku Samariya, ndi kunena kuti iye yekha adali wina wake wamkulu.
  4043. Act 8:10 Kwa iye amene onse adasamalira, kuyambira wam’ng’ono kufikira wamkulu, kunena kuti, Munthu uyu ndiye mphamvu yayikulu ya Mulungu.
  4044. Act 8:11 Ndipo kwa iye adapereka ulemu, chifukwa kwa nthawi yayitali adawalodza iwo ndi matsenga.
  4045. Act 8:12 Koma pamene adakhulupirira Filipi polalikira zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu, ndi dzina la Yesu Khristu, adabatizidwa iwo, amuna ndi akazi.
  4046. Act 8:13 Pamenepo Simoni mwini yekha adakhulupiriranso: ndipo m’mene adabatizidwa, adapitirira kukhala ndi Filipi, ndipo anadabwa; pakuwona zozizwa ndi zizindikiro zimene zidachitidwa.
  4047. Act 8:14 Tsopano pamene atumwi amene adali ku Yerusalemu adamva kuti Samariya adalandira mawu a Mulungu, adatumiza kwa iwo Petro ndi Yohane:
  4048. Act 8:15 Amene, m’mene iwo adatsika kubwerako, adapempherera iwo, kuti akhoze kulandira Mzimu Woyera.
  4049. Act 8:16 (Pakuti kufikira pamenepo nkuti asadagwere pa wina aliyense wa iwo: iwo adangobatizidwa kokha m’dzina la Ambuye Yesu.)
  4050. Act 8:17 Kenaka adayika manja [awo] pa iwo, ndipo adalandira Mzimu Woyera.
  4051. Act 8:18 Ndipo pamene Simoni adawona kuti mwa kuyika manja kwa atumwi Mzimu Woyera adapatsidwa, iye adatenga ndalama [kuti] awapatse.
  4052. Act 8:19 Kunena kuti, Ndipatseni inenso mphamvu yimeneyi, kuti pa wina aliyense amene ndikayika manja, iye akhoze kulandira Mzimu Woyera.
  4053. Act 8:20 Koma Petro adati kwa iye, Ndalama yako iwonongeke ndi iwe, chifukwa iwe walingalira kuti mphatso ya Mulungu ikhoza kugulidwa ndi ndalama.
  4054. Act 8:21 Iwe ulibe gawo kapena cholandira mu ichi: pakuti mtima wako si uli wolunjika pamaso pa Mulungu.
  4055. Act 8:22 Choncho lapa choyipa chako ichi, ndipo pemphera kwa Mulungu, kuti kapena cholingalira cha mtima wako chikhululukidwire iwe.
  4056. Act 8:23 Pakuti ine ndizindikira kuti iwe uli mu ndulu ya chowawa, ndipo [uli] m’nsinga ya chosalungama.
  4057. Act 8:24 Kenaka Simoni adayankha, ndipo anati, Mundipempherere inu kwa Ambuye chifukwa cha ine, kuti chilichonse cha zinthu izi mwanenazi zisandigwere ine.
  4058. Act 8:25 Ndipo iwo, pamene iwo adatha kuchita umboni ndi kulalika mawu a Ambuye, adabwerera [kumka] ku Yerusalemu, ndipo analalikira uthenga wabwino mu midzi yambiri ya Asamariya.
  4059. Act 8:26 Koma mngelo wa Ambuye adayankhula ndi Filipi, kunena kuti, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera ku njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kumka ku Gaza, imene ili chipululu cha mchenga.
  4060. Act 8:27 Ndipo adanyamuka ndi kupita: ndipo, tawonani, munthu wa ku Ethiyopiya, mdindo wa ulamuliro wamphamvu pansi pa Kandake mfumu yayikazi ya a Ethiyopiya, amene adali ndi ulamuliro pa chuma chake chonse, ndipo adadza ku Yerusalemu kudzalambira,
  4061. Act 8:28 Adali akubwerera, ndipo anakhala mu gareta wake akuwerenga Yesaya mneneri.
  4062. Act 8:29 Kenaka Mzimu adati kwa Filipi, Pita pafupi, ndipo udziphatike iwe wekha ku gareta uyu.
  4063. Act 8:30 Ndipo Filipi adathamangira kwa [iye], ndipo anamva iye ali kuwerenga mneneri Yesaya, ndipo adati, Kodi iwe uzindikira chimene iwe ukuwerenga?
  4064. Act 8:31 Ndipo iye adati, Ndingathe ine bwanji, pokhapokha munthu wina anditsogolere ine? Ndipo iye adapempha Filipi kuti iye akwere nakhala pansi ndi iye.
  4065. Act 8:32 Pa malo a malemba pamene adali kuwerengapo padali apa, Iye adatsogozedwa ngati nkhosa kukaphedwa; ndi monga mwana wankhosa ali du pamaso pa womsenga, kotero iye sadatsegula pakamwa pake:
  4066. Act 8:33 M’kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chidachotsedwa: ndipo ndani adzawubukitsa m’badwo wake? Pakuti moyo wake wachotsedwa ku dziko lapansi.
  4067. Act 8:34 Ndipo mdindo wa ulamuliro wamphamvuyo adayankha Filipi, ndipo anati, Ndikupemphani inu, za yani ichi anena mneneri? Za iye yekha, kapena za munthu wina?
  4068. Act 8:35 Kenaka Filipi adatsegula pakamwa pake, ndipo anayamba pa lembo lomweri, ndipo analalikira kwa iye Yesu.
  4069. Act 8:36 Ndipo pamene iwo adapita panjira [pawo], iwo adadza kumadzi ena: ndipo mdindoyo adati, Tawona, [pano pali] madzi; kodi chindiletsa ine ndi chiyani kuti ndibatizidwe?
  4070. Act 8:37 Ndipo Filipi adati, Ngati iwe ukhulupirira ndi mtima wako wonse, iwe ukhoza. Ndipo iye adayankha ndi kunena, Ine ndikhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  4071. Act 8:38 Ndipo iye adalamula kuti gareta liyime: ndipo iwo adatsika onse awiri kulowa m’madzi, Filipi ndi mdindoyo; ndipo adam’batiza iye.
  4072. Act 8:39 Ndipo pamene adakwera kutuluka m’madzi, Mzimu wa Ambuye adakwatula Filipi, [kotero] kuti mdindoyo sadamuwonanso iye: ndipo iye adapita njira yake akukondwera.
  4073. Act 8:40 Koma Filipi adapezedwa ku Azotasi: ndipo popyola adalalikira mu mizinda yonse, kufikira iye adadza ku Kayisareya.
  4074. Act 9:1 Ndipo Saulo, wosaleka kupumira ziwopsezo ndi kupha pa akuphunzira a Ambuye, adanka kwa mkulu wansembe.
  4075. Act 9:2 Ndipo anapempha kwa iye makalata akunka nawo ku Damasikasi ku masunagoge, kuti akapeza ena a njira iyi, kapena anali amuna kapena akazi, iye akhoza kuwabweretsa womangidwa ku Yerusalemu.
  4076. Act 9:3 Ndipo pamene iye anali kuyenda ulendo, adayandikira Damasikasi: ndipo mwadzidzidzi padawala momuzungulira iye kuwunika kochokera kumwamba:
  4077. Act 9:4 Ndipo iye adagwera pansi, ndipo anamva mawu akunena kwa iye, Saulo, Saulo, chifukwa chiyani iwe undinzunza ine?
  4078. Act 9:5 Ndipo iye adati, Ndinu yani, Ambuye? Ndipo Ambuye adati, Ine ndine Yesu amene iwe umzunza: [kuli] kovuta kwa iwe kuti ulimbane ndi zisonga.
  4079. Act 9:6 Ndipo iye akunthunthumira ndiponso kudabwa anati, Ambuye, kodi mufuna kuti ndichite chiyani? Ndipo Ambuye [adati] kwa iye, Uka, ndipo ulowe mu mzinda, ndipo chidzanenedwa kwa iwe chimene iwe uyenera kuchita.
  4080. Act 9:7 Ndipo amunawo amene adayenda naye pamodzi iye adayima du, anamva mawu, koma osawona munthu.
  4081. Act 9:8 Ndipo Saulo adawuka kuchoka pansi; ndipo pamene maso ake adatseguka, iye sadapenya munthu aliyense: koma adamtsogolera ndi dzanja, ndipo anabweretsa [iye] kulowa naye m’Damasikasi.
  4082. Act 9:9 Ndipo adakhala masiku atatu wosawona, ndipo sadadya kapena kumwa.
  4083. Act 9:10 ¶Ndipo kudali wophunzira wina ku Damasikasi dzina lake Ananiyasi; ndipo kwa iye adati Ambuye m’masomphenya, Ananiyasi. Ndipo iye adati, Tawonani, Ine [ndiri pano], Ambuye.
  4084. Act 9:11 Ndipo Ambuye [adati] kwa iye, Uka, ndipo pita ku khwalala limene litchedwa Lolunjika, ndipo ufunse m’nyumba ya Yudasi za [wina] wotchedwa Saulo, wa ku Tarsasi; pakuti, tawona, ali kupemphera,
  4085. Act 9:12 Ndipo wawona m’masomphenya munthu wamwamuna dzina lake Ananiyasi ali kulowa, ndi kuyika dzanja [lake] pa iye, kuti alandire kupenyanso kwake.
  4086. Act 9:13 Kenaka Ananiyasi adayankha, Ambuye, ine ndamva ndi ambiri za munthu uyu, momwe adachitiradi choyipa chachikulu kwa woyera mtima anu ku Yuraselemu.
  4087. Act 9:14 Ndipo pano iye ali nawo ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuyitana pa dzina lanu.
  4088. Act 9:15 Koma Ambuye adati kwa iye, Pita panjira yako: pakuti ali chotengera chosankhika kwa ine, chakunyamula dzina langa pamaso pa anthu Amitundu, ndi mafumu, ndi ana a Israyeli.
  4089. Act 9:16 Pakuti ine ndidzamuwonetsa iye zinthu zazikulu zimene ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.
  4090. Act 9:17 Ndipo Ananiyasi adapita panjira yake, ndipo analowa m’nyumbayo; ndipo atayika manja ake pa iye anati, Mbale Saulo, Ambuye, [inde] Yesu, amene adawonekera kwa iwe panjira pamene iwe unkabwera, wandituma ine, kuti iwe ukhoze kulandira kuwona kwako, ndi kuti udzazidwe ndi Mzimu Woyera.
  4091. Act 9:18 Ndipo nthawi yomweyo padagwa kuchokera m’maso mwake monga adali mamba: ndipo adalandira kuwona nthawi yomweyo, ndipo adawuka, ndipo anabatizidwa.
  4092. Act 9:19 Ndipo pamene iye atalandira chakudya, iye anakhala ndi mphamvu. Kenaka Saulo adakhala pamodzi ndi akuphunzira amene adali ku Damasikasi masiku angapo.
  4093. Act 9:20 Ndipo nthawi yomweyo iye adalalikira Khristu m’masunagoge, kuti iye ali Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  4094. Act 9:21 Koma onse amene adamva [iye] anadabwa, ndipo ananena; Si ali uyu iye amene adawononga iwo amene adayitana pa dzina lomweri m’Yerusalemu, ndipo anadza kuno chifukwa cha cholinga chimenecho, kuti akhoze kubweretsa iwo womangidwa kwa ansembe akulu?
  4095. Act 9:22 Koma Saulo adakulabe kwambiri mu mphamvu, ndipo anadodometsa Ayuda amene amakhala ku Damasikasi, kuwatsimikizira kuti uyu ndi Khristu amene.
  4096. Act 9:23 ¶Ndipo pambuyo pakuti masiku ambiri atakwaniritsidwa, Ayuda adatenga uphungu wakuti amuphe iye:
  4097. Act 9:24 Koma chiwembu chawo chidadziwika kwa Saulo. Ndipo iwo anamdikiriranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe iye.
  4098. Act 9:25 Kenaka wophunzira adamtenga iye usiku, ndipo anamtsitsira [iye] pakhoma la linga m’dengu.
  4099. Act 9:26 Ndipo pamene Saulo adabwera ku Yerusalemu, adayesa kudziphatika kwa wophunzira: koma iwo onse adali ndi mantha ndi iye, ndipo sadakhulupirira kuti iye adali wophunzira.
  4100. Act 9:27 Koma Baranabas adamtenga iye, ndipo anambweretsa [iye] kwa atumwi, ndipo anawafotokozera umo iye adawonera Ambuye m’njira, ndi kuti iye adayankhula kwa iye, ndi momwe iye adalalikira molimba mtima m’Damasikasi m’dzina la Yesu.
  4101. Act 9:28 Ndipo iye adali ndi iwo kulowa ndi kutuluka ku Yerusalemu.
  4102. Act 9:29 Ndipo iye adayankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye Yesu, ndipotu adayankhula natsutsana ndi Ahelene: koma adayendayenda kufuna kumupha iye.
  4103. Act 9:30 [Chimene] pomwe abale adachidziwa, adambweretsa iye kutsikira ku Kayisareya, ndipo anamtumiza apite kumka ku Tarsasi.
  4104. Act 9:31 Kenaka kudakhala mpumulo m’mipingo ya m’Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya, ndipo idakhala yolimbikitsidwa; ndipo poyenda m’kuwopa kwa Ambuye, ndi m’chitonthozo cha Mzimu Woyera, idachulukitsidwa.
  4105. Act 9:32 ¶Ndipo kudachitika, pamene Petro amapita [pamalo] aliwonse, iye adabweranso kutsikira kwa woyera mtima amene ankakhala ku Lidda.
  4106. Act 9:33 Ndipo kumeneko iye adapeza munthu wina dzina lake Eneyasi, amene adagona pa kama wake zaka zinasu ndi zitatu: amene adali wodwala matenda akufa ziwalo.
  4107. Act 9:34 Ndipo Petro adati kwa iye, Eneyasi, Yesu Khristu akuchiritsa iwe: yimirira, ndipo konza kama wako. Ndipo adayimirira nthawi yomweyo.
  4108. Act 9:35 Ndipo onse akukhala ku Lidda ndi ku Saroni adamuwona iye, ndipo anatembenukira kwa Ambuye.
  4109. Act 9:36 ¶Tsopano kudali ku Yopa wophunzira wina dzina lake Tabita, limene potanthawuzidwa litchedwa Dorkasi: mkazi uyu adali wodzala ndi ntchito zabwino ndi za chifundo zimene adazichita.
  4110. Act 9:37 Ndipo kudachitika m’masiku awo, kuti iye adadwala, ndipo anamwalira: amene pamene anamsambitsa, adamgoneka [iye] m’chipinda chapamwamba.
  4111. Act 9:38 Ndipo popeza kuti Lidda adali pafupi ndi Yopa, ndipo wophunzira adamva kuti Petro adali kumeneko, adatumiza kwa iye anthu awiri, kukhumba [iye] kuti asachedwe kudza kwa iwo.
  4112. Act 9:39 Ndipo Petro adanyamuka ndipo anapita nawo limodzi. M’mene iye adabwera, adambweretsa iye m’chipinda chapamwamba: ndipo amayi amasiye onse adayimirirapo pali iye akulira, ndi kuwonetsa malaya ndi zovala zimene Dorkasi adasoka, pamene adali pamodzi ndi iwo.
  4113. Act 9:40 Koma Petro adawatulutsa onse, ndipo anagwada pansi, ndipo anapemphera; ndipo potembenukira [iye] kumtembo adati, Tabita, uka. Ndipo adatsegula maso ake: ndipo pamene adawona Petro, adakhala tsonga.
  4114. Act 9:41 Ndipo iye adampatsa dzanja lake [nam’gwira], ndipo anam’nyamutsa, ndipo m’mene adayitana woyera mtima ndi amayi amasiye, adampereka iye wamoyo.
  4115. Act 9:42 Ndipo chidadziwika ku Yopa konse; ndipo ambiri adakhulupirira mwa Ambuye.
  4116. Act 9:43 Ndipo kudachitika, kuti adakhala iye masiku ambiri m’Yopa ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.
  4117. Act 10:1 Kudali munthu ku Kayisareya, wotchedwa Korneliyasi, kenturiyoni wa gulu lotchedwaChiitale,
  4118. Act 10:2 [Munthu] wopembedza, ndipo anali m’modzi wakuwopa Mulungu ndi nyumba yake yonse, amene adapatsa za chifundo zambiri kwa anthu, ndipo anapemphera kwa Mulungu nthawi zonse.
  4119. Act 10:3 Iye adapenya masomphenya bwino lomwe ngati ora lachisanu ndi chinayi la usana mngelo wa Mulungu alinkudza kulowa kwa iye, ndi kunena kwa iye, Korneliyasi.
  4120. Act 10:4 Ndipo pamene anampenya iye, anachita mantha, ndipo adati, N’chiyani, Ambuye? Ndipo iye adati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zakwera kukhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
  4121. Act 10:5 Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, ndi kuyitana [m’modzi] Simoni, amene atchedwanso Petro:
  4122. Act 10:6 Iye akukhala ndi wina Simoni wofufuta zikopa, amene nyumba yake ili m’mbali mwa nyanja: iye adzakuwuza iwe chimene uyenera kuchita.
  4123. Act 10:7 Ndipo m’mene mngelo amene adayankhula ndi Korneliyasi adanyamuka, iye adayitana awiri a antchito ake, ndi msirikali wopembedza wa iwo amene ankamtumikira kosalekeza;
  4124. Act 10:8 Ndipo m’mene iye adafotokoza zinthu [izi] zonse kwa iwo, iye adawatuma ku Yopa.
  4125. Act 10:9 ¶Pa tsiku lotsatira, ali kupita pa ulendo wawo, ndipo adayandikira mzindawo, Petro adakwera padenga pa nyumba kukapemphera ngati ora la chisanu ndi chimodzi;
  4126. Act 10:10 Ndipo adamva njala kwambiri, ndipo adafuna atadya: koma m’mene adalikukonza [chakudya], iye adagwa ngati m’komoka;
  4127. Act 10:11 Ndipo anawona kumwamba kutatseguka, ndipo chotengera china chake chilinkutsikira kwa iye, chonga ngati chinsalu chachikulu cholumikizika pangodya zake zinayi, ndi kutsikira pa dziko lapansi:
  4128. Act 10:12 M’menemo mudali nyama za miyendo inayi za mitundu yonse za dziko lapansi, ndi nyama zakuthengo, ndi zinthu zokwawa, ndi mbalame za m’lengalenga.
  4129. Act 10:13 Ndipo padadza mawu kwa iye, Tayimirira, Petro, ipha, ndi kudya.
  4130. Act 10:14 Koma Petro adati, Iyayitu, Ambuye; pakuti sindidadye ine ndi kale lonse kanthu ka wamba kapena kodetsedwa.
  4131. Act 10:15 Ndipo mawu [adalankhulanso] kwa iye nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu wayeretsa, [chimenecho] usatchula chinthu wamba.
  4132. Act 10:16 Ichi chidachitika kachitatu: ndipo chotengeracho chidalandiridwanso kulowa kumwamba.
  4133. Act 10:17 Tsopano pamene Petro podabwa mwa yekha chimene masomphenya awa adawawona ayenera kutanthawuza chiyani, tawonani, amuna amene adatumidwa ndi Korneliyasi adali atafunsira za nyumba ya Simoni, adayima pamaso pa chipata.
  4134. Act 10:18 Ndipo adayitana, ndipo anafunsa ngati Simoni, amene adali wotchedwanso Petro, adalikukhala kumeneko.
  4135. Act 10:19 ¶Pamene Petro adali kulingalira pa masomphenya, Mzimu adanena kwa iye, Tawona, amuna atatu akufuna iwe.
  4136. Act 10:20 Choncho imirira, ndipo iwe utsike, ndipo upite ndi iwo, wosakayika kena kalikonse: pakuti ine ndawatuma iwo.
  4137. Act 10:21 Kenaka Petro adatsikira kwa anthuwo amene adatumizidwa kwa iye kuchokera kwa Korneliyasi; ndipo anati, Tawonani, ine ndine amene inu mumfuna: kotero [ndi] chiyani chimene inu mwadzera?
  4138. Act 10:22 Ndipo iwo adati, Korneliyasi, kenturiyoniyo, munthu wolungama, ndi m’modzi amene awopa Mulungu, ndi wa mbiri yabwino pakati pa fuko lonse la Ayuda, adachenjezedwa kuchokera kwa Mulungu mwa mngelo woyera kuti atumize kwa inu [nakuyitaneni] mumuke ku nyumba yake, ndi kuti amve mawu a inu.
  4139. Act 10:23 Kenaka iye adawalowetsa iwo, ndipo anawachereza [iwo], ndipo tsiku lotsatira Petro adanyamuka napita ndi iwo, ndi ena a abale ochokera ku Yopa adamperekeza iye.
  4140. Act 10:24 Ndipo tsiku lotsatira iwo atalowa m’Kayisareya. Ndipo Korneliyasi adalikudikira iwo, ndipo adayitana pamodzi abale ake eni eni ndi abwenzi apafupi.
  4141. Act 10:25 Ndipo pamene Petro amalowa, Korneliyasi adakomana ndi iye, ndipo anagwa pa mapazi ake, ndipo anamlambira [iye].
  4142. Act 10:26 Koma Petro adamuwutsa iye, kunena, Imirira; ine ndinenso munthu.
  4143. Act 10:27 Ndipo pamene ankakamba ndi iye, iye adalowa, ndipo anapeza ambiri amene adasonkhana pamodzi;
  4144. Act 10:28 Ndipo iye adati kwa iwo, Inu mudziwa kuti ndi chinthu chakuswa lamulo kwa munthu amene ali Myuda akhale pamodzi, kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu adandiwonetsera ine kuti ndisatchule aliyense ali munthu wamba kapena wodetsedwa.
  4145. Act 10:29 Choncho ine ndadza [kwa inu] wosakana, nthawi yomweyo m’mene mudanditumizira ine kundiyitana: Ine choncho ndinafunsa za cholinga chimene inu mwandiyitanira ine?
  4146. Act 10:30 Ndipo Korneliyasi adati, Masiku anayi apitawa ine ndidali kusala chakudya kufikira ora ili; ndipo pa ora la chisanu ndi chinayi ine ndinapemphera m’nyumba yanga; ndipo, tawonani, munthu adayimirira pamaso panga wovala chovala chonyezimira.
  4147. Act 10:31 Ndipo adati, Korneliyasi, pemphero lako lamveka, ndipo zopereka zachifundo zako ziri zokumbukirika pamaso pa Mulungu.
  4148. Act 10:32 Choncho tumiza anthu ku Yopa, ndi kuyitanira kuno Simoni, amene wotchedwanso Petro; iye acherezedwa m’nyumba ya [wina] Simoni wofufuta zikopa m’mbali mwa nyanja: amene, pamene adza, adzayankhula kwa iwe.
  4149. Act 10:33 Choncho nthawi yomweyo ndidatumiza kwa inu; ndipo inu mwachita bwino kuti mwadza. Choncho tsopano ife tiri tonse pano pamaso pa Mulungu, kuti timve zinthu zonse zimene mwalamulidwa inu ndi Mulungu.
  4150. Act 10:34 ¶Kenaka Petro adatsegula pakamwa [pake], ndipo anati, Zowona ine ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu pakati pa anthu:
  4151. Act 10:35 Koma m’mitundu yonse iye amene wakumuwopa iye, ndi kuchita chilungamo, ali wolandiridwa ndi iye.
  4152. Act 10:36 Mawu amene [Mulungu] adatumiza kwa ana a Israyeli, kulalikira mtendere mwa Yesu Khristu: (ali Ambuye wa onse:)
  4153. Act 10:37 Mawu amenewo, [Ine ndinena], inu muwadziwa, amene adamvekawo mu Yudeya yense, ndipo adayambira ku Galileya, pambuyo pa ubatizo umene Yohane adawulalikira;
  4154. Act 10:38 Momwe Mulungu adamdzodzera Yesu wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu: amene adapitapita kuchita zabwino, ndi kuchiritsa onse wosawutsidwa ndi mdiyerekezi; pakuti Mulungu anali ndi iye.
  4155. Act 10:39 Ndipo ife tiri mboni za zinthu zonse zimene iye adazichita m’dziko la Ayuda, ndi m’Yerusalemu; amene iwo adamupha ndi kumpachika pa mtengo:
  4156. Act 10:40 Iye Mulungu adamuwukitsa tsiku la chitatu, ndi kuwonetsera iye poyera;
  4157. Act 10:41 Osati kwa anthu onse, koma kwa mboni zosankhidwiratu kale ndi Mulungu, [ngakhale] kwa ife, amene tinadya ndi kumwa ndi iye pamodzi atawuka iye kwa akufa.
  4158. Act 10:42 Ndipo adatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu, ndi kuti tichitire umboni kuti ali iye amene adayikidwa ndi Mulungu [kuti] akhale Woweruza amoyo ndi akufa.
  4159. Act 10:43 Kwa iye aneneri onse aperekera umboni, kuti kudzera m’dzina lake aliyense amene akhulupirira mwa iye adzalandira chikhululukiro cha machimo.
  4160. Act 10:44 ¶Pamene Petro adali chiyankhulire mawu awa, Mzimu Woyera adagwa pa onse amene adamva mawuwo.
  4161. Act 10:45 Ndipo iwo onse akumdulidwe amene adakhulupirira adadabwa, ambiri amene adadza ndi Petro, chifukwa chakuti pa Amitundunso padathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.
  4162. Act 10:46 Pakuti iwo adawamva iwo alikuyankhula ndi malirime, ndi kumkuza Mulungu. Kenaka adayankha Petro,
  4163. Act 10:47 Kodi munthu wina aliyense angaletse madzi, kuti awa asabatizidwe, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?
  4164. Act 10:48 Ndipo iye adalamulira iwo kuti abatizidwe m’dzina la Ambuye. Kenaka adampempha iye kuti atsotse masiku angapo.
  4165. Act 11:1 Ndipo atumwi ndi abale amene adali m’Yudeya adamva kuti Amitundunso adalandira mawu a Mulungu.
  4166. Act 11:2 Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo amene adali akumdulidwe adatsutsana ndi iye.
  4167. Act 11:3 Kunena kuti, Iwe udalowa kwa anthu wosadulidwa, ndipo udadya ndi iwo.
  4168. Act 11:4 Koma Petro adawafotokozera [nkhani iyi], kuyambira poyambira, ndipo anayilongosola [iyo] mwa ndondomeko kwa iwo, kunena kuti,
  4169. Act 11:5 Ine ndidali mu mzinda wa Yopa ndikupemphera: ndipo mkukomoka ine ndidawona masomphenya, Chotengera china chake chilikutsika, chidali monga ngati chinsalu chachikulu, chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa pa ngodya zake zinayi; ndipo chidadza ngakhale kwa ine.
  4170. Act 11:6 Chimenecho pa kuchipenyetsetsa maso anga, ine ndidalingalira, ndipo ndidawona nyama za miyendo inayi za padziko lapansi, ndi nyama zakuthengo, ndi zinthu zokwawa, ndi mbalame za mlengalenga.
  4171. Act 11:7 Ndipo ine ndidamva mawu akunena kwa ine, Imirira, Petro; ipha ndipo udye.
  4172. Act 11:8 Koma ine ndinati, Iyayitu, Ambuye: pakuti palibe kanthu wamba kapena kodetsedwa pa nthawi ina iliyonse kadalowa mkamwa mwanga.
  4173. Act 11:9 Koma mawu adandiyankhanso ine kuchokera kumwamba, Chimene Mulungu wayeretsa, [chimenecho] usatchule iwe chinthu wamba.
  4174. Act 11:10 Ndipo ichi chidachitika katatu: ndipo zidakwezedwanso zonse kupita kumwamba.
  4175. Act 11:11 Ndipo, tawonani, posakhalitsa padali amuna atatu atabwera kale ku nyumba kumene ine ndidali, adatumidwa kwa ine kuchokera ku Kayisareya.
  4176. Act 11:12 Ndipo Mzimu adandiwuza ndinke nawo, wosakayika kalikonse. Kuwonjezera apo abale awa asanu ndi m’modzi adamuka nane; ndipo tidalowa m’nyumba ya bamboyo:
  4177. Act 11:13 Ndipo adatiwuza ife momwe iye adamuwonera mngelo m’nyumba yake, amene adayimirira ndi kunena kwa iye, Tuma anthu ku Yopa, ndipo akayitane Simoni, amene wotchedwanso Petro;
  4178. Act 11:14 Amene adzakuwuza iwe mawu, amene iwe ndi nyumba yako yonse udzapulumutsidwa nawo.
  4179. Act 11:15 Ndipo m’mene ndidayamba kuyankhula, Mzimu Woyera adagwera pa iwo, monga pa ife pachiyambi paja.
  4180. Act 11:16 Kenaka ine ndidakumbukira mawu a Ambuye, momwe iye adanena, Yohane inde anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.
  4181. Act 11:17 Pakuti ngati tsono pamenepo Mulungu adawapatsa iwo mphatso yofanana yomweyi monga [iye adachita] kwa ife, amene adakhulupirira pa Ambuye Yesu Khristu; ndinali yani ine, kuti ndingathe kuletsa Mulungu?
  4182. Act 11:18 Pamene iwo adamva zinthu izi, iwo adakhala du, napereka ulemerero kwa Mulungu, kunena kuti, Potero Mulungu wapatsa kutembenuka kumoyo kwa Amitundunso.
  4183. Act 11:19 ¶Tsopano iwo amene adali wobalalikawo kunjakutali pa chizunzocho chimene chidabuka pa Stefano adayenda kufikira ngati ku Fenisi, ndi Sayipulasi, ndi Antiyoki, kulalikira mawu osati kwa wina yense koma kwa Ayuda wokhawokha.
  4184. Act 11:20 Ndipo ena a iwo adali amuna aku Sayipulasi ndi Sayirene, amene, m’mene adafika ku Antiyoki, adayankhula kwa Ahelene, kulalikira Ambuye Yesu.
  4185. Act 11:21 Ndipo dzanja la Ambuye lidali ndi iwo: ndi chiwerengero chachikulu chidakhulupirira, ndi kutembenukira kwa Ambuye.
  4186. Act 11:22 ¶Kenaka mbiri ya zinthu izi idamveka m’makutu a mpingo umene udali m’Yerusalemu: ndipo adatuma Barnabas, apite mpaka kufikira ku Antiyoki.
  4187. Act 11:23 Amene, m’mene adabwera, ndi pomwe anawona chisomo cha Mulungu, adakondwera; ndipo adawadandawulira onse, kuti ndi kutsimikiza kwa mtima iwo afune kumamatira kwa Ambuye.
  4188. Act 11:24 Pakuti adali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidawonjezeka kwa Ambuye.
  4189. Act 11:25 Kenaka Barnabas adanyamuka kumka ku Tarsasi, chifukwa cha kukafunafuna Saulo:
  4190. Act 11:26 Ndipo m’mene adampeza iye, iye adabweretsa iye ku Antiyoki. Ndipo kudachitika, kuti chaka chonse adasonkhana pamodzi ndi mpingo, ndipo anaphunzitsa anthu aunyinji. Ndipo wophunzira adatchedwa Akhristu koyamba mu Antiyoki.
  4191. Act 11:27 ¶Ndipo m’masiku awa adadza aneneri kochokera ku Yerusalemu kunka ku Antiyoki.
  4192. Act 11:28 Ndipo adayimirira m’modzi wa iwo, dzina lake Agabasi, ndipo anatanthawuzira mwa Mzimu kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse: imene idachitika m’masiku a Klaudiyasi Kayisara.
  4193. Act 11:29 Kenaka wophunzira, munthu aliyense monga mwa kuthekera kwake, adatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale amene amakhala m’Yudeya:
  4194. Act 11:30 Chimene iwonso adachita, ndipo anatumiza kwa akulu mwa manja a Barnabas ndi Saulo.
  4195. Act 12:1 Tsopano pa nthawi imeneyo Herode mfumuyo adatambasula manja [ake] kuwachitira zoyipa ena a mu mpingo.
  4196. Act 12:2 Ndipo adapha Yakobo mbale wa Yohane ndi lupanga.
  4197. Act 12:3 Ndipo chifukwa chakuti anawona kuti chidakondweretsa Ayuda, adapitirira mtsogolo kutenganso Petro. (Awo adali masiku a mkate wopanda chofufumitsa).
  4198. Act 12:4 Ndipo m’mene iye adamgwira iye, iye adamuyika [iye] m’ndende, ndipo anampereka [iye] kwa magulu anayi a alonda, amsunge iye; kulinga kuti atapita Paskha amtulutse kudza ndi iye kwa anthu.
  4199. Act 12:5 Choncho Petro adasungidwa m’ndende: koma pemphero lidachitika kosalekeza ndi mpingo kwa Mulungu chifukwa cha iye.
  4200. Act 12:6 Ndipo pamene Herode adayenera kuti amtulutse, usiku womwewo Petro adalikugona pakati pa asirikali awiri, womangidwa ndi unyolo uwiri: ndipo alonda wokhala pamaso pa khomo adadikira ndende.
  4201. Act 12:7 Ndipo, tawonani, mngelo wa Ambuye adadza pa [iye], ndipo kuwunika kudawala m’ndendemo: ndipo adamenya Petro m’mbali, ndipo anamuwutsa iye, kunena kuti, Tayimirira msanga. Ndipo unyolo wake udagwa kuchoka m’manja [mwake].
  4202. Act 12:8 Ndipo mngelo adati kwa iye, Dzimangire wekha [m’chiwuno], ndipo umange nsapato zako. Ndipo chotero anachita. Ndipo iye adanena kwa iye, Ponya chovala chako mozungulira iwe, ndipo unditsate ine.
  4203. Act 12:9 Ndipo iye adatuluka, ndipo anamtsata iye; ndipo sadadziwa kuti chinali chowona cimene chinachitidwacho ndi mngelo; koma adaganiza kuti iye anawona masomphenya.
  4204. Act 12:10 Ndipo m’mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, iwo adadza ku chipata chachitsulo chakuyang’ana mu mzinda; chimene chidawatsegukira iwo mwa icho chokha: ndipo iwo adatuluka, ndipo anapitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo adachoka kwa iye.
  4205. Act 12:11 Ndipo Petro atabwerera ku umunthu wake, iye adati, Tsopano ndidziwa mwa zowona, kuti Ambuye watuma mngelo wake, ndipo walanditsa ine m’dzanja la Herode, ndi [kuchoka] ku chiyembekezo chonse cha anthu a Chiyuda.
  4206. Act 12:12 Ndipo m’mene adalingalira [chinthuchi], adadza ku nyumba ya Mariya amayi wake a Yohane, wotchedwanso Mariko; kumene ambiri adasonkhana pamodzi kupemphera.
  4207. Act 12:13 Ndipo pamene Petro ankagogoda pa chitseko cha chipata, adadza mtsikana kudzavomera, dzina lake Rhoda.
  4208. Act 12:14 Ndipo pamene adazindikira mawu a Petro, iye sadatsegula pakhomo chifukwa cha kukondwera, koma adathamanga kulowa, ndipo anawawuza momwe Petro anali kuyimira pamaso pa chipata.
  4209. Act 12:15 Koma iwo adati kwa iye, Iwe uli wamisala. Koma adalimbika kutsimikiza kuti zinali motero. Kenaka adanena iwo, Ali mngelo wake.
  4210. Act 12:16 Koma Petro adapitiriza kugogoda: ndipo m’mene adatsegula [chitsekocho], ndi kumuwona iye, iwo anadabwa.
  4211. Act 12:17 Koma iye, pokukodola kwa iwo ndi dzanja kuti akhale chete, adafotokozera iwo umo adamtulutsira Ambuye iye m’ndende. Ndipo iye adati, Pitani muwonetse zinthu izi kwa Yakobo, ndi kwa abale. Ndipo iye adanyamuka, ndipo anapita ku malo ena.
  4212. Act 12:18 Tsopano pamene kutangocha, padali phokoso lalikulu pakati pa asirikali, pa za chimene chidachitika kwa Petro.
  4213. Act 12:19 Ndipo pamene Herode adamfunafuna iye, ndipo wosampeza iye, iye adafunsitsa wodikira, ndipo analamulira kuti [iwo] aphedwe. Ndipo adatsikira kuchokera ku Yudeya kumka ku Kayisareya, ndipo anakhalabe [kumeneko].
  4214. Act 12:20 ¶Ndipo Herode adayipidwa ndi iwo kwakukulu a ku Turo ndi Sidoni: koma iwo anadza ndi mtima umodzi kwa iye, ndipo, m’mene adampanga Blastasi mdindo woyang’anira nyumba ya mfumu bwenzi lawo, adapempha mtendere; chifukwa dziko lawo lidapeza zakudya zochokera ku [dziko] la mfumu.
  4215. Act 12:21 Ndipo pa tsiku loyikika Herode, atavala zovala zachifumu, anakhala pa mpando wake wachifumu, ndipo anafotokoza mawu kwa iwo.
  4216. Act 12:22 Ndipo anthuwo adafuwula, [kunena kuti, ali] mawu a mulungu, osati a munthu.
  4217. Act 12:23 Ndipo posakhalitsa mngelo wa Ambuye adamkantha iye, chifukwa sadampatsa Mulungu ulemerero: ndipo adadyedwa ndi mphutsi, ndipo anamwalira.
  4218. Act 12:24 ¶Koma mawu a Mulungu adakula ndi kuchuluka.
  4219. Act 12:25 Ndipo Barnabas ndi Saulo adabwerera kuchokera ku Yerusalemu, m’mene adakwaniritsa utumiki [wawo], ndipo anatenga pamodzi ndi iwo Yohane, wotchedwanso Mariko.
  4220. Act 13:1 Tsopano kudali mu Mpingo wa ku Antiyoki aneneri ndi aphunzitsi ena ake, ngati Barnabas, ndi Simeoni amene wotchedwanso Nigeri, ndi Lisiyasi wa ku Sayirene, ndi Manayeni, amene adaleredwa ndi Herode woyang’anira gawo lachinayi la dziko, ndi Saulo.
  4221. Act 13:2 Pamene iwowa ankatumikira kwa Ambuye, ndipo anasala chakudya, Mzimu Woyera adati, Mundipatulire ine Barnabas ndi Saulo chifukwa cha ntchito imene ine ndawayitanira iwo.
  4222. Act 13:3 Ndipo pamene adasala chakudya ndi kupemphera, ndi kuyika manja [awo] pa iwo, adawatumiza [iwo] amuke.
  4223. Act 13:4 ¶Chotero iwo, wotumizidwa ndi Mzimu Woyera, adanyamuka kulowa mu Selukiya; ndipo kuchokera kumeneko adayenda m’chombo [kupita] ku Sayipulasi.
  4224. Act 13:5 Ndipo pamene adali ku Salamisi, adalalikira mawu a Mulungu m’masunagoge a Ayuda: ndipo adali nayenso Yohane monga wakuwatumikira [iwo].
  4225. Act 13:6 Ndipo m’mene adapitirira chisumbu nafika ku Pafosi, iwo adapezako munthu wamatsenga wina wake, mneneri wonyenga, Myuda, amene dzina lake linali Baryesu:
  4226. Act 13:7 Amene adali ndi wachiwiri kwa [kazembe], Sergiyasi Paulasi, munthu wanzeru; amene adayitana Barnabas ndi Saulo, ndipo anafunitsa kumva mawu a Mulungu.
  4227. Act 13:8 Koma Elimasi wamatsengayo (pakuti dzina lake litanthawuzidwa motero) adatsutsana ndi iwo, kufuna kupatutsa wachiwiri kwa [kazembe] kuchikhulupiriro.
  4228. Act 13:9 Kenaka Saulo, (amene [wotchedwanso] Paulo,) wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, maso ake adapenyetsetsa iye.
  4229. Act 13:10 Ndipo adati, Wodzala ndi kuchenjera ndi chinyengo chonse, [iwe] mwana wa mdierekezi, [iwe] mdani wa chilungamo chonse, kodi iwe sudzaleka kuyipsa njira zolondola za Ambuye?
  4230. Act 13:11 Ndipo tsopano, tawona, dzanja la Ambuye [liri] pa iwe, ndipo iwe udzakhala wakhungu, wosapenya dzuwa kwa nyengo. Ndipo posakhalitsa lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo adamukamuka nafuna ena kuti amtsogolere pomgwira dzanja.
  4231. Act 13:12 Kenaka wachiwiri kwa [kazembe], pamene anawona chimene chinachitidwacho, adakhulupirira, pokhala wodabwa pa chiphunzitso cha Ambuye.
  4232. Act 13:13 Tsopano pamene Paulo ndi gulu lake adamasuka kuchokera ku Pafosi, iwo adafika ku Perga wa ku Pamfiliya: ndipo Yohane ponyamuka kuchokera kwa iwo anabwerera ku Yerusalemu.
  4233. Act 13:14 ¶Koma pamene iwowa adanyamuka ku Perga, iwo adabwera ku Antiyoki wa m’Pisidiya, ndipo adalowa m’sunagoge tsiku la sabata, ndipo anakhala pansi.
  4234. Act 13:15 Ndipo m’mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge adatuma kwa iwo, kunena kuti, [Inu] amuna [ndi] abale, ngati muli ndi mawu ena aliwonse a kulimbikitsa kwa anthu, nenani.
  4235. Act 13:16 Kenaka Paulo adayimirira, ndipo anakodola ndi dzanja [lake] anati, Amuna a Israyeli, ndi inu amene muwopa Mulungu, mverani.
  4236. Act 13:17 Mulungu wa anthu awa a Israyeli adasankha makolo athu, ndipo anakweza anthuwo pamene adagonera iwo m’dziko la Igupto, ndipo ndi dzanja lokwezeka iye adawatulutsa iwo m’menemo.
  4237. Act 13:18 Ndipo nthawi ya pafupifupi zaka makumi anayi iye adalekerera mchitidwe wawo m’chipululu.
  4238. Act 13:19 Ndipo m’mene adawononga mafuko a anthu asanu ndi awiri a Kanani, iye adawapatsa dziko lawo kwa iwo pakuchita mayere.
  4239. Act 13:20 Ndipo zitatha izi adawapatsa [iwo], woweruza kwa zaka pafupifupi mazana anayi kudza makumi asanu, kufikira Samueli mneneriyo.
  4240. Act 13:21 Ndipo kuyambira pamenepo adapempha mfumu: ndipo Mulungu adapereka kwa iwo Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Banjamini, kwa mpata wa zaka makumi anayi.
  4241. Act 13:22 Ndipo pamene iye adamchotsa iye, iye adawutsira kwa iwo Davide kuti akhale mfumu yawo; kwa iyenso adaperekera umboni, ndipo anati, Ine ndapeza Davide [mwana wamwamuna] wa Jese, munthu wa pa mtima panga, amene adzakwaniritsa chifuniro changa chonse.
  4242. Act 13:23 Kwa mbewu ya munthu uyu Mulungu monga mwa lonjezano [lake] wawutsira kwa Isayeli Mpulumutsi, Yesu:
  4243. Act 13:24 Pamenepo Yohane adalalikira koyamba asadafike iye ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israyeli.
  4244. Act 13:25 Ndipo pamene Yohane amakwaniritsa njira yake, iye adanena, Muganiza inu kuti ine ndine yani? Ine sindine [iye]. Koma, tawonani, akudza wina pambuyo pa ine, amene nsapato za ku mapazi [ake] ine sindiyenera kumasula.
  4245. Act 13:26 Amuna [ndi] abale, ana a mbadwo wa Abrahamu, ndi wina aliyense pakati pa inu awopa Mulungu, kwa inu mawu a chipulumutso ichi atumidwa.
  4246. Act 13:27 Pakuti iwo amene akhala m’Yerusalemu, ndi olamula awo, chifukwa iwo sadamdziwa iye, ngakhale mawu a aneneri amene awerengedwa tsiku lasabata lirilonse, iwo akwaniritsa [iwo] mwa kumtsutsa [iye].
  4247. Act 13:28 Ndipo ngakhale iwo sadapeza chifukwa chakufera [mwa iye], komatu adapempha Pilato kuti iye aphedwe.
  4248. Act 13:29 Ndipo pamene adakwaniritsa zonse zomwe zidalembedwera kwa iye, iwo adamtsitsa [iye] kumuchotsa mu mtengo, ndipo anamuyika [iye] m’manda.
  4249. Act 13:30 Koma Mulungu adamuwukitsa iye kwa akufa.
  4250. Act 13:31 Ndipo iye adawonedwa masiku ambiri ndi iwo amene adabwera pamodzi ndi iye pokwera kuchokera ku Galileya kunka ku Yerusalemu, amene ali mboni zake kwa anthu.
  4251. Act 13:32 Ndipo ife tikulakirani inu za uthenga wosangalatsa, kuti momwe lonjezano limene lidachitidwa kwa makolo,
  4252. Act 13:33 Mulungu wakwaniritsa lomweri kwa ife ana awo, mwakuti iye wawukitsanso Yesu; monganso mwalembedwa m’salmo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga wamwamuna, lero ine ndakubala iwe.
  4253. Act 13:34 Ndipo monga kukhudzana ndi kuti iye adawukitsa iye kwa akufa, [tsopano] wosabwereranso ku chivundi, iye adalankhula pa chidziwitsochi, ine ndidzakupatsani inu zifundo zotsimikizika za Davide.
  4254. Act 13:35 Mwa ichi iye anenanso [m’salmo] lina, Inu simudzapereka Woyera wanu awone chivundi.
  4255. Act 13:36 Pakuti Davide, atatumikira iye mbadwo wake wa iye yekha mwa chifuniro cha Mulungu, adagona tulo, ndipo anayikidwa kwa makolo ake, ndipo anawona chivundi.
  4256. Act 13:37 Koma iye, amene Mulungu adamuwukitsanso, sadawona chivundi.
  4257. Act 13:38 ¶Choncho kudziwike kwa inu, amuna [ndi] abale, kuti kudzera mwa munthu uyu kulalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo:
  4258. Act 13:39 Ndipo mwa iye onse amene akhulupira ali wolungamitsidwa kuchokera ku zinthu zonse, kuchokera ku zimene inu simudakatha kudzilungamitsa mwa chilamulo cha Mose.
  4259. Act 13:40 Choncho chenjerani, kuti chimenecho chingadze pa inu, chimene chili chonenedwa mwa aneneriwo;
  4260. Act 13:41 Tawonani, inu wopeputsa, ndi kuzizwa, ndi kuwonongeka: pakuti ine ndigwira ntchito m’masiku anu, ntchito imene simudzayikhulupirira muli monsemo, ngakhale munthu atalengeza kwa inu.
  4261. Act 13:42 Ndipo pamene Ayuda adatuluka m’sunagoge, Amitundu adapempha kuti mawu awa adzalakidwenso kwa iwo sabata lotsatiralo.
  4262. Act 13:43 Ndipo pamene anthu wosonkhana adabalalika, ambiri a Ayuda ndi wotembenukira kuchipembedzo cha Chiyuda adatsata Paulo ndi Barnabas; amene, poyankhula kwa iwo, adawawumiriza kuti apitirire kukhala m’chisomo cha Mulungu.
  4263. Act 13:44 ¶Ndipo tsiku la sabata linalo udadza pamodzi pafupifupi mzinda wonse kudzamva mawu a Mulungu.
  4264. Act 13:45 Koma pamene Ayuda adawona makamuwo, iwo anadzazidwa ndi kaduka, ndipo analankhula motsutsana nazo zinthu izo zimene zinayankhulidwa ndi Paulo, kusemphanitsa ndi kunyoza [Mulungu].
  4265. Act 13:46 Kenaka Paulo ndi Barnabas adalimbika mtima, ndipo adati, Kudali koyenera kuti mawu a Mulungu akadayenera kuti ayambe ayankhulidwa kwa inu: koma powona inu muwachotsa kwa inu, ndipo mudziweruza nokha osayenera moyo wosatha, tawonani, ife titembenukira kwa Amitundu.
  4266. Act 13:47 Pakuti kotero adatilamulira ife Ambuye [kunena kuti], Ine ndakuyika iwe kuti ukhale kuwunika kwa Amitundu, kuti iwe udzakhala wa chipulumutso kufikira malekezero a dziko lapansi.
  4267. Act 13:48 Ndipo pamene Amitundu adamva ichi, iwo adali wokondwera, ndipo anapereka ulemerero ku mawu a Ambuye: ndipo ambiri monga amene adali woyikidwiratu ku moyo wosatha adakhulupirira.
  4268. Act 13:49 Ndipo mawu a Ambuye anabukitsidwa m’dziko lonsero.
  4269. Act 13:50 Koma Ayuda adawutsa akazi wopembedza ndi wolemekezeka, ndi amuna akulukulu a mu mzindawo, ndipo anawawutsira chizunzo Paulo ndi Barnabas, ndipo adawapitikitsa kuwatulutsa iwo m’malire awo.
  4270. Act 13:51 Koma iwo adasansa fumbi la ku mapazi awo kuwatsutsa iwo, ndipo anadza kulowa mu Ikoniyamu.
  4271. Act 13:52 Ndipo wophunzira adali wodzazidwa ndi chimwemwe, ndi Mzimu Woyera.
  4272. Act 14:1 Ndipo kudachitika mu Ikoniyamu, kuti iwo adalowa onse pamodzi m’sunagoge wa Ayuda, ndipo chotero anayankhula, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene lidakhulupirira.
  4273. Act 14:2 Koma Ayuda wosakhulupirira adatakasa Amitundu, ndikupangitsa maganizo awo kuti awawidwe kuchitira zoyipa abale.
  4274. Act 14:3 Choncho adakhala nthawi yayikulu iwo kunenetsa molimba mtima mwa Ambuye, amene adaperekera umboni kwa mawu a chisomo chake, ndipo anapatsa zizindikiro ndi zodabwitsa kuti zichitidwe ndi manja awo.
  4275. Act 14:4 Ndipo khamu la mu mzinda lidagawikana: ndipo gawo lina lidali ndi Ayuda, ndi gawo lina ndi atumwi.
  4276. Act 14:5 Ndipo pamene padakhala chigumukiro cha Amitundu ndi cha Ayudanso ndi woweruza awo, kuwachitira chipongwe, ndi kuwaponya miyala iwo,
  4277. Act 14:6 Iwo adadziwa za [ichi], ndipo anathawira mu Listra ndi Derbe, mizinda ya Likaoniya, ndi ku chigawo chimene chozungulirapo:
  4278. Act 14:7 Ndipo kumeneko adalalikira uthenga wabwino.
  4279. Act 14:8 ¶Ndipo padakhala munthu wina pa Listra, wopanda mphamvu m’mapazi mwake, wolumala kuchokera m’mimba ya amayi wake, amene adali asadayendepo:
  4280. Act 14:9 Yemweyo adamva Paulo alinkulankhula: amene poyang’anitsitsa iye, ndi kuzindikira kuti adali ndi chikhulupiriro chakuti achiritsidwe,
  4281. Act 14:10 Adati ndi mawu okwera, Imirira pa mapazi ako. Ndipo iye adanzunzuka ndi kuyenda.
  4282. Act 14:11 Ndipo pamene anthu adawona chimene Paulo adachita, iwo adakweza mawu awo, nanena m’chinenero cha Likaoniya, milungu yatsika kubwera kwa ife mokhala monga anthu.
  4283. Act 14:12 Ndipo adamutcha Barnabas, Jupitala; ndi Paulo, Merkuriasi, chifukwa adali wolankhula wamkulu.
  4284. Act 14:13 Pamenepo wansembe wa Jupitala, wokhala kumaso kwa mzinda wawo, adabweretsa ng’ombe ndi maluwa ku zipata, ndipo adafuna akadapereka nsembe pamodzi ndi anthu.
  4285. Act 14:14 [Zimene] pamene atumwi, Barnabas ndi Paulo, adamva [za izo], adang’amba zovala zawo, ndipo anathamanga kulowa mkati mwa anthu, nafuwula,
  4286. Act 14:15 Ndi kunena kuti, Anthunu, bwanji inu mukuchita zinthu zimenezi? Ifenso tiri anthu akumva za umunthu chimodzimodzi ndi inu, ndi kulalikira kwa inu kuti inu mutembenuke kuchoka ku zinthu izi zachabe ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo, amene adalenga kumwamba, ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse zimene ziri momwemo.
  4287. Act 14:16 Amene mu nthawi yakale adalekerera mitundu yonse iyende m’njira zawo.
  4288. Act 14:17 Ngakhale zinali choncho sadadzisiyira iye mwini wopanda mboni, mwakuti adachita zabwino, ndipo anatipatsa ife mvula kuchokera kumwamba, ndi nyengo za kubala zipatso, kudzaza mitima yathu ndi chakudya ndi chikondwerero.
  4289. Act 14:18 Ndipo ndi zonena izi anapeza kuletsa iwo anthuwo, kotero kuti iwo sadapereke nsembe kwa iwo.
  4290. Act 14:19 ¶Ndipo adafika kumeneko Ayuda [ena] ochokera ku Antiyoki ndi Ikoniyamu, amene adakopa anthu, ndipo, atamponya Paulo miyala, anamkokera [iye] kunja kwa mzinda; kumuyesa kuti iye adali atafa.
  4291. Act 14:20 Ngakhale zinali motero chomwecho, pamene wophunzirawo adam’zinga, iye adayimirira, ndipo adabwera kulowa mu’mzinda: ndipo tsiku lotsatira iye adanyamuka ndi Barnabas kumka ku Derbe.
  4292. Act 14:21 Pamene atalalikira uthenga wabwino kwa mzinda umenewo: ndipo ataphunzitsa ambiri, iwo anabwereranso ku Listra, ndi [ku] Ikoniyamu, ndi Antiyoki.
  4293. Act 14:22 Kulimbikitsa miyoyo ya wophunzira, [ndi] kuwadandawulira iwo kuti apitirire kukhalabe m’chikhulupiriro, ndi kuti kudzera zisawutso zambiri tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu.
  4294. Act 14:23 Ndipo pamene iwo adawadzodzera iwo akulu mu mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya, iwo adayikiza iwo kwa Ambuye, pa iye amene iwo adamkhulupirira.
  4295. Act 14:24 Ndipo pamene iwo adapitirira Pisidiya, iwo anabwera ku Pamfiliya.
  4296. Act 14:25 Ndipo pamene iwo adali atalalikira mawu m’Perga, iwo adapita kutsikira kulowa mu Ataliya:
  4297. Act 14:26 Ndipo kuchokera komweko adayenda m’chombo kumka ku Antiyoki, kumene iwo adayikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene iwo adayikwaniritsa.
  4298. Act 14:27 Ndipo pamene iwo adabwera, ndipo atasonkhanitsa mpingo pamodzi, iwo adafotokoza zonse zimene Mulungu adachita ndi iwo, ndi momwe iye adatsegulira khomo la chikhulupiriro kwa Amitundu.
  4299. Act 14:28 Ndipo komweko iwo adakhala nthawi yayitali ndi wophunzira.
  4300. Act 15:1 Ndipo anthu ena amene adadza kuchokera ku Yudeya anaphunzitsa abale, [ndipo anati], Pokhapo inu mutadulidwa monga mwa mwambo wa Mose, inu simungathe kupulumutsidwa.
  4301. Act 15:2 Choncho pamene Paulo ndi Barnabas adachitana makani ndi matsutsano ndi iwo, iwo adatsimikiza kuti Paulo ndi Barnabas, ndi ena a iwo, akwere kumka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsoli.
  4302. Act 15:3 Ndipo powabweretsa pa njira yawo ndi mpingo, iwo anadzera modutsa Fenisi ndi Samariya, nalengeza za kutembenuka mtima kwa Amitundu: ndipo anapangitsa chikondwerero chachikulu kwa abale onse.
  4303. Act 15:4 Ndipo pamene iwo adabwera ku Yerusalemu, iwo adalandiridwa kwa mpingo, ndi [kwa] atumwi ndi akulu, ndipo adalengezanso zinthu zonse zimene Mulungu adachita ndi iwo.
  4304. Act 15:5 Koma adawuka ena a mpatuko wa Afarisi amene adakhulupirira, kunena, Kuti kunali koyenera kuwachita mdulidwe iwo, ndi kuwalamulira [iwo] kuti asunge chilamulo cha Mose.
  4305. Act 15:6 ¶Ndipo atumwi ndi akulu adasonkhana pamodzi kuti alingalire za nkhani iyi.
  4306. Act 15:7 Ndipo pamene padali matsutsano ambiri, Petro adayimirira, ndipo anati kwa iwo, Amuna ndi abale, inu mudziwa momwe kuti nthawi yapitayo Mulungu adapanga chisankho pakati pathu, kuti Amitundu ndi m’kamwa mwanga amve mawu a uthenga wabwino, ndipo akhulupirire.
  4307. Act 15:8 Ndipo Mulungu, amene adziwa mitima, adawachitira iwo umboni, kuwapatsa iwo Mzimu Woyera, monga momwe [iye adachita] kwa ife;
  4308. Act 15:9 Ndipo sadayika kusiyanitsa pakati pa ife ndi iwo, kuyeretsa mitima mwa chikhulupiriro.
  4309. Act 15:10 Choncho tsopano chifukwa chiyani inu muyesa Mulungu, kuyika goli pakhosi la wophunzira, limene kapena makolo athu kapena ife sitidathe kunyamula?
  4310. Act 15:11 Koma ife tikhulupirira kuti kudzera mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu ife tidzapulumuka, ngakhale monga iwo.
  4311. Act 15:12 ¶Kenaka khamu lonse lidakhala chete; ndipo adamvera Barnabas ndi Paulo, akulengeza zozizwa ndi zodabwitsa Mulungu adachita pakati pa Amitundu kudzera mwa iwo.
  4312. Act 15:13 ¶Ndipo pamene iwo adakhala bata Yakobo adayankha, kunena kuti, Amuna [ndi] abale, mvetserani kwa ine;
  4313. Act 15:14 Simiyoni walengeza momwe Mulungu poyamba adayendera Amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a kwa dzina lake.
  4314. Act 15:15 Ndipo ku izi agwirizana mawu a aneneri; monga kudalembedwa.
  4315. Act 15:16 Zitatha izi ine ndidzabwerera, ndipo ine ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chagwa pansi; ndipo ine ndidzamanganso mabwinja a icho ndipo ine ndidzachiyimikanso;
  4316. Act 15:17 Kuti wotsala a anthu akhoze kufunafuna Ambuye, ndi onse Amitundu, pa iwo amene dzina langa lidatchulidwa, atero Ambuye, amene achita zinthu izi zonse.
  4317. Act 15:18 Chodziwika kwa Mulungu ndi ntchito zake zonse kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi.
  4318. Act 15:19 Mwa ichi chiweruzo changa ndi ichi, kuti ife tisawavute iwo ayi, amene kuchokera pakati pa Amitundu ali otembenukira kwa Mulungu:
  4319. Act 15:20 Koma kuti tilembere kwa iwo, kuti apewe zodetsa za mafano, ndi [ku] chiwerewere, ndi [ku zophedwa] mopotola, ndi [ku] mwazi.
  4320. Act 15:21 Pakuti Mose wa nthawi yakale ali nawo mu mzinda uliwonse iwo amene amlalikira iye, wokhala akuwerengedwa m’masunagoge m’tsiku lasabata lirilonse.
  4321. Act 15:22 Kenaka chidakomera atumwi ndi akulu, pamodzi ndi mpingo wonse, kutumiza anthu wosankhidwa a m’gulu lawo eni, ku Antiyoki pamodzi ndi Paulo ndi Barnabas; [wotchedwa], Yuda wotchedwanso Barsabas, ndi Sayilasi, anthu akulu a pakati pa abale:
  4322. Act 15:23 Ndipo iwo adalemba [makalata] mwa iwo m’malembedwe wotere; Atumwi ndi akulu ndi abale [atumiza] moni kwa abale a kwa Amitundu mu Antiyoki ndi Siriya ndi Silisiya:
  4323. Act 15:24 Monga muli mwakuti ife tamva, kuti ena amene adatuluka kuchokera mwa ife adakuvutani ndi mawu, nasokoneza miyoyo yanu; kunena kuti, [Inu muyenera] kuti muchitidwe mdulidwe, ndi kusunga chilamulo: kwa iwo amene ife sitidapereke lamulo [lotero]:
  4324. Act 15:25 Chidawoneka chabwino kwa ife, kusonkhana pamodzi ndi mtima umodzi, kutumiza anthu wosankhidwa kwa inu pamodzi ndi wokondedwa athu Barnabas ndi Paulo,
  4325. Act 15:26 Amuna amene adayika miyoyo yawo pa chiswe chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.
  4326. Act 15:27 Choncho ife tatumiza Yuda ndi Sayilasi, amenenso adzakuwuzani [inu] zinthu zomwezo ndi pakamwa.
  4327. Act 15:28 Pakuti chidawoneka chabwino kwa Mzimu Woyera, ndi kwa ife, kusayika pa inu cholemetsa china chachikulu choposa zinthu izi zoyenerazi;
  4328. Act 15:29 Kuti mupewe ku zakudya zoperekedwa nsembe ku mafano, ndi ku mwazi, ndi ku zinthu zophedwa mopotola, ndi ku chiwerewere: kuchokera ku zimene ngati inu mudzisunga nokha, inu mudzachita bwino. Tsalani bwino inu.
  4329. Act 15:30 Tsono pamene iwo adatumizidwa, iwo adabwera ku Antiyoki; ndipo pamene adasonkhanitsa khamu pamodzi, iwo anapereka kalatayo.
  4330. Act 15:31 [Imene] pamene iwo adayiwerenga, adakondwera chifukwa cha chitonthozocho.
  4331. Act 15:32 Ndipo Yuda ndi Sayilasi, wokhala iwo eni anenerinso, anadandawulira abale ndi mawu ambiri, ndipo anawatsimikizira [iwo].
  4332. Act 15:33 Ndipo pamene iwo adakhala [pamenepo] kanthawi, adalawirana nawo nalola amuke ndi mtendere kuchokera kwa abale kumka kwa atumwi.
  4333. Act 15:34 Mosalabadira zidasangalatsa Sayilasi kuti abakhalabe komweko.
  4334. Act 15:35 Paulonso ndi Barnabas adapitirira kukhalabe m’Antiyoki, kuphunzitsa ndi kulalikira mawu a Ambuye, pamodzi ndi enanso ambiri.
  4335. Act 15:36 ¶Patapita masiku angapo Paulo adati kwa Barnabas, Tiye tibwererenso ndi kuzonda abale athu mu mzinda uliwonse umene talalikiramo mawu a Ambuye, [ndi kuwona] momwe iwo achitira.
  4336. Act 15:37 Ndipo Barnabas adatsimikiza kutenga pamodzi ndi iwo Yohane uja, amene wotchedwanso Mariko.
  4337. Act 15:38 Koma Paulo adaganiza kuti sikwabwino kumtenga iye pamodzi nawo, amene adanyamuka kuchoka kwa iwo kuchokera ku Pamfiliya, ndi kusapita nawo pamodzi ku ntchito.
  4338. Act 15:39 Ndipo kutsutsanaku kudali kwakukulu pakati pa iwo, [kotero] kuti iwo adalekana wina kuchoka kwa mzake: ndipo kotero Barnabas adatenga Mariko ndipo adayenda m’chombo nanka ku Sayipulasi;
  4339. Act 15:40 Ndipo Paulo adasankha Sayilasi, ndipo ananyamuka, woyikizidwa ndi abale ku chisomo cha Mulungu.
  4340. Act 15:41 Ndipo iye adapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, natsimikizira mipingo.
  4341. Act 16:1 Kenaka iye adabwera ku Derbe ndi Listra: ndipo, tawonani, wophunzira wina adali pamenepo, dzina lake Timoteyo, mwana wamwamuna wa mayi wina, amene anali Myuda, ndipo adakhulupirira; koma atate wake adali Mhelene:
  4342. Act 16:2 Amene adachitiridwa umboni wabwino ndi abale aku Listra ndi Ikoniyamu.
  4343. Act 16:3 Iye Paulo adafuna kuti amuke ndi iye; ndipo adamtenga ndi kumuchita mdulidwe iye chifukwa cha Ayuda amene adakhala m’mayikomo: pakuti iwo adadziwa zonse kuti atate wake adali Mhelene.
  4344. Act 16:4 Ndipo pamene adali kupyola mizindayo, adapereka kwa iwo malamulo akuti iwo awasunge, amene adayikidwa ndi atumwi ndi akulu amene amakhala mu Yerusalemu.
  4345. Act 16:5 Ndipo kotero mipingoyo idakhazikika m’chikhulupiriro, ndipo inachuluka m’chiwerengero tsiku ndi tsiku.
  4346. Act 16:6 Ndipo pamene iwo adapita kupyola pa dziko la Frigiya ndi dera la Galatiya, ndipo adaletsedwa ndi Mzimu Woyera kulalikira mawu m’Asiya,
  4347. Act 16:7 Iwo atabwera ku Misiya, adayesa kumka ku Bitiniya: koma Mzimu sadawaloleze iwo.
  4348. Act 16:8 Ndipo iwo podutsa pa Misiya adatsikira kubwera ku Trowasi.
  4349. Act 16:9 Ndipo masomphenya adawonekera kwa Paulo usiku; Padali patayimirira munthu wa Makedoniya, ndipo adampempha iye, kunena kuti, Muwolokere kuno ku Makedoniya, ndipo mudzatithandize ife.
  4350. Act 16:10 Ndipo atawona masomphenyawo, posakhalitsa tidayesa kupita kumka ku Makedoniya, potsimikizira kusonkhanitsa nkhani kuti Ambuye adayitanira ife kuti tikalalikire uthenga wabwino kwa iwo.
  4351. Act 16:11 Choncho tidachokera m’chombo ku Trowasi, ndipo pamene ife tidalunjikitsa ku Samotrasiya, ndipo tsiku lotsatira ku Neyapolisi;
  4352. Act 16:12 Ndipo kuchokera kumeneko [tidafika] ku Filipi, umene uli mzinda waukulu wa mbali imeneyo ya Makedoniya, [ndipo] ndi dziko lolamulidwa ndi dziko lina: ndipo tidakhala mu mzindawo masiku ena.
  4353. Act 16:13 Ndipo pa tsiku lasabata ife tidatuluka ku mzinda kumka ku mbali ya mtsinje, kumene tidaganiza kuti adazolowera kupempherako; ndipo ife tidakhala pansi, ndipo tidayankhula kwa akazi amene adasonkhana [kumeneko].
  4354. Act 16:14 ¶Ndipo mkazi wina dzina lake Lidiya, wogulitsa chibakuwa, wa ku mzinda wa Tiyatira, amene ankalambira Mulungu; adatimva [ife]: amene mtima wake Ambuye adatsegula, kuti iye amvere zinthu zimene zidanenedwa ndi Paulo.
  4355. Act 16:15 Ndipo pamene iye adabatizidwa, ndi a pa nyumba yake, iye adatidandawulira [ife], kunena kuti, Ngati inu mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, lowani m’nyumba yanga, ndipo mukhale [m’menemo]. Ndipo iye adatiwumiriza ife.
  4356. Act 16:16 ¶Ndipo zidachitika kuti, pamene tidali kupita kukapemphera, mtsikana wina amene adagwidwa ndi mzimu wam’bwebwe woloteza za kutsogolo adakomana ndi ife, amene adabweretsera ambuye ake phindu lalikulu pa kunena zakutsogolo:
  4357. Act 16:17 Yemweyo adatsata Paulo ndi ife, ndipo anafuwula, kunena kuti, Anthu awa ndi atumiki a Mulungu wa kumwambamwamba, amene awonetsera kwa ife njira ya chipulumutso.
  4358. Act 16:18 Ndipo ichi iye adachita masiku ambiri. Koma Paulo, pokhumudwa, anatembenuka nati kwa mzimuwo, Ine ndikulamulira iwe m’dzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye. Ndipo iwo udatuluka ora lomwero.
  4359. Act 16:19 ¶Ndipo pamene ambuye ake adawona kuti chiyembekezo cha kupindula kwawo chatha, adagwira Paulo ndi Sayilasi, ndipo anawakokera [iwo] kuwalowetsa m’malo a msika kwa owoweruza.
  4360. Act 16:20 Ndipo adawabweretsa iwo kwa woweruza, kunena kuti, Anthu awa, wokhala Ayuda, avutitsa kwambiri mzinda wathu,
  4361. Act 16:21 Ndipo aphunzitsa miyambo, imene isali yovomelezeka mwa lamulo kwa ife kuyilandira, kapena kuyichita, pokhala Aroma.
  4362. Act 16:22 Ndipo khamulo lidayima pamodzi kutsutsana ndi iwo: ndipo woweruza adang’amba malaya awo; ndi kulamulira kuti awakwapule [iwo].
  4363. Act 16:23 Ndipo pamene adawakwapula mikwingwirima yambiri pa iwo, iwo adawayika [iwo] m’ndende, adalamulira mdindo wa ndendeyo kuti awasunge iwo bwino:
  4364. Act 16:24 Amene, atalandira kulamulira kotero, adawakankhira m’ndende ya mkati, ndipo anamangitsa mapazi awo m’zigologolo.
  4365. Act 16:25 ¶Ndipo pakatikati pa usiku, Paulo ndi Sayilasi adalinkupemphera, ndipo anayimba matamando kwa Mulungu, ndipo a m’ndende adawamva iwo.
  4366. Act 16:26 Ndipo mwadzidzidzi padali chivomerezi chachikulu, chotero chakuti maziko a ndende adagwedezeka: ndipo posakhalitsa makomo onse adatseguka, ndi unyolo wa aliyense udamasuka.
  4367. Act 16:27 Ndipo woyang’anira ndende adadzuka kutulo take, ndipo atawona makomo a ndende otseguka, iye adasolola lupanga lake, ndipo akadadzipha yekha, poyesa kuti a m’ndende adali atathawa.
  4368. Act 16:28 Koma Paulo adafuwula ndi mawu akulu, kunena kuti, Usadzipweteke wekha: popeza ife tonse tiri muno.
  4369. Act 16:29 Kenaka woyang’anira ndende adayitanitsa muwuni, ndipo iye anatumphira mkati, ndipo anabwera alinkunjenjemera, ndipo anagwa pansi pamaso pa Paulo ndi Sayilasi.
  4370. Act 16:30 Ndipo adawatulutsa iwo kunja, ndipo anati, Ambuye, kodi ndichitenji ine kuti ndipulumuke?
  4371. Act 16:31 Ndipo iwo adati, khulupirira pa Ambuye Yesu Khristu, ndipo iwe udzapulumuka, ndi nyumba yako.
  4372. Act 16:32 Ndipo iwo adayankhula kwa iye mawu a Ambuye, ndi kwa onse amene anali m’nyumba yake.
  4373. Act 16:33 Ndipo iye adawatenga iwo ora lomwero la usiku, ndipo anatsuka mikwingwirima [yawo]; ndipo anabatizidwa, iye ndi onse ake, posakhalitsa.
  4374. Act 16:34 Ndipo pamene iye adawabweretsa iwo kulowa m’nyumba yake, iye anawakhazikira chakudya pamaso pawo, ndipo anasangalala, pokhulupirira mwa Mulungu pamodzi ndi nyumba yake yonse.
  4375. Act 16:35 Ndipo pamene kudacha, woweruza adatumiza asirikali achisajenti, kunena kuti, Mukamasule anthu aja azipita.
  4376. Act 16:36 Ndipo wosunga ndende adafotokozera mawu awa kwa Paulo, Woweruza atumiza kuti tikumasuleni inu mumuke: choncho tsopano nyamukani, ndipo mukani mu mtendere.
  4377. Act 16:37 Koma Paulo adati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu osaweruzidwa mlandu wathu, pokhala Aroma, ndipo atiyika [ife] m’ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira kunja ife m’seri? Iyayi ndithu; koma lolani iwo adze wokha ndi kudzatitulutsa kunja ife.
  4378. Act 16:38 Ndipo asirikali achisajentiwo adafotokozera mawuwo kwa woweruza: ndipo iwo adawopa, pamene adamva kuti iwo adali Aroma.
  4379. Act 16:39 Ndipo iwo adadza ndi kuwadandawulira iwo, ndipo adawatulutsa [iwo] kunja, ndipo adafuna [iwo] kuti anyamuke kutuluka mu mzindawo.
  4380. Act 16:40 Ndipo iwo adatuluka m’ndendemo, ndipo analowa [m’nyumba] ya Lidiya: ndipo pamene adawona abale, iwo adawatonthoza iwo, ndipo adanyamuka.
  4381. Act 17:1 Tsopano pamene iwo adapitirira kudzera pa Ampifolisi ndi Apoloniya, adabwera ku Tesalonika, kumene kudali sunagoge wa Ayuda:
  4382. Act 17:2 Ndipo Paulo, monga mwa mwambo, adalowa kwa iwo, ndipo masiku a sabata atatu adafotokozerana maganizo ndi iwo za malembo.
  4383. Act 17:3 Kutsegula ndi kubweretsa chitsimikizo, kuti kudayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuwuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu ameneyu, amene ndimulalikira kwa inu, ndiye Khristu.
  4384. Act 17:4 Ndipo ena a iwo adakhulupirira, ndipo anaphatikana ndi Paulo ndi Sayilasi; ndi Ahelene akupembedza a khamu lalikulu, ndi a akazi akulu osati wowerengeka.
  4385. Act 17:5 ¶Koma Ayuda amene sadakhulupirire, modukidwa mtima, anatenga kwa iwo ena amwano a pabwalo, nasonkhanitsa khamu, ndipo anachititsa mzinda wonse phokoso; ndipo adagumukira ku nyumba ya Jasoni, ndipo anafuna kuwatulutsira kwa anthu.
  4386. Act 17:6 Ndipo pamene sadawapeza iwo, iwo adakokera Jasoni ndi abale ena kwa woweruza a mzinda, kufuwula kuti, Awa amene anatembenuza mozondotsa dziko lapansi abwera kunonso;
  4387. Act 17:7 Amene Jasoni wawalandira: ndipo onse awa achita zotsutsa ku malamulo a Kayisara, kunena kuti pali mfumu yina, [m’modziyo] Yesu.
  4388. Act 17:8 Ndipo iwo adavuta anthu ndi woweruza a mzinda, pamene adamva zinthu izi.
  4389. Act 17:9 Ndipo pamene adalandira chikole kwa Jasoni, ndi kwa wina, iwo adawamasula iwo apite.
  4390. Act 17:10 ¶Ndipo posakhalitsa abale adatumiza Paulo ndi Sayilasi usiku kumka ku Bereya: amene pofika [komweko] adalowa m’sunagoge wa Ayuda.
  4391. Act 17:11 Amenewa adali amakhalidwe a pamwamba koposa a m’Tesalonika, mwakuti iwo adalandira mawu ndi mwakukonzekera kwa mtima konse, ndipo anasanthula malembo tsiku ndi tsiku, ngati zinthu zimenezo zidali zotero.
  4392. Act 17:12 Choncho ambiri a iwo adakhulupirira; ndi akazi wolemekezeka amene anali a Chihelene, ndi a amuna, osati ochepa.
  4393. Act 17:13 Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika adadziwa kuti mawu a Mulungu adalalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, iwo adabwera komwekonso, ndipo anatakasa anthu.
  4394. Act 17:14 Ndipo kenaka posakhalitsa adatumiza Paulo amuke kufikira monga kunali ku nyanja: koma Sayilasi ndi Timoteyo adakhalabe komweko.
  4395. Act 17:15 Ndipo iwo amene adamperekeza Paulo adadza naye ku Atene: ndipo polandira lamulo la kwa Sayilasi ndi Timoteyo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu, iwo adanyamuka.
  4396. Act 17:16 ¶Tsopano pamene Paulo adalindira iwo pa Atene, mzimu wake udavutidwa mwa iye, pamene adawona mzinda wonse wodzipereka kwathunthu ku mafano.
  4397. Act 17:17 Choncho iye adatsutsana m’sunagoge ndi Ayudawo, ndi anthu wopembedza, ndi m’bwalo la malonda tsiku ndi tsiku ndi iwo amene adakomana ndi iye.
  4398. Act 17:18 Kenaka akukonda nzeru ena a Epikuriyani, ndi a Stoyiki, adakumana naye. Ndipo ena adati, Kodi wobwebweta uyu adzanena chiyani? Ndipo ena, Akunga wolalikira milungu yachilendo: chifukwa adalalikira kwa iwo Yesu, ndi kuwuka kwa akufa.
  4399. Act 17:19 Ndipo adamtenga iye, ndi kunka naye ku Arewopagasi, kunena kuti, Ife tidziwe chiphunzitso ichi chatsopano, chimene iwe uchinena, [chili]?
  4400. Act 17:20 Pakuti iwe ufikitsa zinthu zachilendo ku makutu athu: choncho ife tifuna kudziwa zimene zinthu izi zitanthawuza.
  4401. Act 17:21 (Pakuti a Atene onse ndi alendo amene adali kumeneko amataya nthawi yawo osachita kanthu kena, koma kapena kunena, kapena kumva kanthu katsopano.)
  4402. Act 17:22 ¶Kenaka Paulo adayimirira pakati pa phiri la Marsi, ndipo anati, [Inu] amuna a Atene, Ine ndizindikira kuti mzinthu zonse kuti inu muli wokhulupirira za matsenga.
  4403. Act 17:23 Pakuti pamene ine ndinadutsa, ndi kuwona zimene muzilambira, ine ndipeza guwa la nsembe lolembedwa motere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Choncho amene inu mum’pembedza osam’dziwa ameneyo ndim’lalikira kwa inu.
  4404. Act 17:24 Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndi zinthu zonse ziri momwemo, powona kuti iye ali Mbuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’makachisi womangidwa ndi manja;
  4405. Act 17:25 Kapena salambiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu kalikonse, powona iye apatsa kwa zonse moyo, ndi mpweya, ndi zinthu zonse;
  4406. Act 17:26 Ndipo wapanga a magazi amodzi mitundu yonse ya anthu kuti akhale pa nkhope yonse ya dziko lapansi, ndipo walingaliratu nthawizo zoyikidwa kale, ndi malire a pokhala pawo;
  4407. Act 17:27 Kuti iwo afunefune Ambuye, kuti mwina iwo angakhoze kumkhudza, ndi kumpeza iye, ngakhale kuti iye sakhala patali ndi wina aliyense wa ife;
  4408. Act 17:28 Pakuti mwa iye ife tikhala ndi moyo ndi kuyenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a lakatuli anu anena, Pakuti ife tirinso ana ake.
  4409. Act 17:29 Monga muli mwakuti tiri ana a Mulungu, ife sitiyenera kuganiza kuti Umulungu uli wofanana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, wosemedwa ndi luso ndi chipangizo cha munthu.
  4410. Act 17:30 Ndipo nthawi ya kusadziwa uku tsono Mulungu adalekerera; koma tsopano alinkulamulira anthu onse ponseponse kuti alape.
  4411. Act 17:31 Chifukwa adayikiratu tsiku, mu limene iye adzaweruza dziko m’chilungamo ndi munthu [ameneyo] adamdzodzeratu; [kwa amene] iye wapatsa chitsimikizo kwa [anthu] onse, mwakuti iye wamuwukitsa iye kuchokera kwa akufa.
  4412. Act 17:32 ¶Ndipo pamene iwo adamva za kuwuka kwa akufa, ena adanyogodola: ndipo ena adati, Ife tidzamvanso iwe za [nkhani] iyi.
  4413. Act 17:33 Chotero Paulo adanyamuka kuchoka pakati pawo.
  4414. Act 17:34 Ngakhale ziri motero chomwecho ena adadziphatika kwa iye, ndipo anakhulupirira: amene pakati pawo [panali] Diyonisiyasi M’Arewopagiti, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nawo.
  4415. Act 18:1 Zitapita zinthu izi Paulo adanyamuka kuchokera ku Atene, ndipo anadza ku Korinto;
  4416. Act 18:2 Ndipo adapeza Myuda wina dzina lake Akwila, wobadwira mu Pontas, chatsopano anachokera ku Itale, pamodzi ndi mkazi wake Priscila; (chifukwa chakuti Klaudiyasi adalamulira Ayuda onse achoke m’Roma:) ndipo adadza kwa iwo.
  4417. Act 18:3 Ndipo popeza adali wa ntchito imodzimodzi, iye adakhala pamodzi ndi iwo, ndipo adagwira ntchito: pakuti ntchito yawo idali yosoka mahema.
  4418. Act 18:4 Ndipo adafotokozerana maganizo m’sunagoge lasabata lirilonse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.
  4419. Act 18:5 Ndipo pamene Sayilasi ndi Timoteyo adadza kuchokera ku Makedoniya, Paulo adapsinjika mu mzimu, ndipo anachitira umboni kwa Ayuda [kuti] Yesu [anali] Khristu.
  4420. Act 18:6 Ndipo pamene iwo adadzitsutsa wokha, ndi kuchita mwano, iye adakutumula malaya [ake], ndipo anati kwa iwo, Mwazi wanu [ukhale] pa mitu yanu; [ine] ndiribe mlandu: kuyambira tsopano ine ndinka kwa Amitundu.
  4421. Act 18:7 ¶Ndipo iye adanyamuka kumeneko, ndipo analowa m’nyumba ya [munthu] wina, dzina lake Jasitasi, [m’modzi] amene adapembedza Mulungu, nyumba yake idayandikizana ndi sunagoge.
  4422. Act 18:8 Ndipo Krispas, wolamulira wamkulu wa sunagoge, adakhulupirira pa Ambuye ndi nyumba yake yonse; ndipo ambiri a ku Korinto atamva anakhulupirira, ndipo iwo anabatizidwa.
  4423. Act 18:9 Kenaka adati Ambuye kwa Paulo usiku mwa masomphenya, Usawope, koma yankhula, ndipo iwe usakhale chete:
  4424. Act 18:10 Pakuti ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzakuchitira chiwembu iwe kuti akuvulaze: pakuti ndiri ndi anthu ambiri mu mzinda uwu.
  4425. Act 18:11 Ndipo iye adakhalabe [komweko] chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi, kuphunzitsa mawu a Mulungu pakati pa iwo.
  4426. Act 18:12 ¶Tsono pamene Galiyo adali chiwanga cha Akaya, Ayuda adamuwukira Paulo ndi mtima umodzi, nabwera naye ku mpando wachiweruziro,
  4427. Act 18:13 Kunena kuti, [Munthu] uyu akopa anthu alambire Mulungu mosemphana ndi chilamulo.
  4428. Act 18:14 Ndipo pamene Paulo adali tsopano kuti atsegule pakamwa [pake], Galiyo adati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa cholakwa kapena dumbo loyipa, [Inu] Ayuda, chifukwa chikadakhalapo chakuti ine nditakumverani inu:
  4429. Act 18:15 Koma ngati likhala funso la mawu ndi mayina, ndi [la] chilamulo chanu; muyang’ane inu[ku ilo]; pakuti sindidzakhala woweruza wa [milandu] yotero.
  4430. Act 18:16 Ndipo adawapitikitsa iwo kuchokera pa mpando wa chiweruziro.
  4431. Act 18:17 Ndipo Ahelene onse adagwira Sostenes, wolamulira wamkulu wa sunagoge, ndipo anampanda [iye] pamaso pa mpando wa chiweruziro. Ndipo Galiyo sadasamalira za chimodzi cha zinthu zimenezo.
  4432. Act 18:18 ¶Ndipo [zitatha izi] Paulo atakhala [komweko] chikhalire kwa nthawi ndithu, ndipo kenaka iye adatsanzika kwa abale, ndipo anachoka pamenepo m’chombo kulowa mu Siriya, ndipo pamodzi naye Priscila ndi Akwila; popeza adameta mutu [wake] m’Kenkreya: pakuti adali ndi chowinda.
  4433. Act 18:19 Ndipo iye adabwera ku Efeso, ndipo iye adawasiya iwo kumeneko: koma iye yekha adalowa m’sunagoge, anafotokozerana maganizo ndi Ayuda.
  4434. Act 18:20 Ndipo pamene iwo adamfunsa [iye] kuti akhale nthawi yina yowonjezerapo pamodzi ndi iwo, iye sadavomereza ayi;
  4435. Act 18:21 Koma iye adawatsanzika iwo, kunena kuti, ine ndiyenera mwanjira iliyonse kusunga phwando ili limene likudza ku Yerusalemu: koma ndidzabwereranso kwa inu, ngati Mulungu alola. Ndipo iye adayenda ulendo wa pa chombo kuchokera ku Efeso.
  4436. Act 18:22 Ndipo pamene adakocheza pa Kayisareya, ndi kukwera [kumtunda], ndipo analankhula mpingo, iye anatsikira kupita ku Antiyoki.
  4437. Act 18:23 Ndipo iye atakhala [kumeneko] nthawi, iye adanyamuka, ndipo anapita pa dziko [lonse] la Galatiya ndi Frugiya ndi cholinga, cholimbikitsa akuphunzira onse.
  4438. Act 18:24 ¶Ndipo Myuda wina dzina lake Apolos, wobadwira ku Alekizandria, munthu woyankhula mwanzeru, [ndipo] wamphamvu m’malembo, adabwera ku Efeso.
  4439. Act 18:25 Munthu uyu adalangizidwa m’njira ya Ambuye; ndipo pokhala wachangu mu mzimu, iye adanena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Ambuye, wodziwa ubatizo wa Yohane wokha.
  4440. Act 18:26 Ndipo pamene iye adayamba kuyankhula molimba mtima m’sunagoge: amene pamene Akwila ndi Priscila adamumva, iwo adamtengera iye kwa [iwo], ndipo anafotokoza kwa iye njira ya Mulungu moyenerera kopambana.
  4441. Act 18:27 Ndipo pamene iye adafuna kuwoloka kunka kulowa mu Akaya, abale adalembera akalata, kuwadandawulira wophunzira kuti amlandire iye: amene, pamene adabwera, adathangata iwo kwambiri amene adakhulupirira kudzera m’chisomo:
  4442. Act 18:28 Pakuti iye ndi mphamvu adakopa Ayuda, [ndi kuti] pamaso pa anthu, kusonyeza mwa malembo kuti Yesu anali Khristu.
  4443. Act 19:1 Ndipo kudachitika, kuti, pamene Apolos adali ku Korinto, Paulo anadutsa kupyola magombe a mum’tunda nabwera ku Efeso: ndipo atapeza wophunzira ena,
  4444. Act 19:2 Iye adati kwa iwo, Kodi inu mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira? Ndipo iwo adati kwa iye iyayi, Ife sitidamva konse kuti kapena kuli Mzimu Woyera.
  4445. Act 19:3 Ndipo iye adati kwa iwo, Ndi kwa chiyani nanga kumene inu munabatizidwa? Ndipo iwo adati, Ku ubatizo wa Yohane.
  4446. Act 19:4 Kenaka adati Paulo, Yohane ndithudi anabatiza ndi ubatizo wa kulapa, kunena kwa anthu, kuti iwo akhulupirire pa iye amene adzadza pambuyo pake, amene ndi, pa Khristu Yesu.
  4447. Act 19:5 Pamene iwo adamva [ichi], iwo adabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.
  4448. Act 19:6 Ndipo pamene Paulo adayika manja [ake] pa iwo, Mzimu Woyera adadza pa iwo; ndipo adayankhula ndi malirime, ndi kunenera.
  4449. Act 19:7 Ndipo amuna onse adalipo pafupifupi khumi ndi awiri.
  4450. Act 19:8 Ndipo iye adalowa m’sunagoge, ndipo anayankhula molimba mtima kwa nthawi ya miyezi itatu, kutsutsana ndi kukakamiza zinthu zokhudza ufumu wa Mulungu.
  4451. Act 19:9 Koma pamene osiyanasiyana adawumitsa mtima, ndipo sadakhulupirira ayi, koma ananenera zoyipa za njirayo pamaso pa khamu, iye adanyamuka kuchoka kwa iwo, ndipo anapatula akuphunzira, kutsutsana tsiku lirilonse m’sukulu ya Tiranas.
  4452. Act 19:10 Ndipo izi zidapitirira kuchitika nthawi yokwana zaka ziwiri; kotero kuti iwo onse amene ankakhala m’Asiya adamva mawu a Ambuye Yesu, Ayuda ndi Ahelene.
  4453. Act 19:11 Ndipo Mulungu adachita zozizwa zapaderadera mwa manja a Paulo:
  4454. Act 19:12 Kotero kuti kuchokera pa thupi pake adabweretsa kwa wodwala nsalu zopukutira ndi zogwirira ntchito, ndipo nthenda zidachoka kwa iwo, ndi mizimu yoyipa idatuluka mwa iwo.
  4455. Act 19:13 ¶Kenaka ena a Ayuda woyendayenda, wotulutsa ziwanda, adadzitengera pa iwo wokha kutchula pa iwo amene adali ndi mizimu yoyipa dzina la Ambuye Yesu, kunena kuti, Ife tikulamulirani inu mwa Yesu amene Paulo amlalikira.
  4456. Act 19:14 Ndipo padali ana amuna asanu ndi awiri a [wina] Skeva, Myuda, [ndi] mkulu wa ansembe, amene adachita chotero.
  4457. Act 19:15 Ndipo mzimu woyipa udayankha ndi kunena, Yesu ine ndimdziwa, ndi Paulo ine ndimdziwa; koma inu ndinu yani?
  4458. Act 19:16 Ndipo munthu amene mwa iye mudali mzimu woyipa adalumphira pa iwo, ndipo anawagonjetsa iwo, nawalaka iwo, kotero kuti adathawa kutuluka m’nyumba amaliseche ndi wovulazidwa.
  4459. Act 19:17 Ndipo zimenezo zidadziwika kwa onse Ayuda ndi Ahelenenso wokhala ku Efeso; ndipo mantha adagwera pa iwo onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu lidakuzika.
  4460. Act 19:18 Ndipo ambiri amene adakhulupirira adadza, ndi kuvomereza, ndi kuwonetsa ntchito zawo.
  4461. Act 19:19 Ambiri a iwonso amene amagwiritsa ntchito ukadawulo wa matsenga adabweretsa mabuku awo pamodzi, ndipo anawatentha pamaso pa [anthu] onse: ndipo adawerengera mtengo wa izo, ndipo adawupeza [uwo] kuti ndi wa [ndalama] zasiliva zikwi makumi asanu.
  4462. Act 19:20 Chotero mawu a Mulungu adakula mwamphamvu nalakika.
  4463. Act 19:21 ¶Ndipo zitatha zinthu izi, Paulo adatsimikiza mu mzimu, pamene iye atapita kupyola pa Makedoniya ndi Akaya, kuti amke ku Yerusalemu, kunena kuti, Nditakhala ine komweko, ine ndiyenera kuwonanso [ku] Roma.
  4464. Act 19:22 Kotero iye adatuma ku Makedoniya awiri a iwo amene adatumikira kwa iye, Timoteyo ndi Erastasi; koma iye mwini adakhala mu Asiya kwa nyengo.
  4465. Act 19:23 Ndipo nthawi yomweyo padabuka phokoso lambiri lakunena za njirayo.
  4466. Act 19:24 Pakuti munthu [wina] dzina lake Demetriyasi, wosula siliva, amene adapanga tiakachisi tasiliva ta Diyana, adabweretsera phindu lambiri kwa amisiri;
  4467. Act 19:25 Amenenso iye adawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a ntchito yofanana yomweyo, ndipo anati, Amuna, inu mudziwa kuti ndi nthcito iyi ife timapeza chuma chathu.
  4468. Act 19:26 Kuwonjezera apo inu muwona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma pafupifupi mu Asiya yense, Paulo uyu wakopa ndi kutembenuza anthu ambiri, kunena kuti iyi si milungu ayi, imene ipangidwa ndi manja:
  4469. Act 19:27 Kotero kuti si ntchito yathu yokhayi imene ili pachiwopsezo kuti inyonyosoka; komanso kuti kachisi wa mulungu wathu wamkulu wamkazi Diyana akhale wonyozedwa, ndiponso kuti ukulu wake ukhale wowonongedwa, amene Asiya yense ndi dziko lonse lilambira.
  4470. Act 19:28 Ndipo pamene adamva [zonena izi], adali wodzala ndi mkwiyo, ndipo anafuwula, kunena kuti, Wamkulu [ali] Diyana wa kwa Aefeso.
  4471. Act 19:29 Ndipo mzinda wonse udadzaza ndi chisokonezo: ndipo atagwira Gayasi ndi Aristarkasi, amuna a ku Makedoniya, anzake a Paulo woyenda nawo, iwo anathamanga onse ndi mtima umodzi kumka kubwalo la masewero.
  4472. Act 19:30 Ndipo pamene Paulo adafuna kulowa kwa anthu, wophunzira sadamloleza ayi.
  4473. Act 19:31 Ndipo ena a akulu a m’Asiya, amene adali abwenzi ake, adatumiza kwa iye, kumupempha [iye] kuti asadziponye yekha kulowa m’bwalo la masewero.
  4474. Act 19:32 Mwa ichi ena adafuwula chinthu china, ndi ena chinthu china: pakuti msonkhano udasokonezeka; ndipo mbali yaunyinji sidadziwa chifukwa chake cha chimene iwo adasonkhanira.
  4475. Act 19:33 Ndipo iwo adamtulutsa Alekizanda m’khamumo, Ayuda kumuyika iye kutsogolo. Ndipo Alekizanda adakodola ndi dzanja, ndipo akadafuna kupereka chitetezo chake kwa anthu.
  4476. Act 19:34 Koma pozindikira kuti iye adali Myuda, onse ndi mawu amodzi a kwa nthawi pafupifupi maora awiri onse akufuwula, Wamkulu ali Diyana wa kwa Aefeso.
  4477. Act 19:35 Ndipo pamene mlembi wa mzinda adatotholetsa anthuwo, iye adati, [Inu] amuna a ku Efeso, ndani munthu alipo amene sadziwa kuti momwe mzinda wa Efeso ndiwo wolambira wa mulungu wa mkazi wamkulu Diyana, ndi wa [fano] limene lidagwa pansi kuchokera ku Jupita?
  4478. Act 19:36 Powona pamenepo kuti zinthu izi sizingalankhulidwe mozitsutsa, inu muyenera kukhala chete, ndi kusachita kanthu mwachangu.
  4479. Act 19:37 Pakuti inu mwatengera kuno anthu awa, amene sali wolanda a za m’mipingo, kapena wochitira mulungu wanu wamkazi zamwano.
  4480. Act 19:38 Mwa ichi tsono Demetriyasi, ndi amisiri amene ali ndi iye, ali ndi mlandu ndi munthu wina, lamulo liripo, ndipo pali achiwiri awo: aloleni ayimbane mlandu wina ndi mzake.
  4481. Act 19:39 Koma ngati mufunsa kanthu kokhudza zinthu zina, kadzaganiziridwa mu msonkhano wolamulidwa.
  4482. Act 19:40 Pakuti ife tiri mowopsa kuti tayitanidwa kufunsidwa za chipolowe cha tsiku ili, pali popanda chifukwa chake chakuti ife tingakhoze kuyankhapo cha kusonkhana uku.
  4483. Act 19:41 Ndipo pamene adanena motere, iye anabalalitsa msonkhanowo.
  4484. Act 20:1 Ndipo litaleka phokosolo, Paulo adayitanira [kwa iye] wophunzirawo, ndipo m’mene adawakumbatira [iwo], ananyamuka kuti amke kulowa m’Makedoniya.
  4485. Act 20:2 Ndipo pamene adapitirira mbali izo, ndipo atawapatsa iwo chilimbikitso chachikulu, adadza ku Girisi,
  4486. Act 20:3 Ndipo [kumeneko] adakhalako miyezi itatu. Ndipo pamene Ayuda adapangira chiwembu pomudikira iye, pamene iye ankati apite m’chombo kulowa m’Siriya, iye anaganizira zobwerera kudzera ku Makedoniya.
  4487. Act 20:4 Ndipo kumeneko adamperekeza kufikira ku Asiya Sopata wa ku Bereya; ndi a ku Atesalonika, Aristarkas ndi Sekundas; ndi Gayasi wa ku Derbe, ndi Timoteyo; ndi a ku Asiya, Tichikasi ndi Trofimasi.
  4488. Act 20:5 Koma iwowa popita patsogolo anatiyembekeza ife pa Trowasi.
  4489. Act 20:6 Ndipo ife tidapita m’chombo kuchokera ku Filipi atapita masiku a mkate wopanda chofufumitsa, ndipo tidafika kwa iwo ku Trowasi patapita masiku asanu; pamenepo tidatsotsa masiku asanu ndi awiri.
  4490. Act 20:7 Ndipo [tsiku] loyamba la sabata, pamene wophunzira adasonkhana kuti anyeme mkate, Paulo adalalikira kwa iwo, wokonzeka kunyamuka tsiku lotsatira; ndipo adanena chinenere kufikira pakatikati pa usiku.
  4491. Act 20:8 Ndipo mudali nyali zambiri m’chipinda chapamwamba, m’mene iwo adasonkhanamo pamodzi.
  4492. Act 20:9 Ndipo pamenepo padakhala pazenera mnyamata wina dzina lake Yutikasi, wogwidwa nato tulo tatikulu: ndipo pamene Paulo anakhala chilalikire nthawi yayitali, iye pogwidwa nato tulo, ndipo adagwa kuchokera panyumba yosanjikana yachitatu, ndipo adamtola atafa.
  4493. Act 20:10 Ndipo Paulo anatsikirako, ndipo adagwera pa iye, ndipo anamfungatira iye nati, Musadzivute nokha; pakuti moyo wake uli mwa iye.
  4494. Act 20:11 Choncho pamene iye adakweranso, ndi kunyema mkate, ndi kudya, ndi kukamba kwa nthawi yayitali, kufikira ngakhale kucha, kotero iye adanyamuka.
  4495. Act 20:12 Ndipo adadza naye mnyamata ali wamoyo, ndipo anatonthozedwa kwakukulu.
  4496. Act 20:13 ¶Ndipo ife tidapita patsogolo kumka ku chombo, ndipo tidayenda m’chombo kupita ku Asosi, pamenepo tidali ndi cholinga chakumtenga Paulo: pakuti kotero iye adatipangira, kuganizira yekha kuti ayenda pamtunda.
  4497. Act 20:14 Ndipo pamene adakomana ndi ife ku Asosi, ife tidamtenga iye, ndipo tidabwera ku Mitilene.
  4498. Act 20:15 Ndipo ife tidachokera kumeneko, ndipo tidabwera [tsiku] lotsatira pandunji pa Kiyosi; ndipo [tsiku] lotsatira tidafika ku Samosi, ndipo tidakhala pa Trogiliyamu; ndipo [tsiku] lotsatira tidabwera ku Miletasi.
  4499. Act 20:16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima kuyenda m’chombo kudzera ku Efeso, chifukwa sakadataya nthawi m’Asiya: chifukwa iye adafulumira, kuti ngati kukadakhala kotheka kwa iye, kuti akakhale ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste.
  4500. Act 20:17 ¶Ndipo kuchokera ku Miletasi adatuma ku Efeso, ndipo adayitana akulu a mpingo.
  4501. Act 20:18 Ndipo pamene iwo adabwera kwa iye, iye adati kwa iwo, Inu mudziwa, kuyambira tsiku loyamba ndidabwera ku Asiya, kutsatira momwe makhalidwe amene ine ndinakhala pamodzi ndi inu pa nyengo zonse,
  4502. Act 20:19 Kutumikira Ambuye ndi mtima wodzichepetsa, ndi misozi yambiri, ndi mayesero, amene ine adandigwera mwa kudikirira kwa ziwembu za Ayuda.
  4503. Act 20:20 [Ndi] momwe ine sindidakubisirani kanthu kamene kanali kopindulitsa [kwa inu], koma ndakuwonetserani inu, ndi kuphunzitsa inu pagulu, ndi kuchokera nyumba ina kupita nyumba ina.
  4504. Act 20:21 Kuchitira umboni kwa Ayuda, ndi kwa Aheleneso, kulapa kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro chakulinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  4505. Act 20:22 Ndipo tsopano, tawonani, ine ndipita ku Yerusalemu womangidwa mu mzimu, wosadziwa zinthu zimene zidzandigwera ine kumeneko:
  4506. Act 20:23 Kupatula kuti Mzimu Woyera achitira umboni mu mzinda uliwonse, kunena kuti nsinga ndi zisawutso zikhazikikira ine.
  4507. Act 20:24 Koma palibe chimodzi cha zinthu izi chisuntha ine, kapena ine sindiwuyesa kanthu moyo wanga kuti uli wa mtengo wake kwa ine mwini: kotero kuti ine ndikatsirize njira yanga ndi chimwemwe, ndi utumiki, umene ine ndidawulandira kwa Ambuye Yesu, kuti ndichitire umboni uthenga wabwino wa chisomo cha Mulungu.
  4508. Act 20:25 Ndipo tsopano, tawonani, ndidziwa ine kuti inu nonse, amene ine ndidapitapita pakati panu kulalikira ufumu wa Mulungu, simudzawonanso nkhope yanga.
  4509. Act 20:26 Mwa ichi ndikuchitirani umboni [za mbiri yanga] tsiku ili, kuti ine [ndiri] wosalakwa ku mwazi wa [anthu] onse.
  4510. Act 20:27 Pakuti ine sindinanyalanyaza kulalikira kwa inu uphungu wonse wa Mulungu.
  4511. Act 20:28 ¶Choncho tadzichenjerani kwa inu nokha, ndi gulu la busa lonse, pa limene Mzimu Woyera wakupangani [kukhala] woyang’anira, kuti mudyetse mpingo wa Mulungu, umene iye waugula ndi mwazi wa iye yekha.
  4512. Act 20:29 Pakuti ine ndidziwa ichi, kuti nditanyamuka ine mimbulu yolusa idzalowa, yosalekerera busa la gululo.
  4513. Act 20:30 Mwa inunso eni nokha adzawuka anthu, kuyankhula zinthu zolakwika, kuti apatutse wophunzira awatsate iwo.
  4514. Act 20:31 Choncho yang’anirani, ndipo mukumbukire, kuti nthawi ya mpata wa zaka zitatu ine sindidaleka kuchenjeza aliyense wa inu usiku ndi usana ndi misozi.
  4515. Act 20:32 Ndipo tsopano, abale, ine ndikuyikizani inu kwa Mulungu, ndi kwa mawu a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira inu, ndi kupatsa inu cholowa pakati pa onse amene ali woyeretsedwa.
  4516. Act 20:33 Sindidasilira siliva wa munthu aliyense, kapena golidi, kapena chovala.
  4517. Act 20:34 Inde, inu nokha mudziwa, kuti manja awa adatumikira ku zosowa zanga, ndi kwa iwo amene adakhala ndi ine.
  4518. Act 20:35 Ine ndakuwonetsani zinthu zonse, ndidakupatsani chitsanzo, momwe mwakuti pogwira ntchito kotero inu muyenera kuthandiza wofowoka, ndi kukumbukira mawu a Ambuye Yesu, momwe iye adati, Kuli kudalitsika koposa pa kupatsa kupambana kulandira.
  4519. Act 20:36 ¶Ndipo m’mene iye adanena motero, iye adagwada pansi, ndi kupemphera ndi iwo onse.
  4520. Act 20:37 Ndipo iwo onse adalira kwambiri, ndipo anagwera pakhosi la Paulo, ndi kumpsompsona.
  4521. Act 20:38 Kumva chosoni ambiri a iwo chifukwa cha mawu amene adanena, kuti iwo sadzawonanso nkhope yake ayi. Ndipo iwo adamperekeza iye kukalowa m’chombo.
  4522. Act 21:1 Ndipo kudachitika, kuti ife titanyamuka kuchoka kwa iwo, ndi kukankhira chombo m’madzi, tinadza molunjika ku Kusi, ndipo [tsiku] lotsatira ku Rodesi, ndipo pochokera kumeneko ku Patara:
  4523. Act 21:2 Ndipo m’mene tidapeza chombo chakuwoloka kumka ku Fenisiya, ife tidalowamo, ndipo tidanyamuka.
  4524. Act 21:3 Tsopano pamene tidawona Sayiprasi, ife tidachisiya kudzanja lamanzere, ndipo tidayenda m’chombo kulowa m’Siriya, ndipo tidakocheza ku Turo: pakuti pamenepo chombo chidafuna kutula akatundu ake.
  4525. Act 21:4 Ndipo pakupezako wophunzira, tidakhala masiku asanu ndi awiri: amene adanena kwa Paulo kudzera mwa Mzimu, kuti iye asakwera kumka ku Yerusalemu.
  4526. Act 21:5 Ndipo pamene ife tidatsiriza masiku awo, tidanyamuka ndi kumka ulendo wathu; ndipo iwo onse adatibweretsa ku njira yathu, ndi akazi awo ndi ana, kufikira [ife tidali] titatuluka mzindawo: ndipo ife tidagwada pa gombe la nyanja, ndi kupemphera.
  4527. Act 21:6 Ndipo pamene ife tidasiyana wina ndi mzake, ife tidatenga chombo; ndipo iwo adabwereranso kwawo.
  4528. Act 21:7 Ndipo pamene ife tidatsiriza ulendo [wathu] wochokera ku Turo, ife tidabwera ku Ptolemayisi, ndipo tidapereka moni kwa abale, ndipo tidakhala nawo tsiku limodzi.
  4529. Act 21:8 Ndipo [tsiku] lotsatira ife amene tidali a mgulu lake la Paulo, tidachoka, ndipo tidanyamuka, ndipo tidabwera ku Kayisareya: ndipo ife tidalowa m’nyumba ya Filipi mlaliki, amene adali [m’modzi] wa asanu ndi awiri [aja], ndipo tidakhala naye.
  4530. Act 21:9 Ndipo munthuyu adali nawo ana akazi anayi, anamwali, amene amanenera.
  4531. Act 21:10 Ndipo pamene ife tidakhala [kumeneko] masiku ambiri, padabwera kutsika kuchokera ku Yudeya, mneneri wina dzina lake Agabasi.
  4532. Act 21:11 Ndipo pamene adadza kwa ife, iye anatenga lamba wa Paulo, ndipo anamanga manja ndi mapazi ake, ndipo anati, Atero Mzimu Woyera, Motero Ayuda m’Yerusalemu adzam’manga munthu amene ali mwini wa lamba uyu, ndipo adzampereka [iye] m’manja a Amitundu.
  4533. Act 21:12 Ndipo pamene ife tidamva zinthu izi, tonse ife, ndi iwo a komweko, tinam’dandawulira iye kuti asakwere kumka ku Yerusalemu.
  4534. Act 21:13 Kenaka Paulo adayankha, Mutanthawuzanji inu polira ndi kuswa mtima wanga? Pakuti ine ndakonzeka ine sikumangidwa kokha, komatunso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.
  4535. Act 21:14 Ndipo pamene iye sakadakopeka, ife tidaleka, kunena kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.
  4536. Act 21:15 ¶Ndipo atapita masiku awo tidatenga katundu wathu, ndipo tidakwera kupita ku Yerusalemu.
  4537. Act 21:16 Ndipo adamuka nafenso [ena] a wophunzira a ku Kayisareya, ndipo anatenga wina pamodzi nawo Mnasoni wa ku Sayiprasi, wophunzira wakale, amene ife tinayenera kukhalira naye pamodzi.
  4538. Act 21:17 Ndipo pamene ife tidabwera ku Yerusalemu, abale adatilandira ife mokondwera.
  4539. Act 21:18 Ndipo [tsiku] lotsatira Paulo adalowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse adalipo.
  4540. Act 21:19 Ndipo pamene anawayankhula iwo, adalengeza chimodzi chimodzi zinthu zimene Mulungu adachita kwa Amitundu mwa utumiki wake.
  4541. Act 21:20 Ndipo pamene iwo adazimva [izi], adapereka ulemerero kwa Ambuye, ndipo anati, kwa iye, Iwe uwona, mbale, mazana angati a Ayuda omwe alipo amene akhulupirira; ndipo ali nacho changu cha pa chilamulo:
  4542. Act 21:21 Ndipo iwo adawuzidwa za iwe, kuti iwe uphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa Amitundu kuti apatukane naye Mose, kunena kuti asachite mdulidwe ana [awo], kapena asayende motsatira miyambo.
  4543. Act 21:22 Kodi choncho ichi chiyani? Khamu lidzafuna kudza pamodzi: pakuti iwo adzamva kuti iwe wadza.
  4544. Act 21:23 Choncho uchite ichi ife tinena kwa iwe: Tiri nawo amuna anayi amene adachita chowinda pa iwo;
  4545. Act 21:24 Iwo atenge, ndipo udziyeretse wekha pamodzi ndi iwo, ndipo ukhale pa malipiriro pamodzi ndi iwo, kuti amete mitu [yawo]: ndipo onse akhoze kudziwa kuti zinthu izo, za zomwe iwo adawuzidwa zokhudza iwe, nzachabe; koma [kuti] iwe wekhanso uyenda molunjika, ndipo usunga chilamulo.
  4546. Act 21:25 Monga zokhudza Amitundu amene akhulupirira, ife tawalembera [ndi] kuweruza kuti asasamalire zinthu zotero koma, kupatula kokha kuti asale [zinthu] zoperekedwa kwa mafano, ndi ku mwazi, ndi ku zakupha mopotola, ndi ku chiwerewere.
  4547. Act 21:26 Pamenepo Paulo adatenga anthuwo, ndipo tsiku lotsatira kudziyeretsa iye yekha nawo pamodzi adalowa m’kachisi, kukatsimikizira za chimarizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira kuti nsembe yiperekedwe ya wina aliyense wa iwo.
  4548. Act 21:27 ¶Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri atatsala pang’ono kuti amarizidwe, Ayuda amene adali a ku Asiya, pamene iwo anamuwona iye m’kachisi, adatakasa anthu onse, ndipo anamgwira iye,
  4549. Act 21:28 Kufuwula kuti, Amuna a Israyeli, thandizani: Uyu ndi munthu uja, amene aphunzitsa [anthu] onse ponsepo motsutsana ndi anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano: ndipo adapitiriranso kubweretsa Ahelene nalowa nawo m’kachisi, ndipo wadetsa malo ano woyera.
  4550. Act 21:29 (Pakuti adawona kale pamodzi ndi iye mumzinda wa Trofimasi wa Chiefeso; amene iwo adayesa kuti Paulo adambweretsa iye kulowa naye m’Kachisi).
  4551. Act 21:30 Ndipo mzinda wonse udasokonezeka, ndipo anthu adathamanga pamodzi: ndipo anatenga Paulo, ndipo anamkoka kumtulutsa m’kachisi: ndipo nthawi yomweyo makomo adatsekedwa.
  4552. Act 21:31 Ndipo m’mene adayenda kufuna kumupha iye, uthenga udafika kwa kapitawo wamkulu wa gululo, kuti Yerusalemu yense adali m’chisokonezo.
  4553. Act 21:32 Amene mosakhalitsa adatenga asirikali ndi a kenturiyoninso, ndipo anathamanga kutsikira kwa iwo: ndipo pamene iwowa anawona kapitawo wamkulu ndi asirikali, adaleka kumpanda Paulo.
  4554. Act 21:33 Kenaka kapitawo wamkulu anabwera pafupi, ndi kumtenga iye, ndi kulamulira kuti am’mange [iye] ndi unyolo uwiri; ndipo adafunsa kuti iye anali yani, ndi chimene iye anachita?
  4555. Act 21:34 Ndipo ena adafuwula chinthu chimodzi, ena china, pakati pa khamulo: ndipo m’mene iye sadathe kudziwa zowona za chifukwa cha phokosolo, iye adalamulira amuke naye kulowa m’nyumba ya m’linga.
  4556. Act 21:35 Ndipo pamene adafika pa makwerero, kudali kotero, kuti iye adanyamulidwa ndi asirikali chifukwa cha chiwawa cha anthu.
  4557. Act 21:36 Pakuti khamu la anthu lidatsata, ndi kufuwula, Mchotseni iye.
  4558. Act 21:37 Ndipo pamene Paulo ankati atsogololeredwe kulowa m’nyumba ya m’linga, iye adanena kwa kapitawo wamkulu, Mundilola ine ndilankhule kwa inu? Amene adati, Ungalankhule Chihelene?
  4559. Act 21:38 Iwe si uli mu Aigupto, amene asadafike masiku awa udapangitsa chiphokoso, ndi kutsogolera kulowa kuchipululu anthu zikwi zinayi amene adali ambanda?
  4560. Act 21:39 Koma Paulo adati, Ine ndine munthu [amene ndiri] Myuda wa ku Tarsasi, [mzinda] wa mu Silisiya, mbadwa ya mzinda womveka: ndipo, ine ndikupemphani inu, mundilole ine kuti ndiyankhule kwa anthu.
  4561. Act 21:40 Ndipo m’mene iye adamlola iye, Paulo adayimirira pa makwerero, ndipo anakodola ndi dzanja kwa anthuwo. Ndipo pamene padakhala bata lalikulu, iye adayankhula kwa [iwo] m’chinenedwe cha Chihebri, kunena kuti,
  4562. Act 22:1 Amuna, abale, ndi atate, mverani inu chodzikanira changa [chimene ine ndichipereka] tsopano kwa inu.
  4563. Act 22:2 (Ndipo pamene adamva kuti adayankhula m’chinenedwe cha Chihebri kwa iwo, adaposa kukhala chete: ndipo iye ati,)
  4564. Act 22:3 Ine ndithudi ndi munthu [amene ndiri] Myuda, wobadwa m’Tarsasi, [mzinda] wa mu Silisiya, koma ndaleredwa mu mzinda muno pa mapazi a Gamaliyeli; [ndi] wolangizidwa monga mwa machitidwe angwiro a chilamulo cha makolo, ndipo ndidali wachangu chakulinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse tsiku ili.
  4565. Act 22:4 Ndipo ine ndidazunza njira iyi kufikira imfa, kumanga ndi kupereka ku ndende amuna ndi akazi.
  4566. Act 22:5 Monganso mkulu wa ansembe andichitira ine umboni, ndi bwalo lonse la akulu: kuchokera kwa iwo amenenso ine ndidalandira makalata kumka nawo kwa abale, ndipo ndidapita ku Damasikasi, kuti ndiwabweretse iwo amene adali kumeneko womangidwa ku Yerusalemu, kuti iwo akalangidwe.
  4567. Act 22:6 Ndipo kudachitika, kuti pamene ndinkayenda pa ulendo wanga, ndipo nditayandikira ku Damasikasi pafupifupi dzuwa liri pa liwombo, mwadzidzidzi kudawala kuchokera kumwamba kuwunika kwakukulu pondizungulira ine.
  4568. Act 22:7 Ndipo ine ndidagwa pansi, ndipo ndidamva mawu akunena kwa ine, Saulo, Saulo, chifukwa chiyani undinzunza ine?
  4569. Act 22:8 Ndipo ine ndidayankha, Ndinu yani, Ambuye? Ndipo adati kwa ine, Ine ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe umzunza.
  4570. Act 22:9 Ndipo iwo amene adali ndi ine adawonadi kuwunika, ndipo adachita mantha; koma sadamva mawu akuyankhula nane.
  4571. Act 22:10 Ndipo ine ndidati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye adati kwa ine, Imirira, ndipo pita ku Damasikasi; ndipo kumeneko kudzakufotokozedwa kwa iwe za zinthu zonse zimene ziri zoyikika kwa iwe kuti uchite.
  4572. Act 22:11 Ndipo pamene sindidatha kupenya, chifukwa cha ulemerero wa kuwunikako, potsogozedwa ndi kundigwira dzanja la iwo amene adali ndi ine, ine ndidabwera ku Damasikasi.
  4573. Act 22:12 Ndipo wina dzina lake Ananiyasi, bambo wopembedza monga mwa chilamulo, wokhala nawo umboni wabwino wa Ayuda onse amene ankakhala [kumeneko],
  4574. Act 22:13 Adadza kwa ine, ndipo anayimirira, ndipo adati kwa ine, Mbale Saulo, landira kupenya kwako. Ndipo ora lomwero ine ndidapenya pa iyeyo.
  4575. Act 22:14 Ndipo iye adati, Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe, kuti udziwe chifuniro chake, ndipo uwone Wolungamayo, ndipo umve mawu a m’kamwa mwake.
  4576. Act 22:15 Pakuti iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse ya za zimene iwe waziwona ndi kumva.
  4577. Act 22:16 Ndipo tsopano uchedweranji iwe? Tawuka, ndipo ubatizidwe, ndi kusamba kuchotsa machimo ako, kuyitana pa dzina la Ambuye.
  4578. Act 22:17 Ndipo kudachitika, kuti, pamene nditabweranso ku Yerusalemu, ngakhale pamene ine ndidalikupemphera m’kachisi, ine ndidachita ngati kukomoka;
  4579. Act 22:18 Ndipo ndidamuwona iye akunena kwa ine, Chita changu, ndipo iwe mwamsanga tuluka m’Yerusalemu: pakuti iwo sadzalandira umboni wako wokhudza ine.
  4580. Act 22:19 Ndipo Ine ndidati, Ambuye, iwo adziwa kuti ndidali kuyika m’ndende ndi kuwapanda m’masunagoge onse iwo amene ankakhulupirira pa inu:
  4581. Act 22:20 Ndipo pamene mwazi wa Stefano wofera chikhristu udakhetsedwa, inenso ndinali ndikuyimirira pambali pake, ndi kuvomerezana nawo ku imfa yake, ndi kusunga zovala za iwo amene adamupha iye.
  4582. Act 22:21 Ndipo adati kwa ine, Nyamuka: chifukwa ine ndidzakutuma iwe kutali uko kwa Amitundu.
  4583. Act 22:22 ¶Ndipo iwo adamvera iye kufikira mawu awa, ndipo [kenaka] adakweza mawu [awo], ndipo ananena. Achoke [munthu] wotere pa dziko lapansi: pakuti sikuli koyenera kuti iye akhale ndi moyo.
  4584. Act 22:23 Ndipo pamene iwo ankafuwula, ndi kutaya zovala [zawo], ndi kuwaza fumbi mu m’lengalenga,
  4585. Act 22:24 Kapitawo wamkulu adalamulira kuti abwere naye kulowa m’nyumba ya m’linga, ndipo anati ayenera kuti amfufuze iye mwa kumkwapula; kuti iye akhoze kudziwa chifukwa chiyani chakuti iwo amafuwulira mom’tsutsa chomwecho.
  4586. Act 22:25 Ndipo pamene adali kum’manga iye ndi malamba a chikopa, Paulo adati kwa kenturiyoni wakuyimirira pambali pake, Kodi nkuloleka mwa lamulo kwa inu kukwapula munthu amene ali Mroma, ndiponso wosaweruzidwa?
  4587. Act 22:26 Pamene kenturiyoni adamva [ichi], iye adamka ndi kumuwuza kapitawo wamkulu, kunena kuti, Samala chimene iwe uchita: pakuti munthu uyu ndi Mroma.
  4588. Act 22:27 Kenaka kapitawo wa mkuluyo adadza, ndipo anati kwa iye, Ndiwuze ine, iwe ndiwe Mroma? Iye adati, Inde.
  4589. Act 22:28 Ndipo kapitawo wamkulu adayankha, Ndi mtengo wake waukulu ine ndalandira ufulu uwu. Ndipo Paulo adati, Koma ine ndinabadwa [mfulu].
  4590. Act 22:29 Kenaka nthawi yomweyo iwo adanyamuka kuchoka kwa amene adati amfufuze iye: ndipo kapitawo wamkulunso adachita mantha, atazindikira kuti iye anali Mroma, ndiponso chifukwa iye adam’manga iye.
  4591. Act 22:30 Pa tsiku lotsatira, chifukwa iye akadadziwa chifukwa chake chenicheni adam’nenera iye Ayuda, iye adam’masula iye ku msinga [zake], ndipo analamulira ansembe akulu ndi bwalo lonse la akulu kuti asonkhane, ndipo adatsika kubweretsa Paulo, ndipo anamuyika iye pamaso pawo.
  4592. Act 23:1 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m’bwalo la akulu, adati, Amuna [ndi] abale, ine ndakhala moyo ndi chikumbumtima chokoma chonse pamaso pa Mulungu kufikira tsiku ili [la lero].
  4593. Act 23:2 Ndipo wansembe wamkulu Ananiyasi adalamulira akuyimirira pambali pake kuti ampande iye pakamwa pake.
  4594. Act 23:3 Kenaka Paulo adati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, [iwe] khoma loyeretsedwa: pakuti iwe ukhala pansi kuti undiweruze ine monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira ine ndipandidwe mosemphana ndi chilamulo?
  4595. Act 23:4 Ndipo iwo akuyimira pomwepo adati, Iwe ulalatira wansembe wamkulu wa Mulungu?
  4596. Act 23:5 Kenaka Paulo adati, ine sindidadziwa ayi, abale, kuti iye anali wansembe wamkulu: pakuti kwalembedwa, Usam’nenera choyipa wolamula wa anthu ako.
  4597. Act 23:6 Koma pamene Paulo anazindikira kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, iye adafuwula m’bwalomo, Amuna [ndi] abale, ine ndine Mfarisi, mwana wamwamuna wa Mfarisi: chifukwa cha chiyembekezo ndi kuwuka kwa akufa andinenera mlandu.
  4598. Act 23:7 Ndipo pamene adanena motero, kudabuka kusagwirizana pakati pa Afarisi ndi Asaduki: ndipo khamulo lidagawanika [pawiri].
  4599. Act 23:8 Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuwuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu: koma Afarisi avomereza zonse ziwiri.
  4600. Act 23:9 Ndipo chidawuka chiphokoso chachikulu: ndipo alembi ena [omwe adali] a kwa mbali ya Afarisi adayimirira, ndipo anatsutsa, kunena kuti, Ife sitipeza choyipa chilichonse mwa munthu uyu; koma ngati mzimu kapena mngelo wayankhula kwa iye, ife tisalimbane ndi Mulungu.
  4601. Act 23:10 Ndipo pamene padawuka kusagwirizana kwakukulu, kapitawo wamkulu, kuwopa kuti mwina Paulo akadakhoza kukhadzulidwakhadzulidwa ndi iwo, adalamulira asirikali atsike, ndi kuti akantenge iye momkwatula pakati pawo, ndi kuti adze naye [iye] kulowa naye m’nyumba yam’linga.
  4602. Act 23:11 Ndipo usiku wotsatira Ambuye adayimirira pambali pa iye, ndipo anati, Limbika mtima, Paulo: pakuti monga wandichitira umboni mu Yerusalemu, kotero uyenera iwe kundichitiranso umboni ku Roma.
  4603. Act 23:12 ¶Ndipo pamene kunacha, ena a Ayuda adapanga gulu, ndipo anadzimanga iwo okha pansi pa temberero, kunena kuti iwo sadya kapena kumwa kufikira iwo atamupha Paulo.
  4604. Act 23:13 Ndipo iwo adali woposa makumi anayi amene adakonza chiwembu ichi.
  4605. Act 23:14 Ndipo iwo adadza kwa ansembe akulu ndi kwa akulu, ndipo anati, Ife tadzimanga tokha pansi pa temberero lalikulu kuti sitidzadya kanthu kalikonse kufikira titamupha Paulo.
  4606. Act 23:15 Choncho tsopano inu ndi bwalo la akulu mupemphe kwa kapitawo wamkulu kuti atsike kubwera naye kwa inu mawa, monga ngati inu mufuna kufunsa china chake bwino lomwe zokhudza iye: koma ife, kapena pamene iye abwera pafupi, tadzikonzeratu kumupha iye.
  4607. Act 23:16 Ndipo pamene mwana wamwamuna wa mlongo wake wa Paulo adamva za [chiwembu cha] kumdikirira kwawo, iye anapita ndi kulowa m’nyumba ya m’linga, ndipo anamfotokozera Paulo.
  4608. Act 23:17 Kenaka Paulo adadziyitanira m’modzi wa a kenturiyoni kwa [iye], ndipo anati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitawo wamkulu: pakuti iye ali nako kanthu kena kakumfotokozera iye.
  4609. Act 23:18 Kotero iye adamtenga iye, ndipo anapita naye [iye] kwa kapitawo wamkulu, ndipo anati, Paulo wamsinga adandiyitana inekwa [iye], ndipo anandipempha ine ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, amene ali nako kanthu kakuti afotokozere inu.
  4610. Act 23:19 Kenaka kapitawo wamkulu adamgwira iye pa dzanja, ndipo anapita [ndi iye] padera pambali pa awiri, ndipo anamfunsa [iye], Nchiyani ichi chimene uli nacho chakuti undifotokozere?
  4611. Act 23:20 Ndipo iye adati, Ayuda agwirizana kuti akufunseni inu kuti mubweretse kutsika naye Paulo mawa m’bwalo la milandu, monga ngati iwo afuna kufunsitsa kena kake bwino lomwe za iye.
  4612. Act 23:21 Koma inu musagonjere kwa iwo: pakuti amlalira iye a iwo woposa abambo makumi anayi, amene adadzimanga iwo wokha ndi lumbiro, kuti iwo sadzadya kapena kumwa kufikira iwo atamupha iye: ndipo tsopano iwo ali wokonzekera, ayang’anira lonjezano lochokera kwa inu.
  4613. Act 23:22 Kotero kapitawo wamkulu [kenaka] adamulola mnyamatayo anyamuke, ndipo anamlamulira [iye, Uwonetsetse kuti] usawuze munthu aliyense kuti wazindikiritsa zinthu izi kwa ine.
  4614. Act 23:23 Ndipo iye adayitana [kwa iye] a kenturiyoni awiri, kunena kuti, Mukonzeretu asirikali mazana awiri, kuti apite ku Kayisareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, pa ora lachitatu la usiku.
  4615. Act 23:24 Ndiponso mukonzeretu [iwo] nyama [zokwerapo], kuti amkwezepo Paulo, ndi kubwera ndi [iye] wotetezedwa kwa Felikisi kazembeyo.
  4616. Act 23:25 Ndipo iye adalembera kalata m’malembedwe wotere:
  4617. Act 23:26 Klawudiyasi Lisiyasi kwa kazembe wabwino kwambiri Felikisi [nditumiza] malonje.
  4618. Act 23:27 Munthu uyu adatengedwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo: kenaka ine ndidabwera ndi gulu la nkhondo, ndipo ndidamlanditsa iye, nditazindikira kuti anali Mroma.
  4619. Act 23:28 Ndipo pamene ndidafuna kuzindikira chifukwa chake chimene iwo adam’nenera iye, ndidam’bweretsa iye ku bwalo lawo la akulu:
  4620. Act 23:29 Amene ine ndidazindikira kuti adam’nenera za mafunso a chilamulo chawo, koma kukhala alibe kum’nenera kanthu kakuyenera chigamulo choyenera imfa kapena kumangidwa.
  4621. Act 23:30 Ndipo m’mene chidadziwitsidwa kwa ine momwe mwakuti Ayuda amlalira munthuyu, ine nthawi yomweyo ndidam’tumiza kwa inu; ndipo ndaperaka kwa iwonso akum’nenera lamulo kuti anene pamaso panu chimene [iwo anali] nacho chom’tsutsa. Tsalani bwino.
  4622. Act 23:31 Kenaka asirikali, monga kudali kolamulidwa iwo, adatenga Paulo, ndi kubweretsa [iye] usiku ku Antipatrisi.
  4623. Act 23:32 Pa tsiku lotsatira iwo adasiya apakavalo kuti apite ndi iye, ndipo anabwera kupita m’nyumba ya m’linga:
  4624. Act 23:33 Iwowo, m’mene adabwera ku Kayisareya, ndipo atapereka kalata kwa kazembe, anaperekanso Paulo kwa iye.
  4625. Act 23:34 Ndipo m’mene kazembe adawerenga [kalatayo], iye adafunsa za dera limene iye adali [kuchokera]. Ndipo pamene adazindikira kuti [iye adali] wa ku Silisiya;
  4626. Act 23:35 Ine ndidzamva iwe, adati iye, pamene abweranso akukunenera ako. Ndipo iye adalamulira iye kuti asungidwe m’nyumba yoweruzira mlandu ya Herode.
  4627. Act 24:1 Ndipo atapita masiku asanu Ananiyasi mkulu wa ansembe adatsika pamodzi ndi akulu, ndi wowalankhulira wina dzina lake Tertulasi, amene adafotozera kazembeyo za kunenera zomtsutsa Paulo.
  4628. Act 24:2 Ndipo pamene iye adayitanidwa, Tertulasi adayamba kum’nzenga mlandu [iye], kunena kuti, Powona kuti mwa inu tikondwera nalo bata lalikulu, ndi kuti zochita zoyenera kwambiri zimachitika ku dziko ili ndi kuganiziratu za zomwe ziti zibwere,
  4629. Act 24:3 Tichilandira [ichi] nthawi zonse, ndipo m’malo onse, ndi ponsepo, ndi chiyamiko chonse, wolemekezeka koposa Felikisi.
  4630. Act 24:4 Posawerengera, kuti ine ndingawonjeze kukhala wolemetsa kwa inu, ine ndikupemphani inu kuti mutimvere ife mwa chifundo chanu mawu ochepa.
  4631. Act 24:5 Pakuti ife tapeza munthu uyu wa mliri, ndi woyambitsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lapansi, ndi mtsogoleri wa mpatuko wa Anazarene:
  4632. Act 24:6 Amenenso wapitapita kuti ayipse kachisi: amene ife tamtenga, ndipo anayenera kuweruzidwa molingana ndi chilamulo chathu.
  4633. Act 24:7 Koma kapitawo wamkulu Lisiyasi adabwera [pa ife] ndipo ndi chiwawa chachikulu adamtenga [iye] kuchokera m’manja mwathu.
  4634. Act 24:8 Kulamulira kuti wom’nenera iye adze kwa inu: mwa kufunsafunsa kwa amene inu eni mukhoze kudziwa za zinthu izi zonse, za zimene ife tim’nenera iye.
  4635. Act 24:9 Ndipo Ayuda adavomerezananso, kunena kuti zinthu izi zidali chomwecho.
  4636. Act 24:10 ¶Kenaka Paulo, kutachitika kuti kazembe adamkodola iye kuti alankhule, adayankha nati, Monga kuli kwakuti ine ndidziwa kuti inu mwakhala kwa zaka zambiri woweruza wa mtundu uwu, ine ndichita mokondwera koposa kudziyankhira ine ndekha.
  4637. Act 24:11 Chifukwa chakuti inu mukhoze kuzindikira, kuti apita masiku khumi ndi awiri chikwerere ine ku Yerusalemu kuti ndikalambire.
  4638. Act 24:12 Ndipo ine sanandipeza m’kachisi kutsutsana ndi munthu wina aliyense, kapena kusonkhanitsa khamu la anthu, kapena m’masunagoge, kapena mu mzinda:
  4639. Act 24:13 Kapena sangathe iwo kutsimikiza zinthu zimene iwo akundinenera ine tsopano.
  4640. Act 24:14 Koma ichi ndivomereza kwa inu, kuti monga mwa njira yonenedwa chiphunzitso chabodza, moteromo ine ndilambira Mulungu wa makolo anga, kukhulupirira zinthu zonse zimene ziri zolembedwa m’chilamulo ndi mu aneneri.
  4641. Act 24:15 Ndipo ndikukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu, chimene iwo wokha achivomeranso, kuti kudzakhala kuwuka kwa akufa, kwa wolungama ndi wosalungama.
  4642. Act 24:16 Ndipo m’menenso ine ndidziyesera ndekha, kuti ndakhala nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu, ndi [kwa] anthu.
  4643. Act 24:17 Tsopano zitapita zaka zambiri ine ndidadza kutengera zachifundo mtundu wanga, ndi zopereka.
  4644. Act 24:18 Koma padali Ayuda ena a ku Asiya adandipeza ine woyeretsedwa m’Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso.
  4645. Act 24:19 Amene adayenera atakhala kuno pamaso panu, ndi kutsutsa, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.
  4646. Act 24:20 Kapena mulole iwo omwewa ali [kunowa] anene, ngati iwo apeza chochita choyipa chilichonse mwa ine, pamene ndidayimirira ine pamaso pa bwalo la akulu,
  4647. Act 24:21 Koma liwu irilimodzi lokha, limene ndidafuwula poyimirira pakati pawo, Kunena za kuwuka kwa kufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.
  4648. Act 24:22 Ndipo pamene Felikisi adamva zinthu izi, pokhala nacho chidziwitso chonse cha njira [imeneyo], iye adawachedwetsa iwo, ndipo anati, Pamene Lisiyasi kapitawo wamkulu akadzatsika kubwera, ine ndidzapanga chisankho za nkhani yanu.
  4649. Act 24:23 Ndipo adalamulira kenturiyoni kuti asunge Paulo, ndi kuti [iye] akhale nawo ufulu, ndi kuti iye asaletse abale ake kumtumikira kapena kudza kwa iye.
  4650. Act 24:24 Ndipo atapita masiku ena, pamene Felikisi adadza ndi mkazi wake Drusila, amene adali Myuda, anatuma kuyitana Paulo, ndipo adamva iye zokhudza chikhulupiriro mwa Khristu Yesu.
  4651. Act 24:25 Ndipo m’mene ankafotokozerana maganizo pa za chilungamo, chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi adanjenjemera, ndipo anayankha, Pita pa njira yako kwa nthawi ino; pamene ndikhala ndi nyengo yabwino, ine ndidzakuyitana iwe.
  4652. Act 24:26 Iye adayembekezeranso kuti ndalama zidayenera kuperekedwa kwa iye ndi Paulo, kuti mwina akhoze kum’masula iye: mwa ichi adamuyitana iye kawirikawiri, ndi kukamba ndi iye.
  4653. Act 24:27 Koma zitapita zaka ziwiri Porkiyasi Festasi adalowa m’chipinda cha Felikisi: ndipo Felikisi pofuna kusangalatsa Ayuda adamsiya Paulo womangidwa.
  4654. Act 25:1 Tsopano pamene Festasi adabwera kulowa m’chigawocho, atapita masiku atatu iye adakwera kuchokera ku Kayisareya kumka ku Yerusalemu.
  4655. Act 25:2 Kenaka wansembe wamkulu ndi wamkulu wa Ayuda adamuwuza iye zom’nenera Paulo, ndipo anampempha iye,
  4656. Act 25:3 Ndipo anampempha kukonderedwa kwa kumtsutsa iye, kuti iye athe kutuma kwa iye ku Yerusalemu, atamlalira iye m’njira kuti amuphe iye.
  4657. Act 25:4 Koma Festasi adayankha, kuti Paulo asungike ku Kayisareya, ndi kuti iye mwini adzanyamuka posachedwa [kupitako].
  4658. Act 25:5 Choncho aloleni iwo, iye anati, amene pakati pa inu amene akhoza, amuke kutsika ndi [ine], ndipo am’nenere munthu uyu, ngati kuli kanthu kachoyipa mwa iye.
  4659. Act 25:6 Ndipo m’mene iye adatsotsa pakati pa iwo masiku woposera khumi, iye adatsikira kupita ku Kayisareya; ndipo tsiku lotsatira adakhala pa mpando wachiweruziro nalamulira kuti Paulo abweretsedwe.
  4660. Act 25:7 Ndipo m’mene iye adabwera, Ayuda amene adatsika kubwera kuchokera ku Yerusalemu adayimirira pozungulirapo, ndipo anam’nenera zifukwa zambiri ndi zazikulu zotsutsa Paulo, zimene iwo sakadakhoza kuzitsimikizira.
  4661. Act 25:8 Pamene adali kudziyankhira yekha, [adanena], Kapena motsutsa chilamulo cha Ayuda, kapena motsutsa kachisi, kapenanso motsutsa Kayisara, ine sindidachimwira china chilichonse ayi.
  4662. Act 25:9 Koma Festasi, pofuna kuwasangalatsa Ayuda, adayankha Paulo, ndipo anati, Kodi iwe ufuna kukwera kumka ku Yerusalemu, ndipo komweko kuweruzidwa za zinthu izi ndi ine?
  4663. Act 25:10 Kenaka adati Paulo, Ine ndiri kuyimirira pa mpando wa chiweruziro wa Kayisara, pamene ine ndiyenera kuti kuweruzidwe: kwa Ayuda ine sindiwachitira kanthu koyipa, monga inu mudziwa bwino lomwe.
  4664. Act 25:11 Pakuti ngati ine ndiri wochita zoyipa, kapena ndachita kanthu kakuyenera imfa, ine sindikana kufa: koma ngati palibe chimodzi cha zinthu izi zimene awa andinenera nazo ine, palibe munthu akhoza kundipereka kwa iwo. Ine ndipempha chigamulo chachiwiri kwa Kayisara.
  4665. Act 25:12 Kenaka Festasi, atakambirana ndi akulu a bwalo, adayankha, Kodi iwe wapempha chigamulo chachiwiri kwa Kayisara? Kwa Kayisala iwe udzapita.
  4666. Act 25:13 ¶Ndipo atapita masiku ena mfumu Agripa ndi Bernike adabwera ku Kayisareya, kudzamuyankhula Festasi.
  4667. Act 25:14 Ndipo pamene iwo atatsotsako masiku ambiri, Festasi adafotokoza za Paulo kwa mfumu, kunena kuti, Pali munthu wina adamsiya m’nsinga Felikisi:
  4668. Act 25:15 Za amene, pamene ine ndidali ku Yerusalemu, ansembe akulu ndi akulu a Ayuda adandidziwitsa [ine], kupempha [kuti pakhale] chiweruzo chomtsutsa iye.
  4669. Act 25:16 Kwa iwo amene ine ndayankha, Si ali machitidwe a Aroma kupereka munthu aliyense kuti afe, pasadayambe kuti iye amene woneneredwayo akhale mopenyana nawo iwo akum’nenera maso ndi maso, ndi kukhala napo podziyankhira yekha zokhudza mlandu umene uneneredwa pa iye.
  4670. Act 25:17 Choncho, pamene iwo [adasonkhana] kubwera pano, popanda kuchedwetsa kulikonse pa tsiku lotsatira ndidakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndidalamulira kuti munthuyo ambweretse kuno.
  4671. Act 25:18 Amene pamene wom’neneza adayimirira, iwo sadabweretse kalikonse kom’nenera ka zinthu zotero monga ndidazilingalira ine:
  4672. Act 25:19 Koma adali nawo mafunso ena wotsutsana naye a chipembedzo cha iwo wokha, ndi za wina Yesu, amene adafa, amene Paulo adatsimikizira kuti ali ndi moyo.
  4673. Act 25:20 Ndipo chifukwa ine ndinakayika za mafunso otero, ine ndidamfunsa [iye] ngati angafune kupita ku Yerusalemu, ndipo komweko kuweruzidwa za nkhani iyi.
  4674. Act 25:21 Koma pamene Paulo adapempha kuti asungidwe kuti akatulukire kwa Augustasi, ine ndidalamula kuti iye asungidwe kufikira pamene ine ndidzamtumiza kwa Kayisara.
  4675. Act 25:22 Kenaka Agripa adati kwa Festasi, Ine ndifuna nanenso ndimve ndekha munthuyo. Mawa, adati iye, inu mudzamva iye.
  4676. Act 25:23 Ndipo tsiku lotsatira tsono, pamene Agripa adabwera, ndi Bernike, ndi chimwambo chachikulu, ndipo pamene adalowa pa bwalo la milandu, pamodzi ndi akapitawo akulu, ndi amuna wotsogolera a mzinda, pakulamulira kwa Festasi Paulo adabweretsedwa pamenepo.
  4677. Act 25:24 Ndipo Festasi adati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli pamodzi ndi ife pano, inu muwona munthu uyu, za amene khamu lonse la Ayuda achita ndi ine, ku Yerusalemu, ndi kunonso, kufuwula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.
  4678. Act 25:25 Koma pamene ine ndidapeza kuti iye sadachita kanthu koyenera imfa; ndipo kuti iye yekha adapempha kuti akatulukire kwa Augustasi, ine ndatsimikiza mtima kum’tumiza iye.
  4679. Act 25:26 Amene kwa iye ndiribe ine kanthu kotsimikiza kakulembera kwa mbuye wanga. Mwa ichi ine ndam’bweretsa iye kuno pamaso pa inu, ndipo makamaka pamaso pa inu, Mfumu Agripa, kuti, akatha kuyesedwa, ine ndikhoze kukhala nako kanthu kakuti ndilembe.
  4680. Act 25:27 Pakuti chiwoneka kwa ine chopanda nzeru kutumiza wamsinga, ndiponso popanda kusonyeza zifukwa za mlandu [woyikidwa] motsutsa iye.
  4681. Act 26:1 Kenaka Agripa adati kwa Paulo, Iwe uli wololedwa kudzinenera wekha. Kenaka Paulo adatambasula dzanja, ndipo anadziyankhira yekha.
  4682. Act 26:2 Ine ndidziganizira ndekha wosangalala, mfumu Agripa, chifukwa ine ndidzadziyankhira ndekha lero pamaso panu zokhudza zinthu zonse zimene Ayuda andinenera nazo ine:
  4683. Act 26:3 Makamaka [chifukwa ine ndidziwa] inu muli katswiri mu miyambo yonse ndi mafunso amene ali pakati pa Ayuda: mwa ichi ine ndikupemphani inu kuti mundimvere ine moleza mtima.
  4684. Act 26:4 Chikhalidwe cha moyo wanga kuyambira pa ubwana wanga, amene adali poyamba adali pakati pa mtundu wanga ku Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse:
  4685. Act 26:5 Amene anandidziwa ine kuyambira pachiyambi, ngati akadafuna kuchitapo umboni, kuti nditakhala monga mwa mpatuko wam’panipani kwambiri wa chipembedzo chathu [chimene] ine ndidali Mfarisi.
  4686. Act 26:6 Ndipo tsopano ine ndiyimirira ndipo ndiri kuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha lonjezano lopangidwa ndi Mulungu kwa makolo athu.
  4687. Act 26:7 Kwa amene [lonjezano] kwa mafuko athu khumi ndi awiri, mowona mtima kutumikira [Mulungu] kosapumula usiku ndi usana, adayembekezera kuti lidza. Chifukwa cha chiyembekezo chimenecho, mfumu Agripa, ine ndiri kutsutsidwa ndi Ayuda.
  4688. Act 26:8 Kodi chiganizidwa kukhala chinthu chosakhulupirika kwa inu bwanji, kuti Mulungu awukitse akufa?
  4689. Act 26:9 Ine ndithudi ndinaganiza mwa ine ndekha, kuti ndiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu wa ku Nazareti.
  4690. Act 26:10 Chinthu chimenenso ine ndidachita m’Yerusalemu: ndipo ambiri a woyera mtima ine ndidatsekera m’ndende, nditalandira ulamuliro kuchokera kwa ansembe akulu; ndipo pamene iwo amaphedwa, ine ndidalankhula mawu anga kuwatsutsa [iwo].
  4691. Act 26:11 Ndipo ndidawalanga iwo kawirikawiri musunagoge iliyonse, ndi kuwakakamiza [iwo] kuti anene zonyoza Mulungu; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo, ine ndidawazunza [iwo] ngakhale kufikira ku mizinda ya kunja.
  4692. Act 26:12 Pameneponso pamene ndinkapita ine ku Damasikasi ndi ulamuliro ndi ntchito yakuti ndigwire motumidwa kuchokera kwa ansembe akulu.
  4693. Act 26:13 Dzuwa liri pa liwombo, Mfumu, Ine ndidawona panjira kuwunika kuchokera kumwamba, koposa kuwala kwa dzuwa, kukuwala pondizinga ine ndi iwo amene adali paulendo pamodzi ndi ine.
  4694. Act 26:14 Ndipo pamene ife tonse tidagwa pansi, ine ndidamva mawu akunena kwa ine, ndi kunena m’chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, chifukwa chiyani undizunza ine? [Kuli] kovuta kwa iwe kuti ulimbane ndi zisonga.
  4695. Act 26:15 Ndipo ine ndidati, Ndinu yani, Ambuye? Ndipo iye adati, Ine ndine Yesu amene iwe umzunza.
  4696. Act 26:16 Komatu uka, ndi kuyimirira pamapazi ako: pakuti ine ndidawonekera iwe chifukwa cha ichi, kukupanga iwe mtumiki ndi mboni ya zinthu izi zimene iwe waziwona; ndi za zinthu izo m’zimene ine ndidzakuwonekera iwe;
  4697. Act 26:17 Kukulanditsa iwe kwa anthu, ndi [kwa] Amitundu, kwa iwo amene tsopano ine ndikutuma.
  4698. Act 26:18 Kutsegula maso awo, [ndi] kuwatembenuza [iwo] kuchokera kumdima kubwera ku kuwunika, ndi [kuchokera] ku mphamvu ya Satana kubwera kwa Mulungu, kuti iwo akhoze kulandira chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa pakati pa iwo a kuyeretsedwa ndi chikhulupiriro chimene chili mwa ine.
  4699. Act 26:19 Pameneponso, Mfumu Agripa, ine sindidakhala wosamvera ku masomphenya a kumwambawo:
  4700. Act 26:20 Koma ndidasonyeza poyamba kwa iwo ku Damasikasi, ndi ku Yerusalemu, ndi m’madera onse a Yudeya, ndipo [kenaka] kwa Amitundu, kuti iwo alape ndi kutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.
  4701. Act 26:21 Pa zifukwa izi Ayuda adandigwira ine m’kachisi, ndipo anayesayesa kundipha [ine].
  4702. Act 26:22 Choncho polandira thandizo la Mulungu, ine ndiripo kufikira lero, kuchitira umboni kwa ang’ono ndi akulu, osanena zinthu zina komatu zinthu zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzafika:
  4703. Act 26:23 Kuti Khristu ayenera amve zowawa, [ndi] kuti iye akhale woyamba amene ayenera kuwuka kwa akufa, ndi kuwonetsera kuwunika kwa anthu, ndi kwa Amitundu.
  4704. Act 26:24 ¶Koma pamene adali kudziyankhulira mwiniyekha, Festasi adati ndi mawu okwera, Paulo, iwe uli wopenga; kuphunzira kwambiri kwakuchititsa iwe misala.
  4705. Act 26:25 Koma iye adati, Ine sindine wamisala, Festasi womveka koposa; koma ndilankhula kutulutsa mawu achowonadi ndi umunthu wabwino.
  4706. Act 26:26 Pakuti mfumuyo idziwa za zinthu izi, amene ine ndiyankhula pamaso pakenso momasuka: pakuti ine ndatsimikizika kuti palibe kalikonse ka zinthu izi kali kobisikira kwa iye; pakuti chinthu ichi sichidachitika m’seri.
  4707. Act 26:27 Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ine ndidziwa kuti mukhulupirira.
  4708. Act 26:28 Kenaka Agripa adati kwa Paulo, Pafupi iwetu ukadandikopa ine kuti ndikhale Mkhristu.
  4709. Act 26:29 Ndipo Paulo adati, Ndikadakonda kuti Mulungu, kuti osati inu nokha, komanso iwo onse amene akundimva ine lero, akadakhala onse pafupifupi, ndi zonse pamodzi monga ngati momwe ndiri ine, kupatula nsinga izi.
  4710. Act 26:30 Ndipo pamene iye adanena motero, mfumu idayimirira, ndi kazembe, ndi Bernike, ndi iwo amene adakhala nawo pamodzi.
  4711. Act 26:31 Ndipo pamene adali atapita pambali, adayankhula pakati pa iwo wokha, kunena kuti, Munthu uyu sachita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.
  4712. Act 26:32 Kenaka Agripa adati kwa Festasi, Munthu uyu akadakhoza kumasulidwa, akadapanda kupempha chigamulo chachiwiri kwa Kayisara.
  4713. Act 27:1 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m’chombo kumka ku Itale, iwo adapereka Paulo ndi andende ena kwa [wina] dzina lake Juliyasi, kenturiyoni wa gulu la Augustasi.
  4714. Act 27:2 Ndipo m’mene tidalowa m’chombo cha ku Adramitiyamu, ife tidanyamuka, kutanthawuza kuti kuyenda ku malo a ku mbali ya Asiya; ndipo [wina] Aristarkasi m’Makedoniya wa ku Tesalonika, pokhala ali ndi ife.
  4715. Act 27:3 Ndipo [tsiku] lotsatira tidakocheza pa Sidoni. Ndipo Juliyasi adachitira mwachikondi Paulo, ndipo anampatsa [iye] ufulu kuti apite kwa abwenzi ake kuti akadzipumitse yekha.
  4716. Act 27:4 Ndipo pamene ife tidanyamuka kuchoka kumeneko, ife tidapita kunsi kwa Sayipulasi, chifukwa mphepo idawomba moyang’anana [nafe].
  4717. Act 27:5 Ndipo pamene ife tidapyola pa nyanja ya Silisiya ndi Pamfiliya, ife tidafika ku Mira, [mzinda] wa Lisiya.
  4718. Act 27:6 Ndipo pamenepo kenturiyoni adapezako chombo cha ku Alekizandria chilikupita ku Itale; ndipo iye adatikweza ife m’chimenecho.
  4719. Act 27:7 Ndipo m’mene tidayenda pa nyanja pang’onopang’ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Knidasi, mphepo yosatilolanso ife, ife tidapita kunsi kwa Krete, pandunji pa Salimone;
  4720. Act 27:8 Ndipo, popazapo movutika, tidabwera ku malo amene dzina lake litchedwa Pokocheza Pokoma; pafupi ndi pamenepo padali mzinda [wa] Laseya.
  4721. Act 27:9 Tsopano itapita nthawi yambiri, ndipo pamene kuyenda panyanja kudayamba kukhala kowopsa, chifukwa kusala chakudya kudali kutapita kale, Paulo adawachenjeza [iwo],
  4722. Act 27:10 Ndipo ananena kwa iwo, Amuna, Ine ndiwona ine kuti ulendo ukhala ndi kuvulala ndi chiwonongeko chachikulu, osati kwa katundu yekha ndi chombo chokha, komanso kwa miyoyo yathu.
  4723. Act 27:11 Komabe kenturiyoni adakhulupirira pa wa pa chiwongolero ndi mwini wa chombo, koposa zinthu izo zimene zidayankhulidwa ndi Paulo.
  4724. Act 27:12 Ndipo chifukwa doko silidakoma kugonapo nyengo yachisanu, mbali ya gulu lalikulu lidachita uphungu kuti tinyamukenso kumeneko, ngati mwa njira ina iliyonse iwo akhoze kufikira ku Fenisi, ndi [kumeneko] kugonako; [limene liri] doko la ku Krete, ndipo liri moloza kumwera cha ku madzulo ndi kumpoto cha ku madzulo.
  4725. Act 27:13 Ndipo pamene mphepo yamwera imawomba pang’onopang’ono, poganiza kuti iwo adali atafikira cholinga [chawo], adamasula nangula [kumeneko], ndipo anayenda pa nyanja kudutsa m’mbali mwa Krete.
  4726. Act 27:14 Koma asanayende ulendo wautali padawomba mphepo ya namondwe motsutsana [nawo], imene itchedwa Uroklayidoni.
  4727. Act 27:15 Ndipo pamene chombo chinagwidwa, ndipo sichidakhoza kupitanso kulowa m’mphepo mokomana nayo, ife tidangoleka kuti tingoyendetsedwa.
  4728. Act 27:16 Ndipo popita kunsi kwa chisumbu china chimene chitchedwa Klauda, ife tidali ndi ntchito yambiri yakumangitsa mabwato a chombocho:
  4729. Act 27:17 Chimene pamene iwo adawakweza, adagwiritsa ntchito zothandizira, napititsa zingwe pansi pa chombo; ndipo, pakuwopa kuti mwina iwo angagwere mu michenga yotitimira, adatsitsa mathanga, ndipo adayendetsedwa motero.
  4730. Act 27:18 Ndipo poponyedwa kopambana ndi namondwe, [tsiku] lotsatira adapepuza chombo;
  4731. Act 27:19 Ndipo [tsiku] lachitatu ife tidataya ndi manja athu zipangizo za chombo.
  4732. Act 27:20 Ndipo m’mene dzuwa kapena nyenyezi kwa masiku ambiri sizidawoneka, ndipo namondwe wosati wam’ng’ono adagwera pa [ife], chiyembekezo chonse chakuti tipulumuka chidatichokera pomwepo.
  4733. Act 27:21 Koma atadziletsa kwa nthawi yayikulu wosadya kanthu, Paulo adayimirira pakati pawo, ndipo anati, Amuna, inu mudayenera kumvera kwa ine, ndi kusachoka ku Krete, ndipo sitikadadzitengera kuwonongeka ndi kutayika kotere uku.
  4734. Act 27:22 Ndipo tsopano ndikulangizani inu mukhale wolimbika mtima; pakuti sipadzakhala kutaya kwa moyo wa [munthu aliyense] pakati pa inu, koma kwa chombo.
  4735. Act 27:23 Pakuti adayimirira pambali pa ine usiku walero mngelo wa Mulungu, amene ndiri wake, ndiponso amene ine ndimtumikira,
  4736. Act 27:24 Kunena kuti, Usawope, Paulo; iwe uyenera kubweretsedwa pamaso pa Kayisara: ndipo, tawona, Mulungu wakupatsa iwe onse amene akuyenda nawe panyanja pamodzi.
  4737. Act 27:25 Mwa ichi, amuna, khalani olimbika mtima: pakuti ine ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzachitika monga momwe kudanenedwa kwa ine.
  4738. Act 27:26 Ngakhale ziri motero chomwecho ife tiyenera kuponyedwa pa chisumbu china chake.
  4739. Act 27:27 ¶Koma usiku wakhumi ndi chinayi udafika, pamene ife tinali kutengedwa kwina ndi kwina m’nyanja ya Adriyatiki, pafupifupi pakati pa usiku amalinyero adayerekeza kuti adalikuyandikira pafupi ndi dziko lina;
  4740. Act 27:28 Ndipo adayesa kuya kwa madzi, ndipo anapeza [ali] mapazi asanu ndi limodzi: ndipo atapita patsogolo pang’ono, adayesanso, ndipo anapeza [ili] mikwamba khumi ndi isanu.
  4741. Act 27:29 Ndipo pakuwopa kuti mwina ife tingagwere pamiyala, iwo adaponya anangula anayi kutulutsira kumbuyo kwa chombo, ndipo iwo anakhumba kuche.
  4742. Act 27:30 Ndipo m’mene amalinyero adatsala pang’ono kuthawa kutuluka m’chombo, iwo atatsitsira bwato m’nyanja, monga ngati iwo adati akadatulutsa kuponya anangula kutsogolo [kwa chombo],
  4743. Act 27:31 Paulo adati kwa kenturiyoni ndi asirikali, Pokhapo ngati awa atakhala m’chombo, inu simungathe kupulumuka.
  4744. Act 27:32 Kenaka asirikali adadula zingwe za bwato, ndi kulisiya kuti ligwe.
  4745. Act 27:33 Ndipo pamene kudalikucha, Paulo adawachenjeza [iwo] onse kuti adye, kunena kuti, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinayi limene mwakhala ndi kupitirira kusala kudya, osadya kalikonse.
  4746. Act 27:34 Mwa ichi ine ndikupemphani inu mutenge kanthu [kena] kakudya: pakuti ichi ndi [chofunika] kwa thanzi lanu; pakuti sipadzakhala tsitsi limodzi lakugwa kuchokera kumutu kwa wina aliyense wa inu.
  4747. Act 27:35 Ndipo pamene adanena motero, iye adatenga mkate, ndipo anapereka mayamiko kwa Mulungu pamaso pa iwo onse; ndipo m’mene adawunyema [uwo], iye adayamba kudya.
  4748. Act 27:36 Kenaka iwo onse adali wolimba mtima, ndipo iwonso adadyako chakudya [china].
  4749. Act 27:37 Ndipo ife tonse m’chombo tidali anthu mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza mphambu zisanu ndi m’modzi.
  4750. Act 27:38 Ndipo m’mene adali atadya kokwanira, adapepuza chombo, ndipo anataya tirigu m’nyanja.
  4751. Act 27:39 Ndipo pamene kudacha, iwo sadazindikira dzikolo: koma adawona pali dambo laling’ono lina lokhala ndi gombe; mu limenero iwo adaganiza, ngati kukadakhala kotheka, kuyendetsamo chombo.
  4752. Act 27:40 Ndipo m’mene adakweza anangula, iwo adadzisiya [wokha] kulowa m’nyanja, ndipo anamasula zingwe zomanga chiwongolero, ndipo anakweza thanga la kumutu ku mphepo, ndipo analunjikitsa ku gombe.
  4753. Act 27:41 Ndipo pogwera pamalo pamene padakumana nyanja ziwiri, adakokera chombo kumtunda; ndipo kutsogolo kwa chombo kudapanidwa, ndipo kudakhala kosasunthika, koma kumbuyo kudasweka ndi kuwomba kwa mphamvu kwa mafunde.
  4754. Act 27:42 Ndipo uphungu wa asirikali udali wakuti aphe andende, kuti mwina ena a iwo angasambire kutuluka, ndi kuthawa.
  4755. Act 27:43 Koma kentuliyoni, pofuna kupulumutsa Paulo, adawaletsa asachite cholinga [chawo]; ndipo analamula kuti iwo amene angathe kusambira ayambe iwo [wokha] kudziponya [m’nyanjamo], ndi kuti afike kumtunda:
  4756. Act 27:44 Ndipo wotsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa [zidutswa zosweka] za chombo. Ndipo motero kudachitika, kuti iwo onse adapulumuka [kufika] kumtunda.
  4757. Act 28:1 Ndipo pamene iwo adali atapulumuka, kenaka iwo adadziwa kuti chisumbucho chidatchedwa Melita.
  4758. Act 28:2 Ndipo anthu a dziko limenero adatiwonetsera ife zokoma zoposa: pakuti iwo adasonkha moto, ndipo adatilandira wina aliyense wa ife, chifukwa chakuti mvula idalinkugwa, ndi chifukwa cha kuzizira.
  4759. Act 28:3 Koma pamene Paulo adasonkhanitsa mtolo wa nkhuni, ndipo [anaziyika] pa moto, mudatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo idaluma ndikukakamira pa dzanja lake.
  4760. Act 28:4 Koma pamene a dziko lakunjawo adawona chirombocho [chaululu] chikulendewera pa dzanja lake, iwo adanena pakati pa iwo wokha, Popanda chikayiko munthu uyu ndiye wambanda, amene, angakhale adapulumuka m’nyanja, koma chilungamo sichimlola kukhala ndi moyo.
  4761. Act 28:5 Koma adakutumulira chirombocho kumoto, wosamva kupweteka.
  4762. Act 28:6 Ngakhale ziri motero chomwecho iwo adayang’anira pamene iye adayenera kutupa, kapena kugwa pansi ndi kufa mwadzidzidzi: koma m’mene adayang’anira kwa nthawi ndithu, ndi kusawona kupwetekedwa kutachitika pa iye, iwo adasintha maganizo awo, ndipo adanena kuti iye adali mulungu.
  4763. Act 28:7 Pa dera lomwero padali minda mwini wake ndiye mkulu wa chisumbucho, amene dzina lake linali Pabuliyasi; amene adatilandira ife, ndipo anatichereza mokoma masiku atatu.
  4764. Act 28:8 Ndipo kudachitika, kuti atate wake wa Pabuliyasi adagona wodwala nthenda ya malungo ndi yakukha mwazi: kwa iyeyu Paulo adalowa, ndipo anapemphera, nayika manja pa iye, ndipo anamchiritsa iye.
  4765. Act 28:9 Kotero pamene chidachitika ichi, enanso, amene adali nazo nthenda m’chisumbumo, adadza, ndipo anachiritsidwa:
  4766. Act 28:10 Amenenso adatichitira ife ulemu ndi maulemu ambiri; ndipo pamene ife tidanyamuka, iwo adatisenzetsa [ife] ndi zinthu zotero monga zinalizosowa.
  4767. Act 28:11 Ndipo itapita miyezi itatu ife tidanyamuka m’chombo cha ku Alekizandria, chomwe chidagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chimene chizindikiro chake chidali Kasta ndi Polukisi.
  4768. Act 28:12 Ndipo pamene tidakocheza pa Sirakusi, ife tidatsotsa [kumeneko] masiku atatu.
  4769. Act 28:13 Ndipo kuchokera kumeneko tidazungulira ndi kutembenuka kuzungulira kufufuza mbali, ndipo tinabwera ku Rhegiyamu: ndipo litapita tsiku limodzi mphepo yamwera idawomba, ndipo tsiku lotsatira tidabwera ku Putiyoli:
  4770. Act 28:14 Kumene tidapeza abale, ndipo iwo adatipempha tikhale nawo masiku asanu ndi awiri: ndipo potero tidapita ku Roma.
  4771. Act 28:15 Ndipo kuchokera kumeneko, pamene abalewo adamva za ife, iwo adadza kudzakomana nafe kuchokera kubwalo la malonda la Apiyi, ndi ku nyumba za Alendo zitatu: amene pamene Paulo adawawona, iye adayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.
  4772. Act 28:16 Ndipo pamene tidabwera ku Roma, kenturiyoni adapereka a m’ndende kwa kapitawo wamkulu wa ndende: koma Paulo adakhala pa yekha ndi msirikali womdikirira iye.
  4773. Act 28:17 ¶Ndipo kudachitika, kuti atapita masiku atatu Paulo adayitana akulu wa Ayuda pamodzi: ndipo pamene atasonkhana, iye adanena kwa iwo, Amuna [ndi] abale, ndingakhale ine sindidachita kanthu kutsutsa anthu, kapena miyambo ya makolo athu, komatu ine ndidaperekedwa wam’singa kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma.
  4774. Act 28:18 Amene, iwo pamene anandifunsafunsa ine, akadandimasula [ine] ndipite, chifukwa padalibe chifukwa choyenera imfa mwa ine.
  4775. Act 28:19 Koma pamene Ayuda adayankhulapo pakukana [ichi], ine ndidafulumizidwa mtima kupempha chigamulo chachiwiri kwa Kayisala; osati kuti ine ndidali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.
  4776. Act 28:20 Choncho pa chifukwa ichi ine ndakuyitanani inu, kuti ndikuwoneni [inu], ndi kuti ndiyankhule ndi [inu]: chifukwa chakuti pa chiyembekezo cha Israyeli ine ndamangidwa ndi unyolo uwu.
  4777. Act 28:21 Ndipo iwo adati kwa iye, Ife sitidalandira makalata wochokera ku Yudeya wokhudza inu, kapena wina wa abale amene adadza kutisonyeza kapena kuyankhula kanthu koyipa kotsutsa inu.
  4778. Act 28:22 Koma tifuna kumva kwa iwe zimene iwe uganiza: pakuti monga zokhudza gulu la mpatuko uwu, ife tidziwa kuti kwina kulikonse uli woneneredwa mowutsutsa.
  4779. Act 28:23 Ndipo pamene adamkonzera iye tsiku, padadza ambiri kwa [iye] kulowa kunyumba [yake]; kwa amene iye adawafotokozera kuwamasulira ndi kuchitira umboni ufumu wa Mulungu, kutsimikizira iwo zokhudza Yesu, zochokera m’chilamulo cha Mose, ndi [zochokera] mwa aneneri, kuyambira m’mamawa kufikira madzulo.
  4780. Act 28:24 Ndipo ena adakhulupirira zinthu zimene zimalankhulidwazo, ndipo ena sadakhulupirire.
  4781. Act 28:25 Ndipo pamene iwo sadavomerezana pakati pawo, iwo adanyamuka, Paulo atatha kunena mawu amodzi, Mwabwino adayankhula Mzimu Woyera mwa Yesaya m’neneri kwa makolo athu,
  4782. Act 28:26 Kunena kuti, Pita kwa anthu awa, ndi kunena kuti, Kumva inu mudzamva, ndipo simudzamvetsetsa ayi; ndipo kupenya inu mudzapenya, ndipo wosawona ayi;
  4783. Act 28:27 Pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo makutu awo ngosatha kumva, ndipo maso awo iwo adawatseka; kuti mwina iwo angawone ndi maso [awo], ndi kumva ndi makutu [awo], ndi kuzindikira ndi mtima [wawo], ndi kutembenuka, ndipo ine ndingawachiritse iwo.
  4784. Act 28:28 Choncho chidziwike kwa inu, kuti chipulumutso cha Mulungu chitumizidwa kwa Amitundu; ndi [kuti] iwo adzachimva icho.
  4785. Act 28:29 Ndipo pamene adanena mawu awa, Ayuda adanyamuka, ndipo adali ndi kufotokozerana maganizo kwambiri pakati pa iwo wokha.
  4786. Act 28:30 ¶Ndipo Paulo adakhala zaka ziwiri za mphumphu m’nyumba yake yolipira, ndipo analandira onse amene adabwera kwa iye.
  4787. Act 28:31 Kulalikira ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa zinthu izo zimene zikhudzana ndi Ambuye Yesu Khristu, ndi kulimbika konse, popanda munthu womletsa iye.
  4788. Rom 1:1 Paulo mtumiki wa Yesu Khristu woyitanidwa [kukhala] mtumwi, wopatulidwa ku uthenga wabwino wa Mulungu.
  4789. Rom 1:2 (Umene iye adalonjeza m’mbuyomo ndi mawu a aneneri ake m’malembo woyera)
  4790. Rom 1:3 Wokhudza za Mwana wake wamwamuna Yesu Khristu Ambuye wathu, amene adapangidwa mwa mbewu ya Davide, monga mwa thupi;
  4791. Rom 1:4 Ndipo adalengezedwa [kuti] ndi Mwana wamwamuna wa Mulungu ndi mphamvu, monga mwa mzimu wachiyero, mwa kuwuka kwa akufa;
  4792. Rom 1:5 Mwa amene ife tidalandira naye chisomo ndi utumwi, mwakuti tikamvere chikhulupirirocho pakati pa mitundu yonse, chifukwa cha dzina lake;
  4793. Rom 1:6 Amene pakati pawo muli inunso, woyitanidwa a Yesu Khristu.
  4794. Rom 1:7 Kwa onse a ku Roma, wokondedwa a Mulungu, Woyitanidwa [kuti akhale] woyera mtima; Chisomo chikhale ndi inu ndi mtendere kuchokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
  4795. Rom 1:8 Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idalankhulidwa pa dziko lonse lapansi.
  4796. Rom 1:9 Pakuti Mulungu ali mboni yanga amene ndim’tumikira mu mzimu wanga mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake wamwamuna, kuti kosalekeza ndikumbukira inu, masiku onse m’mapemphero anga;
  4797. Rom 1:10 Kupempha, ngati nkutheka tsopano patapita nthawi ndikhale ndi ulendo wopambana mwa chifuniro cha Mulungu wakudza kwa inu.
  4798. Rom 1:11 Pakuti ndilakalaka kuwonana ndi inu, kuti ndikayikize kwa inu mphatso zina za uzimu, kuti inu mukhale okhazikika;
  4799. Rom 1:12 Ndiko kuti, ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse, chanu ndi changa.
  4800. Rom 1:13 Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mukhale wosadziwa, kuti kawirikawiri ndikalingalira mu mtima kuti ndikafike kwa inu, (koma ndinaletsedwa kufikira lero,) kuti ndikakhale ndi zipatso zina mwa inunso, monga mwa anthu Amitundu ena.
  4801. Rom 1:14 Ine ndine wangongole kwa Ahelene ndi kwa Akunja; kwa a nzeru ndi wopanda nzeru.
  4802. Rom 1:15 Kotero, monga momwe ziri mwa ine, ndirikufuna kulalikira uthenga wabwino kwa inunso a ku Roma.
  4803. Rom 1:16 Pakuti sindichita manyazi ndi uthenga wabwino wa Khristu: pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa kwa aliyense amene akhulupirira; kuyambira kwa Myuda, ndiponso Mhelene.
  4804. Rom 1:17 Pakuti m’menemo chawonetsedwa chilungamo cha Mulungu chovumbulutsidwa kuchokera ku chukhulupiriro kupita ku chikhulupiriro: monga kwalembedwa, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhululpiriro.
  4805. Rom 1:18 ¶Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera kumwamba, wavumbulutsidwa pa chisapembedzo chonse chosalungama cha anthu, amene agwira chowonadi m’chosalungama chawo;
  4806. Rom 1:19 Chifukwa chimene chiyenera kudziwidwa cha Mulungu chawoneka mkati mwawo; pakuti Mulungu adachiwonetsera [icho] kwa iwo.
  4807. Rom 1:20 Pakuti zinthu zosawoneka zake kuchokera pa kulengedwa kwa dziko lapansi zawoneka bwino, zozindikirika ndi zinthu zolengedwa, [ngakhale] mphamvu yake yosatha ndi Umulungu wake; kuti iwo akhale opanda chowiringula:
  4808. Rom 1:21 Chifukwa kuti, pamene adadziwa Mulungu, sadam’chitira [iye] ulemu woyenera Mulungu, ndipo sadamuyamika; koma adakhala wopanda pake m’maganizo awo, ndipo mtima wawo wopulukira unadetsedwa.
  4809. Rom 1:22 Povomereza eni wokha kuti ali anzeru iwo adakhala wopusa.
  4810. Rom 1:23 Ndipo adasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, nawufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu wowonongeka, ndi cha mbalame, ndi cha nyama za miyendo inayi, ndi cha zinthu zokwawa.
  4811. Rom 1:24 Mwa ichi Mulungu adawapereka iwo ku zonyansa kudzera m’zilakolako za mitima yawo, kuchititsana matupi awo wina ndi mzake zamanyazi.
  4812. Rom 1:25 Amene adasintha chowonadi cha Mulungu kukhala bodza, napembedza ndikutumikira cholengedwa koposa Wolengayo, amene ali wodalitsika nthawi yosatha. Amen.
  4813. Rom 1:26 Pa chifukwa cha ichi Mulungu adawapereka iwo kuzilakolako zoyipa: pakuti angakhale akazi awo adasandutsa machitidwe awo achilengedwe akakhale machitidwe otsutsana ndi chilengedwe.
  4814. Rom 1:27 Ndipo chimodzimodzinso amuna adasiya magwiritsidwe ntchito a chilengedwe cha akazi, natenthetsana m’chilakolako chawo wina ndi mzake; amuna ndi amuna adachitirana chimene chili chamanyazi, ndipo adalandira mwa iwo wokha mphotho ya kulakwa kwawo komwe kunawayenera
  4815. Rom 1:28 Ndipo monga iwo adakana kukhala naye Mulungu m’chidziwitso [chawo], adawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zomwe ziri zosayenera.
  4816. Rom 1:29 Wodzadzidwa ndi zosalungama zonse, chiwerewere, kuyipa, kusilira, dumbo; wodzala ndi kaduka, kupha, ndewu, chinyengo, udani waukulu, amanong’onong’o;
  4817. Rom 1:30 Akazitape, akumuda Mulungu, achipongwe, wodzitama, amatukutuku, woyambitsa zoyipa, wosamvera akuwabala,
  4818. Rom 1:31 Wosamvetsetsa, womphwanya mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, wosakhululuka, wopanda chifundo.
  4819. Rom 1:32 Amene adziwa chiweruzo chake cha Mulungu; kuti iwo amene achita zinthu zotere ayenera imfa, sangozichita iwo wokha, koma akondwera nawo iwo akuzichita izi.
  4820. Rom 2:1 Choncho uli wopanda chowiringula, munthu iwe, amene uweruza: pakuti m’mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha; pakuti iwe wakuweruza, umachita zinthu zomwezo.
  4821. Rom 2:2 Koma tidziwa kuti chiweruzo cha Mulungu chili mwa chowonadi kwa iwo amene akuchita motsutsana ndi zinthu zotere.
  4822. Rom 2:3 Ndipo uganiza kodi izi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zinthu zotere, ndipo uzichitanso zomwezo, kuti iwe udzapulumuka pa chiweruzo cha Mulungu?
  4823. Rom 2:4 Kapena upeputsa kodi chuma cha ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukutsogolera iwe ku kulapa?
  4824. Rom 2:5 Koma kolingana ndi kuwuma ndi kusalapa mtima kwako, ulikudziwunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
  4825. Rom 2:6 Amene adzapereka kwa munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake.
  4826. Rom 2:7 Kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisawonongeko mwa kupirira pa kuchitabe ntchito zabwino; moyo wosatha:
  4827. Rom 2:8 Koma kwa iwo andewu, ndi wosamvera chowonadi, koma amvera chosalungama, mkwiyo ndi ukali,
  4828. Rom 2:9 Chisawutso ndi kuwawa mtima, pa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoyipa, kwa Myuda poyamba, komanso kwa Mhelene;
  4829. Rom 2:10 Koma ulemerero, ulemu, ndi mtendere, kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kwa Myuda poyamba, komanso kwa Mhelene:
  4830. Rom 2:11 Pakuti kulibe tsankhu kwa Mulungu.
  4831. Rom 2:12 Pakuti onse adachimwa wopanda lamulo adzawonongeka wopanda lamulo: ndi onse amene adachimwa ali m’lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo.
  4832. Rom 2:13 (Pakuti womvera lamulo sakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzalungamitsidwa.
  4833. Rom 2:14 Pakuti pamene anthu Amitundu amene alibe lamulo amachita mwa chilengedwe zinthu zomwe ziri m’lamulo, amenewa, angakhale alibe lamulo, adzikhalira mwa iwo wokha lamulo;
  4834. Rom 2:15 Popeza iwo awonetsa ntchito yalamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni, ndipo maganizo [awo] nthawi ino anenezana kapena akanirana wina ndi mzake;)
  4835. Rom 2:16 Pa tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Khristu zinsinsi za anthu, monga mwa uthenga wabwino wanga.
  4836. Rom 2:17 Tawona, iwe wakutchedwa Myuda, nukhazikika pa lamulo, nudzitamandira pa Mulungu,
  4837. Rom 2:18 Nudziwa chifuniro [chake], nuvomereza zinthu zonse zimene ziri zoposa, utaphunzitsidwa kudzera m’chilamulo,
  4838. Rom 2:19 Nulimbika mu mtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene ali mu mdima.
  4839. Rom 2:20 Mlangizi wa wopanda nzeru, mphunzitsi wa tiwana, wakukhala nacho chidziwitso ndi chowonadi cha m’chilamulo.
  4840. Rom 2:21 Iwe tsono wophunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wolalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?
  4841. Rom 2:22 Iwe wonena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wodana nawo mafano, umafunkha za m’kachisi kodi?
  4842. Rom 2:23 Iwe wodzitamandira pa chilamulo, kudzera m’kuphwanya lamulo sulemekeza iwe Mulungu?
  4843. Rom 2:24 Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu Amitundu, monga kwalembedwa.
  4844. Rom 2:25 Pakuti mdulidwe ndithudi upindula, ngati iwe usunga lamulo; koma ngati uli wophwanya lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa.
  4845. Rom 2:26 Choncho ngati wosadulidwa asunga chilungamo cha chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikungayesedwe ngati mdulidwe?
  4846. Rom 2:27 Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwaniritsa chilamulo, weruza iwe, amene mwa malembo ndi mdulidwe, ulakwira lamulo?
  4847. Rom 2:28 Pakuti si ali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena [si uli] mdulidwe, umene uli wotere pamaso m’thupi:
  4848. Rom 2:29 Koma iye [ali] Myuda, amene akhala wotere mkati; ndipo mdulidwe [uli wa] mtima; mu mzimu, [ndipo] osati m’malembo ayi; amene kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu koma kwa Mulungu.
  4849. Rom 3:1 Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapena pali kupindulanji pa mdulidwe?
  4850. Rom 3:2 Zambiri munjira zonse: chachikulu, pakuti mawu a Mulungu adaperekedwa kwa iwo.
  4851. Rom 3:3 Pakuti nanga bwanji ngati ena sadakhulupirira? Kodi kusakhulupirira kwawo kupangitsa chabe chikhulupiriro cha Mulungu chopanda mphamvu?
  4852. Rom 3:4 Mulungu akuletsa: inde, lolani Mulungu akhale wowona, ndipo munthu aliyense akhale wonama; monga kwalembedwa, kuti inu mukayesedwe wolungama m’maneno anu, ndi kuti mukapambane m’mene muweruzidwa.
  4853. Rom 3:5 Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzanena chiyani ife? [Kodi] ali wosalungama Mulungu amene amabwezera? (ndilankhula monga munthu).
  4854. Rom 3:6 Mulungu akuletsa: ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji dziko lapansi?
  4855. Rom 3:7 Pakuti ngati chowonadi cha Mulungu chichulukitsa chifukwa cha bodza langaku ulemerero wake; nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa?
  4856. Rom 3:8 Ndipo osati [bwanji], (monganso ifetinenezedwa motinamizira ndi kuti ena atsimikiza kuti timanena)? Tichite zoyipa kuti zabwino zikadze? Amene kulanga kwake kuli kolungama.
  4857. Rom 3:9 Ndipo chiyani tsono? Kodiife tiri abwino [oposa iwo]? Iyayi, ndithu: pakuti tidatsimikiza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa ali pansi pa uchimo;
  4858. Rom 3:10 Monga kwalembedwa, Palibe m’modzi wolungama, ayi, palibe [ngakhale] m’modzi;
  4859. Rom 3:11 Palibe m’modzi wakumvetsetsa, palibe m’modzi wakufunafuna Mulungu;
  4860. Rom 3:12 Onsewa apatuka panjira, wonsewa pamodzi akhala wopanda phindu; palibe m’modzi wochita zabwino, ayi, palibe [ngakhale] m’modzi.
  4861. Rom 3:13 M’mero wawo [uli] manda apululu; ndi malirime agwiritsa ntchito chinyengo; ululu wa njoka [uli] pansi pa milomo yawo:
  4862. Rom 3:14 M’kamwa mwawo mudzala [ndi] zotemberera ndi zowawa;
  4863. Rom 3:15 Mapazi awo [achita] liwiro kukhetsa mwazi;
  4864. Rom 3:16 Kusakaza ndi masawutso [kuli] m’njira zawo.
  4865. Rom 3:17 Ndipo njira ya mtendere sanayidziwa;
  4866. Rom 3:18 Kulibe kumuwopa Mulungu pamaso pawo.
  4867. Rom 3:19 Ndipo tidziwa kuti zinthu zirizonse chilamulo chinena, zichiyankhulira iwo ali pansi pa chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi likatsutsidwe pamaso pa Mulungu.
  4868. Rom 3:20 Choncho pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi chilamulo.
  4869. Rom 3:21 ¶Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chopanda lamulo chawonetsedwa, chochitidwa umboni ndi chilamulo ndi aneneri;
  4870. Rom 3:22 Ndicho chilungamo cha Mulungu [chimene chichokera] mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse ndi pa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;
  4871. Rom 3:23 Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;
  4872. Rom 3:24 Alungamitsidwa kwa ulere ndi chisomo chake, mwa chiwombolo cha mwa Khristu Yesu;
  4873. Rom 3:25 Amene Mulungu adamuyika poyera [kuti akhale] nsembe yothetsa mkwiyo mwa chikhulupiriro mu mwazi wake, kuti awonetsere chilungamo chake chifukwa cha chikhululukiro cha machimo amene adachitidwa kale lomwe kudzera m’kulekerera kwa Mulungu.
  4874. Rom 3:26 Kuti awonetsere, [Ndinena], chilungamo chake m’nyengo ino; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.
  4875. Rom 3:27 Pamenepo kudzitamandira [kuli] kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iyayi; koma ndi lamulo la chikhulupiriro.
  4876. Rom 3:28 Choncho timalizira ndikunena kuti munthu alungamitsidwa mwa chikhulupiriro popanda ntchito za lamulo.
  4877. Rom 3:29 [Kodi iye] ali Mulungu wa Ayuda wokha? Iye salinso wawowa Amitundu kodi? Eya, wa Amitundunso:
  4878. Rom 3:30 Powona kuti [ndiye] Mulungu m’modzi, amene adzawayesa amdulidwe wolungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro.
  4879. Rom 3:31 Potero kodi lamulo tiyesa chabe kudzera mu chikhulupiriro? Mulungu akuletsa: inde, tikhazikitsa lamulo.
  4880. Rom 4:1 Tidzanena chiyani tsono kuti Abrahamu kholo lathu, monga mwa thupi, adapeza chiyani?
  4881. Rom 4:2 Pakuti ngati Abrahamu adalungamitsidwa mwa ntchito, iye akhala nacho [choti] adzitamandire; koma osati pamaso pa Mulungu.
  4882. Rom 4:3 Pakuti lembo likuti chiyani? Ndipo Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo chidawerengedwa kwa iye chilungamo.
  4883. Rom 4:4 Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siyiwerengedwa pa iye chisomo koma ya ngongole.
  4884. Rom 4:5 Koma kwa amene sagwira ntchito, koma akhulupirira iye amene alungamitsaiwo wosalungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo.
  4885. Rom 4:6 Monganso Davide afotokoza za mdalitso wake wa munthu, kwa iye amene Mulungu amuwerengera chilungamo chopanda ntchito.
  4886. Rom 4:7 [Kunena kuti] wodala [iwo] amene akhululukidwa zoyipa zawo, ndi iwo aphimbidwa machimo awo.
  4887. Rom 4:8 Wodala munthu amene Ambuye samuwerengera tchimo.
  4888. Rom 4:9 Mdalitso umenewu tsono [ubwera] kwa wodulidwa [okha] kodi, kapena kwa wosadulidwa womwe? Pakuti timati, chikhulupiriro chidawerengedwa kwa Abrahamuku chilungamo.
  4889. Rom 4:10 Tsono chidawerengedwa bwanji? M’mene iye adali wodulidwa kapena wosadulidwa? Sipamene adali wodulidwa ayi, koma wosadulidwa.
  4890. Rom 4:11 Ndipo iye adalandira chizindikiro cha mdulidwe, chisindikizo cha chilungamo cha chikhulupiriro chomwe [iye adali nacho] asanadulidwe: kuti kotero iye akakhale tate wa onse wokhulupirira, angakhale iwo sanadulidwa; koma kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso:
  4891. Rom 4:12 Ndiponso tate wa mdulidwe wa iwo amene si ali a mdulidwe wokha, koma wa iwonso amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha tate wathu Abrahamu, chimene [iye adali nacho] asanadulidwe.
  4892. Rom 4:13 Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolandira cholowa wa dziko lapansi silinali kwa Abrahamu kapena kwa mbewu yake, mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.
  4893. Rom 4:14 Pakuti ngati iwo alamulo [akhala] wolandira cholowa, chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndipo lonjezo layesedwa lopanda mphamvu;
  4894. Rom 4:15 Pakuti chilamulo chichita mkwiyo; pakuti pamene palibe lamulo, palibe kulakwa.
  4895. Rom 4:16 Choncho chilungamo [chichokera] m’chikulupiriro, kuti [chikhale monga] mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbewu yonse; osati kwa iyo ya za chilamulo yokha, koma kwa iyo ya za chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye tate wa ife tonse.
  4896. Rom 4:17 (Monga kwalembedwa, ndakupanga iwe tate wa mitundu yambiri,) pamaso pa Mulungu amene iye adamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndikuyitana zinthu zoti palibe, monga ngati ziripo.
  4897. Rom 4:18 Amene motsutsana ndi chiyemebekezo adakhulupirira m’chiyembekezo cha zosayembekezeka, kuti iye akakhale tate wa mitundu yambiri, monga mwa chonenedwacho; Kotero mbewu yako idzakhala yotero.
  4898. Rom 4:19 Ndipo iye wosafoka m’chikhulupiriro sadalabadira thupi lake, ndiro longa ngati lakufa pamenepo, pokhala iye ngati zaka makumi khumi, ndi kutinso mimba ya Sara imene idali yowuma.
  4899. Rom 4:20 Ndipo poyang’anira lonjezo la Mulungu sadagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma adali wolimba m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemerero;
  4900. Rom 4:21 Nakhazikikanso mu mtima kuti, chimene iye adalonjeza, adali nakonso kuthekera kwakuchichita.
  4901. Rom 4:22 Ndipo choncho ichi chidawerengedwa kwa iye chilungamo?
  4902. Rom 4:23 Tsopano ichi sichidalembedwa chifukwa cha iye yekha, kuti chidawerengedwa kwa iye;
  4903. Rom 4:24 Koma chifukwa cha ifenso, kwa iwo amene chidzawerengedwa, ngati tikhulupirira pa iye amene adawukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu kuchokera kwa akufa;
  4904. Rom 4:25 Amene adaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, nawukitsidwanso chifukwa cha chilungamo chathu.
  4905. Rom 5:1 Choncho pokhala wolungamitsidwa mwa chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
  4906. Rom 5:2 Amene mwa iye tikhoza kulowa mwa chikulupiriro m’chisomo ichi m’mene tiri kuyimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.
  4907. Rom 5:3 Ndipo sichotero chokha, komanso tikondwera m’zisawutsonso: podziwa kuti chisawutso chichita chipiriro;
  4908. Rom 5:4 Ndi chipiriro, chizolowezi; ndi chizolowezi, chiyembekezo;
  4909. Rom 5:5 Ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chidatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
  4910. Rom 5:6 Pakuti pamene tidali chikhalire wopanda mphamvu, pa nthawi yoyikika Khristu adawafera wosapembedza.
  4911. Rom 5:7 Pakuti ndi chovuta kuti munthu adzafera wina wolungama: pakuti mwina mwake wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.
  4912. Rom 5:8 Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake, m’menemo mwakuti, pokhala ife chikhalire wochimwa, Khristu adatifera ife.
  4913. Rom 5:9 Koposa tsono popeza tidayesedwa wolungama ndi mwazi wake, tidzapulumuka ku mkwiyo kudzera mwa iye.
  4914. Rom 5:10 Pakuti ngati, pameneife tidali adani ake, tidayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake wamwamuna, koposa apo, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.
  4915. Rom 5:11 Ndipo sichotero chokha, koma ife tikondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa iye talandira tsopano chotetezera.
  4916. Rom 5:12 Mwa ichi monga uchimo udalowa m’dziko lapansi mwa munthu m’modzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa idafikira anthu wonse; chifukwa kuti onse adachimwa.
  4917. Rom 5:13 (Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo udali m’dziko lapansi: koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo.
  4918. Rom 5:14 Komatu imfa idachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sadachimwe monga machimwidwe ake a Adamu, amene ndi fanizo la iye wakudzayo.
  4919. Rom 5:15 Koma osati monga cholakwa, chomwechonso ili mphatso yaulere. Pakuti ngati ambiriwo adafa chifukwa cha kulakwa kwa m’modziyo, koposa apo chisomo cha Mulungu, ndi mphatso ya chisomo, yomwe ili yodzera mwa m’modzi, Yesu Khristu, yachulukira kwa anthu ambiri.
  4920. Rom 5:16 Ndipo si monga [zinali] kuti mwa amene anachimwayo, [kotero] mphatso: pakuti mlandu udachokera kwa m’modzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere [ili] ya kwa zolakwa zambiri kufikira kutiyesa wolungama.
  4921. Rom 5:17 Pakuti ngati, ndikulakwa kwa munthu m’modzi imfa idachita ufumu kudzera mwa m’modziyo; koposa apo iwo amene akulandira chisomo chochuluka ndi mwa mphatso yachilungamo, adzachita ufumu m’moyo mwa m’modzi, ndiye Yesu Khristu.)
  4922. Rom 5:18 Choncho, monga mwa kulakwa kwa m’modzi [chiweruzo chidafikira] anthu wonse ku kutsutsidwa; chomwechonso mwa chilungamo cha m’modzi mphatso yaulere idabwera kwa anthu onse chilungamitso cha ku moyo.
  4923. Rom 5:19 Pakuti ndi kusamvera kwa munthu m’modzi ambiri adayesedwa wochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa m’modzi ambiri adzayesedwa wolungama.
  4924. Rom 5:20 Momwemo lamulo lidalowa, kuti kulakwa kukachuluke. Koma pamene uchimo udachuluka, pomwepo chisomo chidachuluka koposa:
  4925. Rom 5:21 Kuti monga uchimo wachita ufumu kufikira imfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.
  4926. Rom 6:1 Tidzanena chiyani tsono? Tidzakhalabe mu uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke?
  4927. Rom 6:2 Mulungu akuletsa. Ife amene tiri akufa ku uchimo tidzakhala bwanji chikhalire m’menemo?
  4928. Rom 6:3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tidabatizidwa mwa Khristu Yesu; tidabatizidwa mu imfa yake?
  4929. Rom 6:4 Choncho tidayikidwa m’manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa mu imfa: kuti monga Khristu adawukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano.
  4930. Rom 6:5 Pakuti ngati ife tabzyalidwa pamodzi ndi iye m’chifaniziro cha imfa yake, koteronso tidzakhala [m’chifanizo] cha kuwuka [kwake].
  4931. Rom 6:6 Podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale udapachikidwa pamodzi ndi [iye], kuti thupilo la uchimo likawonongedwe, kuti ife tisatumikirenso uchimo.
  4932. Rom 6:7 Pakuti iye amene adafa adamasulidwa ku uchimo.
  4933. Rom 6:8 Koma ngati ife tidafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso moyo ndi iye;
  4934. Rom 6:9 Podziwa kuti Khristu adawukitsidwa kwa akufa safanso; imfa siyichitanso ufumu pa iye.
  4935. Rom 6:10 Popeza mwakuti anafa iye, adafa ku uchimo kamodzi, ndipo mwakuti iye ali wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.
  4936. Rom 6:11 Chotero inunso mudziwerengere inu nokha wofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.
  4937. Rom 6:12 Choncho musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa, kuti mumvere zilakolako zake.
  4938. Rom 6:13 Ndipo musapereke ziwalo zanu [monga] zida zachosalungama ku uchimo: koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga iwo amene ali amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale [monga] zida za chilungamo.
  4939. Rom 6:14 Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu: popeza simuli pansi pa lamulo koma pa chisomo.
  4940. Rom 6:15 Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitiri pansi pa lamulo, koma pa chisomo? Mulungu akuletsa.
  4941. Rom 6:16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala atumiki ake kumumvera, atumiki ake muli a iye amene inu mulikumvera; kapena za uchimo kulinga ku imfa, kapena a kumvera kulinga ku chilungamo?
  4942. Rom 6:17 Koma ayamikike Mulungu, kuti mudakhala atumiki a uchimo, koma mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene chidakumasulani inu.
  4943. Rom 6:18 Ndipo pamene mudamasulidwa ku uchimo, mudakhala atumiki a chilungamo.
  4944. Rom 6:19 Ndiyankhula manenedwe a anthu chifukwa cha kufoka kwa thupi lanu: pakuti monga inu mudapereka ziwalo zanu zikhale atumiki a chodetsa ndi ku kusayeruzika kulinga ku kusayeruzika; inde kotero ngakhale tsopano perekani ziwalo zanu zikhale atumiki a chilungamo kufikira ku chiyero.
  4945. Rom 6:20 Pakuti pamene inu mudali atumiki a uchimo, mudali mfulu ku chilungamo.
  4946. Rom 6:21 Ndipo mudali nazo zipatso zanji nthawi ija m’zinthu zimene tsopano muchita nazo manyazi? Pakuti chimaliziro cha zinthu zimenezo [chili] imfa.
  4947. Rom 6:22 Koma tsopano pamene mudamasulidwa ku uchimo, ndi kukhala atumiki a Mulungu, muli nacho chipatso chanu chakufikira ku chiyero, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.
  4948. Rom 6:23 Pakuti mphotho yake ya uchimo [ndi] imfa koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
  4949. Rom 7:1 Nanga kodi simudziwa, abale (pakuti ndiyankhula ndi anthu wodziwa lamulo) kuti lamulo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo?
  4950. Rom 7:2 Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna [wake] pomwe ali wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamuna [wakeyo].
  4951. Rom 7:3 Ndipo choncho, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna [wake] wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo: koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo, ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
  4952. Rom 7:4 Mwa ichi, abale anga, inunso mwakhala akufa ku chilamulo mwa thupi la Khristu; kuti mukwatidwe ndi wina, kwa iye amene adawukitsidwa kwa akufa, kuti ife timubalire Mulungu zipatso.
  4953. Rom 7:5 Pakuti pamene tidali m’thupi, zikhumbokhumbo za machimo, zimene zidali mwa chilamulo, zidali kuchita m’ziwalo zathu, kuti zibalire zipatso za ku imfa.
  4954. Rom 7:6 Koma tsopano tidamasulidwa kuchilamulo, popeza tidafa mwa ichi chimene tidagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, osati [mu] chilembo chakale ayi.
  4955. Rom 7:7 Tidzanena chiyani tsono? Kodi chilamulo chili uchimo? Mulungu akuletsa. Ayi, koma ine sindikazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo: pakuti sindikadazindikira chilakolako, pokhapo chilamulo chidanena, Usasirire.
  4956. Rom 7:8 Koma uchimo, pamene udapeza chifukwa mwa chilamulo, udachita mkati mwanga chilakolako champhamvu cha mtundu wonse mwa lamulo. Pakuti popanda lamulo uchimo [unali] wakufa.
  4957. Rom 7:9 Ndipo ine ndidakhalapo kamodzi wamoyo popanda lamulo, koma pamene lamulo lidadza, uchimo udatsitsimuka, ndipo ine ndidafa.
  4958. Rom 7:10 Ndipo lamulo, limene [lidali] lopatsa moyo, ndidalipeza lofikitsa ku imfa.
  4959. Rom 7:11 Pakuti uchimo, pamene udapeza chifukwa mwa lamulo, udandinyenga ine, ndikundipha [ine].
  4960. Rom 7:12 Mwa ichi chilamulo [chili] choyera, ndi chilangizo chake n’choyera, ndi cholungama, ndi chabwino.
  4961. Rom 7:13 Ndipo tsopano chabwino chija chidandikhalira imfa kodi? Mulungu akuletsa. Koma uchimo, kuti uwoneke kuti uli uchimo, wakuchita imfa mwa ine mwa ichi chimene chili chabwino; kuti mwa chilamulo uthe kundichimwitsa kwambiri.
  4962. Rom 7:14 ¶Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili cha uzimu; koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa pansi pa uchimo.
  4963. Rom 7:15 Pakuti chimene ine ndichita ine sindichivomereza; pakuti sindichita chimene ndifuna; koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi.
  4964. Rom 7:16 Koma ngati ndichita chimene sindifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti [chili] chabwino.
  4965. Rom 7:17 Koma tsopano sindine amene ndichichita, koma uchimo wokhalabe mkati mwanga ndiwo.
  4966. Rom 7:18 Ndipo ndidziwa kuti mkati mwanga, (ndiko, m’thupi langa), simukhala chinthu chabwino: pakuti kufuna kulipo mwa ine, koma [momwe] ndingathe kuchitira chabwino sindikupeza.
  4967. Rom 7:19 Pakuti chabwino chimene ndichifuna sindichichita: koma choyipa chimene sindifuna, chimenecho ndichichita.
  4968. Rom 7:20 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndichichita, koma uchimo umene ukhalabe mkati mwanga.
  4969. Rom 7:21 Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino choyipa chilipo ndi ine.
  4970. Rom 7:22 Pakuti ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu mwa munthu wa mkati mwanga.
  4971. Rom 7:23 Koma ndiwona lamulo lina m’ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la m’malingaliro mwanga, ndi kundibweretsa ine mu ukapolo wa lamulo la uchimo umene uli m’ziwalo zanga.
  4972. Rom 7:24 Ho! Munthu wasawuka ine! Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?
  4973. Rom 7:25 Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi malingaliro nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.
  4974. Rom 8:1 Choncho tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa, amene sayenda motsatira thupi, koma motsatira Mzimu.
  4975. Rom 8:2 Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi imfa.
  4976. Rom 8:3 Pakuti chimene chilamulo sichidathe kuchita, popeza chidafoka mwa thupi, Mulungu adatumiza Mwana wake wamwamuna wa iye yekha m’chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, anatsutsa uchimo m’thupi:
  4977. Rom 8:4 Kuti chilungamo cha chilamulo chikakwaniritsidwe mwa ife, amene sitiyendayenda motsatira thupi, koma motsatira mzimu.
  4978. Rom 8:5 Pakuti iwo amene ali otsatira thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo ali otsatira Mzimu, asamalira zinthu za Mzimu.
  4979. Rom 8:6 Pakuti kusamalira za thupi kuli imfa; koma kusamalira za mzimu kuli moyo ndi mtendere.
  4980. Rom 8:7 Chifukwa malingaliro a umunthu adana ndi Mulungu; pakuti sagonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sakhoza kutero.
  4981. Rom 8:8 Chomwecho iwo amene ali m’thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
  4982. Rom 8:9 Koma inu simuli m’thupi ayi, koma mu Mzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Tsopano ngati munthu wina aliyense alibe Mzimu wa Khristu, si ali wake wa iye.
  4983. Rom 8:10 Ndipo ngati Khristu [akhala] mwa inu, thupilo [liri] lakufa chifukwa cha uchimo; koma Mzimu ali moyo chifukwa cha chilungamo.
  4984. Rom 8:11 Koma ngati Mzimu wa iye amene adawukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adawukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhalabe mwa inu.
  4985. Rom 8:12 Choncho, abale, ife tiri angongole osati ake a thupi ayi, kukhala ndi moyo monga mwa thupi.
  4986. Rom 8:13 Pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi Mzimu mufetsa zochita za thupi, mudzakhala ndi moyo.
  4987. Rom 8:14 Pakuti monga ambiri amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.
  4988. Rom 8:15 Pakuti inu simudalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma mudalandira Mzimu wa umwana, umene tifuwula nawo, Abba, Atate.
  4989. Rom 8:16 Mzimu mwini yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu:
  4990. Rom 8:17 Ndipo ngati ana, pomweponso wolandira cholowa; wolandira cholowa ake a Mulungu, ndi wolandira cholowa pamodzi ndi Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi ndi [iye]; kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.
  4991. Rom 8:18 Pakuti ndiyesa kuti masawuko a nyengo yatsopano sayenera [kulinganizidwa] ndi ulemerero umene udzavumbulutsidwa mwa ife.
  4992. Rom 8:19 Pakuti chiyembekezetso chotsimikizika chowona cha cholengedwa chilindira kuwonekera kwa ana a Mulungu.
  4993. Rom 8:20 Pakuti cholengedwacho chigonjetsedwa ku uchabe, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene adachigonjetsa [chomwecho] m’chiyembekezo.
  4994. Rom 8:21 Pakuti chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana amuna a Mulungu.
  4995. Rom 8:22 Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuwula ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.
  4996. Rom 8:23 Ndipo osati [iwo] wokha, komanso ife tomwe; tiri nazo zipatso zoyambirira kucha za Mzimu, inde ifenso amene tibuwula mkati mwathu, kulindira umwana wathu, [ndiko kunena kuti], chiwombolo cha thupi lathu.
  4997. Rom 8:24 Pakuti ife tidapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chiwoneka si chili chiyembekezo ayi; pakuti munthu ndani ayembekezera chimene achipenya?
  4998. Rom 8:25 Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, [pamenepo] tichirindira [icho] ndi chipiriro.
  4999. Rom 8:26 Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti chimene tichipempha monga chiyenera sitidziwa; koma Mzimu mwini yekha atipempherera ndi zobuwula zosatheka kuneneka.
  5000. Rom 8:27 Ndipo iye amene asanthula mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera woyera mtima monga mwa [chifuniro cha] Mulungu.
  5001. Rom 8:28 ¶Ndipo tidziwa kuti kwa iwotu amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, kwa iwotu amene ali woyitanidwa ku cholinga [chake].
  5002. Rom 8:29 Chifukwa kuti iwo amene iye adawadziwiratu, iwowa adawalamuliratu [kuti] afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake wamwamuna, kuti iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri.
  5003. Rom 8:30 Kuwonjezera apo amene iye adawalamuliratuwo, iye adawayitananso, ndipo iwo amene adawayitana, iwotu adawalungamitsa: ndipo amene iye adawalungamitsa, iwotu iye adawapatsanso ulemerero.
  5004. Rom 8:31 Ndipo tidzanena chiyani ku zinthu izi? Ngati Mulungu [ali] ndi ife, angatitsutse ndani?
  5005. Rom 8:32 Iye amene sadatimana Mwana wake wamwamuna wa iye yekha, koma adampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kwaulere pamodzi ndi iye kutipatsanso ife zinthu zonse?
  5006. Rom 8:33 Ndani adzaneneza wosankhidwa a Mulungu? [Ndi] Mulungu amene amalungamitsa.
  5007. Rom 8:34 Ndani [iye] amene amatsutsa? [Ndi] Khristu amene adafa, inde makamaka, ndiye amene adawuka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.
  5008. Rom 8:35 Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsawutso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunzidwa, kapena njala, kapena usiwa, kapena zowopsa, kapena lupanga?
  5009. Rom 8:36 Monga kwalembedwa, Chifukwa cha inu tiri kuphedwa dzuwa lonse; tidawerengedwa monga nkhosa zokaphedwa.
  5010. Rom 8:37 Ayi, m’zinthu zonsezi, ife ndife woposa agonjetsi mwa iye amene adatikonda.
  5011. Rom 8:38 Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale mphamvu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza,
  5012. Rom 8:39 Ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
  5013. Rom 9:1 Ndinena zowona mwa Khristu, sindikunama ayi, chikumbumtima changa chindichitira ine umboni mwa Mzimu Woyera.
  5014. Rom 9:2 Kuti ndadzazidwa ndi chisoni chachikulu ndi kupweteka kosalekeza mu mtima mwanga.
  5015. Rom 9:3 Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi:
  5016. Rom 9:4 Ndiwo a Israyeli; kwa iwo [ali nawo] umwana ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi utumiki [wa Mulungu], ndi malonjezano.
  5017. Rom 9:5 Ndiwo makolo ali awo, ndi kwa iwo monga mwa thupi ndiko [adachokera] Khristu, ndiye ali pamwamba pa zonse, Mulungu wolemekezeka ku nthawi zonse. Amen.
  5018. Rom 9:6 ¶Koma sikuli ngati mawu a Mulungu adakhala chabe ayi. Pakuti [onse] wochokera kwa Israyeli, siali onse a Israyeli:
  5019. Rom 9:7 Sikuti chifukwa ali mbewu ya Abrahamu, [kodi onse] ali ana; koma, mwa Isake, mbewu yako idzayitanidwa.
  5020. Rom 9:8 Ndiko kuti, ana a thupi sakhala [iwo] ana a Mulungu ayi; koma ana a lonjezo awerengedwa kuti ndiwo mbewu.
  5021. Rom 9:9 Pakuti mawu a lonjezo [ndi] amenewa, panyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.
  5022. Rom 9:10 Ndipo si [ichi] chokha, koma Rabekanso pamene adali ndi pakati pa m’modzi, ndi kholo lathu Isake;
  5023. Rom 9:11 (Pakuti [anawo] asanabadwe, kapena asadachite kanthu kabwino kapena koyipa, kuti cholinga cha Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ayi, koma chifukwa cha wakuyitanayo);
  5024. Rom 9:12 Pakuti kudanenedwa kwa iye, Wamkulu adzatumikira wam’ng’ono.
  5025. Rom 9:13 Monga kwalembedwa, ndamukonda Yakobo, koma ndamuda Esawu.
  5026. Rom 9:14 Ndipo tsono tidzanena chiyani? [Kodi chilipo] chosalungama ndi Mulungu? Mulungu akuletsa.
  5027. Rom 9:15 Pakuti adati ndi Mose, ndidzachitira chifundo amene ndifuna kum’chitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndifuna kukhala naye chisoni.
  5028. Rom 9:16 Chotero sichichokera kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene awonetsa chifundo.
  5029. Rom 9:17 Pakuti lembo linena kwa Farawo, Chifukwa cha cholinga chomwechi, ndidakuwutsa iwe, kuti ndikawonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.
  5030. Rom 9:18 Chotero iye achitira chifundo amene iye afuna [kumchitira chifundo], ndipo amene iye afuna iye amuwumitsa mtima.
  5031. Rom 9:19 Ndipo iwe pamenepo udzanena kwa ine, Chifukwa chiyani iye wapeza cholakwa? Pakuti ndani adakaniza chifuniro chake?
  5032. Rom 9:20 Ayi, koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mawu? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene adachipanga [icho]. Undipangiranji ine chotero?
  5033. Rom 9:21 Kodi wowumba mbiya sakhala ndi mphamvu zake padothi, kuwumba ndi ntchintchi yomweyo chotengera chimodzi cha ulemu, ndi china chamanyazi?
  5034. Rom 9:22 [Ndipo] ngati Mulungu; pofuna kuwonetsa mkwiyo [wake]; ndi kuti mphamvu yake idziwike, adalekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko?
  5035. Rom 9:23 Ndikuti iye akathe kudziwitsa chuma cha ulemerero wake pa zotengera za chifundo, zimene iye adazikonzeratu m’mbuyomo ku ulemerero wake.
  5036. Rom 9:24 Ngakhalenso ife amene iye adatiyitana, si a mwa Ayuda wokha komanso a mwa anthu Amitundu?
  5037. Rom 9:25 Monga iye adatinso mwa Hoseya. Ndidzawatcha anthu anga, amene si adali anthu anga; ndi wokondedwa wake, amene si adali wokondedwa.
  5038. Rom 9:26 Ndipo kudzali, [kuti] pamalo pamemepo kudanenedwa kwa iwo, simuli anthu anga; pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.
  5039. Rom 9:27 Yesayanso afuwula za Israyeli, Ngakhale chiwerengerocha ana a Israyeli chikhala monga m’chenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka:
  5040. Rom 9:28 Pakuti iye adzatsiriza ntchito, ndi kuyichita [iyo] mwa chidule m’chilungamo: chifukwa Ambuye adzatsiriza ntchito yake mwa chidule pa dziko lapansi.
  5041. Rom 9:29 Ndipo monga Yesaya adati kale, Kupatula kuti ngati Ambuye wa Makamu akadapanda kutisiyira ife mbewu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadapangidwa kukhala ofanana ndi Gomora.
  5042. Rom 9:30 Kodi tidzanena chiyani tsono? Kuti Amitundu amene sadatsata ku chilungamo, adafikira ku chilungamo ndicho chilungamo cha m’chikhulupriro.
  5043. Rom 9:31 Koma Israyeli, amene adatsata lamulo la chilungamo, sadafikira lamulo la chilungamo.
  5044. Rom 9:32 Mwa ichi? Chifukwa kuti [iwo] sadalitsata [ilo] ndi chikhulupiriro, koma monga zinali mwa ntchito za lamulo. Pakuti adaphunthwa pamwala wophunthwitsa.
  5045. Rom 9:33 Monganso kwalembedwa, Onani, ndikhazika m’Ziyoni mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lokhumudwitsa: Ndipo wokhulupirira pa iye sadzachita manyazi.
  5046. Rom 10:1 Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa la kwa Mulungu kwa Israyeli ndiro, kuti iwo apulumuke.
  5047. Rom 10:2 Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
  5048. Rom 10:3 Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pakuyesa kukhazikitsa chilungamo cha iwo wokha, iwo sadagonja ku chilungamo cha Mulungu.
  5049. Rom 10:4 Pakuti Khristu [ndi] chimaliziro cha lamulo la kulinga ku chilungamo kwa amene aliyense akhulupirira.
  5050. Rom 10:5 Pakuti Mose wafotokoza za chilungamo cha m’lamulo, Kuti munthu amene achita zinthu zimenezi adzakhala nazo moyo.
  5051. Rom 10:6 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mu mtima mwako, Adzakwera ndani kumwambako? (Ndiko kutsitsa pansi Khristu [kuchokera m’mwamba]:)
  5052. Rom 10:7 Kapena, adzatsikira ndani kwakuyako? (Ndiko kukweza Khristu kuchokerakwa akufa.)
  5053. Rom 10:8 Koma chinena chiyani? Mawu ali pafupi ndi iwe, inde m’kamwa mwako, ndi mu mtima mwako: ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tiwalalikira.
  5054. Rom 10:9 Kuti ngati udzavomereza ndi mkamwa mwako Ambuye Yesu, ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuwukitsa kwa akufa, iwe udzapulumuka.
  5055. Rom 10:10 Pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi pakamwa chivomerezo kutengapo chipulumutso.
  5056. Rom 10:11 Pakuti lembo likuti, Amene aliyense akhulupirira paiye, sadzachita manyazi.
  5057. Rom 10:12 Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene: pakuti Mbuye yemweyo wa onse, ali wolemera kwa onse amene ayitana pa iye.
  5058. Rom 10:13 Pakuti amene aliyense adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.
  5059. Rom 10:14 Ndipo iwo adzayitana bwanji pa iye amene sadamkhulipirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji mwa iye amene sadamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?
  5060. Rom 10:15 Ndipo adzalalikira bwanji, pokhapo ngati atumidwa? Monga kwalembedwa, Wokometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wa mtendere, ndi kubweretsa mbiri yabwino ya zinthu zabwino!
  5061. Rom 10:16 Koma iwo onse sadamvera uthenga onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, ndani adakhulupirira zonena zathu?
  5062. Rom 10:17 Chomwecho chikhulupiriro [chidza] mwa kumva, ndi kumva mwa mawu a Mulungu.
  5063. Rom 10:18 Koma ine nditi, sadamva iwo kodi! Inde ndithudi, liwu lawo lidapita ku dziko lonse lapansi, ndi mawu awo kumalekezero a dziko lapansi.
  5064. Rom 10:19 Koma nditi, kodi Israyeli alibe kudziwa? Poyamba Mose anena, Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi [iwo amene] sakhala anthu, ndipo ndi mtundu wopulukira ndidzakwiyitsa inu.
  5065. Rom 10:20 Koma Yesaya ali olimba mtima, nati, Ndidapezedwa ndi iwo amene sadandifunefune; ndidawonekera kwa iwo amene sadandifunsa ine.
  5066. Rom 10:21 Koma kwa Israyeli anena, Tsiku lonse ndatambalitsira manja anga kwa anthu wosamvera ndi wotsutsana.
  5067. Rom 11:1 Choncho ndinena, Mulungu adataya ake kodi? Mulungu akuletsa. Pakuti inenso ndiri mu Israyeli, wa mbewu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.
  5068. Rom 11:2 Mulungu sadataya anthu ake amene iye adawadziwiratu. Kapena inu simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Pomwe iye amachita mapembedzero kwa Mulungu chifukwa cha Israyeli, ndi kuti,
  5069. Rom 11:3 Ambuye, adawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.
  5070. Rom 11:4 Koma linena chiyani yankho la Mulungu kwa iye? Ndidadzisiyira ndekha anthu amuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sadapinda bondo [kwa chifanizo cha] Baala.
  5071. Rom 11:5 Choteronso nthawi yatsopano alipo otsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.
  5072. Rom 11:6 Ndipo ngati ndi chisomo, pamenepo si [chilinso] cha ntchito ayi; ndipo pakutero, chisomo sichikhalanso chisomo. Koma ngati [chili] mwa ntchito, pamenepo sichisomonso: ndipo pakutero ntchito sikhalanso ntchito.
  5073. Rom 11:7 Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israyeli afunafuna sadachipeza; koma osankhidwawo adachipeza, ndipo wotsalawo adachititsidwa khungu;
  5074. Rom 11:8 (Monga kudalembedwa, Mulungu adawapatsa mzimu watulo, kuti maso asapenye, ndi makutu kuti asamve;) kufikira lero lino.
  5075. Rom 11:9 Ndipo Davide akuti, Gome lawo likhala kwa iwo ngati khwekhwe, ndi ngati msampha, ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango iwo:
  5076. Rom 11:10 Maso awo adetsedwe, kuti asapenye, ndipo muweramitse msana wawo nthawi zonse.
  5077. Rom 11:11 Choncho ndinena, Adakhumudwa kodi kuti agwe? Mulungu akuletsa; koma [kuti] ndi kugwa kwawo chipulumutso [chadza] kwa Amitundu, cholinga cha kudzachititsa iwo nsanje.
  5078. Rom 11:12 Ndipo ngati kugwa kwawo kukhala chuma kwa dziko lapansi, ndipo kuchepa kwawo chuma kwa Amitundu; koposa kotani nanga kudzaza kwawo?
  5079. Rom 11:13 Chifukwa ndiyankhula ndi inu Amitundu, popeza ine ndiri mtumwi wa kwa Amitundu, ndikuza ofesi ya [utumiki] wanga;
  5080. Rom 11:14 Kuti ngati nkutheka ndikachititse mkwiyo [iwo amene ndi] a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.
  5081. Rom 11:15 Pakuti ngati kuwataya kwawo [kuli] kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa [kwawo kudzatani], koma moyo wakuchokera kwa akufa?
  5082. Rom 11:16 Ndipo ngati zipatso zoyamba kucha [ziri] zoyera, choteronso thunthu lirinso [loyera]; ndipo ngati muzu uli woyera, choteronso [ziri] nthambi.
  5083. Rom 11:17 Ndipo ngati nthambi zina zithyoledwa, ndipo iwe, wokhala mtengo wa olivi wakuthengo, udawoketsedwa mwa izo, ndipo pamodzi ndi izo ugawana nazo za muzu ndi za mafuta ake a mtengo wa oliviwo.
  5084. Rom 11:18 Usadzitama iwe wekha motsutsana ndi nthambizo. Koma ngati udzitama, si uli iwe amene unyamula muzu ayi, koma muzu ukunyamula iwe.
  5085. Rom 11:19 Iwe udzanena pamenepo, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikawoketsedwemo.
  5086. Rom 11:20 Chabwino; chifukwa chakusakhulupirira iwo adathyoledwa, ndipo iwe uyima mwa chikhulupiriro. Musakhale amakhalidwe wodzikuza, koma kuwopa:
  5087. Rom 11:21 Pakuti ngati Mulungu sadalekerera nthambi za mtundu wake, [usamalire] kuti kapena sadzalekereranso iwe.
  5088. Rom 11:22 Choncho wonani ubwino wake ndi kuwuma mtima kwake kwa Mulungu; pa iwo adagwa, kuwuma kwake; koma kwa iwe ubwino wake wa Mulungu, ngati ukhala chikhalire ubwino [wake]; ngati sutero, adzakusadza iwe.
  5089. Rom 11:23 Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire ndi chisakhulupiriro, adzawoketsedwanso, pakuti Mulungu ndi wakutha kuwawoketsanso.
  5090. Rom 11:24 Pakuti ngati iwe udasadzidwa ku mtengo wa olivi womwe uli wakuthengo mwa chilengedwe, ndipo udawoketsedwa kosiyana ndi chilengedwe ku mtengo wa olivi wabwino: koposa kotani nanga iwo, amene akhala nthambi za chilengedwe, adzawoketsedwa ku mtengo wawo womwewo wa olivi?
  5091. Rom 11:25 Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale wosadziwa chinsinsi ichi, kuti mwina inu mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti khungu lakusawona gawo lina kudadza kwa Israyeli, kufikira chidzalo cha Amitundu chitatha kulowamo.
  5092. Rom 11:26 Ndipo chotero Israyeli yense adzapulumuka; monga kudalembedwa, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi, iye adzachotsa kusowa umulungu kwa Yakobo:
  5093. Rom 11:27 Ndipo ichi [ndi] chipangano changa kwa iwo, pamene ndidzachotsa machimo awo.
  5094. Rom 11:28 Kunena za uthenga wabwino, [iwo ndi] adani chifukwa cha inu: koma ngati kunena za chisankhidwe, [iwo ali] wokondedwa chifukwa cha makolo.
  5095. Rom 11:29 Pakuti mphatso zake ndikuyitana kwake kwa Mulungu [ziribe] kulapika.
  5096. Rom 11:30 Pakuti monga inunso kale simudakhulupirira Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo kudzera m’kusakhulupirira kwawo.
  5097. Rom 11:31 Choteronso iwo sadakhulupirira tsopano, kuti iwonso mwa chifundo chanu iwonso akalandire chifundo.
  5098. Rom 11:32 Pakuti Mulungu adatsekera pamodzi onse m’kusakhulupirira, kuti akachitire chifundo pa onse.
  5099. Rom 11:33 Ha! Kuya kwake kwa chuma pamodzi ndi za nzeru ndi chidziwitso cha Mulungu! Wosasanthulikadi maweruzo [ake], ndi njira zake nzosapezeka!
  5100. Rom 11:34 Pakuti adadziwa ndani malingaliro [a mtima] wa Ambuye? Kapena adakhala phungu wake ndani?
  5101. Rom 11:35 Ndipo adayamba ndani kumpatsa iye, ndipo chidzabwezeretsedwanso kwa iye?
  5102. Rom 11:36 Pakuti kuchokera kwa iye, ndi kudzera mwa iye, ndi kwa iye, [muli] zinthu zonse: kwa iyeyo [ukhale] ulemerero ku nthawi zonse. Amen.
  5103. Rom 12:1 Choncho ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirikakwa Mulungu, [ndiko] kutumikira kwanu koyenera.
  5104. Rom 12:2 Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a dziko ili; koma mukhale wosandulika, mwa kukonzanso kwamalingaliro [a mtima] wanu, kuti mukatsimikize chifuniro chimene [chilicho] chabwino, ndi cholandirika ndi changwiro.
  5105. Rom 12:3 Pakuti ndinena, kupyolera mwa chisomo chopatsidwa kwa ine, kwa munthu aliyense amene ali pakati pa inu, kuti asaganize [mwa iye yekha] koposa kumene ayenera kuganiza; koma aganize yekha bwino lomwe, kolingana ndi kuti Mulungu wampatsa aliyense muyesowo wa chikhulupiriro.
  5106. Rom 12:4 Pakuti monga m’thupi limodzi tiri nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo siziri nayo ntchito imodzimodzi;
  5107. Rom 12:5 Chomwecho ife, [pokhala] ambiri, tiri thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake wina ndi wina.
  5108. Rom 12:6 Ndipo pokhala nazo ife mphatso zosiyana monga mwa chisomo chopatsidwa kwa ife, kapena mphatso yonenera, [tiyeni tinenere] monga mwa muyeso wa chikhulupiriro.
  5109. Rom 12:7 Kapena utumiki, [tiyeni] tidzipereke ku utumiki [wathu]; kapena iye wophunzitsa, pa kuphunzitsa;
  5110. Rom 12:8 Kapena iye wodandawulira, pa kudandawulirako; wogawira [achite] mosavutika mtima; iye woweruza, aweruze ndi khama; iye wochita chifundo, achite mokondwera.
  5111. Rom 12:9 Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; phatikirana nacho chabwino.
  5112. Rom 12:10 M’chikondano chanu wina ndi mzake mukondane ndi chikondi cha ubale chenicheni; m’kulemekezana kuwona wina wotiposa;
  5113. Rom 12:11 Musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, kutumikira Ambuye;
  5114. Rom 12:12 Kukondwera m’chiyembekezo, kupirira m’masawutso; kupitirira kuchita changu m’kupemphera.
  5115. Rom 12:13 Patsani zosowa woyera mtima; wodzipereka pa kuchereza alendo.
  5116. Rom 12:14 Dalitsani iwo akuzunza inu, dalitsani, ndipo musawatemberere.
  5117. Rom 12:15 Kondwani nawo iwo akukondwera; ndipo lirani nawo akulira.
  5118. Rom 12:16 [Mukhale] ndi mtima umodzi kwa wina ndi mzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nawo apansi. Musadziyesa anzeru mwa inu nokha.
  5119. Rom 12:17 Musabwezera munthu aliyense choyipa chosinthana ndi choyipa. Mulingaliririretu za zinthu zowona mtima pamaso pa anthu onse.
  5120. Rom 12:18 Ngati nkutheka monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.
  5121. Rom 12:19 Wokondedwa, musabwezere inu eni choyipa, koma [makamaka] perekani malo kwa mkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, atero Ambuye.
  5122. Rom 12:20 Choncho ngati mdani wako akumva njala, um’dyetse, ngati akumva ludzu, um’patse chakumwa; pakuti pakutero udzawunjika makala a moto pamutu pake.
  5123. Rom 12:21 Musagonje ku choyipa, koma ndi chabwino gonjetsani choyipa.
  5124. Rom 13:1 Moyo uliwonse ugonjere ku mphamvu za ulamuliro. Pakuti palibe mphamvu za ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu: ndipo mphamvu za ulamuliro zomwe ziripo ziyikidwa ndi Mulungu.
  5125. Rom 13:2 Kotero kuti aliyense wotsutsana nazo mphamvuzo, akaniza choyikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzilandirira iwo wokha kulanga.
  5126. Rom 13:3 Pakuti wolamula sakhala wowopsa ku ntchito zabwino, koma ku zoyipa. Ndipo ufuna kodi kusawopa mphamvuzo? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutamanda m’menemo:
  5127. Rom 13:4 Pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu kwa iwe wokuchitira zabwino. Koma ngati uchita choyipa, wopatu; pakuti iye sagwira lupanga kwachabe: pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, wakubwezera ndi [kuchititsa] mkwiyo pa iwo akuchita zoyipa.
  5128. Rom 13:5 Mwa ichi, kuyenera kuti [mukhale] wogonja, sichifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.
  5129. Rom 13:6 Pakuti chifukwa cha ichi muperekenso msonkho: pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.
  5130. Rom 13:7 Perekani kwa anthu onse mangawa awo, msonkho kwa eni [ake] a msonkho; kulipira kwa ena ake akulipidwa, kuwopa kwa eni ake akuwawopa; ulemu kwa eni ulemu.
  5131. Rom 13:8 Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana wina ndi mnzake; pakuti iye amene akonda mzake wakwaniritsa lamulo.
  5132. Rom 13:9 Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Usasirire, ndipo [lingakhale] lamulo lina lirilonse, limangika pamodzi m’mawu amenewa, akunena, Uzikonda woyandikana naye monga udzikonda iwe mwini.
  5133. Rom 13:10 Chikondano sichichitira woyandikana naye choyipa: chotero chikondanocho [chili] chokwaniritsa cha lamulo.
  5134. Rom 13:11 Ndipo kuti, podziwa inu nthawiyo, kuti tsopano [ndiyo] nthawi yabwino yakuwuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu [chili] pafupi koposa pamene tidakhulupirira.
  5135. Rom 13:12 Usiku wapita, ndi usana wayandikira; choncho tivule ntchito za mdima, ndipo tivale chida cha kuwunika.
  5136. Rom 13:13 Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’ziwawa ndi kuledzera ayi, si m’chilakolako chonyansa ndi mowononga ayi, si m’nkhwidzi ndi kaduka ayi.
  5137. Rom 13:14 Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.
  5138. Rom 14:1 Ndipo iye amene ali wofoka m’chikhulupiriro mum’landire iye, [koma] sikuchita naye makani wotsutsana achikayikitso ayi.
  5139. Rom 14:2 Munthu m’modzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse: koma wina wofoka angodya zitsamba.
  5140. Rom 14:3 Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo: pakuti Mulungu wam’landira iye.
  5141. Rom 14:4 Ndani iwe woweruza mtumiki wa mwini wake? Iye ayimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Inde, iye adzagwirizizidwa: pakuti Mulungu ali nako kuthekera kwa kumiyimiriritsa.
  5142. Rom 14:5 Munthu wina aganiza kuti tsiku lina liposa linzake: wina aganiza kuti masiku onse [ali wofanana]. Munthu aliyense akakamizike kwathunthu m’malingaliro a [mumtima] mwake.
  5143. Rom 14:6 Iye wosamalira tsiku, alisamalira [ilo] kwa Ambuye; ndipo iye wosasamalira tsikulo salisamalira [ilo] kwa Ambuye. Ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti iye ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, sakudya mwa Ambuye, ndipo ayamika Mulungu.
  5144. Rom 14:7 Pakuti palibe m’modzi mwa ife adzikhalira moyo yekha, ndipo palibe m’modzi adzifera yekha.
  5145. Rom 14:8 Pakuti tingakhale tiri ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye: choncho tingakhale ndi moyo, kapena tikafa, tiri ake a Ambuye.
  5146. Rom 14:9 Pakuti ndi cholinga ichi Khristu adafera, nawukanso kwa akufa, nakhalanso ndi moyo, kuti iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.
  5147. Rom 14:10 Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Khristu.
  5148. Rom 14:11 Pakuti kwalembedwa, Pomwe ndiri ndi moyo, ati Ambuye, bondo lirilonse lidzapindira ine, ndipo lirime lirilonse lidzavomereza kwa Mulungu.
  5149. Rom 14:12 Chotero aliyense wa ife adzadzinenera yekha mlandu wake kwa Mulungu.
  5150. Rom 14:13 Choncho tisaweruzanenso wina ndi mzake: koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asayike chokhumudwitsa kapena chophuthwitsa pa njira ya mbale wake.
  5151. Rom 14:14 Ndidziwa, ndipo ndakakamizika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe [chinthu] chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye [chikhala] chonyansa.
  5152. Rom 14:15 Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni chakudya [chako], pamenepo iwe ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuwononga iye ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.
  5153. Rom 14:16 Choncho musalole chabwino chanu chisinjiriridwe.
  5154. Rom 14:17 Pakuti ufumu wa Mulungu si uli m’chakudya ndi chakumwa; koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
  5155. Rom 14:18 Pakuti iye amene atumikira Khristu mu zinthu izi [ali] wolandirika kwa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.
  5156. Rom 14:19 Choncho tilondole zinthu zomwe zichitira ku mtendere, ndi zinthu zimene m’modzi angathe kulimbikitsa mzake.
  5157. Rom 14:20 Pakuti chakudya sichiwononga ntchito ya Mulungu. Zinthu zonse ndithu [ziri] zoyera; koma kuli koyipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.
  5158. Rom 14:21 [Kuli] kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena [chilichonse] chimene mbale wako aphunthwapo kapena ndikukhumudwapo, kapena afowoketsedwa.
  5159. Rom 14:22 Uli ndi chikhulupiriro kodi? Ukhale [nacho] kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndi [iye] amene sadziweruza mwini yekha m’zinthu zomwe iye wazivomereza.
  5160. Rom 14:23 Koma iye amene akayika atsutsika ngati akudya, chifukwa [iye akudya] osati mwa chikhulupiriro: popeza chinthu chilichonse chimene sichili cha chikhulupiriro ndi tchimo.
  5161. Rom 15:1 Ife tsono amene tiri wolimba, tiyenera kunyamula zofowoka za wopanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.
  5162. Rom 15:2 Yense wa ife akondweretse woyandikana naye wake, kumchitira [iye] zabwino zakumlimbikitsa.
  5163. Rom 15:3 Pakuti Khristunso sanadzikondweretsa yekha; koma, monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene adakunyoza iwe idagwera pa ine.
  5164. Rom 15:4 Pakuti zinthu zirizonse zomwe zidalembedwa kale zidalembedwa kuti ife tiphunzire, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo tikhale ndi chiyembekezo.
  5165. Rom 15:5 Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wachitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi malingaliro [a mtima] umodzi wina ndi mzake monga mwa Khristu Yesu.
  5166. Rom 15:6 Kuti inu mukhoze ndi malingaliro amodzi [ndi] pakamwa pamodzi mukalemekeze Mulungu, amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  5167. Rom 15:7 Mwa ichi mulandirane wina ndi mzake, monganso Khristu anatilandira ife ku ulemerero wa Mulungu.
  5168. Rom 15:8 Ndipo ndinena kuti Yesu Khristu adakhala mtumiki wa mdulidwe wa chowonadi cha Mulungu, kuti atsimikize malonjezo [wopangidwa] kwa makolo.
  5169. Rom 15:9 Ndi kuti Amitundu akalemekeze Mulungu chifukwa cha chifundo [chake]; monga kwalembedwa, chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani inu pakati pa Amitundu, ndidzayimbira ku dzina lanu.
  5170. Rom 15:10 Ndipo anenanso, Kondwerani Amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.
  5171. Rom 15:11 Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu Amitundu onse; ndipo tamandani iye, inu anthu onse.
  5172. Rom 15:12 Ndiponso, Yesaya anati, Padzakhala muzu wa Jese, ndi iye amene adzawuka kuchita ufumu pa Amitundu; mwa iyeyo Amitundu adzamukhulupirira.
  5173. Rom 15:13 Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe m’kukhulupirira, kuti mukachuluke m’chiyembekezo, kudzera mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
  5174. Rom 15:14 ¶Koma ine ndekhanso, abale anga, ndakakamizika mtima za inu, kuti inu nokhanso muli wodzala ndi ubwino, wodzazidwa ndi kudziwa konse, ndi kukhozanso kudandawulirana wina ndi mzake.
  5175. Rom 15:15 Komabe, abale, ndakulemberani inu molimba mtima koposa monga mu njira ina, mokukumbutsani inu chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu.
  5176. Rom 15:16 Kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Khristu kwa Amitundu, wakutumikira uthenga wabwino wa Mulungu, kuti kudzipereka kwawo kwa Amitundu kulandirike, moyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.
  5177. Rom 15:17 Choncho ndiri nacho kuchokera komweko chodzitamandira cha mwa Khristu Yesu mu zinthu zimene ziri zakwa Mulungu.
  5178. Rom 15:18 Pakuti sindingathe kulimba mtima kuyankhula zinthu izo zimene Khristu sadazichita kudzera mwa ine zakuwapangitsa Amitundu kukhala womvera, mwa mawu ndi zochita.
  5179. Rom 15:19 Kupyolera mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu wa Mulungu; kotero kuti kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Ilurikamu, ndalalikira kwathunthu uthenga wa Khristu.
  5180. Rom 15:20 Inde, chotero ndidalimbika kulalikira uthenga wabwino, pamalo pamene Khristu sadatchulidwe kale, kuti ndisamange pa maziko a munthu wina.
  5181. Rom 15:21 Koma monga kwalembedwa, Kwa iwo amene iye sadayankhulidwe, adzawona: ndi iwo amene sadamve adzamvetsetsa.
  5182. Rom 15:22 Chifukwa chakenso ndidaletsedwa kwambiri kuti ndidze kwa inu;
  5183. Rom 15:23 Koma tsopano pokhala popanda malo ena m’madera awa, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri izi kudza kwa inu;
  5184. Rom 15:24 Nthawi ina iriyonse ndidzapita ku Spain, Ndidzadza kwa inu: Pakuti ndiyembekezera kuwona inu mu ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kudzazidwa ndi chibale [chanu].
  5185. Rom 15:25 Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, kukatumikira kwa woyera mtima.
  5186. Rom 15:26 Pakuti kwakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya kusonkha chopereka cha woyera mtima wosawuka omwe ali ku Yerusalemu.
  5187. Rom 15:27 Pakuti chidakondweretsa iwo ndithudi; ndipo iwo ali angongole awo, Pakuti ngati Amitundu akhala wotengapo gawo pa zinthu zawo za uzimu, ntchito yawonso ndiyo kutumikira iwo mu zinthu zathupi.
  5188. Rom 15:28 Koma choncho pamene ndikatsiriza ichi, ndi kusindikizira chipatso ichi kwa iwo, ndidzadutsa kwa inu, kupita ku Spain.
  5189. Rom 15:29 Ndipo ndidziwa kuti pamene ndidza kwanu, ndidzafika m’kudzaza kwake kwa m’dalitso wa uthengawo wa Khristu.
  5190. Rom 15:30 Ndipo ndikudandawulirani inu, abale, chifukwa cha Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chifukwa cha chikondi cha Mzimu, kuti mumalimbika pamodzi ndi ine m’mapemphero [anu] a kwa Mulungu opempherera ine;
  5191. Rom 15:31 Kuti ndikapulumutsidwe kwa wosakhulupirira aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga umene [ndiri nawo] wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa ndi woyera mtima;
  5192. Rom 15:32 Pakuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.
  5193. Rom 15:33 Tsopano Mulungu wa mtendere [akhale] ndi inu nonse. Amen.
  5194. Rom 16:1 Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu ndiye mtumiki wamkazi wa mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya;
  5195. Rom 16:2 Kuti mum’landire iye mwa Ambuye, monga kuyenera woyera mtima, ndi kuti mum’thandize m’zinthu zirizonse adzafuna kwa inu; pakuti iye yekha adali wothandiza ambiri, ndi ine ndemwe.
  5196. Rom 16:3 Apatseni moni Priska ndi Akwila, antchito anzanga mwa Khristu Yesu.
  5197. Rom 16:4 Amene adapereka makosi awo chifukwa cha moyo wanga: amene si ine ndekha ndiwayamika, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa Amitundu.
  5198. Rom 16:5 Chimodzimodzinso [patsani moni] Mpingo wa Ambuye umene uli m’nyumba mwawo. Patsani moni Epaenetasi wokondedwa wanga, amene ali zipatso zoyamba kucha za Akaya kwa Khristu.
  5199. Rom 16:6 Patsani moni Mariya, amene adadzilemetsa ndi ntchito zambiri pa ife.
  5200. Rom 16:7 Patsani moni Andronikasi ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali womveka pakati pa atumwiwo. Amenenso adali mwa Khristu ndisadakhale ine.
  5201. Rom 16:8 Patsani moni Ampliyasi wokondedwa wanga mwa Ambuye.
  5202. Rom 16:9 Patsani moni Urbane, mthandizi wathu mwa Khristu, ndi Stakusi wokondedwa wanga.
  5203. Rom 16:10 Patsani moni Apelesi, wovomerezeka mwa Khristu. Patsani moni iwo a [m’nyumba] ya Aristobulasi.
  5204. Rom 16:11 Patsani moni Herodiyoni, mbale wanga. Patsani moni iwo a [m’nyumba] ya kwa Narikiso, amene ali mwa Ambuye.
  5205. Rom 16:12 Patsani moni Trufena, ndi Trufosa amene agwira ntchito mwa Ambuye. Patsani moni Persisi wokondedwayo, amene adagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.
  5206. Rom 16:13 Patsani moni Rufusi, wosankhidwa mwa Ambuye ndi amayi wake ndi wanga.
  5207. Rom 16:14 Patsani moni Asunkritasi, Fulegoni, Hermas, Patrobasi, Hermes, ndi abale amene ali nawo.
  5208. Rom 16:15 Patsani moni Filologasindi Yuliya, Nereyusi ndi mlongo wake, ndi Olumpasi, ndi woyera mtima onse ali pamodzi nawo.
  5209. Rom 16:16 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsopsono choyera. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni inu.
  5210. Rom 16:17 Tsopano ndikudandawulirani, abale, zindikirani iwo ayambitsa mipatuko ndi zokhumudwitsa kosalingana ndi chiphunzitso chimene mudachiphunzira inu; ndipo patukani pa iwo.
  5211. Rom 16:18 Pakuti wotere satumikira Ambuye Yesu Khristu wathu, koma mimba zawo; ndipo ndi mawu abwino ndi zolankhula zokoma asocheretsa mitima ya ochepa nzeru.
  5212. Rom 16:19 Pakuti kumvera kwanu kudabuka kudera lalikulu kwa [anthu] onse. Choncho ine ndikondwera m’malo mwanu: koma tsopano ndikadafuna kuti mukakhale anzeru pa chimene chili chabwino, ndi a umbuli pa zoyipa.
  5213. Rom 16:20 Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwa. Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu wathu [chikhale] ndi inu. Amen.
  5214. Rom 16:21 Timoteyo wa ntchito mzanga, ndi Lusiyasi, ndi Yasoni, ndi Sosipata, abale anga, akupatsani moni inu.
  5215. Rom 16:22 Ine Tertiyasi, amene adalemba kalata [iyi] ndikupatsani moni mwa Ambuye.
  5216. Rom 16:23 Gayasi mwini nyumba wolandira ine, ndi mpingo wonse, akupatsani moni inu. Erastasi msungichuma wa mzinda akupatsani moni, ndiponso Kwaritasi mbaleyo.
  5217. Rom 16:24 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu wathu [chikhale] ndi inu nonse. Amen.
  5218. Rom 16:25 Tsopano kwa iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa uthenga wabwino wanga, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwavumbulutso la chinsinsi, chimene chidasungika mobisika kuyambira pamene dziko lapansi lidayamba.
  5219. Rom 16:26 Koma chawonetsedwa tsopano, ndi mwa malemba a aneneri, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kudadziwitsidwa kwa mitundu yonse kumvera kwa chikhulupiriro;
  5220. Rom 16:27 Kwa Mulungu wanzeru yekhayo, [kukhale] ulemerero mwa Yesu Khristu ku nthawi zonse. Amen.
  5221. 1Co 1:1 Paulo, woyitanidwa [kuti akhale] mtumwi wa Yesu Khristu kudzera m’chifuniro cha Mulungu, ndi Sositenes mbale [wathu].
  5222. 1Co 1:2 Kwa mpingo wa Mulungu wokhala m’Korinto, kwa iwo woyeretsedwa mwa Khristu Yesu, woyitanidwa [kuti akhale] woyera mtima, pamodzi ndi onse akuyitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m’malo monse, ndiye wawo ndi wathu:
  5223. 1Co 1:3 Chisomo [chikhale] kwa inu, ndi mtendere, wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi [kuchokera] kwa Ambuye Yesu Khristu.
  5224. 1Co 1:4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse m’malo mwa inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chimene chapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;
  5225. 1Co 1:5 Kuti m’zonse mwalemeretsedwa ndi iye, m’malankhulidwe onse, ndi [mu] chidziwitso chonse.
  5226. 1Co 1:6 Monga momwe umboni wa Khristu udatsimikizidwa mwa inu:
  5227. 1Co 1:7 Kotero kuti musakhale inu m’mbuyo popanda mphatso; pakulindira inu kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu:
  5228. 1Co 1:8 Amenenso adzakutsimikizani inu kufikira chimaliziro, [kuti mukhoze kukhala] wopanda chirema m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.
  5229. 1Co 1:9 Mulungu [ali] wokhulupirika, amene mudayitanidwa mwa iye ku chiyanjano cha Mwana wake wa mwamuna Yesu Khristu, Ambuye wathu.
  5230. 1Co 1:10 ¶Koma ndikudandawulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi [kuti] pasakhale magawano pakati pa inu; koma [kuti] mumangike mwangwiro mu malingaliro a [mtima] umodzi womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.
  5231. 1Co 1:11 Pakuti zinanenedwa kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.
  5232. 1Co 1:12 Tsopano ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; ndi ine wa Apolos; ndi ine wa Kefasi; ndi ine wa Khristu.
  5233. 1Co 1:13 Kodi Khristu wagawika? Kodi Paulo adapachikidwa chifukwa cha inu? Kapena kodi mudabatizidwa m’dzina la Paulo?
  5234. 1Co 1:14 Ndiyamika Mulungu kuti sindidabatiza m’modzi yense wa inu, koma Krispasi ndi Gayasi;
  5235. 1Co 1:15 Kuti anganene m’modzi kuti ndinabatiza m’dzina langa.
  5236. 1Co 1:16 Koma ndidabatizanso a pa banja la Stefanasi; kupatula awa, sindidziwa ngati ndidabatiza wina yense.
  5237. 1Co 1:17 ¶Pakuti Khristu sadandituma ine kubatiza, koma kulalikira uthenga wabwino: si mu nzeru ya mawu, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.
  5238. 1Co 1:18 Pakuti kulalikira kwa mtanda kuli chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tapulumutsidwa ndi mphamvu ya Mulungu.
  5239. 1Co 1:19 Pakuti kwalembedwa, Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi chidziwitso cha wochenjera ndidzachitha.
  5240. 1Co 1:20 [Ali] kuti wanzeru. Mlembi [ali] kuti? [Ali] kuti wotsutsana wa dziko lapansi pano ili? Kodi Mulungu sadayipusitsa nzeru ya dziko lapansi?
  5241. 1Co 1:21 Pakuti pambuyo pa iyo mu nzeru ya Mulungu dziko lapansi mwa nzeru yake silidzadziwa Mulungu, chidamkondweretsa Mulungu mwa chopusa cha kulalikira kupulumutsa iwo akukhulupirira.
  5242. 1Co 1:22 Ndipo popeza Ayuda afuna zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru:
  5243. 1Co 1:23 Koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa Ahelene chopusa:
  5244. 1Co 1:24 Koma kwa iwo woyitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.
  5245. 1Co 1:25 Chifukwa chopusa cha Mulungu ndi cha nzeru yoposa anthu; ndipo chifowoko cha Mulungu ndi cha mphamvu yoposa anthu.
  5246. 1Co 1:26 Pakuti mupenya mayitanidwe anu, abale, kuti siambiri anzeru monga mwa thupi; si ambiri amphamvu, si ambiri a maudindo apamwamba, ayitanidwa.
  5247. 1Co 1:27 Koma Mulungu adasankha zopusa za dziko lapansi kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo Mulungu adasankha zofowoka za dziko lapansi kuti akachititse manyazi zamphamvu;
  5248. 1Co 1:28 Ndipo zinthu zapansipansi za dziko lapansi, ndi zinthu zomwe zinyozeka; adazisankha Mulungu, [inde], ndi zinthu zoti kulibe, kuti zikathetse zinthu zoti ziriko.
  5249. 1Co 1:29 Kuti thupi lirilonse lisadzitamande pamaso pake.
  5250. 1Co 1:30 Koma kwa iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene adayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiwombolo:
  5251. 1Co 1:31 Kuti, monga kwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamandire mwa Ambuye.
  5252. 1Co 2:1 Ndipo ine, abale, m’mene ndidadza kwa inu, sindidadza ndi kuposa kwa mawu kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu umboni wa Mulungu.
  5253. 1Co 2:2 Pakuti ndidatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu kena pakati pa inu, koma Yesu Khristu, ndi iye wopachikidwa.
  5254. 1Co 2:3 Ndipo ine ndidakhala nanu mu ufowoko ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri.
  5255. 1Co 2:4 Ndipo mawu anga ndi kulalikira kwanga sikudakhala ndi mawu wokopa anzeru za munthu, koma m’chiwonetso cha Mzimu ndi cha mphamvu:
  5256. 1Co 2:5 Kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.
  5257. 1Co 2:6 Koma tikuyankhula nzeru pakati pa iwo angwiro: koma si nzeru ya dziko lapansi ili, kapena ya akalonga a dziko lapansi ili, amene amathedwa:
  5258. 1Co 2:7 Koma tiyankhula nzeru ya Mulungu m’chinsinsi, [inde nzeru] yobisikayo, imene Mulungu adayikiratu pasadakhale dziko lapansi ku ulemerero wathu.
  5259. 1Co 2:8 Imene sadayidziwa m’modzi wa akulu a dziko lapansi lino: pakuti akadadziwa [ichi], sakadapachika Mbuye wa ulemerero.
  5260. 1Co 2:9 Koma monga kwalembedwa, Diso silidaziwone, ndi khutu silidazimve, nizisadalowe mu mtima wa munthu, zinthu zimene Mulungu adakonzeratu iwo akumkonda iye.
  5261. 1Co 2:10 Koma kwa ife Mulungu wavumbulutsa [izo] kwa ife mwa Mzimu wake: pakuti Mzimu asanthula zinthu zonse, inde zinthu zakuya za Mulungu.
  5262. 1Co 2:11 Pakuti ndani munthu adziwa zinthu za munthu, koma mzimu wa munthuyo uli mwa iye? Momwenso zinthu za Mulungu palibe munthu azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.
  5263. 1Co 2:12 Tsopano talandira ife, osati mzimu wa dziko lapansi, koma mzimu womwe uli wa Mulungu; kuti tikadziwe zinthu zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwa ulere.
  5264. 1Co 2:13 Zinthu zimenenso tiyankhula, si m’mawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma zimene aphunzitsa Mzimu Woyera; kulinganiza zinthu za mzimu ndi za mzimu.
  5265. 1Co 2:14 Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti ziri zopusa kwa iye; sakhozanso kuzizindikira [izi], chifukwa zizindikiridwa mwa uzimu.
  5266. 1Co 2:15 Koma iye amene ali wa uzimu aweruza zinthu zonse, koma iye yekha saweruzidwa ndi munthu.
  5267. 1Co 2:16 Pakuti ndani wadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akamlangize iye? Koma ife tiri nawo malingaliro a Khristu.
  5268. 1Co 3:1 Ndipo ine, abale sindidakhoza kuyankhula ndi inu monga ndi a uzimu, koma monga a thupi, monga makanda mwa Khristu.
  5269. 1Co 3:2 Ndidadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ayi: pakuti kufikira tsopano simudali wokhoza [kuchilandira], ngakhale tsopano lino simukhoza.
  5270. 1Co 3:3 Pakuti mukadali athupi: pakuti pokhala pakati panu [pali] nkhwidzi, ndi ndewu, ndi mipatuko kodi simuli a thupi, ndi kuyendayenda monga anthu?
  5271. 1Co 3:4 Pakuti pomwe wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mzake, ndine wa Apolos, simuli a thupi kodi?
  5272. 1Co 3:5 Paulo ndani tsono? Ndipo Apolos ali ndani, ndi atumiki amene mudakhulupirira mwa iwo, monganso momwe Ambuye adampatsa munthu aliyense.
  5273. 1Co 3:6 Ndidabzala ine, adathirira Apolos, koma Mulungu adapereka kuchulukitsa.
  5274. 1Co 3:7 Chotero si ali kanthu iye wobzala, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene amapereka kuchulukitsa.
  5275. 1Co 3:8 Tsopano iye wobzalayo ndi iye wothirirayo ali amodzi: ndipo munthu aliyense adzalandira mphotho yake ya iye yekha monga mwa ntchito yake ya iye.
  5276. 1Co 3:9 Pakuti ife ndife antchito pamodzi ndi Mulungu: ndinu chilimo cha Mulungu, [ndinu] nyumba ya Mulungu.
  5277. 1Co 3:10 Molingana ndi chisomo cha Mulungu chimene chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndidayika mazikowo, ndipo wina amangapo. Koma yense ayang’anire umo amangira pamenepo.
  5278. 1Co 3:11 Pakuti palibe munthu wina akhoza kuyika maziko ena koma amene ayikidwawo, amene ndi Yesu Khristu.
  5279. 1Co 3:12 Tsopano ngati munthu wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala ya mtengo wapatali, mtengo, udzu, dziputu.
  5280. 1Co 3:13 Ntchito ya munthu aliyense idzawonetsedwa: pakuti tsikulo lidzasonyeza, chifukwa kuti idzavumbulutsidwa ndi moto; ndipo moto udzayesa ntchito ya munthu aliyense ili yotani.
  5281. 1Co 3:14 Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene wayimanga pamemepo, adzalandira mphotho.
  5282. 1Co 3:15 Ngati ntchito ya munthu wina idzapsa, zidzawonongeka zake zonse: koma iye yekha adzapulumutsidwa; motero monga ndi moto.
  5283. 1Co 3:16 Kodi simudziwa kuti muli kachisi wa Mulungu, ndi [kuti] Mzimu wa Mulungu akhala mwa inu?
  5284. 1Co 3:17 Ngati munthu aliyense awononga kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuwononga; pakuti kachisi wa Mulungu ali woyera, [kachisi] ameneyo ndi inu.
  5285. 1Co 3:18 Munthu aliyense asadzinyenge yekha. Ngati wina ayesa kuti ali wanzeru pakati pa inu pa dziko lino lapansi, iye adzikhalitse wopusa, kuti akakhale wanzeru.
  5286. 1Co 3:19 Pakuti nzeru ya dziko lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m’chenjerero lawo.
  5287. 1Co 3:20 Ndiponso Ambuye azindikira zolingalira za anzeru, kuti ziri zopanda pake.
  5288. 1Co 3:21 Choncho pasakhale munthu m’modzi wodzitamanda mwa anthu. Pakuti zinthu zonse ziri zanu.
  5289. 1Co 3:22 Ngakhale Paulo, kapena Apolos, kapena Kefasi, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena zinthu za makono, kapena zirinkudza; zonse ndi zanu;
  5290. 1Co 3:23 Ndipo inu ndinu a Khristu; ndi Khristu [ndiye] wa Mulungu.
  5291. 1Co 4:1 Munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.
  5292. 1Co 4:2 Koposa apo kuyenera mwa adindo, kuti munthu apezeke wokhulupirika.
  5293. 1Co 4:3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang’ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena ndi chiweruzo cha munthu: inde ine sindidziweruza ndekha.
  5294. 1Co 4:4 Pakuti sindidziwa kanthu kodziyerekezera mwa ine ndekha; chotero sindiri pano monga wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.
  5295. 1Co 4:5 Choncho musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzawonetsera zobisika za mdima; nadzawonetsera ma uphungu a mitima: ndipo pamenepo munthu aliyense adzakhala nawo matamando a kwa Mulungu.
  5296. 1Co 4:6 Koma zinthu izi, abale, ndadziphiphiritsa ndekha ndi [kwa] Apolos chifukwa cha inu; kuti mwa ife mukaphunzire kusaganiza za anthu kopitirira zimene zalembedwa, kuti pasakhale m’modzi wa inu wodzitukumulira kwa wina ndi mzake.
  5297. 1Co 4:7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani [ndi wina?] Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira [icho], udzitamanda bwanji, monga ngati sudachilandira [icho]?
  5298. 1Co 4:8 Tsopano muli wodzadza, tsopano mwalemera, mwalamulira monga mafumu wopanda ife: ndipo kuti mwa Mulungu inu mulamulire, kuti ifenso tikalamulire limodzi ndi inu.
  5299. 1Co 4:9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu adakhazikitsa ife atumwi wotsiriza, monga kudayikidwa ku imfa: pakuti takhala ife chowonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.
  5300. 1Co 4:10 Ife [tiri] wopusa chifukwa cha Khristu, koma [inu] muli anzeru mwa Khristu; ife [tiri] wofowoka, koma inu [muli] amphamvu; inu [muli] wolemekezeka, koma ife [tiri] wonyozeka.
  5301. 1Co 4:11 Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, ndi ludzu, ndipo tiri amaliseche, ndipo tiri okhomedwa, ndipo tiribe malo wokhala wotsimikizika;
  5302. 1Co 4:12 Ndipo tigwira ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha: polalatidwa, tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;
  5303. 1Co 4:13 Ponamiziridwa, tilimbikitsa; takhala monga zonyansa zadziko lapansi, [ndipo tiri] litsiro la zinthu zonse kufikira tsopano.
  5304. 1Co 4:14 Sindilemba zinthu izi kukuchititsani manyazi inu, koma monga ana anga wokondedwa kuchenjeza [inu].
  5305. 1Co 4:15 Pakuti mungakhale muli nawo aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, komatu [mulibe] atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndabala inu mwa uthenga wabwino.
  5306. 1Co 4:16 Mwa ichi ndikupemphani, khalani akutsanza ine.
  5307. 1Co 4:17 Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteyo, amene ali mwana wanga wokondedwa, ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga zomwe ziri mwa Khristu, monga ndiphunzitsa paliponse mu mipingo yonse.
  5308. 1Co 4:18 Tsopano ena adzitukumula, monga ngati sindidalinkudza kwa inu.
  5309. 1Co 4:19 Koma ndidzafika kwa inu posachedwa, akalola Ambuye, ndipo ndidzazindikira, si mawu a iwo wodzitukumula, koma mphamvuyo.
  5310. 1Co 4:20 Pakuti ufumu wa Mulungu si [uli] m’mawu, koma mu mphamvu.
  5311. 1Co 4:21 Mufuna chiyani? Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi [mwa] mzimu wakufatsa?
  5312. 1Co 5:1 Kwamveka paliponse kuti [pali] chiwerewere pakati pa inu, ndipo chiwerewere chotere chonga sichitchulidwa mwa Amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.
  5313. 1Co 5:2 Ndipo mukhala wodzitukumula, ndipo makamaka simudalire, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene achita ntchito iyi.
  5314. 1Co 5:3 Pakuti inedi, monga osakhalako mthupi langa, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndidaliko, [zokhudzana] ndi iye adachita ntchito iyi.
  5315. 1Co 5:4 M’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, posonkhana pamodzi inu, ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu.
  5316. 1Co 5:5 Kumpereka iye wochita chotere kwa Satana kuti liwonongeke thupi, koma mzimu upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye Yesu.
  5317. 1Co 5:6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chofufumitsa pang’ono chifufumitsa mtanda wonse?
  5318. 1Co 5:7 Choncho chotsani chofufumitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli wosafufumitsidwa. Pakuti Khristu paskha wathu waperekedwa chifukwa cha ife.
  5319. 1Co 5:8 Choncho tichite phwando, si ndi chofufumitsa chakale, kapena ndi chofufumitsa cha dumbo ndi kuyipa mtima; koma [mkate] wopanda chofufumitsa wa kuwona mtima, ndi chowonadi:
  5320. 1Co 5:9 Ndidalembera inu, m’kalata ija, kuti musayanjana ndi achiwerewere;
  5321. 1Co 5:10 Komatu osati pamodzi ndi a chiwerewere a dziko lino lapansi, kapena ndi wosirira, kapena wolanda, kapena ndi wopembedza mafano; pakuti mkutero muyenera mukatuluke m’dziko lapansi.
  5322. 1Co 5:11 Koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati munthu wina wotchedwa mbale ali wachiwerewere, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalata, kapena woledzera, kapena wolanda, ndi m’modzi wotere ayi osadya [naye].
  5323. 1Co 5:12 Pakuti nditani nawo akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m’katimo simuwaweruza ndi inu?
  5324. 1Co 5:13 Koma iwo akunja awaweruza Mulungu? Choncho chotsani munthu woyipayo pakati pa inu nokha.
  5325. 1Co 6:1 Alimba mtima wina wa inu, pamene ali nawo mlandu pa mzake, kupita kukaweruzidwa kwa wosalungama, osati kwa woyera mtima?
  5326. 1Co 6:2 Kapena kodi simudziwa kuti woyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi lidzaweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?
  5327. 1Co 6:3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?
  5328. 1Co 6:4 Ngati tsono, inu muli nawo maweruzo a zinthu za moyo uno, khazikitsani iwo kuti aweruze iwo amene ayesedwa apansi mu mpingo.
  5329. 1Co 6:5 Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe m’modzi wanzeru? Ayi, wosati m’modzi iye amene adzakhoza kuweruza pakati pa abale?
  5330. 1Co 6:6 Koma mbale apita kwa a malamulo kukaweruzidwa mlandu ndi mbale, ndipotu ichi kwa wosakhulupirira.
  5331. 1Co 6:7 Ndipo choncho pali cholakwika chotheratu pakati pa inu, chifukwa kuti mupita ku malamulo [a milandu] wina ndi mzake. Chifukwa chiyani inu simunasankhula kutenga kulakwa? Chifukwa ninji kulola [inu eni nokha] kunyengedwa?
  5332. 1Co 6:8 Ayi, muchita cholakwa, nimunyenga, ndipo mutero nawo abale [anu].
  5333. 1Co 6:9 Kapena simudziwa kuti wosalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achiwerewere, kapena wopembedza mafano, kapena achigololo, kapena amuna okhala ngati akazi, kapena akudziyipsa wokha ndi amuna anzawo.
  5334. 1Co 6:10 Kapena mbala, kapena wosirira, kapena woledzera, kapena wolalatira, kapena wolanda, sadzalandira ufumu wa Mulungu.
  5335. 1Co 6:11 Ndipo ena a inu mudali wotere: koma mudasambitsidwa, koma mudapatulidwa, koma mudayesedwa wolungama, m’dzina la Ambuye Yesu ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.
  5336. 1Co 6:12 ¶Zinthu zonse zivomerezeka mwa lamulo kwa ine koma si zonse zipindula. Zinthu zonse zivomerezeka mwa lamulo kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.
  5337. 1Co 6:13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya: koma Mulungu adzawononga zonse iyo ndi izo. Koma thupi siliri la chiwerewere, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa kwa thupi.
  5338. 1Co 6:14 Ndipo Mulungu adawukitsa Ambuye, ndiponso adzawukitsa ife mwa mphamvu yake.
  5339. 1Co 6:15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Kodi tsono ndidzatenga ziwalo za Khristu, ndikuziyesa [izo] ziwalo za mkazi wachiwerewere? Mulungu akuletsa.
  5340. 1Co 6:16 Chiyani kodi? Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, atero iye, adzakhala thupi limodzi.
  5341. 1Co 6:17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.
  5342. 1Co 6:18 Thawani chiwerewere. Tchimo lirilonse munthu amachita liri kunja kwa thupi; koma iye wakuchita chiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.
  5343. 1Co 6:19 Chiyani kodi? Simudziwa kodi kuti thupi lanu liri kachisi wa Mzimu Woyera, [amene ali] mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu, ndipo simuli a inu nokha?
  5344. 1Co 6:20 Pakuti mudagulidwa ndi mtengo: choncho lemekezani Mulungu m’thupi lanu, ndi mu mzimu wanu, zimene ziri zake za Mulungu.
  5345. 1Co 7:1 Tsopano za izi mudandilembera inezi: [kuli] bwino kwa mwamuna kusakhudza mkazi.
  5346. 1Co 7:2 Komabe [popewa] chiwerewere mwamuna aliyense akhale naye mkaziwa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.
  5347. 1Co 7:3 Mwamuna apereke kwa mkazi mangawa ake: chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna.
  5348. 1Co 7:4 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye: ndipo chimodzimodzinso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mkazi ndiye.
  5349. 1Co 7:5 Musamakanizana wina ndi mzake, pokhapokha [patakhala] kuvomerezana kwanu kwa kanthawi, kuti mukadzipereke ku kusala ndi kupemphera; nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusowa kwa kudziletsa kwanu.
  5350. 1Co 7:6 Koma ichi ndinena monga mwa kulola, [si] monga mwa lamulo.
  5351. 1Co 7:7 Pakuti ndikadafuna amuna onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina ya mtundu wotere, wina yonga iyo.
  5352. 1Co 7:8 Choncho ndinena kwa wosakwatiwa ndi kwa akazi a masiye, kuti kuli bwino iwo ngati angakhale monganso ine ndiri.
  5353. 1Co 7:9 Koma ngati sadziwa kudziletsa, aloleni akwatiwe: pakuti nkwabwino kukwatiwa koposa kutentha thupi.
  5354. 1Co 7:10 Ndi wokwatitsidwawo ndiwalamulira, [apatu] si ine ayi, koma Ambuye, Mkazi asamchokere mwamuna [wake]:
  5355. 1Co 7:11 Koma ngati amchokera, akhale wosakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamuna [wakeyo]: ndipo mwamuna asalekane naye mkazi [wake].
  5356. 1Co 7:12 Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye: ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asamleke iye.
  5357. 1Co 7:13 Ndipo mkazi ngati ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asamleke iye.
  5358. 1Co 7:14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa ndi mkazi wakeyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa ndi mwamuna wakeyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala odetsedwa, koma tsopano akhala woyera.
  5359. 1Co 7:15 Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, mloleni iye achoke. Mbaleyo, kapena mlongoyo samangidwa ukapolo nkhani zimenezi; koma Mulungu watiyitanira ifekumtendere.
  5360. 1Co 7:16 Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamuna [wakoyo]? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi [wakoyo]?
  5361. 1Co 7:17 ¶Koma, monga Mulungu wagawira kwa munthu aliyense, monga Ambuye ayitana yense, motero ayende. Ndipo kotero ndikhazikitsa m’mipingo yonse.
  5362. 1Co 7:18 Kodi wayitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi wayitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.
  5363. 1Co 7:19 Mdulidwe si uli kanthu, ndi kusadulidwa sikuli kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.
  5364. 1Co 7:20 Munthu aliyense akhale m’mayitanidwe m’mene iye adayitanidwamo.
  5365. 1Co 7:21 Kodi udayitanidwa [wokhala] mtumiki? Usachisamalira ichi: koma ngati ukhozanso kupangidwa mfulu, gwiritsa [ichi] ntchito.
  5366. 1Co 7:22 Pakuti iye amene adayitanidwa mwa Ambuye, [pokhala] ali mtumiki, ali mfulu wa Ambuye: momwenso iye amene wayitanidwa, [pokhala] ali mfulu, ali mtumiki wa Khristu.
  5367. 1Co 7:23 Mwagulidwa ndi mtengo; musakhale inu akapolo a anthu.
  5368. 1Co 7:24 Abale, munthu aliyense, m’mene iye adayitanidwamo, m’menemo akhale ndi Mulungu.
  5369. 1Co 7:25 ¶Tsopano zokhudza anamwali ndiribe lamulo la Ambuye: koma ndipereka kuweruza kwanga, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.
  5370. 1Co 7:26 Choncho ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo yino, [ndinena], kuti [kuli] kwabwino kwa munthu kukhala moteromo.
  5371. 1Co 7:27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.
  5372. 1Co 7:28 Koma ndipo ngati ukwatira, sudachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sadachimwe. Koma wotere adzakhala nacho chivuto m’thupi, koma inu ndikulekani.
  5373. 1Co 7:29 Koma ichi nditi, abale, nthawi ili yayifupi: chotsala ndi, kuti iwo akukhala nawo akazi akhale monga ngati alibe;
  5374. 1Co 7:30 Ndi iwo akulira, monga ngati sadalira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sadakondwera; ndi iwo akugula, monga ngati alibe kanthu.
  5375. 1Co 7:31 Ndi iwo akuchita nalo dziko lapansili, monga ngati osarichititsa molakwika; pakuti mawonekedwe a dziko ili apita.
  5376. 1Co 7:32 Koma ndifuna kuti mukhale wosadera nkhawa. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, momwe angakondweretsere Ambuye.
  5377. 1Co 7:33 Koma iye wokwatira alabadira zinthu zomwe ziri za dziko lapansi, momwe angakondweretsere mkazi [wake].
  5378. 1Co 7:34 Palikusiyananso pakati pa mkazi wokwatiwa ndi namwali. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mu mzimu: koma wokwatiwayo alabadira za zinthu za dziko lapansi, momwe angakondweretsere mwamuna [wake].
  5379. 1Co 7:35 Ndipo ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma cha kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye wopanda chokusokonezani.
  5380. 1Co 7:36 Koma mwamuna wina aganiza kuti achitira iye yekha chosasangalatsa kwa namwali wake, ngati pali kupitirira pa unamwali [wake], ndipo kukafunika kutero, aloledwe kuchita chimene afuna, iye sachimwa; aloleni iwo akwatiwe.
  5381. 1Co 7:37 Koma iye amene ayima wokhazikika mu mtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nawo ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha kuti asunga namwaliwake, adzachita bwino.
  5382. 1Co 7:38 Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wa mkazi achita bwino; koma iye wosamkwatitsa achita bwino koposa.
  5383. 1Co 7:39 Mkazi amangika ndi lamulo pokhala mwamuna ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna, ali womasuka kuti akwatiwe naye amene afuna; [koma] mwa Ambuye okha.
  5384. 1Co 7:40 Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuweruza kwanga: ndipo ndiganiza kuti insenso ndiri naye Mzimu wa Mulungu.
  5385. 1Co 8:1 Tsopano zokhudza za zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti tiri nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chidzitukumula, koma chikondi chimangirira.
  5386. 1Co 8:2 Ngati munthu wina aliyense aganiza kuti iye adziwa kalikonse, sadziwa kalikonse monga ayenera kudziwa.
  5387. 1Co 8:3 Koma ngati munthu aliyense akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi iye.
  5388. 1Co 8:4 Choncho monga zokhudza kudya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano [si liri] kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti [palibe] Mulungu koma m’modzi.
  5389. 1Co 8:5 Pakuti ngakhalenso iliko yoti yotchulidwa milungu, kapena m’mwamba, kapena pa dziko lapansi, (monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri,)
  5390. 1Co 8:6 Koma kwa ife [pali] Mulungu m’modzi, Atate, amene zinthu [zirizonse] zichokera kwa iye, ndi ife mwa iye; ndi Ambuye m’modzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife kudzera mwa iye.
  5391. 1Co 8:7 Komatu chidziwitso [si chili] mwa onse: koma ena ndi chikumbumtima cha fano kufikira tsopano adyako monga koperekedwa nsembe kwa fano; ndipo popeza chikumbumtima nchofowoka chidetsedwa.
  5392. 1Co 8:8 Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu: kapena ngati, tidya kodi tiri oposa; kapena, ngati sitidya kodi tiri woyipirapo.
  5393. 1Co 8:9 Koma yang’anirani kuti ufulu wanu umenewu ungakhale chophunthwitsa iwo amene ali wofowoka.
  5394. 1Co 8:10 Pakuti ngati munthu aliyense akawona iwe amene uli nacho chidziwitso ulikukhala pa chakudya m’kachisi wa fano, kodi chikumbumtima cha iye amene ali wofowoka, sichidzalimbikitsidwa kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano;
  5395. 1Co 8:11 Ndipo mwa chidziwitso chako mbale wofowokayo adzatayika, amene iye Khristu adamfera.
  5396. 1Co 8:12 Koma pakuchimwira abale motero, ndi kuvulaza chikumbumtima chawo chofowoka, inu muchimwira Khristu.
  5397. 1Co 8:13 Mwa ichi, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama ku nthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.
  5398. 1Co 9:1 Kodi sindine mtumwi? Kodi sindine mfulu? Kodi sindidawona Yesu Khristu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?
  5399. 1Co 9:2 Ngati sindiri mtumwi kwa ena, komatu mosakayikitsa ndiri kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.
  5400. 1Co 9:3 Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi,
  5401. 1Co 9:4 Kodi tiribe ulamuliro wakudya ndi kumwa?
  5402. 1Co 9:5 Kodi tiribe ulamuliro wakuyendayenda naye mlongo, mkazi, monganso atumwi ena, ndi [monga] abale a Ambuye, ndi Kefasi?
  5403. 1Co 9:6 Kapena kodi ine ndekha, ndi Barnabas, tiribe ulamuliro wakusagwira ntchito?
  5404. 1Co 9:7 Msirikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse nadzifunira zake yekha? Ndani abzala munda wa mphesa, ndi kusadyako zipatso zake? Kapena aweta busa ndani, wosadyako mkaka wake wa busalo?
  5405. 1Co 9:8 Kodi ndiyankhula izi monga munthu? Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo?
  5406. 1Co 9:9 Pakuti m’chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamiza pakamwa pa ng’ombe pakupuntha iyo tirigu. Kodi Mulungu asamalira ng’ombe?
  5407. 1Co 9:10 Kapena achinena iye [ichi] konsekonse chifukwa cha ife? Chifukwa cha ife, mosakayikitsa, [izi] zalembedwa: kuti iye wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo; ndi kuti iye wopunthayo m’chiyemebekezo akhale wogawana naye wa chiyembekezo chake.
  5408. 1Co 9:11 Ngati takufeserani inu zinthu za uzimu, [ndi chinthu] chachikulu ngati ife tituta za kuthupi zanu?
  5409. 1Co 9:12 Ngati ena akhala wogawana nawo ulamuliro [umenewu] pa inu, [si] ife nanga koposa? Koma sitichita nawo ulamuliro umenewu; koma timalola zinthuzonse, kuti tingachite chotchinga uthenga wabwino wa Khristu.
  5410. 1Co 9:13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za kachisi amakhala ndi moyo ndi [zinthu] zopatulika? Ndi iwo akuyimirira pa guwa la nsembe agawana nalo guwa la nsembe?
  5411. 1Co 9:14 Chomwechonso Ambuye adakhazikitsa kuti iwo amene alalikira uthenga wabwino akhale ndi moyo ndi uthenga wabwino.
  5412. 1Co 9:15 Koma ine sindidachita nako kanthu ka zinthu izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero kwa ine: pakuti, [kukadakhala] kondikomera ine kufa, koposa kuti munthu asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.
  5413. 1Co 9:16 Pakuti ngakhale ndilalikira uthenga wabwino, ndiribe kanthu kakudzitamandira: pakuti chondikakamiza chayikidwa pa ine; inde, tsoka ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.
  5414. 1Co 9:17 Pakuti ngati ndichita ichi mwakufuna, mphotho ndiri nayo: koma ngati motsutsana ndi chifuniro changa, nyengo yakugawira [ya uthenga wabwino] yaperekedwa kwa ine.
  5415. 1Co 9:18 Mphotho yanga nchiyani tsono? [Ndithudi] kuti pakulalikira uthenga wabwino, ndingapangitse uthenga wabwino wa Khristu ukhale wa ulere, kuti ndisayipse ulamuliro wanga mu uthenga wabwino.
  5416. 1Co 9:19 Pakuti ngakhale ndiri mfulu kwa [anthu] onse, komatu ndakhala ndekha kapolo kwa onse, kuti ndipindule wochuluka.
  5417. 1Co 9:20 Ndipo kwa Ayuda ndidakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo womvera lamulo, monga womvera lamulo, kuti ndipindule iwo womvera malamulo;
  5418. 1Co 9:21 Kwa iwo wopanda lamulo, monga wopanda lamulo, (wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu,) kuti ndipindule iwo wopanda lamulo.
  5419. 1Co 9:22 Kwa wofowoka ndikhala ngati wofowoka, kuti ndipindule iwo wofowoka: ndakhala zinthu zonse kwa [anthu] onse, kuti mwa njira ina iliyonse ndikapulumutse ena.
  5420. 1Co 9:23 Ndipo ndichita izi zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndikakhale potero wogawana nanu.
  5421. 1Co 9:24 Kodi simudziwa kuti iwo akuchita mpikisano wa liwiro athamanga onse, koma m’modzi alandira mphotho? Motero thamangani, kuti mukalandire.
  5422. 1Co 9:25 Koma munthu aliyense wakulimbana za ukatswiri adzikanizira zinthu zonse. Ndipo iwowa [achita ichi] kuti alandire korona wovunda; koma ife wosavunda.
  5423. 1Co 9:26 Choncho ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha; ine ndilimbana chotero, si monga ngati m’modzi womenya mphepo.
  5424. 1Co 9:27 Koma ndilamulira thupi langa, ndipo ndiribweretsa [ilo] kukumvera ulamuliro wanga: kuti, kapena mwa njira ina, pamene nditalalikira kwa ena, ine mwini ndingakhale wotayidwa kunja.
  5425. 1Co 10:1 Kuwonjezera apo, abale, sindifuna kuti mukhale wosadziwa, momwe mwakuti makolo athu onse adali pansi pa mtambo, nawoloka nyanja onse;
  5426. 1Co 10:2 Nabatizidwa onse kwa Mose mu mtambo ndi m’nyanja,
  5427. 1Co 10:3 Ndipo anadya onse chakudya cha uzimu chimodzimodzi;
  5428. 1Co 10:4 Ndipo anamwa onse chakumwa cha uzimu chimodzimodzi; pakuti adamwa mwa Thanthwe la uzimu lakuwatsata: ndipo thanthwe limenero linali Khristu.
  5429. 1Co 10:5 Koma ndi wochuluka a iwo Mulungu sadakondwera nawo; pakuti iwo adakanthidwa m’chipululumo.
  5430. 1Co 10:6 Tsopano zinthu izi zinali chitsanzo chathu, ndi cholinga kuti tisalakalake zoyipa ife, monganso iwowo adalakalaka.
  5431. 1Co 10:7 Kapena musakhale wopembedza mafano, monga [ena] a iwo; monga kwalembedwa, Anthu adakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.
  5432. 1Co 10:8 Kapena tisachite dama, monga ena a iwo adachita, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.
  5433. 1Co 10:9 Kapena tisayese Khristu, monga ena a iwo adayesa, nawonongeka ndi njoka.
  5434. 1Co 10:10 Kapena musang’ung’udze, monga ena a iwo anang’ung’udza, nawonongeka ndi wowonongayo.
  5435. 1Co 10:11 Tsopano zonse izi zidachitika kwa iwowa monga zitsanzo: ndipo zidalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano afikapo.
  5436. 1Co 10:12 Mwa ichi iye wakuganiza kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.
  5437. 1Co 10:13 Sichidakugwerani inu chiyeso koma chomwe chigwera kwa munthu; koma Mulungu [ali] wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzayikanso njira yopulumukirapo, kuti mudzakhoze kupirira [icho].
  5438. 1Co 10:14 Mwa ichi, wokondedwa abale anga, thawani kupembedza mafano.
  5439. 1Co 10:15 Ndinena monga kwa anthu anzeru; weruzani inu chimene ine ndinena.
  5440. 1Co 10:16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichiri chiyanjano cha mwazi wa Khristu? Mkate umene tinyema, si uli chiyanjano chathupi la Khristu kodi?
  5441. 1Co 10:17 Pakuti ife [pokhala] ambiri tiri mkate umodzi, [ndi] thupi limodzi: pakuti ife tonse tiri wogawana a mkate umodzi umenewu.
  5442. 1Co 10:18 Tapenyani Israyeli monga mwa thupi: kodi sali iwo akudya za nsembezo wogawana a guwa la nsembelo?
  5443. 1Co 10:19 Ndinena chiyani tsono? Kapena kuti fano liri kanthu kodi? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu?
  5444. 1Co 10:20 Koma [nditi], kuti zimene Amitundu apereka nsembe, azipereka kwa ziwanda; ndipo osati kwa Mulungu: ndipo sindifuna kuti inu mukhale ndi chiyanjano ndi ziwanda.
  5445. 1Co 10:21 Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda: simungathe kukhala wogawana nawo a gome la Ambuye, ndi a gome la ziwanda.
  5446. 1Co 10:22 Kodi kapena tichititsa nsanje Ambuye? Kodi tiri amphamvu woposa iye?
  5447. 1Co 10:23 Zinthu zonse zilolekakwa ine; koma zinthu zonse sizipindula: zinthu zonse ziloleka kwa ine; koma zinthu zonse sizimangilira.
  5448. 1Co 10:24 Munthu asafune zake za iye yekha, koma munthu aliyense za [chuma cha] mzake.
  5449. 1Co 10:25 Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, [chimenecho] mudye, osafunsa mafunso chifukwa cha chikumbumtima:
  5450. 1Co 10:26 Pakuti dziko lapansi [liri] la Ambuye, ndi kudzala kwakeko.
  5451. 1Co 10:27 Ngati wina wa wosakhulupirira akayitana inu [ku phwando], ndipo mufuna kupita; chilichonse chayikidwira inu, mudye, osafunsa mafunso chifukwa cha chikumbumtima.
  5452. 1Co 10:28 Koma ngati wina akati kwa inu. Ichi chaperekedwa nsembe kwa mafano, musadye chifukwa cha iye wakuwonetsayo, ndi chifukwa cha chikumbumtima; pakuti dziko lapansi liri la Ambuye ndi kudzala kwakeko.
  5453. 1Co 10:29 Ndinena, chikumbumtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uweruzidwa ninji ndi chikumbumtima cha [munthu] wina?
  5454. 1Co 10:30 Ngati ine ndikhala wogawana nawo mwachisomo, ndineneredwa bwanji zoyipa chifukwa cha ichi chimene ndiperekapo mayamiko?
  5455. 1Co 10:31 Choncho mungakhale inu mudya, kapena mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
  5456. 1Co 10:32 Khalani osakhumudwitsa aliyense, kapena kwa Ayuda, kapena kwa Ahelene, kapena kwa Mpingo wa Mulungu:
  5457. 1Co 10:33 Monga inenso ndikondweretsa [anthu] onse [m’zinthu] zonse, wosafuna chipindulo changa, koma [chipindulo] cha ambiri, kuti iwo angathe kupulumutsidwa.
  5458. 1Co 11:1 Khalani wonditsanza ine, monganso ine [ndiri] wa Khristu.
  5459. 1Co 11:2 Tsopano ndikutamandani inu, abale, kuti m’zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo, monga ndidapereka [iyo] kwa inu.
  5460. 1Co 11:3 ¶Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa mwamuna aliyense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi [ndiye] mwamuna; ndipo mutu wa Khristu [ndiye] Mulungu.
  5461. 1Co 11:4 Mwamuna aliyense popemphera kapena ponenera, ataphimba mutu [wake] anyoza mutu wake.
  5462. 1Co 11:5 Koma mkazi aliyense popemphera kapena kunenera wosaphimba mutu [wake] anyoza mutu wake: pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.
  5463. 1Co 11:6 Pakuti ngati mkazi saphimbidwa, asengedwenso: koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, aphimbidwe.
  5464. 1Co 11:7 Pakuti mwamuna sayenera kuphimba mutu [wake], powona kuti ali fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.
  5465. 1Co 11:8 Pakuti mwamuna saliwa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna.
  5466. 1Co 11:9 Pakutinso mwamuna sadalengedwa chifukwa cha mkazi; koma mkazi chifukwa cha mwamuna.
  5467. 1Co 11:10 Chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nawo ulamuliro pamutu [pake], chifukwa cha angelo.
  5468. 1Co 11:11 Komanso kapena mwamuna sakhala wopanda mkazi, kapena mkazi sakhala wopanda mwamuna, mwa Ambuye.
  5469. 1Co 11:12 Pakuti monga mkazi [ali] wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna akhala kudzera mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mulungu.
  5470. 1Co 11:13 Weruzani mwa inu nokha: kodi nkuyenera kuti mkazi apemphere kwa Mulungu, wosaphimba mutu?
  5471. 1Co 11:14 Kodi ngakhale chibadwidwe mwa icho chokha sichitiphunzitsa, kuti, ngati mwamuna aweta tsitsi lalitali, chili chochititsa manyazi kwa iye?
  5472. 1Co 11:15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi lalitali, kuli ulemerero wa kwa iye; pakuti tsitsi [lake] lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.
  5473. 1Co 11:16 Koma akawoneka munthu wina achita ngati motetana, tiribe ife makhalidwe wotere, kapena mipingo ya Mulungu.
  5474. 1Co 11:17 ¶Tsopano pakulengeza ichi [kwa inu] ine sindikutamani [inu], pakuti simusonkhanira chokoma, koma choyipa.
  5475. 1Co 11:18 Pakutitu choyambira pa zonse, posonkhana inu mu mpingo, ndimva kuti pakhala mipatuko mwa inu; ndipo ndikhulupirira pang’ono.
  5476. 1Co 11:19 Pakuti kuyenera kuti pakhale ziphunzitso zonyenga mwa inu, kuti iwo wovomerezedwa awonetsedwe pakati pa inu.
  5477. 1Co 11:20 Choncho, pakusonkhana inu pamalo amodzi, uku [sikuli] kudya mgonero wa Ambuye.
  5478. 1Co 11:21 Pakuti pakudyaku aliyense atenga [wina] asanatenge mgonero wake wa yekha: ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.
  5479. 1Co 11:22 Chiyani? Mulibe kodi nyumba zodyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi inu munyoza mpingo wa Mulungu, ndi kuchititsa manyazi iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m’menemo? Sindikutamani [inu] ayi.
  5480. 1Co 11:23 Pakuti ine ndidalandira kwa Ambuye chimenenso ndidapereka kwa inu, Kuti Ambuye Yesu usiku [womwe] uja adaperekedwa adatenga mkate.
  5481. 1Co 11:24 Ndipo m’mene adayamika, adawunyema, ndipo adati, Tengani, idyani: ichi ndi thupi langa lophwanyidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.
  5482. 1Co 11:25 Chimodzimodzinso [anatenga], chikho atatha kudya, ndi kunena kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga: chitani ichi, mwa kawirikawiri mukamwa [uwo], mukumbukiraine.
  5483. 1Co 11:26 Pakuti mwa kawirikawiri mukadya mkate uwu, ndi kumwa chikho ichi, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira adzadza.
  5484. 1Co 11:27 Mwa ichi, yense amene adzadya mkate, ndi kumwa chikho ichi cha Ambuye, kosayenera, adzakhala wochimwira thupilo ndi mwazi wa Ambuye.
  5485. 1Co 11:28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate umenewo, ndi kumwera chikho [chimenecho].
  5486. 1Co 11:29 Pakuti iye wakudya ndi kumwa mosayenera, adya ndi kumwa ku chiweruzo kwa iye yekha, osazindikira thupi la Ambuyelo.
  5487. 1Co 11:30 Chifukwa cha ichi [ambiri] ali wofowoka ndi wodwala mwa inu, ndipo ambiri agona.
  5488. 1Co 11:31 Chifukwa ngati tikadadziweruza tokha, sitikadaweruzidwa.
  5489. 1Co 11:32 Koma pamene tiweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.
  5490. 1Co 11:33 Mwa ichi, abale anga, pamene musonkhana kuti mudye lindanani.
  5491. 1Co 11:34 Ndipo ngati wina ali ndi njala, adye kwawo; kuti mungasonkhanire ku chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzaziyika mundondomeko ndikadza ine.
  5492. 1Co 12:1 Tsopano za [mphatso] za uzimu, abale, sindifuna kuti mukhale wosadziwa.
  5493. 1Co 12:2 Mudziwa kuti mudali Amitundu, wotengedwa kunka kwa mafano awa wosayankhula, monga mudatsogozedwa.
  5494. 1Co 12:3 Mwa ichi, ndikuwuzani inu, kuti palibe munthu wakuyankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena Yesu ngotembereredwa; ndi [kuti] palibe wina akhoza kunena kuti Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.
  5495. 1Co 12:4 Ndipo pali mphatso zamitundumitundu koma Mzimu yemweyo.
  5496. 1Co 12:5 Ndipo pali mautumiki wosiyana, koma Ambuye yemweyo.
  5497. 1Co 12:6 Ndipo pali machitidwe amitundumitundu, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.
  5498. 1Co 12:7 Koma kwa onse kwapatsidwa mawonekedwe a Mzimu kuti apindule mowonjezerapo.
  5499. 1Co 12:8 Pakuti kwa m’modzi kwapatsidwa mwa Mzimu mawu a nzeru; koma kwa wina mawu a chidziwitso, mwa Mzimu yemweyo.
  5500. 1Co 12:9 Kwa wina chikhulupiriro mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso mwa Mzimu yemweyo;
  5501. 1Co 12:10 Kwa wina kuchita zozizwitsa; kwa wina kunenera; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malirime a [mitundumitundu]; kwa wina mamasulidwe a malirime:
  5502. 1Co 12:11 Koma zonse izi achita Mzimu m’modzi yemweyo, nagawirakwa yense pa yekha monga iye afunira.
  5503. 1Co 12:12 Pakuti monga thupi liri limodzi, ndipo liri nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonse zathupi limodzilo, pokhala zambiri, ziri thupi limodzi: momwemonso [ali] Khristu.
  5504. 1Co 12:13 Pakuti mwa Mzimu m’modzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m’thupi limodzi, ngakhale [tikhale] Ayuda kapena Ahelene, ngakhale [tikhale] akapolo kapena mfulu; ndipo tonse tidamwetsedwa Mzimu m’modzi.
  5505. 1Co 12:14 Pakuti thupi sirikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri.
  5506. 1Co 12:15 Ngati phazi likati, Popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi choncho si liri la thupi?
  5507. 1Co 12:16 Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindiri diso, sindiri wa thupi; kodi choncho si liri la thupi?
  5508. 1Co 12:17 Ngati thupi lonse [likadakhala] diso [kukadakhala] kuti kumvera. Ngati thupi lonse [likadakhala] kumva, [kukadakhala] kuti kununkhiza?
  5509. 1Co 12:18 Koma tsopano, Mulungu wayika ziwalo chilichonse cha izo m’thupi, monga kudamkondweretsa iye.
  5510. 1Co 12:19 Ndipo ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi; [likadakhala] kuti thupi.
  5511. 1Co 12:20 Koma tsopano [ziri] ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.
  5512. 1Co 12:21 Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, sindikufuna iwe: kapenanso mutu kwa mapazi, sindikufunani inu.
  5513. 1Co 12:22 Ayi, makamakatu ziwalo za thupilo, zoyesedwa zofowoka kwambiri, zifunika kwambiri;
  5514. 1Co 12:23 Ndipo [ziwalo] za thupi, zimene tiziyesa zochepa ulemu, pa izi tiyika ulemu wochuluka woposa; ndi ziwalo zathu zosawoneka bwino ziri nako kukongola koposa.
  5515. 1Co 12:24 Pakuti [ziwalo] zokoma zathu ziribe kusowa; koma Mulungu walumikiza thupi pamodzi, napatsa ulemu wochuluka kwa [chiwalo] chosowacho:
  5516. 1Co 12:25 Kuti pasakhale kugawanika m’thupi koma [kuti] ziwalo zisamalane mofanana china ndi chinzake.
  5517. 1Co 12:26 Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva zowawa, ziwalo zina zimva kuwawa pamodzi nacho; kapena chiwalo chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
  5518. 1Co 12:27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo yense pa yekha.
  5519. 1Co 12:28 Ndipo Mulungu wayika ena mu mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pambuyo pake zozizwa, kenaka mphatso za machiritso, mathandizo, kulongosola ntchito, malirime a mitundumitundu.
  5520. 1Co 12:29 [Ali] wonse atumwi kodi? [Ali] aneneri wonse kodi? [Ali] wonse aphunzitsi kodi? [Ali] wonse wochita zozizwa?
  5521. 1Co 12:30 Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse ayankhula ndi malirirme? Kodi onse amasulira?
  5522. 1Co 12:31 Koma funitsitsani mphatso zoposetsa, ndipo komatu ndiwonetsa inu njira yokoma yopambana.
  5523. 1Co 13:1 Ndingakhale ndiyankhula ndi malirime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe chikondi, ndikhala [ngati] mkuwa wotulutsa phokoso, kapena chimbale choyimba cha mkuwa chochita phokoso.
  5524. 1Co 13:2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kukhala [ndi mphatso ya] kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi chidziwitso chonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi ndiri chabe.
  5525. 1Co 13:3 Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa [wosawuka], ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe, ndipo ndiribe chikondi, sizindipindulira ine kanthu.
  5526. 1Co 13:4 Chikondi chikhala chilezere, [ndipo] chili chokoma mtima; chikondi sichichita kaduka; chikondi sichidzitamandira chokha, sichidzikuza.
  5527. 1Co 13:5 Sichichita mwa icho chokha zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima msanga, sichilingalira zoyipa:
  5528. 1Co 13:6 Sichikondwera ndi cholakwa, koma chikondwera m’chowonadi;
  5529. 1Co 13:7 Chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
  5530. 1Co 13:8 Chikondi sichimalephera, koma ngati [pakhala] zonenera, zidzalephera, kapena [pakhala] malirime, adzaleka, kapena [pakhala] nzeru idzatha.
  5531. 1Co 13:9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndipo tinenera mderamdera.
  5532. 1Co 13:10 Koma pamene changwiro chafika, tsono cha mderamdera chidzamalizika.
  5533. 1Co 13:11 Pamene ndidali mwana, ndidayankhula monga mwana, ndidamvetsa monga mwana, ndidaganiza monga mwana: tsopano ndakhala munthu, ndayesa zinthu chabe za chimwana.
  5534. 1Co 13:12 Pakuti tsopano tipenya kudzera m’kalirole, mwa m’dimadima; koma nthawiyo maso ndi maso: koma nthawiyo ndidzazindikiratu, monganso momwe ine ndizindikiridwa.
  5535. 1Co 13:13 Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi [ndicho] chikondi.
  5536. 1Co 14:1 Tsatani chikondi, koma mukhumbe [mphatso] za uzimu, koma koposa kuti mukanenere.
  5537. 1Co 14:2 Pakuti iye wakulankhula lirime [losadziwika] sayankhula kwa anthu ayi, koma kwa Mulungu: pakuti palibe munthu akumvetsetsa [iye]; koma mumzimu ayankhula zinsinsi.
  5538. 1Co 14:3 Koma iye wakunenera ayankhula ndi anthu [ku] kumangirira, ndi kulimbikitsa ndi kutonthoza.
  5539. 1Co 14:4 Iye wakuyankhula lirime [losadziwika], adzimangirira yekha; koma iye wakunenera amangirira mpingo.
  5540. 1Co 14:5 Ndipo ndikadafuna inu nonse muyankhula malirime, koma makamaka kuti mukanenere: pakuti iye wakunenera aposa wakuyankhula malirime, pokhapokha akamasulira, kuti mpingo ukalandire chomangirira.
  5541. 1Co 14:6 Tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kuyankhula malirime, ndikupindulitsani chiyani, pokhapokha ndikayankhula ndi inu mwavumbulutso, kapena mwachidziwitso, kapena mwakunenera, kapena mwachiphunzitso.
  5542. 1Co 14:7 Ndipo ngakhale zinthu zopanda moyo zopereka mawu, ngati toliro, kapena ngoli, pokhapokha ngati zipereka maliridwe osiyanitsa, chidzazindikirika bwanji chimene chiwombedwa kapena kuyimbidwa?
  5543. 1Co 14:8 Pakuti ngati lipenga lipereka mawu wosazindikirika, adzadzikonzekeretsa ndani kunkhondo?
  5544. 1Co 14:9 Momwemonso inu, pokhapokhapo muyankhula ndi lirime mawu wosavuta kuwazindikira, chidzazindikirika bwanji chimene chiyankhulidwa? Pakuti mudzayankhula ku mphepo.
  5545. 1Co 14:10 Iripo, kaya, mitundu yambiri ya mawu pa dziko lapansi, ndipo palibe kamodzi [ka] izo kasowa tanthawuzo.
  5546. 1Co 14:11 Choncho ngati sindidziwa tanthawuzo la mawuwo, ndidzakhala kwa iye woyankhulayo munthu wa dziko lakunja, ndipo woyankhulayo [adzakhala] wakunja kwa ine.
  5547. 1Co 14:12 Momwemo inunso, popeza inu muli achangu cha mphatso za [uzimu], funani kuti mukapambane ku kumangirira kwa mpingo.
  5548. 1Co 14:13 Mwa ichi iye amene ayankhula lirime [losadziwika] apemphere kuti iye amasulire.
  5549. 1Co 14:14 Pakuti ngati ndipemphera m’lirime [losadziwika], mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.
  5550. 1Co 14:15 Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, ndipo ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa: ndidzayimba ndi mzimu, ndipo ndidzayimbanso ndi chidziwitso.
  5551. 1Co 14:16 Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala nawo m’chipinda wosaphunzira adzati Amen bwanji pa kuyamika kwako, powona kuti sadziwa chimene unena?
  5552. 1Co 14:17 Pakutitu iwe ndithudi uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.
  5553. 1Co 14:18 Ndiyamika Mulungu wanga kuti ndiyankhula malirime koposa inu nonse:
  5554. 1Co 14:19 Koma mu mpingo ndifuna koposa kuyankhula mawu asanu ndi chidziwitso changa, kutinso [mwa mawu anga] ndikaphunzitsenso ena, koposa kuyankhula mawu zikwi khumi m’lirime [losadziwika].
  5555. 1Co 14:20 Abale, musakhale ana m’chidziwitso, koma m’choyipa khalani makanda, koma m’chidziwitso akulu msinkhu.
  5556. 1Co 14:21 Kwalembedwa m’chilamulo, ndi [anthu a] malirime ena ndipo ndi milomo yina ndidzayankhula nawo anthu awa; ndipo komatu mwa zonsezo iwo sadzamva ine, anena Ambuye.
  5557. 1Co 14:22 Mwa ichi malirime alia chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira; koma kwa iwo wosakhulupirira: koma kunenera sikutumikira kwa iwo wosakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.
  5558. 1Co 14:23 Choncho ngati mpingo wonse ukasonkhana pamalo amodzi, ndi onse akuyankhula malirime, ndipo akalowemo [iwo amene ali] wosaphunzira, kapena wosakhulupirira, kodi iwo sadzanena kuti inu muli amisala?
  5559. 1Co 14:24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo m’modzi wosakhulupirira, kapena [m’modzi] wosaphunzira, iye ali ndi mlandu kwa onse; aweruzidwa ndi onse:
  5560. 1Co 14:25 Ndipo chotero zobisika za mtima wake zidzawonetsedwa; ndipo chotero pogwetsa nkhope [yake] pansi adzalambira Mulungu, nadzalalikira kuti mwa chowonadi Mulungu ali ndithu mwa inu.
  5561. 1Co 14:26 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo lirime, ali nalo vumbulutso, ali nacho chimasuliro. Lolani zonse zichitike kukumangirira.
  5562. 1Co 14:27 Ngati munthu wina ayankhula lirime [losadziwika, akhale] mwa awiri, koma akachulukitsa [akhale] mwa atatu, ndipo [kuti] mwa kutsatana; ndipo amlole m’modzi amasulire.
  5563. 1Co 14:28 Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu mpingo, ndipo ayankhule kwa iye yekha, ndi kwa Mulungu.
  5564. 1Co 14:29 Aneneri ayankhule awiri kapena atatu, ndi winayo aweruze.
  5565. 1Co 14:30 Ngati [kanthu kena] kavumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, woyambayo akhale chete.
  5566. 1Co 14:31 Pakuti mukhoza nonse kunenera m’modzim’modzi, kuti onse aphunzire, ndi onse atonthozedwe.
  5567. 1Co 14:32 Ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;
  5568. 1Co 14:33 Pakuti Mulungu si ali [woyambitsa] chisokonezo, koma wa mtendere, monga mwa mipingo yonse ya woyera mtima.
  5569. 1Co 14:34 Akazi anu akhale chete m’mipingo: pakuti sikuloledwa kwa iwo kuyankhula: koma [iwo ali wolamulidwa] kuti akhale womvera, monganso chilamulo chinena.
  5570. 1Co 14:35 Ndipo ngati afuna kuphunzira kanthu, afunse amuna awo a iwo wokha kunyumba kwawo: pakuti kunyazitsa mkazi kuyankhula mu mpingo.
  5571. 1Co 14:36 Chiyani? Mawu a Mulungu adatuluka kwa inu? Kapena adafika kwa inu nokha?
  5572. 1Co 14:37 Ngati munthu wina aganiza mwa iye yekha kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri malamulo a Ambuye.
  5573. 1Co 14:38 Koma ngati munthu wina akhala wosadziwa, iye akhale wosadziwa.
  5574. 1Co 14:39 Mwa ichi, abale, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kuyankhula malirime.
  5575. 1Co 14:40 Zinthu zonse zichitike koyenera ndi molongosoka.
  5576. 1Co 15:1 Kupitirira apo ndikudziwitsani, abale, uthenga wabwino umene ndidakulakirani inu, umenenso mudawulandira, umenenso muyimamo.
  5577. 1Co 15:2 Umenenso mupulumutsidwa nawo, ngati mukumbukira zomwe ndidalalikira kwa inu; pokhapokha ngati mudakhulupirira mwachabe.
  5578. 1Co 15:3 Pakuti ndidapereka kwa inu poyamba pa zonse chimenenso ndidalandira, momwe mwakuti Khristu adafera zoyipa zathu monga mwa malembo;
  5579. 1Co 15:4 Ndi kuti adayikidwa m’manda; ndi kuti adawukanso tsiku la chitatu monga mwa malembo;
  5580. 1Co 15:5 Ndi kuti adawonekera kwa Kefasi, kenaka kwa khumi ndi awiriwo;
  5581. 1Co 15:6 Patatha apo, adawoneka pa nthawi imodzi kwa abale woposa mazana asanu, amene wochuluka a iwo atsala kufikira tsopano, koma ena adagona.
  5582. 1Co 15:7 Pambuyo pake, adawonekera kwa Yakobo; kenaka kwa atumwi onse.
  5583. 1Co 15:8 Ndipo potsiriza pake pa onse, adawoneka kwa inenso monga wa m’modzi wobadwa osati pa nthawi yake.
  5584. 1Co 15:9 Pakuti ine ndiri wamng’ono wa atumwi, kotero kuti ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndidazunza mpingo wa Mulungu.
  5585. 1Co 15:10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndiri ine amene ndiri: ndipo chisomo chake [choperekedwa] kwa ine sichidakhala chopanda pake, koma ndidagwira ntchito yochuluka kuposa onse: koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chidakhala ndi ine.
  5586. 1Co 15:11 Choncho ngati [ndinali ine] tsono, kapena iwowa kotero tilalikira, ndi kotero mudakhulupirira.
  5587. 1Co 15:12 Tsopano ngati Khristu alalikidwa kuti wawukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuwuka kwa akufa?
  5588. 1Co 15:13 Koma ngati kulibe kuwuka kwa akufa, Khristunso sadawukitsidwa;
  5589. 1Co 15:14 Ndipo ngati Khristu sadawukitsidwa, ndiye kuti kulalikira kwathu kuli chabe, ndipo chikhulupiriro chanunso chili chabe.
  5590. 1Co 15:15 Inde, ndipo ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa chakuti tidachita umboni kunena za Mulungu kuti adawukitsa Khristu: amene iye sadamuwukitsa, ngati kuli tero kuti akufa sawukitsidwa:
  5591. 1Co 15:16 Pakuti ngati akufa sawukitsidwa, ndiye kuti Khristunso sadawukitsidwa.
  5592. 1Co 15:17 Ndipo ngati Khristu sadawukitsidwa, chikhulupiriro chanu chili chabe; inu muli chikhalire m’machimo anu.
  5593. 1Co 15:18 Kotero iwonso amene agona tulo mwa Khristu ali otayika.
  5594. 1Co 15:19 Ngati tiyemebekezera Khristu m’moyo uno wokha, ife tiri kwa anthu onse womvetsa chisoni koposa.
  5595. 1Co 15:20 Koma tsopano Khristu wawukitsidwa kwa akufa, [ndipo] wakhala chipatso choyamba kucha cha iwo akugona.
  5596. 1Co 15:21 Pakuti monga imfa [idadza] mwa munthu, kuwuka kwa akufa [kudadzanso] mwa munthu.
  5597. 1Co 15:22 Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa moyo.
  5598. 1Co 15:23 Koma munthu aliyense m’dongosolo lake la iye yekha: Khristu chipatso choyamba kucha; pambuyo pake iwo amene ali ake a Khristu pakubwera kwake.
  5599. 1Co 15:24 Pomwepo [padzafika] chimaliziro, pamene iye adzakhale atapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate; pamene adzathetsa kulamulira ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu.
  5600. 1Co 15:25 Pakuti ayenera kuchita ufumu, kufikira atayika adani onse pansi pa mapazi ake.
  5601. 1Co 15:26 Mdani wotsiriza [amene] adzawonongedwa [ndiye] imfa.
  5602. 1Co 15:27 Pakuti iye adayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zayikidwa pansi pa mapazi [ake, izi] zawonetsedwa kuti sawerengapo, iye amene adayika zinthu zonsezo pansi pa iye.
  5603. 1Co 15:28 Ndipo pamene zonsezi zidzagonjetsedwa kwa iye, pomwepo Mwana wa mwamunanso iye mwini yekha adzakhla pansi pa iye amene adamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
  5604. 1Co 15:29 Ngati sikutero adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa, ngati akufa sawuka konse? Chifukwa chiyani iwo abatizidwa chifukwa cha akufa?
  5605. 1Co 15:30 Ndipo n’chifukwa chiyani ife tiyima m’mowopsa ora lirilonse?
  5606. 1Co 15:31 Nditsutsa mwa kukondwera kwanu kumene ndiri nako mwa Khristu Yesu Ambuye wathu, ine ndifa tsiku ndi tsiku.
  5607. 1Co 15:32 Ngati mwa khalidwe la wanthu ndidalimbana ndi zirombo ku Efeso, chindipindulanji ichi ine, ngati akufa sawuka? Tiyeni tidye ndi kumwa pakuti mawa timwalira.
  5608. 1Co 15:33 Musanyengedwe: chiyanjano choyipa chiyipsa makhalidwe wokoma.
  5609. 1Co 15:34 Ukani ku chilungamo, ndipo musachimwe: pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu: ndiyankhula [izi] kunyazitsa inu.
  5610. 1Co 15:35 Koma [munthu] wina adzati, Akufa awukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?
  5611. 1Co 15:36 Wopusa [iwe], chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, pokhapokha chitafa:
  5612. 1Co 15:37 Ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbewu yokha, kapena ya tirigu, kapena [mbewu] yina;
  5613. 1Co 15:38 Koma Mulungu ayipatsa thupi longa afuna iye; ndi kwa mbewu yonse thupi la iyo lokha.
  5614. 1Co 15:39 Nyama yonse siili imodzimodzi; koma [pali] yina ya [mtundu] umodzi nyama ya anthu, nyama yina ndiyo ya zirombo, yina ya nsomba, [ndi] yina ya mbalame,
  5615. 1Co 15:40 [Palinso] matupi a m’mwamba, ndi matupi a padziko; koma ulemerero wa la m’mwamba uli umodzi, ndi [ulemerero] wa la padziko [ndi] winanso.
  5616. 1Co 15:41 [Pali ulemerero] umodzi wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi: pakuti nyenyezi [imodzi] isiyana ndi nyenyezi [ina] mu ulemerero.
  5617. 1Co 15:42 Chomwechonso [kuli] kuwuka kwa akufa. Lifesedwa m’chivundi; liwukitsidwa m’chisavundi:
  5618. 1Co 15:43 Lifesedwa mu m’nyozo, liwukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m’chifowoko, liwukitsidwa mu mphamvu.
  5619. 1Co 15:44 Lifesedwa thupi la chibadwidwe, liwukitsidwa thupi la uzimu. Pali thupi lachibadwidwe, ndipo pali thupi lauzimu.
  5620. 1Co 15:45 Koteronso kwalembedwa, munthu woyamba Adamu, adakhala mzimu wamoyo, Adamu wotsiriza [adapangidwa] mzimu wakupatsa moyo.
  5621. 1Co 15:46 Komatu sichinali choyamba chomwe chili cha uzimu, koma chomwe chili cha chibadwidwe; ndipo pambuyo pake cha uzimu.
  5622. 1Co 15:47 Munthu woyambayo [ali] wa dziko lapansi, wanthaka: munthu wachiwiri [ndiye] Ambuye wochokera kumwamba.
  5623. 1Co 15:48 Monga [ali] wanthakayo, chomwechonso [iwo] anthaka; ndi monga [ali] wakumwamba, chomwechonso [ali] iwo akumwamba.
  5624. 1Co 15:49 Ndipo monga tatenga fanizo la wanthakayo, tidzatenganso fanizo la wakumwambayo.
  5625. 1Co 15:50 Tsopano ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulandira ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilandira chisavundi.
  5626. 1Co 15:51 Tawonani ndikuwonetsani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika.
  5627. 1Co 15:52 M’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa kulira kwa lipenga lotsiriza: pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzawukitsidwa wosavunda, ndipo ife tidzasandulika.
  5628. 1Co 15:53 Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi cha imfa ichi [chiyenera] kuvala chosafa.
  5629. 1Co 15:54 Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chosavunda, ndi chakufa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo chidzafika pokwaniritsidwa chonenedwa chimene chinalembedwa, Imfayo yamezedwa m’chipambano.
  5630. 1Co 15:55 O! imfa, ululu wako [uli] kuti? O! manda, chipambano chako [chili] kuti?
  5631. 1Co 15:56 Ululu wa imfa [ndiwo] uchimo; koma mphamvu ya uchimo [ndicho] chilamulo.
  5632. 1Co 15:57 Koma mayamiko [akhale] kwa Mulungu, amene atipatsa ife chipambano mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  5633. 1Co 15:58 Choncho, abale anga wokondedwa, khalani wokhazikika, wosasunthika, akuchuluka nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye, powona kuti inu mudziwa kuti nchito zanu siziri chabe mwa Ambuye.
  5634. 1Co 16:1 Tsopano zokhudza chopereka cha kwa woyera mtima, monga ndidalangiza mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.
  5635. 1Co 16:2 Pa [tsiku] loyamba la sabata aliyense wa inu asunge yekha, monga momwe Mulungu wampindulitsira, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.
  5636. 1Co 16:3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzavomereza ndi [makalata] anu, amenewo ndidzawatuma abwere nayo mphatso yanu yaufulu ku Yerusalemu.
  5637. 1Co 16:4 Ndipo ngati kuyenera kuti ine ndipitenso, adzapita nane.
  5638. 1Co 16:5 Tsopano ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya: pakuti ndimapyola Makedoniya.
  5639. 1Co 16:6 Ndipo kapena ndidzakhalitsa, inde, ndi kugonera nyengo yozizira ndi inu, kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.
  5640. 1Co 16:7 Pakuti sindifuna kukuwonani tsopano popitirira; pakuti nditsimikiza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.
  5641. 1Co 16:8 Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.
  5642. 1Co 16:9 Pakuti khomo lalikulu ndi lochititsa latsegulidwa kwa ine, ndipo [pali] woletsana nafe ambiri.
  5643. 1Co 16:10 Tsopano ngati adze Timoteyo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha: pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso inenso [ndigwira].
  5644. 1Co 16:11 Choncho musalole munthu aliyense ampeputse iye: koma mumperekeze mumtendere kuti adze kwa ine: pakuti ndimuyembekezera ine pamodzi ndi abale.
  5645. 1Co 16:12 Koma zokhudza mbale [wathu] Apolos, ndidakhumba kwambiri ine kuti iye adze kwa inu pamodzi ndi abale: koma sichidali chifuniro chake kuti adze pa nthawi iyi; koma adzafika pamene awona nthawi yomuyenera.
  5646. 1Co 16:13 Khalani tcheru inu, chirimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni ngati amuna, khalani wochilimika.
  5647. 1Co 16:14 Zinthu zanu zonse zichitike ndi chikondi.
  5648. 1Co 16:15 Ndikupemphani inu, abale (mudziwa banja la Stefana, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi [kuti] adadziyika wokha ku utumiki wotumikira woyera mtima.)
  5649. 1Co 16:16 Kuti inunso mugonjere nokha kwa wotere, ndi kwa wina aliyense wakuthandiza pamodzi ndi ife, ndi kugwira ntchito.
  5650. 1Co 16:17 Ndikondwera ndi kudza kwawo kwa Stefanas, ndi Fortunatas, ndi Akayikas: pakuti chimene chidasowa ku mbali yanu adachikwaniritsa iwo.
  5651. 1Co 16:18 Pakuti adatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu, choncho muwazindikire iwo amene ali wotere.
  5652. 1Co 16:19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni inu. Akupatsani moni mwa Ambuye, Akwila ndi Prisilla, pamodzi ndi mpingo umene uli m’nyumba yawo.
  5653. 1Co 16:20 Abale onse akupatsani moni. Patsanani moni ndi kupsopsonana kwachiyero.
  5654. 1Co 16:21 Moni wa [ine] Paulo ndi dzanja langa.
  5655. 1Co 16:22 Ngati munthu wina sakonda Ambuye Yesu Khristu, akhale pansi pa temberero. Alinkudza Ambuye wathu ndi chiweruzo.
  5656. 1Co 16:23 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu.
  5657. 1Co 16:24 Chikondi change [chikhale] ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Amen.
  5658. 2Co 1:1 Paulo mtumwi wa Yesu Khristu, mwa chifuniro cha Mulungu ndi Timoteyo mbale [wathu], kwa mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi woyera mtima onse amene ali mu Akaya yense:
  5659. 2Co 1:2 Chisomo [chikhale] kwa inu ndi mtendere kuchokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi [kuchokera kwa] Ambuye Yesu Khristu.
  5660. 2Co 1:3 ¶Wodalitsika [ndi] Mulungu amene ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse:
  5661. 2Co 1:4 Wotitonthoza ife mu msawutso yathu yonse, kuti tikathe ife kutonthoza iwo wokhala mu msawutso uliwonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
  5662. 2Co 1:5 Pakuti monga masawutso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.
  5663. 2Co 1:6 Ndipo ngati tisawutsidwa, [ziri] chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masawutso womwewo amene ifenso timva kuti ngati titonthozedwa, [ziri] chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu.
  5664. 2Co 1:7 Ndipo chiyemebekezo chathu cha kwa inu [chili] chokhazikika; podziwa kuti monga muli woyanjana ndi masawutsowo, [kotero] kudzateronso chitonthozo.
  5665. 2Co 1:8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale wosadziwa za chisawutso chathu tidakomana nacho mu Asiya, kuti tidathodwa kwakukulu koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu.
  5666. 2Co 1:9 Koma tokha tidakhala nacho chisawutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisadalire mwa ife tokha, koma mwa Mulungu amene awukitsa akufa.
  5667. 2Co 1:10 Amene adatilanditsa mu imfa yayikulu yotere, ndipo amalanditsa; amene mwa iye tidalira kuti iye adzatilanditsabe [ife];
  5668. 2Co 1:11 Inunso pothandiza pamodzi ndi pemphero la kwa ife; kuti pa mphatso [yakupatsidwa] pa ife yodzera kwa anthu ambiri, mayamiko aperekedwe ndi anthu ambiri m’malo mwa ife.
  5669. 2Co 1:12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko, umboni wa chikumbumtima chathu, kuti mcholinga chimodzi ndi kuwona mtima kwa umulungu, si mu nzeru ya thupi, koma m’chisomo cha Mulungu, ife tidakhala chikhalidwe chathu chodzisunga m’dziko lapansi, koma mochuluka koposa kwa inu.
  5670. 2Co 1:13 Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga kapenanso muzimvetsa; ndipo ndiyembekeza kuti mudzazindikira kufikira chimaliziro;
  5671. 2Co 1:14 Monganso mudatizindikira ife mwa gawo, kuti ife ndife chimwemwe chanu, monga momwe inunso [muli] chimwemwe chathu, m’tsiku la Ambuye Yesu.
  5672. 2Co 1:15 Ndipo m’kulimbika uku ndidafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nalo phindu lachiwiri;
  5673. 2Co 1:16 Ndipo popyola inu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kuchokera ku Makedoniya ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.
  5674. 2Co 1:17 Choncho pamene ine pakufuna chimenechi, kodi ndidachitapo mwakusinthasintha? Kapena zinthu zimene nditsimikiza mtima, kodi nditsimikiza monga mwa thupi, kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi ayi, ayi?
  5675. 2Co 1:18 Koma [monga] Mulungu [ali] wowona, mawu athu kwa inu sakhala eya ndi ayi.
  5676. 2Co 1:19 Pakuti Mwana wamwamuna wa Mulungu, Yesu Khristu, amene adalalikidwa mwa inu ndi ife, ine ndi Silivana ndi Timoteyo, sadakhala eya ndi ayi, koma adakhala mwa iye eya.
  5677. 2Co 1:20 Pakuti malonjezano onse a Mulungu mwa iye [ali] eya; ndi mwa iye Amen, ku ulemerero wa Mulungu mwa ife.
  5678. 2Co 1:21 Koma iye wakutikhazikitsa pamodzi ndi inu mwa Khristu, ndipo watidzoza ife, [ndiye] Mulungu.
  5679. 2Co 1:22 Amenenso adatisindikizaife chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.
  5680. 2Co 1:23 Komanso ine ndiyitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti ndidalekerera inu kuti ndisafikenso ku Korinto.
  5681. 2Co 1:24 Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala wothandizana nacho cimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muyimadi.
  5682. 2Co 2:1 Koma ndidatsimikiza mtima ine ndekha kuti ndisadzadzenso kwa inu ndi chisoni.
  5683. 2Co 2:2 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndani iye amene tsono adzandikondweretsa ine, koma yemweyo amene ndamumvetsa chisoni ine?
  5684. 2Co 2:3 Ndipo ndidalemba ichi chomwechi kwa inu, kuti kapena, pomwe ndidza, ndingakhale nacho chisoni kuchokera kwa iwo amene ndiyenera kukondweretsedwa ine; pokhala ndi chikhulupiriro mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa [ndi chimwemwe] cha inu nonse.
  5685. 2Co 2:4 Pakuti kuchokera m’chisawutso chambiri ndi kuwawa mtima ndidalembera inu ndi misozi yambiri; sikuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi chimene ndiri nacho choposaposatu kwa inu.
  5686. 2Co 2:5 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sadachititsa chisoni ine, koma mwa gawo: kuti ndisasenzetse inu nonse.
  5687. 2Co 2:6 Chilango [ichi] ndi chokwanira kwa munthu wotere. Chimene chidachitidwa kwa ambiri.
  5688. 2Co 2:7 Kotero kwina kuti inu [muthe] kumkhululukira [iye] ndi kumtonthoza [iye], kuti kapena mwina mwake wotereyo angamezedwe ndi chisoni chochuluka.
  5689. 2Co 2:8 Mwa ichi ndikupemphani inu kuti mutsimkize chikondi [chanu] kwa ameneyo[.]
  5690. 2Co 2:9 Ndi cholinga ichinso ndinalemba, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli womvera m’zinthu zonse.
  5691. 2Co 2:10 Kwa iye amene mumkhululukira kanthu, ine [ndimkhululukiranso], pakuti ngati ndinakhululukira chilichonse, kwa iye amene ndinakhululukira [icho], chifukwa cha inu [ndinamkhululukira ine icho] mu umunthu wa Khristu;
  5692. 2Co 2:11 Kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala wosadziwa machenjerero ake.
  5693. 2Co 2:12 Kuwonjezera apa, pamene ndinadza ku Trowa [kudzalalikira] uthenga wabwino wa Khristu, ndipo lidatsegulidwa kwa ine khomo ndi Ambuye.
  5694. 2Co 2:13 Ndidalibe mpumulo mu mzimu wanga; popeza ine sindidampeza Tito mbale wanga; koma polawirana nawo ndidachoka kumeneko kunka ku Makedoniya.
  5695. 2Co 2:14 ¶Koma mayamiko [akhale] kwa Mulungu, amene nthawi zonse atipambanitsa mwa Khristu, namveketsa fungo lachidziwitso chake mwa ife pamalo alionse.
  5696. 2Co 2:15 Pakuti ife ndife kwa Mulungu fungo lokoma la Khristu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuwonongeka;
  5697. 2Co 2:16 Kwa wina [tiri ife] fungo la imfa ku imfa; ndi kwa wina fungo lamoyo ku moyo. Ndipo ndani [ali] wokwanira wa zinthu izi?
  5698. 2Co 2:17 Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akupotoza mawu a Mulungu: koma monga mwa chowona mtima, koma monga mwa Mulungu, pamaso pa Mulungu tiyankhula mwa Khristu.
  5699. 2Co 3:1 Kodi tirikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodiife tisowa, monga ena a [enawo], makalata wovomereza kwa inu? Kapena [makalata] wovomereza kuchokera kwa inu?
  5700. 2Co 3:2 Inu ndinu kalata yathuyolembedwa mu mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi anthu onse:
  5701. 2Co 3:3 [Popeza kuti inu muli] wolengezedwa mowonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, yotumikiridwa ndi ife, yosalembedwa ndi inki, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome a mwala koma m’magome a mitima yathupi.
  5702. 2Co 3:4 Ndipo kudalira kotere tiri nako mwa Khristu kwa Mulungu.
  5703. 2Co 3:5 Sikuti tiri wokwanira pa ife tokha kuganiza kanthu kalikonse monga mochokera mwa ife tokha; koma kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu.
  5704. 2Co 3:6 Amenenso watipanga ife atumiki othekera a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu pakuti chilembo chipha, koma mzimu apatsa moyo.
  5705. 2Co 3:7 Koma ngati utumiki wa imfa, wolembedwa [ndi] wolochedwa m’miyala, udali wa ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sadathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene udalikuchotsedwa:
  5706. 2Co 3:8 Nanga sudzakhala bwanji utumiki wa mzimu ndi ulemerero woposa?
  5707. 2Co 3:9 Pakuti ngati utumiki wa chitsutso [uli] ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira mu ulemerero kwambiri.
  5708. 2Co 3:10 Pakuti chimene chidachitidwa ulemerero sichidachitidwa cha ulemerero moteromo, chifukwa cha ulemrero woposawo.
  5709. 2Co 3:11 Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chidali cha ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho [chili] ulemerero.
  5710. 2Co 3:12 Powona kutitsono tiri nacho chiyemebekezo chotero, tiyankhula momveka bwino kwambiri ndi mosavuta kumva;
  5711. 2Co 3:13 Ndipo si monga Mose, [amene] adayika [chinsalu] chophimba pa nkhope yake kuti ana a Israyeli asayang’anitse pa chimaliziro cha chimene chidalikumalizidwa:
  5712. 2Co 3:14 Koma malingaliro awo adachititsidwa khungu; pakuti kufikira tsiku lino [chinsalu] chophimba chomwecho nchosachotsedwa mu kuwerenga kwa pangano lakale; [chinsalu chophimba] chimenechi chithedwa mwa Khristu.
  5713. 2Co 3:15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, [chinsalu] chophimba chili pa mtima pawo.
  5714. 2Co 3:16 Komabe pamene winaadzatembenukira kwa Ambuye, [chinsalu] chophimbacho chichotsedwa.
  5715. 2Co 3:17 Tsopano Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye [pali] ufulu.
  5716. 2Co 3:18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalilore ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera ku ulemerero kunka ku ulemerero, [monga] mwa Mzimu wa Ambuye.
  5717. 2Co 4:1 Choncho popeza tiri nawo utumiki umenewu, monga talandira chifundo, sitifowoka;
  5718. 2Co 4:2 Koma takaniza zobisika za zosakhulupirika, wosayendayenda mwa kuchenjerera kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi mawonekedwe a chowonadi tivomerezetsa tokha ku chikumbumtima cha munthu aliyense pamaso pa Mulungu.
  5719. 2Co 4:3 Koma ngatinso uthenga wabwino wathu uphimbika, uphimbika kwa iwo akutayika;
  5720. 2Co 4:4 Mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano adachititsa khungu maganizo a iwo amene sakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawale kwa iwo.
  5721. 2Co 4:5 Pakuti sitidzilalikiraifetokha, koma Khristu Yesu Ambuye; ndi ife tokha atumiki anu chifukwa cha Yesu.
  5722. 2Co 4:6 Pakuti Mulungu amene adalamulira kuwala kuchokera mu mdima, wawala m’mitima yathu, kuti [apatse] chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope ya Yesu Khristu.
  5723. 2Co 4:7 ¶Koma tiri nacho chuma ichi m’zotengera za dothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.
  5724. 2Co 4:8 [Ife tiri] wosawutsika mbali zonse, koma wosapsinjika; [ife tiri] wosinkhasinkha, koma wosakhala kakasi;
  5725. 2Co 4:9 Wozunzidwa, koma wosasiyidwa; wokhumudwa, koma wosawonongeka;
  5726. 2Co 4:10 Nthawi zonse tiri kusenza m’thupi kufa kwake kwa Ambuye Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi mwathu.
  5727. 2Co 4:11 Pakuti ife amene tiri ndi moyo tirikuperekedwa ku imfa nthawi zonse chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi lomwe lifa.
  5728. 2Co 4:12 Chotero imfa ichita mwaife, koma moyo mwa inu.
  5729. 2Co 4:13 Ife pokhala nawo mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga momwe kudalembedwa, ine ndidakhulupirira, ndipo choncho ine ndidayankhula; ifenso tikhulupirira, ndipo choncho tiyankhula;
  5730. 2Co 4:14 Podziwa kuti iye amene adawukitsa Ambuye Yesu adzawukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatipereka [ife] pamodzi ndi inu.
  5731. 2Co 4:15 Pakuti zinthu zonsezi [ziri] chifukwa cha kwa inu, kuti chisomo chochulukitsa chingathe mwakudzera m’mayamiko a ambiri akuchulukira ku ulemerero wa Mulungu.
  5732. 2Co 4:16 Pa chifukwa ichi sitifowoka; koma ngakhale umunthu wathu wakunja uvunda, komatu [munthu] wa mkati mwathu akonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.
  5733. 2Co 4:17 Pakuti chisawutso chathu chopepuka, chomwe chili cha kanthawi, chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu [ndi] kulemera kosatha kwa ulemerero;
  5734. 2Co 4:18 Pamene sitipenyerera zinthu zomwe ziwoneka, koma zinthu zomwe siziwoneka, pakuti zinthu zomwe ziwoneka [ziri] za nthawi yochepa, koma zinthu zomwe ziri zosawoneka [ziri] zamuyaya.
  5735. 2Co 5:1 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba yathu ya pansi pano ya chihema [ichi] ikadapasulidwa, tiri nacho chimango cha Mulungu, nyumba yosamangidwa ndi manja, yamuyaya m’miyamba.
  5736. 2Co 5:2 Pakuti m’menemo tibuwula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi nyumba yathu yochokera kumwamba.
  5737. 2Co 5:3 Ngati kuli kwakuti povekedwa sitipezedwa amaliseche.
  5738. 2Co 5:4 Pakuti ife amene tiri mu msasa [uwu] tibuwula, pothodwetsedwa; osati chifukwa chakuti tivulidwe, koma kuvekedwa, kuti cha imfacho chimezedwe ndi moyo.
  5739. 2Co 5:5 Ndipo wotikonzera ife chinthu ichi chimene [ndiye] Mulungu, amenenso watipatsa ife chikole cha Mzimu.
  5740. 2Co 5:6 Choncho [tiri] nako [ife] nthawi zonse kulimbika mtima, podziwa kuti, pamene tiri kwathu m’thupi, sitiri kwa Ambuye.
  5741. 2Co 5:7 (Pakuti tiyendayenda monga mwa chikhulupiriro si mwamawonekedwe:)
  5742. 2Co 5:8 Tilimbika mtima, [ndinena], ndipo ndiri wofuna makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala ndi Ambuye.
  5743. 2Co 5:9 Mwa ichi tigwira ntchito, kuti, kapena tiripo kapena kulibe, tikhale olandiridwa ndi iye.
  5744. 2Co 5:10 Pakuti ife tonse tiyenera kuwonekera pa mpando wa kuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zinthu [zochitidwa] m’thupi [lake]; monga mwa zomwe wachita, kapena [zikhala] zabwino kapena zoyipa.
  5745. 2Co 5:11 Choncho podziwa tsono kuwopsa kwa Ambuye, tikakamiza anthu; koma tiwonetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndikhulupirira kuti tiwonetsedwa m’zikumbumtima zanu.
  5746. 2Co 5:12 Pakuti sitidzivomerezanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira m’malo mwa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakuwayankha iwo akudzitamandira m’mawonekedwe wokha, wosati mumtima.
  5747. 2Co 5:13 Pakuti ngati tiri woyaluka, [titero] kwa Mulungu; ngati tiri mu nzeru zathu, titero chifukwa cha kwa inu.
  5748. 2Co 5:14 Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza ife; popeza tiweruza chotero, kuti ngati m’modzi adafera onse, potero onse adafa;
  5749. 2Co 5:15 Ndi [kuti] adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo wokha, koma kwa iye amene adawafera iwo nawuka kwa akufa.
  5750. 2Co 5:16 Mwa ichi ife sitidziwanso munthu monga mwa thupi: eya, ngakhale tamudziwa Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso [iye] chotero [ife].
  5751. 2Co 5:17 Choncho ngati munthu aliyense [ali] mwa Khristu Yesu [ali] cholengedwa chatsopano; zinthu zakale zapita; tawonani, zinthu zonse zakhala zatsopano.
  5752. 2Co 5:18 Ndipo zinthu zonse ziri zakwa Mulungu, amene adatiyanjanitsa ife kwa iye yekha mwa Yesu Khristu, ndipo watipatsa utumiki wa chiyanjanitso.
  5753. 2Co 5:19 Ndiko kunena, kuti Mulungu adali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa iye yekha, wosawerengera zolakwa zawo kwa iwo; ndipo nayikiza kwa ife mawu a chiyanjanitso.
  5754. 2Co 5:20 Potero tsono tiri akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu adakudandawulirani [inu] kudzera mwa ife; tipempha [inu] m’malo mwa Khristu, muyanjanitsidwe ndi Mulungu.
  5755. 2Co 5:21 Pakuti wampanga iye [kukhala] tchimo m’malo mwathu, amene sadadziwa tchimo; kuti ife tikhoze kupangidwa chilungamo cha Mulungu mwa iye.
  5756. 2Co 6:1 Ife pamenepo [monga] antchito [pamodzi ndi iye], tidandawuliranso inu kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe.
  5757. 2Co 6:2 (Pakuti anena, M’nyengo yolandirika ndidamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza; tawonani, tsopano [ndiyo] nthawi yabwino yovomerezeka, tawonani, tsopano [ndilo] tsiku lachipulumutso.)
  5758. 2Co 6:3 Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe:
  5759. 2Co 6:4 Koma mu [zinthu] zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu; m’kupirira kwambiri, m’zisawutso, m’zikakamizo, m’zopsinja,
  5760. 2Co 6:5 M’mikwingwirima, mu kutsekeredwa m’ndende, m’mapokoso, m’zintchito, m’mkuchezera, m’masalo a chakudya;
  5761. 2Co 6:6 Mwa kuyera, mwa chidziwitso, mwa chilekerero, mwa kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, mwa chikondi chosanyenga,
  5762. 2Co 6:7 Mwa mawu a chowonadi, mwa mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo ku dzanja lamanja ndi la kumanzere,
  5763. 2Co 6:8 Mwa ulemu, ndi mopanda ulemu, mwa mbiri yoyipa ndi mbiri yabwino; monga wosocheretsa, koma [ali] wowona;
  5764. 2Co 6:9 Monga wosadziwika, komatu [tiri] odziwika bwino; monga ali kufa, ndipo, tawonani, tiri ndi moyo; monga wolangika, ndipo wosaphedwa;
  5765. 2Co 6:10 Monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga a umphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga wokhala wopanda kanthu [komatu] akukhala nazo zinthu zonse.
  5766. 2Co 6:11 [Inu] Akorinto, m’kamwa mwathu m’motseguka kwa inu, mtima wathu wakulitsidwa.
  5767. 2Co 6:12 Inu sikuti mwapatsidwa malire mwa ife, koma mumangika inu mu chikondi chanu.
  5768. 2Co 6:13 Tsopano chifukwa cha chibwezero mu chomwechi (ndinena ndi inu ana [anga]) mukulitsidwe inunso.
  5769. 2Co 6:14 ¶Musakhale womangidwa m’goli pamodzi ndi wosakhulupirira; pakuti chilungamo chiyanjana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuwunika kuyanjana bwanji ndi mdima?
  5770. 2Co 6:15 Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?
  5771. 2Co 6:16 Kodi kachisi wa Mulungu akhala ndi mgwirizano wanji ndi mafano? Pakuti inu ndinu kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu adanena, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayenda mwa [iwo], ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga.
  5772. 2Co 6:17 Mwa ichi, Tulukani pakati pawo, ndipo mudzipatule, atero Ambuye, ndipo musakhudze [kanthu] kodetsedwa; ndipo ine ndidzalandira inu.
  5773. 2Co 6:18 Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala ana anga amuna ndi akazi, anena Ambuye Wamphamvu yonse.
  5774. 2Co 7:1 Choncho pokhala nawo malonjezano amenewa, wokondedwa kwambiri, tiyeni tidziyeretse tokha kuchoka ku chodetsa chonse cha thupi ndi mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.
  5775. 2Co 7:2 Tilandireni ife; sitidalakwire munthu aliyense, sitidayipsa munthu aliyense, sitidachenjerera munthu aliyense.
  5776. 2Co 7:3 Sindinena [ichi] kuti ndikutsutseni [inu]; pakuti ndanena kale m’mbuyomu, kuti muli mu mitima yathu kufa ndi kukhala ndi moyo limodzi ndi [inu].
  5777. 2Co 7:4 Kulimbika mtima kwanga [ndi] kwakukulu pakulankhula nanu, kudzitamandira kwanga [ndi] kwakukulu chifukwa cha inu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m’chisawutso chathu chonse.
  5778. 2Co 7:5 Pakutinso, pakudza ife m’Makedoniya thupi lathu lidalibe mpumulo, koma tidavutitsidwa ife mbali zonse; kunjako [kunali] zolimbana, mkatimo [munali] mantha.
  5779. 2Co 7:6 Komabe Mulungu, amene atonthoza wokhumudwa, adatitonthoza ife pa kufika kwake kwa Tito.
  5780. 2Co 7:7 Koma sindikufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene adatonthozedwa nacho mwa inu, pamene adatiwuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, malingaliro anu a changu cha kwa ine; kotero kuti ndidakondwera koposa.
  5781. 2Co 7:8 Kuti ngakhale ndidakumvetsani chisoni ndi kalata yija, sindilapa; ndingakhale ndidalapa; pakuti ndidazindikira kuti kalata yomwe yija idakumvetsani inu chisoni, ngakhale [kuti kunali] kwa nthawi yochepa.
  5782. 2Co 7:9 Tsopano ine ndikondwera, si chifukwa chakuti mudangomvetsedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni cha ku kulapa: pakuti mudamvetsedwa chisoni monga mwa machitidwe a umulungu, kuti inu musakhoze kulandira chiwonongeko chilichonse mwa ife.
  5783. 2Co 7:10 Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chimagwira ntchito ya kulapa kotitengera kuchipulumutso chosamvetsanso chisoni, koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.
  5784. 2Co 7:11 Pakuti, tawonani, chinthu ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni monga machitidwe a umulungu, kudera nkhawa kwakukulu kotani chidachita mwa inu, eya, chodziteteza [koma], inde mkwiyo [koma], inde mantha [koma], inde kukhumbitsa [koma], inde change [koma], inde kubwezera choyipa [koma]! Mu [zinthu] zonse mudatsimikizira nokha kuti muli woyera mtima m’menemo.
  5785. 2Co 7:12 Mwa ichi ndingakhale ndidalembera kwa inu, sindidachita chifukwa cha iye amene adachita choyipa, kapena chifukwa cha iye amene adalakwiridwa, koma kuti chisamaliro cha kwa inu pamaso pa Mulungu chiwonetsedwe kwa inu.
  5786. 2Co 7:13 Choncho tidatonthozedwa m’chitonthozo chanu: eya, ndipo tidakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, pakuti mzimu wake udatsitsimutsidwa ndi inu nonse.
  5787. 2Co 7:14 Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindichita manyazi; koma monga tidalankhula zinthu zonse kwa inu m’chowonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene [ndidachita] pamaso pa Tito, kudakhala chowonadi.
  5788. 2Co 7:15 Ndipo chikondi chake cha mkati chichulukira koposa kwa inu, pamene akumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti ndi mantha ndi kunthunthumira mudamlandira iye.
  5789. 2Co 7:16 Choncho ine ndikondwera kuti ndilimbika mtima mwa inu m’zinthu zonse.
  5790. 2Co 8:1 Kupitirira apo, abale, ife tikudziwitsani za chisomo cha Mulungu chopatsidwa pa mipingo yaku Makedoniya;
  5791. 2Co 8:2 Kuti momwe m’chiyesero chachikulu cha chisawutso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chawo ndi kusawuka kwawo kwambiri zidachulukira ku cholemera cha kuwolowa mtima wawo.
  5792. 2Co 8:3 Pakuti monga mwa mphamvu [yawo], ndichitapo umboni, eya, inde koposa mphamvu [yawo] anali [wofuna iwo] mwa iwo wokha.
  5793. 2Co 8:4 Natipempha ife motidandawulira ife tikhumbe kulandira mphatsoyo, ndi [kuti tidzitengere tokha] chiyanjano cha kutumikira kwa woyera mtima.
  5794. 2Co 8:5 Ndipo [izi adachita iwo], si monga tidayembekeza; koma adayamba kudzipereka wokha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.
  5795. 2Co 8:6 Kotero kuti tinadandawulira Tito, kuti monga adayamba kale, chomwechonso atsirize mwa inu chisomo ichinso.
  5796. 2Co 8:7 Choncho, monga muchulukira mu [zinthu] zonse [mu] chikhulupiriro, ndi m’mawu, ndi m’chidziwitso, ndi [mu] khama lonse, ndi [mu] chikondi chanu cha kwa ife, [onetsetsani] kuti muchulukanso m’chisomo ichi.
  5797. 2Co 8:8 Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama kupita chitsogolo kwa ena, ndi kuyesa chowonadi cha chikondi chanunso.
  5798. 2Co 8:9 Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, angakhale adali wachuma, komatu chifukwa cha inu adakhala wosawuka, kuti inu ndi kusawuka kwake mukakhale achuma.
  5799. 2Co 8:10 Ndipo m’menemo ndipereka langizo [langa]; pakuti chimene chipindulira inu, amene mudayamba kale m’mbuyomo, si kuchita kokha, komanso kufuna, chaka chapitachi.
  5800. 2Co 8:11 Choncho tsopano tsirizani kuchitaku [kwa ichi]; kuti monga [kudali] chivomerezo cha kufuna, [koteronso kuti kukhale] kutsiriza kwake kuchokera m’chimene muli nacho.
  5801. 2Co 8:12 Pakuti ngati poyamba pali mtima wofuna pomwepo, [ichi] chilandiridwa monga momwe munthu ali nacho, ndipo osati monga asowa.
  5802. 2Co 8:13 Pakuti si [ndikutero] kuti anthu ena akamasuke, ndi kuti inu mulemetsedwe:
  5803. 2Co 8:14 Koma mwa kulingana kuchuluka kwanu, [kuti] tsopano nthawi ya makono kuchuluka kwanu [kukwanire] ku kusowa kwawo, kutinso kuchuluka kwawonso [kukwanire] ku kusowa kwanu: kuti pakhale chilingano;
  5804. 2Co 8:15 Monga kwalembedwa, Iye amene [adasonkhetsa] chambiri sichidamtsalira; ndi iye amene [adasokhetsa] pang’ono sichidamsowa.
  5805. 2Co 8:16 Koma mayamiko [akhale] kwa Mulungu, amene adapatsa khama lomweri la kwa inu mu mtima wa Tito.
  5806. 2Co 8:17 Pakutitu adalandira kudandawulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, adatulukira kunka kwa inu mwini wake.
  5807. 2Co 8:18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene matamando ake [ali] mu uthenga wabwino mu mipingo yonse;
  5808. 2Co 8:19 Ndipo si [ichi] chokha, komanso amene adasankhika ndi mipingo, apite limodzi ndi ife m’chisomo ichi, chimene chitumikiridwa ndi ife ku ulemerero wa Ambuye yemweyo, ndi chiwonetsero chakufuna kwa mtima wanu;
  5809. 2Co 8:20 Kupewa ichi, kuti munthu asatizenge mlandu ife mu kuchulukira uku kumene kutumikiridwa ndi ife.
  5810. 2Co 8:21 Pakupereka zinthu zowona, si pa maso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.
  5811. 2Co 8:22 Ndipo tawatumiza iwo ndi mbale wathu, amene tamtsimikizira kawiri kawiri ali wakhama m’zinthu zambiri; koma tsopano wa khama loposatu, pa kulimbika mtima kwakukulu kumene ndiri [nako] kwa inu.
  5812. 2Co 8:23 Kaya [ena afunsa] za Tito, [ali] woyanjana nane ndi wothandizana nane pamodzi zokhudza inu: kapena abale athu [afunsidwa, iwo ali] atumiki a mipingo, [ndi] ulemerero wa Khristu.
  5813. 2Co 8:24 Mwa ichi inu muwawonetsere iwo, ndi pamaso pa mipingo; chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu m’malo mwanu.
  5814. 2Co 9:1 Pakuti monga zokhudza utumiki wa kwa woyera mtima, sikufunika kwa ine kulembera inu;
  5815. 2Co 9:2 Pakuti ndidziwa chivomerezo cha malingaliro anu, chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu kwa Amakedoniya, kuti Akaya adakonzeratu chaka chapita ndipo changu chanu chidatakasa wochulukawo.
  5816. 2Co 9:3 Komatu ndatuma abale, kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m’malo mwake; kuti monga ndidanena, mukakhale wokonzekeratu:
  5817. 2Co 9:4 Kuti mwina akandiperekeze iwo a ku Makedoniya, nadzakupezani inu wosakonzeka, ife (kuti tisanene kuti inu) tingachititsidwe manyazi m’kulimbika kudzitamandira kumeneku.
  5818. 2Co 9:5 Choncho ndidaganiza kuti kufunika kupempha, abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lodziwitsidwa kale, kuti lomwero likhale lokonzeka chomwechi, monga ngati m’dalitso, ndipo si monga mwa kukonda chuma.
  5819. 2Co 9:6 Koma nditi ichi, iye wakufesa mowuma manja mowuma manjanso adzatuta; ndipo iye wakufesa mowolowa manja mowolowa manjanso adzatuta.
  5820. 2Co 9:7 Munthu aliyense monga atsimikiza mu mtima mwake, [kotero apereke], si mokakamiza, kapena mwazofunikira: pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
  5821. 2Co 9:8 Ndipo Mulungu [ali] wakutha kuchulukitsa chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse mu [zinthu] zonse, mukachulukire ku ntchito yonse yabwino;
  5822. 2Co 9:9 (Monga kwalembedwa; Iye anabalalitsa mudera lalikulu, adapatsa kwa wosawuka; chilungamo chake chikhala ku nthawi yonse.
  5823. 2Co 9:10 Tsopano iye wopatsa mbewu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya [chanu], ndi kuchulukitsa mbewu yanu yofesedwa, ndi kuchulukitsa zipatso za chilungamo chanu:)
  5824. 2Co 9:11 Polemeretsedwa inu m’zonse ku kuwolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko kwa Mulungu.
  5825. 2Co 9:12 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sikukwaniritsa zosowa za woyera mtima zokha, koma uchulukiranso mwa mayamiko ambiri kwa Mulungu.
  5826. 2Co 9:13 Popeza kuti mwa kuyesa kwa kuwonadi kwa utumiki umene iwo alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku uthenga wabwino wa Khristu, ndi kwa kuwolowa manja kwa chigawano [chanu] kwa iwo, ndi kwa [anthu] onse;
  5827. 2Co 9:14 Ndipo iwo, mwa pemphero lawo la kwa inu, amene akhumbitsa inu chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.
  5828. 2Co 9:15 Mayamiko [akhale] kwa Mulungu chifukwa cha mphatso yake yosatheka kuneneka.
  5829. 2Co 10:1 Tsopano ine ndekha Paulo ndidandawulira inu mwa kufatsa ndi kudekha kwa Khristu, ine amene pamaso panu [ndikhala] wochepa pakati pa inu, koma pokhala ndiri kwina ine ndilimbika mtima kwa inu:
  5830. 2Co 10:2 Koma ine ndipempha [inu], kuti pokhala ndiri pomwepo ndisalimbike mtima ndi kulimbika mtima kumene ndiganiza ndiri nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi.
  5831. 2Co 10:3 Pakuti ngakhale tiyenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi.
  5832. 2Co 10:4 (Pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi; koma zamphamvu kudzera mwa Mulungu za kutsitsira pansi malinga;)
  5833. 2Co 10:5 Ndikugwetsa malingaliro, ndi chinthu chapamwamba chilichonse chimene chidzikweza potsutsa chidziwitso cha Mulungu, ndi kubweretsa ku undende ganizo lonse ku kumvera Khristu;
  5834. 2Co 10:6 Ndikukhala wokonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pomwe kumvera kwanu kwakwaniritsidwa.
  5835. 2Co 10:7 Kodi mupenyera pa zinthu zopenyeka ndi mawonokedwe akunja? Ngati munthu wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, muloleni iye mwa iye yekha aganizirenso ichi, kuti, monga iye [ali] wa Khristu, koteronso [ife] tiri a Khristu.
  5836. 2Co 10:8 Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro wathu, umene adatipatsa Ambuye ife ku kumangirira, ndipo si ku chiwonongeko chanu, sindiyenera kunyazitsidwa:
  5837. 2Co 10:9 Kuti ndisawoneke monga ngati kukuwopsani mwa makalatawo.
  5838. 2Co 10:10 Pakuti makalatatu [ake], atero iwo, [ali] wolemera ndi amphamvu; komam’kupezeka [kwake] kwa kuthupi [ali] wofowoka, ndi mawu [ake] ndi womvetsa chisoni.
  5839. 2Co 10:11 Wotereyo aganize ichi, kuti, monga tiri ife mu mawu mwa makalata pokhala palibe ife, [tidzakhala ife] woterenso m’machitidwe pokhala tiri pomwepo.
  5840. 2Co 10:12 Pakuti sitilimba mtima kudzipanga a chiwerengero chawo, kapena kudzifananiza ife eni ndi ena a iwo amene adzivomereza wokha; koma iwowa, podziyesera wokha mwa iwo wokha, ndi kudzifananiza iwo wokha pakati pa iwo wokha, alibe nzeru.
  5841. 2Co 10:13 Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso [wathu], koma monga mwa muyeso wa chilekezero cha muyeso chimene Mulungu adatigawira, muyeso wakufikira ngakhale kwa inunso.
  5842. 2Co 10:14 Pakuti sitidzitambasula moposa [muyeso wathu], monga ngati sitidafikira kwa inu: pakuti tadza kufikira kwa inunso mu [kulalikira] uthenga wabwino wa Khristu:
  5843. 2Co 10:15 Wosadzitamandira pa zinthu popitirira muyeso wathu, [ndiko kuti] mwa machititso a ena; koma tiri nacho chiyembekezo kuti pamene chakula chikhulupiriro chanu, kuti tidzakhala titakulitsidwa ndi inu monga mwa ulamuliro wathu kwa kuchulukira,
  5844. 2Co 10:16 Kulalikira uthenga wabwino kupyola [m’mayiko] a mtsogolo mwake mwa inu, [ndi] kusadzitamandira mwa ntchito ya wina mwa zinthu zokonzeka kalekwa ife.
  5845. 2Co 10:17 Koma iye wodzitamandira, adzitamandire iye mwa Ambuye.
  5846. 2Co 10:18 Pakuti si iye amene adzitama yekha avomerezetsedwa, koma iye amene Ambuye amuvomerezetsa.
  5847. 2Co 11:1 Mwenzi kwa Mulungu mutandilola pang’ono mu chopusa changacho; koma ndithu mundilole.
  5848. 2Co 11:2 Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya umulungu; pakuti ndidakupalitsani ubwenzi kwa mwamuna m’modzi, kuti ndikapereke [inu ngati] namwali woyera mtima kwa Khristu.
  5849. 2Co 11:3 Koma ndiwopa, kuti mwa njira yina, monga njoka idanyenga Heva kudzera m’kuchenjerera kwake, maganizo anu angayipsidwe kusiyana nako kusavuta mwa Khristu.
  5850. 2Co 11:4 Pakuti ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitidamlalikira, kapena [ngati] mulandira mzimu wina, umene simunalandira, kapena uthenga wabwino wa mtundu wina, umene simudalandira, mungathe kulolerana naye [iye] bwino lomwe.
  5851. 2Co 11:5 Pakuti ndiyesa kuti sindidaperewera pa kena kalikonse pambuyo pa atumwi woposawo.
  5852. 2Co 11:6 Koma ndingakhale [ine ndiri] wopanda ulemu m’malankhulidwe, koma sinditero m’chidziwitso, koma tawonetsedwa kwathunthu pakati panu mu zinthu zonse.
  5853. 2Co 11:7 Kodi ndapalamula mlandu podzichepetsa ndekha kuti inu mukwezedwe, popeza ndidalalikira kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu mwa ufulu?
  5854. 2Co 11:8 Ndidalanda za mipingo yina, ndikulandira [kwa iwo] malipiro, kuti ndikatumikire inu.
  5855. 2Co 11:9 Ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindidalemetse munthu aliyense: pakuti chimene chidandisowa kwa ine abale akuchokera ku Makedoniya adakwaniritsa: ndipo mu [zinthu] zonse ndidayesetsa ndekha kusakhala wolemetsa kwa inu, ndipo [kotero] ndidzadzisunga [ndekha].
  5856. 2Co 11:10 Monga chowonadi cha Khristu chili mwa ine, palibe munthu adzandiletsa ku kudzitamandira uku mu madera a Akaya.
  5857. 2Co 11:11 Mwa ichi? Chifukwa sindikonda inu? Adziwa Mulungu.
  5858. 2Co 11:12 Koma chimene ine ndichita, chimenecho ine ndidzachita, kuti ndikadule chifukwa kuchokera kwa iwo okhumba chifukwa; kuti m’mene iwo adzitamandiramo, angathekupezedwa monga ife tiri.
  5859. 2Co 11:13 Pakuti wotere [ali] atumwi wonyenga, wochita monyenga, wodziwonetsa ngati atumwi a Khristu.
  5860. 2Co 11:14 Ndipo kulibe kudabwa; pakuti satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuwunika.
  5861. 2Co 11:15 Choncho [sikuli] kanthu kakakulu ngatinso atumiki ake adziwonetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.
  5862. 2Co 11:16 Ndinenenso, munthu asandiyese wopanda nzeru; ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang’ono.
  5863. 2Co 11:17 Chimene ine ndiyankhula, sindiyankhula [ichi] monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m’kulimbika uku kwa kudzitamandira.
  5864. 2Co 11:18 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.
  5865. 2Co 11:19 Pakuti mulolana nawo wopanda nzeru mokondwera, powona kuti [inu nokha] muli anzeru.
  5866. 2Co 11:20 Pakuti mulola ngati wina akubweretsani inu ku ukapolo, ngati wina alakwira [inu], ngati wina alanda [zanu], ngati wina adzikweza yekha, ngati wina akupandani pankhope.
  5867. 2Co 11:21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tidali wofowoka. Komabe m’mene wina alimbika mtimanso (ndilankhula mopanda nzeru,) ndilimbika mtima inenso.
  5868. 2Co 11:22 Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali a Israyeli? Inenso. Kodi ali mbewu ya Abrahamu? Inenso.
  5869. 2Co 11:23 Kodi ali atumiki a Khristu? (ndiyankhula monga wopusa), makamaka ine; m’zisawutso mochulukira, m’mikwingwirima mosawerengeka, m’ndende pafupipafupi, mu imfa kawirikawiri.
  5870. 2Co 11:24 Kwa Ayuda ndidalandira kasanu [mikwingwirima] makumi anayi kupatula umodzi.
  5871. 2Co 11:25 Katatu ndidamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndidaponyedwa miyala, katatu ndidatayika posweka chombo, usiku umodzi ndi usana umodzi ndidakhala mu kuya tsiku limodzi;
  5872. 2Co 11:26 [Mu] maulendo kawirikawiri, mowopsa m’madzi, mowopsa mwa olanda, mowopsa modzera kwa anthu a mtundu [wanga], mowopsa mwa achikunja, mowopsa mu mzinda, mowopsa m’chipululu, mowopsa m’nyanja, mowopsa mwa abale wonyenga;
  5873. 2Co 11:27 M’zolemetsa ndi m’zintchito, m’kuchezera kawirikawiri, m’njala ndi m’ludzu, mkusala kudya kawirikawiri, m’kuzizira ndi umaliseche.
  5874. 2Co 11:28 Popanda zinthu zomwe ziri kunja, chimene chimadza kwa ine tsiku ndi tsiku, chilabadiro cha mipingo yonse.
  5875. 2Co 11:29 Afoka ndani, ndipo ine sindiri wofowoka? Akhumudwitsidwa ndani, ndipo ine sindipsa?
  5876. 2Co 11:30 Ngati ndiyenera kudzitamandira ndidzadzitamandira mu zinthu zomwe zikhudzana ndi kufowoka kwanga.
  5877. 2Co 11:31 Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, iye amene ali wodalitsika ku nthawi yonse, adziwa kuti ine sindinama.
  5878. 2Co 11:32 M’Damasiko kazembe pansi pa mfumu Aretas adalindizitsa mzinda wa Adamasiko ndi gulu la asirikali, kukhumba kuti andigwire ine:
  5879. 2Co 11:33 Ndipo kudzera pa zenera mum’tanga adanditsitsa mbali mwakhoma, ndipo ndidapulumuka m’manja mwake.
  5880. 2Co 12:1 Sikuyenera kwa ine popanda kukayika kudzitamandira; ine ndidzadza ku masomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye.
  5881. 2Co 12:2 Ndidziwa munthu mwa Khristu, zaka khumi ndi zinayi zapitazo (kaya m’thupi, sindinganene; kapena kunja kwa thupi sindinganene; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye kumwamba kwachitatu.
  5882. 2Co 12:3 Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (kaya m’thupi, kapena wopanda thupi, sindinganene; adziwa Mulungu;)
  5883. 2Co 12:4 Mwa momwe iye anakwatulidwa kunka ku paradiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kuyankhula.
  5884. 2Co 12:5 Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; komatu chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m’zofoka zanga.
  5885. 2Co 12:6 Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira; sindidzakhala wopanda nzeru, pakuti ndidzanena chowonadi, koma [tsopano] ndileka, kuti wina angandiganizire ine koposa kumene ayenera kundiwonera [momwe ndiriri] ine, kapena [za zomwe] amva za ine.
  5886. 2Co 12:7 Ndipo kuti ndingakwezeke koposa muyeso kudzera mwa kuchuluka kwa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa muyeso.
  5887. 2Co 12:8 Za ichi ndinapempha Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.
  5888. 2Co 12:9 Ndipo ananena kwa ine, chisomo changa chili chokwanira kwa iwe: pakuti mphamvu yanga ikonzedwa ungwiro mu ufowoko. Choncho makamaka ndidzadzitamandira mokondwera m’maufowoko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
  5889. 2Co 12:10 Choncho ndisangalala m’maufowoko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’manzunzo, m’zipsinjo chifukwa cha Khristu, pakuti pamene ndiri ofoka, pamenepo ndiri wamphamvu.
  5890. 2Co 12:11 Ndakhala wopusa mukudzitamandira; inu mwandikakamiza: pakuti muyenera kundivomereza ine; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m’kanthu konse, ndingakhale ndiri chabe.
  5891. 2Co 12:12 Ndithudi zizindikiro za mtumwi zinachitika pakati pa inu m’chipiriro chonse; mu zizindikiro, ndi zozizwa, ndi machitidwe amphamvu.
  5892. 2Co 12:13 Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi mipingo yina; ngati [kupatula] kuti ine ndekha sindidakulemetsani inu? Ndikhululukireni pa cholakwa ichi.
  5893. 2Co 12:14 Tawonani nthawi yachitatu iyi ndakonzeka ine kudza kwa inu; ndipo sindidzakulemetsani inu: pakuti sindifuna za inu koma inu: pakuti ana sayenera kuwunjikira makolo, koma makolo kuwunjikira ana.
  5894. 2Co 12:15 Ndipo ndidzapereka mokondwera ndi kuperekedwa chifukwa cha inu; ngakhale ndikonda inu kwambiri komaine ndidzakondedwa pang’ono.
  5895. 2Co 12:16 Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu: komabe, pokhala wochenjera, ine ndinakugwirani ndi chinyengo.
  5896. 2Co 12:17 Kodi ndinapindula kwa inu mwa wina aliyense amene ndidamtuma kwa inu?
  5897. 2Co 12:18 Ndidakhumba Tito, ndipo [pamodzi] ndi iye ndidatumiza mbale. Kodi Tito adapindula kwa inu? Kodi sitidayendayenda mu mzimu yemweyo? Kodi [sitidayenda] m’mapazi womwewo?
  5898. 2Co 12:19 Ndiponso mumayesa tsopano lino kuti tiri kuwiringula tokha kwa inu? Tiyankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu: koma wokondedwa kwambiri [ife tichita] zinthu zonse ndi cholinga cha kumangiririka kwanu.
  5899. 2Co 12:20 Pakuti ndiwopa, kuti kaya, pomwe ndadza ine, sindidzakupezani inu wotere wonga ndifuna, ndi [kuti] ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wosanga momwe mufunira, kuti kapena [pangakhale] mitsutso, kaduka, mkwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso:
  5900. 2Co 12:21 [Ndi] kuti kapena, pamene ndadzanso ine, Mulungu wanga angandichepetse pakati pa inu, ndi [kuti] ndingadzalirire ambiriwo amene adachimwa kale, ndipo sanalape pa chodetsa ndi chiwerewere ndi kukhumba zonyansa zimene iwo achita.
  5901. 2Co 13:1 Nthawi [yachitatu iyi] ndiri nkudza kwa inu. Mkamwa mwa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.
  5902. 2Co 13:2 Ndidakuwuzani m’mbuyomu, ndipo ndidaneneratu, monga ngati ndidali pomwepo, kachiwiri; pokhala ine palibe ndalembera kwa iwo adachimwa m’mbuyomo, ndi kwa ena onse, kuti, ngati ndidzanso, sindidzawaleka;
  5903. 2Co 13:3 Popeza mufuna chitsimikizo cha Khristu kuyankhula mwa ine; amene kwa inusi ali wofoka, koma ali wamphamvu mwa inu.
  5904. 2Co 13:4 Pakuti ngakhale iye adapachikidwa kudzera mu ufowoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tiri wofoka mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi iye mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.
  5905. 2Co 13:5 Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro; dzitsimikizireni nokha. Kodi kapena simuzindikira za inu nokha, momwe Yesu Khristu ali mwa inu, pokhapokha muli wosavomerezeka?
  5906. 2Co 13:6 Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitiri wosavomerezeka.
  5907. 2Co 13:7 Tsopano ndipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koyipa; sikuti ife tikawonekere wovomerezeka, koma kuti inu muchite chomwe chili cholemekezeka, tingakhale ife tikhala monga wosavomerezeka.
  5908. 2Co 13:8 Pakuti sitikhoza kuchita kanthu potsutsa chowonadi, koma kwa chowonadi.
  5909. 2Co 13:9 Pakuti tikondwera, pamene tifoka, ndi inu muli amphamvu: ndi ichinso tikhumba, [ndicho] ungwiro wanu.
  5910. 2Co 13:10 Choncho ndalemba zinthu izi pokhala palibe, kuti pokhala ndiri pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye wandipatsa ine wakumangirira, ndipo osati wakuwononga.
  5911. 2Co 13:11 Chomalizira, abale, tsalani bwino. Khalani angwiro, mukhale wotonthozedwa bwino; khalani amtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
  5912. 2Co 13:12 Patsanani moni wina ndi mnzake ndi chipsopsono chopatulika.
  5913. 2Co 13:13 Woyera mtima onse akupatsani moni inu.
  5914. 2Co 13:14 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera, [zikhale] ndi inu nonse. Amen.
  5915. Gal 1:1 Paulo, mtumwi, (wosati [wochokera] mwa anthu, kapena [kudzera] mwa munthu, koma [kudzera] mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene adamuwukitsa iye kwa akufa;)
  5916. Gal 1:2 Ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kupita ku mipingo ya ku Galatiya:
  5917. Gal 1:3 Chisomo [chikhale] kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi, wochokera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  5918. Gal 1:4 Amene adadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife ku dziko loyipa la nyengo yino, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu:
  5919. Gal 1:5 Kwa iye [ukhale] ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.
  5920. Gal 1:6 ¶Ine ndizizwa kuti inu mwachotsedwa msanga motere kwa iye amene adakuyitanani kulowa m’chisomo cha Khristu kutsata uthenga wabwino wina:
  5921. Gal 1:7 Umene si uli wina; koma pali ena amene akuvutani inu, ndi kufuna kukhotetsa uthenga wabwino wa Khristu.
  5922. Gal 1:8 Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera kumwamba, alalikira uthenga wabwino wina uliwonse kwa inu wosiyana ndi umene ife tidalalikira kwa inu, iye akhale wotembereredwa.
  5923. Gal 1:9 Monga tidanena kale, kotero ine tsopano ndinenanso, ngati munthu wina akulalikirani uthenga wabwino wosati umene mudawulandira, akhale wotembereredwa.
  5924. Gal 1:10 ¶Pakuti kodi tsopano ndikakamiza anthu, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Pakuti ngati ine ndidakondweretsa anthu, sindikadakhala mtumiki wa Khristu.
  5925. Gal 1:11 Pakuti ndikutsimikizani inu, abale, kuti uthenga wabwino womwe udalalikidwa ndi ine si uli monga mwa anthu.
  5926. Gal 1:12 Pakutitu sindidawulandira kwa munthu, kapena sindidaphunzitsidwa ndi [iwo], koma mwa vumbulutso la Yesu Khristu.
  5927. Gal 1:13 Pakuti inu mwamva za makhalidwe anga mu nthawi yakale mu chipembedzo cha Chiyuda, mwa momwe mopyola muyeso ndidazunza mpingo wa Mulungu, ndi kuwusakaza iwo:
  5928. Gal 1:14 Ndi kupindulira m’chipembedzo cha Chiyuda koposa ambiri ofanana nane m’dziko langa, kukhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
  5929. Gal 1:15 Koma pamene chidakondweretsa Mulungu, amene adandipatula kuchokera m’mimba mwa mayi wanga, nandiyitana [ine] mwa chisomo chake,
  5930. Gal 1:16 Kuti avumbulutse Mwana wake wamwamuna mwa ine, kuti ndikamlalikire iye mwa achikunja; posakhalitsa sindidakambirana ndi thupi ndi mwazi:
  5931. Gal 1:17 Kapena sindidakwera kumka ku Yerusalemu kwa iwo amene adakhala atumwi ndisadakhale ine, komatu ndidapita ku Arabiya, ndipo ndidabwereranso ku Damasikasi.
  5932. Gal 1:18 Kenaka patapita zaka zitatu, ndidakwera kumka ku Yerusalemu kukawona Petro, ndipo ndidakhala ndi iye masiku khumi ndi asanu.
  5933. Gal 1:19 Koma wina wa atumwi sindidawona aliyense, kupatula Yakobo mbale wa Ambuye.
  5934. Gal 1:20 Tsopano zinthu zomwe ndilembera kwa inu, tawonani, pamaso pa Mulungu ine sindinama ayi.
  5935. Gal 1:21 Pambuyo pake ine ndinadza ku zigawo za Siriya ndi Silisiya;
  5936. Gal 1:22 Ndipo ndidali wosadziwika mwa nkhope kwa mipingo ya ku Yudeya yomwe inali mwa Khristu:
  5937. Gal 1:23 Koma adali atangomva kokha, Kuti iye amene adatizunza mu nthawi yapita tsopano alalikira chikhulupiriro chimene adachiwononga kale.
  5938. Gal 1:24 Ndipo iwo adalemekeza Mulungu mwa ine.
  5939. Gal 2:1 Kenaka patapita zaka khumi ndi zinayi ndidakweranso kumka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabas, ndidamtenganso Tito pamodzi ndi [ine].
  5940. Gal 2:2 Ndipo ndidakwera kumka mwa vumbulutso; ndipo ndidalankhula kwa iwo kuti uthenga wabwino umene ndiwulalikira pakati pa Amitundu, koma m’seri kwa iwo wotchuka, kuti kapena mwa njira zina ndingathamange, kapena ndidathamanga, mwachabe.
  5941. Gal 2:3 Koma ngakhale Tito, amene adali ndi ine, pokhala Mhelene, sadakakamizidwa kuti adulidwe:
  5942. Gal 2:4 Ndipo ichi chifukwa chakuti abale wonyenga mosawazindikira adabweretsedwa, amene adalowa modzibisa mwa m’seri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nawo mwa Khristu Yesu, kuti athe kutibweretsa ife m’goli:
  5943. Gal 2:5 Kwa iwo sitidawapatsa mpata wowagonjera, ayi, ngakhale kwa ora limodzi; kuti chowonadi cha uthenga wabwino chithe kupitirira ndi inu.
  5944. Gal 2:6 Koma kwa awa amene adayesedwa ali kanthu, (kaya adali wotani, sizipanga kanthu kwa ine: Mulungu salandira umunthu wa munthu) pakuti iwo ankawoneka [kukhala womvekawo] mu kukambirana sadawonjezera kanthu kwa ine:
  5945. Gal 2:7 Koma mosiyananiratu, pomwe adawona kuti uthenga wabwino wa kusadulidwa udayikizidwa kwa ine, monga uthenga wabwino wa kumdulidwe kwa Petro;
  5946. Gal 2:8 (Pakuti iye wakuchita mopambana mwa Petro ku utumwi wa a ku mdulidwe, yemweyo adali wamphamvu mwa ine kuloza kwa Amitundu:)
  5947. Gal 2:9 Ndipo pamene Yakobo ndi Kefa, ndi Yohane amene adayesedwa mizati, pakuzindikira chisomocho chidapatsidwa kwa ine, adapatsa ine ndi Barnabas manja a dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife [tipite] kwa achikunja, ndi iwo kwa amdulidwe.
  5948. Gal 2:10 Pokhapo kuti adafuna kuti tikumbukire aumphawi; chomwecho chimene ine ndidali patsogolo kuchichita.
  5949. Gal 2:11 Koma pamene Petro anadza ku Antiyoki, ndidatsutsana naye pamaso; chifukwa chakuti adayenera kupezeka wolakwa.
  5950. Gal 2:12 Pakuti asadafike ena wochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi Amitundu; koma atadza iwo, iye anachoka ndi kudzipatula yekha, powopa iwo amene adali a ku mdulidwe.
  5951. Gal 2:13 Ndipo Ayuda wotsala adadzipatula chimodzimodzi pamodzi naye; kotero kuti Barnabasnso adatengedwa ndi chinyengo chawo.
  5952. Gal 2:14 Koma pamene ndidawona kuti sadayende mowongoka monga mwa chowonadi cha uthenga wabwino, ndidati kwa Petro pamaso pa [iwo] onse, Ngati iwe wokhala Myuda, utsata makhalidwe a Amitundu, ndipo si monga achita Ayuda, bwanji mukakamiza Amitundu akhale monga achita a Ayuda?
  5953. Gal 2:15 ¶Ife [amene tiri] Ayuda pa chibadwidwe, ndipo osati wochimwa a kwa Amitundu.
  5954. Gal 2:16 Podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama mwa ntchito za lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ngakhale ife takhulupirira Yesu Khristu, kuti tikathe kulungamitsidwa mwa chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si mwa ntchito za lamulo; pakuti mwa ntchito za lamulo palibe thupi lidzalungamitsidwa.
  5955. Gal 2:17 Koma ngati, pomwe tifunafuna kulungamitsidwa mwa Khristu, ife eni tokha tipezedwa wochimwa, [kodi] choncho Khristu ali mtumiki wa uchimo? Mulungu akuletsa.
  5956. Gal 2:18 Pakuti ngati ndimanganso zinthu zimene ndaziwononga ine, ndidzipanga ndekha wolakwa.
  5957. Gal 2:19 Pakuti ine kudzera mwa lamulo ndafa ku lamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.
  5958. Gal 2:20 Ndapachikidwa ndi Khristu: komabe ndiri wamoyo; koma osati ine, koma Khristu akhala mwa ine: ndipo moyo umene ndiri nawo tsopano m’thupi ndikhala nawo mwa chikhulupiriro cha Mwana wamwamuna wa Mulungu, amene adandikonda ine, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
  5959. Gal 2:21 Sindichikhalitsa chisomo cha Mulungu chopanda pake; pakuti ngati chilungamo [chidza] mwa lamulo, pamenepo Khristu adafa chabe.
  5960. Gal 3:1 Agalatiya wopusa, wakulodzani inu ndani, kuti inu musamvere chowonadi, amene pamaso panu Yesu Khristu wawonetsedwa mowonekera bwino lomwe, wopachikidwa pakati panu?
  5961. Gal 3:2 Ichi chokha ndikadafuna kuphunzira kwa inu, Mudalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?
  5962. Gal 3:3 Kodi muli wopusa motere? Mutayamba mu Mzimu, kodi tsopano mwakhalitsidwa angwiro mwa thupi?
  5963. Gal 3:4 Kodi mwamva zinthu zowawa zambiri kwachabe? Ngati [ziri choncho] kuti kwachabe.
  5964. Gal 3:5 Choncho iye amene atumikira kwa inu mwa Mzimu, nachita zozizwitsa pakati pa inu, [achita ichi iye] ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?
  5965. Gal 3:6 Monga choteronso Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo.
  5966. Gal 3:7 Choncho inu dziwani kuti iwo amene ali a chikhulupiriro, omwewo ndi ana a Abrahamu.
  5967. Gal 3:8 Ndipo malembo pakuwoneratu kuti Mulungu adzalungamitsa achikunja kudzera mu chikhulupiriro, wolalikidwa kale uthenga wabwino kwa Abrahamu, [kunena], Mwa iwe mitundu yonse idzadalitsidwa.
  5968. Gal 3:9 Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.
  5969. Gal 3:10 Pakuti onse ochuluka amene ali a ntchito za lamulo ali pansi pa temberero: pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa [ali yense] amene sakhalabe m’zinthu zonse zomwe zalembedwa m’buku la chilamulo kuzichita izi.
  5970. Gal 3:11 Koma kuti palibe munthu alungamitsidwa ndi lamulo pamaso pa Mulungu, chodziwikiratu [ichi]: pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.
  5971. Gal 3:12 Ndipo chilamulo si chili cha chikhulupiriro: koma, Munthu amene achita zimenezo adzakhala ndi moyo mu izo.
  5972. Gal 3:13 Khristu watiwombola ife ku temberero la chilamulo, atapangidwa kukhala temberero m’malo mwathu: pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa [ali yense] amene apachikidwa pa mtengo.
  5973. Gal 3:14 Kuti dalitso la Abrahamu lithe kudza kwa Amitundu kudzera mwa Yesu Khristu; kuti tikathe kulandira lonjezano la Mzimu kudzera mwa chikhulupiriro.
  5974. Gal 3:15 ¶Abale, ndinena monga m’manenedwe a anthu; Ngakhale [litakhala] pangano la munthu, komatu [ngati litakhala kuti] latsimikizika, palibe munthu alithetsa, kapena kuwonjezerapo.
  5975. Gal 3:16 Tsopano kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake malonjezanowo adapangidwa. Sadanena, Ndipo kwa mbewu, ngati kunena zambiri; koma ngati imodzi, Ndipo kwa mbewu yako, amene ali Khristu.
  5976. Gal 3:17 Ndipo ichi ndinena, [kuti] pangano, limene lidatsimikizika kale la Mulungu mwa Khristu, lamulolo limene lidadza pambuyo zitapita zaka mazana anayi ndi mphambu makumi atatu siringathe kufafaniza, kuti lipange lonjezolo likhale lopanda ntchito.
  5977. Gal 3:18 Pakuti ngati cholowa [chili] chochokera ku lamulo, [si chilinso] cha lonjezano: koma Mulungu adalipereka kwa Abrahamu mwa lonjezano.
  5978. Gal 3:19 Mwa ichi tsono [ntchito] ya chilamulo n’chiyani? Chidawonjezedwa chifukwa cha zolakwa, kufikira mbewu ikadza kwa iye amene lonjezano lidapangidwa; [ndipo] lidakhazikidwa ndi angelo m’dzanja la mkhalapakati.
  5979. Gal 3:20 Tsopano mkhalapakati si [mkhalapakati] wa m’modzi, koma Mulungu ali m’modzi.
  5980. Gal 3:21 Chilamulo tsono [chili] chotsutsana nawo malonjezano a Mulungu? Mulungu akuletsa: pakuti ngati pakadakhala kuti chidapatsidwa chilamulo chimene chikadakhoza kupatsa moyo, ndithudi chilungamo chikadakhoza kukhala mwa lamulo.
  5981. Gal 3:22 Komatu lembo lamalizitsa zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa iwo akukhulupirira.
  5982. Gal 3:23 Koma chisanadze chikhulupiriro, ife tidasungidwa pansi pa lamulo, wotsekedwa ku chikhulupriro chimene pambuyo pake chidzavumbulutsidwa.
  5983. Gal 3:24 Mwa ichi chilamulo chidakhala namkungwi wathu [kuti atibweretse ife] kwa Khristu, kuti tikathe kulungamitsidwa ndi chikhulupiriro.
  5984. Gal 3:25 Koma pakuti chikhulupiriro chadza, sitirinso pansi pa namkungwi.
  5985. Gal 3:26 Pakuti muli inu nonse ana a Mulungu mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
  5986. Gal 3:27 Pakuti monga ambiri mwa inu mwabatizidwa mwa Khristu mwavala Khristu.
  5987. Gal 3:28 Palibe Myuda kapena Mhelene, palibe kapolo kapena mfulu, palibe mwamuna kapena mkazi: pakuti muli nonse m’modzi mwa Khristu Yesu.
  5988. Gal 3:29 Ndipo ngati [muli a] Khristu, potero muli mbewu ya Abrahamu, ndi wolandira cholowa monga mwa lonjezo.
  5989. Gal 4:1 Tsopano ndinena, [Kuti] wolandira cholowa, nthawi yonse imene ali mwana, sasiyana konse ndi wantchito, ngakhale iye ali mbuye wa zonse;
  5990. Gal 4:2 Koma akhala pansi pa oyang’anira ndi olamulira, kufikira nthawi yokhazikika ndi atate.
  5991. Gal 4:3 Koteronso ife, pamene tidali ana, tidali mu ukapolo pansi pa miyambo ya dziko lapansi:
  5992. Gal 4:4 Koma pomwe nthawi idakwaniritsidwa, Mulungu adatuma Mwana wake wamwamuna wopangidwa mwa mkazi, wopangidwa pansi pa lamulo,
  5993. Gal 4:5 Kukawombola iwo amene anali pansi pa lamulo, kuti ife tithe kulandiridwa monga ana amuna.
  5994. Gal 4:6 Ndipo popeza muli ana amuna, Mulungu watumiza Mzimu wa Mwana wake wamwamuna alowe m’mitima yanu, kufuwula, Abba, Atate.
  5995. Gal 4:7 Mwa ichi iwe si ulinso wantchito, koma mwana wamwamuna; ndipo ngati ndi mwana wamwamuna, pamenepo wolandira cholowa cha Mulungu kudzera mwa Khristu.
  5996. Gal 4:8 Komatu pamenepo, pamene inu simunadziwa Mulungu, mudachita utumiki kwa iyo yosakhala milungu mwa chibadwidwe;
  5997. Gal 4:9 Koma tsopano, pambuyo pakuti mwadziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofowoka ndi yopanda phindu, imene mukhumba kubwerezanso kukhala mu ukapolo?
  5998. Gal 4:10 Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nthawi, ndi zaka.
  5999. Gal 4:11 Ndiri ndi mantha ndi inu, kuti kapena ndidagwira pa inu ntchito pachabe.
  6000. Gal 4:12 Abale, ndikudandawulirani inu, khalani monga momwe [ndiri] ine; pakuti inenso [ndiri] monga inu: simudandivulaze ine konse ayi.
  6001. Gal 4:13 Inu mudziwa kuti mwa kufowoka kwa thupi, ndidalalikira uthenga wabwino kwa inu poyamba.
  6002. Gal 4:14 Ndipo yesero langa lomwe linali m’thupi langa inu simudalipeputsa, kapena kulikana, koma mudandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga [ngati] Khristu mwini.
  6003. Gal 4:15 Kuli kuti tsono kudalitsika komwe inu munakulankhula? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, ngati [kukadakhala kuti] nkotheka, mukadakolowola maso a inu eni, ndi kuwapereka iwo kwa ine.
  6004. Gal 4:16 Choncho kodi ine ndasanduka mdani wanu, chifukwa ndikuwuzani chowona?
  6005. Gal 4:17 Iwo achita changu kukhumba inu, [koma] si kokoma ayi; inde, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukathe kuwakhudza iwowa.
  6006. Gal 4:18 Koma [kuli] kwabwino kufunafuna mwachangu nthawi zonse mu [chinthu] chabwino, osati pokhapokha pomwe ndikhala nanu pamodzi ine.
  6007. Gal 4:19 Tiana tanga, amene chifukwa cha inu ndiri kumvanso zowawa za kubala inu kufikira Khristu awumbike mwa inu.
  6008. Gal 4:20 Ndikhumba nditakhala pamodzi nanu tsopano lino, ndi kusintha mawu anga; chifukwa ndiri mchikayiko pa inu.
  6009. Gal 4:21 ¶Ndiwuzeni, inu amene mukhumba kukhala pansi pa lamulo, kodi simumamva chilamulo?
  6010. Gal 4:22 Pakuti kwalembedwa, kuti Abrahamu adali nawo ana amuna awiri, m’modziyo wobadwa mwa mdzakazi, winayo wobadwa mwa mfulu.
  6011. Gal 4:23 Komatu iye [amene] anali wa mdzakazi anabadwa motsata thupi; koma iye wa mfuluyo [anali] mwa lonjezano.
  6012. Gal 4:24 Zinthu izi ndizo chophiphiritsa: pakuti awa ndi mapangano awiriwo; limodzilo kuchokera ku phiri la Sinayi, lakubalira ana ku ukapolo, amene ndi Hagara.
  6013. Gal 4:25 Pakuti Hagara ndiye phiri la Sinayi mu Arabiya, ndipo afanana ndi Yerusalemu wa lero; ndipo ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake.
  6014. Gal 4:26 Koma Yerusalemu amene ali m’mwamba ali waufulu, amene ali mayi wa ife tonse.
  6015. Gal 4:27 Pakuti kwalembedwa, Kondwera, [iwe] chumba amene subala ayi; bowoleza nufuwule, iwe amene sumva ululu wa kubala: pakuti [mkazi] wosiyidwa ali ndi ana wochuluka kwambiri oposa ana a iye ali naye mwamuna.
  6016. Gal 4:28 Tsopano ife, abale, monga Isake anali, tiri ana a lonjezano.
  6017. Gal 4:29 Komatu monga pa nthawi imeneyo iye wobadwa motsata thupi adazunza [iye] wobadwa motsata Mzimu, momwemonso [ziri] choncho tsopano.
  6018. Gal 4:30 Koma lembo linena chiyani? Tulutsa mdzakazi ndi mwana wake wamwamuna: pakuti mwana wamwamuna wa mdzakazi sadzalandira cholowa pamodzi ndi mwana wamwamuna wa mfulu.
  6019. Gal 4:31 Potero tsono, abale, si tiri ana a mdzakazi, komatu a mfuluyo.
  6020. Gal 5:1 Choncho chilimikani mu ufulu umene Khristu watipanga ife mfulu, ndipo musakhale wokodwanso ndi goli la ukapolo.
  6021. Gal 5:2 Tawonani, ine Paulo ndinena kwa inu, kuti ngati mudulidwa, Khristu sadzakupindulirani inu kanthu.
  6022. Gal 5:3 Pakuti ndichitanso umboni kwa munthu aliyense amene ali wodulidwa, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.
  6023. Gal 5:4 Khristu wakhala wosachita kanthu kwa inu, wina aliyense wa inu amene mulungamitsidwa ndi lamulo; mwagwa kuchoka ku chisomo.
  6024. Gal 5:5 Pakuti ife kudzera mwa Mzimu, tidikira ndi chiyembekezo cha chilungamo cha mwa chikhulupiriro.
  6025. Gal 5:6 Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe ulibe mphamvu, kapena kusadulidwa; koma chikhulupiriro chakugwira ntchito mwa chikondi.
  6026. Gal 5:7 Inu mudathamanga bwino; ndani adakuletsani inu kuti inu musamvere chowonadicho?
  6027. Gal 5:8 Kukopa uku [sikudza] kuchokera kwa iye amene adakuyitanani.
  6028. Gal 5:9 Chofufumitsa mkate chochepa chifufumitsa mtanda wonse.
  6029. Gal 5:10 Ine ndiri ndi chikhulupiriro mwa inu kudzera mwa Ambuye, kuti simudzakhala nawo mtima wina: koma iye wakuvuta inu adzasenza chiweruzo chake, aliyense yemwe angakhale.
  6030. Gal 5:11 Ndipo ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, chifukwa chiyani ndizunzidwanso? Pamenepo chokhumudwitsa cha mtanda chidatha.
  6031. Gal 5:12 Ndikadafuna iwo ngakhale akadachotsedwa iwo amene avuta inu.
  6032. Gal 5:13 Pakuti, abale, mwayitanidwa inu kukhala mfulu; chokhacho [musachite] nawo ufulu wanu chothandizira ku [za] thupi, koma mwa chikondi tumikiranani wina ndi mzake.
  6033. Gal 5:14 Pakuti chilamulo chonse chikwaniritsidwa m’mawu amodzi, [monga] mu awa: Iwe Udzakonda woyandikana naye monga iwe mwini.
  6034. Gal 5:15 Koma ngati mulumana ndi kudyana wina ndi mzake, samalani mungamezane wina ndi mzake.
  6035. Gal 5:16 ¶Ichi ine ndinena tsono, Yendani mu Mzimu, ndipo simudzakwaniritsa chilakolako cha thupi.
  6036. Gal 5:17 Pakuti thupi lilakalaka kutsutsana nawo Mzimu, ndi Mzimu kutsutsana nalo thupi: pakuti izi sizilingana china kwa chinzake: kuti inu musathe kuchita zinthu zimene muzifuna.
  6037. Gal 5:18 Koma ngati inu mukhala wotsogoleredwa mwa Mzimuyo, si muli inu pansi pa lamulo.
  6038. Gal 5:19 Tsopano ntchito za thupi zawonekera, zomwe ndi [izi]; Chigololo, chiwerewere, chodetsa, kukhumba zonyansa.
  6039. Gal 5:20 Kupembedza mafano, ufiti, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,
  6040. Gal 5:21 Njiru, kupha, kuledzera, mchezo ndi zina zotere: za zimene ine ndikuwuziranitu inu, monga ndidakuwuzaninso [inu] nthawi yapita, kuti iwo akuchita zinthu zotere sadzalandira ufumu wa Mulungu.
  6041. Gal 5:22 Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kupirira, kudekha, kukoma mtima, chikhulupiriro.
  6042. Gal 5:23 Chifatso, chiletso; palibe lamulo lotsutsa zimenezo.
  6043. Gal 5:24 Ndipo iwo amene ali a Khristu apachika [pa mtanda] thupi pamodzi ndi zokhumba ndi zilakolako.
  6044. Gal 5:25 Ngati tiri ndi moyo mu Mzimu, tiyeni ife tiyende mu Mzimunso.
  6045. Gal 5:26 Tisakhale ife wokhumba ulemerero wachabe, kuyambana wina ndi mzake, akuchitirana njiru wina ndi mzake.
  6046. Gal 6:1 Abale, ngati munthu agwidwa nako kulakwa, inu amene muli a uzimu, mubwezeretse woteroyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, kuti mwina ungayesedwe nawenso.
  6047. Gal 6:2 Nyamuliranani inu zothodwetsa za wina ndi mzake, ndipo kotero mukwaniritse chilamulo cha Khristu.
  6048. Gal 6:3 Pakuti ngati wina adziyesa yekha ali kanthu, pamene ali chabe, iye adzinyenga yekha.
  6049. Gal 6:4 Koma munthu aliyense atsimikizire ntchito yake ya iye mwini, ndipo pamenepo ndi pomwe iye adzakhala nako kukondwera yekha mwa iye yekha, ndipo osati mwa wina.
  6050. Gal 6:5 Pakuti munthu aliyense adzasenza katundu wake wa iye mwini.
  6051. Gal 6:6 Iye amene aphunzitsidwa mawu ayenera agawire iye amene aphunzitsa mu zithu zonse zabwino.
  6052. Gal 6:7 Musanyengedwe; Mulungu sanamizidwa; pakuti chimene munthu achifesa chimenecho iye adzatuta.
  6053. Gal 6:8 Pakuti wakufesa ku thupi lake adzatuta kuchokera mthupi chivundi, koma iye wakufesa ku Mzimu, adzatuta kuchokera mu Mzimu moyo wosatha.
  6054. Gal 6:9 Ndipo tiyeni ife tisaleme pakuchita zabwino: pakuti mu nyengo yoyenerera tidzatuta ngati ife tikapanda kufowoka.
  6055. Gal 6:10 Monga potero pomwe ife tiri nawo mpata, tiyeni tichitire zabwino anthu onse, makamaka iwo amene ali a pa nyumba ya chikhulupiriro.
  6056. Gal 6:11 Mukuwona kukula kwa malemba amene ine ndalembera kwa inu ndi dzanja langa la ine mwini.
  6057. Gal 6:12 ¶Monga ambiri amene akhumba kupanga chiwonetsero chokoma mu thupi, iwo akukangamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti akuwopa kuti mwina angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu.
  6058. Gal 6:13 Pakuti ngakhale iwo womwe wodulidwa sasunga lamulo; koma akhumba kuti inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m’thupi lanu.
  6059. Gal 6:14 Koma Mulungu akuletsa kuti ine ndisadzitamandire, kupatula mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa iye dziko lapansi lapachikidwira kwa ine, ndi ine ku dziko lapansi.
  6060. Gal 6:15 Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe ulibe kanthu, kapena kusadulidwa kulibe kanthunso, koma cholengedwa chatsopano.
  6061. Gal 6:16 Ndipo iwo ambiri amene ayenda monga mwa lamulo ili, mtendere [ukhale] pa iwo, ndi chifundo, ndi pa Israyeli wa Mulungu.
  6062. Gal 6:17 Kuyambira tsopano munthu asandivute ine: pakuti ndiri nazo ine m’thupi mwanga zipsera za Ambuye Yesu.
  6063. Gal 6:18 Abale, mtendere wa Ambuye wathu Yesu Khristu [ukhale] ndi mzimu wanu. Amen.
  6064. Eph 1:1 Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, kwa woyera mtima amene ali ku Efeso, ndi kwa iwo wokhulupirika mwa Khristu Yesu:
  6065. Eph 1:2 Chisomo [chikhale] kwa inu, ndi mtendere, kuchokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi [kuchokera] kwa Ambuye Yesu Khristu.
  6066. Eph 1:3 ¶Wolemekezeka [akhale] Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene watidalitsa ife ndi madalitso wonse a uzimu [m’malo] a kumwamba mwa Khristu:
  6067. Eph 1:4 Monga iye watisankha ife mwa iye asadakhale maziko a dziko lapansi, kuti ife tikhale woyera ndi wopanda chirema pamaso pa iye m’chikondi:
  6068. Eph 1:5 Atatikonzeratu ife tilandiridwe kukakhala ana kudzera mwa Yesu Khristu kwa iye, monga mwa kukoma kwa chifuniro chake,
  6069. Eph 1:6 Ku matamando a ulemerero wa chisomo chake, m’mene iye watipanga ife kulandiridwa mwa wokondedwayo.
  6070. Eph 1:7 Mwa iye tiri ndi mawomboledwe kudzera m’mwazi wake, chikhululukiro cha machimo, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.
  6071. Eph 1:8 M’mene iye wachulukitsira kwa ife mu nzeru zonse, ndi machitidwe osamalitsa;
  6072. Eph 1:9 Atatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga mwa kumkomera kwake kumene watsimikiza mwa iye yekha:
  6073. Eph 1:10 Kuti mu makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo kuti akathe kusonkhanitsa pamodzi mu m’modzi zinthu zonse mwa Khristu, zonse zimene ziri kumwamba, ndi zomwe ziri pansi; [inde ngakhale] mwa iye:
  6074. Eph 1:11 Mwa iyenso talandira cholowa, pokhala wokonzeketsedweratu monga mwa cholinga cha iye amene achita zinthu zonse motsata uphungu wa chifuniro cha iye mwini:
  6075. Eph 1:12 Kuti ife tikakhale kwa matamando a ulemerero wake, amene tidayamba kukhulupirira mwa Khristu.
  6076. Eph 1:13 Mwa iye amene inunso, [mudakhulupirira], mutamva mawu a chowonadi, uthenga wabwino wa chipulumutso chanu: amene mwa iye mutakhulupirira, mudasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,
  6077. Eph 1:14 Chimene chili choyikidwa choyamba cha cholowa chathu, kufikira akawomboledwe ogulidwa akeake, ku matamando a ulemerero wake.
  6078. Eph 1:15 Mwa ichi inenso, m’mene ndidamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu, ndi chikondi kwa oyera mtima onse,
  6079. Eph 1:16 Sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukutchulani inu m’mapemphero anga;
  6080. Eph 1:17 Kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, athe kupatsa kwa inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso mu chidziwitso cha iye:
  6081. Eph 1:18 Maso a kuzindikira kwanu okhala owalitsika, kuti mukazindikire inu chiyembekezo cha mayitanidwe ake, nchiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa woyera mtima,
  6082. Eph 1:19 Ndi chiyani [ichi] ukulu woposa wa mphamvu yake kwa ife amene tikhulupirira, monga mwa magwiridwe ntchito a mphamvu yake yamphamvu,
  6083. Eph 1:20 Imene iye adachita mwa Khristu, pamene adamuwukitsa iye kwa akufa, namkhazikitsa [iye] pa dzanja lake lamanja [m’malo] a kumwamba,
  6084. Eph 1:21 Patali pamwamba pa a ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lirilonse limene litchedwa, osati m’dziko lapansi lino lokha, komanso mwa ilo limene liyenera kudza:
  6085. Eph 1:22 Ndipo adayika [zinthu] zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa iye [kuti akhale] mutu wa [zinthu] zonse ku mpingo,
  6086. Eph 1:23 Umene liri thupi lake, chidzalo cha iye amene adzaza zonse mu zonse.
  6087. Eph 2:1 Ndipo inu [wakupatsani moyo] iye, amene mudali akufa mu zolakwa ndi machimo;
  6088. Eph 2:2 Mu zimene nthawi yakale mudayendamo, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi ili, monga mwa kalonga wa mphamvu za m’lengalenga, mzimu umene tsopano uchita mwa ana akusamvera:
  6089. Eph 2:3 Amene pakati pawo ife tonse chidakhala chikhalidwe chathu mu nthawi yakale mzilakolako za thupi lathu, kukwaniritsa zokhumba za thupi, ndi za maganizo; ndipo tidali mwa chibadwidwe ana a mkwiyo, monganso enawo.
  6090. Eph 2:4 Koma Mulungu amene ali wolemera mu chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene ife adatikonda nacho,
  6091. Eph 2:5 Ngakhale pomwe ife tidali akufa m’machimo, watipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (mwa chisomo inu muli wopulumutsidwa;)
  6092. Eph 2:6 Ndipo watiwukitsa [ife] pamodzi, natikhazikitsa [ife] pamodzi [m’malo] a kumwamba mwa Khristu Yesu:
  6093. Eph 2:7 Kuti m’nyengo ziri nkudza akathe kuwonetsera chuma choposa cha chisomo chake mu kukoma mtima [kwake] kwa ife kudzera mwa Khristu Yesu.
  6094. Eph 2:8 Pakuti munapulumutsidwa ndi chisomo kudzera m’chikhulupiriro; ndipo ichi chosachokera kwa inu eni: [chili] mphatso ya Mulungu:
  6095. Eph 2:9 Osati cha ntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
  6096. Eph 2:10 Pakuti ife ndife chipango chake, wolengedwa mwa Khristu Yesu kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu adazikhazikitsiratu kale kuti ife tiyende mu izo.
  6097. Eph 2:11 ¶Mwa ichi kumbukirani, kuti kale inu [pokhala] Amitundu m’thupi, amene mutchedwa Wosadulidwa ndi chimene chitchedwa Mdulidwe mu thupi wopangidwa ndi manja;
  6098. Eph 2:12 Kuti pa nthawi imeneyo inu mudali wopanda Khristu, wokhala alendo ku ulamuliro ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo ku mapangano a lonjezano, wokhala wopanda chiyembekezo, ndi wopanda Mulungu m’dziko lapansi:
  6099. Eph 2:13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene nthawi ina [kale] mudali kutali mwasendezedwa pafupi ndi mwazi wa Khristu.
  6100. Eph 2:14 Pakuti iye ali mtendere wathu, amene wapanga onse awiri kukhala m’modzi, nagwetsa pansi khoma la pakatilo logawa [pakati pa ife];
  6101. Eph 2:15 Atathetsa udani m’thupi lake, [ngakhale] chilamulo chomwe [chidali ndi] malangizo; kuti awapange mwa iye yekha awiriwa munthu m’modzi watsopano, [potero] kuchita mtendere;
  6102. Eph 2:16 Ndi kuti akathe kuyanjanitsa awiriwa ndi Mulungu mthupi limodzi ndi mtandawo, atapha udaniwo pamenepo:
  6103. Eph 2:17 Ndipo adadza nalalikira mtendere kwa inu amene mudali kutali, ndi kwa iwo amene adali pafupi.
  6104. Eph 2:18 Pakuti kudzera mwa iye ife tonse awiri tiri nawo malowedwe mwa Mzimu m’modzi kwa Atate.
  6105. Eph 2:19 Choncho tsopano si mulinso alendo ndi wongobwera, komatu muli mbadwa pamodzi ndi woyera mtima, ndi a banja la Mulungu;
  6106. Eph 2:20 Ndipo mwamangidwa pa maziko a atumwi ndi aneneri, Yesu Khristu mwini wokhala [mwala] wa pangodya;
  6107. Eph 2:21 Amene mwa iye mamangidwe onse wolumikizika bwino pamodzi, akula kuti akhale kachisi woyera mwa Ambuye:
  6108. Eph 2:22 Amene mwa iye inunso muli womangidwa pamodzi kukhala mokhalamo mwa Mulungu kudzera mwa Mzimu.
  6109. Eph 3:1 Chifukwa cha ichi ine Paulo, wandende wa Yesu Khristu wa inu Amitundu,
  6110. Eph 3:2 Ngati mudamva za kuperekedwa kwa chisomo cha Mulungu chimene chidapatsidwa ine cha kwa inu:
  6111. Eph 3:3 Momwe mwakuti umo mwa vumbulutso adandizindikiritsira ine chinsinsicho; (monga ndidalemba kale mu mawu ochepa,
  6112. Eph 3:4 Mwa chimene, pamene inu muwerenga, mukhoza kuzindikira chidziwitso changa mu chinsinsi cha Khristu.)
  6113. Eph 3:5 Chimene mu nyengo zina sichidazindikiritsidwa kwa ana amuna a anthu, monga chili tsopano chovumbulutsidwa kwa atumwi ndi ananeri ake woyera mwa Mzimu;
  6114. Eph 3:6 Kuti Amitundu akhale wolandira nawo cholowa pamodzi, ndi a thupi limodzi, ndi wolandira malonjezano ake mwa Khristu ndi uthenga wabwino:
  6115. Eph 3:7 Umene mwa iwo ndidapangidwa mtumiki, monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu chopatsidwa kwa ine mwa machitidwe opambana a mphamvu yake.
  6116. Eph 3:8 Kwa ine, amene ndiri wochepa kuposa wochepetsa wa woyera mtima onse, chisomo ichi chapatsidwa, kuti ndilalikire pakati pa a Amitundu chuma chosafufuzika cha Khristu;
  6117. Eph 3:9 Ndi kuwapanga [anthu] onse awone chimene [chili] chiyanjano cha chinsinsicho, chimene kuyambira kuyamba kwa dziko chabisidwa mwa Mulungu, amene adalenga zinthu zonse mwa Yesu Khristu:
  6118. Eph 3:10 Ku cholinga chakuti tsopano ku maukulu ndi maulamuliro a [m’malo] a kumwamba akathe kuzindikiritsidwa mwa mpingo nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,
  6119. Eph 3:11 Monga mwa cholinga cha muyaya chimene adachilinga mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:
  6120. Eph 3:12 Amene mwa iye tiri ndi kulimbika mtima ndi malowedwe ndi chitsimikizo mwa chikhulupiriro cha iye.
  6121. Eph 3:13 ¶Mwa ichi ndikhumba kuti inu musafowoke pa zisawutso zanga chifukwa cha inu, zimene ndi ulemerero wanu.
  6122. Eph 3:14 Chifukwa cha ichi ndipinda mawondo anga kwa Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,
  6123. Eph 3:15 Amene kuchokera kwa iye banja lonse la kumwamba ndi la padziko lapansi litchulidwa,
  6124. Eph 3:16 Kuti akupatseni inu, monga mwa chuma cha ulemerero wake, kuti mukhale wolimbikitsidwa ndi mphamvu mwa Mzimu wake mwa munthu wam’kati;
  6125. Eph 3:17 Kuti Khristu athe kukhala chikhalire m’mitima yanu mwa chikhulupiriro; kuti inu, pokhala wozika mizu ndi wokhazikika m’chikondi,
  6126. Eph 3:18 Muthe kuzindikira pamodzi ndi woyera mtima onse, chomwe [chili] kupingasa, ndi utali, ndi kuzama, ndi kukwera;
  6127. Eph 3:19 Ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chomwe chiposa chidziwitso, kuti mukathe kudzazidwa ndi chidzalo chonse cha Mulungu.
  6128. Eph 3:20 Tsopano kwa iye amene ali ndi kuthekera kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha kapena kuziganiza, monga mwa mphamvu imene ichita mwa ife,
  6129. Eph 3:21 Kwa iye [kukhale] ulemerero mu mpingo mwa Khristu Yesu kufikira nyengo zonse, kumuyaya. Amen.
  6130. Eph 4:1 Ine choncho, wandende mwa Ambuye ndikudandawulirani inu muyende koyenera mayitanidwe amene inu mudayitanidwa nawo,
  6131. Eph 4:2 Ndi kudzichepetsa konse ndi chifatso, ndi chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mzake mu chikondi;
  6132. Eph 4:3 Ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mu chimangiriro cha mtendere.
  6133. Eph 4:4 [Pali] thupi limodzi ndi Mzimu m’modzi, monganso momwe mwayitanidwa m’chiyembekezo chimodzi cha mayitanidwe anu;
  6134. Eph 4:5 Ambuye m’modzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,
  6135. Eph 4:6 Mulungu m’modzi ndi Atate wa wonse, amene [ali] pamwamba pa wonse, ndi kudzera mwa wonse, ndi mwa inu nonse.
  6136. Eph 4:7 Koma kwa yense wa ife chapatsidwa chisomo monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu.
  6137. Eph 4:8 Mwa ichi anena, Pamene adakwera m’mwamba, adatsogolera ndende undende, naninkha mphatso kwa anthu.
  6138. Eph 4:9 (Tsopano ichi chakuti adakwera, nchiyani ichi koma kuti iye adatsikiranso poyamba ku madera a kunsi kwa dziko?
  6139. Eph 4:10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso adakwera m’mwamba popitiriratu miyamba yonse, kuti akathe kudzaza zinthu zonse.)
  6140. Eph 4:11 Ndipo iye adapatsa ena, atumwi; ndi ena, aneneri; ndi ena, alaliki; ndi ena, abusa ndi aphunzitsi;
  6141. Eph 4:12 Kuti akakonzekeretse woyera mtima, ku kugwira ntchito ya utumiki, kuti amangirire thupi la Khristu:
  6142. Eph 4:13 Kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wamwamuna wa Mulungu, ku munthu wangwiro, ku muyeso wamsinkhu wa chidzalo cha Khristu:
  6143. Eph 4:14 Kuti ife [kuchokera apo] tisakhalenso makanda, wokankhidwa uku ndi uko, ndi kutengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso, ndi chinyengo cha anthu, [ndipo] mwakuchenjera, m’menemo alindira kuti anyenge;
  6144. Eph 4:15 Koma pakuyankhula chowonadi m’chikondi; tithe kukula kufikira iye m’zinthu zonse, amene ali mutu [ndiye] Khristu:
  6145. Eph 4:16 Amene kuchokera mwa iye thupi lonse lolumikizidwa ndi kugwirizana pamodzi ndipo moyandikana mwa chimene mfundo yonse ipereka, monga mwa kuchititsa mwa muyeso wake chiwalo chonse, achita machulukidwe a thupi kufikira ku chimangiriro cha ilo mwini mwa chikondi.
  6146. Eph 4:17 Choncho ine ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti inu kuyambira apo musayendanso monganso Amitundu ena ayendera, mu uchitsiru wa [m’malingaliro] mwawo,
  6147. Eph 4:18 Wodetsedwa m’nzeru zawo, kuchititsidwa kukhala alendo kuchoka ku moyo wa Mulungu chifukwa cha kusazindikira kuli mwa iwo, chifukwa cha khungu la mitima yawo:
  6148. Eph 4:19 Amenenso popeza adadutsa pakumvaimva kanthu konse adadzipereka wokha ku kukhumba zonyansa, kuti achite chidetso ndi umbombo,
  6149. Eph 4:20 Koma inu simudaphunzira Khristu chotero;
  6150. Eph 4:21 Ngatitu kuli kwakuti inu mudamva iye, ndi kuti mwaphunzitsidwa ndi iye, monga chowonadi chili mwa Yesu:
  6151. Eph 4:22 Kuti muvule zokhudza makhalidwe anu woyamba a munthu wakale, amene ali wovunda monga mwa zilakolako za chinyengo;
  6152. Eph 4:23 Ndi kukhala wokonzedwanso [mwatsopano] mu mzimu wa malingaliro anu;
  6153. Eph 4:24 Ndi kuti muvale munthu watsopano, amene monga mwa Mulungu adalengedwa m’chilungamo ndi m’chiyero chowonadi.
  6154. Eph 4:25 Mwa ichi, mutataya mabodza, yankhulani munthu aliyense zowona yense ndi woyandikana naye: pakuti tiri ziwalo za wina ndi mzake.
  6155. Eph 4:26 Kwiyani, koma musachimwe: dzuwa lisalowe muli mu m’kwiyo wanu:
  6156. Eph 4:27 Kapena kupatsa malo kwa mdiyerekezi.
  6157. Eph 4:28 Iye amene amaba asabenso: koma makamaka iye agwire ntchito, kugwira ntchito ndi manja [ake] chinthu chimene chili chabwino, kuti akathe kupereka kwa iye amene asowa.
  6158. Eph 4:29 Musalole malankhulidwe wovunda kutuluka m’kamwa mwanu, koma chimene chili chabwino chikagwira ntchito yakumangirira, kuti chikatumikire chisomo kwa akumvetsera.
  6159. Eph 4:30 Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene inu mudasindikizidwa chizindikiro kufikira tsiku la chiwombolo.
  6160. Eph 4:31 Chiwawo chonse, ndi mkwiyo, ndi kupsa mtima, ndi mapokoso a chiwawa, ndi mayankhulidwe oyipa, zichotsedwe kwa inu, pamodzi ndi kufuna kuchitirana choyipa konse:
  6161. Eph 4:32 Ndipo mukhale ochitirana zabwino wina ndi mzake, a mtima wofewa, akukhululukirana wina ndi mzake, monganso Mulungu chifukwa cha Khristu wakukhulukirani inu.
  6162. Eph 5:1 Choncho khalani inu akutsatira a Mulungu, monga ana wokondedwa;
  6163. Eph 5:2 Ndipo yendani m’chikondi, monganso Khristu adatikonda ife, ndipo wadzipereka yekha chifukwa cha ife chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ya fungo lonunkhira bwino.
  6164. Eph 5:3 Koma dama, ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, chisatchulidwe ichi ndi kamodzi komwe pakati pa inu, monga kuyenera woyera mtima;
  6165. Eph 5:4 Kapena chochititsa manyazi, kapena mayankhulo opusa, kapena nthabwala, zimene si ziri zoyenera: koma makamaka kupereka chiyamiko.
  6166. Eph 5:5 Pakuti ichi muchidziwe, kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena munthu wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.
  6167. Eph 5:6 Asakunyengeni inu munthu ndi mawu wopanda pake: pakuti chifukwa cha zinthu izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
  6168. Eph 5:7 Choncho inu musakhale wolandirana nawo.
  6169. Eph 5:8 Pakuti nthawi ina [kale] mudali mdima, koma tsopano [inu muli] kuwunika mwa Ambuye: yendani monga ana a kuwunika:
  6170. Eph 5:9 (Pakuti chipatso cha Mzimu [chili] mu ubwino wonse, ndi chilungamo ndi chowonadi;)
  6171. Eph 5:10 Kutsimikiza chomwe chili cholandirika kwa Ambuye.
  6172. Eph 5:11 Ndipo musakhale ndi chiyanjano ndi ntchito zosabala zipatso za mdima, koma makamaka muzitsutse [izo].
  6173. Eph 5:12 Pakuti ndi za manyazi kungakhale kunena za zinthu izo zomwe zichitidwa ndi iwo m’seri.
  6174. Eph 5:13 Koma zinthu zonse zimene zatsutsika, ziwonetsedwa ndi kuwunika: pakuti chilichonse chimene chiwonetsa ndicho kuwunika.
  6175. Eph 5:14 Mwa ichi anena, Uka iwe amene ugona, ndipo uwuke kwa akufa, ndipo Khristu adzakupatsa iwe kuwunika.
  6176. Eph 5:15 Potero tsono penyani kuti muyende mwanzeru, osati monga opusa, koma monga anzeru,
  6177. Eph 5:16 Kuwombola nthawi, popeza masiku ali woyipa.
  6178. Eph 5:17 Mwa ichi musakhale wopanda nzeru, koma zindikirani chimene chifuniro cha Ambuye [chili].
  6179. Eph 5:18 Ndipo musaledzere ndi vinyo, m’mene muli chikhalidwe cholakwika; komatu mudzazidwe ndi Mzimu;
  6180. Eph 5:19 Ndikuyankhula kwa inu eni m’masalmo ndi nyimbo ndi nyimbo za uzimu, kuyimba ndi kuyimbira mokometsera mumtima mwanu kwa Ambuye;
  6181. Eph 5:20 Ndikupereka mayamiko nthawi zonse chifukwa cha zinthu zonse kwa Mulungu ndi Atate m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;
  6182. Eph 5:21 Kugonjerana inu eni kwa wina ndi mzake mu kuwopa Mulungu.
  6183. Eph 5:22 ¶Akazi, gonjerani kwa amuna anu a inu eni, monganso kwa Ambuye.
  6184. Eph 5:23 Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monganso Khristu ali mutu wa mpingo: ndipo iye ali mpulumutsi wa thupilo.
  6185. Eph 5:24 Choncho monga mpingo uli pansi kwa Khristu, koteronso akazi okwatiwa [akhale] kwa amuna awo mu zinthu zonse.
  6186. Eph 5:25 Amuna, kondani akazi anu, monganso Khristu adakonda mpingo, nadzipereka yekha chifukwa cha iwo;
  6187. Eph 5:26 Kuti akathe kuwupatula, atawupatula ndi kuwusambitsa iwo ndi kuwuyeretsa kwa madzi mwa mawu,
  6188. Eph 5:27 Kuti iye akathe kuwupereka kwa iye yekha mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kena kotere; koma kuti iwo ukhale woyera ndi wopanda chirema.
  6189. Eph 5:28 Kotero ayenera amuna kukonda akazi awo monga ngati matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake, adzikonda yekha.
  6190. Eph 5:29 Pakuti munthu sadayambe wadana nalo thupi la iye mwini; komatu alidyetsa ndi kulisamalira, monganso Ambuye mpingowo:
  6191. Eph 5:30 Pakuti ife tiri ziwalo za thupi lake, za m’nofu wake ndi za mafupa ake.
  6192. Eph 5:31 Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake, ndipo adzalumikizidwa kwa mkazi wake, ndipo iwo awiriwo adzakhala mnofu umodzi.
  6193. Eph 5:32 Ichi ndi chinsinsi chachikulu: koma ine ndinena zokhudza Khristu ndi mpingo.
  6194. Eph 5:33 Komabe wina aliyense wa inu pa yekha kotero akonde mkazi wakewake monga iye yekha; ndipo mkaziyo [awone] kuti akulemekeza mwamuna [wake].
  6195. Eph 6:1 Ana, mverani makolo anu mwa Ambuye: pakuti ichi nchoyenera.
  6196. Eph 6:2 Lemekeza atate wako ndi amayi wako; (lomwe ndi lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano;)
  6197. Eph 6:3 Kuti kuthe kukhala bwino ndi iwe, ndi kuti iwe uthe kukhala kwa nthawi yayitali padziko.
  6198. Eph 6:4 Ndipo, inu atate, musawapute ana anu: komatu muwalere iwo mchisamaliro ndi chilangizo cha Ambuye.
  6199. Eph 6:5 Antchito, khalani womvera kwa iwo amene ali ambuye [anu] monga mwa thupi, ndi kuwopa ndi kunthunthumira, ndi mwa mtima wanu umodzi, monga kwa Khristu;
  6200. Eph 6:6 Si monga mwa kutumikira mwapamaso, monga okondweretsa anthu; komatu monga atchito a Khristu; kuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;
  6201. Eph 6:7 Ndi chifuniro chabwino kuchita utumiki, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi:
  6202. Eph 6:8 Podziwa kuti chinthu chilichonse chabwino munthu aliyense achichita, chomwechi adzalandira kwa Ambuye, angakhale [ali] kapolo kapena mfulu.
  6203. Eph 6:9 Ndipo, inu ambuye, chitani zinthu zomwezi kwa iwo; nimuleke kuwawopsa: podziwa kuti Ambuye wanunso ali kumwamba; palibenso kuchitira anthu tsankhu mwa iye.
  6204. Eph 6:10 ¶Chomaliza, abale anga, khalani wolimba mwa Ambuye, ndi m’mphamvu ya kulimba kwake.
  6205. Eph 6:11 Valani zida zonse za Mulungu; kuti muthe kuchilimika potsutsa machenjerero achinyengo a mdiyerekezi.
  6206. Eph 6:12 Chifukwa kuti sitilimbana potsutsana nalo thupi ndi mwazi, koma potsutsa ma ukulu, potsutsa ma ulamuliro, potsutsa akulamulira a mdima a dziko lapansi lino, potsutsa chauzimu choyipa cha [m’malo] a m’mwamba.
  6207. Eph 6:13 Mwa ichi mudzitengere kwa inu zida zonse za Mulungu, kuti inu mukhoze kuyima chitsutsire mu tsiku loyipa, ndipo mutachita zonse, muchilimike.
  6208. Eph 6:14 Choncho chilimikani, mutadzimangirira m’chiwuno mwanu ndi chowonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;
  6209. Eph 6:15 Ndi mapazi anu [ovekedwa] nsapato ndi makonzekeredwe a uthenga wabwino wa mtendere;
  6210. Eph 6:16 Pamwamba pa zonse, kutenga chishango cha chikhulupiriro, chimene mudzatha kuzima nacho mivi yoyaka moto yonse ya woyipayo.
  6211. Eph 6:17 Ndipo mutenge chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu:
  6212. Eph 6:18 Kupemphera nthawi zonse ndi pemphero lonse ndi kupempha mwa Mzimu, ndi kudikira m’menemo ndi chipiriro chonse ndi kupempherera woyera mtima wonse;
  6213. Eph 6:19 Ndi ine, kuti kulankhula mawu kupatsidwe kwa ine, kuti ndikhoze kutsegula pakamwa panga molimba mtima, kuti ndizindikiritse chinsinsicho cha uthenga wabwino,
  6214. Eph 6:20 Chifukwa cha umene ndiri kazembe mu unyolo: kuti m’menemo ndikayankhule molimba mtima, monga momwe ine ndiyenera kuyankhulira.
  6215. Eph 6:21 Koma kuti inunso mukhoze kudziwa zochitika za m’moyo wanga, [ndi] momwe ndichitira, Tichikasi, mbale wokondedwayo ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye adzakudziwitsani inu zinthu zonse:
  6216. Eph 6:22 Amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha cholinga chomwecho, kuti mukadziwe zochitika za m’miyoyo ya ife, ndi [kuti] akakhoze kutonthoza mitima yanu.
  6217. Eph 6:23 Mtendere [ukhale] kwa abale, ndi chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro, kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.
  6218. Eph 6:24 Chisomo [chikhale] ndi iwo onse amene akonda Ambuye wathu Yesu Khristu mowonadi. Amen.
  6219. Php 1:1 Paulo ndi Timoteyo, akapolo a Yesu Khristu, kwa woyera mtima wonse mwa Khristu Yesu amene ali ku Filipi, pamodzi ndi woyang’anira ndi madikoni:
  6220. Php 1:2 Chisomo [chikhale] kwa inu, ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi [zochokera] kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  6221. Php 1:3 ¶Ndiyamika Mulungu wanga pakukumbukira kulikonse kwa inu,
  6222. Php 1:4 Nthawi zonse m’pemphero langa lirilonse la kwa inu nonse kuchita pempho mokondwera,
  6223. Php 1:5 Chifukwa cha chiyanjano chanu mu uthenga wabwino kuyambira tsiku loyambalo kufikira tsopano lino;
  6224. Php 1:6 Pokhala wotsimikizika mwa chomwe ichi, kuti iye amene wayamba ntchito yabwino mwa inu adzayichita [iyi] kufikira tsiku la Yesu Khristu:
  6225. Php 1:7 Monga momwe kundiyenera ine kuganiza ichi za inu nonse, popeza ndiri ndi inu mu mtima mwanga; kuti m’kumangidwa kwanga ndi m’chodzikanira cha uthenga wabwino ndi matsimikizidwe a uthenga wabwino, inu nonse muli woyanjana nane a chisomo changa.
  6226. Php 1:8 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, momwe ndilakalakira kwakukulu inu nonse m’chikondi cha Khristu Yesu.
  6227. Php 1:9 Ndipo ine ndipemphera ichi, kuti chikondi chanu chisefukire ndi kusefukira m’chidziwitso, ndi [mu] chiweruzo chonse;
  6228. Php 1:10 Kuti mukayese zinthu zomwe ziri zopambana; kuti mukakhale a mtima wowona ndi wopanda cholakwa kufikira tsiku la Khristu;
  6229. Php 1:11 Wodzala nazo zipatso zachilungamo, zimene zidza mwa Yesu Khristu, ku ulemerero ndi matamando a Mulungu.
  6230. Php 1:12 Koma ndikadafuna inu kuti muzindikire, abale, kuti zinthu [zimene zidachitika] kwa ine zachitika makamaka ku kupitiriza kwa uthenga wabwino;
  6231. Php 1:13 Kotero kuti kumangidwa kwanga mwa Khristu kwawonekera m’nyumba ya chifumu, ndi [malo] ena onse;
  6232. Php 1:14 Ndi ambiri mwa abale mwa Ambuye, pokhala ndi chikhulupiro ndi kumangidwa kwanga, ali olimbika mtima koposa kuyankhula mawu a Mulungu wopanda mantha.
  6233. Php 1:15 Ena alalikiradi Khristu chifukwa cha kaduka ndi mikangano; ndi ena chifukwa cha kufuna kwabwino:
  6234. Php 1:16 M’modziyo alalikira Khristu mwa chotetana, kosati kowona, kulingalira kuti awonjezere chisawutso ku kumangidwa kwanga:
  6235. Php 1:17 Koma winayo atero mwa chikondi, podziwa kuti ndayikidwa chifukwa cha chitetezo cha uthenga wabwino.
  6236. Php 1:18 Nchiyani tsono? Chokhacho, mu njira zonse, kaya monamizira, kaya m’chowonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m’menemo ine ndikondwera, inde, ndipo ndidzakondwera.
  6237. Php 1:19 Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzatembenukira ku chipulumutso changa mwa pemphero lanu, ndi mwa kukwaniritsa kwa zosowa kwa Mzimu wa Yesu Khristu.
  6238. Php 1:20 Monga mwakuyembekezera mwakulingaliritsa ndi chiyembekezo [change], kuti pasakhale chinthu chidzandichititsa manyazi, koma [kuti] ndi kulimbika mtima konse, monga mwa nthawi zonse, [koteronso] tsopanonso Khristu adzakuzidwa m’thupi langa, kaya mwa moyo, kapena mwa imfa.
  6239. Php 1:21 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo [ndi] Khristu, ndi kufa [kuli] kupindula.
  6240. Php 1:22 Koma ngati ine ndikhala ndi moyo m’thupi, ichi [ndi] chipatso cha ntchito yanga: komatu chimene ndidzasankha sindichidziwa.
  6241. Php 1:23 Pakuti ndipanidwa nazo ziwiri, pokhala nacho chikhumbo cha kunyamuka, ndi kukakhala ndi Khristu, chomwe chili chabwino koposaposatu:
  6242. Php 1:24 Komabe kukhala m’thupi [ndi] kofunika koposa kwa inu.
  6243. Php 1:25 Ndipo pokhala nako kulimbika mtima kumeneku, ine ndidziwa kuti ndidzakhala ndi kupitirira ndi inu nonse chifukwa cha kupitiriza kwanu ndi chimwemwe cha chikhulupiriro;
  6244. Php 1:26 Kuti kukondwera kwanu kukhoze kuchuluka mwa Yesu Khristu kwa ine mwa kubweranso ine kwa inu.
  6245. Php 1:27 Chokhachi, umbadwa wanu ukhale monga kuyenera uthenga wabwino wa Khristu: kuti ngati ndidza ndi kuwona inu, kapena kulibe, ndikhoze kumva zochitika kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi moyo umodzi kugwira pamodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha uthenga wabwino;
  6246. Php 1:28 M’kanthu konse, wosawopsezedwa ndi adani anu: chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chiwonongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho chimene chili cha kwa Mulungu;
  6247. Php 1:29 Pakuti kwa inu kwapatsidwa m’malo mwa Khristu, si kukhulupirira iye kokha, komanso kumva zowawa chifukwa cha iye;
  6248. Php 1:30 Kukhala nacho chilimbano chomwechi mudachiwona mwa ine, ndipo tsopano mukumva [chikhala] mwa ine.
  6249. Php 2:1 Ngati tsono [muli] chitonthozo china chilichonse mwa Khristu, ngati chitonthozo china chilichonse cha chikondi, ngati chiyanjano china chilichonse cha Mzimu, ngati kuli chikondi china chilichonse ndi zifundo zokoma,
  6250. Php 2:2 Kwaniritsani inu chimwemwe changa, kuti mukhale olingalira chimodzimodzi, akukhala nacho chikondi chofanana, [okhala ndi] mtima umodzi, a maganizo amodzi.
  6251. Php 2:3 [Musalole] kanthu kalikonse [kachitidwe] chifukwa cha chotetana kapena monga mwa kudzikweza kwambiri; komatu mu kudzichepetsa mtima aliyense ayese mzake woposa iwo eni.
  6252. Php 2:4 Munthu aliyense asapenyerere zinthu zake za iye yekha, koma munthu aliyense apenyererenso pa zinthu za ena.
  6253. Php 2:5 Lolani mtima uwu ukhale mwa inu, umene udalinso mwa Khristu Yesu:
  6254. Php 2:6 Amene, pokhala nawo mapangidwe a Mulungu, sadachiyese cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu:
  6255. Php 2:7 Koma adadzipanga yekha kukhala wopanda ulemu, ndipo anatenga mawonekedwe a kapolo, ndipo anapangidwa kukhala m’mafanizidwe a anthu:
  6256. Php 2:8 Ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, iye adadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pa mtanda.
  6257. Php 2:9 Mwa ichi Mulungu wamkwezetsa iye pamwambamwamba, ndipo anampatsa iye dzina limene liri pamwamba pa mayina onse:
  6258. Php 2:10 Kuti pa dzina la Yesu bondo lirilonse lipinde, la [zinthu] za kumwamba, ndi [zinthu] za pa dziko lapansi, ndi [zinthu] za pansi pa dziko lapansi;
  6259. Php 2:11 Ndi [kuti] lirime lirilonse livomere kuti Yesu Khristu [ali] Ambuye, ku ulemelero wa Mulungu Atate.
  6260. Php 2:12 Mwa chi, wokondedwa anga, monga momwe mwamvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, koma tsopano koposa ine palibe, gwirani ntchito ya chipulumutso cha inu eni ndi mantha ndi kunthunthumira.
  6261. Php 2:13 Pakuti ndi Mulungu amene achita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe chifukwa cha kukoma mtima [kwake].
  6262. Php 2:14 Chitani zinthu zonse kopanda kung’ung’udza ndi makani:
  6263. Php 2:15 Kuti mukhoze kukhala wopanda chifukwa chotsitsidwa nacho ndi wosapweteka, ana a Mulungu, wopanda vuto, pakati pa dziko lokhotakhota ndi lopotoka, amene pakati pa iwo muwale monga nyali m’dziko lapansi;
  6264. Php 2:16 Ogwiritsitsa mawu a moyo; kuti ine ndikathe kukhala wa chimwemwe m’tsiku la Khristu; kuti ine sindidathamanga kwachabe, kapena kugwiritsa ntchito kwachabe.
  6265. Php 2:17 Inde, ndipo ngatinso ine ndiperekedwa pa nsembe ndi kutumikira ku chikhulupiriro chanu, ine ndiri ndi chimwemwe, ndi kukondwera pamodzi ndi inu nonse.
  6266. Php 2:18 Pa chifukwa chomwechonso inu mukondwera, ndi kukondwera pamodzi ndi ine.
  6267. Php 2:19 Koma ine ndikudalira mwa Ambuye Yesu kutumiza Timoteyo kwa inu posachedwapa, kuti inenso ndikakhale ndi chitonthozo chabwino, pomwe ndazindikira momwe inu muli.
  6268. Php 2:20 Pakuti ine ndiribe munthu wa malingaliro a mtima wofanana ndi otero, amene mwachibadwidwe adzasamalira za momwe inu muli.
  6269. Php 2:21 Pakuti onse atsata za iwo wokha, osati zinthu zomwe ziri za Yesu Khristu.
  6270. Php 2:22 Koma muzindikira matsimikizidwe a iye, kuti, monga mwana wamwamuna ndi atate wake, watumikira pamodzi ndi ine mu uthenga wabwino.
  6271. Php 2:23 Choncho ameneyo ine ndiyembekeza kumtuma tsopanoli, posachedwetsetsa monga m’mene ndikapenyerera monga momwe zidzakhalira ndi ine.
  6272. Php 2:24 Koma ine ndikhulupirira mwa Ambuye kuti inenso mwini ndidza msanga.
  6273. Php 2:25 Komatu ndidayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafroditasi, mbale wanga, ndi mzanga wogwira naye ntchito, ndi msirikali mzanga, koma mthenga wanu, ndi amene adanditumikira pa zosowa zanga.
  6274. Php 2:26 Popeza adali wolakalaka inu nonse, navutika mtima, chifukwa chakuti mudamva kuti adadwala.
  6275. Php 2:27 Pakutidi adadwaladi pafupi imfa: koma Mulungu adamchitira chifundo; koma osati iye yekha, koma inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chowonjezera pa chisoni.
  6276. Php 2:28 Choncho ine ndamtuma iye mosamalitsa koposa, kuti, pakumuwonanso iye, mukhoze kukondwera, ndi kuti inenso ndikakhoze kukhala ndi chisoni chochepa.
  6277. Php 2:29 Choncho mumlandire iye mwa Ambuye ndi chisangalalo chonse; nimuchitire ulemu woterewa:
  6278. Php 2:30 Pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu adafika pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.
  6279. Php 3:1 Chomalizira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulemba zinthu zomwezo kwa inu, kwa ine si [chili] chowopsa, koma kwa inu [chili ichi] chitetezo.
  6280. Php 3:2 Chenjerani ndi agalu, chenjerani ndi wochita zoyipa, chenjerani ndi odzidula.
  6281. Php 3:3 Pakuti ife ndife mdulidwe, amene tilambira Mulungu mu Mzimu, ndi okondwa mwa Yesu Khristu, ndipo tiribe kukhulupirira mu thupi.
  6282. Php 3:4 Ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m’thupi. Ngati munthu wina aliyense aganiza kuti ali nako ako iye angakhoze kukhulupirira m’thupi, ine kwambiri:
  6283. Php 3:5 Wochitidwa mdulidwe tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israyeli, [wa] fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, monga mokhudzana ndi chilamulo; Mfarisi;
  6284. Php 3:6 Zokhudza changu, wozunza mpingo; monga mwa chilungamo cha m’chilamulo, wosalakwa.
  6285. Php 3:7 Koma zinthu zonse zimene zidali phindu kwa ine, zimenezo ndidayesa chitayiko chifukwa cha Khristu.
  6286. Php 3:8 Inde nzosakayikitsa, ndipo ndiyesa zonse [zikhale] chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chidziwitso cha Khristu Ambuye wanga: chifukwa cha iyeyu ndataya zinthu zonse, ndipo ndiziyesa ndowe, kuti ndikakhoze kupindula Khristu,
  6287. Php 3:9 Ndikupezedwa mwa iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa, chomwe chili cha chilamulo, koma chomwe chili cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chimene chili cha Mulungu mwa chikhulupiriro:
  6288. Php 3:10 Kuti ndikhoze kumdziwa iye, ndi mphamvu ya kuwuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;
  6289. Php 3:11 Ngati nkotheka mwa njira ina iliyonse ndikakhoze kufikira ku kuwuka kwa akufa.
  6290. Php 3:12 Osati ngati kuti ine ndalandira kale, kapena kuti ndakonzeka kale wangwiro; koma ine nditsatira, ngati kuti ine ndikhoze kuchigwira chimene ichi chimenenso ine ndigwidwa nacho cha Khristu Yesu.
  6291. Php 3:13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira; koma chinthu chimodzi [ichi] ndichichita; kuyiwala zinthu zomwe ziri m’mbuyo, ndikutambalitsira ku zinthu zomwe ziri m’tsogolo,
  6292. Php 3:14 Ine ndimakankha kutsatira chizindikiro cha mfupo wa mayitanidwe a m’mwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
  6293. Php 3:15 Choncho tiyeni tonsefe, monga ambiri amene tsono adapangidwa a mgwiro, tilingilire mumtima motero; ndipo ngati mu chinthu china chilichonse mulingalira mwa mtundu wina, Mulungu adzavumbulutsira ngakhale ichinso kwa inu.
  6294. Php 3:16 Komabe, kumene ife tidachilandira kale, tiyeni tiyende mu lamulo lomweri, tiyeni tiganizire chinthu chimodzimodzicho.
  6295. Php 3:17 Abale, khalani nonse pamodzi akutsatira anga, ndipo zindikirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife a chitsanzo.
  6296. Php 3:18 (Pakuti ambiri ayenda, za iwo amene ine ndidakuwuzani kawirikawiri, ndipo tsopano ndikuwuzani ngakhale kulira, [kuti iwo ali] adani a mtanda wa Khristu:
  6297. Php 3:19 Amene chitsiriziro chawo [chili] chiwonongeko, amene Mulungu wawo [ali] mimba [yawo], ulemerero [wawo] uli m’manyazi awo, amene asamalira za zinthu za pa dziko.)
  6298. Php 3:20 Pakuti umbadwa wathu uli kumwamba; kuchokera komwekonso tilindira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu:
  6299. Php 3:21 Amene adzasanduliza thupi lathu lapansipansi, kuti lifananizidwe ndi thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene iye akhoza ngakhale ku kugonjetsa zinthu zonse kwa iye mwini.
  6300. Php 4:1 Choncho, abale anga wokondedwa ndi wolakalakidwa, chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, wokondedwa [anga].
  6301. Php 4:2 ¶Ndidandawulira Euodiya, ndipo ndidandawulira Sintike, kuti akhoze kukhala ndi mtima umodzi mwa Ambuye.
  6302. Php 4:3 Ndipo ine ndikupemphanso iwe, wa m’goli mzanga wowona, uthandize akazi awo amene adagwira nane ntchito pamodzi mu uthenga wabwino, pamodzinso ndi Klementi, ndi [pamodzi] ena aja antchito anzanga, amene mayina awo [ali] m’buku la moyo.
  6303. Php 4:4 Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse; [ndipo] ndibwerezanso kunena, Kondwerani.
  6304. Php 4:5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse, Ambuye [ali] pafupi.
  6305. Php 4:6 Musadere nkhawa pa kena kalikonse; koma mu chinthu chilichonse mwa pemphero ndi pembedzero pamodzi ndi chiyamiko zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
  6306. Php 4:7 Ndipo mtendere wa Mulungu, wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu kudzera mwa Khristu Yesu.
  6307. Php 4:8 Chomaliza, abale, zinthu zirizonse zowona, zinthu zirizonse zolemekezeka, zinthu zirizonse [ziri] zolungama, zinthu zirizonse [ziri] zoyera, zinthu zirizonse [ziri] zokongola, zinthu zirizonse ziri za mbiri yabwino; ngati [kuli] chabwino china, kapena [pakhala] chitamando china chilichonse, lingirirani pa zinthu izi.
  6308. Php 4:9 Zinthu zimenezo, zimene mudaziphunzira ndi kuzilandira, ndi kumva, ndi kuwona mwa ine, chitani: ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala ndi inu.
  6309. Php 4:10 Koma ine ndidakondwera kwakukulu mwa Ambuye, kuti tsopano kumapeto kwake chisamaliro chanu cha kwa ine chakulanso, kumenenso mudasamalirako, koma mudasowa mpata.
  6310. Php 4:11 Osati kuti ine ndinena monga mwa chokhumba: pakuti ine ndaphunzira, mwina mulimonse momwe ndiri, m’menemo kukhala wokhutitsidwa.
  6311. Php 4:12 Ndidziwa momwe kupeputsidwa kumachitikira, ndipo ndadziwa kukhala nazo zosefukira: kulikonse ndi m’zinthu zonse ndalangizidwa kukhala wakukhuta ndi kukhala ndi njala, kukhala nazo zokusefukira ndi kukhala wosowa.
  6312. Php 4:13 Ndingathe kuchita zinthu zonse kudzera mwa Khristu wondipatsa mphamvuyo.
  6313. Php 4:14 Ngakhale ziri choncho mwachita bwino, kuti mudayanjana nane m’chisawutso changa.
  6314. Php 4:15 Tsopano inu Afilipi mudziwanso, kuti m’chiyambi cha uthenga wabwino, pamene ndidachoka kutuluka ku Makedoniya, siwudayanjana nane Mpingo uliwonse m’makhalidwe a chopereka ndi kulandira, koma inu nokha.
  6315. Php 4:16 Pakuti ngakhale m’Tesalonika mudatumiza kamodzi ndi kubwerezanso pa chosowa changa.
  6316. Php 4:17 Osati chifukwa chakuti nditsata mphatso: koma ndikhumba chipatso chimene chikhoza kuchulukira kwa inu.
  6317. Php 4:18 Koma ine ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira: ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafroditasi zinthu [zimene zidatumizidwa] kuchokera kwa inu, m’nunkho wa fungo lokoma, nsembe yolandirika, yokondweretsa bwino Mulungu.
  6318. Php 4:19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
  6319. Php 4:20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu [kukhale] ulemerero ku nthawi za nthawi, Amen.
  6320. Php 4:21 Patsani moni woyera mtima aliyense mwa Khristu. Abalewo amene ali ndi ine akupatsani moni inu.
  6321. Php 4:22 Woyera mtima onse akupatsani moni inu, makamaka iwo a nyumba ya Kayisara.
  6322. Php 4:23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu [chikhale] ndi inu nonse. Amen.
  6323. Col 1:1 Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteyo mbale [wathu].
  6324. Col 1:2 Kwa woyera mtima ndi abale wokhulupirika mwa Khristu amene ali ku Kolose: Chisomo [chikhale] kwa inu, ndi mtendere, wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
  6325. Col 1:3 ¶Tipereka mayamiko kwa Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, kupempherera inu nthawi zonse,
  6326. Col 1:4 Kuyambira pamene tidamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu, ndi chikondi [chimene muli nacho] kwa woyera mtima onse,
  6327. Col 1:5 Chifukwa cha chiyembekezo chimene chayikidwira kwa inu kumwamba, chimene inu mudachimva kale m’mawu a chowonadi cha uthenga wabwino;
  6328. Col 1:6 Umene wafika kwa inu, monga [uli] m’dziko lonse lapansi; ndipo umabala chipatso, monganso [uchita] mwa inu, kuyambira tsiku lomwe mudamva [za uwo, ndipo] mwadziwa chisomo cha Mulungu m’chowonadi:
  6329. Col 1:7 Monga momwe munaphunzira kwa Epafrasi wantchito mzathu wokondedwa, amene kwa inu ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu;
  6330. Col 1:8 Amenenso adafotokozera kwa ife chikondi chanu mu Mzimu.
  6331. Col 1:9 Mwa chifukwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva [uwo], sitileka kupempherera inu, ndi kukhumba kuti mukhoze kudzadzidwa ndi chidziwitso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chizindikiritso cha uzimu;
  6332. Col 1:10 Kuti mukhoze kuyenda koyenera Ambuye mu kumkondweretsa monse, kukhala akubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kuchuluka m’chizindikiritso cha Mulungu;
  6333. Col 1:11 Kulimbikitsidwa ndi m’chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, ku chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe;
  6334. Col 1:12 Kupereka mayamiko kwa Atate, amene adatipanga kukwaniritsa kukhala woyenera ife kulandira nawo cholowa cha woyera mtima m’kuwunika:
  6335. Col 1:13 Amene watilanditsa ife ku mphamvu za mdima, ndipo watisuntha [ife] kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wake wamwamuna wokondedwa:
  6336. Col 1:14 Amene mwa iye tiri nawo mawomboledwe kudzera mu mwazi wake, ngakhale kukhululukidwa kwa machimo:
  6337. Col 1:15 Amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chilichonse:
  6338. Col 1:16 Pakuti mwa iye zinthu zonse zidalengedwa, zimene ziri kumwamba, ndi zimene ziri padziko lapansi, zowoneka ndi zosawoneka, ngakhale [itakhala] mipando ya chifumu, kapena maufumu, kapena maulamuliro, kapena zimphamvu: zinthu zonse zidalengedwa ndi iye, ndi kwa iye:
  6339. Col 1:17 Ndipo iye ali woyamba wa zonse; ndipo mwa iye zinthu zonse zikhala.
  6340. Col 1:18 Ndipo iye ali mutu wathupilo, mpingo: amene ali chiyambi, wobadwa woyamba wochokera mwa akufa; kuti mu [zinthu] zonse akhoze kukhala iye woyambirira.
  6341. Col 1:19 Pakuti kudamkomera [Atate] kuti mwa iye chidzalo chonse chikhale;
  6342. Col 1:20 Ndipo, atapereka mtendere kudzera m’mwazi wa mtanda wake, mwa iye kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, kudzera mwa iye [ine] ndinena, kapena [zitakhala zinthu] za pa dziko, kapena zinthu zakumwamba.
  6343. Col 1:21 Ndipo inu, amene nthawi ina [kale] mudakhala alendo ndi adani m’malingaliro [anu] ndi ntchito zoyipa, koma tsopano wakuyanjanitsani.
  6344. Col 1:22 M’thupi lake la umunthu kudzera mu imfa, kukawonetsera inu woyera ndi wopanda chirema ndi wosatsutsika pamaso pake:
  6345. Col 1:23 Ngatitu mukhalabe m’chikhulupiriro, wochilimika ndi wokhazikika ndi wosasunthika kuchotsedwa ku chiyembekezo cha uthenga wabwino, umene mudamva, [ndi] umene wolalikidwa kwa cholengedwa chilichonse chimene chili pansi pa thambo; umene ine Paulo ndapangidwa kukhala mtumiki.
  6346. Col 1:24 Amene tsopano ndikondwera m’zowawa zanga chifukwa cha inu, ndi kukwaniritsa zoperewera za chisawutso cha Khristu m’thupi langa chifukwa cha thupi lake; limene ndilo mpingo:
  6347. Col 1:25 Umene ine ndapangidwa kukhala mtumiki, monga mwakuperekedwa kwa Mulungu kumene kwapatsidwa kwa inechifukwa cha inu, kukakwaniritsa mawu a Mulungu;
  6348. Col 1:26 [Ngakhale] chinsinsicho chidabisika kuyambira pa nthawizo ndi ku mibadwoyo, koma tsopano chawonetsedwa kwa woyera mtima ake:
  6349. Col 1:27 Kwa iwo amene Mulungu adafuna kuwadziwitsa chimene [chili] chuma cha ulemerero wa chinsinsi ichi pakati pa Amitundu; amene ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero:
  6350. Col 1:28 Amene ife timlalikira, kuchenjeza munthu aliyense, ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse; kuti tiwonetsere munthu aliyense wangwiro mwa Khristu Yesu:
  6351. Col 1:29 Ku umene ine ndigwiranso ntchito, kuyesetsa monga mwa machitidwe ake, amene achitachita mwa ine ndi mphamvu.
  6352. Col 2:1 Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndiri nayo chifukwa cha inu, ndi [kwa] iwowa a m’Lawodikeya, ndi [kwa] onse ambiri a iwo amene sadawone nkhope yanga m’thupi;
  6353. Col 2:2 Kuti mitima yawo ikhoze kutonthozedwa, yokhala yolumukizika pamodzi m’chikondi, ndi kufikira ku chuma chonse cha chidzalo cha kumvetsetsa, ku chizindikiro cha chinsinsi cha Mulungu, ndi cha Atate, ndi cha Khristu;
  6354. Col 2:3 Amene mwa iye chuma chonse cha nzeru ndi chidziwitso zabisika.
  6355. Col 2:4 ¶Ndipo ichi ndinena, kuti mwina munthu wina aliyense asakusocheretseni inu ndi mawu wokopakopa.
  6356. Col 2:5 Pakuti ndingakhale sindiri kwa inu m’thupi, komatu ndiri pamodzi ndi inu mu mzimu, wokondwera ndi kupenya dongosolo lanu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu mwa Khristu.
  6357. Col 2:6 Choncho monga momwe inu mudalandira Khristu Yesu Ambuye, [chotero] yendani inu mwa iye:
  6358. Col 2:7 Wozika mizu ndi womangiririka mwa iye, ndi wokhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa m’menemo ndi chiyamiko.
  6359. Col 2:8 Chenjerani kuti mwina munthu wina aliyense asakuwonongeni inu kudzera mu kukonda nzeru kwake ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsatira mfundo za dziko lapansi, osati potsata Khristu.
  6360. Col 2:9 Pakuti mwa iye chikhala chidzalo chonse cha uMulungu m’thupi.
  6361. Col 2:10 Ndipo inu muli athunthu mwa iye, amene ali mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro:
  6362. Col 2:11 Amenenso mumadulidwa mwa iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m’mavulidwe a thupi la machimo a thupi mwa m’dulidwe wa Khristu:
  6363. Col 2:12 Woyikidwa m’manda pamodzi ndi iye mu ubatizo, momwemonso mudawukitsidwa pamodzi [ndi] iye kudzera m’chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene adamuwukitsa iye kwa akufa.
  6364. Col 2:13 Ndipo inu, pokhala akufa m’machimo anu ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, iye wakupatsani moyo pamodzi ndi iye, atakhululukira inu zolakwa zanu zonse;
  6365. Col 2:14 Atafafaniza cholembedwa cha zoyikikazo chimene chidali chotsutsana nafe, chimene chidali chosiyana ndi ife, ndipo adachichotsa panjirapo, kuchikhomera ichi ku mtanda wake;
  6366. Col 2:15 [Ndipo] atavula maukulu ndi maulamuliro, adawawonetsera iwo poyera, nawagonjetsera iwo mu uwo.
  6367. Col 2:16 Choncho munthu aliyense asakuweruzeni inu m’chakudya, kapena m’chakumwa, kapena m’kunena za tsiku loyera, kapena lokhala mwezi, kapena za [masiku] a sabata:
  6368. Col 2:17 Zimene ziri chithunzithunzi cha zinthu zirinkudza; koma thupi [ndi] la Khristu.
  6369. Col 2:18 Munthu aliyense asakunyengeni za mphotho yanu mu kudzichepetsa mwini wake ndi kulambira kwa angelo, ndi kukhalira mu zinthu izo zimene sadaziwona, wodzitukumula chabe mwa zolingalira za thupi lake.
  6370. Col 2:19 Ndipo wosagwira Mutuwo, kumene kuchokerako thupi lonse mwa mfundo ndi mitsempha, lotumikiridwa kudyetsedwa, ndi lokowanidwa pamodzi, likula ndi makulidwe a Mulungu.
  6371. Col 2:20 Mwa ichi ngati mudafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, chifukwa chiyani, monga ngati mukhala moyo m’dziko lapansi, kodi mugonjera ku zoyikikazo.
  6372. Col 2:21 (Usakhudza; usalawa; usagwira;
  6373. Col 2:22 Zimene zonse ziri zakuwonongedwa pozigwiritsa ntchito;) monga mwa malamulo ndi ziphunzitso za anthu?
  6374. Col 2:23 Zinthu zimene ziri nawotu ndithu mawonetsedwe a nzeru m’chifuniro chakulambira, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupilo; osakhala ndi ulemu wina uliwonse ku chikhutitso cha ku thupi.
  6375. Col 3:1 Ngati inu tsono mudawukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zinthu zomwe ziri za kumwamba, kumene Khristu akhala pa dzanja lamanja la Mulungu.
  6376. Col 3:2 Lingalirani pa zinthu za kumwamba, osati pa zinthu za pa dziko lapansi.
  6377. Col 3:3 Pakuti inu mudafa, ndipo moyo wanu wabisika ndi Khristu mwa Mulungu.
  6378. Col 3:4 Pamene Khristu, [amene ali] moyo wathu, adzawoneka, pa nthawi imeneyo inunso mudzawonekera pamodzi ndi iye mu ulemerero.
  6379. Col 3:5 Choncho fetsani ziwalozo ziri padziko; chiwerewere, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako champamvu choyipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano:
  6380. Col 3:6 Chifukwa cha zinthu zimene izi m’kwiyo wa Mulungu umadza pa ana a kusamvera:
  6381. Col 3:7 Mu zimene inunso mudayendamo nthawi zina, pamene mudakhala ndi moyo wanu m’menemo.
  6382. Col 3:8 Koma tsopano inunso tayani izi zonse; kupsa mtima, mkwiyo, kufuna kuchitirana zoyipa, zamwano, zolankhula zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu.
  6383. Col 3:9 Musamanamizana wina ndi mzake; powona kuti mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake;
  6384. Col 3:10 Ndipo mwavala [munthu] watsopano, amene wakonzeka m’chidziwitso kutsata chifanizo cha iye adamulenga iye:
  6385. Col 3:11 Pamene palibe Mhelene kapena Myuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, Wakunja, Msikuti, kapolo [ngakhale] mfulu: komatu Khristu [ali] zonse, ndi mu m’zonse.
  6386. Col 3:12 Choncho valani, monga wosankhidwa a Mulungu, woyera ndi wokondedwa, mitima ya zifundo zokoma, kukoma mtima, kudzichepetsa kwa malingaliro, chifatso, kuleza mtima;
  6387. Col 3:13 Kulolerana wina ndi mzake, ndi kukhululukirana wina ndi mzake, ngati wina ali nawo makangano pa wina aliyense: monganso Khristu adakhululukira inu, kotero inunso [chitani].
  6388. Col 3:14 Ndipo koposa izi zonse [valani] chikondi, chimene ndicho chomangira cha ungwiro.
  6389. Col 3:15 Ndipo lolani mtendere wa Mulungu uchite ufumu m’mitima yanu, kumene kulingakonso mudayitanidwa m’thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.
  6390. Col 3:16 Lolani mawu a Khristu akhalitse mwa inu mochuluka mu nzeru yonse, kuphunzitsa ndi kulimbikitsana wina ndi mzake mu masalmo ndi nyimbo za m’buku ndi nyimbo za uzimu, kuyimba ndi chisomo mu mtima mwanu kwa Ambuye.
  6391. Col 3:17 Ndipo chilichonse chimene muchita m’mawu kapena mu ntchito, [chitani] zonse m’dzina la Ambuye Yesu, kupereka mayamiko kwa Mulungu ndi Atate mwa iye.
  6392. Col 3:18 Akazi, gonjerani inu eni kwa amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
  6393. Col 3:19 Amuna, kondani akazi [anu], ndipo musawawire mtima iwo.
  6394. Col 3:20 Ana, mverani makolo anu m’zinthu zonse, pakuti ichi akondwera nacho Ambuye.
  6395. Col 3:21 Atate, musaputa ana anu [ku mkwiyo], kuti mwina mwake angataye mtima.
  6396. Col 3:22 Antchito, mverani m’zinthu zonse ambuye [anu] monga mwa thupi, wosati utumiki wa pamaso, monga wokondweretsa anthu; komatu mu mtima umodzi, akuwopa Ambuye:
  6397. Col 3:23 Ndipo chilichonse chimene muchichita, chitani [icho] mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, wosati kwa anthu ayi;
  6398. Col 3:24 Podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa: pakuti mutumikira Ambuye Khristu.
  6399. Col 3:25 Koma iye wakuchita cholakwa adzalandira chosalungama chifukwa cha cholakwa chimene wachitacho: ndipo palibe tsankhu pa anthu.
  6400. Col 4:1 Ambuye [iwo amene ali ndi antchito], chitirani antchito [anu] chimene chili cholungama ndi cholingana, podziwa kuti inunso muli naye Ambuye kumwamba.
  6401. Col 4:2 Pitirirani m’kupemphera, ndipo mudikire momwemo ndi mayamiko;
  6402. Col 4:3 Panthawi yomweyo kutimphereranso ife, kuti Mulungu atitsegulire ife khomo la kulankhula; kuti tiyankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m’ndende:
  6403. Col 4:4 Kuti ndichiwonetse ichi, monga ine ndiyenera kuyankhulira.
  6404. Col 4:5 Muyende mu nzeru ndi iwo akunja, kuwombola nthawi.
  6405. Col 4:6 Lolani zoyankhula zanu [zikhale nthawi zonse] ndi chisomo, zokoleretsedwa ndi mchere, kuti inu mukadziwe momwe inu muyenera kuyankhira munthu aliyense.
  6406. Col 4:7 ¶Zonse za ine Tichikasi adzazizindikiritsa kwa inu, [amene ali] mbale wokondedwa, ndi mtumiki wokhulupirika ndi wantchito mzanga mwa Ambuye:
  6407. Col 4:8 Amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha cholinga ichi chomwe, kuti akadziwe za kwa inu, ndi kutonthoza mitima yanu;
  6408. Col 4:9 Pamodzi ndi Onesimasi, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali m’modzi wa inu. Adzadziwitsa kwa inu zinthu zonse zimene [zachitidwa] kuno.
  6409. Col 4:10 Aristakasi wa m’ndende mzanga akupatsani moni, ndi Markasi, mwana wamwamuna wa mlongo wa Barnabas, (kukhudza iye amene mudalandira malamulo: ngati abwera kwa inu, mumulandire iye;)
  6410. Col 4:11 Ndi Yesu, wotchedwa Yustasi, amene ali a mdulidwe. Iwo wokha [ali] antchito [anzanga] a mu Ufumu wa Mulungu; amene akhala otonthoza mtima kwa ine.
  6411. Col 4:12 Epafrasi, amene ali [m’modzi] wa inu, wantchito wa Khristu, akupatsani moni, wakugwira ntchito molimbika nthawi zonse chifukwa cha inu m’mapemphero, kuti mukhoze kuyima angwiro ndi athunthu m’chifuniro chonse cha Mulungu.
  6412. Col 4:13 Pakuti ndimachitira iye umboni, kuti ali ndi changu chachikulu cha kwa inu, ndi iwo amene ali m’Lawodikeya, ndi iwo a mu Herapolisi.
  6413. Col 4:14 Luka, dotolo wokondedwa, ndi Demasi, akupatsani inu moni.
  6414. Col 4:15 Patsani moni abale amene ali m’Lawodikeya, ndi Numfasi, ndi mpingowo umene uli m’nyumba yake.
  6415. Col 4:16 Ndipo pamene kalata iyi iwerengedwa pakati panu, muwapangitse kuti iwerengedwenso ku mpingo wa Alawodikeya; ndi kuti inunso chimodzimodzinso muwerenge [kalata] yochokera ku Lawodikeya.
  6416. Col 4:17 Ndipo munene kwa Arkipasi, Samaliratu ku utumiki umene iwe udawulandira mwa Ambuye, kuti iwe uwukwaniritse iwo.
  6417. Col 4:18 Moniwu ndi wa dzanja la ine Paulo. Kumbukirani undende wanga. Chisomo [chikhale] ndi inu. Amen.
  6418. 1Th 1:1 Paulo, ndi Silvanasi, ndi Timoteyo, kwa mpingo wa Atesalonika [umene uli] mwa Mulungu Atate ndi [mwa] Ambuye Yesu Khristu: Chisomo [chikhale] kwa inu, ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
  6419. 1Th 1:2 ¶Tipereka mayamiko kwa Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kutchula inu m’mapemphero athu;
  6420. 1Th 1:3 Kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi ntchito za chikondi, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu ndi Atate wathu;
  6421. 1Th 1:4 Podziwa, abale wokondedwa, chisankhidwe chanu cha Mulungu.
  6422. 1Th 1:5 Pakuti uthenga wabwino wathu si udadza kwa inu m’mawu mokha, komanso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi mchitsimikizo chachikulu; monga mudziwa tidakhala anthu wotani mwa inu chifukwa cha inu.
  6423. 1Th 1:6 Ndipo mudakhala wotitsatira athu, ndi a Ambuye, mutalandira mawuwo m’chisawutso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera:
  6424. 1Th 1:7 Kotero kuti inu mudali chitsanzo kwa iwo onse akukhulupirira m’Makedoniya ndi m’Akaya.
  6425. 1Th 1:8 Pakuti kuchokera kwa inu kudamveka mawu a Ambuye wosati m’Makedoniya ndi m’Akaya mokha, komanso m’malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidafalikira; kotero kuti sikufunika kwa ife kuyankhula kanthu.
  6426. 1Th 1:9 Pakuti iwo wokha awonetsa za ife momwe malowedwe athu a kwa inu adali; ndi momwe mudatembenukira kwa Mulungu posiyana nawo mafano kuti mutumikire Mulungu weniweni wamoyo;
  6427. 1Th 1:10 Ndikulindirira Mwana wake wamwamuna kuchokera kumwamba, amene adamuwukitsa kwa akufa, [ndiye] Yesu, amene adatipulumutsa ife ku mkwiyo ulinkudza.
  6428. 1Th 2:1 Pakuti inu eni, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sadakhala wopanda phindu:
  6429. 1Th 2:2 Koma ngakhale kuti tidamva zowawa kale, ndipo adatichititsa manyazi, monga inu mudziwa, ku Filipi, tidalimbika mtima mwa Mulungu wathu kuyankhula ndi inu uthenga wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.
  6430. 1Th 2:3 Pakuti kudandawulira kwathu si kudali kwa kubisa chowonadi, kapena kwa ku chidetso, kapena m’chinyengo:
  6431. 1Th 2:4 Koma monga adativomera Mulungu kuti tiyikizidwe m’kudaliridwa ndi uthenga wabwino, koteronso tiyankhula; wosati monga wokondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.
  6432. 1Th 2:5 Pakuti nthawi iliyonse sitidagwiritsa ntchito mawu wosyasyalika, monga mudziwa, kapena chovala chakusirira, mboni [ndi] Mulungu:
  6433. 1Th 2:6 Kapena sitidafuna kwa anthu ulemerero, kapena kwa inu, kapena [ngakhale] kwa ena, pamene tikadakhoza kukhala wokulemetsani, monga atumwi a Khristu.
  6434. 1Th 2:7 Koma tidakhala wodekha pakati pa inu, monga m’mene mlezi afukata ana ake:
  6435. 1Th 2:8 Potero pokhala wokhudzidwa ndi chikhumbo cha kwa inu, tidali wofuna tikadakhala kuti tapereka kwa inu, si uthenga wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu eni, popeza mudali wokondedwa kwa ife.
  6436. 1Th 2:9 Pakuti inu mukumbukira, abale, ntchito yathu ndi chivuto: pogwira ntchito usiku ndi usana, chifukwa chakuti tingakhale cholemetse kwa wina aliyense wa inu, ife tidalalikira kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu.
  6437. 1Th 2:10 Inu [ndinu] mboni, ndi Mulungunso, m’mene moyera mtima ndi molungama ndi mosapezeka [ndi chifukwa] chotsutsidwa nacho tidakhalira kwa inu akukhulupirira:
  6438. 1Th 2:11 Monga inu mudziwa momwe ife tidadandawulira ndi kutonthozera ndi kulamulira wina aliyense wa inu, monga atate [achitira] ana ake.
  6439. 1Th 2:12 Kuti muyende koyenera Mulungu, amene adakuyitanani inu kulowa ufumu wake ndi ulemerero.
  6440. 1Th 2:13 Mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, chifukwa, pamene mudalandira mawu a Mulungu amene mudawamva kwa ife, simudawalandire [iwo] monga mawu a anthu, koma monga ali mu chowonadi, mawu a Mulungu, amenenso agwira ntchito bwino lomwe mwa inu amene mukhulupirira.
  6441. 1Th 2:14 Pakuti inu, abale, mudakhala akutsanza a mipingo ya Mulungu imene mu Yudeya ili mwa Khristu Yesu: popeza inunso mwamva kuwawa zinthu zochokera kwa anthu a mtundu wanu womwe, monganso iwo [achitira] Ayuda:
  6442. 1Th 2:15 Amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri awo eni, ndipo atizunza ife; ndipo sakondweretsa Mulungu, ndipo atsutsana nawo anthu onse:
  6443. 1Th 2:16 Kutiletsa ife kuti tisayankhule kwa Amitundu kuti akhoze kupulumutsidwa; kudzazitsa machimo awo nthawi zonse; chifukwa mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.
  6444. 1Th 2:17 Koma ife, abale, titachotsedwa kwa inu kanthawi mu kupezeka, osati mu mtima, tidayesetsa koposaposatu kuwona nkhope yanu ndi chikhumbo chachikulu.
  6445. 1Th 2:18 Mwa ichi tikadadza kwa inu, ngakhale ine Paulo, kamodzi kapena kawiri; koma Satana adatiletsa.
  6446. 1Th 2:19 Pakuti chiyembekezo chathu [chili] chiyani, kapena chimwemwe, kapena korona wakukondwera? Si muli inu nanga mkupezeka kwa Ambuye wathu Yesu Khristu pakufika kwake?
  6447. 1Th 2:20 Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.
  6448. 1Th 3:1 Mwaichi pamene sitikadakhoza kudziletsabe, tidaganiza kuti ndi kwabwino kuti tisiyidwe tokha pa Atene;
  6449. 1Th 3:2 Ndipo tidatuma Timoteyo, mbale wathu ndi mtumiki wa Mulungu, ndi wantchito mzathu mu uthenga wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu zokhudza chikhulupiriro chanu:
  6450. 1Th 3:3 Kuti munthu aliyense asasunthike ndi zisawutso izi: pakuti mudziwa nokha kuti tidayikidwa ife ku zimenezo.
  6451. 1Th 3:4 Pakuti ndithudi, pamene tidali ndi inu, tidakuwuziranitu m’mbuyomo kuti tidzayenera kumva chisawutso; monga zidachitika, ndipo inu mudziwa.
  6452. 1Th 3:5 Mwa chifukwa ichi inenso, pamene sindikakhoza kudziletsabe, ndidatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena mwa njira ina woyesayo adakuyesani inu, ndipo ntchito yathu ikakhala yopanda phindu.
  6453. 1Th 3:6 Koma tsopano pamene anafika Timoteyo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kubweretsera ife mbiri yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondano chanu, ndi kuti muli ndi chikumbukiro chabwino cha ife nthawi zonse, pokhumba koposa kutiwona ife; monga ifenso [kukuwonani] inu:
  6454. 1Th 3:7 Choncho, abale, tidatonthozedwa pa inu mu kupsinjika kwathu konse ndi chisawutso chathu chonse mwa chikhulupiriro chanu:
  6455. 1Th 3:8 Pakuti tsopano tiri ndi moyo, ngati inu muchilimika mwa Ambuye.
  6456. 1Th 3:9 Pakuti tikhoza kuperekanso kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, chifukwa cha chimwemwe chonse chimene ife tikondwera nacho chifukwa cha inu pamaso pa Mulungu wathu;
  6457. 1Th 3:10 Usiku ndi usana kupemphera koposatu kuti tikawone nkhope yanu, ndi kupangitsa ungwiro chimene chili choperewerera pa chikhulupiriro chanu?
  6458. 1Th 3:11 Tsopano Mulungu mwini yekha ndi Atate wathu, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, atitsogolere m’njira yakufika kwa inu.
  6459. 1Th 3:12 Ndipo Ambuye akupangeni inu kuti muchuluke ndi kukula mu chikondi kwa wina ndi mzake, ndi kwa [anthu] onse, monganso ife [tichita] kwa inu:
  6460. 1Th 3:13 Kuti kumapeto kwake akakhoze kukhazikitsa mitima yanu yopanda chifukwa mu chiyero pamaso pa Mulungu, amene ndi Atate wathu, pakufika kwa Ambuye wathu Yesu Khristu pamodzi ndi woyera mtima ake onse.
  6461. 1Th 4:1 Kupitirira apo tsono tikupemphani inu, abale, ndi kukudandawulirani [inu] mwa Ambuye Yesu, kuti monga mwalandira kwa ife momwe muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, [kotero] inu chulukani ndi kuchuluka koposa.
  6462. 1Th 4:2 Pakuti mudziwa malamulo tidakupatsani inu mwa Ambuye Yesu.
  6463. 1Th 4:3 Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, [ngakhale] chiyeretso chanu, kuti mudzipatule ku chiwerewere:
  6464. 1Th 4:4 Kuti aliyense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu;
  6465. 1Th 4:5 Kosati m’chisiriro cha chilakolako champhamvu chonyansa, monganso Amitundu amene samudziwa Mulungu:
  6466. 1Th 4:6 Kuti asapitirireko [munthu] aliyense ndi kunyenga mbale wake mu nkhani ina iliyonse: chifukwa chakuti Ambuye [ndiye] wobwezera wa zonse zotero, monganso tidakuchenjezeranitu inu ndi kuchita umboni.
  6467. 1Th 4:7 Pakuti Mulungu sadayitana ife ku chidetso, koma ku chiyero.
  6468. 1Th 4:8 Choncho iye amene anyoza, sanyoza munthu, koma Mulungu, amene waperekanso kwa ife Mzimu Woyerawake.
  6469. 1Th 4:9 Koma monga zokhudza chikondano cha pa abale sikufunika kuti ndilembere kwa inu: pakuti inu eni mumaphunzitsidwa ndi Mulungu kukondana wina ndi mzake;
  6470. 1Th 4:10 Ndipo zowonadi inu muchita ichi kwa abale onse amene ali m’Makedoniya yense: koma tikupemphani inu, abale, kuti muchuluke ndi kuchuluka koposa;
  6471. 1Th 4:11 Ndi kuti inu muphunzire kukhala chete, ndi kuchita za inu eni, ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tidakulamulirani;
  6472. 1Th 4:12 Kuti mukhoze kuyenda mowona mtima pa iwo a kunja, ndi [kuti] mukhoze kukhala osasowa kanthu.
  6473. 1Th 4:13 ¶Koma ine sindikadafuna inu kuti mukhale osadziwa, abale, zokhudza iwo amene ali kugona, kuti inu musamve chisoni, monganso enawo amene alibe chiyembekezo.
  6474. 1Th 4:14 Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira ndi kuwukanso, koteronso iwo akugona mwa Yesu Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye.
  6475. 1Th 4:15 Pakuti ichi tinena kwa inu m’mawu a Ambuye, kuti ife amene tiri ndi moyo [ndi] okhalapobe kufikira kubwera kwa Ambuye sitidzakhala patsogolo pa iwo amene ali kugonawo.
  6476. 1Th 4:16 Pakuti Ambuye mwini yekha adzatsika kumwamba ndi mfuwu, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndipo ndi kulira kwa lipenga la Mulungu: ndipo akufa mwa Khristu adzawuka choyamba:
  6477. 1Th 4:17 Pamenepo ife wokhala ndi moyo [ndi] wotsala tidzakwatulidwa ndi iwo pamodzi m’mitambo, kukakomana ndi Ambuye mum’mlengalenga: ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.
  6478. 1Th 4:18 Mwa ichi, tonthozanani wina ndi mzake ndi mawu awa.
  6479. 1Th 5:1 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, inu mulibe kufunikira kwakuti ndilembere kwa inu.
  6480. 1Th 5:2 Pakuti inu nokha mudziwa bwino kwambiri kuti tsiku la Ambuye motero lidzadza monga mbala usiku.
  6481. 1Th 5:3 Pakuti pamene iwo adzanena, Mtendere ndi chitetetezo; pamenepo mwadzidzidzi chiwonongeko chidzawagwera iwo, monga zowawa zakubereka za mkazi wapakati; ndipo sadzapulumuka konse.
  6482. 1Th 5:4 Koma inu, abale, simuli mu mdima, kuti tsiku ilo lidzakupitirireni inu monga mbala.
  6483. 1Th 5:5 Muli inu nonse ana a kuwunika, ndi ana a usana: sitiri a usiku, kapena a mdima.
  6484. 1Th 5:6 Choncho tsono ife tisagone, monga [achitira] enawo; komatu tidikire ndipo tisaledzere.
  6485. 1Th 5:7 Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo amene aledzera amaledzera usiku.
  6486. 1Th 5:8 Koma tiyeni ife, amene tiri a usana, tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi, ndi cha chisoti, chiyembekezo cha chipulumutso.
  6487. 1Th 5:9 Pakuti Mulungu sadatiyika ife ku mkwiyo, koma kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,
  6488. 1Th 5:10 Amene adatifera ife, kuti, kapena tidzuka kapena kugona, tikhale ndi moyo pamodzi ndi iye.
  6489. 1Th 5:11 Mwa ichi tonthozanani eni nokha pamodzi, ndipo mangiriranani wina ndi mzake, monganso mumachita.
  6490. 1Th 5:12 ¶Ndipo ife tikupemphani inu, abale, kuwadziwa iwo amene agwira ntchito pakati pa inu, ndipo ali akuluakulu anu mwa Ambuye, amakuwuzani inu choyenera kuchita;
  6491. 1Th 5:13 Ndi kuwachitira ulemu wapamwamba mwa chikondi chifukwa cha ntchito yawo. [Ndipo] khalani ndi mtendere pakati pa inu eni nokha.
  6492. 1Th 5:14 Tsopano tidandawulira inu abale, achenjezeni iwo amene ali osamvera malamulo, tonthozani oganiza mofowoka, chilikizani wofoka, mukhale woleza mtima kwa [anthu] onse.
  6493. 1Th 5:15 Penyani kuti wina asabwezere choyipa ku choyipa kwa [munthu] aliyense; koma nthawi zonse mutsatire chimene chili chabwino, pakati pa inu eni, ndi kwa [anthu] onse.
  6494. 1Th 5:16 Kondwerani nthawi zonse.
  6495. 1Th 5:17 Pempherani kosalekeza.
  6496. 1Th 5:18 Mu zinthu zonse yamikani: pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu mwa Khristu Yesu chokhudza inu.
  6497. 1Th 5:19 Musazime Mzimuyo.
  6498. 1Th 5:20 Musanyoze mauneneri.
  6499. 1Th 5:21 Yesani zinthu zonse; gwiritsitsani chimene chili chabwinocho.
  6500. 1Th 5:22 Mupewe mawonekedwe onse a choyipa.
  6501. 1Th 5:23 Ndipo Mulungu wa mtendere amene ayeretse inu kwathunthu; ndipo [ine ndipemphera Mulungu] mzimu wanu wonse ndi moyo wanu ndi thupi lanu, zisungidwe zopanda chirema pa kudza kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  6502. 1Th 5:24 Wokhulupirika [ali] iye wakuyitana inu, amenenso adzachita [ichi].
  6503. 1Th 5:25 Abale, tipempherereni ife.
  6504. 1Th 5:26 Patsani moni abale onse ndi chipsopsono chopatulika.
  6505. 1Th 5:27 Ndikulamulirani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse woyera mtima.
  6506. 1Th 5:28 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu [chikhale] ndi inu. Amen.
  6507. 2Th 1:1 Paulo, ndi Silvanasi, ndi Timoteyo, kwa mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu:
  6508. 2Th 1:2 Chisomo kwa inu, ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
  6509. 2Th 1:3 ¶Tiri woyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuli koyenera, chifukwa chakuti chikhulupiriro chanu chikula mopambana, ndi chikondi cha wina aliyense wa inu nonse kwa wina ndi mzake chichuluka;
  6510. 2Th 1:4 Kotero kuti ife eni tokha tidzitamandira mwa inu m’mipingo ya Mulungu chifukwa cha chipiriro chanu ndi chikhulupiriro chanu ndi mazunzo anu onse ndi zisawutsozo zimene inu mupirira:
  6511. 2Th 1:5 [Chimene chili] chikole chowonetsedwa cha chiweruzo cholungama cha Mulungu, kuti mukawerengedwe woyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumva nawo zowawa:
  6512. 2Th 1:6 Powona kuti [ichi ndi] chinthu cha chilungamo kwa Mulungu kuti abwezere chizunzo kwa iwo amene akuvuta inu;
  6513. 2Th 1:7 Ndi kwa inu amene muzunzidwa pumulani pamodzi ndi ife, pa nthawi imene Ambuye Yesu adzavumbulutsidwa kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu,
  6514. 2Th 1:8 M’lawi lamoto kubwezera chilango kwa iwo amene sadziwa Mulungu, ndi iwo amene samvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu Khristu:
  6515. 2Th 1:9 Amene adzalangidwa ndi chiwonongeko chosatha chochokera ku nkhope ya Ambuye, ndi kuchokera ku ulemerero wa mphamvu yake;
  6516. 2Th 1:10 Pamene adzadza kuti adzalemekezedwe mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwitsidwa mwa iwo onse amene akhulupirira (pakuti umboni wathu tidawuchita pakati pa inu udakhulupiridwa) mu tsiku lija.
  6517. 2Th 1:11 Mwa ichi ife tipempherera inu nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akadakhoza kukuwerengani inu oyenera a mayitanidwe [awa], ndi kukwaniritsa kukondwera kwabwino konse kwa ubwino wake, ndi ntchito ya chikhulupiriro ndi mphamvu:
  6518. 2Th 1:12 Kuti dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu likhoze kulemekezedwa mwa inu, ndi inu mwa iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
  6519. 2Th 2:1 Tsopano tikupemphani inu, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi [mwa] kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye.
  6520. 2Th 2:2 Kuti inu musamagwedezeka m’maganizo anu msanga, kapena kuvutika, kapena mwa mzimu, kapena mwa mawu, kapena mwa kalata monga yolembedwa kuchokera kwa ife, monga ngati tsiku la Khristu layandikira.
  6521. 2Th 2:3 Musalole munthu akunyengeni mwa njira ina iliyonse: pakuti [tsiku limenero silidzafika], pokhapo choyamba chifike chipatukocho, ndi kuti avumbulutsidwe munthu wauchimoyo, mwana wamwamuna wa chiwonongeko;
  6522. 2Th 2:4 Amene atsutsana nadzikweza yekha pamwamba pa zonse zimene zitchedwa Mulungu, kapena zimene zilambiridwa; kotero kuti iye monga Mulungu akhala pansi mu kachisi wa Mulungu, kudziwonetsera yekha kuti ali Mulungu.
  6523. 2Th 2:5 Simukumbukira kodi, kuti, pa nthawi imene ndinakhala ndi inu, ine ndidakuwuzani zinthu izi?
  6524. 2Th 2:6 Ndipo inu tsopano muchidziwa chimene chimletsa kuti iye akhoze kuvumbulutsidwa m’nyengo yake ya iye.
  6525. 2Th 2:7 Pakuti chinsinsi cha kusamvera lamulo chikugwira ntchito kale: chokhachi chakuti tsopano iye womletsa [adzamletsa], kufikira pamene iye akhale atachotsedwa pa njira.
  6526. 2Th 2:8 Ndipo pamenepo Woyipayo adzavumbulutsidwa, amene Ambuye adzamuwononga ndi mzimu wa pakamwa pake, ndipo adzamuwononga ndi kuwala kwa kudza kwake.
  6527. 2Th 2:9 [Ngakhale iye], kudza kwake kuli kotsata ntchito za Satana ndi mphamvu yonse ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama,
  6528. 2Th 2:10 Ndipo ndi chinyengo chonse cha chosalungama mwa iwo amene akuwonongeka; chifukwa sanalandira chikondi cha chowonadicho, kuti iwo akhoze kupulumutsidwa.
  6529. 2Th 2:11 Ndipo chifukwa cha ichi Mulungu adzatumiza kwa iwo machitidwe olimba akusocheretsa, kuti iwo akhulupirire bodza:
  6530. 2Th 2:12 Kuti iwo onse akhoze kuwonongeka amene sanakhulupirire chowonadicho, koma anakondwera mu chosalungama.
  6531. 2Th 2:13 Koma ife tiri oyenera kupereka mayamiko kwa Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, pakuti Mulungu kuyambira pa chiyambi anakusankhani inu ku chipulumutso kudzera chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha chowonadi.
  6532. 2Th 2:14 Kumene iye anayitanira inu mwa uthenga wabwino wathu, ku kulandira ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
  6533. 2Th 2:15 Choncho, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene inu munaphunzitsidwa, kapena mwa mawu, kapena kalata yathu.
  6534. 2Th 2:16 Tsopano Ambuye wathu Yesu Khristu mwini yekha, ndi Mulungu, amene ndiye Atate wathu, amene watikonda ife, ndipo watipatsa [ife] chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chabwino mwa chisomo,
  6535. 2Th 2:17 Atonthoze mitima yanu, ndi kukhazikitsa inu mu mawu aliwonse abwino ndi ntchito.
  6536. 2Th 3:1 Chomaliza, abale, mutipempherere ife, kuti mawu a Ambuye afalikire [momasuka], ndi kulemekezedwa, monganso [ziri] ndi inu:
  6537. 2Th 3:2 Ndi kuti tikhoze kulanditsidwa m’manja a anthu onse amene ali osachitirana zabwino ndi woyipa: chifukwa anthu [onse] si ali ndi chikhulupiriro.
  6538. 2Th 3:3 Koma Ambuye ali wokhulupirika, amene adzakukhazikitsani inu, ndi kukusungani [inu] ku choyipa.
  6539. 2Th 3:4 Ndipo ife tiri ndi chikhulupiriro mwa Ambuye zokhudza inu, kuti inu mumachita ndiponso mudzachita zinthu zimene ife tikulamulirani inu.
  6540. 2Th 3:5 Ndipo Ambuye atsogolere mitima yanu kulowa m’chikondi cha Mulungu, ndi kulowa m’chipiriro choyembekezera Khristu.
  6541. 2Th 3:6 Tsopano ife tikulamulirani inu, abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti musiye kuyenda pamodzi ndi mbale aliyense amene ayenda mosalongosoka, ndikusatsata mwambo umene iye adawulandira kwa ife.
  6542. 2Th 3:7 Pakuti inu nokha mudziwa momwe muyenera kutitsatira ife: pakuti ife sitidakhala pakati pa inu mosalongosoka;
  6543. 2Th 3:8 Kapena ife sitinadya mkate chabe wa munthu aliyense; koma kugwira ntchito ndi chivuto ndi chipsinjo usiku ndi usana, kuti tingakhoze kulemetsa wina wa inu:
  6544. 2Th 3:9 Osati chifukwa kuti ife tiribe ulamuliro, koma kudzipanga ife eni tokha chitsanzo kwa inu kuti mutsatire ife.
  6545. 2Th 3:10 Pakutinso ngakhale pamene tidali ndi inu, ichi tidakulamulirani kuti, ngati wina aliyense safuna kugwira ntchito, iye asadyenso.
  6546. 2Th 3:11 Pakuti tikumva kuti pali ena mwa inu amene ayenda pakati panu mosalongosoka, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina.
  6547. 2Th 3:12 Koma tsopano amene ali otere ife tilamulira ndi kudandawulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti ndi kachetechete iwo agwire ntchito, nadye chakudya cha iwo wokha.
  6548. 2Th 3:13 Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.
  6549. 2Th 3:14 Koma ngati wina samvera mawu athu mwa kalata iyi, m’dziweni bwinobwino ameneyo. Kuti musayanjane naye, kuti iye achite manyazi.
  6550. 2Th 3:15 Koma musamuyese [iye] monga mdani, koma mu mlangize [iye] ngati mbale.
  6551. 2Th 3:16 Tsopano Ambuye wa mtendere iye mwini akupatseni inu mtendere nthawi zonse, mwa njira ina iliyonse. Ambuye [akhale] ndi inu nonse.
  6552. 2Th 3:17 Moni wa Paulo ndi dzanja la ine mwini, chimene ndi chikole m’kalata iliyonse: kotero ndilemba.
  6553. 2Th 3:18 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu [chikhale] ndi inu nonse. Amen.
  6554. 1Ti 1:1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa lamulo la Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, [amene ali] chiyembekezo chathu;
  6555. 1Ti 1:2 Kwa Timoteyo, [mwana wanga wamwamuna] weniweni m’chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, [ndi] mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
  6556. 1Ti 1:3 ¶Monga ndidakulamulira iwe kuti ukhalebe ku Efeso, pamene ndidapita ine m’Makedoniya, kuti ukhoze kulamulira ena kuti asaphunzitse chiphunzitso china.
  6557. 1Ti 1:4 Kapena asasamale nkhani zachabe ndi mawerengedwe osalekeza a mibadwo, amene atumikira mafunso, m’malo mwa kumangirira kwa umulungu kumene kuli m’chikhulupiriro: [kotero uchite].
  6558. 1Ti 1:5 Tsopano chitsirizo cha chilamuliro ndi chikondi chochokera mu mtima woyera, ndi [cha] chikumbumtima chabwino ndi [cha] chikhulupiriro chosanyenga:
  6559. 1Ti 1:6 Kuchokera ku zimenezo ena pozilambalala adapatukira kutsata kulankhula kopusa;
  6560. 1Ti 1:7 Ofuna kukhala aphunzitsi a lamulo; wosamvetsa ngakhale zimene iwo anena, kapena ku zimene iwo azitsimikiza.
  6561. 1Ti 1:8 Koma tidziwa kuti lamulo [ndi labwino], ngati munthu aligwiritsa nchito monga mwa lamulo;
  6562. 1Ti 1:9 Podziwa ichi, kuti lamulo silipangidwa kwa munthu wolungama, koma kwa wosayeruzika ndi wosamvera, kwa wosapembedza, ndi kwa wochimwa, kwa osayera ndi amnyozo, kwa akupha a atate ndi akupha a amayi, kwa akupha anthu,
  6563. 1Ti 1:10 Kwa achigololo, kwa iwo akudziyipsa eni wokha pakuchita zoyipa ndi amuna, kwa akuba anthu, kwa amabodza, kwa anthu wolumbira zonama, ndipo ngati pangathe kukhala kanthu kena kamene kali kosemphana ndi chiphunzitso cholamitsa;
  6564. 1Ti 1:11 Molingana ndi uthenga wabwino wa ulemerero wa Mulungu wodalitsika, umene udasungitsidwa kwa ine.
  6565. 1Ti 1:12 Ndipo ndiyamika Khristu Yesu Ambuye wathu, amene wandipatsa ine kuthekera, chifukwa cha chimene iye adandiwerengera ine kukhala wokhulupirika, kundiyika ine mu utumiki;
  6566. 1Ti 1:13 Amene kale ndidali wamwano, ndi wozunza, ndi wovulaza: koma ndidalandira chifundo, popeza ndidachita [ichi] wosazindikira m’kusakhulupirira.
  6567. 1Ti 1:14 Ndipo chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu ndi chikhulupiriro ndi chikondi chimene chili mwa Khristu Yesu.
  6568. 1Ti 1:15 Ichi [ndi] chonena chokhulupirika ndi choyenera kulandirika konse, kuti Khristu Yesu anadza m’dziko lapansi kupulumutsa wochimwa; amene wa iwo ine ndiri woposa.
  6569. 1Ti 1:16 Komabe chifukwa cha ichi ndidalandira chifundo, kuti mwa ine poyamba Yesu Khristu akakhoze kuwonetsa kuleza mtima konse, kuti kukhale chitsanzo cha kwa iwo amene kuyambira tsopano adzakhulupirira pa iye kufikira moyo wosatha.
  6570. 1Ti 1:17 Tsopano kwa Mfumu yosatha, yosafa, yosawoneka, Mulungu yekhayo wa nzeru, [ukhale] ulemu ndi ulemerero kufikira nthawi za nthawi. Amen.
  6571. 1Ti 1:18 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga wamwamuna Timoteyo, malingana ndi mauneneri amene adapita kale kutsogolo kwa iwe, kuti iwe mwa iwo ulimbane nayo nkhondo yabwino.
  6572. 1Ti 1:19 Kugwira chikhulupiriro, ndi chikumbumtima chokoma; chimene ena adachitaya chokhudza chikhulupiriro adawonongeka;
  6573. 1Ti 1:20 A iwo amene ali Humaneyasi ndi Alekizanda; amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusayankhula zonyoza Mulungu.
  6574. 1Ti 2:1 Ndidandawulira tsono, kuti, poyamba pa zonse, mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, [ndi] kupereka kwa mayamiko, kuti zichitike chifukwa cha anthu onse;
  6575. 1Ti 2:2 Kwa mafumu, ndi [kwa] onse amene ali mu ulamuliro; kuti tikhoze kukhala m’moyo wachete ndi wa mtendere mu umulungu wonse ndi mowona mtima.
  6576. 1Ti 2:3 Pakuti ichi [ndi] chabwino ndi chovomerezeka pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;
  6577. 1Ti 2:4 Amene afuna anthu onse apulumuke, ndi kufika ku chidziwitso cha chowonadi.
  6578. 1Ti 2:5 Pakuti [pali] Mulungu m’modzi ndi mkhala pakati m’modzi pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu ameneyo Khristu Yesu;
  6579. 1Ti 2:6 Amene adadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse; kuti akachitidwe umboni m’nyengo yoyikika.
  6580. 1Ti 2:7 Umene adandiyika ine mlaliki wake ndi mtumwi, (ndinena zowona mwa Khristu, ndipo sindinama ine;) mphunzitsi wa Amitundu m’chikhulupiriro ndi chowonadi.
  6581. 1Ti 2:8 Choncho ine ndifuna kuti amunawo apemphere kulikonse, kukweza manja woyera, wopanda mkwiyo ndi kukayika.
  6582. 1Ti 2:9 Mu chikhalidwe chomwechonso, akazi adziveke wokha mu chovala chosapereka chilakolako cha chiwerewere, ndi nkhope ya manyazi ndi chidziletso; osati ndi tsitsi loluka, kapena golidi, kapena ngale, kapena malaya a mtengo wapatali;
  6583. 1Ti 2:10 Koma (umo mokomera akazi akuvomereza umulungu) ndi ntchito zabwino.
  6584. 1Ti 2:11 Mulole kuti mkazi aphunzire mwachete m’kugonjera konse.
  6585. 1Ti 2:12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna, koma kuti akhale chete.
  6586. 1Ti 2:13 Pakuti Adamu adayamba kulengedwa, kenaka Heva.
  6587. 1Ti 2:14 Ndipo Adamu sadanyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa adali mu kuswa lamulo.
  6588. 1Ti 2:15 Koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhalabe m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyero pamodzi ndi chidziletso.
  6589. 1Ti 3:1 Ichi [ndi] chonena chowona, ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, ayifuna ntchito yabwino.
  6590. 1Ti 3:2 Woyang’anira tsono akhale wopanda chifukwa chotsutsidwa nacho, mwamuna wa mkazi m’modzi, watcheru, wodziletsa, wa khalidwe labwino, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;
  6591. 1Ti 3:3 Wosati woledzera, kapena womenyana ndewu, wosapeza chuma mu njira zolakwika, komatu wopirira, wopanda mapokoso, wosasirira;
  6592. 1Ti 3:4 Amene aweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nawo ana ake wogonjera ndi kulemekeza konse;
  6593. 1Ti 3:5 (Pakuti ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasamalira bwanji mpingo wa Mulungu?)
  6594. 1Ti 3:6 Asakhale amene watembenuka mtima kumene, kuti podzitukumula ndi kunyada angagwe mu kutsutsa kwa mdiyerekezi.
  6595. 1Ti 3:7 Kuwonjezera apo ayeneranso kukhala ndi umboni wabwino kwa iwo amene ali kunja; kuti mwina ungamgwere mtonzo ndi msampha wa mdiyerekezi.
  6596. 1Ti 3:8 Momwemonso madikoni [ayenera akhale] wolemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, wosapeza chuma mu njira zolakwika;
  6597. 1Ti 3:9 Wosunga chinsinsi cha chikhulupiriro mu chikumbumtima chowona.
  6598. 1Ti 3:10 Ndipo iwowa ayambenso ayesedwa; kenako iwo atumikire mu udindo wa dikoni, akakhala [wopezeka] wopanda chifukwa chotsutsidwa nacho.
  6599. 1Ti 3:11 Momwemonso akazi [awo ayenera] akhale wolemekezeka, wosadiyerekeza, wodziletsa, wokhulupirika mu zinthu zonse.
  6600. 1Ti 3:12 Madikoni akhale amuna a mkazi m’modzi, woweruza bwino ana awo ndi nyumba za iwo wokha.
  6601. 1Ti 3:13 Pakuti amene iwo anagwiritsa ntchito bwino udindo wa dikoni adzitengera kwa iwo wokha mbiri yabwino ndi kulimbika kwakukulu m’chikhulupiriro chimene chili mwa Khristu Yesu.
  6602. 1Ti 3:14 Zinthu izi ndilembera kwa iwe, kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa:
  6603. 1Ti 3:15 Koma ngati ndichedwa, kuti ukhoze kudziwa momwe uyenera kukhalira m’nyumba ya Mulungu, imene ili mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa maziko a chowonadi.
  6604. 1Ti 3:16 Ndipo popanda chitsutsano chinsinsi cha umulungu n’chachikulu: Mulungu adawonekera m’thupi, adalungamitsidwa mu Mzimu, adapenyeka ndi angelo, adalalikidwa mwa Amitundu, adakhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
  6605. 1Ti 4:1 Tsopano Mzimu anena monenetsa, kuti m’nthawi zotsiriza ena adzachoka ku chikhulupiriro, kusamalira mizimu yokopa, ndi ziphunzitso za ziwanda;
  6606. 1Ti 4:2 Kulankhula mabodza m’chinyengo; kukhala ndi chikumbumtima chawo chowotchedwa monga ndi chitsulo chamoto;
  6607. 1Ti 4:3 Akuletsa kukwatira, [ndi kulamulira] kusiyitsa kudya nyama, zimene Mulungu wazilenga kuti azilandire ndi chiyamiko iwo amene akhulupirira ndi kudziwa chowonadi.
  6608. 1Ti 4:4 Pakuti cholengedwa chilichonse cha Mulungu [chili] chabwino, ndipo palibe choyenera kukanidwa, ngati chikhala cholandiridwa ndi chiyamiko:
  6609. 1Ti 4:5 Pakuti chiyeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.
  6610. 1Ti 4:6 Ngati ukumbutsa abale za zinthu izi, iwe udzakhala mtumiki wabwino wa Yesu Khristu, woleredwa bwino m’mawu a chikhulupiriro ndi chiphunzitso chabwino chimene iwe wachifikira.
  6611. 1Ti 4:7 Koma ukane nkhani zachabe ndi nthano za akazi okalamba, ndipo udzizoloweretse [maka] ku umulungu.
  6612. 1Ti 4:8 Pakuti masewera olimbitsa thupi apindula pang’ono: koma umulungu upindula ku zinthu zonse, pokhala nalo lonjezano la moyo uli tsopano, ndi la umene ulinkudza.
  6613. 1Ti 4:9 Ichi [ndi] chonena chokhulupirika ndi choyenera kulandiridwa konse.
  6614. 1Ti 4:10 Pakuti choncho tigwira ntchito ndi kulandira chitonzo, chifukwa tidalira mwa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa iwo amene akhulupirira.
  6615. 1Ti 4:11 ¶Zinthu izi lamulira ndi kuphunzitsa.
  6616. 1Ti 4:12 Usalole munthu apeputse unyamata wako; koma iwe khala chitsanzo kwa iwo wokhulupirira, m’mawu, m’makhalidwe, m’chikondi, mu mzimu, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.
  6617. 1Ti 4:13 Kufikira ndidza ine, udzipereke ku kuwerenga, ku kudandawulira, ku chiphunzitso.
  6618. 1Ti 4:14 Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, imene idapatsidwa kwa iwe mwa uneneri, ndi kuyika kwa manja a akulu [a mpingo].
  6619. 1Ti 4:15 Ulingalire pa zinthu izi; udzipereke wekha kwathunthu ku izo; kuti kupindula kwako kuwonekere kwa onse.
  6620. 1Ti 4:16 Udziyang’anire iwe mwini, ndi ku chiphunzitsocho; ukhalebe mu izi: pakuti pochita ichi iwe udzadzipulumutsa wekha, ndi iwo akumva iwe.
  6621. 1Ti 5:1 Wamkulu usamdzudzule, koma umdandawulire [iye] ngati atate; [ndi] abambo achichepere ngati abale;
  6622. 1Ti 5:2 Akazi akulu ngati amayi; aang’ono ngati alongo, ndi kuyera mtima konse.
  6623. 1Ti 5:3 Chitira ulemu amasiye amene ali a masiye ndithu.
  6624. 1Ti 5:4 Koma ngati mayi wamasiye wina ali nawo ana kapena zidzukulu, iwowa aphunzire kuyamba kuwonetsa chipembedzo kunyumba kwawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ndi chabwino ndi cholandirika pamaso pa Mulungu.
  6625. 1Ti 5:5 Tsopano iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, amadalira mwa Mulungu, nakhalabe m’mapembedzero ndi mapemphero usiku ndi usana.
  6626. 1Ti 5:6 Koma iye wakukhala m’zomkondweretsa adafa pamene ali ndi moyo.
  6627. 1Ti 5:7 Ndipo m’zinthu izi ulamulire kuti iwo akhoze kukhala wopanda chirema.
  6628. 1Ti 5:8 Koma ngati wina siakwaniritsa zosowa za iye mwini, makamaka iwo a m’banja lake, iye wakana chikhulupiriro, ndipo ali woyipa kuposa wosakhulupirira.
  6629. 1Ti 5:9 Asawerengedwe wamasiye ngati sadafike zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna m’modzi.
  6630. 1Ti 5:10 Wonenendwa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a woyera mtima, ngati adathandizapo wosawutsidwa, ngati adatsatadi mwakhama ntchito zonse zabwino.
  6631. 1Ti 5:11 Koma amasiye aang’ono uwakane; pakuti pamene zilakolako zawo ziwakokera kuchoka kwa Khristu, iwo afuna kukwatiwa;
  6632. 1Ti 5:12 Pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chawo choyamba.
  6633. 1Ti 5:13 Ndiponso iwo aphunzira [kukhala] aulesi, oyendayenda kuchokera ku nyumba ina kupita ku nyumba ina; koma wosati ulesi kokha, komanso otanganidwa ndi zokondweretsa thupi, woyankhula zosayenera.
  6634. 1Ti 5:14 Choncho ine ndifuna amayi aang’ono akwatiwe, abale ana, atsogolere nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulankhula monyoza.
  6635. 1Ti 5:15 Pakuti ena apatuka kale kumbali kutsata Satana.
  6636. 1Ti 5:16 Ngati pali mwamuna kapena mkazi amene akhulupirira ali nawo amasiye, iwo awathandize iwo, ndipo mpingo usalemetsedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.
  6637. 1Ti 5:17 ¶Akulu a amene aweruza bwino awerengedwe woyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akugwira ntchito m’mawu ndi m’chiphunzitso.
  6638. 1Ti 5:18 Pakuti malembo anena, Iwe usapunamize ng’ombe imene imapuntha tirigu. Ndipo, Wogwira ntchito [ali] woyenera mphotho yake.
  6639. 1Ti 5:19 Pa chotsutsa wamkulu usalandire chom’nenezera, koma pamaso pa mboni ziwiri kapena zitatu.
  6640. 1Ti 5:20 Iwo amene achimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti ena akhoze kuchitanso mantha.
  6641. 1Ti 5:21 Ine ndikulamulira [iwe] pamaso pa Mulungu, ndi Ambuye Yesu Khristu, ndi angelo wosankhidwa, kuti iwe usunge zinthu izi kopanda kusiyanitsa m’modzi pamaso pa wina, wosachita kanthu mwa tsankhu.
  6642. 1Ti 5:22 Usafulumira kuyika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nawo machimo a anthu ena: udzisunge wekha woyera mtima.
  6643. 1Ti 5:23 Usakhalenso wakumwanso madzi, koma ugwiritse ntchito vinyo wochepa chifukwa cha m’mimba mwako ndi kudwala kwako kobwera kawirikawiri.
  6644. 1Ti 5:24 Machimo a anthu ena ali owoneka kale, atsogola kumka ku chiweruzo; ndipo [anthu] enanso ziwatsata.
  6645. 1Ti 5:25 Momwemonso ntchito zabwino [za ena] zawonekera kale; ndipo zina zimene zosati zotere sizikhoza kubisika.
  6646. 1Ti 6:1 Mulole onse ambiri amene ali antchito monga ali pansi pa goli awerenge ambuye a iwo wokha woyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso [chake] zisachitidwe mwano.
  6647. 1Ti 6:2 Ndipo iwo akukhala nawo ambuye wokhulupirira, asawapeputse [iwo] popeza ali abale; koma makamaka awatumikire [iwo], popeza ali wokhulupirika ndi wokondedwa, woyanjana nawo pa chothandizacho. Zinthu izi uziphunzitse ndi kudandawulira.
  6648. 1Ti 6:3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nawo mawu otukula moyo, [ngakhale] mawu a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kwa chiphunzitso chili molingana ndi chipembedzo;
  6649. 1Ti 6:4 Iye ali wodzitukumula, wosadziwa kanthu, koma wokonda za mafunso ndi makani a mawu, kumene zichokerako kaduka, ndewu, chikhalidwe chamwano, mayerekezo woyipa,
  6650. 1Ti 6:5 Makani achilendo a anthu woyipsika maganizo, ndi wosowa chowonadi, akuyesa kuti kupindula chuma ndi umulungu: kwa otere udzipatule wekha.
  6651. 1Ti 6:6 Koma umulungu pamodzi ndi kukhutitsidwa zipindulitsa kwakukulu.
  6652. 1Ti 6:7 Pakuti sitidatenga kanthu polowa m’dziko [ili] lapansi, [ndiponso izi] ndizotsimikizika sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano.
  6653. 1Ti 6:8 Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.
  6654. 1Ti 6:9 Koma iwo amene adzakhala achuma agwa m’chiyesero ndi mu msampha, ndi [mu] zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zimene zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.
  6655. 1Ti 6:10 Pakuti chikondi cha pa ndalama ndiwo muzu wa choyipa chonse: chimene ena pochisirira, adalakwa kuchoka ku chikhulupiriro, nadzipyoza iwo eni kudzera mu zisoni zambiri.
  6656. 1Ti 6:11 ¶Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu izi; nutsate chilungamo, umulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.
  6657. 1Ti 6:12 Menya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira pa moyo wosatha, umene iwenso adakuyitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.
  6658. 1Ti 6:13 Ndikulamulira iwe pamaso pa Mulungu, amene apatsa zinthu zonse moyo, ndi [pamaso pa] Khristu Yesu, amene adachitira umboni chivomerezo chabwino pamaso pa Pontiyasi Pilato;
  6659. 1Ti 6:14 Kuti iwe usunge lamulo ili lopanda banga, lopanda chosavomerezeka, kufikira mawonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu:
  6660. 1Ti 6:15 Limene adzaliwonetsa m’nyengo za iye yekha, [amene ali] wodala ndi Mwini Mphamvu yekhayo, Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye;
  6661. 1Ti 6:16 Amene iye yekha ali nako kusafa, wakukhala m’kuwunika kosakhoza kufikako munthu; amene palibe munthu adamuwona, kapena akhoza kumuwona: kwa iye [kukhale] ulemu ndi mphamvu kwa muyaya. Amen.
  6662. 1Ti 6:17 Lamulira iwo amene ali a chuma m’dziko lapansi ili, kuti asakhale moyo wodzikweza, kapena asadalire chuma chosadziwika kukhala kwake, koma mwa Mulungu wamoyo, amene atipatsa ife molemera mu zinthu zonse kuti tikondwere;
  6663. 1Ti 6:18 Kuti iwo achite zabwino, kuti iwo alemere mu ntchito zabwino, okonzekera kugawira, wofuna kuyanjana;
  6664. 1Ti 6:19 Ndikudziyikira iwo wokha maziko abwino pokonzekera nyengo ikudzayi, kuti iwo akakhoze kugwira moyo wosatha.
  6665. 1Ti 6:20 Timoteyo; sunga chimene chayikizidwa ku chikhulupiriro chako, kupewa zokamba zopanda pake [ndi] zotsutsana, ndi zotsutsana za sayansi zomwe mwabodza zitchedwa [chidziwitso]:
  6666. 1Ti 6:21 Chimene ena pochivomereza, adalakwa mokhudzana ndi chikhulupiriro. Chisomo [chikhale] ndi iwe. Amen.
  6667. 2Ti 1:1 Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo mwa Khristu Yesu,
  6668. 2Ti 1:2 Kwa Timoteyo, mwana wanga wamwamuna wokondedwa: Chisomo, chifundo, [ndi] mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.
  6669. 2Ti 1:3 ¶Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo [anga] ndi chikumbumtima choyera, kuti kosalekeza ndikumbukira iwe m’mapemphero anga usiku ndi usana;
  6670. 2Ti 1:4 Kukhumba kwakukulu kofuna kuwona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndikhoze kudzadzidwa nacho chimwemwe;
  6671. 2Ti 1:5 Pamene ndikumbukira chikhulupiriro chako chosanamizira chili mwa iwe, chimene chidakhala poyamba mwa ambuye wako Loyisi, ndi mwa mayi wako Yunisi; ndipo ndakopeka mtima kuti [chili] mwa iwenso.
  6672. 2Ti 1:6 Mwa ichi ndikukumbutsa iwe kuti uyitakase mphatso ya Mulungu, imene ili mwa iwe ya mwa kuyika kwa manja kwanga.
  6673. 2Ti 1:7 Pakuti Mulungu sadatipatsa ife mzimu wa mantha; koma wa mphamvu, ndi chikondi, ndi woganiza bwino.
  6674. 2Ti 1:8 Potero tsono usachite manyazi ndi umboni wa Ambuye wathu, kapena ndi ine wandende wake: koma ukhale olandirana nawo masawutso a uthenga wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;
  6675. 2Ti 1:9 Amene watipulumutsa ife, ndi kutiyitana [ife] ndi mayitanidwe woyera, si monga mwa ntchito zathu, koma monga mwa cholinga cha iye yekha ndi chisomo, chimene chidapatsidwa kwa ife mwa Khristu Yesu lisadayambe dziko lapansi,
  6676. 2Ti 1:10 Koma ichi tsopano chawonetsedwa mwa kuwonekera kwa Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, amene wagonjetsa imfa, ndipo wabweretsa moyo ndi chosavunda ku kuwunika kudzera mu uthenga wabwino:
  6677. 2Ti 1:11 Ku umene ndasankhidwapo ine mlaliki, ndi mtumwi, ndi mphunzitsi wa Amitundu.
  6678. 2Ti 1:12 Chifukwa cha ichinso ndimva zowawa izi: komabe sindichita manyazi: pakuti ndidziwa iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndakopeka mtima kuti iye ndiwokwanitsa kusunga chimene ndadzipereka nacho kwa iye pokonzekera tsiku lijalo.
  6679. 2Ti 1:13 Gwira chitsanzo cha mawu omveka bwino, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.
  6680. 2Ti 1:14 Kuti chinthu chabwino chimene chidaperekedwa kwa iwe uchisunge mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.
  6681. 2Ti 1:15 Ichi iwe uchidziwa, kuti onse amene ali mu Asiya abwezedwa [kuchoka] kwa ine; a iwo amene ali Fugelasi ndi Hermagenesi.
  6682. 2Ti 1:16 Ambuye apereke chifundo kwa banja la Onesiforasi; pakuti adatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sadachita manyazi ndi unyolo wanga:
  6683. 2Ti 1:17 Koma, pamene iye adali ku Roma, iye adandifunafuna ine ndi khama, ndipo anandipeza [ine].
  6684. 2Ti 1:18 Ambuye ampatse iye kuti akhoze kupeza chifundo ndi Ambuye m’tsiku lijalo: ndi momwe m’zinthu zambiri iye adatumikira kwa ine mu Efeso, iwe uzindikira bwino lomwe.
  6685. 2Ti 2:1 Choncho iwe, mwana wanga wamwamuna, khala wolimbika m’chisomo chimene chili mwa Khristu Yesu.
  6686. 2Ti 2:2 Ndipo zinthu zimene wazimva kwa ine pakati pa mboni zambiri, zomwezi iwe uyikize kwa amuna wokhulupirika, amene adzatha kuphunzitsa enanso.
  6687. 2Ti 2:3 Choncho iwe upirire zowawa, monga msirikali wabwino wa Yesu Khristu.
  6688. 2Ti 2:4 Palibe munthu amene amenya nkhondo akodwa nazo zochitika za wamba za moyo [uwu]; kuti akhoze kukondweretsa iye amene adamsankha kuti akhale msirikali.
  6689. 2Ti 2:5 Ndipo ngatinso munthu ayesana nawo m’makani a masewero, [koma] iye savekedwa korona, pokhapo ngati adayesana monga mwa lamulo.
  6690. 2Ti 2:6 Wam’munda amene agwira ntchito ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo.
  6691. 2Ti 2:7 Lingalira chimene ine ndinena; ndipo Ambuye akupatsa iwe kumvetsa m’zinthu zonse.
  6692. 2Ti 2:8 Kumbukira kuti Yesu Khristu wa mbewu ya Davide, adawukitsidwa kwa akufa molingana ndi uthenga wabwino wanga:
  6693. 2Ti 2:9 M’mene ine ndimva mavuto a zowawa, monga wochita zoyipa, [ngakhale] mpaka ku unyolo; koma mawu a Mulungu samangidwa.
  6694. 2Ti 2:10 Mwa ichi ndipirira m’zinthu zonse chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutso chimene chili mwa Khristu Yesu pamodzi ndi ulemerero wosatha.
  6695. 2Ti 2:11 [Ndi] chonena chokhulupirika: Pakuti ngati tidamwalira ndi [iye], tidzakhalanso ndi moyo ndi iye:
  6696. 2Ti 2:12 Ngati tivutika, tidzachitanso ufumu ndi [iye]: ngati timkana [iye], iyeyunso adzatikana ife:
  6697. 2Ti 2:13 Ngati tikhala wosakhulupirira, [koma] iyeyu akhala wokhulupirika; iye sakhoza kudzikana yekha.
  6698. 2Ti 2:14 ¶Za zinthu izi uwakumbutse iwo, ndi kuwalamulira iwo pamaso pa Ambuye kuti asachite makani ku mawu wosapindulitsa kanthu, [koma] wogwetsa iwo akumva.
  6699. 2Ti 2:15 Phunzira kuti udziwonetsere wekha wovomerezeka kwa Mulungu, mwamuna wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wogawa molunjika nawo bwino mawu a chowonadi.
  6700. 2Ti 2:16 Koma pewa nkhani zosalemekeza chipembedzo ndi zopanda pake: pakuti adzachulukirabe kutsata zopanda umulungu.
  6701. 2Ti 2:17 Ndipo mawu awo adzadya monga [chironda cha] matenda a khansa; a iwo amene ali Humaneyasi ndi Filetasi;
  6702. 2Ti 2:18 Amene mokhudzana ndi chowonadi adalakwa, kunena kuti kuwuka kwa akufa kwachitika kale; ndi kuwononga chikhulupiriro cha ena.
  6703. 2Ti 2:19 Komatu maziko a Mulungu ayimikidwa mokhazikika, wokhala ndi chosindikizira ichi, Ambuye adziwa iwo amene ali ake. Ndipo, Aliyense wakutchula dzina la Khristu adzipatule ku choyipa.
  6704. 2Ti 2:20 Koma m’nyumba yayikulu si muli zotengera za golide ndi siliva zokha, komanso za mtengo ndi dothi; ndi zina za ku ulemu ndi zina ku zopanda ulemu.
  6705. 2Ti 2:21 Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha ku izi, adzakhala chotengera cha ku ulemu, chopatulika, ndi choyenera kuchigwiritsa ntchito mbuye, [ndi] chokonzekeretsedwa ku ntchito iliyonse yabwino.
  6706. 2Ti 2:22 Thawanso zilakolako za unyamata: koma utsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuyitana pa Ambuye ndi mtima woyera.
  6707. 2Ti 2:23 Koma mafunso wopusa ndi wosaphunzira upewe, podziwa kuti abala mikangano.
  6708. 2Ti 2:24 Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita mkangano; koma akhale woleza mtima kwa [anthu] onse wodziwa kuphunzitsa, wodekha,
  6709. 2Ti 2:25 Wolangiza iwo akudzitsutsa iwo mofatsa; kuti mwina Mulungu awapatse iwo kutembenuka [mtima] ku kuzindikira kwa chowonadi;
  6710. 2Ti 2:26 Ndi [kuti] iwo akakhoze kudzipulumutsa ku msampha wa mdiyerekezi, amene adagwidwa ndi iye ukapolo mwa chifuniro chake.
  6711. 2Ti 3:1 Ichi udziwenso, kuti m’masiku wotsiriza nthawi zowawitsa zidzafika.
  6712. 2Ti 3:2 Pakuti anthu adzakhala wodzikonda iwo wokha, wokonda ndalama, wodzitamandira, wodzikuza, amwano, wosamvera akuwabala, wosayamika, wosayera mtima,
  6713. 2Ti 3:3 Wopanda chikondi chachibadwidwe, wosayanjanitsika, wozenga milandu yabodza, wosakhoza kudziletsa, wochititsa mantha, wonyoza iwo amene ali abwino.
  6714. 2Ti 3:4 Wosagonjera, aliwuma, wodzitukumula [ndi wonyada], wokonda zokondweretsa koposa kukonda Mulungu;
  6715. 2Ti 3:5 Akukhala nawo mawonekedwe a umulungu, koma akukana mphamvu yake: kwa wotero udzipatule.
  6716. 2Ti 3:6 Pakuti a wotere ali iwo amene akwawira m’nyumba, nagwira akazi wopusa wolemetsedwa ndi machimo, wotengedwa ndi zilakolako za mitundumitundu,
  6717. 2Ti 3:7 Wophunzira nthawi zonse, ndipo sakhoza konse kufika ku chidziwitso cha chowonadi.
  6718. 2Ti 3:8 Tsopano monga momwe Yanes ndi Yambres adatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho chowonadi: anthu wovunda malingaliro, wosavomerezedwa mokhudzana ndi chikhulupiriro.
  6719. 2Ti 3:9 Koma sadzapitirirapo: pakuti kupusa kwawo kudzawonekera kwa [anthu] onse, monga kwawonso kunali.
  6720. 2Ti 3:10 Koma iwe wadziwa kwathunthu chiphunzitso changa, makhalidwe a moyo, cholinga, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro.
  6721. 2Ti 3:11 Mazunzo, kumva zowawa, zotere zonga adandichitira mu Antiyoki, mu Ikoniyamu, mu Lustra; mazunzo wotani amene ine ndawamva: koma mu onsewo Ambuye adandilanditsa ine.
  6722. 2Ti 3:12 Inde, ndi onse akufuna kukhala m’moyo wa umulungu mwa Khristu Yesu adzamva mazunzo.
  6723. 2Ti 3:13 Koma anthu woyipa ndi wonyenga adzayipirayipirabe, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.
  6724. 2Ti 3:14 Koma ukhalebe iwe mu zinthu zimene waziphunzira ndi zimene watsimikizika mtima nazo, podziwa amene iwe waziphunzirako [izo];
  6725. 2Ti 3:15 Ndi kuti kuyambira uli mwana iwe wadziwa malembo woyera, amene ali wokhoza kukupatsa iwe nzeru kufikira chipulumutso kudzera m’chikhulupriro cha mwa Khristu Yesu.
  6726. 2Ti 3:16 Malemba onse [ali] operekedwa mwa kuwuziridwa kwa Mulungu, ndipo [ali] opindulitsa pa chiphunzitso, pa chitsutsano, pa kukonza zolakwika, pa malangizo mu chilungamo:
  6727. 2Ti 3:17 Kuti munthu wa Mulungu akhoze kukhala wangwiro, wokonzeka kwathunthu ku kuchita ntchito zonse zabwino.
  6728. 2Ti 4:1 Choncho ndikulamulira [iwe] pamaso pa Mulungu, ndi Ambuye Yesu Khristu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa pa kuwoneka kwake ndi ufumu wake;
  6729. 2Ti 4:2 Lalikira mawu; khala wachangu pa nyengo yake, pamene isali nyengo yake; tsutsa, dzudzula, dandawulira ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.
  6730. 2Ti 4:3 Pakuti idzafika nthawi imene sadzapirira chiphunzitso cholamitsa; komatu potsata zilakolako za iwo wokha iwo adzadziwunjikira iwo eni aphunzitsi, pokhala nawo makutu oyabwa.
  6731. 2Ti 4:4 Ndipo adzatembenuza makutu [awo] kuchoka ku chowonadi, ndipo adzapatukira ku nthano.
  6732. 2Ti 4:5 Koma iwe khala maso m’zinthu zonse, imva zowawa, gwira ntchito ya mlaliki, chita chitsimikizo chathunthu cha utumiki wako.
  6733. 2Ti 4:6 Pakuti tsopano ndiri wokonzeka kuperekedwa, ndipo nthawi yakunyamuka kwanga yayandikira.
  6734. 2Ti 4:7 Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza njira [yanga], ndasunga chikhulupiriro:
  6735. 2Ti 4:8 Kuyambira tsopano kupita mtsogolo payikidwira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, koma kwa iwo onse amenenso adakonda kuwonekera kwake.
  6736. 2Ti 4:9 ¶Chita khama lako kuti udze kwa ine msanga:
  6737. 2Ti 4:10 Pakuti Demasi wandisiya ine, atakonda dziko latsopano lapansi ili, ndipo wanyamuka kupita ku Tesalonika; Kreseni ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.
  6738. 2Ti 4:11 Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Mariko, nudze naye pamodzi ndi iwe: pakuti ali wopindulitsa kwa ine ku utumiki.
  6739. 2Ti 4:12 Ndipo Tichikasi ine ndamtuma ku Efeso.
  6740. 2Ti 4:13 Chovala [cha pamwamba] chimene ndidachisiya ku Trowasi kwa Karpasi, pamene udza iwe, uchibweretse [nawe pamodzi], ndi mabuku, [koma] makamaka zikopa zija zolembedwapo.
  6741. 2Ti 4:14 Alekizanda wosula mkuwa adandichitira zoyipa zambiri: Ambuye ampatse iye mphotho molingana ndi ntchito zake:
  6742. 2Ti 4:15 Ameneyo iwenso uchenjere naye; pakuti adatsutsana nawo mawu athu kwakukulu.
  6743. 2Ti 4:16 Pa choyankha changa choyamba padalibe munthu m’modzi adayima ndi ine, koma [anthu] onse adandisiya: [Ine ndipemphera Mulungu] kuti chisakhoze kuyikidwa ku mlandu wawo.
  6744. 2Ti 4:17 Koma Ambuye adayima ndi ine, ndipo anandilimbikitsa; kuti kudzera mwa ine kulalikira kukhoze kudziwika kwathunthu, ndi [kuti] Amitundu onse akhoze kumva: ndipo ndidalanditsidwa m’kamwa mwa mkango.
  6745. 2Ti 4:18 Ndipo Ambuye adzandilanditsa ine ku ntchito yonse yoyipa, ndipo adzandisunga [ine] kulowa ufumu wake wa kumwamba: kwa iye [ukhale] ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.
  6746. 2Ti 4:19 Upatse moni Priska ndi Akwila, ndi banja la Onesiforasi.
  6747. 2Ti 4:20 Erastasi adakhalira ku Korinto: koma Trofimasi ine ndamsiya wodwala ku Miletamu.
  6748. 2Ti 4:21 Chita khama lako kudza isanadze nyengo yozizira. Eubulo akukupatsa moni iwe, ndi Puden, ndi Linasi, ndi Klaudiya, ndi abale onse.
  6749. 2Ti 4:22 Ambuye Yesu Khristu [akhale] ndi mzimu wako. Chisomo [chikhale] ndi iwe. Amen.
  6750. Tit 1:1 Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, malingana ndi chikhulupiriro cha wosankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha chowonadi chomwe chili motsata umulungu;
  6751. Tit 1:2 Mu chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, amene sanganame, adalonjeza lisadakhale dziko lapansi;
  6752. Tit 1:3 Koma panyengo zoyikika adawonetsa mawu ake kudzera mu kulalikira, amene adandisungitsa ine malingana ndi lamulo la Mulungu Mpulumutsi wathu;
  6753. Tit 1:4 Kwa Tito, mwana [wanga] wamwamuna kutsata chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo, chifundo, [ndi] mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu Mpulumutsi wathu.
  6754. Tit 1:5 ¶Chifukwa cha ichi ine ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zinthu zimene zinali zosowa, ndi kuyika akulu mu mzinda uliwonse, monga ndidakusankha iwe:
  6755. Tit 1:6 Ngati wina ali wopanda chifukwa chotsutsidwa nacho, mwamuna wa mkazi m’modzi, wokhala nawo ana wokhulupirika wosanenezedwa za kukhala moyo wosalabadira zotsatira kapena wosamvera malamulo.
  6756. Tit 1:7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chifukwa chotsutsidwa nacho, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliwuma, wosapsa mtima msanga, wosayandikira ku vinyo, wosachita chiwawa, wosati wopeza chuma mu njira zolakwika.
  6757. Tit 1:8 Koma wokonda kuchereza alendo, wokonda anthu abwino, wodekha, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;
  6758. Tit 1:9 Wogwiritsitsa mawu wokhulupirika monga waphunzitsidwa, kuti akhoze kukhala nako kuthekera mwa chiphunzitso cholamitsa kuti alimbikitse ndi kutsutsa wotsutsana naye.
  6759. Tit 1:10 Pakuti alipo ambiri wosamvera malamulo woyankhula zopanda pake ndi wonyenga, makamaka iwo a ku mdulidwe:
  6760. Tit 1:11 Amene pakamwa pawo payenera kutsekedwa, amene apasula mabanja athunthu, kuphunzitsa zinthu zimene sayenera kutero, chifukwa cha kufuna kupeza chuma mu njira zonyansa.
  6761. Tit 1:12 Wina wa iwo eni, [ndiye] mneneri wa iwo wokha, adati, Akrete [ali] abodza nthawi zonse, zirombo zoyipa, wokonda kudya kwambiri.
  6762. Tit 1:13 Uwu uli umboni wowona. Chifukwa cha ichi uwadzudzule kolimba, kuti akakhale wolama m’chikhulupiriro;
  6763. Tit 1:14 Osasamala nthano za Chiyuda, ndi malamulo a wathu, amene apatuka kusiyana nacho chowonadi.
  6764. Tit 1:15 Kwa woyera mtima zonse [ziri] zoyera: koma mwa iwo wodetsedwa ndi wosakhulupirira kulibe [kanthu] koyera; koma ngakhale malingaliro awo ndi chikumnbumtima chawo chili chodetsedwa.
  6765. Tit 1:16 Iwo amavomeneza kuti iwo adziwa Mulungu; koma ndi ntchito amkana [iye], pokhala wonyanzitsa, ndi wosamvera, ndipo ku ntchito zonse zabwino wosavomerezeka.
  6766. Tit 2:1 Koma iwe yankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa:
  6767. Tit 2:2 Kuti wokalamba akhale watcheru, wolemekezeka, wodziletsa, wolama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro.
  6768. Tit 2:3 Momwemonso akazi wokalamba, kuti [akhale] m’makhalidwe woyenera chiyero, wosati wozenga milandu yabodza, wosamwetsa vinyo, aphunzitsi a zinthu zokoma.
  6769. Tit 2:4 Kuti akhoze kuphunzitsa akazi aang’ono kuti akhale wosaledzera, akonde amuna awo, akonde ana awo,
  6770. Tit 2:5 [Kuti akhale] oganiza bwino, angwiro, wosunga a kunyumba, abwino, akumvera amuna a iwo okha, kuti mawu a Mulungu angalankhulidwe zamwano.
  6771. Tit 2:6 Momwemonso anyamata uwadandawulire akhale a malingaliro wodziletsa.
  6772. Tit 2:7 Mzinthu zonse udziwonetsere iwe wekha chitsanzo cha ntchito zabwino: m’chiphunzitso [kuwonetsera] chosavunda, ulemekezeko, owona mtima.
  6773. Tit 2:8 Mawu olama, amene sangatsutsidwe; kuti iye amene ali mbali yakutsutsana nawe akhoze kuchita manyazi, posakhala nako kanthu koyipa kunenera inu.
  6774. Tit 2:9 [Uwadandawulire] antchito kuti akhale omvera ambuye awo a iwo wokha, [ndi] kuwakondweretsa [iwo] mu [zinthu] zonse; wosawayankhanso;
  6775. Tit 2:10 Wosaba, koma kuwonetsa kukhulupirira konse kwabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mulungu Mpulumutsi wathu mu zinthu zonse.
  6776. Tit 2:11 ¶Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chibweretsa chipulumutso chawonekera kwa anthu onse.
  6777. Tit 2:12 Kutiphunzitsa ife kuti, pokana kusapembedza ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino wodziletsa, mwachilungamo, ndi wopembedza, mu dziko lapansi la panoli;
  6778. Tit 2:13 Kulindirira chiyembekezo chodala chimenecho, ndi mawonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Khristu Yesu;
  6779. Tit 2:14 Amene anadzipereka yekha m’malo mwa ife, kuti akakhoze kutiwombola ife ku zoyipa zonse, nakadziyeretsere kwa iye yekha anthu akhale ake apaderadera, achangu pa ntchito zabwino.
  6780. Tit 2:15 Zinthu izi yankhula, ndipo udandawulire, ndi kudzudzula ndi ulamuliro wonse. Usalole munthu akupeputse iwe.
  6781. Tit 3:1 Uwakumbutse iwo agonjere ku maufumu ndi maulamuliro, amvere woweruza, kukhala okonzeka ku ntchito iliyonse yabwino,
  6782. Tit 3:2 Asalankhule zoyipa za munthu aliyense, asakhale a ndewu, [koma] akhale odekha, nawonetsere chifatso chonse kwa anthu onse.
  6783. Tit 3:3 Pakuti ifenso tidali nthawi zina [kale] opusa, osamvera, wonyengedwa, otumikira zilakolako zamitundimitundu ndi zokondweretsa, wokhala m’moyo wa malingaliro ofuna kuchitira ena zoyipa ndi kaduka, a udani, [ndi] wodana wina ndi mzake.
  6784. Tit 3:4 Koma zitapita izo kukoma mtima, ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu cha kwa anthu chidawonekera,
  6785. Tit 3:5 Zosati zochokera m’ntchito za chilungamo zimene ife tachita, koma monga mwa chifundo chake adatipulumutsa ife, mwakutsuka kwa kubadwanso, ndi makonzedwe atsopano a Mzimu Woyera;
  6786. Tit 3:6 Amene iye adatsanulira pa ife mochulukira kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu;
  6787. Tit 3:7 Kuti pokhala wolungamitsidwa ndi chisomo cha iye, ife tipangidwe wolandira cholowa malingana ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.
  6788. Tit 3:8 ¶[Ichi ndi] chonena chokhulupirika, ndipo zinthu izi ndifuna iwe ulimbitse mawu pafupipafupi, kuti iwo amene adakhulupirira mwa Mulungu akhoze kusamalitsa kukhalabe ochita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zokoma ndi zopindulitsa kwa anthu.
  6789. Tit 3:9 Koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndewu, ndi makani a pamalamulo; pakuti ziri zosapindulitsa ndi zachabe.
  6790. Tit 3:10 Munthu amene ali wokana chowona nakhulupirira chiphunzitso chabodza, atachenjezedwa koyamba ndi kachiwiri akanidwe;
  6791. Tit 3:11 Podziwa kuti iye amene ali woteroyo wakhotetsedwa, ndipo achimwa, wodzitsutsa iye mwini yekha.
  6792. Tit 3:12 Pamene ndidzatuma Artemasi kwa iwe, kapena Tichikasi, chita changu kudza kwa ine ku Nikopolisi: pakuti ndatsimikiza mtima kukhala kumeneko nyengo yozizira.
  6793. Tit 3:13 Bweretsani Zenasi woyimirira milandu ndi Apolos pa ulendo wawo mwachangu, kuti pasakhale kanthu kosowa kwa iwo.
  6794. Tit 3:14 Ndipo mulole athunso aphunzire kusunga ntchito zabwino kuzichitira pa zofunikira, kuti iwo asakhale wosabala zipatso.
  6795. Tit 3:15 Wonse amene ali ndi ine akupatsani moni. Apatseni moni iwo amene atikonda ife mu chikhulupiriro. Chisomo [chikhale] ndi inu nonse. Amen.
  6796. Phm 1:1 Paulo wandende wa Yesu Khristu, ndi Timoteyo mbale [wathu], kwa Filimoni wokondedwa kwambiri, ndi wantchito mzathu,
  6797. Phm 1:2 Ndi kwa Apiya wokondedwa [wathu], ndi Arkipasi msirikali mzathu, ndi kwa mpingo uli m’nyumba yako:
  6798. Phm 1:3 Chisomo kwa inu, ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.
  6799. Phm 1:4 Ndiyamika Mulungu wanga, kutchula iwe nthawi zonse m’mapemphero anga,
  6800. Phm 1:5 Pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro, uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa woyera mtima onse;
  6801. Phm 1:6 Kuti chiyanjano cha chikhulupiriro chako chikhale chakukwaniritsa cholinga mwa kuvomereza kwa chabwino chilichonse chili mwa inu mwa Khristu Yesu.
  6802. Phm 1:7 Pakuti tiri nacho chimwemwe chachikulu ndi chisangalatso pa chikondi chako, chifukwa mitima ya woyera mtima yatonthozedwa mwa iwe, mbale.
  6803. Phm 1:8 ¶Mwa ichi, ndingakhale ndikhoza kulimbika mtima kwakukulu mwa Khristu kukulamulira iwe chimene chili choyenera.
  6804. Phm 1:9 Koma makamaka chifukwa cha chikondi ndidandawulira [iwe], pokhala m’modzi wotere monga Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Yesu Khristu.
  6805. Phm 1:10 Ndikudandawulira iwe chifukwa cha mwana wanga Onesimasi, amene ndam’bala m’ndende:
  6806. Phm 1:11 Amene kale anali kwa iwe wosakupindulira, koma tsopano wopindula kwa iwe ndi ine:
  6807. Phm 1:12 Amene ine ndamtumanso, choncho iwe umulandire iye, ichi ndi, chikondi changa:
  6808. Phm 1:13 Amene ndikadatha kukhala naye, kuti m’malo mwako akadanditumikira ine m’ndende za uthenga wabwino:
  6809. Phm 1:14 Koma wopanda kudziwa mtima wako sindidafuna kuchita kanthu; kuti kupindula kwako kusakhale monga kunali mokakamiza, komatu mwakufuna.
  6810. Phm 1:15 Pakuti kapena adachoka kwa nyengo, ndi kuti udzamulandire iye kwa nthawi zonse;
  6811. Phm 1:16 Osatinso tsopano monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka kwa ine, koma nanga koposa kotani kwa iwe, m’thupi, ndi mwa Ambuye?
  6812. Phm 1:17 Ngati tsono undiyesa ine woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.
  6813. Phm 1:18 Koma ngati adakulakwira iwe, kapena kungongola [iwe] kanthu, undiwerengere ine kameneko;
  6814. Phm 1:19 Ine Paulo, ndalemba [iyi] ndi dzanja langa langa, ndidzabwezera ine: ngakhale kuti sindinena nawe iwe za momwe uli wamangawa wanga ngakhale osatchula za iwe mwini.
  6815. Phm 1:20 Inde, mbale, ndilole ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Ambuye.
  6816. Phm 1:21 Pokhala ndi kulimbika mtima ndi kumvera kwako ndidakulembera iwe, podziwa kuti iwe udzachitanso koposa chimene ine ndinena.
  6817. Phm 1:22 Koma ndi zonsezo undikonzerenso pogona: pakuti ndikhulupirira kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.
  6818. Phm 1:23 Akupatsani moni Epafrasi, wandende mzanga mwa Khristu Yesu;
  6819. Phm 1:24 Markasi, Aristarkasi, Demas, Lukasi, antchito anzanga.
  6820. Phm 1:25 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu [chikhale] ndi mzimu wako. Amen.
  6821. Heb 1:1 Mulungu, amene mu nthawi zosiyansiyana ndi m’njira zosiyanasiyana adayankhula mu nthawi zakale kwa atate mwa aneneri,
  6822. Heb 1:2 Walankhula m’masiku ano otsiriza kwa ife mwa Mwana [wake] wamwamuna, amene iye adamuyika wolandira cholowa wa zinthu zonse, amene mwa iyenso adalenga mayiko;
  6823. Heb 1:3 Ameneyo pokhala ali chonyezimira cha ulemerero [wake], ndi chizindikiro chenicheni cha iye [mwini], nanyamula zonse ndi mawu a mphamvu yake, m’mene adachita chiyeretso mwa iye yekha cha machimo athu, adakhala padzanja lamanja la Ukulu m’mwamba;
  6824. Heb 1:4 Atapangidwa kukhala wakuposa angelo, monga momwe iye adalandira mwa cholowa dzina lakuposa iwo.
  6825. Heb 1:5 Pakuti ndi kwa uti mwa angelo adati nthawi iliyonse, Iwe ndiwe mwana wanga wamwamuna, tsiku la lero ndakubala iwe? Ndiponso ine ndidzakhala kwa iye Atate, Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana wamwamuna?
  6826. Heb 1:6 Ndiponso, pamene abweretsa wobadwa woyamba kulowa naye m’dziko, iye anena, Ndipo angelo onse a Mulungu amlambire iye.
  6827. Heb 1:7 Ndipo za angelo anena, Amene apanga angelo ake mizimu, ndi atumiki ake akhale lawi la moto.
  6828. Heb 1:8 Koma ponena za Mwana wamwamuna, [iye ati], Mpando wachifumu wanu, Mulungu, [uli] wa nthawi za nthawi: ndipo ndodo yachifumu yachilungamo [ndiyo] ndodo ya ufumu wanu.
  6829. Heb 1:9 Inu mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choyipa; choncho Mulungu, [amene] ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero pamwamba pa anzanu.
  6830. Heb 1:10 Ndipo, Inu, Ambuye, pachiyambi mudayika maziko ake a dziko lapansi; ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu:
  6831. Heb 1:11 Iwo adzawonongeka; koma inu mutsala; ndipo iwo wonse adzasuluka monga chichitira chovala;
  6832. Heb 1:12 Ndipo monga chovala inu mudzawapinda iwo, ndipo iwo adzasinthika: koma inu muli chimodzimodzi, ndipo zaka zanu sizidzatha.
  6833. Heb 1:13 Koma ndi kwa uti wa angelo, adati pa nthawi ina iliyonse, Khala pa dzanja lamanja langa, kufikira ine nditayika adani ako popondera pa mapazi ako?
  6834. Heb 1:14 Kodi si ali iwo onse mizimu yotumikira, kutumidwa kukatumikira kwa iwo amene adzakhala wolandira cholowa cha chipulumutso?
  6835. Heb 2:1 Choncho tiyenera kusamalira zinthu zimene tazimva, kuti kapena pa nthawi ina iliyonse tingazilole izo [kutayika].
  6836. Heb 2:2 Pakuti ngati mawu amene adayankhulidwa ndi angelo adakhala wokhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chidalandira mphotho yobwezera yolungama;
  6837. Heb 2:3 Kodi tidzapulumuka bwanji ife, ngati sitisamala chipulumutso chachikulu chotere; Chimene poyamba Ambuye ndiwo adayamba kuchiyankhula, ndipo chidatsimikizidwa kwa ife ndi iwo amene adamumva [iye];
  6838. Heb 2:4 Powachitira umboni [iwo] Mulungu, ndi zizindikiro ndi zodabwitsa, ndi zozizwa za mitundumitundu, ndi mphatso za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake?
  6839. Heb 2:5 Pakuti sadagonjetsera angelo dziko lirinkudza, limene tilankhula za ilo.
  6840. Heb 2:6 Koma wina adachita umboni pamalo ena nati, Munthu ndi ndani, kuti mumkumbukira iye? Kapena mwana wamwamuna wa munthu kuti mumuyendera iye?
  6841. Heb 2:7 Inu mudampanga wochepa pang’ono koposa angelo; inu mumveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuyika iye woyang’anira ntchito za manja anu:
  6842. Heb 2:8 Inu mwayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake. Pakutero kuti iye adayika zinthu zonse pansi pa iye, iye sadasiye kanthu [kamene kali] kosayikidwa pansi pa iye. Koma tsopano sitiwona zinthu zonse zimgonjera iye.
  6843. Heb 2:9 Koma tiwona Yesu, amene adamchepetsa pang’ono ndi angelo chifukwa cha zowawa za imfa, wovekedwa korona wa ulemerero ndi ulemu; kuti iye mwa chisomo cha Mulungu alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.
  6844. Heb 2:10 Pakuti chidasanduka iye, amene kwa iye [ziri] zinthu zonse, ndipo mwa iye ziri zinthu zonse, pobweretsa ana amuna ambiri alowe mu ulemerero, kupanga mtsogoleri wa chipulumutso chawo wangwiro kudzera mu zowawa,
  6845. Heb 2:11 Pakuti onse awiri iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa [ali] mwa m’modzi: pa chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.
  6846. Heb 2:12 Kunena, ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, m’kati mwa mpingo ndidzayimba matamando kwa inu.
  6847. Heb 2:13 Ndiponso, ndidzayika kudalira kwanga mwa iye. Ndiponso, tawonani ine ndi ana amene Mulungu wandipatsa ine.
  6848. Heb 2:14 Powona kuti monga ana ali olandirana nawo a thupi ndi mwazi, iyenso momwemo adatenga nawo makhalidwe omwewo; kuti kudzera mwa imfa akakhoze kumuwononga iye amene adali nayo mphamvu ya imfa, ameneyo ndiye, mdiyerekezi;
  6849. Heb 2:15 Ndipo adawombola iwo amene kudzera m’mantha a imfa anali onse m’moyo wawo wonse pansi pa ukapolo.
  6850. Heb 2:16 Pakuti ndithudi iye sadatenge pa iye [chilengedwe cha] angelo; koma iye adatenga pa [iye] mbewu ya Abrahamu.
  6851. Heb 2:17 Mwa ichi mu zinthu zonse kudali koyenera iye kuti afanizidwe ndi abale [ake], kuti akhoze kukhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu [za] kwa Mulungu, kukapanga chiyanjanitso chifukwa cha uchimo wa anthu.
  6852. Heb 2:18 Pakuti mwa ichi kuti popeza iye mwini yekha wamva zowawa poyesedwa, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.
  6853. Heb 3:1 Mwa ichi, abale woyera mtima, wolandirana nawo mayitanidwe akumwamba, lingalirani za Mtumwi ndi Mkulu wansembe wa chivomerezo chathu, Khristu Yesu;
  6854. Heb 3:2 Amene adali wokhulupirika kwa iye adamuyikayo, monganso Mose [anali wokhulupirika] m’nyumba yake yonse.
  6855. Heb 3:3 Pakuti, [munthu] ameneyu anayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga iye amene amanga nyumba ali ndi ulemu woposa nyumbayo.
  6856. Heb 3:4 Pakuti nyumba iliyonse idamangidwa ndi [munthu] wina; koma iye amene adamanga zonse [ndiye Mulungu].
  6857. Heb 3:5 Ndipo Mosetu ndithudi [adali] wokhulupirika m’nyumba yake yonse, monga wantchito, kuchitira umboni wa zinthuzo zimene zidzayankhulidwa mtsogolo;
  6858. Heb 3:6 Koma Khristu monga Mwana wamwamuna wosunga nyumba yake; amene nyumba yake ndife, ngati tigwiritsa chitsimikizo ndi chimwemwe cha chiyembekezo kuchigwira mpaka kumapeto.
  6859. Heb 3:7 Mwa ichi, (monga anena Mzimu Woyera, lero ngati mudzamva mawu ake,
  6860. Heb 3:8 Musawumitse mitima yanu, monga mu kuwawitsa mtima, mtsiku la mayesero m’chipululu:
  6861. Heb 3:9 Pamene makolo anu adandiyesa ine, ndikundivomereza ine, ndikuwona nthito zanga zaka makumi anayi.
  6862. Heb 3:10 Mwa ichi ndidakwiya nawo m’badwo umenewo, ndipo ndidati, Nthawi zonse amalakwa m’mitima [yawo]; ndipo sadadziwe njira zanga.
  6863. Heb 3:11 Chotero ine ndilumbira mu ukali wanga, Sadzalowa mu mpumulo wanga.)
  6864. Heb 3:12 Samalirani, abale, kuti kapena mungakhale mwa wina aliyense wa inu mtima woyipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.
  6865. Heb 3:13 Koma limbikitsanani wina ndi mzake tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa Lero; kuti mwina wina wa inu angawumitsidwe ndi chenjerero la uchimo.
  6866. Heb 3:14 ¶Pakuti tapangidwa ife wolandira wa Khristu, ngatitu tigwiritsitsa chiyambi cha chitsimikizo chathu kuchigwira mpaka kumapeto;
  6867. Heb 3:15 Pamene kwanenedwa, Lero ngati mudzamva mawu ake, musawumitse mitima yanu, monga mu kuwukira.
  6868. Heb 3:16 Pakuti ena pamene adamva, adawawitsa mtima: komatu si onse aja adatuluka mu Igupto ndi Mose.
  6869. Heb 3:17 Koma ndi ayani adakwiya nawo zaka makumi anayi? [Kodi si] iwo amene adachimwa aja, amene mitembo yawo idagwa m’chipululu?
  6870. Heb 3:18 Ndipo ndi ayani adawalumbirira iye kuti asalowe mpumulo wake, koma kwa iwo amene sadakhulupirire?
  6871. Heb 3:19 Chotero tiwona kuti sadakhoza kulowa umo chifukwa cha kusakhulupirira.
  6872. Heb 4:1 Choncho tiyeni tikhale ndi mantha, kuti, kapena, lonjezano lidasiyidwira [ife] lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angawoneke ngati kuti adaperewera ku ilo.
  6873. Heb 4:2 Pakuti kwa ifenso udalalikidwa uthenga wabwino, monganso kwa iwo: koma mawu wolalikidwawo sadapindula nawo iwowa posasanganizidwa ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva [iwo].
  6874. Heb 4:3 Pakuti ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga iye adanena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mu mpumulo wanga: ngakhale kuti ntchitozo zidatsirizika kuyambira ku maziko a dziko lapansi.
  6875. Heb 4:4 Pakuti iye adanena pa malo ena za [tsiku] lachisanu ndi chiwiri moteromo, Ndipo Mulungu adapumula tsiku la chisanu ndi chiwiri, ku ntchito zake zonse.
  6876. Heb 4:5 Ndipo pa [malo] awanso, Ngati iwo adzalowa mpumulo wanga.
  6877. Heb 4:6 Powona pamenepo choncho kuti patsaladi kuti ena alowe m’menemo, ndi iwo amene uthenga wabwino udalalikidwa koyamba kwa iwo sadalowamo chifukwa cha kusakhulupirira:
  6878. Heb 4:7 Kenanso, ayika malire tsiku lina lake, kunena mwa Davide, Lero, itapita nthawi yayikulu yakuti, monga kwanenedwa, Lero ngati mudzamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.
  6879. Heb 4:8 Pakuti ngati Yesu adawapatsa iwo mpumulo, kodi kenaka patsogolo pake sakadayankhulanso za tsiku lina.
  6880. Heb 4:9 Choncho patsalira mpumulo kwa anthu a Mulungu.
  6881. Heb 4:10 Pakuti iye amene walowa mpumulo wake, wapumulanso mwini ku ntchito zake, monganso Mulungu [anachita] ku zake za iye.
  6882. Heb 4:11 Choncho tichite khama kuti tilowe mpumulo umenewo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwechi cha kusakhulupirira.
  6883. Heb 4:12 Pakuti mawu a Mulungu [ali] a moyo, ndi a mphamvu, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa mbali [zonse] ziwiri, nabowola [mopyoza] ngakhale kufikira kugawa pakati moyo ndi mzimu, ndi a zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, ndipo [ali] ozindikira zolingalira ndi zofuna za mtima.
  6884. Heb 4:13 Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake: koma zonse [ziri] pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pa iye amene tichita naye.
  6885. Heb 4:14 ¶Powona kuti tsono tiri naye mkulu wansembe wamkulu, amene wapyoza kulowa miyamba, Yesu Mwana wamwamuna wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo [chathu].
  6886. Heb 4:15 Pakuti si tiri naye mkulu wansembe amene sangathe kukhudzidwa ndi zofoka zathu; koma m’njira zonse anayesedwa monga ife, [komatu] wopanda uchimo.
  6887. Heb 4:16 Choncho tiyeni tilimbe mtima kubwera ku mpando wachifumu wachisomo, kuti tikalandire chifundo, ndi kupeza chisomo chakutithandiza m’nthawi yakusowa.
  6888. Heb 5:1 Pakuti mkulu wansembe aliyense wotengedwa pakati pa anthu amayikidwa chifukwa cha anthu m’zinthu [za] kwa Mulungu, kuti akhoze kupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo:
  6889. Heb 5:2 Amene akhoza kumva chifundo pa wosadziwa ndi iwo amene achoka panjira; popeza iye yekhanso amazingidwa ndi chifowoko.
  6890. Heb 5:3 Ndipo pa chifukwa chimenecho iye ayenera, monga m’malo mwa anthuwo, moteronso m’malo mwa iye yekha, kupereka chifukwa cha machimo.
  6891. Heb 5:4 Ndipo palibe munthu adzitengera ulemu uwu mwini yekha, koma iye amene wayitanidwa ndi Mulungu, monga [anali] Aroni.
  6892. Heb 5:5 Koteronso Khristu sadadzilemekeza mwini yekha kukhala mkulu wansembe; koma iye amene adati kwa iye, Iwe ndiwe Mwana wanga wamwamuna, lero ine ndakubala iwe.
  6893. Heb 5:6 Monga iye adanenanso [pamalo] ena, Iwe [ndiwe] wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melekizedeki.
  6894. Heb 5:7 Amene m’masiku ake okhala m’thupi, pamene adapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kolimba ndi misozi kwa iye amene adali nako kuthekera kwa kum’pulumutsa iye mu imfa, ndipo adamvedwa chifukwa adawopa;
  6895. Heb 5:8 Angakhale adali Mwana wamwamuna, komabe iye adaphunzira kumvera mwa zinthu zimene iye adamva nazo kuwawa;
  6896. Heb 5:9 Ndipo popangidwa kukhala wangwiro, adakhala iye woyambitsa wa chipulumutso chosatha kwa iwo onse amene amvera iye;
  6897. Heb 5:10 Woyitanidwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melekizedeki.
  6898. Heb 5:11 Kwa iye tiri nazo zinthu zambiri za kunena, ndipo zovuta kuzimasulira, powona inu muli wogontha m’mamvedwe.
  6899. Heb 5:12 Pakuti ngakhale pamene mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nthawiyi, muli nako kusowanso kuti wina akuphunzitseninso zimene [zikhala] zoyamba za chiyambidwe cha maneno a mawu a Mulungu; ndipo mukhala wonga wofuna mkaka, osati chakudya cholimba.
  6900. Heb 5:13 Pakuti yense wakudya mkaka [ali] wopanda chizolowezi cha mawu achilungamo: pakuti ali khanda.
  6901. Heb 5:14 Koma chakudya cholimba chili cha iwo amene ali akulu misinkhu, [ngakhale] iwo amene mwa chifukwa cha kuchita nazo adazoloweretsa zizindikiritso zawo kuzindikira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.
  6902. Heb 6:1 Choncho, posiya mfundo za chiphunzitso cha Khristu, tiyeni ife tipite chitsogolo ku ungwiro; osayikanso maziko a kulapa kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha kwa Mulungu,
  6903. Heb 6:2 A chiphunzitso cha maubatizo, ndi a chakuyika kwa manja, ndi a chakuwuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.
  6904. Heb 6:3 Ndipo ichi tidzachita, ngati Mulungu alola.
  6905. Heb 6:4 Pakuti [si kuli] kotheka kwa iwo amene adayamba awunikiridwa, ndipo nalawa mphatso ya kumwamba, napangidwa kukhala wolandirana naye Mzimu Woyera.
  6906. Heb 6:5 Ndipo alawa mawu wokoma a Mulungu, ndi mphamvu za dziko lirinkudza,
  6907. Heb 6:6 Ngati akagwa [kupatuka] pa njirayo, kuwakonzanso iwo kuti alapenso; powona iwo alikudzipachikiranso iwo wokha Mwana wamwamuna wa Mulungu kwatsopano, namuyika iye pomchititsa manyazi poyera.
  6908. Heb 6:7 Pakuti nthaka imene imwa mvula imene imadza pa iyo kawirikawiri, nipatsa zitsamba zoyenera iwo amene adazilimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:
  6909. Heb 6:8 Koma imene ibala minga ndi mitungwi ikanidwa, ndipo [ili] pafupi ndi kutembereredwa; chitsiriziro chake [ndicho] kuti itenthedwe.
  6910. Heb 6:9 Koma, wokondedwa, tiri ndi chikhulupiriro cha zinthu zabwino pa inu, ndi zinthu zimene ziyenda pamodzi ndi chipulumutso, ngakhale titero pakuyankhula kwathu.
  6911. Heb 6:10 Pakuti Mulungu si [ali] wosalungama kuti ayiwale ntchito yanu ndi ntchito ya chikondi, imene mwayiwonetsera ku dzina lake, mwakuti inu mwatumikira woyera mtima, ndipo mutumikira.
  6912. Heb 6:11 Ndipo ife tikhumba kuti aliyense wa inu awonetsere changu chomwechi kuchidzalo chachitsimikizo cha chiyembekezo mpaka chimaliziro:
  6913. Heb 6:12 Kuti musakhale a ulesi, koma wotsatira a iwo amene kudzera mwa chikhulupiriro ndi chipiriro adalandira malonjezano.
  6914. Heb 6:13 Pakuti pamene Mulungu adapanga lonjezano kwa Abrahamu, chifukwa iye sakadalumbirira pa wina [pakuti panalibe] wamkulu, adalumbirira mwa iye yekha;
  6915. Heb 6:14 Kunena kuti, Zowona kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.
  6916. Heb 6:15 Ndipo chotero, iye atatha kupirira modekha adalandira lonjezano.
  6917. Heb 6:16 Pakuti anthu ndithudi alumbirira mwa wamkulu: ndipo lumbiro lachitsimikizo [liri] kwa iwo mathero a matsutsano onse.
  6918. Heb 6:17 M’menemonso Mulungu, pofuna mochuluka kuwonetsera kwa wolowa a lonjezano uphungu wake wosasinthika, adatsimikizira [ilo] mwa lumbiro:
  6919. Heb 6:18 Kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, mwa chimene [kudali] kosatheka kuti Mulungu aname, tikhoze kukhala nacho ife chitonthozo cholimba, amene athawira kukabisalamo kuti tikagwiritsitse chiyembekezo choyikika pamaso pathu:
  6920. Heb 6:19 [Chiyembekezo] chimene tiri nacho monga nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndipo chimene chilowa m’kati mwa [chinsalu] chotchinga.
  6921. Heb 6:20 M’mene wotitsogolera wa ife adalowa, ndiye Yesu, wopangidwa kukhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melekizedeki.
  6922. Heb 7:1 Pakuti Melekizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba, amene adakomana ndi Abrahamu pobwerera iye atawapha mafumu aja, namdalitsa iye;
  6923. Heb 7:2 Amenenso Abrahamu adampatsa limodzi la magawo khumi la zonse; pokhala poyamba pomasulidwa Mfumu ya chilungamo, ndipo patatha aponso Mfumu ya Salemu, imene ili, Mfumu ya mtendere;
  6924. Heb 7:3 Wopanda atate, wopanda amayi, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, wokhala wopanda chiyambi cha masiku, kapena kutha kwa moyo; koma wofanizidwa ndi Mwana wamwamuna wa Mulungu, akhala wansembe kosalekeza.
  6925. Heb 7:4 Tsopano tapenyani momwe munthu uyu ukulu wake [unaliri], kwa iye amene ngakhale Abrahamu kholo lalikulu adampatsa gawo limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.
  6926. Heb 7:5 Ndipo ndithudi iwowa amene ali ana a Levi, amene alandira ntchito ya unsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge gawo limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kuti, kwa abale awo, ngakhale kuti atuluka m’chiwuno cha Abrahamu:
  6927. Heb 7:6 Koma iye amene mawerengedwe achibadwidwe chake sachokera mwa iwo adatenga gawo limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene adali nawo malonjezano.
  6928. Heb 7:7 Ndipo popanda chitsutsano konse wamng’ono adalitsidwa ndi wamkulu.
  6929. Heb 7:8 Ndipo pano anthu amene amafa amalandira chakhumi; koma kumeneko iye [alandira iwo], kwa amene kudachitiridwa umboni kuti ali ndi moyo.
  6930. Heb 7:9 Ndipo monga ngati momwe ndinganene, Levinso, wakulandira za chakhumi adapereka chakhumi mwa Abrahamu.
  6931. Heb 7:10 Pakuti adali akadali m’chiwuno cha atate wake, pamene Melekizedeki adakomana naye.
  6932. Heb 7:11 Choncho ngati ungwiro ukadakhala mu unsembe wa Chilevi, (pakuti pa ulamuliro wake anthu adalandira chilamulo,) chosowa choposa chotani [chomwe chinalipo] kuti awuke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melekizedeki, ndipo wosayitanidwa monga mwa dongosolo la Aroni?
  6933. Heb 7:12 Pakuti unsembe kukhala wosinthidwa, pali kufunikanso kusintha kwa lamulo.
  6934. Heb 7:13 Pakuti iye amene zinthu izi zinenedwa akhala wa fuko lina, kwa limene palibe munthu adatumikira pa guwa la nsembe.
  6935. Heb 7:14 Pakuti ndizodziwikiratu kuti Ambuye wathu adatuluka mwa Yuda; kwa fuko ili Mose sadayankhula kanthu ka unsembe.
  6936. Heb 7:15 Ndipo tsono ndizodziwikiratu koposa ndithu: mwakuti monga mwa mafananidwe a Melekizedeki awuka wansembe wina,
  6937. Heb 7:16 Amene wapangidwa, osati monga mwa lamulo la thupi, koma monga mwa mphamvu ya moyo wopanda malire.
  6938. Heb 7:17 Pakuti iye achitira umboni, Iwe [ndiwe] wansembe wa nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melekizedeki.
  6939. Heb 7:18 Pakutitu ndithudi kuli kuchotsa kwake kwa lamulo lidadza kalelo chifukwa cha kufoka kwake ndi kusapindulitsa kwake.
  6940. Heb 7:19 Pakuti chilamulo sichidapanga kanthu kalikonse kukhala kangwiro, koma kubweretsa kwa chiyembekezo chabwino [kudachitadi]; mwa chimenecho ife tiyandikira nacho chifupi kwa Mulungu.
  6941. Heb 7:20 Ndipo monga momwe kudachitika kuti kopanda lumbiro [iye adapangidwa kukhala wansembe]:
  6942. Heb 7:21 (Chifukwa ansembe ajawa adapangidwa popanda lumbiro; koma uyu ndi lumbiro mwa iye amene adanena kwa iye, Ambuye walumbira ndipo sadzalapa, Iwe [ndiwe] wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melekizedeki:)
  6943. Heb 7:22 Mwa zambiri zotero Yesu wapangidwa kukhala chitsimikizo cha pangano loposa.
  6944. Heb 7:23 Ndipo iwo zowonadi adali ansembe ambiri, chifukwa iwo adaletsedwa asakhalebe mwa chifukwa cha imfa:
  6945. Heb 7:24 Koma [munthu] uyu, chifukwa kuti iye akhalabe nthawi yosatha, ali nawo unsembe wosasinthika.
  6946. Heb 7:25 Mwa ichi ali nako kuthekeranso kupulumutsa iwo konsekonse amene abwera kwa Mulungu mwa iye, powona iye akhala nawo moyo wamuyaya kuwapembedzera iwo.
  6947. Heb 7:26 Pakuti mkulu wa ansembe wotere adakhala wotiyenera ife, [amene ali] woyera mtima, wopanda choyipa, wosadetsedwa, wopatulidwa kwa wochimwa, ndi wopangidwa kukhala wopitirira pamwamba pa miyamba;
  6948. Heb 7:27 Amene sasoweka tsiku ndi tsiku, monga akulu a nsembe aja, kupereka nsembe, poyamba chifukwa cha machimo ake mwini, ndipo kenaka chifukwa cha a anthu: pakuti ichi adachita kamodzi, pamene adadzipereka mwini yekha.
  6949. Heb 7:28 Pakuti chilamulo chimapanga anthu [kukhala] akulu a ansembe amene ali nacho chifoko; koma mawu a lumbiro, limene lidalipo chifukwa cha chilamulo, lipanga Mwana wamwamuna, amene ali wopatulidwa ku nthawi zosatha.
  6950. Heb 8:1 Tsopano kwa zinthu izi zimene tanenazi [uwu ndiwo] uthunthu: Tiri naye mkulu wa nsembe wotere, amene adayikidwa pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu m’miyamba;
  6951. Heb 8:2 Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema chowona, chimene Ambuye adachimanga, osati munthu ayi.
  6952. Heb 8:3 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense ayikidwa kupereka mphatso ndi nsembe: mwa ichi [kuli] kofunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka.
  6953. Heb 8:4 Pakuti iye akadakhala padziko lapansi, iye sakadakhala wansembe, powona kuti pali iwo ansembe amene apereka mphatso monga mwa lamulo:
  6954. Heb 8:5 Amene atumikira kwa chitsanzo ndi mthunzi wa zinthu zakumwambazo, monga Mose achenjezedwa ndi Mulungu m’mene adati ayambe kupanga chihema: pakuti, Tawona, atero iye, [kuti] iwe upange zinthu zonse monga mwa chitsanzocho chowonetsedwa kwa iwe m’phiri.
  6955. Heb 8:6 Koma tsopano iye walandira utumiki wopambana koposa, mwa momwenso ali nkhoswe ya pangano [labwino] loposa, limene lidakhazikidwa pa malonjezano [abwino] woposa.
  6956. Heb 8:7 Pakuti ngati [pangano] lija loyamba likadakhala lopanda cholakwika, pamenepo sipakadafunika malo ofunidwa a lachiwiriro.
  6957. Heb 8:8 Pakuti powapezera iwo chirema, iye anena, Tawonani, akudza masiku, atero Ambuye, pamene ine ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda:
  6958. Heb 8:9 Losati malingana ndi pangano limene ndidachita ndi makolo awo mu tsikuli ndidawatenga iwo ndi dzanja kuwatsogolera atuluke m’dziko la Igupto; chifukwa chakuti iwo sadakhalebe m’pangano langa, ndipo ine sindidawasamalira iwo, atero Ambuye.
  6959. Heb 8:10 Pakuti [ili] ndiro pangano limene ndidzalipanga ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku awo, atero Ambuye; ine ndidzayika malamulo anga kuwalonga m’malingaliro awo, ndi kuwalemba pa mtima pawo: ndipo ndidzakhala kwa iwo Mulungu; ndipo iwo adzakhala kwa ine anthu:
  6960. Heb 8:11 Ndipo siadzaphunzitsa yense woyandikana naye wake, ndipo munthu aliyense mbale wake, kunena, Dziwa Ambuye: pakuti onse adzadziwa ine kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu.
  6961. Heb 8:12 Pakuti ndidzachitira chifundo kusalungama kwawo, ndipo machimo awo ndi zoyipa zawo ine sindidzazikumbukanso.
  6962. Heb 8:13 Mwakunena iye, [Pangano] latsopano, adapangitsa loyambali kukhala lakale. Tsopano chimene chivunda ndi kusukuluka, [chili] chokonzeka kukanganuka.
  6963. Heb 9:1 Pamenepo ndithudi [pangano] loyambali lidali nazo zoyikika za kutumikira Umulungu, ndi malo wopatulika a pa dziko lapansi.
  6964. Heb 9:2 Pakuti padali chihema chokonzeka; choyamba chija, m’menemo [mudali] choyikapo nyali, ndi gome, ndi mkate wowonekera; amene atchedwa malo wopatulika.
  6965. Heb 9:3 Ndipo kupitirira chinsalu chotchinga chachiwiri, chihema chimene chitchedwa Malo Woyeretsetsa a onse;
  6966. Heb 9:4 Amene adali nayo mbale ya zofukizira yagolidi, ndi likasa la chipangano lokutidwa ponsepo ndi golidi, m’menemo [mudali] mbiya yagolidi mudali mana, ndi ndodo ya Aroni imene idaphukayo, ndi magome a chipangano;
  6967. Heb 9:5 Ndi pamwamba pake Akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pa mpando wa chifundo; za zimene izi sitikhoza kunena tsopano mwapadera.
  6968. Heb 9:6 Tsopano pamene zinthu izi zidakonzeka motero, ansembe amalowa nthawi zonse m’chihema choyamba, kutsiriza kugwira ntchito [ya Mulungu].
  6969. Heb 9:7 Koma kulowa m’chachiwiri, [amapita] mkulu wa ansembe yekha kamodzi chaka chilichonse, wosati wopanda mwazi, umene amapereka chifukwa cha iye mwini yekha, ndi [chifukwa cha] zolakwa za anthu:
  6970. Heb 9:8 Mzimu Woyera adatsimikizira ichi, kuti njira yolowa nayo kumalo woyeretsetsa a onse idali isadawonetsedwe, pokhala chihema choyamba chidali chili chiyimire:
  6971. Heb 9:9 Chimene chidali chifaniziro cha ku nthawi imene idalipo, m’mene mphatso ndi nsembezo zidaperekedwa zimene sizikadatha kumpanga iye amene adachita ntchitoyi kukhala wangwiro, polumikiza ndi za chikumbumtima;
  6972. Heb 9:10 [Chimene chidayima] m’nyama zokha ndi zakumwa, ndi masambidwe wosiyanasiyana, ndi zoyikika za thupi, zoyikidwa [pa iwo] kufikira nthawi yakukonzanso.
  6973. Heb 9:11 Koma Khristu atafika Mkulu wansembe wa zinthu zabwino zirinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangidwa ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chomanga ichi;
  6974. Heb 9:12 [Kosati] kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa iye yekha, adalowa kamodzi kumalo woyera, atapeza chiwombolo chosatha [cha ife].
  6975. Heb 9:13 Pakuti ngati mwazi wa ng’ombe zamphongo ndi wa mbuzi, ndi phulusa la ng’ombe yayikazi yosabalapo wowaza pa iwo wodetsedwa, upatula kufikira chiyeretso cha thupi:
  6976. Heb 9:14 Koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene kudzera mwa Mzimu wamuyaya adadzipereka yekha wopanda banga kwa Mulungu, kuyeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa kukatumikira Mulungu wamoyo?
  6977. Heb 9:15 Ndipo pa chifukwa ichi iye ali nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti mwa njira ya imfa, ya chiwombolo cha zolakwa [zimene zidali] pa chipangano choyamba, iwo woyitanidwawo akhoze kulandira lonjezano la cholowa chosatha.
  6978. Heb 9:16 Pakuti pamene [pali] pangano, pafunika pakhale imfa ya mwini panganolo.
  6979. Heb 9:17 Pakuti pangano [likhala] ndi mphamvu pamene anthu afa: popanda apo silikhala ndi mphamvu konse pokhala mwini pangano ali ndi moyo.
  6980. Heb 9:18 Pameneponso ngakhale [chipangano] choyambacho sichidaperekedwa popanda mwazi.
  6981. Heb 9:19 Pakuti pamene Mose adayankhula lamulo lirilonse kwa anthu onse monga mwa chilamulo, adatenga mwazi wa ana a ng’ombe ndi mbuzi, pamodzi, ndi madzi ndi ubweya wofiyira, ndi hisope, nawaza buku, ndi anthu onse,
  6982. Heb 9:20 Nanena, Uwu [ndi] mwazi wa chipangano umene Mulungu wadzilumikizitsa kwa inu.
  6983. Heb 9:21 Kupitirira apo adawazanso chihema, ndi zotengera zonse za utumiki.
  6984. Heb 9:22 Ndipo pafupifupi zinthu zonse mwa lamulo ziri zoyeretsedwa ndi mwazi, ndipo popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa.
  6985. Heb 9:23 Choncho [kunali] kofunika kuti zifaniziro za zinthu za m’Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma za kumwamba izo zokha ziyenera ziyeretsedwe ndi nsembe zabwino zoposa izi.
  6986. Heb 9:24 Pakuti Khristu sadalowa m’malo woyera wopangidwa ndi manja, [amene ndi] chithunzithunzi cha owonawo; koma kulowa kumwamba komwe, tsopano kuwonekera pamaso pa Mulungu m’malo mwa ife:
  6987. Heb 9:25 Kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri, monga mkulu wa nsembe alowa m’malo woyera chaka ndi chaka ndi mwazi wa ena;
  6988. Heb 9:26 Pakutero tsono anayenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira maziko a dziko lapansi: koma tsopano kamodzi kokha kumatsiriziro a dziko lapansi wawonekera iye kuchotsa uchimo mwa nsembe ya mwini yekha.
  6989. Heb 9:27 Ndipo monga kwayikikatu kwa anthu kamodzi kuti afe, ndipo pambuyo pa ichi chiweruziro:
  6990. Heb 9:28 Chotero Khristunso adaperekedwa nsembe kamodzi kusenza machimo a ambiri; kwa iwo amene amyang’anira adzawonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo kufikira chipulumutso.
  6991. Heb 10:1 Pakuti chilamulo, pokhala nacho chithunzithunzi cha zinthu zabwino zirinkudza, [ndipo] wosati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sizikhozatu ndi nsembe zomwezo zinkaperekedwa chaka ndi chaka kosalekeza, kuwapanga angwiro iwo obwera.
  6992. Heb 10:2 Pakutero tsono iwo sakadayenera kusiya kuperekedwa? Chifukwa kuti wolambirawo pamene ayeretsedwa kamodzi sakadayenera kukhala nachonso chikumbumtima cha machimo.
  6993. Heb 10:3 Koma mu [nsembe izi muli] chikumbukironso chopangidwa cha machimo chaka ndi chaka.
  6994. Heb 10:4 Pakuti [si kuli] kotheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo ndi mbuzi ukachotse machimo.
  6995. Heb 10:5 Mwa ichi pamene adabwera m’dziko lapansi, iye anena, Nsembe ndi chopereka simudzazifuna, koma thupi inu mudandikonzera ine:
  6996. Heb 10:6 Mu nsembe zopsereza ndi [nsembe] za kwa machimo inu simudakondwera.
  6997. Heb 10:7 Pamenepo ine ndidati, Tawonani ndafika, (mu mpukutu wa buku izi zalembedwa za ine,) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.
  6998. Heb 10:8 Pamwamba pamene iye adanena, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi [zopereka] za kwa machimo simudzazifuna, kapena kukondwera [mwa izo]; zimene ziperekedwa monga mwa lamulo;
  6999. Heb 10:9 Kenaka adanena iye, Tawonani, ndabwera kudzachita chifuniro chanu Mulungu. Iye achotsa choyambacho, kuti akhoze kuyika chachiwiricho.
  7000. Heb 10:10 Mwa chifuniro chimenecho ife tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi [kwa nthawi zones].
  7001. Heb 10:11 Ndipotu wansembe aliyense amayima tsiku ndi tsiku kutumikira ndi kupereka kawirikawiri nsembe zomwezi, zimene sizikhoza konse kuchotsa machimo:
  7002. Heb 10:12 Koma munthu uyu, m’mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo kwa muyaya, adakhala pansi padzanja lamanja la Mulungu;
  7003. Heb 10:13 Kuchokera pamenepa adikirira kufikira adani ake apangidwa kukhala chopondapo mapazi ake.
  7004. Heb 10:14 Pakuti ndi nsembe imodzi adawayesera angwiro chikhalire iwo amene apatulidwa.
  7005. Heb 10:15 [Pameneponso] Mzimu Woyeranso ali mboni kwa ife: wa chimene adachinena kale,
  7006. Heb 10:16 Ili [ndi] pangano limene ndidzapanga ndi iwo atapita masiku awo, atero Ambuye, ndidzayika malamulo anga m’mtima mwawo, ndipo pa maganizo awo ine ndidzawalemba iwo;
  7007. Heb 10:17 Ndipo machimo awo ndi zoyipa zawo sindidzakumbukiranso.
  7008. Heb 10:18 Tsopano pomwe pali chikhululukiro cha izi, [palibenso] chopereka cha kwa uchimo.
  7009. Heb 10:19 ¶Choncho pokhala, abale, kulimbika mtima chakulowa m’malo woyeretsetsa ndi mwazi wa Yesu,
  7010. Heb 10:20 Mwa njira yatsopano ndi ya moyo, imene adapatulira kwa ife, mwa chinsalu chotchinga, ndicho kunena, thupi lake;
  7011. Heb 10:21 Ndipo [pokhala] naye wansembe wamkulu woyang’anira nyumba ya Mulungu;
  7012. Heb 10:22 Tiyeni tiyandikire pafupi ndi mtima wowona m’chitsimikizo chathunthu cha chikhulupiriro, wokhala ndi mitima yathu yowazidwa kuchoka ku chikumbumtima choyipa, ndi matupi athu wosambitsidwa ndi madzi woyera.
  7013. Heb 10:23 Tiyeni tigwiritse chivomerezo cha chikhulupiriro [chathu] wosagwedera; (pakuti ali wokhulupirika amene adalonjezayo;)
  7014. Heb 10:24 Ndipo tiganizire wina ndi mzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino:
  7015. Heb 10:25 Wosaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga achitira ena; komatu tilimbikitsane [wina ndi mzake]: ndiko koposa kwambiri, monga momwe muwona tsiku liri kuyandikira.
  7016. Heb 10:26 Pakuti ngati ife tichimwa mwakufuna dala titatha kulandira chidziwitso cha chowonadi, palibenso nsembe ina yotsalira yoperekedwa chifukwa cha machimo.
  7017. Heb 10:27 Koma kulindira kwina kowopsa kwa chiweruziro ndi kutentha kwake kwa moto wakuwononga, umene udzameza wotsutsana nawo.
  7018. Heb 10:28 Iye amene adapeputsa chilamulo cha Mose anafa wopanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:
  7019. Heb 10:29 Kwa kulanga koposa kotani, mukuganiza inu, iye adzaganizidwa woyenera, amene adapondereza pansi pa phazi Mwana wamwamuna wa Mulungu, nawerengera mwazi wa chipangano, umene adayeretsedwa nawo, chinthu wamba, ndipo wachitira wosapereka ulemu kwa Mzimu wa chisomo?
  7020. Heb 10:30 Pakuti timdziwa iye amene wanena, Kubwezera chilango [kuli] kwanga, ine ndidzabwezera, atero Ambuye. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.
  7021. Heb 10:31 [Chili chinthu] chowopsa kugwa m’manja a Mulungu wamoyo.
  7022. Heb 10:32 Koma takumbukirani masiku akale, m’mene, inu mutawunikiridwa, mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa;
  7023. Heb 10:33 Mwa mbali ina, pamene mudachitidwa chinthu chodabwitsa pakuchiwona mwa zitonzo ndi zisawutso; ndi mbali ina, pamene mudalawana nawo [pamodzi] iwo wozolowera kuchitidwa zotere.
  7024. Heb 10:34 Pakuti mudamva chifundo ndi ine mu undende wanga, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, podziwa mwa inu eni nokha kuti muli nacho kumwamba chuma choposa chachikhalire.
  7025. Heb 10:35 Choncho musataye kulimbika mtima kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.
  7026. Heb 10:36 Pakuti inu muyenera kupirira, kuti, pamene inu mwachita chifuniro cha Mulungu, inu mukakhoze kulandira lonjezano.
  7027. Heb 10:37 Pakuti katsala kanthawi kakang’onong’ono, ndipo iye amene adzadzeyo adzabwera, ndipo sadzachedwa.
  7028. Heb 10:38 Tsopano wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro: ndipo ngati [munthu aliyense] abwerera m’mbuyo, moyo wanga sudzakhala ndi kukondwera mwa iye.
  7029. Heb 10:39 Koma ife si ndife a iwo amene abwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.
  7030. Heb 11:1 Tsopano chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeredwa, chitsimikizo cha zinthu zosapenyeka.
  7031. Heb 11:2 Pakuti mwa ichi akulu adalandira umboni wabwino.
  7032. Heb 11:3 Kudzera mu chikhulupiriro tidziwa kuti mayiko [adakonzedwa] ndikumalizidwa ndi mawu a Mulungu, kotero kuti zinthu zimene zipenyeka sizidapangidwa kuchokera mwa zinthu zimene ziwoneka.
  7033. Heb 11:4 Mwa chikhulupiriro Abeli adapereka kwa Mulungu nsembe yopambana yoposa ija ya Kayini, mwa imene adachitidwa umboni nayo kuti adali wolungama, Mulungu nachitapo umboni pa mphatso zake: ndipo mwa iyi iye, ayankhulabe angakhale adafa.
  7034. Heb 11:5 Mwa chikhulupiriro Enoki adatengedwa kupita kumwamba kuti asawone imfa; ndipo sadapezeka, chifukwa chakuti Mulungu adamtenga: pakuti asadamtenge adachitidwa umboni, kuti iye adakondweretsa Mulungu.
  7035. Heb 11:6 Koma popanda chikhulupiriro [si kuli] kotheka kumkondweretsa [iye]: pakuti iye amene akudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti ali, ndi [kuti] ali wopereka mphotho kwa iwo akumfuna iye mwa khama.
  7036. Heb 11:7 Mwa chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zisanapenyekepo, ndipo pochita mantha, adamanga chombo cha kupulumutsiramo nyumba yake; mwa chimene adatsutsa nacho dziko lapansi, ndipo anakhala wolandira cholowa wa chilungamo chomwe chili mwa chikhulupiriro.
  7037. Heb 11:8 ¶Mwa chikhulupiriro Abrahamu, poyitanidwa kuti atuluke kunka kulowa malo amene ayenera pambuyo pake kudzalandira ngati cholowa, adamvera; ndipo adatuluka, wosadziwa kumene adamukako.
  7038. Heb 11:9 Mwa chikhulupiriro iye adakhala mlendo kudziko la lonjezano, monga [mu] dziko la chilendo, kukhala m’mahema ndi Isake ndi Yakobo, wolandira cholowa pamodzi ndi iye a lonjezano lomwero:
  7039. Heb 11:10 Pakuti adayang’anira mzinda umene uli nawo maziko, umene m’misiri wake ndi womanga wake [ndiye] Mulungu.
  7040. Heb 11:11 Kudzera mu chikhulupiriro Saranso adalandira mphamvu yakukhala ndi pakati poyembekezera mbewu, ndipo adabereka mwana atapitirira msinkhu wakubala, chifukwa adampeza kuti ali iye wokhulupirika amene adalonjeza.
  7041. Heb 11:12 Choncho kudaphuka kumeneko m’modzi, ndi iye ngati wakufa, [aunyinji] ngati nyenyezi za m’mlengalenga mu kuchuluka, ndi ngati mchenga umene uli m’mbali mwa nyanja wosawerengeka.
  7042. Heb 11:13 Awa onse adamwalira m’chikhulupiriro, wosalandira malonjezanowo, koma powawona patali, ndipo adakakamizidwa ndi [iwo], ndi kuwagwiritsitsa [iwo], ndi kuvomereza kuti anali alendo ndi wongodutsa padziko.
  7043. Heb 11:14 Pakuti iwo amene anena zinthu zotere alengeza momveka bwino kuti alikufunafuna kwawo.
  7044. Heb 11:15 Ndipo zowonadi, ngati iwo akadakhala wosamalira za [dziko] limene iwo adachokerako, iwo akadakhoza kukhala ndi mwayi wakuti akadakhoza kubwerera.
  7045. Heb 11:16 Koma tsopano akhumba [dziko] labwino koposa, ndilo, la kumwamba: mwa ichi Mulungu sachita manyazi kuyitanidwa ndi iwo Mulungu wawo: pakuti iye wawakonzera iwo mzinda.
  7046. Heb 11:17 Mwa chikhulupiriro Abrahamu, pamene iye adayesedwa, adapereka nsembe Isake: ndipo iye amene adalandira malonjezano adapereka mwana wake wamwamuna wa iye yekha,
  7047. Heb 11:18 Amene kudanenedwa za iye, Kuti mwa Isake mbewu yako idzayitanidwa:
  7048. Heb 11:19 Powerengera iye kuti Mulungu ndiwakutha kuwukitsa iye, ngakhale kuchokera kwa akufa; kuchokera komwe adamlandiranso iye mchithunzithunzi.
  7049. Heb 11:20 ¶Mwa chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau zokhudza zinthu zirinkudza.
  7050. Heb 11:21 Mwa chikhulupiriro Yakobo, pamene adali kumwalira, anadalitsa onse awiri ana a Yosefe; ndipo analambira, [atatsamira] pa mutu wa ndodo yake.
  7051. Heb 11:22 Mwa chikhulupiriro, Yosefe, pamene atamwalira, adatchula za manyamukidwe a ana a Israyeli; nalamulira za mafupa ake.
  7052. Heb 11:23 ¶Mwa chikhulupiriro Mose, pamene anabadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi makolo ake, chifukwa adawona kuti [iye adali] mwana woyenera; ndipo sadawopa lamulo la mfumu.
  7053. Heb 11:24 Mwa chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu adakana kutchulidwa mwana wake wamwamuna wa mwana wamkazi wa Farawo;
  7054. Heb 11:25 Kusankhula kuchitidwa zoyipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, koposa kukhala nazo zomkondweretsa za uchimo kwa kanthawi kochepa;
  7055. Heb 11:26 Nawerenga chitonzo cha Khristu chuma choposa chuma cha mu Igupto: pakuti iye adayang’anira kubwezera kwa mphotho.
  7056. Heb 11:27 Mwa chikhulupiriro adachoka mu Igupto, wosawopa mkwiyo wa mfumu: pakuti adapirira molimbika, monga ngati kuwona wosawonekayo.
  7057. Heb 11:28 Kudzera mu chikhulupiriro iye adasunga Paskha, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti mwina iye wakuwononga ana woyamba kubadwa angawakhudze iwo.
  7058. Heb 11:29 Mwa chikhulupiriro adawoloka nyanja Yofiyira kuyenda ngati padziko lowuma; limene Aigupto poyesanso kutero adamizidwa.
  7059. Heb 11:30 Mwa chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa pansi, atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.
  7060. Heb 11:31 Mwa chikhulupiriro Rahabu wachiwerewere uja sadawonongeka pamodzi ndi iwo amene sadakhulupirire, pamene adalandira azondi ndi mtendere.
  7061. Heb 11:32 ¶Ndipo ine ndinena chiyaninso china? Pakuti nthawi idzandiperewera kuti ndifotikozere za Gidiyoni, ndi [za] Baraki, ndi [za] Samsoni, ndi [za] Yefita; [za] Davidenso, ndi Samueli ndi [za] aneneri:
  7062. Heb 11:33 Amene kudzera mu chikhulupiriro adagonjetsa maufumu, adachita chilungamo, adalandira malonjezano adatseka pakamwa pa mikango,
  7063. Heb 11:34 Nazima chiwawa cha [mphamvu ya] moto, napulumuka ku lupanga lakuthwa, kuchoka ku kufoka iwo analimbikitsidwa, adakula mphamvu mu kulimbana, adapitikitsa magulu a nkhondo ya achilendo.
  7064. Heb 11:35 Akazi adalandira akufa awo kuwukitsidwanso kwa akufa: ndipo ena adanzunzidwa, wosalola kuwomboledwa; kuti akakhoze kulandira chiwukitso chabwino choposa;
  7065. Heb 11:36 Ndipo ena adayesedwa ndi zitonzo [zankhanza] ndi mikwapulo, inde, kuwonjezera apo nsinganso ndi kutsekeredwa m’ndende:
  7066. Heb 11:37 Adaponyedwa miyala, adachekedwa pakati, adayesedwa, adaphedwa ndi lupanga: adayendayenda wovala zikopa za nkhosa ndi za mbuzi; nakhala wosowa, wosawutsidwa, wochitidwa zoyipa;
  7067. Heb 11:38 (A iwo amene dziko lapansi silidayenera iwo:) anayendayenda m’zipululu, ndi [mu] mapiri, ndi [mu] mapanga, ndi m’mauna a dziko lapansi.
  7068. Heb 11:39 Ndipo awa onse, atalandira umboni wabwino kudzera mu chikhulupiriro, sadalandira lonjezanolo:
  7069. Heb 11:40 Mulungu atakonzera chinthu china chabwino kwa ife, kuti iwo popanda ife asayesedwe angwiro.
  7070. Heb 12:1 Mwa ichi ifenso powona tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, tiyeni titaye cholemera chilichonse, ndi tchimo limene limatizinga [ife] mosavuta, ndipo tiyeni tithamange mwa chipiriro mpikisanowo adatiyikira ife.
  7071. Heb 12:2 Poyang’anira kwa Yesu woyamba ndi womaliza wa chikhulupiriro [chathu], amene chifukwa cha chimwemwe choyikidwa pamaso pake adapirira mtanda, nanyoza manyazi, ndipo wayikidwa pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
  7072. Heb 12:3 Pakuti talingalirani iye amene adapirira chotsutsana chotere cha wochimwa kutsutsana ndi iye mwini, kuti mwina mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.
  7073. Heb 12:4 Inu simunakaniza mpaka tsopano kufikira mwazi, kulimbana motsutsa tchimo.
  7074. Heb 12:5 Ndipo mwayiwala dandawuliro limene lilankhula kwa inu monga kwa ana, Mwana wanga wamwamuna usapeputse iwe kulanga kwa Ambuye kapena usakomoke pamene udzudzulidwa ndi iye:
  7075. Heb 12:6 Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana wamwamuna aliyense amene amlandira.
  7076. Heb 12:7 Ngati mupirira kulangidwa, Mulungu achita nanu monga ngati ana amuna; pakuti mwana wamwamuna wanji amene atate samulanga?
  7077. Heb 12:8 Koma ngati mukhala wopanda kulangidwa, chimene onse adalawako, pamenepo muli a m’thengo, osati ana amuna.
  7078. Heb 12:9 Kuwonjezera apo tidali nawo atate a thupi lathu akutilanga [ife], ndipo tidawalemekeza [iwo]: kodi makamaka sitidzagonjera koposa Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
  7079. Heb 12:10 Pakuti iwo ndithudi kwa masiku wowerengeka adatilanga [ife] monga kudawakomera eni; koma iye chifukwa cha kukatipindulitsa [ife], kuti tikakhoze kukhala olandirana nawo a chiyero chake.
  7080. Heb 12:11 Tsopano palibe chilango chokonza chikhalidwe chilichonse cha nthawi ino chimveka kukhala chokondweretsa, koma chowawa: ngakhale ziri choncho pambuyo pake chipereka chipatso cha mtendere cha chilungamo kwa iwo wozoloweretsedwa nacho.
  7081. Heb 12:12 Mwa ichi kwezekani manja amene alendewera, ndi mawondo wolobodoka;
  7082. Heb 12:13 Ndipo lambulani misewu yolunjika ya mapazi anu, kuti mwina chimene chili cholumala chisapatulidwe pa njira; koma makamaka chichiritsidwe.
  7083. Heb 12:14 Londolani mtendere ndi [anthu] onse, ndi chiyero chimene, akapanda ichi palibe adzawona Ambuye:
  7084. Heb 12:15 Kuyang’anira mwakhama kuti mwina pangakhale munthu wina wakulephera za chisomo cha Mulungu; kuti mwina muzu wina wake wakuwawa mtima ungaphuke kuvuta [inu], ndipo pa chimenecho aunyinji angadetsedwe;
  7085. Heb 12:16 Kuti mwina pangakhale [wina] wachiwerewere, kapena wam’nyozo, ngati Esau, amene ndi kachakudya kakang’ono kamodzi adagulitsa ukulu wake wobadwa nawo.
  7086. Heb 12:17 Pakuti mudziwa kutinso pambuyo pake, pamene adafuna kulandira cholowa cha dalitsolo, iye adakanidwa: pakuti sadapeza malo wolapa, ngakhale adalifuna mosamalitsa ndi misozi.
  7087. Heb 12:18 ¶Pakuti simudabwera ku phiri limene likhoza kukhudzika, ndi kutenthedwa ndi moto, kapena ku kudetsedwa, ndi mdima, ndi namondwe,
  7088. Heb 12:19 Ndi liwu la lipenga, ndi liwu la mawu olankhulidwa; [liwu] limene iwo amene adamvawo adapempha kuti mawuwo asalankhulidwenso kwa iwo:
  7089. Heb 12:20 (Pakuti sadakhoza kupirira chimene chidalamulidwacho, ndipo ngati kotero nyama ikhudza phiriro, idzaponyedwa miyala, kapena kulasidwa ndi muvi:
  7090. Heb 12:21 Ndipo mawonekedwewo adali wowopsa wotero, [kuti] Mose adati, Ndiwopatu ndi kunthunthumira kwakukulu;)
  7091. Heb 12:22 Koma mwabwera ku phiri la Ziyoni, ndi ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa kumwamba, ndi ku unyinji wochuluka wa angelo,
  7092. Heb 12:23 Ndi kwa msonkhano wa onse ndi mpingo wa wobadwa woyamba, amene ali wolembedwa kumwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya wolungama wopangidwa angwiro,
  7093. Heb 12:24 Ndi kwa Yesu mkhalapakati wa chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza, umene ulankhula zinthu zabwino zoposa [izo] za wa Abele.
  7094. Heb 12:25 Penyani kuti inu musamkane iye amene alankhulayo. Pakuti ngati iwo sadapulumuka amene adamkana iye amene adalankhula padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, ngati tipatuka kuchoka kwa iye amene [ayankhula] kuchokera kumwamba:
  7095. Heb 12:26 Amene mawu ake adagwedeza dziko lapansi: koma tsopano walonjeza, kunena, Kamodzinso ine ndigwedeza si dziko lapansi lokha komanso kumwamba.
  7096. Heb 12:27 Ndipo mawu [awa], Kamodzinso, alozera kuchotsa kwake kwa zinthu zimene zagwedezedwa, monga kwa zinthu zimene zapangidwa, kuti zinthu zimene sizingagwedezeke zitsale.
  7097. Heb 12:28 Mwa ichi ife polandira ufumu umene sungasunthike, tiyeni tikhale nacho chisomo, mwa chimene tikakhoze kutumikira nacho Mulungu molandiridwa pamodzi ndi kumchitira ulemu ndi mantha:
  7098. Heb 12:29 Pakuti Mulungu wathu [ndi] moto wonyeketsa.
  7099. Heb 13:1 Lolani chikondi cha pa able chipitirire.
  7100. Heb 13:2 Musakhale woyiwala kuchereza alendo: pakuti mwa ichi ena adachereza angelo mosawadziwa.
  7101. Heb 13:3 Kumbukirani am’singa, monga womangidwa nawo pamodzi; [ndi] iwo wochitidwa zoyipa, monga inunso muli m’thupi.
  7102. Heb 13:4 Ukwati ndi wochitidwa ulemu mwa onse, ndi pogona pasadetsedwa: koma achiwerewere ndi achigololo Mulungu adzawaweruza.
  7103. Heb 13:5 [Mulole] makhalidwe anu [akhale] wosakonda chuma; [ndipo mukhale] wokwaniritsidwa ndi zinthu zimene muli nazo: pakuti iye wati, Ine sindidzakusiya iwe, kapena kukutaya iwe.
  7104. Heb 13:6 Kotero kuti tikhoze molimbika mtima kunena, Ambuye [ndiye] mthandizi wanga; ndipo sindidzawopa chimene munthu adzandichitira ine.
  7105. Heb 13:7 Kumbukirani iwo amene ali ndi ulamuliro pa inu, amene adayankhula kwa inu Mawu a Mulungu: amenewo mutsanze chikhulupiriro chawo, polingalira chitsiriziro cha makhalidwe [awo].
  7106. Heb 13:8 Yesu Khristu ali chimodzimodzi dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse.
  7107. Heb 13:9 Musatengedwe ndi ziphunzitso za mitundumitundu ndi zachilendo. Pakuti [chili chinthu] chabwino kuti mtima ukhazikitsidwe ndi chisomo; osati ndi zakudya, zimene sizidawapindulira iwo amene adatengeka nazo.
  7108. Heb 13:10 Tiri nalo guwa la nsembe, pa limene alibe ufulu wa kudyako iwo akutumikira chihema.
  7109. Heb 13:11 Pakuti matupi a nyama izo, zimene mwazi wa izo umabweretsedwa kulowa m’malo woyera ndi mkulu wa nsembe, chifukwa cha machimo, amatenthedwa kunja kwa msasa.
  7110. Heb 13:12 Mwa ichi Yesunso, kuti akhoze kuyeretsa anthuwo mwa mwazi wa iye yekha, adamva zowawa kunja kwa chipata.
  7111. Heb 13:13 Choncho tiyeni ife tituluke tipite kwa iye kunja kwake kwa msasa, wosenza chitonzo chake.
  7112. Heb 13:14 Pakuti pano ife tiribe mzinda wokhalitsa, koma tifunafuna umene ulinkudzawo.
  7113. Heb 13:15 Chfukwa chake mwa iye tiyeni tipereke nsembe yamatamando kwa Mulungu wosalekeza, ndiyo ya, chipatso cha milomo [yathu] yopereka mayamiko ku dzina lake.
  7114. Heb 13:16 Koma kuchita zabwino ndi kugawira ena musayiwale: pakuti ndi nsembe zotere Mulungu akondwera bwino nazo.
  7115. Heb 13:17 Mverani iwo amene ali ndi ulamuliro pa inu, ndipo mugonjere eni nokha: pakuti ayang’anira miyoyo yanu, monga ayenera kufotokoza za zochitika; kuti akhoze kuchita ichi ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi [chili] chosapindulitsa kwa inu.
  7116. Heb 13:18 Mutipempherere ife: pakuti tikhulupirira kuti tiri nacho chikumbumtima chokoma, m’zinthu zonse wofuna kukhala wopanda chinyengo.
  7117. Heb 13:19 Koma ine ndikudandawulirani [inu] koposa makamaka kuchita ichi, kuti ndikhoze kubwezeretsedwa kwa inu mofulumirirapo.
  7118. Heb 13:20 Tsopano Mulungu wa mtendere, amene anawukitsanso kwa akufa Ambuye wathu Yesu, ameneyo mbusa wa mkulu wa nkhosa, kudzera m’mwazi wa chipangano chosatha,
  7119. Heb 13:21 Apange inu angwiro mu ntchito iliyonse yabwino kuti muchite chifuniro chake, kugwira nchito mwa inu zimene ziri zokondweretsa m’maso mwake, kudzera mwa Yesu Khristu; kwa iye [kukhale] ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
  7120. Heb 13:22 Ndipo ine ndikulimbikitsani inu, abale, lolani mawu a chidandawuliro: pakuti ine ndalemba kalata kwa inu m’mawu ochepa.
  7121. Heb 13:23 Dziwani kuti mbale [wathu] Timoteyo wamasulidwa; ndi iye, ngati iye akudza posachedwa, ine ndidzakuwonani inu.
  7122. Heb 13:24 Apatseni moni onse amene ali ndi ulamuliro pa inu, ndi woyera mtima onse. Iwo a ku Itale akupereka moni kwa inu.
  7123. Heb 13:25 Chisomo [chikhale] ndi inu nonse. Amen.
  7124. Jas 1:1 Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri amene ali obalalika m’mayiko a kunja, moni.
  7125. Jas 1:2 ¶Abale anga, muchiyese chonse chimwemwe chokha, pamene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu;
  7126. Jas 1:3 Podziwa [ichi], kuti chiyeso cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.
  7127. Jas 1:4 Koma lolani chipiriro chikhale nayo ntchito [yake] yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi amphumphu, osasowa kanthu.
  7128. Jas 1:5 Ngati wina wa inu asowa nzeru, apemphe iye kwa Mulungu, amene apatsa kwa [anthu] onse modzala manja, ndipo satonza; ndipo iyo idzapatsidwa kwa iye.
  7129. Jas 1:6 Koma iye apemphe m’chikhulupiriro, wosakayika konse. Pakuti iye amene akayika afanana ndi funde la nyanja loyendetsedwa ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.
  7130. Jas 1:7 Pakuti asaganize munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye.
  7131. Jas 1:8 Munthu wa mitima iwiri [ali] wosakhazikika pa njira zake zonse.
  7132. Jas 1:9 Mbale wokhala modzichepetsa akondwere kuti iye wakwezedwa:
  7133. Jas 1:10 Koma achumawo, kuti atsitsidwa pansi: pakuti monga duwa la udzu iye adzapita.
  7134. Jas 1:11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, koma lawumitsa udzu, ndipo duwa lake lathothoka, ndi kukongola kwa mawonekedwe ake kuwonongeka: koteronso munthu wachuma adzafota m’njira zake.
  7135. Jas 1:12 Wodala [ali] munthu amene apirira mayesero: pakuti pamene wayesedwa, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye walonjeza kwa iwo akumkonda iye.
  7136. Jas 1:13 Poyesedwa munthu aliyense asanena, Ine ndiyesedwa ndi Mulungu: pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa, kapena iye mwini sayesa munthu:
  7137. Jas 1:14 Koma munthu aliyense ayesedwa, pamene chimkoka chilakolako chake cha iye mwini, ndipo anyengedwa.
  7138. Jas 1:15 Ndipo pamene chilakolakocho chayima, chimabala uchimo: ndipo uchimo, pamene wakula msinkhu, umabala imfa.
  7139. Jas 1:16 Musanyengedwa, abale anga wokondedwa.
  7140. Jas 1:17 Mphatso iliyonse yabwino ndi mphatso iliyonse yangwiro zichokera kumwamba, ndipo zitsika kuchokera kwa Atate wa mawuniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa kutembenuka.
  7141. Jas 1:18 Mwa chifuniro chake mwini adatibala ife ndi mawu a chowonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba kucha za zolengedwa zake.
  7142. Jas 1:19 Mwa ichi, abale anga wokondedwa, munthu aliyense akhale wachangu pakumvetsera, wodekha poyankhula, wosakwiya msanga.
  7143. Jas 1:20 Pakuti mkwiyo wa munthu si ubala chilungamo cha Mulungu.
  7144. Jas 1:21 Mwa ichi chotsani chinyanso chonse ndi chichulukiro cha choyipa, ndipo landirani ndi chifatso mawu owokedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.
  7145. Jas 1:22 ¶Koma khalani akuchita mawu, ndipo wosati akumva kokha, kudzinyenga eni nokha.
  7146. Jas 1:23 Pakuti ngati munthu ali wakumva mawu, ndipo wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirore:
  7147. Jas 1:24 Pakuti wadziyang’anira yekha, napita pa njira yake, ndipo nthawi yomweyo nayiwala adali munthu wotani.
  7148. Jas 1:25 Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro la ufulu, napitirira [m’menemo], ameneyo posakhala wakumva wakuyiwala, komatu wakuchita wa ntchitoyo, munthu amaneyu adzakhala wodala m’kuchita kwake.
  7149. Jas 1:26 Ngati wina adziyesera kuti ali wopembedza, ndiye wosamanga lirime lake, koma anyenga mtima wake mwini, kupembedza kwake kwa munthu uyu [kuli] kopanda pake.
  7150. Jas 1:27 Chipembedzo choyera ndi chosadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndi ichi, Kuchezera ana ndi amayi amasiye m’chisawutso chawo, [ndi] kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ochokera ku dziko lapansi.
  7151. Jas 2:1 Abale anga, musakhale nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, [Ambuye] wa ulemerero, ndi kusamala mawonekedwe a anthu.
  7152. Jas 2:2 Pakuti akabwera mu msonkhano wanu munthu wovala mphete ya golide, ndi chovala chokongoletsa, ndipo akabweranso munthu wosawuka m’chovala chalitsiro;
  7153. Jas 2:3 Ndipo inu mukapereka ulemu kwa iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pa malo abwino; ndipo mukanena kwa wosawukayo, Iwe ima uko, kapena khala pansi pa mpando wa mapazi anga:
  7154. Jas 2:4 Kodi pamenepo simudasiyanitsa mwa inu nokha, ndipo mwakhala woweruza woganizira zoyipa?
  7155. Jas 2:5 Mverani, abale anga wokondedwa, Kodi Mulungu sadasankha wosawuka a dziko lapansi wolemera m’chikhulupiriro, ndi wolowa nyumba a ufumu umene adawulonjeza kwa iwo akumkonda iye?
  7156. Jas 2:6 Koma inu mwanyoza wosawuka. Kodi achuma sakusawutsani inu, nakukokerani iwo ku mabwalo a milandu?
  7157. Jas 2:7 Kodi sachitira mwano iwowa dzina lolemekezekali limene mwa ilo inu muyitanidwa nalo?
  7158. Jas 2:8 Ngati inu mudzakwaniritsa lamulolo la chifumu monga mwa malembo, Uzikonda woyandikana naye monga udzikonda wekha, muchita bwino:
  7159. Jas 2:9 Koma ngati mulemekeza mawonekedwe a munthu, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga wolakwa.
  7160. Jas 2:10 Pakuti aliyense amene adzasunga lamulo lonse, ndipo tsono akakhumudwa pa [gawo] limodzi, iyeyu ali wochimwira onse.
  7161. Jas 2:11 Pakuti iye amene adanena, Usachite chigololo, adatinso, Usaphe. Tsopano ngati iwe ukapanda kuchita chigololo, koma iwe ukapha, iwe wakhala wolakwira lamulo.
  7162. Jas 2:12 Motero inu yankhulani, ndipo motero chitani, monga iwo amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.
  7163. Jas 2:13 Pakuti adzakhala ndi chiweruziro chopanda chifundo, iye amene sadawonetse chifundo; ndi chifundo chikondwera kutsutsana nacho chiweruziro.
  7164. Jas 2:14 N’chiyani [chimene icho] chipindula, abale anga, ngakhale munthu akanena ali nacho chikhulupiriro, ndipo alibe ntchito? Kodi chikhulupiriro chikhoza kumpulumutsa iye?
  7165. Jas 2:15 Ngati mbale kapena mlongo akakhala wamaliseche, ndipo chikamsowa chakudya cha pa tsiku.
  7166. Jas 2:16 Ndipo wina wa inu akanena kwa iwo, Mukani mu mtendere, mukafunde [inu] ndi kukhuta; osawapatsa iwo zinthu zimene ziri zosowa za ku thupi; n’chiyani [chimene icho] chipindula?
  7167. Jas 2:17 Momwenso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa, chikakhala chokha.
  7168. Jas 2:18 Inde, munthu akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndiri nazo ntchito: undiwonetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuwonetsa iwe chikhulupiriro changa mwa ntchito zanga.
  7169. Jas 2:19 Ukhulupirira iwe kuti pali Mulungu m’ modzi; uchita bwino: ziwandanso zikhulupirira, ndipo zinthunthumira.
  7170. Jas 2:20 Koma ufuna kudziwa kodi, Iwe munthu wopusa, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa?
  7171. Jas 2:21 Kodi Abrahamu kholo lathu, si adayesedwe wolungama ndi ntchito, pamene adapereka mwana wamwamuna Isake nsembe pa guwa la nsembe?
  7172. Jas 2:22 Upenya iwe momwe chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro?
  7173. Jas 2:23 Ndipo adakwaniritsidwa malembo amene anena, Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kwa iye kudayikidwa chilungamo; ndipo adatchedwa Bwenzi la Mulungu:
  7174. Jas 2:24 Mupenya tsono momwe ndi ntchito munthu ayesedwa wolungama, osati ndi chikhulupiriro chokha.
  7175. Jas 2:25 Momwemonso Rahabi mkazi wadamayo sadayesedwa wolungama ndi ntchito, pamene adalandira amithenga, ndipo adawatulutsa [iwo] adzere njira yina?
  7176. Jas 2:26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, kotero chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufanso.
  7177. Jas 3:1 Abale anga, musakhale aphunzitsi ambiri, podziwa tidzalandira kuweruzidwa kwakukulu.
  7178. Jas 3:2 Pakuti mu zinthu zambiri tikhumudwitsa ambiri. Ngati munthu aliyense sakukhumudwitsa m’mawu, yemweyo [ali] munthu wangwiro, [ndipo] wokhoza kumanganso thupi lonse.
  7179. Jas 3:3 Tawonani, tiyikira akavalo zogwirira kamwa lawo, kuti atimvere ife; ndipo ife tipotolozanso thupi lawo lonse.
  7180. Jas 3:4 Tawonani zombonso, zimene zingakhale [izo] n’zazikulu kwambiri, ndipo zitengedwa ndi mphepo zolimba, komatu zikhotetsedwa ndi tsigiro laling’ono kwambiri, kulikonse kumene afuna wowongolera.
  7181. Jas 3:5 Kotero lirimenso monga chiwalo chaching’ono, ndipo lidzitamandira zinthu zazikulu. Tawonani, mitengo ya nkhalango imene kamoto kakang’ono kayatsa!
  7182. Jas 3:6 Ndipo lirime [ndi] moto; dziko la chosalungama: kotero ndi momwe lirime liri mwa ziwalo zathu, kuti lidetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe achibadwidwe; ndipo liyatsidwa ndi moto wa ku nyanja ya moto.
  7183. Jas 3:7 Pakuti mtundu uliwonse wa nyama, ndi wa mbalamenso, wa njoka, ndi wa zinthu za m’nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zizoloweretsedwa ndi anthu:
  7184. Jas 3:8 Koma lirime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; [liri] losaweruzika loyipa, lodzala ndi ululu wakupha.
  7185. Jas 3:9 Timayamika nalo Mulungu, ndiye Atate; ndi lomwero titemberera nalo anthu, amene adapangidwa monga mwa mafanizidwe a Mulungu.
  7186. Jas 3:10 Kuchokera m’kamwa momwemo mutuluka dalitso ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kukhala zotero.
  7187. Jas 3:11 Kodi kasupe atulutsa pa una womwewo madzi [wokoma] ndi owawa?
  7188. Jas 3:12 Kodi mtengo wa mkuyu, abale anga, ukhoza kubala ma olivi? Kapena mpesa, kubala nkhuyu? Kotero kasupe sakhoza kutulutsa madzi a mchere ndi wokoma.
  7189. Jas 3:13 Ndani [ali] munthu wanzeru ndi wovekedwa chidziwitso mwa inu? Awonetsere kuchokera m’makhalidwe ake abwino ntchito zake ndi nzeru yofatsa.
  7190. Jas 3:14 Koma ngati muli nako kaduka kowawa ndi chotetana m’mitima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho chowonadi.
  7191. Jas 3:15 Nzeru iyi siyotsika kuchokera m’mwamba, komatu [ili] ya pa dziko lapansi, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya za ziwanda.
  7192. Jas 3:16 Pakuti pomwe [pali] kaduka ndi zotetana, pamenepo [pali] chisokonekero ndi ntchito ya choyipa iliyonse.
  7193. Jas 3:17 Koma nzeru yochokera m’mwamba poyamba ili yoyera, kenaka yamtendere, yodekha, ndipo yosavuta kumveka bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, ndi yopanda chinyengo.
  7194. Jas 3:18 Ndipo chipatso cha chilungamo chili chofesedwa mu mtendere kwa iwo akuchita mtendere.
  7195. Jas 4:1 [Zibwera] kuchokera kuti nkhondo ndi zolimbana mwa inu? Kodi [sizichokera izo, inde] ku zilakolako zanu zoyipa zimene zichita nkhondo m’ziwalo zanu?
  7196. Jas 4:2 Mulakalaka, ndipo simukhala nazo: mukupha, ndipo mukhumba mukhale nazo, ndipo simukhoza kupeza: mulimbana ndi kuchita nkhondo; komatu simukhala nazo, chifukwa simupempha.
  7197. Jas 4:3 Inu mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha molakwika, kuti mukachimwaze [icho] pochita zilakolako zanu zoyipa.
  7198. Jas 4:4 Inu amuna ndi akazi achigololo, kodi simudziwa kuti ubwenzi ndi dziko lapansi ndi udani ndi Mulungu? Potero aliyense amene adzakhala bwenzi la dziko lapansi ndi mdani wa Mulungu.
  7199. Jas 4:5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe, Mzimuyo amene akhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?
  7200. Jas 4:6 Koma apatsa chisomo choposa. Mwa ichi iye anena, Mulungu akaniza wodzikuza, koma apatsa chisomo kwa wodzichepetsa.
  7201. Jas 4:7 Gonjerani eni nokha kwa Mulungu. Kanizani mdiyerekezi, ndipo adzathawa kuchoka kwa inu.
  7202. Jas 4:8 Yandikirani kwa Mulungu, ndipo iye adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja [anu, inu] wochimwa; ndipo yeretsani mitima [yanu], inu a mitima iwiri.
  7203. Jas 4:9 Khalani wosawutsidwa, bumani, lirani misozi: ndipo kuseka kwanu kusanduke kubuma, ndi chimwemwe [chanu] ku chisoni.
  7204. Jas 4:10 Dzichepetseni nokha pamaso pa Ambuye, ndipo iye adzakukwezani inu.
  7205. Jas 4:11 Musamanenerana zoyipa wina ndi mzake, abale, Iye wonenera zoyipa mbale [wake], ndipo aweruza mbale wake, anenera choyipa lamulo, ndipo aweruza lamulo: koma ngati iwe uweruza lamulo, si uli wochita lamulo, koma woweruza.
  7206. Jas 4:12 Pali wopereka lamulo m’modzi, amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga: iwe ndiwe yani woweruza mzako?
  7207. Jas 4:13 Bwerani tsopano, inu amene munena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mzinda wakuti, ndikukhala komweko chaka ndi kugula ndi kugulitsa, ndi kupeza phindu:
  7208. Jas 4:14 Pamene inu simudziwa chimene [chidzakhala] mawa. Pakuti moyo wanu uli chiyani? Uli tsono mthunzi, umene uwoneka kanthawi kakang’ono, ndi kenaka ukanganuka.
  7209. Jas 4:15 Mwa chimenechi [mudayenera] kunena, Ngati Ambuye alola, tidzakhala ndi moyo, ndi kuchita ichi, kapena icho.
  7210. Jas 4:16 Koma tsopano mudzitamandira m’kudzikuza kwanu: kudzitamandira kulikonse kotero kuli koyipa.
  7211. Jas 4:17 Choncho kwa iye amene adziwa kuchita chabwino, ndipo sachita [icho], kwa iye ndi tchimo.
  7212. Jas 5:1 Nanga tsopano, [inu] anthu achuma, lirani misonzi ndi kuchema chifukwa cha masawutso anu amene adzadza pa [inu].
  7213. Jas 5:2 Chuma chanu chavunda ndi zovala zanu zadyedwa ndi njenjete.
  7214. Jas 5:3 Golide wanu ndi siliva wanu zadyeka ndi dzimbiri; ndipo dzimbiri lake lidzakhala umboni woneneza inu, ndipo lidzadya nyama yanu monga ngati unali moto. Mwakundika chuma cha masiku wotsiriza.
  7215. Jas 5:4 Tawonani, malipiro a antchitowo amene adakolola m’minda yanu, amene inu muwasunga osawapatsa inu mwa chinyengo, afuwula: ndipo mafuwuwo a iwo amene akololawo adalowa m’makutu a Ambuye wamakamu.
  7216. Jas 5:5 Mwakhala m’moyo wodyerera pa dziko lapansi, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwanenepetsa mitima yanu, monga m’tsiku lakupha.
  7217. Jas 5:6 Inu mwatsutsa [ndipo] mwapha wolungamayo, [ndipo] iye sadakaniza inu.
  7218. Jas 5:7 ¶Choncho lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Tawonani, wam’munda alindira chipatso chamtengo wake cha dziko lapansi, ndipo ali ndi kuleza mtima ndi icho, kufikira iye akalandira mvula ya myundo ndi masika.
  7219. Jas 5:8 Khalani inunso woleza mtima; khazikitsani mitima yanu: pakuti kudza kwake kwa Ambuye kwayandikira.
  7220. Jas 5:9 Musayipidwe wina ndi mzake, abale, kuti mungatsutsidwe: tawonani, woweruza wayima pakhomo.
  7221. Jas 5:10 Tengani, abale anga, aneneri, amene adayankhula m’dzina la Ambuye, kukhala chitsanzo cha kumva zowawa, ndi cha kuleza mtima,
  7222. Jas 5:11 Tawonani, tiwawerengera kukhala wosangalala iwo amene apirira. Mwamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwawona chitsirizo cha Ambuye; kuti Ambuye ali wachisoni, ndi wachifundo chokoma.
  7223. Jas 5:12 Koma pamwamba pa zinthu zonse, abale anga, musalumbire, kungakhale mwa kutchula kumwamba, kapena mwa dziko lapansi, kapena mwa lumbiro lina lirilonse: koma inde wanu akhale inde, ndi iyayi [wanu], akhale iyayi; kuti mungagwe m’chiweruzo.
  7224. Jas 5:13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Iye ayimbe masalmo.
  7225. Jas 5:14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziyitanire akulu a mpingo; ndipo iwo apemphere pa iye, kumdzoza iye ndi mafuta m’dzina la Ambuye:
  7226. Jas 5:15 Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuwukitsa iye; ndipo ngati adachita machimo, adzakhululukidwa kwa iye.
  7227. Jas 5:16 Vomerezani zolakwa [zanu] wina kwa mzake, ndipo wina apempherere mzake kuti mukhoze kuchiritsidwa. Pemphero la chikhulupiriro cholimba ndi lochitachita la munthu wolungama lipindula kwakukulu.
  7228. Jas 5:17 Eliya adali munthu wakumva za mthupi zomwezi monga ife, ndipo adapemphera motsimikizira kuti mvula isavumbwe: ndipo siyidagwa mvula pa dziko lapansi zaka zitatu miyezi isanu ndi umodzi.
  7229. Jas 5:18 Ndipo iye adapempheranso, ndipo kumwamba kudapereka mvula, ndi dziko linabala zipatso zake.
  7230. Jas 5:19 Abale, ngati wina wa inu asochera kuchoka ku chowonadi, ndipo wina ambweza iye;
  7231. Jas 5:20 Adziwe iye, kuti iye amene abweza wochimwa ku njira yosochera yake adzapulumutsa moyo ku imfa, ndipo adzabisa machimo aunyinji.
  7232. 1Pe 1:1 Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa alendo wobalalika konse ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,
  7233. 1Pe 1:2 Wosankhidwa mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, kudzera m’chiyeretso cha Mzimu, kufikira ku kumvera ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo chikhale kwa inu, ndi mtendere, zichulukitsidwe.
  7234. 1Pe 1:3 ¶Adalitsike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, iye amene monga mwa chifundo chake chochuluka, watibalanso ife ku chiyembekezo chamoyo, mwa kuwuka kwa Yesu Khristu kwa akufa,
  7235. 1Pe 1:4 Ku kulandira cholowa chosavunda, ndi chosadetsa, ndi chosasuluka, chosungidwira inu kumwamba,
  7236. 1Pe 1:5 Amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
  7237. 1Pe 1:6 M’menemo inu mukondwera kwakukulu, kungakhale tsopano kwa kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu:
  7238. 1Pe 1:7 Kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo ali a mtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale chiyesedwa ndi moto, chikapezedwe chochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa kuwonekera kwa Yesu Khristu:
  7239. 1Pe 1:8 Amene mungakhale simudamuwona, inu mumkonda; mwa iye, mungakhale inu simumpenya [iye], komatu mukhulupirira, inu mukondwera ndi chimwemwe chosaneneka ndi chodzala ndi ulemerero:
  7240. 1Pe 1:9 Kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, [ngakhale] chipulumutso cha miyoyo [yanu].
  7241. 1Pe 1:10 Amene mwa chipulumutso chimene aneneri achifunafuna ndi kufufuza mosamalitsa, amene adanenera za chisomo [chimene chikadabwera] pa inu.
  7242. 1Pe 1:11 Kufufuza chiyani, kapena nthawi yotani Mzimu wa Khristu amene anali mwa iwo adalozera, pamene adachitiratu umboni wa masawutso a Khristu, ndi ulemerero umene unayenera kutsatira.
  7243. 1Pe 1:12 Kwa amene kudavumbulutsidwa, wosati kwa iwo eni, koma kwa ife, adatumikira zinthuzo, zimene zawuzidwa kwa inu mwa iwo amene adalalikira uthenga wabwino kwa inu ndi Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba; zinthu zimene angelo adakhumba kuwonamo.
  7244. 1Pe 1:13 ¶Mwa ichi mangani m’chiwuno cha malingaliro anu, mukhale wodzisunga, ndipo muyembekeze mpaka kumapeto chisomo chimene chiyenera kubweretsedwa kwa inu pa vumbulutso la Yesu Khristu;
  7245. 1Pe 1:14 Monga ana womvera, wosadzifanizitsa eni nokha monga mwa zilakolako zakale mu kusadziwa kwanu:
  7246. 1Pe 1:15 Koma monga iye wakuyitana inu ali woyera, khalani inunso woyera m’makhalidwe anu onse;
  7247. 1Pe 1:16 Chifukwa kwalembedwa, khalani inu woyera, pakuti ine ndine woyera.
  7248. 1Pe 1:17 Ndipo ngati mukayitana pa Atate, iye mopanda tsankho pakati pa anthu aweruza monga mwa ntchito ya munthu aliyense, khalani [pano] ndi mantha nthawi ya kukhala alendo kwanu:
  7249. 1Pe 1:18 Chifukwa inu mudziwa kuti simudawomboledwa ndi zinthu zovunda, [monga] golide ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe [wolandiridwa] ndi miyambo kuchokera kwa makolo anu;
  7250. 1Pe 1:19 Koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali wa Khristu, monga wa mwanawankhosa wopanda chirema ndi banga:
  7251. 1Pe 1:20 Amene ndithudi adasankhidwiratu asadakhazikike maziko a dziko lapansi, koma adawonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi kuchitira inu,
  7252. 1Pe 1:21 Amene mwa iye mukhulupirira mwa Mulungu, amene adamuwukitsa iye kwa akufa, ndi kumpatsa iye ulemerero; kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zikhoze kukhala pa Mulungu.
  7253. 1Pe 1:22 Powona mwayeretsa moyo wanu mwa kumvera chowonadi mwa Mzimu ku chikondi chosanyenga cha pa abale, [onani kuti] mukondane kwenikweni wina ndi mzake ndi mtima woyera:
  7254. 1Pe 1:23 Wobadwanso mwatsopano, osati ndi mbewu yowola, koma yosawola, mwa Mawu a Mulungu, amene akhala moyo ndipo akhala kwa muyaya.
  7255. 1Pe 1:24 Popeza, matupi onse [ali] ngati udzu, ndipo ulemerero wonse wa munthu ngati duwa la udzu. Udzuwo ufota, ndi duwa lake ligwa:
  7256. 1Pe 1:25 Koma mawu a Ambuye akhala kwa muyaya. Ndipo awa ndiwo mawu amene mwa uthenga wabwino alalikidwa kwa inu.
  7257. 1Pe 2:1 Mwa ichi pakutaya kufunirana choyipa konse, ndi chinyengo chonse, ndi mawonekedwe wonyenga, ndi kaduka, ndi mayankhulidwe aliwonse woyipa,
  7258. 1Pe 2:2 Monga makanda obadwa kumene, khumbani mkaka wopanda chinyengo wa mawu, kuti mukakule nawo:
  7259. 1Pe 2:3 Ngati kukhala kotero kuti mwalawa kuti Ambuye ali wachisomo.
  7260. 1Pe 2:4 Kwa iye amene pakudza, [monga ku] mwala wamoyo, wokanidwatu ndithu ndi anthu, koma wosankhika ndi Mulungu, wamtengo wake,
  7261. 1Pe 2:5 Inunso, ngati miyala yamoyo, mwamangidwa nyumba ya uzimu, ansembe woyera mtima, kukapereka nsembe za uzimu, zolandiridwa kwa Mulungu mwa Yesu Khristu.
  7262. 1Pe 2:6 Mwa ichi kwalembedwa m’malemba, Tawonani, ndiyika m’Ziyoni mwala waukulu wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wapatali: ndipo iye wokhulupirira iye sadzanyazitsidwa.
  7263. 1Pe 2:7 Kwa inu tsono amene mukhulupirira, [ali wa] mtengo wapatali: koma kwa iwo amene akhala wosamvera, mwala umene womangawo adawukana, womwewo wapangidwa mutu wa pa ngodya.
  7264. 1Pe 2:8 Ndipo mwala wakukhumudwitsa, ndi thanthwe lophunthwitsa, [ngakhale kwa iwo] akukhumudwa pa mawu, pokhala wosamvera: kumenekonso iwo adayikidwako.
  7265. 1Pe 2:9 Koma inu [ndinu] mbadwa zosankhika, ansembe achifumu, fuko loyera [mtima], anthu a mwini wake; kotero kuti mukawonetsere matamando a iye amene adakuyitani kukutulutsani mumdima kulowa kuwunika kwake kodabwitsa:
  7266. 1Pe 2:10 Amene mu nthawi yakale [si mudali] anthu, koma tsopano [muli] anthu a Mulungu: amene kale simudalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
  7267. 1Pe 2:11 Wokondedwa kwambiri, ine ndikudandawulirani [inu] ngati alendo ndi wogonera, mupewe zilakolako za thupi, zimene zichita nkhondo kutsutsana ndi moyo;
  7268. 1Pe 2:12 Pokhala ndi makhalidwe anu wosanyenga pakati pa Amitundu: kuti, m’mene akamba za inu ngati wochita zoyipa, akhoze ndi ntchito [zanu] zabwino, zimene akadzaziwona, akalamekeze Mulungu m’tsiku loyenderedwa.
  7269. 1Pe 2:13 Gonjerani eni nokha kwa zoyikika zonse za anthu chifukwa cha Ambuye: ngakhale kutakhala kwa mfumu, monga mutu;
  7270. 1Pe 2:14 Kapena kwa akazembe, monga kwa iwo amene atumidwa ndi iye kukalanga wochita zoyipa, ndi ku chitamandiro cha iwo amene achita bwino.
  7271. 1Pe 2:15 Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti, ndikuchita kwabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu wopusa:
  7272. 1Pe 2:16 Monga mfulu, koma wosagwiritsa ntchito ufulu [wanu] monga chobisira chikhumbo chochitirana zoyipa, koma ngati atumiki a Mulungu.
  7273. 1Pe 2:17 Chitirani ulemu [anthu] onse. Kondani abale. Wopani Mulungu. Chitirani mfumu ulemu.
  7274. 1Pe 2:18 Antchito, [mukhale] wogonjera ambuye [anu] ndi kuwopa konse; osati kwa abwino ndi wodekha okha, komanso amakhalidwe oyipa.
  7275. 1Pe 2:19 Pakuti [ichi] ndi choyamikika, ngati munthu chifukwa cha chikumbumtima kwa Mulungu apirira mu zopweteka, pakumva zowawa zosamuyenera.
  7276. 1Pe 2:20 Chifukwa cha chitamandiro [chanji], ngati, pamene mubwanyulidwa chifukwa cha zolakwa zanu, inu mudzachilola mopirira? Koma ngati, pamene muchita bwino, ndi kumva zowawa [chifukwa icho], muchilola mopirira, [ichi] ndi cholandirika ndi Mulungu.
  7277. 1Pe 2:21 Pakuti kwa ichi inu mudayitanidwa: pakutinso Khristu adamva zowawa chifukwa cha ife, kutisiyira ife chitsanzo, kuti inu mukalondole mapazi ake:
  7278. 1Pe 2:22 Amene sadachita tchimo, kapena chinyengo sichidapezedwa m’kamwa mwake:
  7279. 1Pe 2:23 Amene, pochitidwa chipongwe, sadabwezera chipongwe, pamene adamva zowawa, sadawopseza ayi, koma adadzipereka [iye mwini] kwa iye woweruza molungama:
  7280. 1Pe 2:24 Amene adasenza machimo athu mwini yekha mthupi mwake pamtengo, kuti ife, pokhala akufa ku machimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo: ndi mikwingwirima ya ameneyo inu mudachiritsidwa.
  7281. 1Pe 2:25 Pakuti mudali monga nkhosa zosochera; koma tsopano mwatembenukira kwa Mbusa ndi Woyang’anira wa miyoyo yanu.
  7282. 1Pe 3:1 Momwemonso, akazi inu, [mukhale] wogonjera kwa amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, iwonso akhoze kukodwa wopanda mawu mwa makhalidwe a akazi;
  7283. 1Pe 3:2 Pamene iwo awona makhalidwe anu woyera [kuphatikizapo] kuwopa kwanu.
  7284. 1Pe 3:3 Amene kukometsera kwanu kusakhale [kukometsera] kwa kunja, kwa kuluka tsitsi, ndi kuvala za golidi, kapena kwa kuvala chovala;
  7285. 1Pe 3:4 Koma [akhale] munthu wobisika wa mtima, m’chimene chili chosawola, [ndicho chokometsera] cha mzimu wofatsa ndi wachete, chimene pamaso pa Mulungu cha mtengo wake wapatali.
  7286. 1Pe 3:5 Pakuti mu njira iyi mu nthawi yakale akazinso woyera mtima, amene adadalira mwa Mulungu, adadzikometsera eni wokha, pokhala wogonjera kwa amuna awo a iwo wokha:
  7287. 1Pe 3:6 Monganso Sara adamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye: amene inu muli ana ake akazi, pokhapokha mukachita bwino, osawopa chowopsa chilichonse.
  7288. 1Pe 3:7 Momwemonso, amuna inu, khalani nawo [iwo] monga mwa chidziwitso, kupereka ulemu kwa mkazi, monga kwa chotengera chofowoka, monganso wolandira cholowa pamodzi [ndi inu] wa chisomo cha moyo; kuti mapemphero anu asakhale wolepheretsedwa.
  7289. 1Pe 3:8 Chomaliza, [khalani inu] nonse a mtima umodzi, wokhala a chifundo wina ndi mzake, wokonda monga abale, [khalani] achisoni, [khalani] wodzichepetsa:
  7290. 1Pe 3:9 Osabwezera choyipa kwa choyipa, kapena kuchitira mwano kwa kuchitira mwano: komatu [bwezerani] dalitso; podziwa kuti ku ichi inu mwayitanidwa, kuti mulandire dalitso.
  7291. 1Pe 3:10 Pakuti iye amene adzakonda moyo, ndi kuwona masiku abwino, iye aletse lirime lake ku choyipa, ndi milomo yake kuti isayankhule chinyengo:
  7292. 1Pe 3:11 Iye apewe choyipa, nachite chabwino, afunefune mtendere, ndipo awutsatire uwo.
  7293. 1Pe 3:12 Pakuti maso a Ambuye ali pa wolungama, ndi makutu ake [ali otseguka] ku mapemphero awo: koma nkhope ya Ambuye [ili] yotsutsana ndi iwo amene achita zoyipa.
  7294. 1Pe 3:13 Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choyipa, ngati muli wotsatira a chimene chili chabwino?
  7295. 1Pe 3:14 Koma ngatinso mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, wosangalala inu: ndipo musawope kuwopsa kwawo, kapena mtima wanu usavutike;
  7296. 1Pe 3:15 Koma mumpatulikitse Ambuye Mulungu m’mitima yanu: ndipo [khalani] wokonzeka nthawi zonse [kupereka] yankho kwa munthu aliyense amene akukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu komatu ndi chifatso ndi mantha:
  7297. 1Pe 3:16 Pokhala nacho chikumbumtima chabwino; kuti, umo akunenerani inu zoyipa, monga wochita zoyipa, iwo akhoze kuchita manyazi iwo amene akunenerani mwabodza makhalidwe anu abwino mwa Khristu.
  7298. 1Pe 3:17 Pakuti [kuli] kwabwino, ngati chifuniro cha Mulungu chitero, kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, kusiyana ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoyipa.
  7299. 1Pe 3:18 Pakuti Khristunso wamva zowawa kamodzi chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa wosalungama, kuti akhoze kutitengera ife kwa Mulungu, wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mwa Mzimu:
  7300. 1Pe 3:19 Mwa chimenechonso adapita ndi kulalikira kwa mizimu idali m’ndende;
  7301. 1Pe 3:20 Imene m’nthawi yakale idali yosamvera, pamene kamodzi kuleza mtima kwa Mulungu kudalindira m’masiku a Nowa, pamene chombo chidali kukonzekera, m’menemo wowerengeka, ndiwo, miyoyo isanu ndi itatu idapulumutsidwa mwa madzi.
  7302. 1Pe 3:21 Chimenenso chili chifaniziro chimene [ndicho] ubatizo chimene chitipulumutsanso tsopano, (kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu yankho lake la chikumbumtima chabwino kwa Mulungu,) mwa kuwuka kwa akufa kwa Yesu Khristu:
  7303. 1Pe 3:22 Amene anapita kulowa kumwamba, ndipo ali pa dzanja lamanja la Mulungu; angelo, ndi ma ulamuliro ndi zimphamvu zimgonjera iye.
  7304. 1Pe 4:1 Popeza tsono Khristu adamva zowawa m’thupi chifukwa cha ife, mudziveke inu eninso ndi mtima womwewo: pakuti iye amene wamva zowawa m’thupi walekana nalo tchimo;
  7305. 1Pe 4:2 Kuti nthawi [yake] yotsatira asakhalenso iye ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma ku chifuniro cha Mulungu.
  7306. 1Pe 4:3 Pakuti m’nthawi [yathu] yakale ikhoze kukwanira ife kuti idachita chifuniro cha Amitundu, pamene tidayendayenda ife m’kukhumba zonyansa, mzilakolako, kuledzera, madyerero, mayimwayimwa, ndi kupembedza mafano koyipa:
  7307. 1Pe 4:4 M’menemo iwo aganiza nchachilendo kuti simuthamanga ndi [iwo] kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, akuyankhula zoyipa za [inu]:
  7308. 1Pe 4:5 Amene adzayenera kunena wokha [zochita zawo] kwa iye amene ali wokonzeka kuweruza a moyo ndi akufa.
  7309. 1Pe 4:6 Pakuti chifukwa cha ichi ndicho chimene udalalikidwa uthenga wabwino kwa iwonso amene adafawo, kuti akhoze kuweruzidwa monga mwa anthu m’thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.
  7310. 1Pe 4:7 Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi: choncho khalani atcheru, ndipo dikirani m’mapemphero.
  7311. 1Pe 4:8 Pamwamba pa zinthu zonse mukhale nacho chikondano chenicheni pakati pa inu nokha: pakuti chikondano chidzakwirira unyinji wa machimo.
  7312. 1Pe 4:9 Gwiritsani ntchito kucherezana wina ndi mzake opanda kusungirana mangawa.
  7313. 1Pe 4:10 Monga munthu aliyense walandira mphatsoyo, [koteronso] mutumukire yomweyo wina ndi mzake, ngati adindo abwino a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu.
  7314. 1Pe 4:11 Ngati ayankhula munthu wina, [iyeyu ayankhule] ngati manenedwe a Mulungu; ngati munthu wina atumikira, [iyeyu achite ichi] monga mwa kuthekera kumene Mulungu apatsa: kuti Mulungu m’zinthu zonse alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene kwa iye kukhale ulemerero ndi ulamuliro ku nthawi za nthawi. Amen.
  7315. 1Pe 4:12 Wokondedwa, musaganize ichi n’chachilendo kukhudza za mayesedwe amoto amene ali kukuyesani inu, ngati kuti chinthu china cha chilendo chidachitika kwa inu:
  7316. 1Pe 4:13 Koma kondwerani, popeza inu muli wolawana nawo a zowawa zake za Khristu; kuti, pamene ulemerero wake uvumbulutsidwa mukakhoze kusangalalanso ndikukondwera kopambana.
  7317. 1Pe 4:14 Ngati munyozedwa chifukwa cha dzina la Khristu, muli inu wodala; pakuti mzimu wa ulemerero ndi wa Mulungu apuma pa inu: kumbali yawo iye amamuyankhulira zoyipa, koma kumbali yanu iye alemekezedwa.
  7318. 1Pe 4:15 Koma wina wa inu asamve zowawa ngati wambanda, kapena [ngati] mbala, kapena [ngati] wochita zoyipa, kapena ngati wodudukira nkhani za anthu ena.
  7319. 1Pe 4:16 Koma ngati [munthu wina] akumva zowawa chifukwa choti ndi Mkhristu asachite iye manyazi; koma iye alemekeze Mulungu m’malo mwa ichi.
  7320. 1Pe 4:17 Chifukwa nthawi [yafika] kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu: koma ngati [ichi] poyamba [chiyamba] pa ife, kodi chitsiriziro chidzakhala chotani cha iwo wosamvera uthenga wabwino wa Mulungu?
  7321. 1Pe 4:18 Ndipo ngati wolungama apulumuka ndikuyesetsa kokhakokha, kodi wosapembedza ndi wochimwa adzawoneka kuti?
  7322. 1Pe 4:19 Mwa ichi aloleni iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu ayike kusunga kwa miyoyo yawo kwa [iye] mwa kuchita bwino, monga kwa Wolenga wokhulupirika.
  7323. 1Pe 5:1 Akulu amene ali mwa inu ine ndiwadandawulira, amenenso ine ndiri mkulu, ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndiponso wolandira nawo ulemerero umene udzavumbulutsidwa:
  7324. 1Pe 5:2 Dyetsani busa la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira limenero, osati mokangamiza; koma mwa kufuna; osapeza chuma mu njira zolakwika, koma [wa malingaliro] okonzeka.
  7325. 1Pe 5:3 Kapena monga okhala ambuye pa cholowa [cha Mulungu], koma wokhala zitsanzo za busalo.
  7326. 1Pe 5:4 Ndipo pamene adzawoneka Mbusa wamkulu, inu mudzalandira korona wa ulemerero amene sasuluka.
  7327. 1Pe 5:5 Momwemonso, inu achichepere, gonjerani inu eni kwa akulu. Inde, nonse [a inu] mukhale ogonjerana wina ndi mzake, ndipo muvale kudzichepetsa: pakuti Mulungu akaniza wodzikuza, koma apatsa chisomo kwa wodzichepetsa.
  7328. 1Pe 5:6 Choncho dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti akhoze kukukwezani panthawi yoyikika:
  7329. 1Pe 5:7 Kutaya nkhawa yanu yonse pa iye, pakuti iye asamalira inu.
  7330. 1Pe 5:8 Khalani wodzisunga, khalani tcheru, chifukwa mdani wanu mdiyerekezi, monga ngati mkango wobuma ayendayenda, kufunafuna wina amene ankhoza kumlikwira:
  7331. 1Pe 5:9 Ameneyo mumkanize mokhazikika m’chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo ziri nkumvedwa mwa abale anu ali m’dziko lapansi.
  7332. 1Pe 5:10 Koma Mulungu wa chisomo chonse, amene watiyitana ife kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu Yesu, mutamva inu zowawa kwa kanthawi kochepa, adzapanga inu angwiro, kukhazikitsa, kulimbikitsa, kupatsa bata [inu].
  7333. 1Pe 5:11 Kwa iye [kukhale] ulemerero ndi ulamuliro ku nthawi za nthawi. Amen.
  7334. 1Pe 5:12 Mwa Silvanasi, mbale wokhulupirika kwa inu, monga ndiganiza, ndalemba mwa chidule, kulimbikitsa, ndi kuchita umboni, kuti ichi ndi chisomo chowona cha Mulungu chimene inu muyimamo.
  7335. 1Pe 5:13 [Mpingo umene] uli ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi ndi [inu], ukupatsani moni; momwenso [achita] Markasi mwana wanga wamwamuna.
  7336. 1Pe 5:14 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsopsono cha chikondi. Mtendere [ukhale] ndi inu nonse amene muli mwa Khristu Yesu. Amen.
  7337. 2Pe 1:1 Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu, kwa iwo amene alandira chikhulupiriro cha mtengo wapatali chomwecho ndi ife kudzera m’chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu:
  7338. 2Pe 1:2 Chisomo ndi mtendere zichulukitsidwe kwa inu kudzera m’chidziwitso cha Mulungu, ndi cha Yesu Ambuye wathu,
  7339. 2Pe 1:3 Malingana ndi momwe mphamvu ya umulungu wake watipatsa ife zinthu zonse zimene [ziloza] ku moyo ndi umulungu, kudzera m’chidziwitso cha iye amene watiyitana ife ku ulemerero ndi ukoma:
  7340. 2Pe 1:4 Mwa izi zapatsidwa kwa ife malonjezano akulu ndithu ndi a mtengo wake: kuti mwa izi mukakhale wogawana nawo chikhalidwe cha umulungu wake, mutapulumuka ku chivundi chili pa dziko lapansi kudzera m’chilakolako.
  7341. 2Pe 1:5 Ndipo pambali pa ichi, kupereka changu chonse, muwonjezere ku chikhulupiriro chanu ubwino; ndi ku ubwino chidziwitso;
  7342. 2Pe 1:6 Ndipo ku chidziwitso kudziletsa; ndi ku kudziletsa chipiriro; ndi ku chipiririro umulungu;
  7343. 2Pe 1:7 Ndi ku umulungu chisamaliro cha pa abale; ndi ku chisamaliro cha pa abale chikondi.
  7344. 2Pe 1:8 Pakuti ngati zinthu izi zikhala mwa inu, ndi kuchuluka, zimakupangani [inu kuti musakhale] wowuma kapena wosabala zipatso mu chidziwitso cha Ambuye wathu Yesu Khristu.
  7345. 2Pe 1:9 Koma iye amene alibe zinthu izi ali wakhungu, ndipo sangathe kuwona patali, ndipo wayiwala kuti anatsukidwa ku machimo ake akale.
  7346. 2Pe 1:10 Mwa ichi makamaka, abale, chitani [khama ndi] changu kukhazikitsa mayitanidwe ndi masankhulidwe anu: pakuti mukachita zinthu izi, simukhumudwa konse ayi.
  7347. 2Pe 1:11 Pakuti chotero polowera padzapatsidwa kwa inu ochuluka, kulowera mu ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.
  7348. 2Pe 1:12 Mwa ichi, ine sindidzalekerera kukukumbutsani inu nthawi zonse za zinthu izi, mungakhale inu muzidziwa [izo], ndipo mukhazikike m’chowonadi cha tsopano lino.
  7349. 2Pe 1:13 Inde, ndichiganiza ichi choyenera, nthawi zonse pamene ndikhala ine mchihema ichi, kukutakasani inu pa kukumbutsani [inu];
  7350. 2Pe 1:14 Podziwa kuti posachedwa ndiyenera kuvula msasa wanga uwu, monganso ngakhale Ambuye wathu Yesu Khristu wandiwonetsa ine.
  7351. 2Pe 1:15 Kuwonjezera apo ine ndidzayesetsa kuti nditamwalira ine mudzakhale nthawi zonse wokumbukira zinthu izi.
  7352. 2Pe 1:16 Pakuti sitidatsata miyambi yokonzedwa mwakuchenjera, pamene tidakudziwitsani mphamvu ndi mabweredwe a Ambuye Yesu Khristu, koma tidali mboni zopenya ndi maso ukulu wake.
  7353. 2Pe 1:17 Pakuti adalandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pamene padabwera mawu wotere kwa iye wochokera ku ulemerero wopambana. Uyu ndi Mwana wanga wamwamuna wokondedwa amene mwa iye ndikondwera kwambiri.
  7354. 2Pe 1:18 Ndipo mawu awa amene adachokera kumwamba ife tidawamva, pamene tidali pamodzi ndi iye m’phiri loyera lija.
  7355. 2Pe 1:19 Tiri nawonso mawu a chinenero wokhazikika koposa; umene kwa iwo inu muchita bwino powasamalira, monga nyali imene iwunikira m’malo a mdima, kufikira ku mbandakucha, ndipo ikakwera nyenyezi yanthanda mu mitima yanu:
  7356. 2Pe 1:20 Podziwa ichi poyamba, kuti palibe uneneri wa lembo uli wa mamasulidwe a mwa ilo lokha,
  7357. 2Pe 1:21 Pakuti uneneri sudadze mu nthawi yakale ndi chifuniro cha munthu: koma anthu woyera a Mulungu adayankhula [monga iwo] adafulumizidwa ndi Mzimu Woyera.
  7358. 2Pe 2:1 Koma padalinso aneneri wonyenganso pakati pa anthuwo, monganso ngakhale padzakhala aphunzitsi wonyenga pakati pa inu, amene adzabweretsamo mwachinsinsi chiphunzitso chabodza chomwe chibweretsa mipatuko yowononga, ngakhale kukana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo eni chiwonongeko chakudza mwachangu.
  7359. 2Pe 2:2 Ndipo ambiri adzatsata njira zawo za chiwonongeko; pa chifukwa cha iwo njira ya chowonadi idzanenedwa zoyipa.
  7360. 2Pe 2:3 Ndipo kudzera m’chisiriro, iwo ndi mawu wonyenga adzakupangani malonda: amene chiweruzo chawo cha kale lonse sichidachedwa, ndipo chiwonongeko chawo sichiwodzera.
  7361. 2Pe 2:4 Pakuti ngati Mulungu sadalekerera angelo adachimwawo, koma adawaponya [iwo] pansi ku malo a mazunzo oyembekezera chiweruzo akufa ochimwa, ndipo anawayika [iwo] ku maunyolo amdima, asungike kufikira chiweruzo;
  7362. 2Pe 2:5 Ndipo sadalekerera dziko lapansi lakale, koma adapulumutsa Nowa [munthu] wachisanu ndi chitatu, mlaliki wa chilungamo, kubweretsamo chigumula pa dziko lapansi la wosapembedza;
  7363. 2Pe 2:6 Ndi kusandutsa mizinda ya Sodomu ndi Gomora phulusa adayitsutsa iyo mwa kuyigwetsa, kuwapanga iwo chitsanzo cha iwo amene mtsogolo akhale wosapembedza.
  7364. 2Pe 2:7 Ndipo adapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi amankhalidwe wonyansa a woyipa.
  7365. 2Pe 2:8 (Pakuti wolungama ameneyo pakukhala pakati pa iwo, mu kuwona ndi kumva, adazunza moyo [wake] wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito [zawo] zosayeruzika;)
  7366. 2Pe 2:9 Ambuye adziwa kupulumutsa wopembedza ku mayesero, ndi kusunga wosalungama kufikira tsiku lachiweruzo kuti akalangidwe:
  7367. 2Pe 2:10 Koma makamaka iwo akuyenda motsata zathupi m’chilakolako cha chidetso, napeputsa olamulira; Osawopa kanthu [ali iwowa], wotsata chifuniro cha iwo eni, sachita mantha kulankhulira zamwano akulu aulemu wawo.
  7368. 2Pe 2:11 Mosiyana ndi angelo, angakhale ali woposa mphamvu ndi wolimbitsa, sadambweretsa iwo chowatsutsa chamwano pamaso pa Ambuye.
  7369. 2Pe 2:12 Koma awa, ngati zamoyo zopanda nzeru, zopangidwa kuti zitengedwe ndi kuwonongedwa, alankhula zoyipa kwa zinthu zimene iwo sazimvetsa, ndipo adzawonongeka kwathunthu m’chivundi chawo eni;
  7370. 2Pe 2:13 Ndipo adzalandira mphotho ya chosalungama, monga iwo amene achitenga chinthu chabwino kuchita chiwawa m’nthawi ya masana. [Iwo ndiwo] mawanga ndi zirema, akukondwera eni ake m’madyerero ndi zinyengo zawo eni pamene akudya nanu;
  7371. 2Pe 2:14 Wokhala nawo maso wodzala ndi chigololo, ndipo sakhoza kuleka uchimo; kunyengerera miyoyo yosakhazikika: mtima umene iwo awuzoloweretsa ndi machitidwe wosirira; ana wotembereredwa:
  7372. 2Pe 2:15 Amene asiya njira yolunjika, ndipo asokera, atatsata njira ya Balamu mwana [wamwamuna] wa Bosori, amene adakonda malipiro a chosalungama;
  7373. 2Pe 2:16 Koma adadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwake: bulu wopanda mawu woyankhula ndi mawu a munthu adaletsa misala ya mneneriyo.
  7374. 2Pe 2:17 Iwo ali zitsime zopanda madzi, mitambo imene ingotengedwa ndi mphepo yamkuntho, amene kwa iwo mdima wakuda bii usungidwira kosatha.
  7375. 2Pe 2:18 Pakuti pamene ayankhula [mawu] wotukumuka kwambiri achabe, anyengerera kudzera mu zilakolako za thupi, ndi [kudzera] m’zonyansa [zambiri], iwo amene adali woyera adapulumuka kuchokera kwa iwo a wokhala m’cholakwa.
  7376. 2Pe 2:19 Pamene akuwalonjeza iwo ufulu, iwo eni ali atumiki achivundi: pakuti iye amene munthu agonjetsedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake.
  7377. 2Pe 2:20 Pakuti ngati iwo atapulumuka zodetsa za dziko lapansi kudzera mu chidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, iwo akodwanso m’menemo, ndipo agonjetsedwa, kutsiriza kwawo kuli koyipa koposa pachiyambi.
  7378. 2Pe 2:21 Pakuti kukadakhala kwa iwo chinthu chabwino akadapanda kudziwa njira ya chilungamo, kusiyana, ndikuti atayidziwa [iyo], kubwerera kuchoka ku lamulo loyera lopatsidwa kwa iwo.
  7379. 2Pe 2:22 Koma ichi chidawachitikira iwo monga mwa mwambi wowona, Galu wabwereranso ku masanzi ake; ndi nkhumba imene idasamba yabwereranso kukunkhulika m’thope.
  7380. 2Pe 3:1 Kalata yachiwiri iyi, abale, tsopano ndilembera kwa inu; mwa [onse awiri] amene ine nditakasa malingaliro anu woyera mwa njira ya kukukumbutsani:
  7381. 2Pe 3:2 Kuti mukumbukire mawu amene adalankhulidwa kale ndi aneneri woyera, ndipo ndi lamulo la ife la atumwi a Ambuye ndi Mpulumutsi:
  7382. 2Pe 3:3 Podziwa ichi poyamba, kuti masiku wotsiriza adzafika wonyoza, woyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,
  7383. 2Pe 3:4 Ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira muja makolo adamwalira, zonse zikhalabe monga [izo zinali] chiyambire cha chilengedwe.
  7384. 2Pe 3:5 Pakuti ichi ayiwala mwakufuna dala, kuti mwa mawu a Mulungu miyamba idakhala kale lomwe, ndi dziko lidayimirira kuchoka m’madzi ndi m’madzi:
  7385. 2Pe 3:6 Mwa izi dziko lapansi limene lidali masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka;
  7386. 2Pe 3:7 Koma miyamba ndi dziko lapansi, zimene ziri masiku ano, ndi mawu womwewo zayikika, zosungikira kumoto kukonzekera tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu wosapembedza.
  7387. 2Pe 3:8 Koma, wokondedwa, ichi chimodzi musakhale wosadziwa, kuti tsiku limodzi [likhala] kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.
  7388. 2Pe 3:9 Ambuye si ali wozengereza nalo lonjezano lake, monga anthu ena achiyesa chizengerezo; koma ali woleza mtima kwa ife, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike ku kulapa.
  7389. 2Pe 3:10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala mu usiku; m’mene miyamba idzapita ndi phokoso lalikulu, ndi za m’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko lapansinso ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa.
  7390. 2Pe 3:11 [Powona] kuti [tsono] zinthu izi zonse zidzasungunuka, kodi muyenera inu kukhala [anthu] wotani nanga m’makhalidwe wopatulika [wonse] ndi umulungu,
  7391. 2Pe 3:12 Akuyang’anira ndi kufulumirira ku kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m’menemo miyamba pokhala pamoto idzasungunuka ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu?
  7392. 2Pe 3:13 Ngakhale ziri choncho ife, monga mwa lonjezano lake, tiyang’anira miyamba yatsopano ndi dziko latsopano, m’menemo mukhala chilungamo.
  7393. 2Pe 3:14 Mwa ichi, wokondedwa, popeza muyang’anira zinthu zotero, chitani changu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, wopanda banga, ndi wopanda chirema.
  7394. 2Pe 3:15 Ndipo dziwerengereni [kuti] kupirira kwa Ambuye wathu [ndicho] chipulumutso; ngakhale monganso mbale wathu wokondedwa Paulo kolingana ndi nzeru zopatsidwa kwa iye wakulemberani inu;
  7395. 2Pe 3:16 Monganso mu makalata [ake] onse pokamba momwemo za zinthu izi; m’mene muli zinthu zina zovuta kuzimvetsetsa, zimene anthu iwo amene ali wosaphunzira ndi wosakhazikika apotoza, monganso [iwo] atero nawo malembo ena, ku chiwonongeko cha iwo eni.
  7396. 2Pe 3:17 Choncho, inu, wokondedwa, mudziwa [zinthu izi] kale, chenjerani kuti inunso, potengedwa ndi kulakwa kwa iwo wosayeruzika, mungagwe kuchoka ku chikhazikiko chanu.
  7397. 2Pe 3:18 Koma kulani mu chisomo, ndi mu chidziwitso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu. Kwa iye [kukhale] ulemerero tsopano ndi nthawi zamuyaya. Amen.
  7398. 1Jn 1:1 Icho chimene chidaliko kuyambira pachiyambi, chimene ife tachimva, chimene tachiwona ndi maso athu, chimene tachipenyerera, ndipo manja athu achigwira cha Mawu a moyo;
  7399. 1Jn 1:2 (Pakuti moyowo udawonetsedwa, ndipo ife tawuwona [iwo], ndi kuchita umboni, ndipo tiwonetsa kwa inu moyo wosatha umenewo, umene udali pamodzi ndi Atate, ndipo udawonetsedwa kwa ife;)
  7400. 1Jn 1:3 Icho chimene ife tachiwona ndi kuchimva tichilalikira ife kwa inu kuti inunso mukhoze kukhala ndi chiyanjano pamodzi ndi ife: ndipo zowona chiyanjano chathu [chili] ndi Atate, ndi Mwana wake wamwamuna Yesu Khristu.
  7401. 1Jn 1:4 Ndipo zinthu izi tilemba ife kwa inu kuti chimwemwe chanu chikhoze kukhala chodzadza.
  7402. 1Jn 1:5 Uwu tsono ndi uthenga tawumva kwa iye, ndipo tilalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuwunika, ndipo mwa iye mulibe mdima uliwonse.
  7403. 1Jn 1:6 Tikati kuti tiri ndi chiyanjano ndi iye, ndi kuyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita chowonadi:
  7404. 1Jn 1:7 Koma ngati tiyenda m’kuwunika, monga iye ali m’kuwunika, tikhala ndi chiyanjano wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Khristu Mwana wake wamwamuna utisambitsa kutiyeretsa ku uchimo wonse.
  7405. 1Jn 1:8 Tikanena kuti tiribe uchimo, tidzinyenga ife eni tokha, ndipo chowonadi sichili mwa ife.
  7406. 1Jn 1:9 Ngati tivomereza machimo athu, iye ali wokhulupirika ndi wolungama kutikhululukira machimo [athu], ndi kutiyeretsa ku chosalungama chilichonse.
  7407. 1Jn 1:10 Ngati tinena kuti sitidachimwe, timuyesa iye wonama, ndipo mawu ake si ali mwa ife.
  7408. 1Jn 2:1 Ana anga aang’onoang’ono, zinthu izi ine ndilembera kwa inu kuti musachimwe. Ndipo ngati munthu wina achimwa, tiri naye nkhoswe kwa Atate, Yesu Khristu wolungamayo:
  7409. 1Jn 2:2 Ndipo iye ndiye nsembe yothetsa mkwiyo ya machimo athu: koma osati athu wokha, komanso [machimo] a dziko lonse lapansi.
  7410. 1Jn 2:3 Ndipo umu tidziwa kuti timdziwa iye, ngati tisunga malamulo ake.
  7411. 1Jn 2:4 Iye wonena kuti, Ndimdziwa iye, koma sasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo chowonadi mulibe mwa iye.
  7412. 1Jn 2:5 Koma iye amene asunga mawu ake, mwa iyeyu ndithudi chikondi cha Mulungu chikhala changwiro: umu tidziwa kuti tiri mwa iye.
  7413. 1Jn 2:6 Iye amene anena kuti akhala mwa iye ayeneranso mwini wake kuyenda, monga adayenda iyeyo.
  7414. 1Jn 2:7 Abale, sindilembera lamulo latsopano kwa inu, komatu lamulo lakale limene mudali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo lakalero ndilo mawu amene mudawamva kuyambira pachiyambi.
  7415. 1Jn 2:8 Kenanso, ine ndilembera kwa inu lamulo latsopano, ndicho chimene chili chowona mwa iye ndi mwa inu: chifukwa mdima wapita, ndi kuwunika kowona tsopano kuli kuwala.
  7416. 1Jn 2:9 Iye amene anena kuti ali m’kuwunika, namuda mbale wake akhala ali mumdima ngakhale kufikira tsopano lino.
  7417. 1Jn 2:10 Iye amene akonda mbale wake akhala m’kuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.
  7418. 1Jn 2:11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima umenewo wachititsa khungu maso ake.
  7419. 1Jn 2:12 Ndikulemberani inu, ana aang’ono, popeza machimo anu akhululukidwa mwa dzina lake.
  7420. 1Jn 2:13 Ndikulemberani inu, atate, popeza mwamdziwa iye [amene] ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani inu, anyamata, popeza mwamlaka woyipayo. Ndikulemberani inu, ana aang’ono, popeza mwadziwa Atate.
  7421. 1Jn 2:14 Ndakulemberani inu, atate, popeza mwamdziwa iye [amene ali] kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani inu, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi Mawu a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woyipayo.
  7422. 1Jn 2:15 Musakonde dziko lapansi, kapena zinthu [zimene ziri] m’dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye.
  7423. 1Jn 2:16 Pakuti zonse zimene [ziri] m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi, ndi chilakolako cha maso, ndi matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ziri za dziko lapansi.
  7424. 1Jn 2:17 Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake: koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.
  7425. 1Jn 2:18 ¶Ana aang’ono, ndi nthawi yotsiriza iyi: ndipo monga mwamva kuti wotsutsa Khristu adzadza, ngakhale tsopano alipo wotsutsa Khristu ambiri; m’menemo ife tidziwa kuti iyi ndi nthawi yotsiriza.
  7426. 1Jn 2:19 Adatuluka mwa ife, komatu si adali a ife; pakuti akadakhala a ife; [mosakayikira] akadapitirirabe kukhala ndi ife: koma [iwo adatuluka], kuti iwo akhoze kuwonetsedwa kuti iwo onse sadali a ife.
  7427. 1Jn 2:20 Koma inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zinthu zonse.
  7428. 1Jn 2:21 Sindidakulemberani inu chifukwa simudziwa chowonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera ku chowonadi.
  7429. 1Jn 2:22 Wabodza ndi ndani koma iye wokanayo kuti Yesu si ali Khristu? Iye ndiye wotsutsa Khristu, amene akana Atate ndi Mwana wamwamuna.
  7430. 1Jn 2:23 Wina aliyense wokana Mwana wamwamuna, yemweyo alibe Atate: [koma] iye wovomereza Mwana wamwamuna ali ndi Atatenso.
  7431. 1Jn 2:24 Lolani chimenecho chikhale mwa inu, chimene mwachimva kuyambira pachiyambi. Ngati chimene mwachimva kuyambira pachiyambi chikhalabe mwa inu, inunso mudzapitirira kukhalabe mwa Mwana wamwamuna, ndi mwa Atate.
  7432. 1Jn 2:25 Ndipo ili ndi lonjezano limene iye adatilonjezera ife, [ndiwo] moyo wosatha.
  7433. 1Jn 2:26 [Zinthu] izi ndakulemberani inu zokhudza iwo akukopa inu.
  7434. 1Jn 2:27 Koma kudzoza kumene mwalandira kuchokera kwa iye kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni: koma monga kudzoza komweko kuphunzitsa inu za zinthu zonse, ndipo kuli kowona, sikuli bodza ayi, ndipo monga kwa kuphunzitsa inu, mudzakhala mwa iye.
  7435. 1Jn 2:28 Ndipo tsopano, ana aang’ono, khalani mwa iye; kuti, pamene iye adzawonekera, tidzakhoze kukhala nako kulimbika mtima, ndi kusachita manyazi pamaso pa iye pa kudza kwake.
  7436. 1Jn 2:29 Ngati mudziwa kuti ali wolungama, mudziwa kuti aliyensenso wochita chilungamo ali wobadwa mwa iye.
  7437. 1Jn 3:1 Tawonani, chikondi chotani chotere cha Atate chimene chapatsidwa kwa ife, kuti titchedwe ana amuna a Mulungu: Choncho dziko lapansi silitidziwa ife, popeza silidamdziwe iye.
  7438. 1Jn 3:2 Wokondedwa, tsopano tiri ana amuna a Mulungu, ndipo sichidawoneke chimene tidzakhala: Koma tidziwa kuti, pamene adzawoneka iye, tidzakhala wofanana ndi iye; pakuti tidzamuwona iye monga ali.
  7439. 1Jn 3:3 Ndipo munthu aliyense amene ali nacho chiyembekezo ichi mwa iye, adziyeretse yekha, monga iyeyu ali woyera.
  7440. 1Jn 3:4 Aliyense wakuchita tchimo achimwiranso lamulo: pakuti tchimo ndilo kuswa lamulo.
  7441. 1Jn 3:5 Ndipo mudziwa kuti iyeyu adawonetsedwa kudzachotsa machimo athu; ndipo mwa iye mulibe tchimo.
  7442. 1Jn 3:6 Aliyense wokhala mwa iye sachimwa ayi: aliyense wakuchimwa sadamuwone iye, kapena kumdziwa iye.
  7443. 1Jn 3:7 Ana aang’ono, musalole munthu akusokeretseni inu: iye wochita chilungamo ali wolungama, monga iyeyu ali wolungama.
  7444. 1Jn 3:8 Iye wochita tchimo ali wake wa mdiyerekezi; pakuti mdiyerekezi adachimwa kuyambira pachiyambi. Chifukwa cha cholinga ichi Mwana wamwamuna wa Mulungu adawonetsedwa, ndiko kuti akhoze kuwononga ntchito za mdiyerekezi.
  7445. 1Jn 3:9 Aliyense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo; chifukwa mbewu yake ikhalabe mwa iye: ndipo sangachimwe, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.
  7446. 1Jn 3:10 M’menemo awonekera ana a Mulungu, ndi ana a mdiyerekezi: aliyense wosachita chilungamo si ali wochokera mwa Mulungu; ngakhale iye wosakonda mbale wake.
  7447. 1Jn 3:11 Pakuti uwu ndiwo uthenga mudawumva kuyambira pachiyambi, kuti tiyenera kukondana wina ndi mzake.
  7448. 1Jn 3:12 Osati monga Kayini, [amene] adali wochokera mwa woyipayo, ndipo adamupha mbale wake. Ndipo adamupha iye chifukwa chiyani? Popeza ntchito zake zidali zoyipa, ndi za mbale wake zolungama.
  7449. 1Jn 3:13 Musazizwe, abale anga, ngati likudani inu dziko lapansi.
  7450. 1Jn 3:14 Ife tidziwa kuti tachoka kufika ku imfa kulowa m’moyo, chifukwa tikonda abale. Iye amene sakonda mbale [wake] akhala mu imfa.
  7451. 1Jn 3:15 Aliyense womuda mbale wake ali wakupha munthu: ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.
  7452. 1Jn 3:16 Umo tizindikira chikondi [cha Mulungu], chifukwa iye adapereka moyo wake chifukwa cha ife: ndipo ife tiyenera kupereka miyoyo [yathu] chifukwa cha abale.
  7453. 1Jn 3:17 Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, ndipo awona mbale wake ali wosowa, ndipo atseka mtima [wa chifundo] kwa iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?
  7454. 1Jn 3:18 Ana anga aang’ono, tisakonde mu mawu, kapena ndi lirime, komatu m’kuchita ndi m’chowonadi.
  7455. 1Jn 3:19 Umo tizindikira kuti ife tiri a chowonadi, ndipo tidzakhazikitsa mitima yathu pamaso pake.
  7456. 1Jn 3:20 Pakuti ngati mtima wathu utitsutsa ife, Mulungu ali wamkulu woposa mtima wathu, ndipo adziwa zinthu zonse.
  7457. 1Jn 3:21 Wokondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa ife, [pamenepo] tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu.
  7458. 1Jn 3:22 Ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zinthu zimene ziri zokondweretsa pamaso pake.
  7459. 1Jn 3:23 Ndipo lamulo lake ndi ili, Kuti tikhulupirire pa dzina la Mwana wake wamwamuna Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mzake, monga iye adatipatsa ife lamulo.
  7460. 1Jn 3:24 Ndipo iye amene asunga malamulo ake akhala mwa iye, ndi iye mwa ameneyo. Ndipo m’menemo ife tidziwa kuti iye akhala mwa ife, mwa Mzimu amene adatipatsa ife.
  7461. 1Jn 4:1 Wokondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: chifukwa aneneri wonyenga ambiri apita kulowa m’dziko lapansi.
  7462. 1Jn 4:2 M’menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: Mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi uchokera mwa Mulungu:
  7463. 1Jn 4:3 Ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi suchokera kwa Mulungu: ndipo uwu ndiwo [mzimu] wa wokana Khristu, umene mudamva kuti uyenera kudza; ndipo ngakhale tsopano ulimo kale m’dziko lapansi.
  7464. 1Jn 4:4 Inu ndinu a Mulungu, ana aang’ono, ndipo mwapambana iwo: chifukwa ali wamkulu iye wakukhala mwa inu koposa iye wakukhala m’dziko lapansi.
  7465. 1Jn 4:5 Iwo ndiwo a dziko lapansi: choncho ayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera iwo.
  7466. 1Jn 4:6 Ife ndife a Mulungu: iye amene adziwa Mulungu atimvera; iye amene si ali wa Mulungu satimvera ife. Momwemo ife tidziwa mzimu wa chowonadi, ndi mzimu wachisokeretso.
  7467. 1Jn 4:7 ¶Wokondedwa, tikondane wina ndi mzake: pakuti chikondi ndi cha Mulungu; ndipo aliyense amene akonda, ali wobadwa kuchokera kwa Mulungu, ndipo adziwa Mulungu.
  7468. 1Jn 4:8 Iye amene sakonda sadziwa Mulungu; pakuti Mulungu ndiye chikondi.
  7469. 1Jn 4:9 Umo chidawonetsedwa chikondi cha Mulungu kwa ife, chifukwa kuti Mulungu adatuma Mwana wake wamwamuna wobadwa yekha alowe m’dziko lapansi, kuti tikhoze kukhala ndi moyo mwa iye.
  7470. 1Jn 4:10 Umu muli chikondi, sikuti ife tidakonda Mulungu, koma kuti iye adatikonda ife, ndipo adatuma Mwana wake wamwamuna [akhale] nsembe yothetsa mkwiyo chifukwa cha machimo athu.
  7471. 1Jn 4:11 Wokondedwa, ngati Mulungu adatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mzake.
  7472. 1Jn 4:12 Palibe munthu adawona Mulungu nthawi ina iliyonse. Ngati tikondana wina ndi mzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife.
  7473. 1Jn 4:13 M’menemo tidziwa ife kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, chifukwa adatipatsa ife cha Mzimu wake.
  7474. 1Jn 4:14 Ndipo ife tawona ndi kuchita umboni kuti Atate adatuma Mwana wamwamuna [kuti akhale] Mpulumutsi wa dziko lapansi.
  7475. 1Jn 4:15 Aliyense amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wamwamuna wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
  7476. 1Jn 4:16 Ndipo ife tadziwa ndi kukhulupirira chikondicho chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi; ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndi Mulungu akhala mwa iye.
  7477. 1Jn 4:17 M’menemu chikondi chathu chikhala changwiro, kuti tikhoze kukhala nako kulimbika mtima m’tsiku la chiweruziro: chifukwa monga iyeyu ali, momwemo tiri ife m’dziko lapansi.
  7478. 1Jn 4:18 Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitulutsa mantha: chifukwa mantha ali nacho chizunzo. Iye amene achita mantha sakhala wangwiro m’chikondi.
  7479. 1Jn 4:19 Ife tikonda iye, chifukwa anayamba iye kutikonda ife.
  7480. 1Jn 4:20 Ngati munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye amene sakonda mbale wake amene wamuwona, akonda Mulungu bwanji amene sadamuwona?
  7481. 1Jn 4:21 Ndipo lamulo ili tiri nalo lochokera kwa iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.
  7482. 1Jn 5:1 Aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu: ndipo yense wakukonda iye amene adabala akondanso iye amene adabadwa kuchokera mwa iye.
  7483. 1Jn 5:2 Ndi ichi tidziwa kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kusunga malamulo ake.
  7484. 1Jn 5:3 Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu; kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake si ali wolemetsa.
  7485. 1Jn 5:4 Pakuti chilichonse chimene chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi: ndipo ichi ndi chipambano chimene chigonjetsa dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.
  7486. 1Jn 5:5 Ndani iye amene agonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wamwamuna wa Mulungu?
  7487. 1Jn 5:6 Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, [ndiye] Yesu Khristu; wosati mwa madzi wokha, koma mwa madzi ndi mwazi. Ndipo ndi Mzimu amene achita umboni, chifukwa Mzimu ndiye chowonadi.
  7488. 1Jn 5:7 Pakuti pali atatu akuchita umboni kumwamba, Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera: ndipo iwo atatu ali m’modzi.
  7489. 1Jn 5:8 Ndipo pali atatu akuchita umboni m’dziko lapansi, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi: ndipo awa atatu agwirizana mwa m’modzi.
  7490. 1Jn 5:9 Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uli oposa: pakuti uwu ndi umboni wa Mulungu umene iye wachita umboni za Mwana wake wamwamuna.
  7491. 1Jn 5:10 Iye amene amkhulupirira Mwana wamwamuna wa Mulungu ali nawo umboni mwa iye yekha: iye wosakhulupirira Mulungu amupanga iye kukhala wonama; chifukwa iye sakhulupirira umboni wa Mulungu adawupereka wa Mwana wake wamwamuna.
  7492. 1Jn 5:11 Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu wapereka kwa ife moyo wosatha, ndi moyo umene uli mwa Mwana wake wamwamuna.
  7493. 1Jn 5:12 Iye amene ali ndi Mwana wamwamuna ali nawo moyo; [ndipo] iye amene alibe Mwana wamwamuna wa Mulungu alibe moyo.
  7494. 1Jn 5:13 Zinthu izi ndakulemberani inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wamwamuna wa Mulungu; kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, ndi kuti mukhoze kukhulupirira padzina la Mwana wamwamuna wa Mulungu.
  7495. 1Jn 5:14 Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako mwa iye, kuti, ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake atimvera ife:
  7496. 1Jn 5:15 Ndipo ngati tidziwa kuti atimvera, chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tiri nazo zinthu izi tinazipempha kwa iye.
  7497. 1Jn 5:16 Ngati wina awona mbale wake ali kuchimwa tchimo [limene liri] losati la ku imfa, apemphe, ndipo iye adzampatsa iye moyo wa iwo akuchita tchimo losati la ku imfa. Pali tchimo la ku imfa: sindinena kuti mupemphere za ilo.
  7498. 1Jn 5:17 Chosalungama chilichonse ndi uchimo: ndipo pali tchimo losati la ku imfa.
  7499. 1Jn 5:18 Tidziwa kuti yense wobadwa mwa Mulungu sachimwa; koma iye wobadwa mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woyipayo samkhudza.
  7500. 1Jn 5:19 [Ndipo] tidziwa ife kuti tiri a Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa choyipa.
  7501. 1Jn 5:20 Ndipo tidziwa kuti Mwana wamwamuna wa Mulungu wafika, ndipo watipatsa ife kumvetsetsa, kuti tikhoze kumdziwa iye amene ali wowona, ndipo ife tiri mwa wowonayo, [ndiye] mwa Mwana wake wamwamuna Yesu Khristu. Uyu ndiye Mulungu wowona, ndi moyo wosatha.
  7502. 1Jn 5:21 Ana aang’ono, dzisungireni inu eni nokha kupewa mafano. Amen.
  7503. 2Jn 1:1 Mkuluyo kwa mkazi wosankhika ndi ana ake, amene ine ndimkonda m’chowonadi; ndipo osati ine ndekha, komanso iwo onse amene adziwa chowonadi;
  7504. 2Jn 1:2 Chifukwa cha chowonadi, chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha.
  7505. 2Jn 1:3 Chisomo chikhale ndi inu, chifundo, [ndi] mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kuchokera kwa Ambuye Yesu Khristu, Mwana wamwamuna wa Atate, m’chowonadi ndi m’chikondi.
  7506. 2Jn 1:4 Ndinakondwera kwakukulu kuti ndapeza za ana anu alikuyenda m’chowonadi, monga tidalandira lamulo lochokera kwa Atate.
  7507. 2Jn 1:5 Ndipo tsopano ndikudandawulirani inu, mkazi, wosati monga ndidalembera lamulo latsopano kwa inu, koma lomwero limene tidali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake.
  7508. 2Jn 1:6 Ndipo ichi ndi chikondi, kuti tiyenda motsatira malamulo ake. Ili ndi lamulo, Kuti, monga inu mwamva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo:
  7509. 2Jn 1:7 Pakuti wonyenga ambiri alowa m’dziko lapansi, amene savomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi. Ameneyu ndi wonyenga ndi wokana Khristu.
  7510. 2Jn 1:8 Mudzipenyerere nokha, kuti tisataye zimene tidazichita, koma kuti tilandire mphotho yathunthu.
  7511. 2Jn 1:9 Aliyense amene achimwa, ndipo sakhala m’chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Iye amene akhala m’chiphunzitso cha Khristu, iye ali nawo Atate ndi Mwana wa mwamuna.
  7512. 2Jn 1:10 Ngati akadza wina aliyense kwa inu, ndipo sabweretsa chiphunzitso ichi, musamulandire iye m’nyumba [mwanu], ndipo musamulonjere iye:
  7513. 2Jn 1:11 Pakuti iye wakumulonjera iye ayanjana nazo ntchito zake zoyipa.
  7514. 2Jn 1:12 Pokhala nazo zinthu zambiri zakukulembera kwa inu, ine sindifuna [kulemba] ndi pepala ndi cholembera: koma ndikhulupirira kudza kwa inu, ndi kuyankhula nanu maso ndi maso, kuti chimwemwe chathu chikhoze kukhala chodzaza.
  7515. 2Jn 1:13 Ana a mlongo wako wosankhika, akupatsani inu moni. Amen.
  7516. 3Jn 1:1 Mukuluyo kwa Gayasi wokondedwa, amene ndimkonda m’chowonadi.
  7517. 3Jn 1:2 Wokondedwa, ine ndikhumba pamwamba pa zinthu zonse kuti iwe ulemere ndi kukhala m’thanzi, monga moyo wako ulemera.
  7518. 3Jn 1:3 Pakuti ndidakondwera kwakukulu, pamene adafika abale ndi kuchita umboni za chowonadi chomwe chili mwa iwe, monganso iwe umayenda m’chowonadi.
  7519. 3Jn 1:4 Ine ndiribe chimwemwe choposa koposa kumva kuti ana anga alikuyenda m’chowonadi.
  7520. 3Jn 1:5 Wokondedwa, iwe uchita mokhulupirika chilichonse chimene uchitira abale, ndi alendo womwe;
  7521. 3Jn 1:6 Amene achitira umboni za chikondi chako pamaso pa mpingo: amene ngati iwe uwaperekeza pa ulendo wawo monga mwa machitidwe a umulungu, iwe udzachita bwino:
  7522. 3Jn 1:7 Pakuti chifukwa cha dzina lake adatuluka, osalandira kanthu kalikonse kwa Amitundu.
  7523. 3Jn 1:8 Mwa ichi ife tiyenera kulandira wotere, kuti ife tikhoze kukhala wothandizana nawo ku chowonadi.
  7524. 3Jn 1:9 Ndidalembera kwa mpingo: koma Diyotrefesi, amene akonda kukhala woyamba wa iwo, satilandira ife ayi.
  7525. 3Jn 1:10 Mwa ichi, ngati ndikadza ine, ndidzakumbuka ntchito zake zimene iye achitazi, zakulankhula zosokonezeka pa ife ndi mawu otifunira zoyipa: ndipo posamkwanira izi, iye salandiranso abale iye yekha, ndipo awaletsa iwo wofuna kuwalandira, nawataya [iwo], nawachotsa mu mpingo.
  7526. 3Jn 1:11 Wokondedwa, osatsatira chimene chili choyipa, koma chimene chili chabwino. Iye amene achita zabwino ali wa Mulungu: koma iye amene achita zoyipa sanamuwone Mulungu.
  7527. 3Jn 1:12 Demetriyasi ali ndi mbiri yabwino kwa [anthu] onse, ndi ya chowonadi chomwe: inde, ndipo ifenso tichita umboni: ndipo mudziwa kuti umboni wathu uli wowona.
  7528. 3Jn 1:13 Ndinali nazo zinthu zambiri zakuti ndilembe, koma sindidzatero ndi inki ndi cholembera kulembera kwa iwe.
  7529. 3Jn 1:14 Koma ndikhulupirira kukuwona iwe msanga, ndipo tidzayankhulana maso ndi maso. Mtendere [ukhale] kwa iwe. Abwenzi [athu] akukupatsa moni. Uperekere moni kwa abwenzi mowatchula mayina awo.
  7530. Jud 1:1 Yuda, wantchito wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo wopatulidwa ndi Mulungu Atate, ndi wosungidwa mwa Khristu Yesu, [ndi] woyitanidwa:
  7531. Jud 1:2 Chifundo kwa inu, ndi mtendere ndi chikondi, zichulukitsidwe.
  7532. Jud 1:3 Wokondedwa, pamene ndidachita changu chonse chakulembera kwa inu za chipulumutso cha ife tonse, kudali kofunika kwa ine kulembera kwa inu ndi kulimbikitsa [inu] kuti mulimbane motsimikiza chifukwa cha chikhulupiriro chimene chinapatsidwa kamodzi kwa woyera mtima.
  7533. Jud 1:4 Pakuti pali anthu ena adakwawira m’seri, amene kale adayikidwiratu ku chiweruzo ichi, anthu wopanda umulungu, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chokhumba zonyansa, ndi kukana Ambuye Mulungu m’modzi, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.
  7534. Jud 1:5 Choncho ine ndikukumbutsani inu, ngakhale inu mudadziwapo izi kamodzi, za momwe Ambuye, atapulumutsa anthu kuwatulutsa m’dziko la Igupto, pambuyo pake adawononga iwo amene sadakhulupirira.
  7535. Jud 1:6 Ndi angelo amene sadasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu adasiya pokhala pawo, iye wawasunga m’singa zosatha pansi pa mdima kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.
  7536. Jud 1:7 Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuyizungulira m’chikhalidwe chomwecho, kudzipereka eni wokha kuchiwerewere, ndi kutsata zilakolako zathupi zachilendo, yayikidwa kukhala chitsanzo, yovutika kubwezeredwa kwa moto wosatha.
  7537. Jud 1:8 Momwemonso iwo awa olota odetsedwa ayipsa matupi, napeputsa ulamuliro, nalankhula zoyipa za maulemu.
  7538. Jud 1:9 Komatu Mikayeli mkulu wa angelo pakuchita makani ndi mdiyerekezi adatsutsana za thupi la Mose, sadayerekeze kumbweretsera iye chomtsutsa chamwano, koma adati, Ambuye akudzudzule iwe.
  7539. Jud 1:10 Koma iwowa alankhula zoyipa za zinthu zimene sazidziwa: ndipo zimene azidziwa mwa chibadwidwe, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi adzidetsa nazo iwo eni.
  7540. Jud 1:11 Tsoka kwa iwo! Pakuti apita m’njira ya Kayini, ndipo athamanga mwa kukonda chuma potsata chisokero cha Balamu chifukwa cha mphotho, ndipo anawonongeka m’chitsutsano cha Kore.
  7541. Jud 1:12 Awa ndiwo mawanga mu maphwando anu a chikondi, pamene akudya nanu pamodzi, akudzidyetsa eni wokha mopanda mantha: [iwo ali] mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo imene chipatso chake chifota, yopanda chipatso, yokufa kawiri, yozulidwa ku mizu;
  7542. Jud 1:13 Mafunde wowopsa a nyanja ya mchere, akuchita thovu la manyazi a iwo wokha; nyenyezi zoyendayenda, zomwe zasungidwira mdima wakuda bii wosatha.
  7543. Jud 1:14 Ndipo Enokenso, wachisanu ndi chiwiri kuchokera kwa Adamu, adanenera za zinthu izi, kunena kuti, Tawona, akudza Ambuye ndi woyera mtima ake zikwi khumi,
  7544. Jud 1:15 Kudzachitira chiweruzo pa onse, ndi kutsutsa onse amene ali wopanda umulungu pakati pa iwo onse pa zochita zopanda umulungu zawo zimene achita mwa kupanda umulungu, ndi pa [zokamba] zawo zolimba zimene wochimwa wopanda umulungu adayankhula pakutsutsa iye.
  7545. Jud 1:16 Awa ndi wong’ung’udza, wodandawula, akuyenda monga mwa zilakolako zawo; ndipo pakamwa pawo ayankhula mawu wodzikuza, akukhala nawo anthu a anthu m’kuwatama chifukwa cha kupindula.
  7546. Jud 1:17 ¶Koma, wokondedwa mukumbukire inu mawu wonenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu;
  7547. Jud 1:18 Momwe iwo adanena kwa inu [kuti] payenera kudzakhala wotonza pa nthawi yotsiriza, amene adzayenera kuyenda motsatira zilakolako zopanda umulungu za iwo eni.
  7548. Jud 1:19 Iwo ndiwo wodzipatukitsa wokha, a makhalidwe azilakolako za thupi, wosakhala naye Mzimu.
  7549. Jud 1:20 Koma inu, wokondedwa, podzimanga nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, kupemphera mu Mzimu Woyera,
  7550. Jud 1:21 Mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu, kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu kufikira ku moyo wosatha.
  7551. Jud 1:22 Ndipo kwa ena khalani [ndi] chifundo, kupangitsa kusiyana:
  7552. Jud 1:23 Ndipo ena muwapulumutse ndi mantha, kuwakwatula [iwo] ku moto; podana nawonso malaya wochitidwa mawanga ndi thupi.
  7553. Jud 1:24 Tsopano kwa iye amene akhoza kukusungani ku kugwa, ndi kukuperekani [inu] wopanda chirema pamaso pa ulemerero wake ndi chimwemwe chopitirira,
  7554. Jud 1:25 Kwa Mulungu wanzeru m’modzi yekha Mpulumutsi wathu, [kukhale] ulemerero ndi ufumu, ndi ulamuliro mphamvu, tsopano ndi ku nthawi zonse. Amen.
  7555. Rev 1:1 Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu adapereka kwa iye, achiwonetsere kwa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa; ndipo adatuma ndi kuchizindikiritsa [ichi] ndi mngelo wake kwa mtumiki wake Yohane:
  7556. Rev 1:2 Amene adachita umboni za mawu a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, ndi wa zinthu zonse zimene iye adaziwona.
  7557. Rev 1:3 Wodala [ali] iye amene awerenga, ndi iwo amene amva mawu a chinenero ichi, ndi kusunga zimene zalembedwa m’menemo: pakuti nthawi yayandikira.
  7558. Rev 1:4 ¶Yohane kwa mipingo isanu ndi iwiri imene ili mu Asiya: chisomo chikhale kwa inu, ndi mtendere, kuchokera kwa iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kuchokera kwa mizimu isanu ndi iwiri imene ili pamaso pa mpando wachifumu wake;
  7559. Rev 1:5 Ndi kuchokera kwa Yesu Khristu, [amene ali] mboni yokhulupirikayo, [ndi] wobadwa woyamba wa akufa, ndi kalonga wa mafumu a dziko lapansi. Kwa iye amene adatikonda ife, natisambitsa ku machimo athu mu mwazi wa iye mwini.
  7560. Rev 1:6 Ndipo watipanga ife tikhale mafumu ndi ansembe kwa Mulungu ndi Atate wake; kwa iye [kukhale] ulemerero ndi ulamuliro kufikira nthawi za nthawi. Amen.
  7561. Rev 1:7 Tawonani, iye adza ndi mitambo; ndipo diso lirilonse lidzampenya iye, ndi iwonso amene adampyoza iye: ndipo mafuko onse a padziko adzalira chifukwa cha iye. Ngakhale choncho, Amen.
  7562. Rev 1:8 Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi chitsiriziro, atero Ambuye, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvu yonse.
  7563. Rev 1:9 ¶Ine Yohane, amenenso ndiri mbale wanu, ndi woyanjana nanu m’chisawutso, ndi mu ufumu ndi chipiriro cha Yesu Khristu, ndidakhala pa chisumbu chotchedwa Patimos, chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi cha umboni wa Yesu Khristu.
  7564. Rev 1:10 Ndinali mu Mzimu pa tsiku la Ambuye, ndipo ndidamva kumbuyo kwanga mawu akulu, ngati a lipenga,
  7565. Rev 1:11 Kunena, ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza: ndipo, Chimene iwe upenya, lemba m’buku, nulitumize [ilo] kwa mipingo isanu ndi iwiri, imene ili mu Asiya; ku Efeso, ndi ku Smuna, ndi ku Pergamos, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sardis, ndi ku Filadefiya, ndi ku Laodikeya.
  7566. Rev 1:12 Ndipo ndidatembenuka kuti ndiwone wonena mawu amene adayankhula ndi ine. Ndipo nditatembenuka, ndidawona zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi;
  7567. Rev 1:13 Ndipo pakati pa zoyikapo nyali zisanu ndi ziwirizo [wina] wonga Mwana wamwamuna wa munthu, wovala chovala chofikira ku mapazi ake, atamangira lamba lagolidi pachifuwa.
  7568. Rev 1:14 Mutu wake ndi tsitsi [lake zidali] zoyera ngati ubweya, kuyera ngati chipale chofewa; ndipo maso ake [adali] ngati lawi la moto:
  7569. Rev 1:15 Ndi mapazi ake ngati mkuwa wosalala ndi wonyezimira, ngati kuti zidatenthedwa m’ng’anjo; ndi mawu ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.
  7570. Rev 1:16 Ndipo m’dzanja lake lamanja adali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: ndi mkamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse: ndipo nkhope yake ngati dzuwa liwala mu mphamvu yake.
  7571. Rev 1:17 Ndipo pamene ndidamuwona iye, ine ndidagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Ndipo adasanjika dzanja lake lamanja pa ine, kunena kwa ine, Usawope; ine ndine woyamba ndi wotsiriza:
  7572. Rev 1:18 Ine [ndi] amene ali wamoyo; ndipo ndidali wakufa; ndipo, tawona, ine ndiri wamoyo ku nthawi zonse, Amen; ndipo ndiri nawo mafungulo a nyanja ya moto ndi imfa.
  7573. Rev 1:19 Lemba zinthu zimene iwe waziwona, ndi zinthu zimene ziripo, ndi zinthu zimene zidzakhala mtsogolomo;
  7574. Rev 1:20 Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene iwe udaziwona mu dzanja langa lamanja, ndi zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri za golidi. Nyenyezi zisanu ndi ziwirizo ndiwo angelo a mipingo isanu ndi iwiri: ndipo zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri zimene iwe udaziwona ndiyo mipingo isanu ndi iwiri.
  7575. Rev 2:1 Kwa Mngelo wa mpingo wa ku Efeso lemba; Zinthu izi anena iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m’dzanja lake lamanja, iye amene ayenda pakati pa zoyikapo nyali zagolidi zisanu ndi ziwiri;
  7576. Rev 2:2 Ine ndidziwa ntchito zako, ndi ntchito zako zolemetsa, ndi chipiriro chako, ndi momwe mwakuti iwe sukhoza kulola iwo amene ali woyipa: ndipo udayesa iwo amene anena ali atumwi, ndipo si ali ayi, ndipo wawapeza iwo abodza:
  7577. Rev 2:3 Ndipo iwe walola, ndipo uli nacho chipiriro, ndipo chifukwa cha dzina langa wagwira ntchito zolemetsa, ndipo sudalema.
  7578. Rev 2:4 Komabe ndiri nako [kanthu] kotsutsana ndi iwe, chifukwa kuti udasiya chikondi chako choyamba.
  7579. Rev 2:5 Choncho kumbukira kumene iwe wagwerako, ndipo lapa, nuchite ntchito zoyamba; kapena apo ayi ine ndidzadza kwa iwe msanga, ndipo ndidzachotsa choyikapo nyali chako pamalo pake, pokhapokha iwe ulape.
  7580. Rev 2:6 Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolayitani, zimene inenso ndidana nazo.
  7581. Rev 2:7 Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena ku mipingo. Kwa iye amene apambana ine ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo, umene uli pakati pa Paradiyizi wa Mulungu;
  7582. Rev 2:8 ¶Ndipo kwa mngelo wa mpingo wa mu Smuna lemba; Zinthu izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene adali wakufa, koma ali ndi moyo;
  7583. Rev 2:9 Ine ndidziwa ntchito zako, ndi chisawutso chako, ndi umphawi, (komatu iwe uli wachuma) ndipo [ine ndidziwa] zonyoza Mulunguza iwo amene anena kuti ali Ayuda, ndipo si ali ayi, komatu [ali] sunagoge wa Satana.
  7584. Rev 2:10 Usawope china chilichonse cha zimene uti udzamve kuwawa: tawona, mdiyerekezi adzaponya [ena] a inu m’ndende, kuti inu mukhoze kuyesedwa; ndipo mudzakhala nacho chisawutso masiku khumi: khala iwe wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ine ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.
  7585. Rev 2:11 Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena kwa mipingo; Iye amene apambana sadzavulazidwa ndi imfa yachiwiri.
  7586. Rev 2:12 ¶Ndipo kwa mngelo wa mpingo wa mu Pergamos lemba; Zinthu izi anena iye amene akhala nalo lupanga lakuthwa lokhala ndi mbali ziwiri;
  7587. Rev 2:13 Ine ndidziwa ntchito zako, ndi kumene iwe ukhalako kuja, [ngakhale] kumene [uli] mpando wa Satana: ndipo ugwiritsitsa dzina langa, ndipo sudakane chikhulupiriro changa, angakhale m’masiku a Antipasi [adali] mboni yanga yokhulupirika yophedwa, amene adaphedwa pakati pa inu, kumene akhala Satana.
  7588. Rev 2:14 Komatu ine ndiri nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, chifukwa uli nawo kumeneko iwo akusunga chiphunzitso cha Balamu, amene adaphunzitsa Balaki kuponya [tsenga la] chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, ndi kuti achite chiwerewere.
  7589. Rev 2:15 Kotero iwe ulinawonso iwo akusunga chiphunzitso cha Anikolayitani, chinthu chimene ndidana nacho.
  7590. Rev 2:16 Lapa; apo ayi ndidzadza kwa iwe msanga, ndipo ndidzachita nkhondo kutsutsana ndi iwo ndi lupanga la mkamwa mwanga.
  7591. Rev 2:17 Iye amene ali nalo khutu, amve iye chimene Mzimu anena ku mipingo; Kwa iye amene apambana ine ndidzampatsa adye mana wobisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwa, limene munthu aliyense salidziwa koma iye wakuwulandira [uwo].
  7592. Rev 2:18 Ndipo kwa mngelo wa mpingo wa mu Tiyatira lemba; Zinthu izi anena Mwana wamwamuna wa Mulungu, wakukhala nawo maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wosalala ndi wonyezimira;
  7593. Rev 2:19 Ine ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi utumiki, ndi chikhulupiriro, ndi chipiriro chako, ndi ntchito zako zotsiriza [zikhala] zochuluka kuposa zoyambazo.
  7594. Rev 2:20 Koma ine ndiri nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, chifukwa iwe ulola mkazi uja Yezebeli, amene adzitcha yekha mneneri, kuphunzitsa ndi kukopa atumiki anga kuti achite chiwerewere, ndi kudya zinthu zoperekedwa nsembe ku mafano.
  7595. Rev 2:21 Ndipo ndampatsa iye mpata kuti alape kusiyana nacho chiwerewere chake; koma sakulapa.
  7596. Rev 2:22 Tawona, ndidzamponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo ndi iye ku chisawutso chachikulu, pokhapokha atalapa iwo kuleka ntchito zawo.
  7597. Rev 2:23 Ndipo ine ndidzapha ana ake ndi imfa; ndipo mipingo yonse idzadziwa kuti ine ndine amene ayesa malingaliro ndi mitima: ndipo ine ndidzapereka kwa aliyense wa inu monga mwa ntchito zanu.
  7598. Rev 2:24 Koma kwa iwe ndinena, ndi kwa ena onse a ku Tiyatira, ambiri a iwo amene alibe chiphunzitso ichi, ndi iwo amene sadadziwa zakuya za Satana; monga iwo anena, ine sindidzakusanjikizani inu katundu wina.
  7599. Rev 2:25 Koma chimene inu muli nacho [kale] gwiritsitsani kufikira ine ndidza.
  7600. Rev 2:26 Ndipo iye amene apambana, ndi kusunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzampatsa ulamuliro pa mayiko:
  7601. Rev 2:27 Ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo; monga zotengera za wowumba mbiya iwo adzaphwanyidwa mapale: monga inenso ndidalandira kwa Atate wanga.
  7602. Rev 2:28 Ndipo ndidzampatsa iye nyenyezi [ya nthanda], yam’bandakucha.
  7603. Rev 2:29 Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena ku mipingo.
  7604. Rev 3:1 Ndipo kwa mngelo wa mpingo wa mu Sardis lemba; Zinthu izi anena iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri; Ine ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo ndiwe wakufa.
  7605. Rev 3:2 Khala wodikira, ndipo limbikitsa zinthu zimene zitsalira, zimene ziri pafupi kufa: pakuti sindinapeza ntchito zako zangwiro pamaso pa Mulungu.
  7606. Rev 3:3 Choncho kumbukira momwe udalandirira ndi kumvera, ndipo gwiritsitsa, ndipo ulape. Choncho ngati iwe sudikira, ndidzafika pa iwe ngati mbala, ndipo sudzadziwa nthawi yake ndidzadza pa iwe.
  7607. Rev 3:4 Uli nawo mayina wochepa mu Sardis amene sanadetse zovala zawo; ndipo adzayenda ndi ine m’zoyera: pakuti ali woyenera.
  7608. Rev 3:5 Iye amene apambana, yemweyo adzavekedwa zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza dzina lake m’buku la moyo, koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.
  7609. Rev 3:6 Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena kwa mipingo.
  7610. Rev 3:7 ¶Ndipo kwa mngelo wa mpingo wa mu Filadefiya lemba; Zinthu izi anena iye amene ali Woyera, iye amene ali Wowona, iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, iye amene atsegula ndipo palibe munthu atseka, ndipo atseka, ndipo palibe munthu atsegula;
  7611. Rev 3:8 Ine ndidziwa ntchito zako: tawona ndayika pamaso pako khomo lotseguka, ndipo palibe munthu akhoza kutsekapo: pakuti uli nayo mphamvu yochepa, ndipo wasunga mawu anga, ndipo sudakane dzina langa.
  7612. Rev 3:9 Tawona, ndidzawapanga iwo a sunagoge wa Satana, amene anena ali Ayuda, ndipo iwo si ali ayi, koma anama; tawona, ndidzawadzetsa iwo ndi kulambira pa mapazi ako, ndi kudziwa kuti ine ndakukonda iwe.
  7613. Rev 3:10 Chifukwa chakuti iwe udasunga mawu a chipiriro changa, inenso ndidzakusunga mu ora la kuyesedwa, limene lidzadza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala pa dziko lapansi.
  7614. Rev 3:11 Tawona, ndidza msanga: gwiritsitsa chimene uli nacho, kuti munthu angalande korona wako.
  7615. Rev 3:12 Iye amene apambana ine ndidzampanga iye mzati wa mkachisi wa Mulungu wanga, ndipo sadzatulukamonso: ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, [umene uli] Yerusalemu watsopano, umene ubwera kutsika kutuluka kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga: ndipo [ine ndidzalemba pa iye] dzina langa latsopano.
  7616. Rev 3:13 Iye amene ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena ku mipingo.
  7617. Rev 3:14 ¶Ndipo kwa mngelo wa ku mpingo wa kwa Alawodikeya lemba; Zinthu izi anena Amen, mboni yokhulupirika ndi yowona, woyamba wa chilengedwe cha Mulungu;
  7618. Rev 3:15 Ine ndidziwa ntchito zako, kuti si uli wozizira kapena wotentha: Ine ndikadafuna iwe utakhala wozizira kapena wotentha.
  7619. Rev 3:16 Potero tsono chifukwa uli wofunda; ndipo wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula mkamwa mwanga.
  7620. Rev 3:17 Chifukwa chakuti unena, ine ndine wolemera, ndipo chuma ndiri nacho, ndipo osasowa kanthu; ndipo iwe sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosawuka, ndi wakhungu ndi wamaliseche:
  7621. Rev 3:18 Ine ndikulangiza ugule kwa ine golidi woyesedwa m’moto, kuti ukakhale wachuma; ndi zovala zoyera, kuti iwe ukhoze kuvekedwa, ndi [kuti] manyazi a umaliseche wako usawonekere; ndi kudzoza maso ako ndi mankhwala wopaka m’maso, kuti iwe ukawone.
  7622. Rev 3:19 Monga ambiri ngati iwo ndiwakonda, Ine ndiwadzudzula ndi kupereka chilango: choncho chita changu, ndi kulapa.
  7623. Rev 3:20 Tawona, ine ndayima pakhomo, ndipo ndigogoda: ngati munthu wina aliyense akumva mawu anga ndi kutsegula pakhomo, ine ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi ine.
  7624. Rev 3:21 Kwa iye wakupambana ine ndidzampatsa kukhala pansi pamodzi ndi ine pa mpando wachifumu wanga, ngakhale monga inenso ndidapambana, ndipo ndakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.
  7625. Rev 3:22 Iye ali nalo khutu, amve chimene Mzimu anena ku mipingo.
  7626. Rev 4:1 Zitachitika izi ine ndidapenya, ndipo, tawonani, khomo lidatseguka kumwamba: ndipo mawu woyamba amene ndidawamva [adali] ngati lipenga likuyankhula ndi ine; amene adati, Kwera kuno, ndipo ine ndidzakuwonetsa zinthu zimene ziyenera kuchitika kuyambira pano kunka mtsogolo.
  7627. Rev 4:2 Ndipo posakhalitsa ndidali mu Mzimu; ndipo, tawonani, mpando wachifumu udayikidwa kumwamba ndipo wina adakhala pa mpandowo.
  7628. Rev 4:3 Ndipo iye amene adakhala pakumuyang’ana ngati jaspa ndi mwala wa sardini: ndipo [padali] utawaleza wozinga mpando wachifumuwo, mawonekedwe ake ngati emaradi.
  7629. Rev 4:4 Ndipo pozungulira mpando wachifumu [padali] mipando makumi awiri mphambu zinayi: ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri ndi mphambu zinayi, atavala zovala zoyera; ndipo pa mutu pawo padali makorona agolidi.
  7630. Rev 4:5 Ndipo kuchokera kumpando wachifumuwo, mudatuluka mphenzi ndi mabingu ndi mawu: Ndipo [padali] nyali zisanu ndi ziwiri za moto zikuyaka pamaso pa mpando wachifumu, zimene ziri Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu.
  7631. Rev 4:6 Ndipo pamaso pampando wachufumuwo, padali nyanja yamandala yonga kurisitalo: ndipo pakati pa mpando wachifumuwo, ndi pozungulira mpandowo, [padali] zamoyo zinayi zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.
  7632. Rev 4:7 Ndipo chamoyo choyamba [chidali] chofanana ndi mkango, ndi chamoyo chachiwiri chofanana ndi mwana wang’ombe, chamoyo chachitatu chidali ndi nkhope ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinayi [chidali] chofanana ndi chiwombankhanga chakuwuluka.
  7633. Rev 4:8 Ndipo chilichonse cha zamoyo zinayi pachokha chidali nawo mapiko asanu ndi limodzi pa [iye wokhala] mochizungulira; ndipo [zidali izo] zodzala ndi maso mkati: ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena Woyera, Woyera, Woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, amene adali, amene ali, ndi amene adzadza.
  7634. Rev 4:9 Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi mayamiko kwa iye adakhala pa mpando wachifumu, amene akhala ndi moyo kwa nthawi za muyaya.
  7635. Rev 4:10 Akulu makumi awiri ndi mphambu zinayi amagwa pansi pamaso pa iye amene adakhala pa mpando wachifumu, ndi kulambira iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za muyaya, naponya pansi makorona awo pamaso pa mpando wachifumu, kunena,
  7636. Rev 4:11 Muyenera inu, Ambuye, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu: pakuti inu mwalenga zinthu zonse, ndipo mwachifuniro chanu zikhala ndipo zidalengedwa.
  7637. Rev 5:1 Ndipo ine ndidawona m’dzanja lamanja la iye amene adakhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa mkati ndi kunja kumbuyo kwake, losindikizidwa ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.
  7638. Rev 5:2 Ndipo ndidawona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mawu okwera, Ndani ayenera kutsegula bukulo, ndi kumasula zosindikizira zake?
  7639. Rev 5:3 Ndipo padalibe munthu m’modzi kumwamba, kapena pa dziko lapansi, kapena pansi pa dziko, wakutha kutsegula buku, kapena kupenyapo.
  7640. Rev 5:4 Ndipo ndidalira kwambiri, chifukwa munthu aliyense sadapezeke woyenera kutsegula ndi kuwerenga bukulo, kapena kupenyapo.
  7641. Rev 5:5 Ndipo m’modzi wa akulu adanena ndi ine, Usalire: tawona, Mkango wa mfuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana [kuti] atsegula buku ndi kumasula zosindikizira zapamenepo zisanu ndi ziwiri.
  7642. Rev 5:6 ¶Ndipo ine ndidawona, ndipo, tawonani pakati pa mpando wachifumu ndi pa zamoyo zinayi, ndi pakati pa akulu, padayima Mwanawankhosa ngati adaphedwa, wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri, zimene ziri mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yotumidwa ilowe m’dziko lonse lapansi.
  7643. Rev 5:7 Ndipo adadza ndi kutenga bukulo ku dzanja lamanja la iye amene adakhala pa mpando wachifumu.
  7644. Rev 5:8 Ndipo pamene iye adatenga bukulo, zamoyo zinayi [ndi] akulu makumi awiri ndi mphambu zinayi zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nawo azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zonunkhira, zimene ndizo mapemphero a woyera mtima.
  7645. Rev 5:9 Ndipo adayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Mwayenera kulandira bukulo ndi kumasula zosindikizira zake: chifukwa inu munaphedwa, ndipo mwatiwombolera ife kwa Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi lirime, ndi anthu, ndi dziko;
  7646. Rev 5:10 Ndipo watipanga ife a kwa Mulungu wathu mafumu ndi ansembe: ndipo tidzalamulira padziko lapansi.
  7647. Rev 5:11 Ndipo ine ndidawona, ndipo ine ndidamva mawu a angelo ambiri pozungulira mpando wachifumu ndi zamoyo ndi akulu: ndipo chiwerengero chawo chidali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;
  7648. Rev 5:12 Kunena ndi mawu okwera, Wayenera Mwanawankhosa, amene adaphedwa kulandira mphamvu, ndi chuma, ndi nzeru, ndi chilimbiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi dalitso.
  7649. Rev 5:13 Ndipo cholengedwa chilichonse chili kumwamba, ndi padziko lapansi, ndi pansi padziko lapansi, ndi zimene zonga ziri m’nyanja, ndi zonse ziri m’menemo, ndidazimva ine ziri kunena, Dalitso, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, [zikhale] kwa iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa kwa nthawi za muyaya.
  7650. Rev 5:14 Ndipo zamoyo zinayi zidati, Amen. Ndipo akulu mphambu zinayi ndi makumi awiri zidagwa pansi ndi kulambira iye amene akhala ndi moyo kunthawi za nthawi.
  7651. Rev 6:1 Ndipo ine ndidawona pamene Mwanawankhosa atatsegula chimodzi cha zosindikizira, ndipo ine ndinamva, ngati phokoso la bingu chimodzi mwa zamoyo zinayi kunena, Idza ndipo uwone.
  7652. Rev 6:2 Ndipo ine ndidapenya, ndipo tawonani kavalo woyera: ndipo iye amene adakhala pa iye adali nawo uta; ndipo korona adapatsidwa kwa iye: ndipo adapita kogonjetsa, ndi kuti akagonjetse.
  7653. Rev 6:3 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachiwiri, ndidamva chamoyo chachiwiri chikunena, Idza ndipo uwone.
  7654. Rev 6:4 Ndipo adatuluka kavalo wina, amene [adali] wofiyira: ndipo [mphamvu] zidapatsidwa kwa iye amene adakhala pamenepo ya kuchotsa mtendere padziko lapansi, ndikuti aphane wina ndi mzake: ndipo pamenepo padapatsidwa kwa iye lupanga lalikulu.
  7655. Rev 6:5 Ndipo pamene iye adatsegula chosindikizira chachitatu, ndidamva chamoyo chachitatu chikunena, Idza ndipo uwone. Ndipo ine ndidapenya, tawonani, kavalo wakuda; ndipo iye amene adakhala pa iye adali nazo zoyesera m’dzanja lake.
  7656. Rev 6:6 Ndipo ine ndidamva mawu pakati pa zamoyo zinayi kunena, Muyeso wa tirigu kwa lupiya, ndi miyeso itatu ya balere kwa lupiya; ndipo [ona] iwe kuti usavulaze mafuta ndi vinyo.
  7657. Rev 6:7 Ndipo pamene iye adatsegula chosindikizira chachinayi, ndidamva mawu a chamoyo chachinayi chikunena, Idza ndipo uwone.
  7658. Rev 6:8 Ndipo ine ndidapenya, ndipo tawonani kavalo wotumbuluka: ndipo dzina la iye amene adakhala pa iye linali Imfa, ndipo nyanja ya moto idatsatira ndi iye. Ndipo mphamvu zidapatsidwa kwa iwo pa dera lachinayi la dziko lapansi, kupha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko lapansi.
  7659. Rev 6:9 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachisanu, Ine ndidawona pansi pa guwa la nsembe miyoyo ya iwo amene adaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu ndi cha umboni umene adasunga:
  7660. Rev 6:10 Ndipo iwo adafuwula ndi mawu okwera, kunena kuti, Kwa nthawi yayitali bwanji, O! Ambuye, woyera ndi wowona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango mwazi wathu pa iwo akukhala padziko lapansi?
  7661. Rev 6:11 Ndipo mwinjiro yoyera idapatsidwa kwa aliyense wa iwo; ndipo kunanenedwa kwa iwo, kuti apumulebe kwa kanthawi kochepa, kufikira atumiki anzawonso atakwaniranso ndi abale, amene adzaphedwa monganso [iwo], kuti kukhale kokwaniritsidwa.
  7662. Rev 6:12 Ndipo ine ndidawona pamene adatsegula chisindikiziro chachisanu ndi chimodzi, ndipo, tawonani, padali chivomerezi chachikulu; ndi dzuwa linada bii monga chiguduli cha ubweya, ndi mwezi udakhala ngati mwazi;
  7663. Rev 6:13 Ndipo nyenyezi za kumwamba zidagwa pa dziko lapansi, monga mkuyu utaya nkhuyu zake nthawi isanakwane, pamene ugwedezedwa ndi mphepo yolimba.
  7664. Rev 6:14 Ndipo kumwamba kudanyamuka monga ngati mpukutu pamene ukulungidwa pamodzi; ndi phiri lirilonse ndi chisumbu chilichonse zidasunthidwa kuchoka m’malo mwawo.
  7665. Rev 6:15 Ndipo mafumu a dziko lapansi, ndi anthu akulu, ndi anthu achuma, ndi akazembe, ndi anthu amphamvu, ndi anthu a ukapolo onse, ndi anthu a ufulu onse anadzibisa iwo eni m’mapanga ndi m’matanthwe a m’mapiri;
  7666. Rev 6:16 Ndipo adanena kwa mapiri ndi matanthwe, Gwerani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa:
  7667. Rev 6:17 Pakuti tsiku lalikulu la mkwiyo wake lafika; ndipo ndani amene adzakhoza kuyima?
  7668. Rev 7:1 Ndipo zitachitika zinthu izi ine ndidawona angelo anayi alinkuyimirira pa ngodya zinayi za dziko lapansi, akugwira mphepo zinayi za dziko lapansi, kuti mphepo zisawombe padziko lapansi, kapena panyanja, kapena pa mtengo wina uliwonse.
  7669. Rev 7:2 Ndipo ndidawona mngelo wina akukwera kuchokera mbali ya kum’mawa, ali nacho chosindikizira cha Mulungu wamoyo: ndipo adafuwula ndi mawu okwera kwa angelo anayiwo, kwa iye amene kudapatsidwa kuvulaza dziko lapansi ndi nyanja,
  7670. Rev 7:3 Kunena, Musavulaze dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titasindikiza chisindikiziro atumiki a Mulungu wathu pa mphumi pawo.
  7671. Rev 7:4 Ndipo ine ndidamva chiwerengero cha iwo osindikizidwa chisindikiziro, [ndipo iwo anasindikizidwa] zikwi makumi khumi ndi makumi anayi ndi zinayi a onse amafuko a ana Israyeli.
  7672. Rev 7:5 Mwa fuko la Yuda adasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Rubeni adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Gadi adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.
  7673. Rev 7:6 Mwa fuko la Aseri adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Nafutali adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Manase adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.
  7674. Rev 7:7 Mwa fuko la Simeon adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Levi adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.
  7675. Rev 7:8 Mwa fuko la Zebuloni adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Yosefe adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Benjamini adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.
  7676. Rev 7:9 ¶Zitachitika izi, ine ndidapenya, ndipo, tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu adakhoza kuliwerenga, a mayiko onse, ndi mafuko, ndi anthu, ndi malirime, adayimirira pamaso pa mpando wachifumu, ndi pamaso pa Mwanawankhosa, wovala mikanjo yoyera, ndi a kanjedza m’manja mwawo;
  7677. Rev 7:10 Ndipo adafuwula ndi mawu okwera, kunena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.
  7678. Rev 7:11 Ndi kwa angelo onse adayimirira pozungulira mpando wachifumu, ndi [kuzungulira] akulu ndi zamoyo zinayizo ndipo zidagwa nkhope pansi pamaso pa mpando wachifumu nalambira Mulungu,
  7679. Rev 7:12 Kunena, Amen: Dalitso, ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi mphamvu, ndi chilimbiko, [zikhale] kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za muyaya. Amen.
  7680. Rev 7:13 Ndipo m’modzi wa akulu adayankha, kunena ndi ine, Ndi ndani awa amene avala mikanjo yoyera? Ndipo iwo achokera kuti?
  7681. Rev 7:14 Ndipo ine ndidati kwa iye, Mbuye, mudziwa ndinu. Ndipo adati kwa ine, Awa ndi iwo amene wochokera kutuluka m’chisawutso chachikulu, ndipo adatsuka mikanjo yawo, ndipo adayiyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.
  7682. Rev 7:15 Choncho ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amtumikira iye usana ndi usiku m’kachisi mwake: ndipo iye amene akhala pa mpando adzakhala pakati pawo.
  7683. Rev 7:16 Iwo sadzamvanso njala, kapena ludzu; kapena silidzawawalira dzuwa, kapena kutentha kulikonse.
  7684. Rev 7:17 Chifukwa Mwanawankhosa ali pakati pa mpando wachifumu adzawadyetsa iwo, ndipo adzawatsogolera ku akasupe amadzi amoyo: ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse m’maso mwawo.
  7685. Rev 8:1 Ndipo pamene adatsegula chisindikiziro chachisanu ndi chiwiri, kudali chete kumwamba monga kwa nthawi ya theka la ora.
  7686. Rev 8:2 Ndipo ndidawona angelo asanu ndi awiri amene adayima pamaso pa Mulungu; ndipo kwa iwo kudapatsidwa malipenga asanu ndi awiri.
  7687. Rev 8:3 Ndipo mngelo wina adadza nayima pa guwa la nsembe, ali nacho chotengera cha zofukiza chagolidi; ndipo kudapatsidwa zofukiza zambiri, kuti azipereke [izo] pamodzi ndi mapemphero a woyera mtima onse pamwamba pa guwa la nsembe lagolidi, limene lidali pamaso pa mpando wachifumu.
  7688. Rev 8:4 Ndipo utsi wazofukiza, [umene udadza] pamodzi ndi mapemphero a woyera mtima, udakwera kumwamba pamaso pa Mulungu kutuluka m’dzanja la mngelo.
  7689. Rev 8:5 Ndipo mngeloyo adatenga mbale ya zofukizayo, nayidzaza ndi moto wa pa guwa la nsembe nayiponya padziko lapansi; ndipo padakhala mawu, ndi mabingu, ndi mphenzi, ndi zivomerezi.
  7690. Rev 8:6 Ndipo angelo asanu ndi awiri amene adali nawo malipenga asanu ndi awiri adadzikonzekeretsa kuti alize.
  7691. Rev 8:7 ¶Ndipo mngelo woyamba adaliza, ndipo pamenepo padatsatira matalala ndi moto zosanganizikana ndi mwazi, ndipo adaziponya pa dziko lapansi: ndipo gawo limodzi la magawo atatu la mitengo zidawotchedwa, ndipo udzu wonse wobiriwira udawotchedwa.
  7692. Rev 8:8 Ndipo mngelo wachiwiri adaliza, ndipo kudali monga ngati phiri lalikulu lakupsa ndi moto lidaponyedwa m’nyanja: ndipo gawo limodzi la magawo atatu la nyanja lidasanduka mwazi;
  7693. Rev 8:9 Ndipo gawo limodzi la magawo atatu la zolengedwa zimene zidali m’nyanja, ndipo zidali nawo moyo zidafa; ndipo gawo limodzi la magawo atatu la zombo lidawonongeka.
  7694. Rev 8:10 Ndipo mngelo wachitatu adaliza, ndipo idagwa nyenyezi yayikulu kuchokera kumwamba, yoyaka ngati nyali, ndipo idagwa pa gawo limodzi la magawo atatu la mitsinje, ndi pa kasupe wa madzi;
  7695. Rev 8:11 Ndipo dzina lake la nyenyeziyo litchedwa Chowawa: ndipo gawo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa chifukwa cha madziwa, pakuti adasandutsidwa owawa.
  7696. Rev 8:12 Ndipo mngelo wachinayi adaliza, ndipo gawo limodzi la magawo atatu la dzuwa lidamenyedwa, ndi gawo limodzi la magawo atatu la mwezi; ndi gawo limodzi la magawo atatu la nyenyezi; kotero monga gawo limodzi la magawo awo atatu la izo linadetsedwa, ndipo tsiku silidawale kwa gawo limodzi la magawo atatu a ilo, ndi chimodzimodzinso usiku.
  7697. Rev 8:13 Ndipo ine ndidawona, ndipo ndidamva mngelo akuwuluka kudutsa pakati pa kumwamba, kunena ndi mawu okwera, Tsoka, tsoka, tsoka, kwa iwo akukhala padziko lapansi chifukwa cha mawu enawo a lipenga la angelo atatu, amene ayeneranso kuti alize!
  7698. Rev 9:1 Ndipo mngelo wachisanu adawomba, ndipo ndidawona nyenyezi kuchokera kumwamba idagwa padziko lapansi: ndipo adampatsa iye chifungulo cha dzenje lopanda malire.
  7699. Rev 9:2 Ndipo adatsegula pa dzenje lopanda malire; ndipo padakwera utsi wotuluka m’dzenjemo, ngati utsi wa ng’anjo yayikulu; ndipo dzuwa ndi mpweya zinada chifukwa cha utsi wa kudzenjewo.
  7700. Rev 9:3 Ndipo mudatuluka mu utsimo wa kudzenjewo dzombe pa dziko: ndipo kwa ilo kudapatsidwa mphamvu, monga zinkhanira za dziko lapansi zirinayo mphamvu.
  7701. Rev 9:4 Ndipo lidalamulidwa ilo kuti lisavulaze udzu wa padziko lapansi, kapena chobiriwira chilichonse, kapena mtengo uli wonse; koma anthu amene alibe chisindikiziro cha Mulungu pamphumi pawo.
  7702. Rev 9:5 Ndipo kwa ilo kudapatsidwa kuti asawaphe iwo, komatu kuti iwo azunzidwe miyezi isanu: ndipo mazunzidwe awo [adali] mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu.
  7703. Rev 9:6 Ndipo m’masiku amenewo anthu adzafunafuna imfa, ndipo sadzayipeza iyo; ndipo adzakhumba kumwalira, ndipo imfa idzathawa kwa iwo.
  7704. Rev 9:7 Ndipo mawonekedwe a dzombelo [adali] ofanana ndi akavalo wokonzekeretsedwa kupita ku nkhondo; ndi pamitu pawo [padali] ngati a korona wonga a golidi, ndipo nkhope zawo [zidali] ngati nkhope za anthu.
  7705. Rev 9:8 Ndipo lidali nalo tsitsi longa tsitsi la akazi, ndipo mano ake adali ngati [mano] a mikango.
  7706. Rev 9:9 Ndipo lidali nazo zikopa zapachifukwa, ngati zikopa zapachifuwa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko awo [udali] ngati mkokomo wa magareta a kavalo ambiri akuthamangira ku nkhondo.
  7707. Rev 9:10 Ndipo lidali ndi michira yofanana ndi ya chinkhanira, ndipo mudali mbola m’michira yawo: ndipo mphamvu yawo idali yakuti avulaze anthu miyezi isanu.
  7708. Rev 9:11 Ndipo lidali nayo mfumu pa iwo, [amene ndiye] mngelo wa dzenje lopanda malire; amene dzina lake m’lirime la Chihebri Abadoni, koma m’lirime la Chihelene ali nalo dzina [lake] Apoliyoni.
  7709. Rev 9:12 Tsoka loyamba lapita; [ndipo], tawonani, akudzanso matsoka awiri kuyambira pano kunka m’tsogolomo.
  7710. Rev 9:13 Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi adaliza, ndipo ndidamva mawu wochokera kunyanga zinayi za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu.
  7711. Rev 9:14 Kunena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi amene adali nalo lipenga, Masula angelo anayi womangidwa mu mtsinje wa ukulu wa Ufurati.
  7712. Rev 9:15 Ndipo angelo anayi adamasulidwa, amene adakonzekeretsedwa kwa ora limodzi, ndi tsiku limodzi, ndi mwezi umodzi, ndi chaka chimodzi, kuti akaphe gawo limodzi la magawo atatu la anthu.
  7713. Rev 9:16 Ndipo chiwerengero cha a nkhondo cha a pakavalo [chidali] zikwi makumi awiri kuchulukitsa zikwi khumi: ndipo ndidamva chiwerengero cha iwo.
  7714. Rev 9:17 Ndipo kotero ndidawona akavalo m’masomphenya, ndi iwo amene adakhala pa iwo, ali nazo zikopa zapachifuwa zamoto, mwala wa jakinti, ndi sulfure: ndi mitu ya akavalo [inali] ngati mitu ya mikango; ndipo mkamwa mwawo mudatuluka moto ndi utsi ndi mwala wa sulfure.
  7715. Rev 9:18 Ndi itatu imeneyi gawo limodzi la magawo atatu a anthu lidaphedwa, ndi moto, ndi utsi, ndi mwala wa sulfure, umene udatuluka m’kamwa mwawo.
  7716. Rev 9:19 Pakuti mphamvu yawo ili m’kamwa mwawo, ndi m’michira yawo: pakuti michira yawo [idali] yofanana ndi njoka, ndipo zidali nayo mitu, ndipo ndi iyo izo zivulaza:
  7717. Rev 9:20 Ndipo anthu wotsala wosaphedwa nayo miliriyo sadalape ku ntchito ya manja awo, kuti iwo asapembedze ziwanda, ndi mafano agolidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi mwala, ndi a mtengo: zimene sizikhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda:
  7718. Rev 9:21 Ndipo sadalapa iwo umbanda wawo, kapena za nyanga zawo, kapena za chiwerewere chawo, kapena za umbala wawo.
  7719. Rev 10:1 Ndipo ndidawona mngelo wina wamphamvu alikutsika kumwamba, atavala mtambo: ndipo utawaleza unali pa mutu pake, ndi nkhope yake [idali] ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto:
  7720. Rev 10:2 Ndipo iye adali nako m’dzanja lake kabuku kakang’ono kotsegula: ndipo adaponda phazi lake lamanja panyanja ndi [phazi] lamanzere [lake] pa mtunda,
  7721. Rev 10:3 Ndipo adafuwula ndi mawu okwera, monga ngati mkango [pamene] ubangula: ndipo pamene adafuwula, mabingu asanu ndi awiri adayankhula mawu awo.
  7722. Rev 10:4 Ndipo pamene adayankhula mawu awo mabingu asanu ndi awiriwo, ndidatsala pan’gono kuti ndilembe: ndipo ndidamva mawu wochokera kumwamba akunena kwa ine, Sindikiza nacho chizindikiro zinthu zimene adayankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe izo ayi.
  7723. Rev 10:5 Ndipo mngelo amene ine ndidamuwona alikuyimirira pa nyanja ndi pa mtunda adakweza dzanja lake kuloza kumwamba,
  7724. Rev 10:6 Ndipo analumbira pa iye amene akhala ndi moyo ku nthawi za muyaya, amene adalenga kumwamba, ndi zinthu zimene ziri m’menemo, ndi dziko lapansi, ndi zinthu zimene ziri m’menemo, ndi nyanja, ndi zinthu zimene ziri m’menemo, kuti pasakhalenso nthawi yopitirira:
  7725. Rev 10:7 Koma m’masiku a mawu a mngelo wachisanu ndi chiwiri, pamene iye adzayamba kuwomba, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kutsirizika, monga adalengeza kwa atumiki ake aneneri.
  7726. Rev 10:8 Ndipo mawu ndidawamva wochokera kumwamba adabwerezanso kundiyankhula ine, ndipo ananena, Muka [ndipo] tenga kabuku kakang’ono kotsegula kamene kali m’dzanja la mngelo amene wayimirira panyanja ndi padziko.
  7727. Rev 10:9 Ndipo ndidapita kwa mngelo, ndipo ndidanena kwa iye, Ndipatse kabuku kakang’onoko. Ndipo adanena kwa ine, Tenga [iko], ndipo udye iko; ndipo kadzapangitsa m’mimba mwako kuwawa, koma kadzakhala m’kamwa mwako kozuna ngati uchi:
  7728. Rev 10:10 Ndipo ine ndidatenga kabuku kakang’onoko m’dzanja la mngelo, ndipo ndidadya iko; ndipo kadali mkamwa mwanga kozuna ngati uchi: ndipo nditangokadya iko, m’mimba mwanga mudawawa.
  7729. Rev 10:11 Ndipo iye adati kwa ine, Uyenera iwe kubwerezanso kunenera pa anthu ambiri, ndi mayiko, ndi malirime, ndi mafumu.
  7730. Rev 11:1 Ndipo kudapatsidwa kwa ine bango ngati ndodo: ndipo mngeloyo adayimirira, kunena kuti, Nyamuka, ndi kuyesa kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo amene alambiramo.
  7731. Rev 11:2 Koma bwalo limene liri kunja kwa kachisi ulisiye, ndipo usaliyesa ilo; pakuti lapatsidwa iro kwa Amitundu: ndipo mzinda woyera iwo adzawupondereza pansi pa phazi miyezi makumi anayi [ndi] mphambu ziwiri.
  7732. Rev 11:3 Ndipo ndidzapatsa [mphamvu] kwa mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi ndi mazana awiri [ndi] makumi asanu ndi limodzi, zitavala chiguduli.
  7733. Rev 11:4 Izi ndizo mitengo iwiri ya olivi, ndi zoyikapo nyali ziwiri zakuyimirira pamaso pa Mulungu wa dziko lapansi.
  7734. Rev 11:5 Ndipo munthu wina akadzavulaza izo, moto utuluka m’kamwa mwawo, nuwononga adani awo: ndipo wina akafuna kuzivulaza izo, ayenera iye kuphedwa munjira yotero.
  7735. Rev 11:6 Izi ziri nawo ulamuliro wakutseka kumwamba, kuti isagwe mvula masiku a kunenera kwawo: ndipo ali ndi ulamuliro pa madzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi miliri yonse, mwa kawirikawiri monga zifuna.
  7736. Rev 11:7 ¶Ndipo pamene zidzakhala zitatsiriza umboni wawo, chirombo chimene chikwera kutuluka m’dzenje lopanda malire chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzawapambana, ndi kuzipha izo.
  7737. Rev 11:8 Ndipo mitembo yawo [idzagona] mu msewu wa mzinda waukuluwo, umene mwauzimu utchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wathu adapachikidwa.
  7738. Rev 11:9 Ndipo iwo a anthuwo ndi malirime ndi mafuko adzapenya mitembo yawo masiku atatu ndi theka, ndipo sadzalola mitembo yawo kuyikidwa m’manda.
  7739. Rev 11:10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwera pa izo, ndipo adzasekera, nadzatumizirana mphatso wina ndi mzake; chifukwa aneneri awa awiri adazunza iwo akukhala padziko lapansi.
  7740. Rev 11:11 Ndipo atapita masiku atatu ndi theka Mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu udalowa mwa izo, ndipo adayimirira chiliri pa mapazi awo; ndipo mantha akulu adagwera pa iwo amene adawapenya.
  7741. Rev 11:12 Ndipo adamva mawu akulu akuchokera kumwamba akunena kwa izo, Idzani kukwera kuno. Ndipo anakwera kunka kumwamba mu mtambo; ndipo adani awo adawapenya iwo.
  7742. Rev 11:13 Ndipo pa ora lomwero padali chivomerezi chachikulu, ndipo gawo limodzi la magawo khumi la mzinda lidagwa, ndipo m’chivomerezicho adaphedwa a anthu zikwi zisanu ndi ziwiri: ndipo wotsalawo adachititsidwa mantha, ndipo adapereka ulemerero kwa Mulungu wa kumwamba.
  7743. Rev 11:14 Tsoka lachiwiri lapita; [ndipo], tawonani, tsoka lachitatu lidza msanga.
  7744. Rev 11:15 Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri adaliza; ndipo padali mawu akulu kumwamba, kunena, Maufumu a dziko lapansi ili akhala [maufumu] a Ambuye wathu, ndi a Khristu wake; ndipo adzachita ufumu kufikira muyaya.
  7745. Rev 11:16 Ndipo akulu makumi awiri ndi mphambu zinayi, amene adakhala pamaso pa Mulungu pa mipando yawo, adagwa pnsi pa nkhope zawo, ndipo analambira Mulungu,
  7746. Rev 11:17 Kunena kuti, Ife tipereka kwa inu mayamiko, Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, amene muli, ndipo mudali, ndipo mudzali; chifukwa mwadzitengera kwa inu mphamvu yanu yayikulu, ndipo mwalamulira.
  7747. Rev 11:18 Ndipo mayiko adakwiya, ndipo wadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa, yakuti iwo aweruzidwe, ndi yakuti inu mupereke mphotho kwa atumiki anu aneneri, ndi kwa woyera mtima, ndi iwo amene awopa dzina lanu, aang’ono ndi akulu; ndikuwononga iwo amene awononga dziko lapansi.
  7748. Rev 11:19 Ndipo kachisi wa Mulungu adatsegulidwa kumwamba, ndipo mudawoneka m’kachisi mwake likasa la chipangano chake: ndipo padali mphenzi, ndi mawu, ndi mabingu, ndi chivomerezi, ndi matalala akulu.
  7749. Rev 12:1 Ndipo chidawoneka chodabwitsa chachikulu kumwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi pansi pa mapazi ake, ndipo pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri:
  7750. Rev 12:2 Ndipo ali ndi pakati adafuwula, alikubuwula mukubereka, ndipo adamva zowawa kuti abale.
  7751. Rev 12:3 Ndipo chidawoneka chodabwitsa china kumwamba; ndipo tawonani chinyama chonga njoka chachikulu chofiyira, chachikulu chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake akorona asanu ndi awiri.
  7752. Rev 12:4 Ndipo mchira wake udaguza gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi za kumwamba, ndipo unaziponya padziko lapansi: ndipo chinjoka chidayimirira pamaso pa mkazi wakuti abale, kuti icho chikam’meze mwanayo akangobadwa.
  7753. Rev 12:5 Ndipo anabala mwana wachimuna amene adayenera kulamulira mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo mwana wake adakwatulidwa kupita kwa Mulungu, ndi [ku] mpando wachifumu wake.
  7754. Rev 12:6 Ndipo mkazi adathawa kulowa kuchipululu, kumene adali nawo malo okonzedweratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri [ndi] mphambu makumi asanu ndi limodzi.
  7755. Rev 12:7 ¶Ndipo kudali nkhondo kumwamba: Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinyama chonga njoka; ndi chinyama chonga njoka ndi angelo ake chidachita nkhondo.
  7756. Rev 12:8 Ndipo sichidalaka; ndipo sadapezekanso malo awo kumwamba.
  7757. Rev 12:9 Ndipo chidaponyedwa pansi chinyama chonga njoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdiyerekezi, ndi Satana, amene anyenga dziko lapansi: iye adaponyedwa pansi kudziko lapansi, ndi angelo ake anaponyedwa pamodzi ndi iye.
  7758. Rev 12:10 Ndipo ndidamva mawu okwera akunena kumwamba, Tsopano chafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake: pakuti woneneza wa abale athu waponyedwa pansi, amene anawaneneza iwo pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.
  7759. Rev 12:11 Ndipo iwo adampambana iye mwa mwazi wa Mwanawankhosa, ndi mwa mawu a umboni wawo; ndipo sadakonda moyo wawo kufikira imfa.
  7760. Rev 12:12 Choncho, kondwerani [inu] miyamba, ndi inu akukhala m’menemo. Tsoka wokhala pa dziko lapansi ndi a m’nyanja! Chifukwa mdiyerekezi wabwera kutsikira kwa inu, wokhala nawo mkwiyo waukulu, pakuti adziwa kuti kamtsalira iye kanthawi kochepa.
  7761. Rev 12:13 Ndipo pamene chinyama chonga njoka chidawona kuti chidaponyedwa pansi padziko, chidazunza mkazi amene adabala mwana wachimuna.
  7762. Rev 12:14 Ndipo kwa mkazi kudapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu, kuti akhoze kuwuluka kulowa m’chipululu, kulowa m’malo ake, kumene adyetsedwa kwa kanthawi ndi zinthawi, ndi theka la nthawi, wochotsedwa pa nkhope ya chinjoka.
  7763. Rev 12:15 Ndipo chinjokacho chidalavula m’kamwa mwake madzi ngati chigumula potsata mkazi, kuti iye akapangitse iye akakokololedwe ndi chigumula.
  7764. Rev 12:16 Ndipo dziko lidathandiza mkaziyo, ndipo dziko lidatsegula pakamwa pake, ndi kumeza chigumula chimene chinyama chonga njoka chidalavula m’kamwa mwake.
  7765. Rev 12:17 Ndipo chinyama chonga njoka chidakwiya ndi mkaziyo, nichinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala ambewu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, ndipo ali nawo umboni wa Yesu Khristu.
  7766. Rev 13:1 ¶Ndipo ine ndidayimirira pa mchenga wa nyanja, ndipo ndidawona chirombo chikutuluka m’nyanja, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi, ndi panyanga zake akorona khumi, ndi pamitu yakeyo dzina lonyoza Mulungu.
  7767. Rev 13:2 Ndipo chirombo ndidachiwonacho chidafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake [ngati mapazi] a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango: ndipo chinyama chonga njoka chidampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wake, ndi ulamuliro waukulu.
  7768. Rev 13:3 Ndipo ndidawona umodzi wa mitu yake udakhala monga ngati udalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la ku imfa lidapola: ndipo dziko lonse lapansi lidazizwa potsata chirombocho.
  7769. Rev 13:4 Ndipo adalambira chinyama chonga njoka, chimene chidachipatsa mphamvu chirombocho; ndipo adalambira chirombo, kunena, Ndani [iye] afanana ndi chirombo? Ndipo ndani akhoza kumenya nkhondo ndi iye?
  7770. Rev 13:5 Ndipo kudapatsidwa kwa iye m’kamwa moyankhula zinthu zazikulu ndi zonyoza Mulungu; ndipo ulamuliro udapatsidwa kwa icho wakupitirira miyezi makumi anayi ndi iwiri.
  7771. Rev 13:6 Ndipo chidatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kunenera zamwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo amene akhala kumwamba.
  7772. Rev 13:7 Ndipo kudapatsidwa kwa icho kuchita nkhondo ndi woyera mtima, ndi kuwapambana iwo: ndipo mphamvuidapatsidwa [kwa] iye ya pafuko lirilonse, ndi malirime, ndi mitundu.
  7773. Rev 13:8 Ndipo onse amene akhala padziko lapansi adzachilambira icho, amene mayina awo sadalembedwa m’buku la moyo la Mwanawankhosa wophedwa kuyambira kumaziko a dziko lapansi.
  7774. Rev 13:9 Ngati munthu wina ali nalo khutu, iye amve.
  7775. Rev 13:10 Iye amene atsogolera ku ukapolo adzamuka ku ukapolo: iye amene apha ndi lupanga ayenera iye kuphedwa ndi lupanga. Apa pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha woyera mtima.
  7776. Rev 13:11 Ndipo ine ndidawona chirombo china chilikutuluka pansi pa dziko; ndipo icho chidali nazo nyanga ziwiri ngati za Mwanawankhosa, ndipo icho chidayankhula ngati chinyama chonga njoka.
  7777. Rev 13:12 Ndipo chichita ulamuliro wonse wachirombo choyamba pamaso pake, ndipo chichititsa dziko ndi iwo amene akhala m’menemo kuti alambire chirombo choyamba, chimene bala lake la ku imfa lidapola.
  7778. Rev 13:13 Ndipo chichita zodabwitsa zazikulu, kotero kuti chitsitsa moto uchokere kumwamba nugwe padziko m’kuwona kwa anthu.
  7779. Rev 13:14 Ndi kusokeretsa iwo amene akhala padziko lapansi [mwanjira ya] machitidwe a zozizwa zimene icho chidapatsidwa mphamvu yakuchita m’kuwona kwa chirombo; kunena kwa iwo amene akhala padziko lapansi, kuti iwo apange fano kwa chirombo, chimene chidali nalo bala la lupanga, ndipo chidakhala ndi moyo.
  7780. Rev 13:15 Ndipo adali ndi mphamvu yakupatsa moyo fano la chirombo, kuti fano la chirombo liyankhule, ndi kupangitsa kuti ambiri onse amene sadzalambira fano la chirombo aphedwe.
  7781. Rev 13:16 Ndipo chipangitsa kuti onse, onse aang’ono ndi akulu, achuma ndi wosawuka, mfulu ndi kapolo, kuti alandire chizindikiritso pa dzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.
  7782. Rev 13:17 Ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, kupatula iye yekha wakukhala nacho chizindikiro, kapena dzina la chirombo, kapena chiwerengero cha dzina lake.
  7783. Rev 13:18 Pano pali nzeru. Iye wakukhala nako kumvetsetsa awerenge chiwerengero cha chirombocho: pakuti chili chiwerengero cha munthu; ndipo chiwerengero chake [chili] mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi imodzi kudza zisanu [ndi] chimodzi.
  7784. Rev 14:1 Ndipo ine ndidapenya, ndipo, tawonani, Mwanawankhosayo adayimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana ndi makumi anayi ndi zinayi, ali nalo dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo.
  7785. Rev 14:2 Ndipo ndidamva mawu wochokera kumwamba, ngati mawu a mkokomo wamadzi ambiri, ngati mawu a bingu lalikulu: ndipo ndidamva mawu amene oyimba azeze akuyimba azeze awo:
  7786. Rev 14:3 Ndipo adayimba monga ngati ili nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinayi, ndi akulu: ndipo palibe munthu adakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana ndi makumi anayi ndi zinayi, amene adali wowomboledwa kuchokera kudziko lapansi.
  7787. Rev 14:4 Awa ndiwo amene adali wosadetsedwa ndi akazi; pakuti iwo ali anamwali. Awa ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Awa ndiwo amene adawomboledwa kuchokera pakati pa anthu, [ndiwo] zipatso zoyambirira kucha za kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.
  7788. Rev 14:5 Ndipo m’kamwa mwawo simudapezeka chinyengo: pakuti ali wopanda chirema pamaso pampando wachifumu wa Mulungu.
  7789. Rev 14:6 ¶Ndipo ndidawona mngelo wina ali kuwuluka pakati pa kumwamba, wakukhala nawo uthenga wabwino wamuyaya kuti awulalikire kwa iwo amene akhala pa dziko lapansi, kwa dziko lirilonse, ndi fuko, ndi lirime ndi anthu,
  7790. Rev 14:7 Kunena ndi mawu okwera, Wopani Mulungu, perekani ulemerero kwa iye; pakuti ora lachiweruziro chake lafika: ndipo lambirani iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja ndi akasupe a madzi.
  7791. Rev 14:8 Ndipo adatsatira mngelo wina, kunena, Babuloni wagwa, wagwa, mzinda waukuluwo chifukwa udapangitsa kuti mitundu yonse imwe kwa vinyo wa mkwiyo wa chiwerewere chake.
  7792. Rev 14:9 Ndipo mngelo wachitatu adatsatira, kunena ndi mawu okwera, Ngati munthu wina aliyense alambira chirombocho ndi fano lake, ndi kulandira chizindikiritso [chake] pa mphumi pake, kapena m’dzanja lake,
  7793. Rev 14:10 Yemweyonso adzamwako kwa vinyo wa mkwiyo wa Mulungu, amene athiridwa wopanda kusanganiza m’chikho cha mkwiyo wake; ndipo iye adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo woyera, ndi pamaso pa Mwanawankhosa:
  7794. Rev 14:11 Ndipo utsi wa mazunzo awo ukwera ku nthawi za muyaya: ndipo sapuma usana ndi usiku, amene alambira chirombocho ndi fano lake, ndi aliyense amene alandira chizindikiritso cha dzina lake.
  7795. Rev 14:12 Apa pali chipiriro cha woyera mtima: apa ali iwo amene asunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.
  7796. Rev 14:13 Ndipo ine ndidamva mawu wochokera kumwamba kunena kwa ine, Lemba, Wodala [ali] akufa amene amwalira mwa Ambuye kuyambira tsopano kupita mtsogolo: Inde, ananena Mzimu, kuti akhoze kupumula kuntchito zawo; pakuti ntchito zawo ziwatsata iwo.
  7797. Rev 14:14 Ndipo ine ndidapenya, ndipondidawona mtambo woyera, ndi pamtambopo [wina] padakhala monga Mwana wamwamuna wa munthu, wakukhala naye korona wa golidi pa mutu pake, ndi m’dzanja lake, zenga lakuthwa.
  7798. Rev 14:15 Ndipo mngelo wina adatuluka m’kachisi, wofuwula ndi mawu okwera kwa iye amene adakhala pamtambo, Tumiza zenga lako, ndi kukolola; pakuti yafika nthawi yakukolola; pakuti zokolola za dziko zakhwima:
  7799. Rev 14:16 Ndipo iye amene adakhala pamtambo adaponya zenga lake padziko lapansi, ndipo dziko lapansi linakololedwa.
  7800. Rev 14:17 Ndipo mngelo wina adatuluka m’kachisi amene ali kumwamba, iye anali nalonso zenga lakuthwa.
  7801. Rev 14:18 Ndipo mngelo wina adatuluka kuchokera kuguwa la nsembe, amene adali nayo mphamvu pa moto; ndipo adalira ndi fuwu lokwera kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, kunena, Tumiza zenga lakuthwa, ndi kusokhetsa matsango a mpesa wa m’dziko lapansi; pakuti mphesa zake zakhwima kwathunthu.
  7802. Rev 14:19 Ndipo mngelo adaponya zenga lake ku dziko lapansi, nasonkhetsa mphesa za dziko lapansi, ndi kuziponya [izo] moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.
  7803. Rev 14:20 Ndipo moponderamo mphesa mudapondedwa kunja kwa mzinda, ndipo mwazi udatuluka moponderamo mphesa, nufikira mpaka kuzomangira pakamwa za pa akavalo, mpata wa mitunda mazana awiri.
  7804. Rev 15:1 Ndipo ine ndidawona chizindikiro china kumwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri ndiyo yotsiriza; pakuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.
  7805. Rev 15:2 Ndipo ine ndidawona ngati nyanja ya mandala yosanganiza ndi moto: ndipo iwo amene adapeza chipambano pa chirombocho, ndi fano lake, ndi pa chizindikiritso chake, [ndi] pa chiwerengero cha dzina lake, adayimirira pa nyanja ya mandala, akukhala nawo azeze a Mulungu.
  7806. Rev 15:3 Ndipo iwo ayimba nyimbo ya Mose mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, ndikuti, Ntchito zanu [ziri] zazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse; zolungama ndi zowongoka [ziri] njira zanu, inu Mfumu ya woyera mtima.
  7807. Rev 15:4 Ndani amene sadzakuwopani inu ndikusapereka ulemerero kwa dzina lanu, Ambuye? Pakuti [inu] nokha [ndinu] woyera: chifukwa mayiko onse adzadza nadzalambira pamaso panu; popeza ziweruzo zanu zawonetsedwa.
  7808. Rev 15:5 ¶Ndipo zitatha izi ine ndinawona, ndipo tawonani, pa kachisi wa chihema cha umboni kumwamba padatsegulidwa.
  7809. Rev 15:6 Ndipo angelo asanu ndi awiri adatuluka m’kachisi, akukhala nayo miliri isanu ndi iwiriyo, atavala zovala zabafuta zoyera ndi zonyezimira, ndipo pachifuwa pawo atamangira malamba agolidi.
  7810. Rev 15:7 Ndipo chimodzi cha zamoyo zinayi chidapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu, amene akhala ndi moyo ku nthawi za muyaya,
  7811. Rev 15:8 Ndipo kachisi adadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu, ndi kuchokera ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu adakhoza kulowa m’kachisi kufikira itakwaniritsidwa miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.
  7812. Rev 16:1 Ndipo ine ndidamva mawu akulu akutuluka kuchokera ku kachisi kunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani pa njira zanu, ndipo tsanulirani mbale za mkwiyo wa Mulungu kudziko lapansi.
  7813. Rev 16:2 Ndipo woyamba adapita, ndi kutsanulira mbale yake ku dziko lapansi; ndipo kudakhala chironda chopweteka ndi chosawutsa pa anthu akukhala nacho chizindikiritso cha chirombo, ndi [pa] iwo wolambira fano lake.
  7814. Rev 16:3 Ndipo mngelo wachiwiri adatsanulira mbale yake pa nyanja; ndipo idakhala ngati mwazi wa [munthu] wakufa; ndipo chamoyo chilichonse cha m’nyanja chidafa.
  7815. Rev 16:4 Ndipo mngelo wachitatu adatsanulira mbale yake pa mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo izo zidasanduka mwazi.
  7816. Rev 16:5 Ndipo ine ndidamva mngelo wa madziwo akunena, Inu muli wolungama, Ambuye, amene muli, ndipo mudali, ndipo mudzakhala, pakuti mwaweruza chotero.
  7817. Rev 16:6 Popeza akhetsa mwazi wa woyera mtima ndi aneneri, ndipo inu mudawapatsa mwazi kuti amwe; pakuti iwo ali oyenera.
  7818. Rev 16:7 Ndipo ine ndidamva wina kutuluka kuguwa la nsembe, kunena, Ngakhale choncho, Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, chiweruzo chanu [chili] chowona ndi cholungama.
  7819. Rev 16:8 Ndipo mngelo wachinayi adatsanulira mbale yake pa dzuwa; ndipo mphamvu idapatsidwa kwa iye kuti atenthe anthu ndi moto.
  7820. Rev 16:9 Ndipo anthu adatenthedwa ndi kutentha kwakukulu, ndipo adanenera zamwano dzina la Mulungu, amene ali nayo mphamvu pa miliri iyi: ndipo iwo sadalape kuti apatse iye ulemerero.
  7821. Rev 16:10 Ndipo mngelo wachisanu adatsanulira mbale yake pa mpando wa chirombo; ndipo ufumu wake unadzadza ndi mdima; ndipo adatafuna malirime awo chifukwa cha ululu.
  7822. Rev 16:11 Ndipo adanenera zamwano Mulungu wa kumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zironda zawo; ndipo sadalape ntchito zawo.
  7823. Rev 16:12 Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi adatsanulira mbale yake pa mtsinje waukulu wa Furate; ndipo madzi ake adawuma, kuti ikhoze kukonzedwa njira ya mafumu wochokera kum’mawa.
  7824. Rev 16:13 Ndipo ine ndidawona mizimu itatu yonyansa yokhala ngati achule [ikutuluka] m’kamwa mwa chinyama chonga njoka, ndi m’kamwa mwa chirombo, ndi mwa mneneri wonyenga
  7825. Rev 16:14 Pakuti ali mizimu ya ziwanda, yakuchita zozizwa, [imene] ipita kunka kwa mafumu a kudziko lapansi ndi a dziko lonse, kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvu zonse.
  7826. Rev 16:15 Tawonani, ine ndidza ngati mbala. Wodala [ali] iye amene adikira, ndi kusunga zovala zake, kuti mwina iye angayende wamaliseche, ndipo iwo kupenya manyazi ake.
  7827. Rev 16:16 Ndipo iye adawasonkhanitsira iwo pamodzi ku malo wotchedwa mchinenedwe cha m’Chihebri Armagedon.
  7828. Rev 16:17 Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri adatsanulira mbale yake mum’lengalenga; ndipo mudatuluka mawu akulu kutuluka kuchokera mu kachisi wakumwamba, kuchokera kumpando wachifumu, kunena, Chachitika.
  7829. Rev 16:18 Ndipo padali mawu, ndi mabingu, ndi mphenzi; ndipo padali chivomerezi chachikulu, chotero chonga sichidachitikeponso chiyambire anthu padziko lapansi, chivomerezi champhamvu chotero, [ndi] chachikulu ndithu.
  7830. Rev 16:19 Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawidwa patatu, ndipo mizinda ya mayiko idagwa: ndipo Babuloni wamkulu adakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti awupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.
  7831. Rev 16:20 Ndipo zilumba zonse zidathawa, ndipo mapiri sadapezeke.
  7832. Rev 16:21 Ndipo pamenepo adagwa pa anthu matalala akulu wochokera kumwamba, [mwala uliwonse] wolemera pafupifupi talenti imodzi: ndipo anthu adanenera zamwano Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo; pakuti mliri wake udali waukulu koposa.
  7833. Rev 17:1 Ndipo panadza m’modzi mwa angelo asanu ndi awiri amene adali nazo mbale zisanu ndi ziwiri, ndipo adayankhula ndi ine, kunena, Idza kuno; ndidzawonetsa kwa iwe chiweruziro cha mkazi wa chigololo wamkulu amene akhala pa madzi ambiri:
  7834. Rev 17:2 Amene ndi iye mafumu adziko adachita chiwerewere, ndipo iwo akukhala padziko adaledzeretsedwa ndi vinyo wa chiwerewere chake.
  7835. Rev 17:3 Ndipo iye adanditenga ine mu mzimu, kunka nane kuchipululu: ndipo ndidawona mkazi alinkukhala pa chirombo cha mtundu wofiyirira, chodzala ndi mayina amwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
  7836. Rev 17:4 Ndipo mkazi adavala chovala cha nsalu ya pepo ndi mtundu wofiyirira, nakongoletsedwa ndi golidi ndi miyala ya mtengo wake ndi ngale, anali nacho m’dzanja lake chikho chagolidi chodzala ndi zonyansitsa ndi zodetsa za chiwerewere chake:
  7837. Rev 17:5 Ndipo pamphumi pake padali dzina lolembedwa, CHINSINSI, BABULONI WAMKULU, AMAYI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO LAPANSI.
  7838. Rev 17:6 Ndipo ndidawona mkazi ataledzera ndi mwazi wa woyera mtima, ndi mwazi wa wophedwa a Yesu: ndipo pamene ine ndidamuwona iye, ndidadabwa kwakukulu.
  7839. Rev 17:7 Ndipo mngelo adanena kwa ine, Chifukwa chiyani iwe uzizwa? Ine ndikuwuza iwe chinsinsi cha mkaziyo, ndi cha chirombocho chimene chim’tenga iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
  7840. Rev 17:8 Ndipo chirombo chimene iwe udachiwona, ndipo kulibe; ndipo chidzatuluka m’dzenje lopanda malire, ndi kunka kuchitayiko: ndipo iwo akukhala pa dziko lapansi adzazizwa, amene mayina awo sadalembedwe m’buku la moyo chiyambire makhazikitsidwe a maziko a dziko lapansi, pakuwona chirombo chimene chidalipo, koma kulibe, ndipo chilipo.
  7841. Rev 17:9 Ndipo pano [pali] malingaliro amene ali nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri, amene mkaziyo akhalapo.
  7842. Rev 17:10 Ndipo ali mafumu asanu ndi awiri: asanu agwa, imodzi ilipo, [ndipo] yinayo siyinadze; ndipo iyo ikafika, iyenera iyo kupitirira kanthawi kochepa.
  7843. Rev 17:11 Ndipo chirombocho chimene chidalipo, ndipo kulibe, ichi ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili cha zisanu ndi ziwirizo, nichimuka kuchitayiko.
  7844. Rev 17:12 Ndipo nyanga khumi zimene udaziwona ndi mafumu khumi, amene adali asadalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu kwa ora limodzi pamodzi ndi chirombo.
  7845. Rev 17:13 Iwo ali nawo mtima umodzi, ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho.
  7846. Rev 17:14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawapambana iwo: chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu: ndi iwo amene ali naye [ali] woyitanidwa, ndi wosankhidwa, ndi wokhulupirika.
  7847. Rev 17:15 Ndipo iye anena kwa ine, Madziwo amene udawawona, pamene akhala mkazi wachigololoyo, ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mayiko, ndi malirime.
  7848. Rev 17:16 Ndipo nyanga khumi zimene iwe udaziwona pa chirombocho, izi zidzadana ndi huleyo, ndipo adzamkhalitsa iye wabwinja ndi wamaliseche, ndikudya nyama yake, ndi kumuwotcha iye ndi moto.
  7849. Rev 17:17 Pakuti Mulungu adayika m’mitima mwawo kukwaniritsa chifuniro chake, ndikugwirizana, ndi kupereka ufumu wawo kwa chirombocho, kufikira mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa.
  7850. Rev 17:18 Ndipo mkaziyo amene udamuwona ndiye mzinda waukuluwo, umene uchita ufumu pa mafumu a dziko lapansi.
  7851. Rev 18:1 Ndipo zitachitika zinthu izi ndidawona mngelo wina wotsika pansi kuchokera kumwamba, wakukhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko lidawunikidwa ndi ulemerero wake.
  7852. Rev 18:2 Ndipo adafuwula kwamphamvu ndi mawu wolimba, kunena, Babuloni wamkulu wagwa, wagwa, ndipo wasandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zokhala ndi udani.
  7853. Rev 18:3 Pakuti mayiko onse aledzera ku vinyo wa mkwiyo wa chiwerewere chake, ndipo mafumu adziko achita naye chiwerewere chake, ndipo wochita malonda adziko adalemera ndi mphamvu yakudyerera kwake.
  7854. Rev 18:4 ¶Ndipo ine ndidamva mawu ena wochokera kumwamba, kunena, Tulukani mwa iyeyo, anthu anga, kuti musakhale woyanjana ndi machimo ake, ndi kuti musalandire miliri yake.
  7855. Rev 18:5 Chifukwa machimo ake afikira kumwamba, ndipo Mulungu wakumbukira zosalungama zake.
  7856. Rev 18:6 Perekani kwa iye mphotho monganso iyeyu adapereka mphotho kwa inu, ndipo muwirikizire kwa iye kuwirikiza kwake monga mwa ntchito zake: mchikhomo chimene iye adadzadza dzadzani kwa kuwirikiza kwake.
  7857. Rev 18:7 Monga momwe adadzipatsira iye ulemerero, nakhala moyo wachisangalalo, momwemo mumpatse chinzunzo ndi chomvetsa chisoni: pakuti adanena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu yayikazi, wosati wamasiye ine, ndipo sindidzawona chisoni.
  7858. Rev 18:8 Choncho miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo adzapserera ndi moto: pakuti wamphamvu [ali] Ambuye Mulungu wakumuweruza iye.
  7859. Rev 18:9 Ndipo mafumu a dziko lapansi, amene achita chiwerewere nakhala moyo wachisangalalo ndi iye, ndipo adzamlira iye nadzamlira maliro pamene adzawona utsi wakuyatsidwa kwake.
  7860. Rev 18:10 Poyima patali chifukwa cha kuwopa chinzunzo chake, kunena, Tsoka, tsoka mzinda waukuluwo Babuloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chako.
  7861. Rev 18:11 Ndipo wochita malonda a dziko lapansi adzalira ndi kubuma pa uwo; pakuti palibe munthu agulanso malonda awo:
  7862. Rev 18:12 Malonda a golidi, ndi siliva, ndi a miyala ya mtengo wapatali, ndi a ngale, ndi a nsalu ya bafuta, ndi chibakuwa, ndi ya siliki, ndi yofiyirira, ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi zotengera za mitundu yonse za minyanga, ndi zotengera za mitundu yonse za mtengo wake wapatali, ndi mkuwa, ndi zachitsulo, ndi za nsangalabwi.
  7863. Rev 18:13 Ndi Sinamoni, ndi zonunkhira, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi zinyama, ndi nkhosa, ndi malonda a akavalo, ndi akapolo, ndi miyoyo ya anthu.
  7864. Rev 18:14 Ndipo zipatso zimene moyo wako udazilakalaka zachoka kwa iwe, ndipo zinthu zonse zimene zidali zabwino ndi zolongosoka zachoka kwa iwe, ndipo iwe sudzazipezanso izi konse.
  7865. Rev 18:15 Wogulitsa zinthu izi, amene adalemeretsedwa ndi iye, adzayima patali chifukwa cha mantha a chizunzo chake, kulira ndi kuchita maliro,
  7866. Rev 18:16 Ndi kunena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu wovala bafuta, ndi nsalu ya pepo, ndi yofiyirira, ndi wokometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wapatali, ndi ngale!
  7867. Rev 18:17 Pakuti mu ora limodzi chuma chachikulu chotere chasanduka chabe. Ndipo mwini chombo aliyense, ndi wonse wopanga zombo, ndi amalinyero, ndi ambiri akuchita malonda m’mbali mwa nyanja, adayima patali,
  7868. Rev 18:18 Ndipo adalira pomwe anawona utsi wa kutentha kwake, kunena kuti, [Mzinda] uti [uli] ofanana ndi mzinda waukulu uwu!
  7869. Rev 18:19 Ndipo adathira fumbi pamitu pawo, nafuwula, kulira ndi kuchita maliro, kunena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, m’mene adalemeretsedwa nawo wonse adali nazo zombo m’nyanja pa chifukwa cha kulemera kwake! Pa ora limodzi wasanduka bwinja.
  7870. Rev 18:20 Kondwera pa iye, [iwe] kumwamba, ndi [inu] atumwi woyera mtima ndi aneneri; chifukwa Mulungu wabwezerera inu pa iye.
  7871. Rev 18:21 Ndipo mngelo wamphamvu adanyamula mwala ngati mphero yayikulu, nawuponya [uwo] m’nyanja, kunena, Chotero ndi chiwawa mzinda waukulu Babuloni udzagwetsedwa pansi, ndipo sudzapezekanso ayi.
  7872. Rev 18:22 Ndipo mawu a anthu woyimba azeze, ndi woyimba, ndi woyimba zitoliro, ndi wowomba malipenga, sadzamvekanso konse nthawi ina iriyonse mwa iwe; ndipo palibe munthu waluso, waluso lina lirilonse [iye angakhale nalo] sadzapezekanso mwa iwe; ndi kulira kwa mwala wa mphero sikudzamvekanso konse mwa iwe;
  7873. Rev 18:23 Ndipo kuwunika kwa nyali sikudzawunikiranso konse mwa iwe; ndi mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe: pakuti wotsatsa malonda anu adali anthu womveka a dziko lapansi; pakuti ndi matsenga ako mayiko onse adanyengedwa.
  7874. Rev 18:24 Ndipo mwa iye mudapezeka mwazi wa aneneri, ndi woyera mtima, ndi onse amene adaphedwa padziko lapansi.
  7875. Rev 19:1 Ndipo zitachitika zinthu izi ine ndidamva mawu akulu a khamu lalikulu kumwamba, kunena, Alleluya; Chipulumutso, ndi ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, kwa Ambuye Mulungu wathu:
  7876. Rev 19:2 Pakuti maweruzo ake [ali] wowona ndi wolungama: chifukwa iye waweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene adayipsa dziko lapansi ndi chiwerewere chake, ndipo anabwezera mwazi wa atumiki ake padzanja la mkaziyo.
  7877. Rev 19:3 Ndipo iwo adanenanso, Alleluya. Ndipo utsi wake unakwera ku nthawi za muyaya.
  7878. Rev 19:4 Ndipo akuluwo makumi awiri mphambu zinayi ndi zamoyo zinayi adagwa pansi ndipo adalambira Mulungu amene adakhala pa mpando wachifumu, kunena, Amen; Alleluya.
  7879. Rev 19:5 ¶Ndipo mawu adachokera kumpando wachifumu, kunena, Lemekezani Mulungu wathu, inu atumiki ake onse, ndi inu nonse amene mumuwopa iye, aang’ono ndi akulu.
  7880. Rev 19:6 Ndipo ine ndidamva akukhala ngati mawu a khamu lalikulu, ndi ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mawu a mabingu wolimba, kunena, Alleluya: pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse achita ufumu.
  7881. Rev 19:7 Tiyeni tikondwere ndi kusekera, ndi kupereka ulemerero kwa iye: pakuti ukwati wa Mwanawankhosa wadza, ndipo mkazi wake wadzikonzekeretsa.
  7882. Rev 19:8 Ndipo kwa iye kudapatsidwa avale bafuta wosalala, wosada ndipo woyera: pakuti bafuta ndiye zolungama za woyera mtima.
  7883. Rev 19:9 Ndipo iye adanena ndi ine, Lemba, Wodala [ali] iwo amene ayitanidwa ku phwando la mgonero la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo iye adanena ndi ine, Awa ndiwo maneno wowona a Mulungu.
  7884. Rev 19:10 Ndipo ine ndidagwa pamapazi ake kuti ndimlambire iye. Ndipo iye adanena ndi ine, [Uwone kuti] usachite [ichi]: ine ndine mtumiki mzako, ndi a iwo a abale ako amene ali nawo umboni wa Yesu: lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo mzimu wa uneneri.
  7885. Rev 19:11 Ndipo ine ndidawona kumwamba kutatseguka, ndipo tawonani kavalo woyera; ndi iye amene adakhala pa iye [adali] wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona, ndipo m’chilungamo iye aweruza ndi kuchita nkhondo.
  7886. Rev 19:12 Maso ake ali ngati lawi la moto, ndipo pamutu pake [padali] akorona ambiri; ndipo adali nalo dzina lolembedwa, limene sadalidziwa wina aliyense, koma iye yekha.
  7887. Rev 19:13 Ndipo [adali] wovekedwa ndi chovala choviyikidwa m’mwazi: ndipo atchedwa dzina lake, Mawu a Mulungu.
  7888. Rev 19:14 Ndipo magulu a nkhondo amene adali kumwamba adamtsata iye wokwera pa akavalo woyera, wovala bafuta wosada ndi woyera.
  7889. Rev 19:15 Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti ndi ilo akanthe nalo mafuko: ndipo iye adzawalamulira ndi ndodo ya chitsulo: ndipo aponda iye moponderamo mphesa mwa vinyo wa ukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvu zonse.
  7890. Rev 19:16 Ndipo ali nalo pa chovala [chake] ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.
  7891. Rev 19:17 Ndipo ndidawona mngelo alikuyima m’dzuwa; ndipo adafuwula ndi mawu akulu, kunena kwa mbalame zonse zimene ziwuluka pakati pa mlengalenga, Idzani ndi kudzisonkhanitsa eni nokha ku phwando la mgonero la Mulungu wamkulu;
  7892. Rev 19:18 Kuti mukhoze kudya nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitawo, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi nyama ya iwo akhala pa iwo, ndi nyama ya [anthu] onse, mfulu ndi akapolo, aang’ono ndi akulu.
  7893. Rev 19:19 Ndipo ine ndidawona chirombocho, ndi mafumu a dziko lapansi, ndi magulu a nkhondo awo, wosonkhanidwa pamodzi kuchita nkhondo ndi iye amene adakhala pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.
  7894. Rev 19:20 Ndipo chidatengedwa chirombocho, ndi pamodzi ndi iye mneneri wonyenga amene adachita zozwizitsa pamaso pake, zimene iye adasokeretsa nazo iwo amene adalandira chizindikiritso cha chirombo, ndi iwo amene adalambira fano lake. Iwo onse awiri adaponyedwa ali ndi moyo m’nyanja yamoto yakutentha ndi sulfure.
  7895. Rev 19:21 Ndipo wotsalawa adaphedwa ndi lupanga la iye amene adakhala pa kavalo, [lupanga] limene ndilo lotuluka kuchokera m’kamwa mwake: ndipo mbalame zonse zidakhuta ndi nyama zawo.
  7896. Rev 20:1 Ndipo ine ndidawona mngelo akubwera kutsika kuchokera kumwamba, ali nacho chifungulo cha dzenje lopanda malire ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.
  7897. Rev 20:2 Ndipo iye adagwira chinyama chonga njoka, njoka yokalamba yakaleyo, ndiye Mdiyerekezi, ndi Satana, ndipo adam’manga iye zaka chikwi.
  7898. Rev 20:3 Namponya ku dzenje lopanda malire, ndi kumtsekera iye, ndi kuyika chisindikiziro pa iye, kuti iye asanyengenso mayiko kufikira kukwaniritsidwa kwa zaka chikwi: ndipo patatha izi adzayenera kumasulidwa iye kanthawi kochepa.
  7899. Rev 20:4 Ndipo ine ndidawona mipando ya chifumu, ndi iwo amene adakhala pa iyo, ndipo chiweruzo chidaperekedwa kwa iwo: ndipo [ine ndidawona] miyoyo ya iwo amene adawadula mitu chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi iwo amene sadalambira chirombocho, kapena fano lake, kapena sadalandira chizindikiritso [chake] pamphumi, kapena m’manja awo; ndipo adakhala ndi moyo nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi chimodzi.
  7900. Rev 20:5 Koma wotsala a akufa sadakhalanso ndi moyo kufikira zitatha zaka chikwi. Uku [ndiko] kuwuka kwa akufa koyamba.
  7901. Rev 20:6 Wodala ndi woyera [ali] iye amene ali ndi gawo pa kuwuka koyamba: pa iwowa imfa yachiwiri ilibe mphamvu, koma iwo adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwi.
  7902. Rev 20:7 Ndipo pamene zaka chikwizidzatha, Satana adzamasulidwa kutuluka m’ndende yake,
  7903. Rev 20:8 Ndipo adzatuluka kukanyenga mayiko amene ali mu mbali zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa pamodzi ku nkhondo: chiwerengero chawo cha iwo amene [chili] ngati mchenga wa kunyanja.
  7904. Rev 20:9 Ndipo iwo adakwera nafalikira m’lifupi mwa dziko lapansi, nazungulira msasa wa woyera mtima, ndi mzinda wokondedwawo: ndipo moto udatsika kuchokera kwa Mulungu kutuluka kumwamba, ndi kuwanyeketsa iwo.
  7905. Rev 20:10 Ndipo mdiyerekezi amene adawasocheretsa iwo adaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure, kumene chirombocho ndi mneneri wonyengayo [ali], ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za muyaya.
  7906. Rev 20:11 ¶Ndipo ndidawona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi iye amene adakhala pa iwo, amene kuchokera ku nkhope ya dziko ndi kumwamba zidathawa; ndipo sadapezeka malo a iwo.
  7907. Rev 20:12 Ndipo ine ndidawona akufa, aang’ono ndi akulu atayimirira pamaso pa Mulungu; ndipo mabuku adatsegulidwa: ndipo buku lina lidatsegulidwa, limene ndiro [buku] la moyo: ndipo akufa adaweruzidwa kuchokera mu zinthu zimene zidalembedwa m’mabukuwo, monga mwa ntchito zawo.
  7908. Rev 20:13 Ndipo nyanja idapereka akufawo amene adali m’menemo; ndipo imfa ndi nyanja ya moto zidapereka akufawo adali m’menemo: ndipo iwo adaweruzidwa munthu aliyense monga mwa ntchito zawo.
  7909. Rev 20:14 Ndipo imfa ndi malo a mazunzo oyembekezera chiweruzo akufa ochimwa zidaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyi ndi imfa yachiwiri.
  7910. Rev 20:15 Ndipo wina aliyense amene sadapezeka wolembedwa m’buku la moyo adaponyedwa m’nyanja ya moto.
  7911. Rev 21:1 Ndipo ine ndidawona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano: pakuti kumwamba koyamba ndi dziko loyamba zidapita; ndipo kunalibenso nyanja.
  7912. Rev 21:2 Ndipo ine Yohane ndidawona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, kubwera kutsika kuchokera kwa Mulungu kutuluka kumwamba, wokonzekeretsedwa monga ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.
  7913. Rev 21:3 Ndipo ine ndidamva mawu akulu wochokera kumwamba kunena, Tawonani, chihema cha Mulungu [chili] pamodzi ndi anthu, ndipo adzakhala ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake, ndipo Mulungu mwiniyekha adzakhala ndi iwo, [ndipo adzakhala] Mulungu wawo.
  7914. Rev 21:4 Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse kuyichotsa m’maso mwawo; ndipo sipadzakhalanso imfa, kapena chisoni, kapena kulira, ndipo sipadzakhalanso kumva kuwawa: pakuti zinthu zoyambazo zapita.
  7915. Rev 21:5 Ndipo iye amene adakhala pa mpando wachifumu, adati, Tawonani, ine ndipanga zonse zikhale zatsopano. Ndipo adati kwa ine, Lemba: pakuti mawu awa ali wokhulupirika ndi wowona.
  7916. Rev 21:6 Ndipo iye adati kwa ine, Zachitika. Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi chitsiriziro. Ine ndidzapereka kwa iye amene akumva ludzu la kasupe wa madzi a moyo kwa ulere.
  7917. Rev 21:7 Iye amene apambana adzalandira cholowa cha zinthu zonse; ndipo ine ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana wanga wamwamuna.
  7918. Rev 21:8 Koma amantha, ndi wosakhulupirira, ndi wonyansa, ndi akupha, ndi achigololo, ndi a matsenga, ndi opembedza mafano, ndi abodza wonse, adzakhala ndi cholowa chawo m’nyanja imene ndi yotentha ndi moto ndi sulfure: imene ili imfa yachiwiri.
  7919. Rev 21:9 Ndipo panadza m’modzi kwa ine m’modzi wa angelo asanu ndi awiri amene adali nazo mbale zisanu ndi ziwiri zodzala ndi miliri isanu ndi iwiri, ndipo adayankhula ndi ine, kunena, Idza kuno, ine ndidzakuwonetsa iwe mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.
  7920. Rev 21:10 ¶Ndipo iye adanditenga ine mu mzimu kunka ku phiri lalikulu ndi lalitali, ndipo anandiwonetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu woyera, wotsika kutuluka kuchokera kumwamba kwa Mulungu,
  7921. Rev 21:11 Wokhala nawo ulemerero wa Mulungu: kuwunika kwake [kudali] kofanana ndi mwala wopambana wa mtengo wapatali, ndi inde mwala wa jaspa, woyengeka ngati krustalo;
  7922. Rev 21:12 Ndipo udali nalo linga lalikulu ndi lalitali, ndipo udali nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pa zipatapo angelo khumi ndi awiri, ndi mayina wolembedwapo, amene ali [mayina] a mafuko khumi ndi awiri a mafuko a ana a Israyeli:
  7923. Rev 21:13 Kum’mawa zipata zitatu; ndi kumpoto zipata zitatu; ndi kum’mwera zipata zitatu; ndi kumadzulo zipata zitatu.
  7924. Rev 21:14 Ndipo linga la mzindawo lidali nawo maziko khumi ndi awiri, ndi m’menemo mayina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.
  7925. Rev 21:15 Ndipo iye amene adayankhula ndi ine adali nalo bango lagolidi kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake.
  7926. Rev 21:16 Ndipo mzinda udali wofanana ngodya zonse zinayi, ndi mulitali mwake ulingana ndi mulifupi mwake: ndipo adayesa mzinda ndi bangolo, mitunda chikwi chimodzi ndi mazana asanu. Mulitali mwake ndi mulifupi mwake ndi msinkhu wake ziri zolingana.
  7927. Rev 21:17 Ndipo iye adayesa linga lake, ma phazi ndi theka zana mphambu makumi anayi kudza zinayi, [malingana ndi] muyeso wa munthu, umene uli, kwa mngelo.
  7928. Rev 21:18 Ndipo zomangira za linga lake ndiye jaspa: ndipo mzindawo [unali] golidi woyengeka, wofanana ndi mandala woyera.
  7929. Rev 21:19 Ndipo maziko a linga la mzindawo [adali] wokometsedwa ndi miyala ya mtengo wapatali ya mitundumitundu. Maziko woyamba adali jaspa; achiwiri, safiro; achitatu, kalekidoni; achinayi, emaraldi;
  7930. Rev 21:20 Achisanu, sardonik; achisanu ndi chimodzi, sardiyasi; achisanu ndi chiwiri, krusolite; achisanu ndi chitatu, berilo, achisanu ndi chinayi, a topazi; akhumi, a krusoprasi; akhumi ndi chimodzi, mwala wa jakinti; akhumi ndi chiwiri, ametisti.
  7931. Rev 21:21 Ndipo zipata khumi ndi ziwiri [zinali] ngale khumi ndi ziwiri: chipata chilichonse pachokha chinali cha ngale imodzi: ndipo msewu wa mzinda [unali] wagolidi woyengeka, monga ngati mandala wowonekera.
  7932. Rev 21:22 Ndipo ine sindidawona kachisi m’menemo: pakuti Ambuye Mulungu wamphamvu zonse ndi Mwanawankhosa ndiwo kachisi wake.
  7933. Rev 21:23 Ndipo mzindawo unalibe kosowekera dzuwa, kapena mwezi, wakuwalira mu iwo: pakuti ulemerero wa Mulungu uwunikira umenewu, ndipo Mwanawankhosa ndiye nyali yake.
  7934. Rev 21:24 Ndipo mafuko a iwo amene ali wopulumutsidwa adzayenda mu kuwunika kwake: ndipo mafumu a dziko lapansi abweretsa ulemerero ndi ulemu wawo kulowa nawo momwemo.
  7935. Rev 21:25 Ndipo zipata zake sizidzatsekedwa konse usana: pakuti sikudzakhala usiku kumeneko.
  7936. Rev 21:26 Ndipo iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mafuko nadzalowa nawo momwemo.
  7937. Rev 21:27 Ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kodetsedwa, kapena [china chilichonse] chakuchita chonyansa, kapena [kunena] bodza: koma iwo wokha amene adalembedwa m’buku la moyo la Mwanawankhosa.
  7938. Rev 22:1 Ndipo iye adandiwonetsa mtsinje woyengeka wa madzi a moyo, wowonekera ngati kristalo, wotuluka ku mpando wa chifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.
  7939. Rev 22:2 Pakati pa msewu wake, ndi tsidya lirilonse la mtsinje, padali pamenepo mtengo wa moyo, wakubala zipatso [zamitundu yosiyanasiyana] khumi ndi ziwiri, [ndi] kupatsa zipatso zake mwezi uliwonse: ndipo masamba a mtengo [anali] akuchiritsa nawo mafuko,
  7940. Rev 22:3 Ndipo sipadzakhalanso temberero: koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo atumiki ake adzamtumukira iye:
  7941. Rev 22:4 Ndipo adzawona nkhope yake; ndipo dzina lake [lidzakhala] pamphumi pawo.
  7942. Rev 22:5 Ndipo sipadzakhalanso usiku kumeneko; ndipo iwo safuna nyali, kapena kuwunika kwa dzuwa; pakuti Ambuye Mulungu apereka kwa iwo kuwunika: ndipo adzachita ufumu ku nthawi za muyaya.
  7943. Rev 22:6 ¶Ndipo iye adati kwa ine, Mawu awa [ali] wokhulupirika ndi wowonadi: ndipo Ambuye Mulungu wa aneneri woyera adatuma mngelo wake kuwonetsera atumiki ake za zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa.
  7944. Rev 22:7 Tawona, Ine ndidza msanga: wodala [ali] iye amene asunga mawu a chinenero cha buku ili.
  7945. Rev 22:8 Ndipo ine Yohane ndidawona zinthu zimenezi, ndipo ndidazimva [izo]. Ndipo pamene ndidamva ndi kupenya ndinagwa pansi kuti ndilambire pamaso pa mapazi a mngelo amene adandiwonetsa zinthu izi.
  7946. Rev 22:9 Ndipo adanena iye ndi ine, Tapenya, [iwe usachite ichi] ayi: pakuti ine ndine mtumiki mzako, ndi wa kwa abale ako aneneri, ndi wa iwo amene asunga zonenedwa za buku iri: lambira Mulungu.
  7947. Rev 22:10 Ndipo adanena ndi ine, Usasindikiza chizindikiro mawu awa a uneneri wa buku ili: pakuti nthawi yayandikira.
  7948. Rev 22:11 Iye amene ali wosalungama, akhale wosalungamabe: ndi iye amene ali wonyansa, akhalebe wonyansa: ndi iye amene ali wolungama, akhalebe wolungama: ndi iye amene ali woyera, akhalebe woyera.
  7949. Rev 22:12 Ndipo, Tawonani, ine ndidza msanga; ndipo mphotho yanga [ili] ndi ine, yakupatsa munthu aliyense monga momwe ntchito yake idzakhalira.
  7950. Rev 22:13 Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi chitsiriziro, chiyambi ndichitsiriziro.
  7951. Rev 22:14 Wodala ali iwo amene achita malamulo ake, kuti akhoze kukhala nawo ufulu pa mtengo wa moyo, ndi kuti akhoze kulowa mu mzinda kudzera pa zipata.
  7952. Rev 22:15 Pakuti kunja [kuli] agalu, ndi anyanga, ndi achigololo, ndi akupha, ndi wopembedza mafano, ndi wina aliyense wakukonda ndi kupeka bodza.
  7953. Rev 22:16 Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukakuchitirani inu umboni zinthu izi m’mipingo. Ine ndine muzu ndi wobadwa kwa Davide, [ndi] nyenyezi yowala ya nthanda ya mbandakucha.
  7954. Rev 22:17 Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idza. Ndipo iye amene akumva ludzu adze. Ndipo aliyense wofuna, muloleni atenge madzi a moyo kwaulere.
  7955. Rev 22:18 Pakuti ine ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mawu a uneneri wa buku ili, Ngati munthu adzawonjezera pa zinthu izi, Mulungu adzamuwonjezera iye miliri imene yalembedwa m’buku ili:
  7956. Rev 22:19 Ndipo ngati munthu aliyense adzachotsako pa mawu a buku a uneneri uwu, Mulungu adzamchotsera iye gawo lake kuchotsa m’buku la moyo, ndi kuchotsa mu mzinda woyerawo, ndi [kuchokera] pa zinthu zimene zalembedwa m’buku ili.
  7957. Rev 22:20 Iye amene achitira umboni zinthu izi anena, Ndithudi ine ndidza msanga. Amen. Ngakhale choncho, idzani, Ambuye Yesu.
  7958. Rev 22:21 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu [chikhale] ndi inu nonse. Amen.
  7959.